Page 1
1
NDONDOMEKO ZA NJIRA
ZA
KUCHULUKITSA
HARVESTIME INTERNATIONAL INSTITUTE
Phunziro limeneri ndi gawo limodzi la maphunziro a Harvest International Institute ndipo
cholinga chake ndi kukonzekeretsa okhulupilira kuti akatute zokolora zambiri zauzimu.
Mutu waukulu mumaphunzirowa ndikuphunzitsa zimene Yesu anaphunzitsa, zimene
zinasandulitsa anthu wamba monga asodzi, otolera misonkho ndi ena kulalikira Uthenga
Wabwino ndi kuwonetsera mphamvu ya uthengawo mu nthawi yawo.
Bukuli ndi phunziro limodzi mwa maphunziro ambiri amene cholinga chake ndikuwakopa
okhulupilira kuti akakonze dongosolo, kuyendetsa, ndi kubweretsa pamodzi anthu kuti Uthenga
Wabwino ukalalikidwe.
@Harvestime International Institute
Page 2
2
ZAMKATI MWA BUKULI
Kagwiritsidwe Ntchito Ka Bukuli……………………………………………………….…..........3
Ndondomeko Zothandizira Kuphunzira Limodzi Pagulu…………………………………………4
Mau Oyamba……………………………………………………………………………………....5
Zolinga za Maphunzirowa…………………………………………………………………...........7
NDONDOMEKO ZA NJIRA ZA KUCHULUKITSA
1. Asodzi a Anthu……………………………………………………………………………......8
2. Tsiku la Zinthu Zochepa………………………………………………………………..........16
3. Mafanizo a Kuchuliktsa……………………………………………………………………...40
4. Chimodzi Kuphatikiza Chimodzi Zimakhala Zopitilira Ziwiri…………………………...…50
5. Mawu Oyamba a Kukula kwa Mpingo………………………………………………………58
6. Kukula kwa Mkati……………………………………………………………………………70
7. Kukula mu Chiwerengero…………………………………………………………………....90
8. Kukula Mmadera…………………………………………………………………………...104
9. Kukula Polumikiza…………………………………………………………………………112
10. Zisankho Kapena Ophunzira……………………………………………………………….127
11. Kukula Mopinimbira……………………………………………………………………….143
12. Malo Ochitirapo Maphunziro………………………………………………………………154
13. Mayankho a Mafunso Odziyetsa Nokha……………………………………………………163
Page 3
3
KAGWIRITSIDWE NTCHITO KA BUKULI
KAKONZEDWE KA BUKULI
Phunziro liri lonse limakhala ndi zinthu izi:
Zolinga: Izi ndi zimene mukuyenera kukwaniritsa kapena kudziwa pa mapeto pa phunziro.
Welengani zimenezi musanayambe phunziro lanu.
Vesi Yotsogololera: Ndimeyi imatsindika mfundo yayikulu mu phunziro lathu.
Zopezeka mu Magawo: Gwiritsani ntchito Baibulo lanu kuti mufufuze mavesi amene
sanalembedwe mu bukuli koma angotchulidwa.
Mayeso Odziyesa Nokha: Osathamangira kulememba mayeso musanamalize kuwerenga
chaputala, komanso polemba musagwiritse ntchito Baibulo kapena bukuli polemba mayesowa.
Mayankho amayesowa muwapeza kumapeto a bukuli.
Zophunzira Zowonjezera: Ndime imeneyi ikuthandizani kuti muwerenge mau Mulungu ndi
kuzamitsa ukadaulo wanu pophunziro komanso kugwiritsa ntchito mu utumiki zimene mwa.
Mayeso Omaliza: ngati mwayamba kuphunzira phunziroli mukuyenera kulemba mayeso
pamapeto a phunziroli ndipo mayesowo aperekedwa kwa aphunzitsi anu kuti mupatsidwe
malikisi.
ZOWELENGA ZINA ZOFUNIKA POPHUNZIRA PHUNZIROLI
Mudzafunikira Buku Lopatulika
Page 4
4
NDONDOMEKO ZOTHANDIZIRA KUPHUNZIRA LIMODZI PAGULU
MKUMANO WOYAMBA
Kutsekulira: Yamabani ndi pemphero ndi kudziwana wina ndi mnzake ndipo ophunzira
alembetse mayina.
Khazikitsani Ndondomeko Zapagulu: Musankhe amene atsogolere mkumano wanu,
sankhaninso malo ndi masiku amene mudzikumana.
Mayamiko ndi Matamando: Yitanirani kupezeka kwa Mzimu Woyera pamene muchita
mkumano wanu.
Gawani Mabuku Kwa Ophunzira: Awuzeni ophunzira dzina laphunziro, zolinga zake ndi
dongosolo.
Perekani Nchito Yoyamba. Ophunzira ayenera kuwerenga ma chaputala amene apatsidwa
ndikulemba mayeso odziyesa okha isanafike nthawi ya mkumano wina. Ndipo kuchuluka kwa
machaputala amene adziphunzitsidwa pa mkumano uli onse kuzitengera kutalika kwa chaputala
komanso kumvetsetsa kwa ophunzira.
MKUMANO WACHIWIRI NDI KUKUMANA KWINA PATSOGOLO
Kutsekulira: Tsekulirani ndi pemphero kenako lembani mayina awophunzira atsopano
ndikuwapatsa buku lawo. Muyitane mayina a wophunzira amene abwera. Komanso osayiwala
mayamiko ndi matamando kwa Mulungu.
Kukumbutsira: Yambani ndi kubwereza mwachidule zimene munaphunzitsa mu mkumano
wanu womaliza.
Phunziro: Afunseni ophunzira ndemanga zawo kapena mafunso okhudza phunziro limene
aphunzira komanso mmene angagwiritsire ntchito zimene aphunzira pamoyo wawo ndi utumiki.
Mayeso Odziyesa Nokha: Konzetsani mayeso amene ophunzira amaliza ndipo mukhonza
kusankha kupereka mayankha kapena kuwachotsa mubukuli kuti ophunzira adzipezere okha
mayankho.
Mayeso omaliza: Pamapeto pa maphunziro amenewa, gulu la ophunzira onse lidzapemphedwa
kulemba mayeso omaliza ndipo aphunzitsi awonetsetse kuti ophunzira wina aliyense ali ndi buku
laphunziroli.
Page 5
5
MAWU OYAMBA
Baibulo limakamba za kulengedwa kwa dziko lapansi komanso Adamu ndi Hava (Genesis 1).
Lamulo loyamba limene Mulungu anawapatsa ndi loti achulukane:
Mulungu ndipo adalenga munthu m'cifanizo cace, m'cifanizo ca Mulungu
adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.
Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, mucuruke,
mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa
mbalame za m'mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.
(Genesis 1:27-28).
Kuchulukanaku sikunali kwa kuthupi kokha ayi, komanso kunali kwa ku uzimu. Monga mmene
Adamu ndi Hava amachulukana ku thupindiye kuti akanalidzadza dzikoli ndi enanso ngati
iwowo; amene anamdziwa Mulungu ndi kuyenda mu chiyanjano ndi Iye. Akanakhala
akuchulukana mu uzimu monganso kuthupi.
Kugwa kwa munthu ku uchimo kunaika dongosolo lochulukanali pa chiposezo (Genesis 3).
Tchimo linabweretsa imfa ya kuthupi imene inatchinga kuchulukana kwa kuthupi (Genesis
2:17). Tchimo linabweretsanso imfa ya uzimu imene ndi kulekana kwa uzimu kwa munthu
wochimwa ndi Mulungu wolungama. Ukunso kunatchinga kuchulukana kwa uzimu.
Pakuti Mulungu anamkonda munthu kwambiri, choncho adapanga dongosolo lopulumutsa anthu
ku imfa ya uzimu yowawayi. Mulungu anatumiza Yesu Khristu kufera zolakwa za anthu onse.
Yesu analipira chilango cha imfa mmalo mwathu, keneko anagonjetsa imfa pa kuukanso ku imfa
(Yohane 20).
Munthu aliyense ayenera kusankha kulandira dongosolo la Mulungu la chipulumutso pa
kupempha chikhululukiro cha machimo ndi kulandira Yesu ngati Mpulumutsi. Monga
wokhulupirira mwa Yesu amene machimo ake akhululukidwa, ndiye kuti mwapulumutsidwa ku
imfa ya uzimu.
Ngakhale kuti thupi loonekali lidzafa tsiku lina, mudzakhalabe ndi moyo ku uzimu ndipo
mudalandira matupi atsopano amene adzakhala ndi moyo nthawi zonse.
...Koma tonse tidzasandulika, m'kamphindi, m'kutwanima kwa diso, pa lipenga
lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osabvunda, ndipoife
tidzasandulika…Ndipo pamene cobvunda ici cikadzabvala cisabvundi ndi caimfa ici
cikadzabvala cosafa, pamenepo padzacitika mau olembedwa, 20 Imfayo yamezedwa
m'cigonjetso (1 Akorinto 15:51,52,54).
Page 6
6
Pamene mwalandira Yesu ngati mpulumutsi wanu, zili ngati kulengedwanso ndi Mulungu
kachiwiri. Baibulo limati “kubadwanso mwatsopano”:
Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu
sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu (Yohane 3:3).
Moti “Kubadwa mwatsopano” sikutanthauza kubadwa kuthupi. Kumatanthauza kubadwa ku
uzimu. Mumalengedwanso ku uzimu monga olengedwa atsopano mwa Khristu. Ndinu
“atsopano” chifukwa simukhalanso mu uchimo ndi kuchita makhalaidwe akale a uchimo:
Cifukwa cace ngati munthu ali yense ali mwa Kristu ali wolengedwa watsopano;
zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano (2 Akorinto 5:17).
Pa chiyambi cha dziko lapansi, Mulungu koyambirira analamulira anthu ake olengedwe
mwatsopano kuti achulukane. Lamulo lake loyamba lolenganso, okhulupirira “obadwa
mwatsopano” ndi chimodzimodzi. Tikuyenera kuchulukana mu uzimu ndi kulidzadza dziko
lapansi ndi ena ngati mmene ifeyo tilili; anthu amene ndi okonda Mulungu ndi kuyenda
muchiyanjano ndi Iye.
Pamene Yesu anayitana anthu kuti amutsatire, uku kunali kuitanira anthu ku chichulukitso cha
uzimu (Luka 5:10). Lamulo lake lomaliza kwa okhulupirira linali loti achulukane ku uzimu
(Machitidwe 1:8). Kuti tikwanitse kufikira anthu zikwi amene akufa ku uchimo asanamve
uthenga, okhulupirira aliyense akuyenera kukhala ochitachita ndi kuphunzira mfundo za
kuchukana ku uzimu.
Phunziroli limagawanso ndi njira za Mbaibulo za kukhala ochitachita mu uzimu zimene
zikupangitsani inu kuchuluka mwa kumvera lamulo la Mulungu. Muphunzira za mmene
mungachulukanire ku uzimu monga munthu komanso ngati gulu pa tchalitchi. Ngati mugwiritse
ntchito mfundo za Mbaibulo zimene zikuphunzitsidwa mu phunziro, muzakhala ndi udindo wa
kuchulukana zikwi kwa okhulupirira ophunzitsidwa ndi olimbikira.
Ngati mukuphunzira maphunziro a Havestime International Institute mwandondomeko, phunziro
ili ndi lachitatu mu mabuku atatu, amene amakamba za kuchulukitsa antchito ophunzitsika a ku
uzimu kupyolera kumapeto kwa buku lachiwiri.
Maphunziro amene akupezeka mu buku la chitatu ndi awa “Kuumba Maonedwe a Dziko a
Mbaibulo,” “Njira Zophunzitsira,” Njira Zochukitsa,” ndi “Mfundo za Mphamvu.” Maphunziro
amenewa amabweretsa chidziwitso cha chosowa cha ku uzimu cha dziko lapansi ndi
kulongosolo za mmene mungafikirire chosowacho kudzera mu ziphunzitso ndi maulaliki a
Mbaibulo, kuchulukana ndi machitachita a mphamvu za uzimu.
Page 7
7
ZOLINGA ZA MAPHUNZIROWA
Pakutha pa phunziroli muyenera:
Kubalana ku uzimu kudzera mu kugwiritsa ntchito njira zochulukana za Mbaibulo.
Kuomba mkota pa mfundo za kuchulukana zimene zinaphunzitsidwa mu mafanizo a
Mchipanagano Chatsopano.
Kulongosola mmene okhulupirira angachulukanire ku uzimu pa kubadwisa mazana a
okhulupirira atsopano.
Kupanga kunyumba kwanu ngati malo ochulukaniranapo ku uzimu.
Kuomba mkota pa mfundo za kuchulukana mkati mwa mpingo.
Kuomba mkota pa mfundo za kukulitsa kuchulukana kwa mpingo.
Kuomba mkota pa mfundo za kutalikitsa kuchulukana kwa mpingo.
Kuomba mkota pa mfundo za kulumikiza kuchulukana kwa mpingo.
Kulimbikitsa otembenuka mtima kumene kuti asangokhala ophunzira kokha ayi.
Kudziwa zinthu zimene zimatchinga kuchulukana ku uzimu.
Kukhazikitsa Havestime International Institute ngati malo ochulukana ku uzimu.
Page 8
8
CHAPUTALA CHA 1
ASODZI A ANTHU
ZOLINGA:
Pakutha pa chaputalachi muyenera:
Kulemba Vesi Lotsogolera kuchokera pamtima.
Kudziwa lamulo loyamba ndi lotsiriza la Yesu kwa ophunzira ake.
Kupereka tanthauzo la “kuchukitsa.”
Kulongosola za kuchulukana kwa ku uzimu.
Kupereka tanthauzo la “njira.”
Kupereka tanthauzo la “ndondomeko za njira”
Kulongosola “njira zosiyanasiyana za kuchulukitsa ku uzimu”
Kuomba mkota pa mfundo za usodzi wodziwika umene tingautanthauzire ku usodzi wa
uzimu.
VESI LOTSOGOLERA:
Ndipo Yesu ananena nao, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu
asodzi a anthu (Marko 1:17).
MAWU OYAMBA
Pamene Yesu anayamba utumiki wake pa dziko lapansi, anayitana anthu ambiri kuti akhala
ophunzira ake oyamba:
Ndipo Yesu ananena nao, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu
asodzi a anthu (Marko 1:17).
Lamulo loyamba kwa akuphunzira amenewa linali likuti achulukane ku uzimu. Ngati
amamutsatira, Iye anawapanga “asodzi a anthu.” Akanachulukana pamene “amasodza” amuna
ndi akazi ku uzimu.
Uthenga wotsiriza wa Yesu kwa akuphunzira ake unali owaytanira ku kuchulukana ku uzimu:
Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo
mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi
kufikira malekezero ace a dziko.
Page 9
9
Ndipo m'mene adanena izi, ali cipenyerere iwo, ananyamulidwa; ndipo mtambo
unamlandira iye kumcotsa kumaso kwao (Machitidwe 1:8-9).
Kodi ophunzira akanakwaniritsa bwanji ntchito yotumidwa ndi Yesu? Kodi zikanatheka bwanji
gulu la anthu ochepawa kuchulukana mkufikira dziko lonse?
NJIRA ZOCHULUKITSA
Yesu anaulula njira zenizeni zimene zikanapangisa ophunzira ake kukwaniritsa lamulo
lochulukana ku uzimu. Lamulo loyamba limenenso ndi lofunika linaperekedwa ngati gawo la
kutumidwa ku Machitidwe 1:8. Ophunzira akanachulukana kudzera mu kulandira mphamvu ya
Mzimu Woyera. Njira zina zinaululidwa pamene ophunzira a Yesu anayamba kuchuluka ndi
kufikira dziko lapansi ndi uthenga wabwino. Njira zimenezi zikupezeka mmabuku a Machitidwe
ndi Makalata mu Chipangano Chatsopano.
Phunziroli limalongosola njira za kuchulukanaku. Limaphunzitsa za mmene mungagwiritsire
ntchito kuti muchulukane ku uzimu ndi kukwaniritsa lamulo la Mulungu. Koma koyamba,
muyenera kumvetsetsa pamene tikuti “kuchulukana.” Mawu oti “kuchulukana” akutanthauza
kuti kukhala ambiri mu chiwerengero pa kuberekana. Kuchulukana ndi njira yochulukitsa.
Pamene chinthu chachulukitsidwa, ndiye kuti chikuonjezeraka mobwereza mu mchitidwe
ofanana.
Mu dziko limene timakhalali, amuna ndi akazi amachulukana pokhala ndi ana. Amachulukana
kuthupi. Kuchulukana ku uzimu kumachitika pochulukana ku uzimu. Okhulupirira
amachulukana pogawana uthenga wabwino ndi anthu ena, ndi kuwatsogolera kukhala
okhulupirira, ndi kuwakhazikitsa kukhala ophunzira a Ambuye Yesu Khristu.
Baibulo limaulula za njira za Mulungu za kuchulukana ku uzimu. Choncho “njira” ndi dongosolo
lofuna kukwaniritsa cholinga chapaderadera. Tsono “ndondomeko za njira” ndi dongosolo la
njira zimene zimaikidwa pamodzi kuti mukathe kufikira cholinga chanu.
Motero “Ndondomeko za njira zochulukitsa” ndi njira zimene zimapangitsa okhulupirira kufikira
cholinga chawo cha kuchulukana ku uzimu. Cholinga sichisintha. Tikuyenera kuchulukana ku
uzimu pa kufikira dziko lonse lapansi ndi uthenga wabwino. Pali njira zambiri zimene tingathe
kugwiritsa ntchito kuti tithe kufikira cholingachi. Njirazi ndi “ndondomeko” kapena
madongosolo osiyanasiyana amene tingathe kuchuluka.
Pamene munthu agwira ntchito limodzi ndi njira za Mulungu zochulukitsa, zotsatira zake ndi
kuchulukana ku uzimu. Moti okhulupirira amachulukana mkati mwa mmimba umene ndi
mpingo.
Page 10
10
KUITANIDWA KU NTCHITO
Anthu amene Yesu anawaitana koyamba ngati akuphunzira ake anali asodzi. Anali anthu a
ntchito zawo. Samasodza nsomba zawo pakamodzi. Amagwiritsa ntchito maukonde a akulu
ndipo amapha nsomba zochuluka zosiyanasiyana.
Pamene Yesu anawaitana kuti akhale “asodzi a anthu,” amawaululira dongosolo la kuchulukana
ku uzimu. Ophunzira ake amayenera “kusodza” amuna ndi akazi kuchokera ku maiko onse,
zikhalidwe, ziyankhulo ndi mbali zonse za anthu. Maukonde awo a uzimu amayenera adzadze.
Yesu anaitanira anthu ku ntchito. Iye ananena kuti adzawapanga kukhala asodzi a wanthu.
Sadzakhala ozangoyang’anira ntchito dongosolo la Mulungu. Koma adzakhala otenga nawo
mbali pamene adzakhala akusodzera miyoyo ya muyaya ya amuna ndi akazi.
Kuitana kwa Yesu kukadali chimodzimodzi lero lino. Tikuyenera kukhala asodzi a anthu. Ngati
sitikusodza, ndiye kuti sitikutsatira.
ASODZI A ANTHU
Kodi ndi chifukwa chiyani Yesu adagwiritsa chitsanzo cha usodzi poitana ophunzira ake?
Koyamba, chifukwa choti chanali chitsanzo choti akanatha kuchimvetsa mwachangu. Anthu
amenenewa moyo wawo unali usodza. Moti kusodzaku chinali chinthu chimene amachipatsa
nthawi ndi mphamvu yawo. Pamene Yesu anawaitana kuti akhale asodzi a anthu, iwowo
anamvetsa kuti ayamba “kusodza” anthu ku uzimu, monganso mmene amasodzera nsomba
kudziko lapansi. Amatha kumvetsanso zimene zimafunika pa kuitanaku. Kusodza ku uzimu
kumafuna kupereka nthawi komanso mphamvu zawo.
Chachiwiri, Yesu anagwiritsa ntchito chitsanzo cha usodzi poitana ophunzira chifukwa pali
mfundo za kusodza kwa kuthupi kumene kutha kugwiritsidwa ntchito ku uzimu. Mfundozi ndi
izi:
MUKUYENERA KUPITA KUMENE KUMAPEZEKA NSOMBA:
Ngati mukufuna kusodza nsomba, mukuyenera kupezeka kumene nsomba zimapezeka. Nsomba
zimapezeka mmadzi. Simuzasodza nsomba pamene mukuzidikira pamwamba pa phiri kapena
mkatimkati mwa chipululu.
Monga wokhulupirira, mukuyenera kumene kupita kumene nsomba zili ku uzimu. Amuna ndi
akazi amakhala mdziko. Simungamadikirire mu mpingo kuti osakhulupirira akupezeni
Page 11
11
momwemo. Mukuyenera kupita kaya ndi pamsika, kusukulu, mmalo ogwiramo ntchito ndi
“kusodza” paliponse pamene pali anthu osapulumutsidwa.
MUKUYENERA KUZINDIKIRA MALO:
Pamene mukusodza ku dziko lapansi, ndi zofunikira kuganizirapo za malo. Mukuyenera
kuonetsetsa kuya kwa madzi pa nthawi imeneyo. Mukuyenera kudziwa kuti madziwo ndi
amchere kapene ayi. Mukuyenera kuonetsetsa mmene mphepo ikuombera. Zinthu zonsezi za
kudzikozi zimatha kukudziwitsani za mtundu wa ngalawa imene komanso njira zimene
mugwiritse ntchito pofuna kusodza.
Momwemonse kudziko lapansi. Mukuyenera kuzindikira malo anu amene mukapezeko amuna
ndi akazi. Kodi zosowa zawo ndi chani? Nanga zimene zikuchitika mmoyo wawo ndi chani? Izi
zidzakuthandizani kudziwa njira zimene mugwiritse ntchito posodza miyoyo yawo.
Pamene Yesu anakumana ndi mkazi pa chitsime ku Yohane 4, Anazindikira malo amene
anampeza iye. Mkaziyo amafuna madzi. Yesu anagwiritsa ntchito madziwo kuti adziwe chosowa
chake cha ku uzimu. Njira imene anagwiritsa ntchito “inamuululira” mu Ufumu wa Mulungu.
Mudzikoli ngati mukugwiritsa ntchito njira zosodzera mtundu wa nsomba umene umakhala
mmadzi amchere, simungasodze nsomba za mtundu umenewo chifukwa sizikhala mmadzi
amchere. Koma zimapezeka mmadzi a bwinobwino.
Ngati simuzindikira malo a mudziko la uzimu, muzapezeka kuti mukusodza mtundu wa nsomba
mmadzi amchere amene nsombazo sizikhalamo. Izi zili chonchi chifukwa simutha kumvetsa
kumene anthu amapezeka ndi mmene mungawafikirire.
MUKUYENERA KUGWIRTSA NTCHITO NJIRA ZOSIYANASIYANA:
Msodzi wabwino amagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zosodzera nsomba. Amagwiritsa
ntchito zakudya zosiyanasiya kuti athe kukopa nsomba. Amagwiritsanso zipangizo
zosiyanasiyana zophera nsomba monga zitsulo, maukonde, mikondo kapena madengu. Motero
nsomba zosiyana zimakopekanso ndi njira zosiyana zophera. Ichi ndi chifukwa chake nsodzi
ayenera kugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zophera nsomba.
Choncho nsodzi atha kuphunzira zina mwa njirazi mmabuku omwe amakamba za usodzi. Atha
kuphunzira njirz zina ndi zimene zimachitika komanso kuoneka zokhudza usodzi. Motero njira
zimene amagwiritsa ntchito zimasintha, koma cholinga sichimasintha ndiko kusodza nsomba.
Page 12
12
Choncho ngati muli nsodzi wa uzimu wochitachita, mukuyenera kugwiritsa ntchito njira
zosiyanasiyana. Chomwechonso anthu osiyanasiyana amakopeka ndi uthenga wabwino
wolalikidwa mu njira zosiyana. Ena amatha kuvulazidwa ndi uthenga wabwino pomwe ena
amatha kutonthozedwa ndi uthenga wabwino omwewo mu nthawi yosowa. Ena “amakhuzidwa”
ndi njoranzo zosiyanasiyana.
Njira za kusodza mu uzimu ndi zosiyananso, koma cholinga nthawi zonse chimakhala
chomwecho…ndiko kusodza miyoyo ya anthu.
MUKUYENERA KOPONYA NDI KUKOKA:
Kaya mukugwirtsa ntchito chitsulo chosodzera, ukonde, mkondo kumene mumasodza,
mukuyenera kuponya mmadzi ndi kukokanso kawiri.
Mu dziko lathuli, mmene mumaponyera ukonde mmadzi ndizofunuka ndithu. Kuponya kwanu
kukuyenera kukhala kwa chindunji. Mukuyeneranso kugwitsa ntchito chotengera kuti
musungiremo nsomba zanu mukasodza.
Mu dziko la uzimu, talonjezedwa kuti “ngati tiponya mawu a Mulungu” sadzabwerera chabe.
Adzakwaniritsa cholinga chimene chake mmitima ndi mmiyoyo ya anthu (Yesaya 55:11).
Pamene mugwiritsa ntchito mawu a Mulungu, mudzakhala chindunji nthawi zonse. Zotsatira
zake “azasodza” amuna ndi akazi.
MUKUYENERA KUDZIWA NTHAWI:
Nthawi ya tsiku ndi nyengo za pachaka zimakhudza usodzi mdziko lathu. Nsomba zina
zimathawa ndipo simungazisodze mmadera komanso mnyengo zina. Nsomba zambiri
zimasodzedwa kumayambiriro a tsiku pamene zikuyanndikira pamwamba pa madzi kuti zidye.
Ngati mukusodza mu nyengo yolakwika kapene mu nthawi yosayenera, simungasodze nsomba
zambiri.
Nthawi ndi yofunikira ngakhale ku usodzi wa ku uzimu. Muphunzira kutsogolo kwa phunziroli
za kufunika kwa “kusodza” malo olandirika a mdziko pamene nsomba “zimaluma” ku uzimu.
MUKUYENERA KUKHALA ODEKHA:
Munthu amene ndi nsodzi wa kudera lathu amayenera kukhala odekha. Amayenera kudikira
nsomba kuti zilowe mu ukonde. Momwemonse usodzi wa ku uzimu wa kudziko:
Page 13
13
Potero, lezani mtima, abale, kufikira kudza kwace kwa Ambuye. Taonani, wolima
munda alindira cipatso cofunikatu ca dziko, ndi kuleza mtima naco kufikira
cikalandira mvula ya myundo ndi masika (Yakobo 5:7).
KUCHULUKANA KU UZIMU
Kusodza kwa dziko lapansi kumachulukitsa nsomba. Kusodza kwa dziko la uzimu
kumachulukitsa anthu mu Ufumu wa Mulungu. Kuberekana kwa anthu kumachulukitsa
chiwerengero cha anthu. Kubalananso mu uzimu kumachulukitsa anthu ku uzimu.
Kuchulukana kwa umunthu ndi zotsatira za moyo. Kuberekana kwa ku uzimu ndi zotsatiranso za
moyo. Sizimabwera kudzera mu dongosolo la munthu ayi. Kuchulukana ku uzimu kumabwera
kudzera mmoyo wa uzimu ochokera kwa Mulungu.
Mu thupi la munthu, kubalana kumayamba mmimba mwa mkazi ndi dzila limodzi la moyo.
Dzilalo limachulukana ku “mimba” ya uzimu ya mpingo. Muphunzira za mmene kuchulukana
kwa ku uzimu kumayambira pamene mukuphunzira za “Tsiku la Zinthu Zochepa” mu chaputala
chikudzachi.
Page 14
14
MAYESO ODZIYETSA NOKHA
1. Lembani Vesi Lotsogolera kuchokera pamtima.
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
2. Kodi malamulo oyamba ndi otsiriza amene Yesu anapereka kwa ophunzira ake ndi ati?
___________________________________________________________________________
3. Kodi kuchulukana ndi chani?
___________________________________________________________________________
4. Kodi wokhulupirira amachulukana bwanji ku uzimu?
___________________________________________________________________________
5. Perekani tanthauzo la mawu oti “njira.”
___________________________________________________________________________
6. Perekani tanthauzo la mawu oti “ndondomeko za njira.”
___________________________________________________________________________
7. Longosolani kutanthauza kwa mawu awa “ndondomeko za njira zochulukana ku uzimu.”
___________________________________________________________________________
8. Ombani mkota pa za mfundo usodzi wa kudziko umene umapereka tanthauzo la usodzi
wa ku uzimu.
___________________________________________________________________________
(Mayankho a mafunsowa akupezeka kumapeto kwenkweni kwa bukuli).
Page 15
15
KUPITILIZA KUPHUNZIRA
Maitanidwe a Yesu ochulukana ku uzimu si oti munthu atha kusankha kapena kuganizira.
Ndi lamulo ndithu. Werengani tchatili limaene likufananitsa kutuma kwakukulu kumene
Baibulo limakamba. Onani mavesi onse mu Baibulo lanu. Onaninso ulamuliro umene
mulinawo kuti mukwaniritse lamulolo. Onetsetsani kukula kwake kwa utumiki wanu,
uthenga wake, ndi ntchito zimene mukuyenera kuchita mkatikati mochulukana.
Mabuku Ulamuliro Kukula kwake Uthenga Ntchito
Mateyu Ulamuliro Mitundu yonse Zinthu zonse Kupanga
28:1-20 onse zimene Yesu ophonzira
Analamulira pa kupita,
Kubatiza
kuphunzitsa
Marko Dzina la Dziko lonse Uthenga Mukani
16:15 Yesu kwa zolengedwa wabwino mukalalikire,
Zonse kuchiritsa
odwala
Luka Dzina la Mitundu yonse Kulapa kulalikira
24:46-49 Yesu kuyambira Kukhululukidwa kulengeza
Yerusalemu machimo kuchita umboni
Yohane otumidwa ndi (Kukula kwa utumiki, uthenga, ndi ntchito ndi zofanana
20:21 Yesu monga monga ngati Yesu).
Otumidwa ndi
Atate
Machitidwe Mphamvu ya Yerusalemu Mkhristu Mboni
1:8 Mzimu Woyera Yudeya, Samaria
Ndi malekezero a
Dziko lapansi
Page 16
16
CHAPUTALA CHA 2
TSIKU LA ZINTHU ZOCHEPA
ZOLINGA:
Pakutha pa chaputalachi muyenera:
Kulemba Vesi Lotsogolera kuchokera pamtima.
Kuomba mkota pa za mfundo za kuchukukitsa.
Kudziwa mitundu ya kukula mu uzimu.
Kulemba mndandanda wa mavesi amene amasonyeza kuti kuchukana ndi za Malemba.
Kudziwa zinthu zimene zimaulula zolakwika zokhuza kukula mu chiwerengero.
VESI LOTSOGOLERA:
Pakuti wapeputsa tsiku la tinthu tating'ono ndani? (Zakariya 4:10).
MAWU OYAMBA
Kukula mu thupi la munthu kumayamba ndi dzira limodzi la moyo zimene ndi zotsatira za ubale
waukulu pakati pa mkazi ndi mamuna. Dziralo limachulukana mkati mwa mmimba ya mkazi
kufikira munthu wina amalengedwa. Pamene chakhwima, munthu watsopanoyi amakhalanso ndi
kuthekera kochulukana.
Kukula ku uzimu kumayamba ndi ubale wa pakati pa munthu ndi Ambuye Yesu Khristu. Moyo
wa uzimu umalowa mkati mwa moyo ndi mzimu wa munthu amene walandira Yesu ngati
mpulumutsi. Malawi a moyo, utetezedwa mkati mwa mimba ya uzimu ya mpingo, umakula
kufikira wophunzira watsopano amalengedwa. Wophunzira ameneyi amakhalanso ndi kuthekera
kubadwisa ku uzimu potsogolera enanso kwa Ambuye Yesu Khristu.
Palibe kanthu ndi kudziko la kuthupi kaya la ku uzimu, kuchulukana kumayamba ndi chithu
chimodzi chamoyo ngati dzira. Izi ndi zimene Mulungu ananena:
Pakuti wapeputsa tsiku la tinthu tating'ono ndani? (Zakariya 4:10).
Muchaputala ichi muyamba ndi zinthu zazing’ono. Muphunzira mfundo zenizeni za kuchulukana
ndi mitundu ya kukula mu uzimu. Muphunziranso chidwi cha Mulungu pa kuchulukana kwa ku
uzimu ndi zinthu zina zimene zimaonetsa maganizo olakwika pa kukula mu chiwerengero.
Muyamba ndi mfundo zenizeni, zinthu zochepa zimene zazikulu zimachokerapo.
Page 17
17
MFUNDO ZENIZENI ZA KUCHULUKANA
Mukuyenera kumvetsa mfundo zenizeni za kuchulukana ku uzimu kuti muthe kuphunzira ndi
kugwiritsa ntchito ndondomeko za njira zake. Mfundo za kuchulukana sizimasintha, komano
njira zimene mumagwiritsa ntchito ndi zimene zimasintha. Njira zimasintha, koma cholinga
chimakhala chomwecho chomwecho sichimasintha.
Cholinga komanso mfundo za Mulungu nthawi zonse zimakhala zomwezo, koma njira zofikira
zolingazi zimasintha. Cholinga cha Mulungu kuchokera pachiyambi chakhala….
...Kuti pa tinakonzedwe a makwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi
zonse mwa Kristu, za kumwamba, ndi za padziko (Aefeso 1:10).
Monga moyo wawo wa uzimu wa anthu ake ndi masinthidwe a mbiri ya nyengo za amitundu,
Mulungu amasintha njira zake monga zifunikira kuti akwaniritse cholinga chake. Mwachitsanzo,
pamene atate mbanja la Israyeli analephera ntchito yawo ku uzimu, Mulungu anadzutsa
ansemba. Pamene ansembe anayamba za chinyengo, anaitana aneneri kukhala ngati atsogoleri a
kuuzimu.
Yesu anagwiritsa ntchito njira zosiyana za utumiki. Sanathandize anthu onse mofanana. Njira
zake zinali zosiyana, koma cholinga chake chinali sichinasinthe ndiko …Kukhudza ndi kusintha
miyoyo ya anthu.
Izi ndi zina mwa mfundo zenizeni zimene mukuyenera kudzimvetsa mu “tsiku la zinthu
zochepa” musanayambe kuchulukana:
MULUNGU AMAKHALA NDI CHIDWI NDI GULU LA ANTHU:
Chidwi cha Mulungu nthawi zonse chakhala pa dziko lonse:
Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace
wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nao moyo
wosatha (Yohane 3:16).
Mulungu….
...wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa (II Petro 3:9).
Yesu anaonetsa chidwi chomwecho pamene anati:
Page 18
18
Pakuti Mwana wa munthu anadza kufunafuna ndi kupulumutsa, cotayikaco (Luka
19:10).
…pakuti sindinadza kudzaitana olungama, koma ocimwa (Mateyu 9:13).
Mulungu amakhuzidwa ndi gulu la anthu. Amakhuzidwanso ndi chiwerengero. Komanso
amkhuzidwa ndi kuchulukana kwa okhulupirira amene amachulukana pa kulalikira uthenga
wabwino. Pamene mukuyamba phunziro la njira zochulukitsa, muyamba ndi chidwi chomwecho
ngati Mulungu—amene akufikira dziko lonse ndi uthenga wabwino.
NDI MULUNGU AMENE AMABWERETSA KUKULA:
Kuchulukana mu uzimu sikungakwaniritsidwe popandapo Mulungu. Mulungu ndiye amene
amabweretsa kukula:
…kama Mulungu anakulitsa (I Akorinto 3:6).
MUNTHU AYENERA KUGWIRIZANA NDI MFUNDO ZA MULUMGU:
Mmawu mulu mfundo za Mulungu zimene zimagwiritsidwa ntchito mmagawo onse a moyo ndi
utumiki wathu. Mulungu amagwira ntchito kudzera mwa anthu amene amadziwa kugwiriza ndi
mfundozi. Kuchokera pa chiyambi cha dziko lapansi, Mulungu wakhala akugwira ntchito
padzikoli kudzera mwa anthu. Adampatsa Adamu ndi Hava ntchito yosamalira munda.
Anagwiritsa ntchito munthu wotchedwa Nowa kuti ateteze moyo pa dziko munthawi ya
chigumula cha madzi.
Mulungu anadzutsa Abrahamu kukhala woyamba wa mtundu wa Israyeli umene kudzera mwa
iye anadziululu yekha kwa mitundu ina ya dziko lapansi. Mulungu anagwiritsanso ntchito
aneneri, mafumu ndi oweruza kuti akwaniritse cholinga chake mu nthawi ya Chipangano
Chakale.
Muchipangano Chatsopano, munthu wotchedwa Yohane Mbatizi, “anakonzekeretsa njira ya
Ambuye.” Yesu anayamba utumiki wake ndi anthu wamba ndipo pamene anabwerera
kumwamba adasiya tsogolo lake la Uthenga wabwino mmanja mwa akuphunzira ake. Nkhani
yonse ya Mbaibulo ndi imodzi ya kwa munthu amene akugwirizana ndi mfundo za Mulungu ndi
cholinga chofuna kufikira cholinga chake.
Izi ndi zoona mu kuchulukana kwa ku uzimu. Mulungu samusiya munthu kumbali kuti afalitse
mau ake. Amagwiritsa ntchito anthu amene amavetsa ndi kugwirizana ndi mfundo zake za
kuchulukana. Paulo anaomba mkota za mgwirizano wa ubalewu:
Page 19
19
Ndinanka ine, anathirira Apolo; kama Mulungu anakulitsa (I Akorinto 3:6).
Paulo anatsindika za change cha okhulupirira kukwaniritsa udindo wawo mu dongosolo la
Mulungu.
Pakuti, amene ali yense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka. 14Ndipo iwo
adzaitana bwanji pa iye amene sanamkhulupirira? ndipo adzakhulupirira bwanji
iye amene sanamva za iye? ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira? Aroma
(10:13-14).
YESU NDIYE MASO ATHU A KUCHULUKITSA:
Yesu anati:
Ndipo Ine, m'mene ndikakwezedwa kudziko, ndidzakoka anthu onse kwa Ine
ndekha (Yohane 12:32).
Yesu apapa amalankhula za “kukweza pamwamba” pa mtanda pamene anafera zochimwa za
anthu onse. Kupyolera mu imfa yake, adzakoka anthu onse mwa mphamvu ya uthenga wake.
Pamene mugawira anthu uthenga wabwino, Yesu amakwezedwa pamwamba. Pamene
wakwezedwa mmoyo wanu ndi mumpingo wanu, anthu amaitanidwa ndi mphamvu ya uthenga
wabwino. Kuchulukanatu ndi kotheka ngati Yesu wakwezedwa pamwamba.
MAWU A MULUNGU AMAYAMBITSA KUKULA:
Yesu anafotokozapo za fanizo la kukula mu Mateyu 13:1-9. Analongosola fanizolo kuyambira
Mateyu 13:18-23. Werengani ndimeyi mu Baibulo lanu. Mu fanizoli, mbewu zimaimira Mau a
Mulungu. Mulungu analonjeza kuti pamene tabzala Mau ake, sadzapita pachabe.
Momwemo adzakhala mau anga amene aturuka m'kamwa mwanga, sadzabwerera
kwa Ine cabe, koma adzacita cimene ndifuna, ndipo adzakula m'mene
ndinawatumizira (Yesaya 55:11).
…Waona bwino pakuti Ine ndidzadikira mau anga kuwacita (Yeremiya 1:12).
Mawu a Mulungu ndiwo amene amabweretsa kusintha mmiyoyo ya anthu. Kusinthako
kumabweretsa kukula komanso kuchukukana molingana ndi Mau a Mulungu.
MZIMU WOYERA AMABWERETSA KUCHULUKANA:
Page 20
20
Mu unthenga wake otsiriza wa Yesu kwa ophunzira ake anati:
Komatu mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala
mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira
malekezero ace a dziko (Machitidwe 1:8).
Mphamvu ya Mzimu Woyera ndi imene imapangitsa kuchulukana. Mphatso za Mzimu Woyera
zimakonzekeretsa kuchulukana. Chipatso cha Mzimu Woyyera chimapangitsa kuberekana.
Tisanthula nchito ya Mzimu Woyera mu kuchulukana kwa ku uzimu kumapeto kwa phunziroli.
KUCHULUKANA NDI UDINDO WOTHANDIZANA:
Mu nthawi ya mpingo woyamba, kufalikira kwa uthenga wabwino sikunali kwa azibusa, aneneri,
alaliki, ndi aphunzitsi amene anali ndi mipingo yawo ayi. Okhulupirira wina aliyense wa
Chipangano Chatsopano amachulukana ku uzimu. Ngati tikufuna tifikire dziko ndi uthenga
wabwino tikuyenera kuchita ngati mpingo woyamba. Kuyambira atsogoleri ndi anthu wamba
akuyenera kugawana udindo wa kuchulukana ku uzimu. Kukula kwa dziko mu chiwerengero
kukufunika membala wina aliyense amene ali mu thupi la Khristu kubwerera ku dongosolo la
utumiki wa mu Chipangano Chatsopano. Sitingafikira dziko lapansi ndi kumangodzionetsera
kapena kudzipereka mosakwanira.
Pali ndithu akhristu okwanira mu dziko lapansi amene angathe kufikira dziko lonse lapansi ndi
uthenga wabwino. Koma amene akusowa ndi chiwerengero chokwanira cha akhoza kukhudzika
ndi kuvomera mwayi wa kuchulukana.
Lamulo limene linaperekedwa ndi Yesu kwa okhulupirira loti “mukani” kudziko lonse ndi
uthenga wabwino. Simukuyenera kudikira lamulo loti “mukani” chifukwa linaperekedwa kale.
Mogwirizana ndi uthenga wabwino, lamulo ndi lakuti “mukani” ndipo penyetsetsani zoletsa,
osati kusiya ndi kudikira “kumuka.”
MITUNDU YA KUKULA
Baibulo limatiuza za mitundu inayi ya kukula kapena kuchulukana:
KUKULA MU MADERA:
Kukula kumeneku kunaloseredwa kale ndi Ambuye Yesu:
Page 21
21
Komatu mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala
mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira
malekezero ace a dziko (Machitidwe 1:8).
Kukula kukuyenera kufikira ngakhale madera a mitundu yonse ya dziko lapansi.
KUKULA MU CHIWERENGERO:
Mpingo ukuyenera kukula mu chiwerengero pamene ukukula mmadera. Kukula mu
chiwerengero kwa mpingo kumapezeka mu buku la Machitidwe. Mwachitsanzo, mpingo unakula
kuchokera 12 kufika 120 Machitidwe 1:15, mkuzafika 3,000 Mchitidwe 2:41 ndi kuzafika 5,000
Machitidwe 4:4.
KUKULA KU MITUNDU:
Mpingo woyamba unakulanso ku mitundu. Uthenga wabwino unafalikira kupitilira Ayuda
mpaka amitundu (anthu a mitundu yonse).
KUKULA KU UZIMU:
Kukula mu chiwerengero si ndiye kuti ndi kukuchukana ku uzimu. Pamene mukuphunzira
phunziroli, kukula ku uzimu kwa mkati ndikofunikiranso. Otsatira a Yesu akuyenera kukula mu
makhalidwe a uzimu momwemonso mu chiwerengero.
Koma kulani n'cisomo ndi cizindikiritso ca Ambure wathu ndi Mpulumutsi Yesu
Khristu (II Petro 3:18).
Khumbo la Mulungu ndi loti…
Koma ndi kucita zoona mwa cikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira iye amene ali
mutu ndiye Kristu (Aefeso 4:15).
KUSINDIKA ZA CHIWERENGERO
Anthu ambiri amakana nkhani ya kuchulukana ku uzimu ndi kukula kwa mpingo chifukwa
amakhulupirira kuti kumakamba za chiwerengero ndi zolakwika. Komatu Mbaibulo muli mawu
ambiri amene amakamba za chiwerengero. Mwachtsanzo onani Numeri 1:1-3; 2:23-24; 26:1-4;
Chibvumbulutso 7:9; 20:8; Genesis 22:17; ndi Ahebri 6:14.
Page 22
22
Yesu analankhulapo za mafanizo ambiro okhuza kukula mu chiwerengero. Muziphunzira
zimenezi mu phunziro lina. Anaonetseranso kuti kukula kwenikweni kwa chiwerengero
kunalembedwa Kumwamba:
Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala cimwemwe Kumwamba cifukwa ca wocimwa
mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anai
mphambu asanu ndi anai, amene alibe kusowa kutembenuka mtima (Luka 15:7).
Kuchulukanaku kumapezekanso mu mbiri ya mpingo mu buku la Machitidwe. Chidule cha
kukula kwa mpingo kumapezeka mu buku la Machitidwe monga 1:15; 2:41; 4:4; 6:7; 9:31;
12:24; 16:5; 19:20; ndi 28:30-31.
Simukuyanera kukana nkhani ya kuchulukana chifukwa cha mavuto ochepa amene apezeka
chifukwa cha maganizo olakwika a zakuchulukana. Komano, mukuyenera kudziwa ndi kuthana
ndi mavutowo. Pali kuganiza kolakwika pa nkhani ya kuchulukana pamene zinthu izi
zikupezeka:
KUKULA MU CHIWERENGERO NKOFUNIKA KUPOSA KUKULA MU UZIMU:
Pamene kukula mu uzimu kwaleka kukopa gulu la anthu, pamakhala kulakwa kolankhulano za
chiwerengero. Atumiki ambiri amalankhula zimene anthu amazikonda kuzimva ndi cholinga
chofuna kukopa khamu lambiri. Koma Baibulo limachenjeza kuti…
Pakuti idzafika nthawi imene sadzalola ciphunzitso colamitsa; komatu poyabwa
m'khutu adzadziuniikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha: ndipo
adzalubza dala pacoonadi, nadzapatukira kutsata nthanu zacabe (II Timoteo 4:3-4).
KUDZIKWEZA KUMATSOGOLA:
Werengani I Mbiri 21:18. Chidwi cha Davide pa chiwerengero chimogozana ndi Satana ndipo
unali mchitidwe wa kudzikudza. Pamene muyamba kusangalala ndi khamu lalikulu la anthu,
ndiye kuti chidwi chanu ndi cholakwika.
KUDZIYENEREZA KUMAKHALAPO:
Pali tchimo la kuthupi limeme pa Agalatiya 5:20 amalitcha kuti “kudzidierekeza” kumene ndi
mchitidwe wa ngati nsanje, umene zotsatira zake ndi kuzifanizira ndi anthu ena pa nkhani ya
chipambano. Pamene muli a nsanje chifukwa cha mautumiki a pamwamba ndi kuyamba
kumazifanizira ndi ena ndi cholinga choti mukule, ndiye kuti muli ndi maganizo pa nkhani ya
chiwerengero.
Page 23
23
CHIDWI CHIMAKHALA PA KUKULA KWA MPINGO MMALO MWA UFUMU WA
MULUNGU
Cholinga cha kuchulukana mu uzimu ndiko kutembenuza anthu anthu kupita kwa Yesu Khristu
ndi kuyamba kuwaphunzitsa kufikira akhala anthu odalilika, ndi wochitachita mu ufumu wa
Mulungu. Pali kusiyana pakati pa kukula kwa mpingo ndi kukula kwa ufumu. Ngati mpingo
woyamba ugawanika ndipo 100 mwa mamembala awo akupita ku mpingo wachiwiri, ndiye kuti
kukula kwa mpingo kwachitika mu mpingo wachiwiri, koma palibe kukula kwa Ufumu.
Kuchulukana sikunachitike. Kwangokhala kusinthana kwa mamembala omwe analipo kale.
Cholinga cha kuchulukana si kukopa mamembala atsopano kuchoka mu mpingo wina, koma
kufikira iwo amene sanamve uthenga wabwino. Kuika chidwi pa chiwerengero ndi zolakwika
pamene cholinga cha kukula kwa mpingo chikusinthana ndi kukula kwa Ufumu.
MUNTHU MMODZI AMAKANIDWA:
Yesu anatumikira kwa anthu ambiri panthawi ya utumiki wake (Luka 6:17; 7:11; 8:37; 9:14-16;
14:26; 23:27; Yohane 6:2). Koma Yesu sanakane munthu ngakhale mmodzi chifukwa cha
khamu la anthu. Amaitana anthu ngakhale pakati pa khamu la anthu ndi kuwatumikira (Yohane
5:3-13; Marko 5:24-34). Mu Yohane 4, anatumikira kwa mkazi mmodzi amene pamapeto pake
anabweretsa khamu la mudzi wonse kwa Yesu.
Ku machitidwe 8 pali nkhani ya chitsitsimutso chachikulu chimene analalikira Filipo mu mzinda
wa Samariya. Mkatikati mwa mikumano yawo Mulungu analankhula kwa Filipo kuti achoke ku
Samariya ndi kupita ku chipululu pakati pa Yerusalemu ndi Gaza.
Filipo mwachangu anachoka mkusiya chitsitsimutso chachikulu chimene amatumikira.
Anachoka kudziko kumene kunali anthu ambiri pamodzi mkupita kumalo ayekha. Annsiya
khamu ndi cholinga chofuna kutumikira munthu mmodzi, mdindo wa ku Itopiya amane
amachokera ku Yerusalemu. Munthuyi mkutheka anali ndi kuthekera kofalisa uthenga wabwino
mu mbali yonse ya Afilika.
Zaka zambiri zapitazo ku Mangalande pa ntchito ya umishoni anthu awiri okha ndi amene
amapezeka chifukwa cha nyengo yoipa. Mtumiki woyitanidwayo amayesera kupempha
Achimwenye amane amkagwira ntchito kummawa kwa Amerika, koma anaganiza kuti
amaononga nthawi chifukwa cha kuchepa kwa anthu. Koma mmodzi wa anthu awiriwa anamva
kuitana kwa Mulungu ndipo anapereka moyo wake kwa Mulungu. Mwezi usanathe anagulitsa
malonda ake ndipo amakonzeka kukagwira ntchito kwa Amwenye kummawa kwa Amerika.
Anakhalako zaka 35 akuchita utumiki pakati pa athuwa. Dzina lake linali David Brainard.
Page 24
24
Musanyoze zinthu zochepa. Kumbukirani, kuwala kochepa kungawale kuposa mmene dzuwa
limawalira…kukhoza kuwala usiku.
CHIDWI CHIMACHOKA PA ANTHU MKUKHALA PA ZINTHU:
Pamene kuchulukana kwabweretsa kukula kwa mpingo, chidwi chathu nthawi zambiri
chimachoka pa anthu mkupita pa zinthu. Chifukwa cha kukula, mamangidwe a mpingo waukulu
amafunika ndipo zochita zimachoka pa kuchulukitsa ophunzira mkupita pa mamangidwe a
mpingo. Pamene chidwi chanu chachikulu chili pa mamangidwe ndi cholinga chofuna kukhala
ndi anthu ambiri, chiwerengero chimapangitsa inu kuiwala cholinga chanu chenicheni.
Mulungu amakhuzidwa kwambiri ndi anthu kuposa mamangidwe. Mbiri ya Baibulo ya ntchito
ya Mulungu mdziko imakhala pa anthu. Pamene kuchuluka kwapangitsa kuchotsa chidwi pa
anthu mkuika pa zinthu monga mamangidwe, ndiye kuti zimenezi ndi zolakwika.
ENA AMAWERUZIDWA POYANG’ANA CHIWERENGERO:
Sibwino kuweruza uzimu wa munthu wina kapena utumiki poyang’ana chiwerengero. Khamu
lanthu si chizindikiro cha uzimu. Chipambano mu chiwerengero nthawi zina si umboni oti
mpingo walephera kukhala mpingo. Nthawi zina, kukhulupirika ku Mau a Mulungu ndipo Yesu
Khristu amabweza osati kukopa. Mwachitsanzo, pamene Yesu anayamba kuphunzitsa uthenga
wosatchuka wa imfa yake, ambir amene amamutsata Iye amasiya kumutsata (Yohane 6:52-64).
Pali zifukwa zina zimene zimapangitsa kuti kukula kusaoneke. Baibulo limaphunzitsa kuti pali
nyengo zina za kukula mu zimu monganso pali kukula kwa zinthu ku dziko. Mu dziko lathuli,
nyengo zina za chaka zomera sizimaberekana. Zimakhala opanda masamba kapena zipatso
mkumaoneka ngati nthambi zokufa pa nthaka. Koma mu nyengo yoyenera, zomerazi
zimaberekana moti masamba komanso zipatso zimaonekera.
Momwemonso kudziko la uzimu. Pali nthawi zina pamene malo ena mdzikomu amalandira
uthenga wabwino kuposa malo ena. Pa kudziwa ndandandawu wa kakulidwewu mukhoza kuika
chidwi pa zochita zanu za moyo wa uzimu mmunda “kupsa mkukolora.”
Ndondomeko za chiwerengero cha Mulungu sizifanana ndi za munthu. Tipaphatikiza kuti
tichukulukane. Koma nthawi zina Mulungu amachotsera ndi cholinga chofuna kuchulukana.
Pamene Hananiya ndi Safira anachotsedwa mu mpingo chifukwa cha uchimo (Machitidwe 5),
okhulupirira anaonjezeredwa (Machitidwe 5:14). Nthawi zina Mulungu amagwiritsa ntchito
mgawano pofuna kuchulukitsa. Pamene Paulo ndi Banaba anagawana, Mulungu anachulukitsa
mphamvu ya umishoni (Machitidwe 15:36-41). Nthawi zambiri Mulungu amachepetsa
Page 25
25
chiwerengero ndi cholinga chofuna kukwaniritsa cholinga chake chachikulu. Werengani nkhani
ya Gideoni mu Oweruza 7.
Musaweruze utumiki kapena munthu poyang’ana chiwerengero. “Osapeputsa zinthu zochepa.
Pamene mnyamata anapereka mkatendi nsomba ziwiri kwa Yesu, zinafikira chosowa cha khamu
la anthu amene anali ndi njala. Mulungu amagwiritsa ntchito zinthu zonyozeka, mkuzidalitsa, ndi
kudzigwiritsa ntchito ku ulemerero wa dzina lake.
ZOTSATIRA ZAKE NDI KUBWERETSA KHOLOLA
Pokana maganizo olakwikwa otsindikiza za chiwerengero zisalepheretse maphunzirowa ndi
kugwiritsa ntchito njira za kuchulukutsa. Fanizo la (Mateyu 25:14-30) likuonetseratu kuti
Mulungu amayembekezera inu kuti muchulukane ndi zimene mwapatsidwa choncho kukhala ndi
madandaulo chifukwa cha mantha sizoloredwa.
Kodi simunena inu, kuti, Yatsala miyezi inai, ndipo kudza kumweta? Onani
ndinena kwa inu, Kwezani maso anu, nimuyang'ane m'minda, kuti mwayera kale
kufikira kumweta (Yohane 4:35).
Pamene Mulungu atumiza okolola mmunda wa uzimu ku dziko, amafuna iwo abwere ndi kholola
osati madandaulo:
Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kupfuula mokondwera.
Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa;
Adzabweranso ndithu ndi kupfuula mokondwera, alikunyamula mitolo yace
(Masalmo 126: 5-6).
Page 26
26
MAYESO ODZIYETSA NOKHA
1. Lembani Vesi Lotsogolera kuchokera pamtima.
___________________________________________________________________________
2. Lembani mfundo zenizeni za kuchulukitsa zimene mwaphunzira mu phunziroli.
___________________________________________________________________________
3. Tchulani mitundu inayi ya kukula mu uzimu.
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
4. Lembani mavesi amene amaonetsa chidwi kuti kuchulukana ndi zochokera Mmalemba.
___________________________________________________________________________
5. Lembani mwachidule zinthu zimene mwaphunzira zosonyeza kuganiza kolakwikwa pa
kukula mu chiwerengero.
________________________________________________________________________
6. Zoona kapena Zonama: ngati chiganizo chili choona, lembani “zoona” mumpata
koyambirira kwa chiganizo. Ngati chiganizo chili chonama, lembani “zonama mumpata.
a. _______________Amaika chidwi pa chiwerengero si za Mmalemba.
b. _______________Ngati mpingo sukukula, ndiye kuti uzimu palibe.
(Mayankho a mafunsowa akupezeka kumapeto kweikweni kwa bukuli).
Page 27
27
KUPITILIZA KUPHUNZIRA
Buku la Machitidwe limatiuza nkhani ya kuchulukana kwa mpingo woyamba. Gwiritsani ntchito
magawowa kuti muphunzire bukuli la Chipangano Chatsopano. Magawowa amatsata dongosolo
la kuchulukana la Ambuye limene limnaperekedwa pa Machitidwe 1:8 pa za kufalitsa uthenga
wabwino kuchokera ku Yerusalemu, kupita ku Yudeya, Samariya, ndi malekedzero a dziko
lapansi.
Wolemba buku: Luka
Kumene amalembera: Bukuli amalembera okhulupirira onse, ngakhale amalembera kwa
munthu wotchedwa Tiofelo.
Cholinga chimene amalembera buku: Ichi chikupezeka mu Machitidwe 1:1-2. Bukuli limaika
chidwi pa zimene Yesu anapitiliza kuchita ndi kuphunzitsa atangokwera kupita kumwamba mu
thupi lake la uzimu, ndiye Mpingo.
Vesi Lotsogolera: Machitidwe 1:8
Mawu oyamba
Machitdwe 1:1-11
I. Mawu oyamba: 1:1-2
A. Kwa: Teofelo: 1:1
B. Okhuzana: Zimene Yesu adapitiliza kuchita ndi kuphunzitsa atangopita kumwamba
mu thupi lake la ulemerero, Mpingo: 1:1-2
II. Utumiki wa Yesu atatha kuukitsidwa: 1:3
A. Masiku ake: Makumi anayi: 1:3
B. Cholinga chake: Zitsikimizo zosakaikitsa: 1:3
C. Uthenga wake: Ufumu wa Mulungu: 1:3
III. Mkumano wotsiriza wa Yesu ndi akuphunzira ake: 1:4-8
Page 28
28
A. Lamulo la ophunzira: 1:4-5
B. Funso la ophunzira: 1:6
C. Chenjezo kwa ophunzira: 1:7
D. Kutuma ophunzira: 1:8
IV. Kukwera kwa Yesu kupita kumwamba: 1:9-11
A. Kulongosola za kukwerako: 1:9
B. Kulengeza za kubwera kwake kwachiwiri: 1:10-11
Gawo Loyamba:
Kupanga mboni ku Yerusalemu
Machitidwe 1:12-7
I. Kukonzekeretsa mboni: 1:12-2:4
A. Ophunzira aYesu kudikirira ku Yerusalemu: 1:12-26
1. Kusonkhana kwa ophunzira: 1:12-15
a. Malo awo okumaniranapo: 1:12-13
b. Chiwerengero chawo ndi mayina awo: 1:13-15
c. Cholinga chawo: 1:14
2. Chilimbikitso chopita kwa ophunzira: 1:15-22
a. Wolankhula: Petulo: 1:15
b. Uthenga 1:16-22
(l) Chiyambi: 1:16-20
(2) Malangizo: 1:21-22
3. Yankho la akuphunzira: 1:23-26
a. Maina oti asankhidwe: 1:23
b. Pemphero: 1:24-25
c. Maere: 1:26
B. Ubatizo mwa Mzimu Woyera: 2:1-4
1. Mmene zinakhalira: 2:1
2. Anthu: 2:1
3. Malo ake: 2:1
4. Chochitikacho: 2:2-4
a. Mphepo: 2:2
Page 29
29
b. Malilime a moto: 2:3
c. SKulankhula: 2:4
Gawo Lachiwiri: Ntchito yochitira umbini ku Yerusalemu
Machitdwe 2:5-7
I. Mboni zoyamba: 2:4-40
A. Mmene umboni unaperekedwera: 2:4-6
B. Zotsatira za umboni: 2:7-13
C. Ulaliki wa Petulo: 2:14-36
1. Uneneri wokhuzana ndi nthawi: 2:17
2. Uneneri wokhuzana ndi mzimu: 2: 17-18
3. Uneneri wokhuzana ndi chochitikacho: 2:19-20
4. Uneneri wokhuzana ndi chipulumutso: 2:21
5. Ntchito ya Yesu: 2:22-36
a. Yesu adatsimikizidwa ndi Mulungu: 2:22
b. Yesu adapachikidwa: 2:23
c. Yesu adauka kwa akufa: 2:24-32
d. Yesu adakwezedwa pa dzanja lamanja la Mulungu: 2:33-35
e. Yesu ndi Mbuye ndi Khristu: 2:36
D. Zotsatira atamva uthenga: 2:37-40
1. Kutsutsika: 2:37
2. Kufunsa: 2:37
3. Langizo: 2:38
4. Malonjezo: 2:38-39
5. Chilimbikitso: 2:40
II. Mpingo woyamba: 2:41-47
A. Chiwerengero cha anthu mu mpingo woyamba: 2:41
1. Chizindikiro chawo: Iwo amene adalandira Mawu.
2. Chiwerengero chinali: Zikwi zitatu 3,000
B. Makhalidwe a Uzimu a mpingo woyamba: 2:42
1. Chiphunzitso cha atumwi.
2. Chiyanjano cha oyera mtima.
3. Mgonero.
4. Pemphero.
C. Chikhalidwe cha mpingo woyamba: 2:44-46
Page 30
30
1. Machitdwe awo a moyo watsiku ndi tsiku: 2:44-45
2. Kulambira ndi kuchitira umboni tsiku ndi tsiku: 2:46
3. Kuchita chiyanjano mmanyumba: 2:46
4. Umodzi: 2:46
D. Umboni wa mpingo watsopano: 2:46-47
1. Chikhalidwe cha umboni: 2:46-47
2. Zotsatira za umboni: 2:47
III. Chozizwa choyamba: 3:1-26
A. Mmene chozizwa chinalili: 3:1-11
1. Malo ake: 3:1
2. Munthu ndi chosowa chake: 3:2-3
3. Uthenga: 3:4-6
4. Chozizwa: 3:7-8
5. Zimene khamu linachita: 3:9-11
B. Kulongosola chozizwa: 3:12-18
1. Munthuyo sanachiritsidwe ndi mphamvu ya atumwi: 3:12
2. Munthuyo anachiritsidwa ndi Mulungu kuti apereke ulemerero kwa Yesu:
3:13-15
3. Munthuyo anachiritsidwa mwa chikhulupiriro mdzina la Yesu: 3:16
4. Munthuyo anachiritsidwa kuti akaonetsere kukwaniritsidwa kwa uneneri:
3:17-18
C. Uthenga wa Petulo: 3:19-26
1. Lonjezo limene Petulo adalinena: 3:19-21
a. Chimene Mulungu adatsimikizira Israyeli kuchita: 3:19
b. Chimene Mulungu adalonjeza kuchita: 3:19-21
2. Uneneri wa aneneri: 3:22-26
a. Uneneri wa Mose ndi aneneri: 3:22-24
b. Lonjezo la pangano: 3:25
c. Dongosolo la Mesiya: 3:26
IV. Chitsutso choyamba: 4:1-31
A. Kumangidwa: 4:1-4
1. Choyambitsa chitsutso: 4:1
2. Cholinga cha chitsutso: 4:2
3. Mtundu wa chitsutso: 4:3
Page 31
31
B. Kuyesedwa: 4:5-14
1. Kubwalo la milandu: 4:5-6
2. Mafunso akubwalo la minlandu: 4:7
3. Mawu a Petulo: 4:8-12
a. Maziko a yankho lake: 4:8
b. Yankho lake: 4:9-10
c. Umboni wake wa Yesu: 4:10-12
d. Chilengezo chake cha chipulumutso: 4:12
4. Umboni wa oweruza milandu: 4:13-14
a. Chikhalidwe cha umboni: 4:13
b. Umboni wa munthu amene anachiritsidwa: 4:14
5. Chisankho: 4:15-22
a. Kufuna uphungu: 4:15-17
b. Chisanhko: 4:17-18
c. Yankho la Petulo ndi Yohane: 4:19-20
d. Kumasulidwa: 4:21-22
6. Zimene adachita: 4:21-31
a. Pemphero la mpingo: 4:23-30
b. Ntchito ya mpingo: 4:31
V. Mwambo oyamba wa tchimo: 4:32-5:16
A. Dongosolo la mpingo: 4:32-37
1. Chiyanjano chake: 4:32
2. Umboni wake: 4:33
3. Chuma chake: 4:32-37
B. Tchimo loyamba ndilo loononga chiyanjano: 5:1-10
1. Tchimo: 5:1-2
2. Kuonekera poyera kwa tchimo: 5:3-4
3. Mwambo wake wa tchimo: 5:5-10
C. Zotsatira za mwambo: Umboni wobala chipatso wa chiyanjano: 5:11-16
1. Malingaliro a mantha a mamembala: 5:11
2. Umodzi: 5:12
3. Zozizwa: 5:12, 15-16
4. Zomwe anthu adachita: 5:12-14
Page 32
32
VI. Chizunzo choyamba: 5:17-43
A. Maziko a chitsutso: 5:17
B. Zotsatira za chitsutso: 5:18
C. Chiombolo cha Mulungu: 5:19-26
1. Ntchito Zake: 5:19
2. Lamulo Lake: 5:20
3. Zomwe adachita ndi lamulo Lake: 5:21
4. Kuzindikira ntchito zake: 5:21-23
5. Zotsatira za ntchito Zake: 5:24-26
D. Kuyesedwa: 5:27-40
1. Lamulo la akuluakulu: 5:27-28
2. Chozitchinjiriza cha Petulo: 5:29-32
3. Kusanthula kwa akuluakulu: 5:33-39
4. Chisankho chosalungama cha akuluakulu: 5:40
E. Zotsatira za chizunzocho: 5:41-42
1. Chikondwerero: 5:41
2. Umodzi: Kukumana tsiku ndi tsiku limodzi: 5:42
3. Kuchitira umboni: Kuphunzitsa ndi Kulalikira: 5:42
VII. Atumiki oyamba: 6:1-7
A. Kufunikira kwa atumikiwo: 6:1
B. Atumikiwo anasankhidwa: 6:2-4
1. Maziko a kusankhidwako: 6:2
2. Cholinga cha kus: 6:2 ankhidwako
3. Chisankhocho: 6:3
4. Kufunikira kwa kusankhidwako: 6:4
C. Atumiki akhazikitsidwa: 6:5-6
1. Njira zomwe zidatsatidwa: 6:5-6
2. Amuna anasankhidwa: 6:5
3. Kuzozedwa kwao: 6:6
D. Zotsatira za atumikwo: 6:7
1. Mawu anachulukitsidwa: 6:7
2. Ophunzira anachuluka: 6:7
3. Kumvera ku chikhulupiriro: 6:7
VIII. Wophedwa woyamba kamba ka chikhulupiriro: 6:8-8:1
Page 33
33
A. Mmene analili Stefano: 6:3-15
1. Mmodzi wa asanu ndi awiri: 6:3,5
2. Wozazidwa ndi Mzimu Woyera: 6:5
3. Munthu wa mbiri yabwino: 6:3
4. Munthu wa chikhulupirio: 6:5
5. Munthu wa nzeru: 6:3, 10
6. Munthu wa mphmvu: 6:8
7. Mboni yadalilika: 6:9-10
B. Chizunzo cha Stefano: 6:11-15
C. Uthenga wa Stefano: 7:1-53
1. Abrahamu: 7:1-8
2. Makolo a Mchipangano chakale: 7:9-16
3. Mose: 7:17-43
a. Ku Aigupto: 7:17-28
b. Muchipululu: 7:29-43
4. Chihema: 7:44-50
a. Cha Mose: 7:44
b. Cha Yoswa: 7:45
c. Cha Davide: 7:45-46
d. Cha Solomoni: 7:47-50
e. Cha Mulungu: 7:48-50
5. Aneneri: 7:51-53
D. Umboni wa Stefano: 7:54-8:1
1. Malingaliro a akuluakulu: 7:54
2. Chilengezo cha Stefano: 7:55-56
3. Zomwe akuluakulu anachita: 7:57-59
4. Imfa ya Stefano: 7:59-8:1
Gawo Lachitatu: Umboni wa ku Yudeya ndi ku Samariya
Machitidwe 8-12
I. Kusintha: Zotsatira za imfa ya Stephano: 8:1-4
A. Chizunzo: 8:1,3
B. Kuikidwa mmanda kwa Stefano: 8:2
C. Umboni wopitirira wa mpingo: 8:4
II. Umboni wa Filipo: 8:5-40
A. Utumiki wa ku Samariya: 8:5-25
Page 34
34
1. Umboni wa Filipo: 8:5-13
a. Ntchito ya Filipo: 8:5-7, 12
b. Zimene a Samaliya adachita: 8:6-12
c. Simoni wa nyanga: 8:9-13
2. Ntchito ya Petulo ndi Yohane: 8:14-17
a. Kubwera kwa Petulo ndi Yohane: 8:14
b. Kubwera kea Mzimu Woyera: 8:15-17
c. Zimene Simoni adachita: 8:18-19
d. Chenjezo la Simoni: 8:20-24
B. Utumiki wa ku Aitiyopiya: 8:26-40
1. Kukonzekera: 8:26-28
2. Umboni: 8:29-35
3. Zomwe adachita: 8:36-38
C. Kusintha kupita ku Azotu: 8:39-40
III. Umboni wa Saulo: 9:1-31
A. Kusanthulika mtima kwa Saulo: 9:1-9
1. Cholinga chake: 9:1-2
2. Masomphenya ake: 9:3-9
3. Mawu ake: 9:4-7
4. Kuchita khungu: 9:8-9
B. Kutumidwa kwa Saulo kudzera kwa Hananiya: 9:10-19
1. Maitanidwe: 9:10-16
2. Kutumidwa: 9:17-19
C. Ntchito ya Saulo: 9:20-31
1. Saulo ku Damasiko: 9:20-25
a. Umboni wake: 9:20-22
b. Zimene adachita: 9:21-23
c. Kuthawa kwake: 9:23-25
2. Saulo ku Yerusalemu: 9:26-30
a. Kulandiridwa kwake: 9:26-28
b. Ntchito yake: 9:28-29
c. Kuchoka kwake: 9:29-30
D. Kusintha: Mpukulo mu mpingo: 9:31
IV. Umboni wa Petulo: 9:32-12:35
Page 35
35
A. Ku Luda: 9:32-35
1. Okhulupirira: 9:32
2. Munthu wodwala: 9:33
3. Kuchiritsidwa kwa munthu wodwala: 9:34
4. Zomwe adachita: 9:35
B. Ku Yopa: 9:36-43
1. Imfa ya Dorika: 9:36-37
2. Kuitanidwa kwa Petulo: 9:38-39
3. Utumiki wa Petulo: 9:40-41
4. Zotsatira za utumiki: 9:42-43
C. Ku Kaisareya: 10:1-48
1. Masomphenya a Koneriyo: 10:1-8
a. Koneriyo: 10:1-2
b. Masomphenya a Koneriyo: 10:3-6
c. Zomwe adachita Koneriyo: 10:7-8
2. Masomphenya a Petulo: 10:9-22
a. Msomphenya: 10:9-12
b. Kulankhula: 10:13-16
3. Kufika kwa otumidwa: 10:17-22
4. Kufika kunyumba ya Koneriyo: 10:23-48
a. Ulendo: 10:23
b. Kulandiridwa: 10:24-27
c. Chilongosolo: 10:27-28
d. Funso: 10:29
e. Yankho: 10:30-33
f. Ulaliki osamalizitsa: 10:34-43
(1) Mulungu opanda tsankhu: 10:34-35
(2) Kufalikira kwa Uthenga wabwino: 10:36-37
(3) Uthenga wa uthenga wabwino: 10:38-43
g. Zimene Koneriyo adachita: 8:44-48
D. Ku Yerusalemu: 11:1-12:25
1. Vuto lobwera kamba ka kusandulika kwa a mitundu: 11:1-18
a. Vuto lake: 11:1-3
b. Kulongosola ntchito ya Mulungu pakati a mitundu: 11:4-17
(1) Masomphenya: 11:4-10
(2) Alendo: 11:11
(3) Ulendo: 11:12-16
c. Chisankho: 4:18
Page 36
36
V. Mpingo wa ku Antiokeya ku Asuri: 11:19-30
A. Chitsitsimutso cha ku Antiokeya: 11:19-21
B. Kufika kwa Banaba: 11:22-24
C. Saulo asankhidwa ngati mbusa wophunzitsa: 11:25-26
D. Zimene Agabo anaulula: 11:27-30
VI. Chizunzo cha Herode: 12:1-25
A. Kuphedwa kwa Yakobo: 12:1-2
B. Kumangidwa kwa Petulo: 12:3-4
C. Kumasulidwa kwa Petulo 12:5-19
D. Imfa ya Herode: 12:20-23
VII. Kulalikidwa kwa Mawu: 12:24-25
Gawo Lachinayi: Umboni ku dziko lonse lapansi
Machitidwe 13-28
I. Ulendo woyamba wochita utumiki: 13:1-14:28
A. Kuitanidwa ku utumiki: 13:1-3
B. Utumiki ku Pafo wa ku Ku: 13:4-12
C. Utumiki ku Antiokeya wa Mpisidiya: 13:13-50
1. Kupita ku Pisidiya: 13:13-16
2. Uthenga: 13:17-37
a. Chipulumutso cha mu Eksodo: 13:17
b. Ulendo wa mu Chipululu: 13:18
c. Kugonjetsa Kanani: 13:19
d. Ulamuliro wa Saulo ndi Davide: 13:20-23
e. Utumiki wa Yohane Mbatizi: 13:24-25
f. Kupachikidwa ndi kuuka Kwa Yesu: 13:26-37
g. Kuitanidwa: 13:38-41
3. Mmene adayankhira kuitanako: 13:42-50
D. Utumiki ku Ikoniyo: 13:51-14:5
E. Utumikiku Lustra: 14:6-25
F. Utumiki ku Antiokeya: 14:26-28
Page 37
37
II. Mkumano wa akuluakulu ku Yerusalemu: 15:1-35
A. Vuto lake: 15:1-3
B. Mkumano wa akuluakulu: 15:4-21
1. Mkumano woyamba: 15:4-5
2. Mkumano wa mseli wa atumwi ndi akuluakulu: 15:6
3. Mkumano wachiwiri: 15:7-21
a. Uthenga wa Petulo: 15:7-11
b. Uthenga wa Paulo ndi Banaba: 15:12
c. Uthenga wa Yakobo: 15:13-21
C. Chisankho: 15:19-21
D. Makalata: 15:22-35
III. Ulendo wachiwiri wa utumiki: 15:36-18:22
A. Kutsutsana: 15:36-41
B. Utumiki wa ku Lustra: 16:1-5
C. Utukiwa wa ku Trowa: 16:6-10
D. Utumiki wa ku Filipo: 16:11-40
E. Utumiki wa ku Tesalonika: 17:1-9
F. Utumiki wa ku Bereya: 17:10-14
G. Utumiki wa ku Atene: 17:15-34
H. Utumiki wa ku Korinto: 18:1-18
I. Utumiki wa ku Efeso: 18:19-21
J. Yerusalemu ndi Antioki: 18:22
IV. Ulendo wachitatu wa utumiki: 18:23-21:14
A. Ku Galatiya: 18:23
B. Utumiki wa ku Efeso: 18:24-19:41
1. Apolosi: 18:24-28
2. Ophunzira a Yohane: 19:1-7
3. Sukulu ya ku Turano: 19:8-12
4. Ana a Skeva: 19:13-17
5. Kupereke otembenuka: 19:18-20
6. Chisankho: 19:21
7. Otchinjiriza Demetriyo: 19:23-41
C. Utumuki wa ku Makedoniya ndi ku Helene: 20:1-5
Page 38
38
D. Utumiki wa ku trowa: 20:6-12
E. Utumiki wa ku Mitilene: 20:13-38
1. Ulendo: 20:13-16
2. Mkumano ndi akuluakulu a ku Efeso: 20:17-35
a. Kuunika utumiki wake: 20:17-21
b. Kuona za kutsogolo: 20:22-24
c. Chikumbumtima cha Paulo: 20:25-27
d. Chenjezo 20:28-31
e. Kuvomerezeka kwa Mulungu: 20:32
f. Chitsanzo cha Paulo mu mtsautso: 20:33-35
3. Kusanzikana: 20:36-38
F. Utumiki wa ku Turo: 21:1-6
G. Utumiki wa ku Ptolemayi: 21:7
H. Utumiki wa ku Kaesareya: 21:8-14
V. Ulendo wotsiriza wa ku Yerusalemu ndi kwa Aroma: 21:15-28:31
A. Yerusalemu: 21:15-23:32
1. Kusintha kupita ku Yerusalemu: 21:15-17
2. Mphekesera zosutsana ndi Paulo: 21:18-30
a. Kuti anaphwanya chilamulo cha Mose: 21:18-26
b. Kuti anadetsa malo oyera: 21:27-30
3. Zimene Paulo adachita: 21:23-26
4. Kupulumuka kwa Paulo: 21:30-32
5. Zimene Paulo adayankha: 21:33-23:10
a. Khamu la Chiyuda: 22:1-23
b. Kenturiyo wa Chiroma: 22:24-26
c. Kapitao wamkuru: 22:26-30
d. Bwalo la akuru: 23:1-10
(l) Chivomerezo cha Paulo: 23:1
(2) Kukumana ndi Mkulu wansembe: 23:2-5
(3) Kugawanika kwa bwalo: 23:6-10
6. Chivumbulutso kwa Paulo: 23:11
7. Chiwembu chofuna kupha Paulo: 23:12-15
8. Kupulumuka kwa Paulo: 23:16-32
a. Chiwembu chiululika: 23:16-22
b. Kalata: 23:25-30
c. Kuthawa: 23-32
Page 39
39
B. Ku Kaesareya: 23:33-26:32
1. Pa maso pa Felike: 23:33-24:27
a. Chitsutso cha Tertulo: 24:1-9
b. Yankho la Paulo: 24:10-21
c. Yankho la Felike: 24:22-27
2. Pamaso pa Festo: 25:1-12
3. Felike ndi Agripa: 25:13-27
4. Pamaso pa Agripa: 26:1-32
a. Paulo adzilankhulira yekha: 26:1-23
b. Kuitanira ku chipulumutso: 26:24-29
c. Chigamulo: 26:30-32
C. Ulendo wa kwa Aroma: 27:17-28:31
1. Mafunde: 27:1-44
2. Njoka: 28:1-6
3. Machiritso: 28:7-10
4. Ulendo upitilira: 28:11-15
D. Kwa Aroma: 28:16-31
l. Mkumano ndi Ayuda: 28:16-29
2. Utumiki: 28:30-31
Page 40
40
CHAPUTALA CHA 3
MAFANIZO A KUCHULUKITSA
ZOLINGA:
Pakutha pa chaputachi muyenera:
Kulemba Vesi Lotsogolera kuchokera pamtima.
Kupereka tanthauzo la mawu oti “fanizo.
Kulongosola chifukwa chimene Yesu amagwiritsa ntchito mafanizo.
Kuzindikra mfundo za kuchulukitsa mu mafanizo amene Yesu amaphunzitsa.
VESI LOTSOGOLERA:
Ndipo ndi mafanizo otere ambiri analankhula nao mau, monga anakhoza kumva;
(Marko 4:33).
MAWU OYAMBA
Phunziroli likukhazikika pa mfundo za kuchulukana molingana ndi mmene Yesu anaphunzitsira
pa utumiki wake. Fanizo ndi nkhani imene imakamba zitsanzo zochokera ku dziko limene
timakhala pofuna kuonetsera choonadi ku uzimu.
Tanthauzo lenileni la mawu oti “fanizo” ndi “kuika pambali, kufanizira.” Mu mafanizo, Yesu
amafanizira zitsanzo za kudziko ndi choonzdi cha uzimu. Fanizo ndi nkhani yochitika kudziko
imene ili ndi tanthauzo ku uzimu.
CHIFUKWA CHIYANI MAFANIZO
Ophunzira ake nthawi ina anamufunsa Yesu chifukwa chimene amagwiritsa ntchito mafanizo
pofuna kuphunzitsa choonadi cha uzimu.
Ndipo ophunzirawo anadza, nati kwa Iye, Cifukwa canji muphiphiritsira iwo
m'mafanizo? (Mateyu 13:10).
Yesu anayankha:
Ndipo Iye anayankha nati, Cifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za
Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwa kwa iwo (Mateyu 13:11).
Kumvetsetsa choonadi ku uzimu chimene chaphunzitsidwa mu fanizo zinapatsidwa kwa
ophunzira chifukwa anali ndi maganizo a uzimu. Amene analibe maganizo a uzimu mkumamva
mafanizo amalephera kumvetsetsa. Choonadi chauzimu chimveka ndi maganizo a uzimu:
Page 41
41
Koma munthu wa cibadwidwe ca umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu:
pakuti aziyesa zopusa; ndipo sakhoza kuzizindikira, cifukwa ziyesedwa mwauzimu
(I Akorinto 2:14).
Munthu wa maganizo a uzimu ndi amene wabadwanso mwatsopano ku uzimu. Amene ali ndi
maganizo a uzimu amamvetsa mfundo zimene zimachokera mmafanizo. Amene ndi anthupi, a
maganizo a uchimo sangamvetse.
UTHENGA WABWINO WA UFUMU
Pamene Yesu anatuma akuphunzira ake kupita kudziko lonse kukalalikira uthenga wabwino,
Anati kwa iwo…
Ndipo uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse
lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo
cidzafika cimariziro (Mateyu 24:14).
Uthenga wabwino umene mukuyenera kufalitsa kudziko lapansi ndi uthenga wabwino wa
ufumu. Ndi uthenga umene ndi wa kubadwa, moyo ndi utumiki wa Yesu. Komanso ndi uthenga
wa imfa ya machimo a anthu onse ndi kuuka kwake kuchokera ku imfa. Mukuyenera kuuza
anthu za mmene anthu za mmene angalowere mu ufumu wa Mulungu kudzera mu kubadwanso
ku uzimu ndi kuwaphunzitsa mmene angakhalire moyo watsopano wa ufumu…….
MAFANIZO A KUCHULUKANA
Yesu anaphunzitsa mafanizo ambiri okhudza ufumu wa Mulungu. Ena mwa iwo anali mafanizo
a mmene ufumu ungafalikire ku dziko lonse lapansi. Mafanizo ali mmusiwa okhudza kukula kwa
Ufumu amaululu mfundo za kuchulukana. Onani ndi kuwerenga mafanizowa Mbaibulo lanu:
Nkhosa yosochera: Mateyu 18:12-14; Luka 15:4-7
Ndalama yotaika: Luka 15:8-10
Mwana olowerera: Luka 15:11-32
Mafanizowa amaululu chidwi cha Mulungu pa otaika ndi change chowafuna kuti abwerere mu
Ufumu wa Mulungu. Sizitengera chfukwa chimene anataikira. Nkhosa zinasochera kutali.
Ndalama inataika chifukwa cha kusasamala. Mwana anasochera chifukwa cha kugalukira kwake.
Mukuyenera kuchita mmene mungathere kuti mupeze otayika mu uchimo. Pitani kumene
amapezeka, osadikiraiwo kuti akupezeni. Mulungu sakhudzidwa ndi mmene anataikira, komatu
kuti apezeke basi.
Phwando lalikulu lopanda kanthu: Luka 14:15-23
Page 42
42
Kuchulukana kusathe chufukwa choti ena akana atatha kuyitamidwa ku uthenga wabwino.
Mukuyenera kuwafuna iwo amene ali ndi njala ya uzimu, ndi kwabweretsa ku phwando
lokonzedwa ndi Ambuye.
Mkuyu wosabala: Luka 13:6-9
Yesu anawauza fanizo la mkuyu wosabala. Mtengo wamkuyu ndi chizindikiro chooneka cha
mtundu Israyeli. Mulungu anakweza Israyeli ngati mtundu umene kudzera mwa iye adzaululu
Ufumu wa Mulungu ku dziko. Mulungu anayetsetsa kupeza “mtengo” wa Israyeli kuti ukabale
“zipatso” pakati pa mitundu yosadziwa Mulungu pakugawana nawo chidziwitso cha Mulungu
woona. Mulungu sakondwera ndi mitengo imene sibala zipatso.
Matalente: Mateyu 25:14-30; Luka 19:11-27
Munthu wa pa ulendo wautali: Marko 13:34-37
Akapolo: Mateyu 24:43-51; Luke 12:39-46
Akapolo oyang’anira: Luka 12:36-38
Woyang’anira wokhulupirika: Mateyu 25:14-30
Mafanizo a “akapolowa” amaika chidwi pa mdindo woyang’anira wamzeru pa uthenga wa
Ufumu umene waperekedwa kwa okhulupirira. Wokhulupirira aliyense papatsidwa “matalente”
kapena kuthekera kwapaderadera koti agwiritse ntchito polalikira uthenga wabwino. Kaya
kuthekera kwanu nkochepa kapena kwakukulu, mukuyenera kuchulukitsa zimene Mulungu
wakupatsani.
Kapolo aliyense akuyenera kuchuluka. Pamene Yesu adzabwerera ku dziko lapansi, iwo amene
agwiritsa ntchito mphatso zawo moyenera adzapatsidwa mphoto (Luka 16:10-12). Iwo amene
sakuchulukana amayesedwa osakhulupirika:
Pakuti Mwana wa munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate wace, pamodzi ndi
angelo ace; ndipo pomwepo Iye adzabwezera kwa anthu onse monga macitidwe ao
(Mateyu 16:27).
Yesu amadziwa mfundo ya muyeso pa kuchulukana:
Koma iye amene sanacidziwa, ndipo anazicita zoyenera mikwapulo,
adzakwapulidwa pang'ono. Ndipo kwa munthu ali yense adampatsa zambiri, kwa
iye adzafuna zambiri; ndipo amene anamuikizira zambiri, adzamuuza abwezere
zoposa (Luka 12:48).
Page 43
43
Ufumu wa Mulungu umafalikira pakugwiritsa ntchito luso la uzimu lopatsidwa ndi Mulungu.
Ngati mugwiritsa ntchito zimene Mulungu wakupatsani, luso lanu lidzachuluka. Ndipo ngati
simuligwiritsa ntchito adzkulandani.
Wofetsa: Mateyu 13:3-8; Marko 4:3-8; Luka 8:5-8
Uthenga wa Ufumu umafalikira pofesa mbewu ya Mau a Mulungu. Sipangakhale kuchulukana
popanda Mau a Mulungu. Zipatso zimatengera moyo umene uli mu mbewu (amene ndiwo Mau a
Mulungu) ndi mmene nthaka ikuchitira (ndi mmene munthu achitira akamva Mau a Mulungu).
Pamakhalamachitidwe osiyana pamene mbewu ya Mau ikufetsedwa.
Udindo wanu ndi kungofetsa. Pamene mufetsa mbewu ya Mau a Mulungu, nthaka idzakonzeka
ndi kupereka zokolola. Nthaka ina imalephera kupereka zochuluka. Ngakhale Yesu anakumana
ndi nthaka yokanika pa nthawi ya utumiki wake.
Ndipo kumeneko sanakhoza Iye kucita zamphamvu konse, koma kuti anaika manja
ace pa anthu odwala owerengeka, nawaciritsa.
Ndipo anazizwa cifukwa ca kusakhulupirira kwao (Marko 6:5-6).
Nansongole ndi Tirigu: Mateyu 13:24-30
Pamene mukuchulukitsa Ufumu wa Mulungu pa kuonjezereka kwa okhulupirira atsopano,
Satana nayenso amayesera kugonjetsa ntchitoyo. Adzadzala anthu amene adzakhala ngati
Nansongole pakati pa mbewu zabwino za Ufumu wa Mulungu.
Anthu ena amene amavomereza kukhala okhulupirira ndi kuyamba kubwera mu mpingo mu njira
yochulukitsa, nthawi zina sakhala oona mtima. Amakhala nansongole odzalidwa ndi Satana.
Yesu safuna muwononge nthawi yanu kusiyanitsa pakati pa nansongole ndi tirigu. Pitilirani
kudzala mbewu ndi kuchulukana. Pa tsiku lokolola pamene Yesu adzabwera, nansongole
adzasiyanitsidwa kuchokera ku zokololazo.
Nkhoka yoponyedwa mnyanja: Mateyu 13:47-50.
Yesu anafanizira kukula kwa Ufumu wa Mulungu ndi nkhoka yaikulu imene iponyedwa
mnyanja. Nsomba zamitundu yonse zimalowamo, koma pamene nkhoka iponyedwa kumtunda
nsombazo zimasiyanitsidwa ndi zinthu zina zimene sizabwino.
Page 44
44
Ufumu udzakoka anthu a mitundu yonse. Ambiri adzalowamo. Ena adzakhala oona mtima ena
ayi. Pa tsiku lomaliza la chiweruzo pamene Mulungu adzakoka nkhoka, “nsomba” zabwino ndi
zoipa zizasiyanitsidwa. Inu simunaitanidwe kusiyanitsa koma kusodza.
Mbewu ya Mpiru: Mateyu 13:31-32; Marko 4:31-32; Luka 13:19
Ufumu wa Mulungu udzachuluka ngati mbewu ya mpiru. Mbewu ya mpiri ndi yaing’ono, koma
imakula mkukhala yokhwima. Ufumu wa Mulungu padziko umakhala ndi chiyamba
chaching’ono. Pamene Yesu anabwerera kumwamba atatha utumiki padziko, anasiya gulu la
anthu lochepa kulalikira uthenga wabwino. Okhulupirira ochepawa anachulukana kufikira zikwi
la omutsatira Iye ku mitundu yonse ya anthu.
Chotupitsa Mkate: Mateyu 13:33; Luka 13:21
Monga chotupitsa mkate mu choikiramo, Ufumu wa Mulungu udzachulukitsidwa kufikira dziko
lonse. Momwemonso chotupitsa, mphamvu ya Ufumu wa Mulungu siili kunja koma ili mkati.
Mpesa ndi Nthambi zake: Yohane 15:1-16
Fanizoli limafotokoza ubale wa pakati pa Yesu ndi kubala zipatso. Yesu ndi mpesa wa uzimu
ndipo ife ndizo nthambi. Simungabale chipatso mwa inu nokha. Mungathe kuchulukana ngati
mukhala mwa olumikizika ku moyo wa wochokera ku nthambi, ndiye Yesu. Yesu akufuna
kusanza moyo wanu pochotsa chilichonse chimene sichibala chipatso ndi cholinga chakuti inu
mukabale chipatso cha uzimu chokhalitsa.
Zokolola: Mateyu 9:37-38; Luka 10:2
Mu fanizo ili, munda ukuimira dziko. Zokolola ndi khamu la anthu amene akonzeka kulandira
uthenga wabwino. Zokolola zochuluka zikudikira kuti zikololedwe ndi ogwira ntchito a
Mulungu.
MFUNDO ZINA ZA KUCHULUKITSA
Yesu anaphunzitsa mfundo zina zochulukitsa mwachidule:
Kuunika kwa Dziko: Mateyu 5:14-16; Luka 8:16
Ufumu wa Mulungu udzachuluka ngati wokhulupirira akuoneka ngati kuwala kochokera ku
mzinda umene uli pamwamba kuonekera kutali. Tikyenera kubweretsa kuunika kwa dziko
(Yesu) ku dziko limene lili mu mdima wa uzimu. Ufumu udzachuluka pamene anthu abwera ku
kuwala.
Page 45
45
Mchere wa dziko: Luka 14:34
Mu nthawi ya Mbaibulo, mchere umathiridwa pa nyama kuti isaonongeke. Okhulupirira ali ngati
“mchere” wothiridwa pa dziko ndi uthenga wa kuteteza (chipulumutso). Ufumu udzachuluka
anthu apulumuke ku “chivundi” (imfa ya uzimu) ya tchimo.
Chuma cha kumwamba: Mateyu 6:19-21; Luka 12:15
Okhulupirira sakuyenera kukhala ndi chidwi ndi kudzichulukitsira chuma cha dziko lapansi.
Tayitanikwa ku chichulukitso cha uzimu. Pamene mukugawana uthenga wabwino,
mumachulukitsa chuma cha chanu cha uzimu kumwamba.
Chipata chotakata: Mateyu 7:13
Simungapereke chiweruzo choyenera poyang’ana chiwerengero. Njira yak u Gehena ili yotakata
ndipo ambiri amapita kumeneko koma njira yaku moyo wosatha amapitako ndi ochepa.
Ntchito Zambiri: Mateyu 7:22
Ambiri adzachita ntchito zodabwitsa. Moti padzakhala kukula ndi kuchuluka. Komatu kuchita
zodabwitsa zambiri sikofanana ndi kuchita chifuniro ndi kukwaniritsa cholinga cha Mulungu.
Zodabwitsa za Mulungu zikuyenera kuchitidwa ndi anthu Ake mu njira Yake.
Zochepa ndi Zambiri: Mateyu 10:42; Mateyu 14:15-21
Chilichonse chochitika mu dzina la Yesu, ngakhale choneka chochepa, ndi chofunikira.
Chozizwa cha mikate ndi nsomba chimaonetsera mmene Mulungu amachulukitsira ndi
kugwiritsa ntchito zochepa zimene tingapereke.
Kukula kumafuna Kusintha: Marko 2:21-22; 7:13
Kukula kwatsopano kumafuna kusintha. Simungasunge chatsopano mu chotengera cha
makhalidwe a zakale ndi a uchimo. Kuthekera kwa mphamvu ya Mau a Mulungu
kumalepheretsedwa ndi anthu amene amakakamira makhalidwe akale ndi kukana kusintha.
Kupeza pa Kutaya: Marko 8:34-37; 10:29-30
Kulandira pa Kupereka: Luka 6:38
Mfundo za dziko lapansi zimaphunzitsa kuti mumapeza pofuna zambiri. Yesu anaphunzitsa kuti
mumapeza chilichonse pamene mutaya chilichonse. Chimene chimaoneka chotayika mu dziko
mumachipeza mu dziko la uzimu.
Imfa imabweretsa Moyo: Yohane 12:24
Page 46
46
Kudzera mu imfa ya Yesu, ambiri analandira moyo. Pofuna kuchulukitsa, mbewu iyenera kufa.
Kudzera mu imfa moyo unabwera. Kuti mukhale ophunzira weniweni mukuyenera kufa ku
zokhumba za thupi. Mukuyenera “kufa” ku uchimo. Mukuyenera kukaniza njira zanu potsata
Yesu.
Mpingo wa pa thanthwe: Mateyu 16:18
Ufumu wa Mulungu unakhazikika pa thanthwe Yesu Khristu. Palibe kukula popanda Iye. Yesu
anati, “Ndizamanga mpingo wanga.” Ndipo anati palibe munthu amene abwera kwa Ite ngati
Atate samuitana (Yohane 6:44).
Chitsutso chimayenera kukhalako, koma “makomo a imfa” sangakhoze kugonjetsa cholinga cha
Mulungu pofuna kukulitsa Ufumu wake.
…Ici sicitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu (Mateyu 19:26).
…Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira (Marko 9:23).
MFUNDO YAIKULU YA KUCHULUKITSA
Mfundo yaikulu ya kuchulukitsa imene Yesu anaphunzitsa inaperekedwa Mmau Ake otsiriza
kwa ophunzira ake. Lamulo lake linaulula cholinga chake chachikulu polalikira uthenga
wabwino ndi kuchulukitsa atsopano ndi ophunzira:
Cifukwa cace mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo
m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:
ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo
onani, Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira cimariziro ca nthawi ya
pansi pano (Mateyu 28:19-20).
Ndipo ananena nao, mukani ku dziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino
kwa olengedwa onse (Marko 16:15).
Ndipo anati kwa iwo, Kotero kwalembedwa, kuti Kristu amve zowawa, nauke kwa
akufa tsiku lacitatu;
Ndi kuti kulalikidwe m'dzina lace kulapa ndi kukhululukidwa kwa macimo kwa
mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu.
Inu ndinu mboni za izi (Luka 24:46-48).
Page 47
47
Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo
mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi
kufikira malekezero ace a dziko (Machitidwe 1:8).
CHIDULE
Ziphunzitso za Yesu zimaonetsera kuti Iye sakondwera ndi:
-Kusodza opanga kugwira.
-Phwando lopanda kanthu.
-Kufesa opanda kulolola.
-Mtengo wosabala zipatso.
-Nkhosa yotaika imene sibwerera mnkhola.
-Ndalama yotaika imene sinapezeke.
-Mwana wolowelera amene sanapezeke.
-Kapolo wosabala zipatso.
-Nthaka ya uzimu yosachita bwino.
-Zokolola zakupsa zimene sizinakololedwe
Atate athu amene safuna kuti ngakhale mmodzi atayike, amakondwera ndi zotsatira kudzera mu
kuchulukana kwa uzimu:
Comweco siciri cifuniro ca Atate wanu wa Kumwamba kuti mmodzi wa ang'ono
awa atayike (Mateyu 18:14).
Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena aciyesa cizengerezo; komatu aleza
mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa (II
Petro 3:9).
Page 48
48
MAYESO ODZIYETSA NOKHA
1. Lembani Vesi Lotsogolera kuchokera pamtima.
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
2. Perekani tanthauzo la mawu oti “fanizo.”
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
3. Kodi ndi chifukwa chiyani Yesu amaphunzitsa ophunzira ake mu mafanizo?
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
4. Pa pepala lapadera, longosolani mwachidule mfundo za kuchulukana mu fanizo lililonse
pansipa:
Phwando la pa gome lopanda kanthu:
Mtengo wamkuyu wosabala:
Nkhosa yosochera, ndalama ndi mwana:
Mafanizo a kapolo:
Wofesa:
Nansongole ndi Tirigu:
Nkhoka:
Mbewu ya mpiru:
Chotupisa mkate:
Mpesa ndi nthambi zake:
(Mayankho a mafunsowa akupezeka kumapeto kwenikweni kwa bukuli).
Page 49
49
KUPITILIZA KUPHUNZIRA
1. Kuyambira zaka 12 kufikira pamene Yesu amayamba utumiki, Baibulo silimapereka
tsatanetsatane wa zimene zinachitika mmoyo wake mu nthawi imeneyi. Ndi vesi limodzi
lokha limene limaulula za kukula kwa ku uzimu mu nthawi imeneyi.
Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi cisomo ca Mulungu
cinali pa iye (Luka 2:40).
Kuti ukhale wamphamvu, kukula kwa ku uzimu kukuyenera kubwera poyamba utumiki
usanayambe.
2. Pamene nthawi imayandikira kumapeto, Satana adzagwiritsa ntchito mfundo zake
zochulukitsa. Werengani mavesiwa:
-Aneneri onyenga adzauka: Mateyu 24:11
-Anthu ambiri adzanyengedwa: Mateyu 24:11
-Uchimo udzachuluka: Mateyu 24:12
-Ambiri adzataya choonadi cha uthenga wabwino: II Atesalonika 2:3
-Mazunzo a okhulupirira adzachuluka: Mateyu 24:9-10
-Chodetsa ndi nkhani zopanda pake zidzachuluka: II Timoteo 2:16
Page 50
50
CHAPUTALA CHA 4
CHIMODZI KUPHATIKIZA CHIMODZI ZIMAKHALA ZOPITILIRA ZIWIRI
ZOLINGA:
Pakutha pa chaputalachi muyenera:
Kulemba Vesi Lotsogolera kuchokera pamtima.
Kupereka tanthauzo la mawu oti “umboni.”
Kupereka tanthauzo la mawu oti “otumikira.”
Kupereka tanthauzo la mawu oti “mkulu wampingo”
Kulongosola tanthauzo la mawu oti “maitanidwe” a otumikira.
Kuolongosola dongosolo la Mulungu lochulukitsa pofalitsa uthenga wabwino.
Kutchula anthu awiri a Mchipangano Chatsopano ngati chitsanzo cha kuchulukitsa.
Kulongosola mmene mungachulukire ku uzimu.
Kuyamba kuchulukana ku uzimu.
VESI LOTSOGOLERA:
Ndipo zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zomwezi uikize kwa anthu
okhulupirika, amene adzadziwa kuphunzitsa enanso (II Timoteo 2:2).
MAWU OYAMBA
Kukula kwa munthu kumayamba ndi selo imodzi ya moyo. Ndipo seloyo imayamba
kuchulukana kwambiri kufikira kuti munthu amapezeka kuti wapangidwa. Atatha kubadwa,
ntchitoyo imapitilira mwa mwana. Maselo a munthu amapitilira kuchulukana ndi kuyamba
kukula. Izi zili chomwechonso ndi ndi kudziko la uzimu. Munthu aliyense amene wakumana ndi
moyo watsopano mwa Yesu ali chomwechonso ndi selo ya munthu. Wokhulupirira aliyense
ayenera kubereka ku uzimu. Uthenga wabwino umalalikidwa pamene okhulupirira amachuluka
mu njira imeneyi.
Chaputala ichi chikuulula za udindo wanu ngati munthu ku moyo wanu wa uzimu. Muphunzira
dongosolo la Mulungula kuchulukana ku uzimu limene ndi “1 kuphatikiza 1 zimakhala zoposa
ziwiri.
Page 51
51
ZOLEPHERETSA
Vuto limene Yesu anali nawo kwa okhulupirira linali kufikira dziko lonse lapansi ndi uthenga
wabwino (Mateyu 28:19; Machitidwe 1:8). Lero tikukhala mu dziko limene likukula. Zikwi za
anthu akubadwa tsiku ndi tsiku. Chiwerengero cha dziko chikukula kwambiri.
Pali anthu ambiri amene sanafikilidwe ndi uthenga wabwino mdzikoli ndipo ambiri sanamvepo
za Yesu. Magulu a anthu amenewa ndi ankhaninkhani amene sanafikilidwe ndi uthenga
wabwino. Midzi komanso komanso madera ambiri alibe mipingo. Maiko ambiri kulibe azibusa
ambiri ophunzitsidwa ku mipingo imene ilipo.
Kodi tingapambane bwanji ndi vutoli pamene Yesu akuti tifikire dziko lonse ndi uthenga
wabwino?
DONGOSOLO LA MULUNGU
Mulungu ali ndi dongosolo lapaderadera lofuna kufikira dziko lapansi ndi uthenga wabwino.
Mwachidule, Yesu anawauza ophunzira ake kuti…
Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo
mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi
kufikira malekezero ace a dziko (Machitidwe 1:8).
Dongosolo la Mulungu ndi ili: Mzimu Woyera ndi mphamvu ya umulungu yopezeka kuseli kwa
kuchulukana, Yesu ndiye mwini nkhani wa uthenga, ndipo dziko lonse lidzakhala lolandira
uthenga wabwino.
Ophunzira ndi mnthumwi za kuchulukana. Njira za Mulungu kwa ophunzira ndi kuchitira
“umboni” wa uthenga wabwino. Choncho kuchitira “umboni” ndiko kunena zimene waona,
wamva, kapena kukumana nazo. Mu bwalo la milandu, mboni ndiye amene amavomereza za
chinthu kapena munthu. Monga mboni, mukuyenera kuchitira umboni za Yesu ndi cholinga
chake cha chipulumutso kwa anthu onse. Pali mitundu iwiri ya maumboni opezeka mbwalo la
milandu la malamulo. Umboni woyamba ndi wolankhula zokhuza nkhani. Umboni wina ndi
otsimikizira.
Mzimu Woyera amakuthandizani kuchitira umboni kaya wolankhula kudzera mu kuonetsera
mphamvu ya Mulungu.
KUGAWANA PAKATI PA AKULU A MPINGO NDI ATUMIKI
Dongosolo la Mulungu kwa okhulupirira aliyense ndi lochitira umboni wa uthenga wabwino.
Mpingo woyamba unakula pamene amatsatira dongosololi. Wokhulupirira aliyense amagawana
uthenga wabwino ndipo anali wochitachita ku uzimu. Makomo awo amakhala malo
ochulukaniranapo. Mpingo unakula ndi kuchulukana pamene okhulupirira amachitira umboni wa
uthenga wabwino.
Page 52
52
Pamene mpingo ukukula, Mulungu anaitana anthu ena kuti azitumikira nthawi yawo yonse
monga abusa, alaliki, aneneri, aphunzitsi ndi atumwi. Kwa nthawi yaitali, okhulupirira anakhala
gawo limodzi la magulu awiri mu mpingo. Amakhala akulu ampingo kapena atumiki wamba.
Atumikiwa amakhala gulu limodzi la anthu wosankhidwa ndi Mulungu. Tanthauzo lake ndi
lakuti anthu onse a Mulungu. Choncho atumiki amenewa amadziwidwa ngati anhtu amene
satumikira nthawi yawo yonse mu mpingo ayi.
Kenako pali akulu a mpingo amene anaphunzira bwino pa ntchito yawo ya utumiki mu mpingo.
Awa kwa iwo utumiki umakhala ngati ntchito yawo ya nthawi yonse ku mpingo. Akhoza
kusankhidwa kapena osasankhidwa ndi mpingo.
Kwa nthawi yaitali, mu mbiri ya mpingo, kusiyana pakati pa atumiki ndi atumiki wamba
kunayamba. Moti atumiki wamva ansiya kukhala ochulukana mu mpingo. Anayamba kusiyira
ntchito yofalitsa uthenga ku dziko kwa atumiki omwe anali ndi nthawi yonse yotumikira.
Palibe mtumiki wophunzira amene akhoza kukwaniritsa ntchito yonse yonse imene mpingo
unatumidwa kuti ukachite. Ichi ndi chifukwa chimodzi chimene sitinafikire dziko lapansi ndi
uthenga wabwino. Okhulupirira apereka udindo wawo kwa atumiki. Baibulo limaphunzitsa za
kugawana kwa ntchito mu mpingo, koma munthu wina aliyense akuyenera kukangalika kufalisa
uthenga wabwino. Onani Machitidwe 6:1-6.
Pamene mpingo wa ku Yerusalemu imachulukana, zinayamba kufunikira kuti agawane ntchito
kuti afikire zosowa zonse za mu mpingo. Atsogoleri anadzipereka okha ku Mau a Mulungu ndi
kupemphero. Atumiki wamba amagwira ntchito monga kutumikira amasiye ndi ntchito zina
zotumukira. Koma ngakhale okhulupirira amatumikira mosiyanasiyana mu mpingo, onse
anakangalika kufalisa uthenga wabwino.
Stefano anali mmodzi mwa atumiki wamba amene anasankhidwa kugwira ntchito ina, koma
anachitira umboni wamphamvu wauthenga wabwino. (Machitidwe 6:8-11). Filipo anali mtumiki
wambanso amene anasankhidwa kuti atumikire zinthu zina. Anagawana uthenga wabwino ndi a
Samariya (Machitidwe 8:5-12).
Pamene chizunzo chinabwera ku Yerusalemu ndipo okhulupirira mkubalalikana mmizinda
anapitilira kukhala mboni za uthenga wabwino.
Pamenepo ndipo iwo akubalalitsidwa anapitapita nalalikira mauwo (Machitidwe
8:4).
Kwa okhulupirira enieni sipakhala kugawana pakati pa opatulika ndi a kudziko chifukwa Yesu
ndi Ambuye wa onse.
Page 53
53
MAITANIDWE A ATUMIKI WAMBA
Ngati mukufuna mumvetsetse maitanidwe a uzimu a mtumiki wamba, mubwerere ku
Chipangano Chakale. Dongosolo la Mulungu linali kwa mtundu wonse wa Israyeli kuti ukhale
“ansembe” kapena “atumiki.”
Ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika (Eksodo
19:6)
Monga ansembe, munthu aliyense wa Israyeli anali mboni wa Mulungu woona kwa
osakhulupirira.
Kukhazikitsidwa kwa udindo wa unsembe sikunasinthe ndondomeko ya Mulungu pa Israyeli.
Unsembe unali ngati ntchito ya “utumiki” wa utsogoleri wa masiku a lero. Koma mtundu wonse
umatumikirabe ngati atumiki a uthenga wa Mulungu mitundu yosadziwa Mulungu.
Mu Chipangano Chatsopano, okhulupirira apatsidwa maitanidwe ofanana. Akutchedwa ansembe
kapena atumiki a uthenga wabwino:
Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe acifumu, mtundu woyera mtima,
anthu a mw ni wace, kotero kuti mukalakire zoposazo za iye amene anakuitanani
muturuke mumdima, mulowe kuunika kwace kodabwitsa (II Petro 2:9).
Kuitanidwa kwa okhulupirira ndiko kuti akachitire umboni wa Mulungu amene anawatulutsa mu
mdima wa uzimu ndi kulowa mu “kuwala” kwa Yesu Khristu (Yohane 9:5).
Okhulupirira amaudzidwa kuti “ayende moyenera molingana ndi maitanidwe awo amene alimo”
(Aefeso 4:1). Pali maitanidwe amodzi ndiwo kuchitira umboni wa uthenga wabwino. Imeneyi
ndi ntchito ya okhulupirira onse. Munthu wina aliyense adzayankhapo pa za mmene anachitira
ku maitanidwe ake.
Maitanidwe amenewa samakhazikika chifukwa cha maphunziro kapena kuthekera kwa kudziko.
Mulungu amagwiritsa ntchito anthu wamba ndi cholinga chakuti Iye yekhayo alandire
ulemerero.
Pakuti penyani maitanidwe anu, abale, kuti saitanidwa ambiri anzeru, monga mwa thupi;
ambiri amphamvu, mfulu zambiri, iai;
Koma Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, kuti akacititse manyazi anzeru;
ndipo zofoka za dziko lapansi Mulungu anazisankhula, kuti akacititse manyazi
zamphamvu;
Ndipo zopanda pace za dziko lapansi, ndi zonyozeka, anazisankhula Mulungu, ndi zinthu
zoti kulibe; kuti akathere zinthu zoti ziriko; kuti thupi liri lonse lisadzitamande pamaso pa
Mulungu (I Akorinto 1:2-29).
Page 54
54
MACHITIDWE A KUCHULUKANA
Dongosolo la Mulungu la kuchulukana ndi lofanana ndi la kudziko la uzimu. Paulo anamuuza
Timoteo mawu awa mwachidule:
Ndipo zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zomwezi uikize kwa anthu
okhulupirika, amene adzadziwa kuphunzitsa enanso (II Timoteo 2:2).
Paulo anamuuza Timoteo kuti asankhe anthu okhulupirika ndi kuwapereka ku zinthu zimene
anaphunzitsidwa ndi Paulo. Anthu okhulupirika amenewa akuyenera kukhala ndi kuthekera
kophunzitsa ena. Kupyolera mu dongosolo limeneli la kuchulukana, uthenga wabwino ungafikire
ku dziko lapansi.
Pofuna kuona mmene dongosolo la Mulungu la kuchulukana mmene limagwirira ntchito,
werengani tchati mmusimu. Tchatili likuonetsa nthawi ya pachaka imene munthu
angatembenuze munthu wina ndi kumuphunzitsa kukhala mkhristu wodalilika. Mu zoona zake
zikhoza kutenga nthawi kapena ayi potengera munthu amene achitayo. Choncho sizotheka
kukhazikika pa malire a nthawi. Koma ngati mkhristu akhoza kufikira munthu mmodzi ndi
kumuphuzitsa pa chaka ndipo nayenso aphunzitsa wina pa chaka, dziko likhoza kufikilidwa ndi
uthenga wabwino.
TIYAMBE BWANJI
Chipangano chatsopano chimaulula uthenga wabwino unafalikira mmadera oyandikana.
Kutanthauza kuti mukhoza kufalisa uthenga mosavuta pogwiritsa ntchito magulu a anzanu,
achibale, ndi ogwira nawo ntchito limodzi.
Mwachitsanzo, Yesu anaitani nsodzi mmodzi wotchedwa Andreya. Iyeyi anagawana uthenga ndi
mbale wake Petro. Ndipo anagawana ndi asodzi anzawo. Posakhalitsa gulu la anthu onse la
asodzi linamtsata Yesu.
Mmoyo wathu wa tsiku ndi tsiku atumiki osaitanidwa sikuti angokhala okongoletsa mpingo
kapena kumene amakhala ayi. Iwonso ndi akazembe a Ufumu kwa anzawo, achibale komanso
ogwira nawo ntchito limodzi. Kaya ndi kusukulu, kuntchito, kubanja, mmudzi, tikhoza
kuchitanso utumiki.
Luka 16:19-31 amakmba nkhani ya mwini chuma amene anapita ku Gehena. Munthuyi
anafunitsitsa atabwerera kuti akalalkire kwa a pabanja pake koma nthawi inamuthera.
Musadikire kufikira nthawi yofalisa uthenga ndi anzanu ikuthereni.
Page 55
55
MPHATSO ZA MZIMU NDI KUCHULUKANA
Umboni weniweni wa ubatizo wa Mzimu Woyera ndiko kukhala wamphamvu pochitira umboni
wa uthenga wabwino. Mphamvu ya Mzimu Woyera imapangitsa akhristu kuchulukana ku uzimu
(Machitidwe 1:8).
Njira imodzi imene Mzimu Woyera amapatsa mphamvu wokhulupirira ndi kudzera mu mphatso
za uzimu. Okhulupirira aliyense anapatsidwa mphatso za uzimu zomukuonzekeretsa kuchita
utumiki kwa ena. Mphatsozi ndi ndi kuthekera kwa uzimu kopatsidwa ndi Mzimu Woyera.
Ngati simudziwa mphatso za uzimu zimene Mulungu wakupatsani, funsani a Harvestime
International Institute akupatseni phunziro la “Utumiki wa Mzimu Woyera.” Phunziroli
limakamba za mphatso za uzimu.
KUKULA KWA UFUMU
Wokhulupirira aliyense akuyenera kukhala wochitachita. Koma kuchulukana chabe kwa
okhulupirira sikukwanira. Wokhulupirira ayenera kudzipereka pa mpingo umene ali ndi cholinga
chokhala pa umodzi woona ndi okhulupirra ena. Mpingi uyeneranso kuchulukana pawokha.
Mpingo uyenera kumakula mwa okha ku uzimu ndi kupitilira kukula, mmalire, ndi makulidwe
ena. Mwaonanso udindo wanu wochukitsa ngati munthu. Mu chaputala chikubwerachi,
muphunzira za mmene mungachulukire ngati gulu pakati pa mpingo.
Page 56
56
MAYESO ODZIYESA NOKHA
1. Lembani Vesi Lotsogolera kuchokera pamtima.
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
2. Perekani tanthauzo la mawu oti “mboni.”
___________________________________________________________________________
3. Perekani tanthauzo la mawu oti “atumiki wamba.”
___________________________________________________________________________
4. Perekani tanthauzo la mawu oti “atumiki oitanidwa.”
___________________________________________________________________________
5. Fotokoza “maitanidwe” a atumiki wamba.”
___________________________________________________________________________
6. Kodi dongosolo la Mulungu la kuchulukitsa pa kulalikita uthenga wabwino ndi chani?
___________________________________________________________________________
7. Ndi anthu ati awiri mu Chipangano Chatsopano amene anali chitsanzo cha kuchulukana
ku uzimu?
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
8. Ndi njira iti yabwino yoyamba kuchulukana ku uzimu?
___________________________________________________________________________
(Mayankho a mafunsowa akupezeka kumapeto kwenkweni kwa bukuli).
Page 57
57
KUPITILIZA KUPHUNZIRA
1. Mu chaputala chimene chikuthachi ndi mwaphunzira za mafanizo a kuchulukana.
Onaninso mafanizo otsatirawa kawiri. Mu fanizo lililonse aliyense anali ndi udindo
wochulukana mokhulupirika.
-Matalente: Mateyu 25:14-30; Luka 19:11-27
-Munthu wa paulendo wautali: Marko 13:34-37
-Akapolo: Mateyu 24:43-52; Luka 12:39-46
-Akapolo woyang’anira: Luka 12:36-38
-Woyang’anira wokhulupirika: Mateyu 25:14-20
2. Werengani kukambirana kwa pakati pa Yesu ndi Petro mu buku la Yohane 21:15-22. Mu
Machitidwe 10:22 werengani mawu a Yesu amene analankhula kwa Paulo pa nthawi
imene amatembenuka mtima.
Chidwi chanu chisakhale poti kaya ena akukwaniritsa udindo wawo wolalikira uthenga
kapena ayi. Simukuyenera kufunsa ngati Petro, “Kodi munthuyu adzatani?” Chidwi
chanu chikhale ngati cha Paulo, “Kodi ndidzatani Ambuye?”
Page 58
58
CHAPUTALA CHA 5
MAWU OYAMBA A KUKULA KWA MPINGO
ZOLINGA:
Pakutha pa chaputalachi muyenera:
Kulemba Vesi Lotsogolera kuchokra pamtima.
Kudziwa mpingo weniweni.
Kulongosola mmene mpingo unayambira.
Kulemba zitsanzo za Mpingo mu Baibulo.
Kudziwa cholinga cha Mpingo Mbaibulo.
Kudziwa mitundu inayi ya kukula kwa Mpingo.
Kulemba chidule cha utumiki wa Mzimu Woyera pa kukula kwa Mpingo.
VESI LOTSOGOLREA:
Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili
ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzaulaka uwo
(Mateyu 16:18).
MAWU OYAMBA
Mu chaputala chomaliza mwaphunzira za udindo wa wokhulupirira aliyense wochulukana ku
uzimu pofalisa uthenga wabwino. Mulungu ali ndi dongosolo lapaderadera mwa okhulupirira
amene angofika kwa Iye. Akuyenera kukhala gawo limodzi la chiyanjano cha okhulupirira
anzawo mu Mpingo. Okhulupirira ayenera kuberekana aliyense mumpingo, pakutero mpingo
umachulukana.
Chaputala ichi chikuonetsera dongosolo la Mulungu ku Mpingo ngati malo ochulukiranapo ku
uzimu. Machaputala anayi otsatira akufotokoza za mitundu ya kukula kwa mpingo.
MPINGO
Tikamakamba za “Mpingo” sitikamba za bungwe kapena mpingo opangidwa ndi anthu.
Mawu okuti “Mpingo” amatanthauza “oitanidwa.” Tikamakamba za Mpingo, timakamba za
chiyanjano cha dziko lapansi cha iwo amene ndi okhulupirira owona amene ayitanidwa kuchoka
ku dziko lapansi kulowa mu Ufumu wa Mulungu.
Page 59
59
Chifukwa cha cholinga cha utumiki, chiyanjano chimenechi cha dziko lapansi cha okhulupirira
chagawidwa mmangulu awo amene amasonkhana. Maguluwa amenewa amatchedwa Mpingo.
Ena mwa magulu amenewa amakhala oyima pawokha. Pamene ena amasonkhana ndi mabungwe
monga Assemblies of God, Baptist ndi Methodist komanso ena.
Munthu sumakhala gawo la Mpingo woona pokhala limodzi ndi bungwe koma pokhala
wobadwa mwatsopano ndi kulowa mu Ufumu wa Mulungu. Izi zimachitika zimachitka
povomereza ndi kulapa machimo ndi kulandira Yesu ngati Ambuye ndi mpulumutsi wa moyo
wanu. Mutatha kukhala wokhulupirira, dongosolo la Mulngu pa moyo wanu ndilo kukhala
mmodzi wa anthu wokhulupirra mu chiyanjano chimene ndi Mpingo.
MMENE MPINGO UMAYAMBIRA
Mu Chipangano Chakale mtunda wa ana a Israyeli unasankhidwa ngati gulu la anthu limene
kudzera mwa iwo Mulungu adzadziululu yekha kwamitundi una ya anthu. Kwa nthawi yaitali
Israyeli analephera udindowu.
Mu nthawi ya Chipangano Chatsopano pamene Yesu anabwera padziko lapansi, Israyeli
anamkana ngati Mesiya. Chifukwa cha ichi, Mulungu anadzutsa gulu lina la anthu limene
anasankha kudzionetsera ku dziko. Gulu limeneli likutchedwa Mpingo.
Kutchulidwa koyamba kwa “Mpingo” ndi pamene Yesu analongosola za mmene Mpingo
ungamangidwire.
Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili
ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzaulaka uwo
(Mateyu 16:18).
Mu ndime imeneyi Yesu anaulula kuti Petro adzakhala mmodzi wa miyala ya maziko a uzimu a
Mpingo woyamba. Izi zikutanthauza kuti adzakhala ofunika mmakulidwe ndi maumbidwe ake.
Tanthauzo la Petro ndiye kuti “thanthwe kapena mwala.”
Yesu ananena yekha kuti kwa Iye yekha, “…pa thanthwe ILI ndidzamanga Mpingo wanga.”
Amaonetsera kuti Mpingo udzakhazikika pa Iye. Adzakhala thanthwe limene Mpingo
udzmangidwa. Padzakhala miyala ina yaing’ono (anthu ngati Petro). Koma zoona zake,
okhulupirira amatchedwa “miyala yamoyo” amene ali gawo limodzi la Mpingo:
Inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kun mukhale
ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu
mwa Yesu Kristu (I Petro 2:5).
Maziko a “miyala ya moyo” ndi “Thanthwe.” Thanthwelo ndiye Yesu ndipo limalongosola
malire a Mpingo. Mpingo sukhala mpingo woona pokhapokha wamangidwa pa Yesu Khristu.
Page 60
60
Kwa zaka zambiri Minpingo yambiri yosiyana papanga zolinga za mabungwe komanso
mautumiki. Ngati ali akhazikikadi pa maziko a Yesu, ndiye kuti ali gawo limodzi la chiyanjano
cha okhulupirira cha pa dziko lapansi:
Thupi limodzi ndi Mzimu mmodzi, monganso anakuitanani m'ciyembekezo cimodzi
ca maitanidwe anu;
Ambuye mmodzi, cikhulupiriro cimodzi, ubatizo umodzi.
Mulungu mmodzi ndi Atate wa onse amene ali pamwamba pa onse, ndi mwa onse,
ndi m'kati mwa zonse (Aefeso 4:4-6).
Yesu ananena kuti “makoma a imfa” sadzaulaka mpingo woona. Izi zikutanthauza kuti Mpingo
udzakumana ndi chitsutso chachikulu cha Satana, koma sudzagonjetsedwa.
Buku la Machitidwe limakamba za chitutso choyamba cha mpingo (Machitidwe 8). Kuyambira
mu mbiri kufikra pano, mpingo wakhala ukulandira chitsutso chachikulu, koma udzakhalabe
ndipo udzapitilira kukhalapobe. Udzakwaniritsa zolinga za Mulungu.
MMENE MPINGO UMAKHALIRA
Baibulo limagwiritsa zitsanzo zambiri polongosola mpingo. Zitsanzozi zimaululu zambiri
zokhuza maziko ndi cholinga cha mpingo. Onani zitsanzo za Mbaibulo zotsatirazi zokhudza
Mpingo:
Munthu watsopano: Aefeso 2:14-15
Thupi la Khristu: Aefeso 1:22-23; 5:30; I Akorinto 12:27
Kachisi kapena nyumba ya Mulungu: Aefeso 2:21-22; I Akorinto 3:9,16: I Timoteo 3:15; I Petro
2:5
Ansembe achifumu: I Petro 2:5,9; Chibvumbulutso1:6; 5:10
Mkwati wa Khristu: II Akorinto 11:2; Mateyu 25:6; Aefeso 5:22-32
Okhala mnyumba ya Mulungu: Aefeso 2:19
Nkhosa za Mulungu: Yohane 10:1-29; I Petro 5:3-4; Ahebri 13:20; Machitidwe 20:28
Pali mpingo umodzi koma Mbaibulo ukudziwika ndi magawo ambiri. Ukutchedwa:
Mpingo wa Mulungu: Machitidwe 20:28; I Akorinto1:2; 10:32; 11:22; 15:9; I Timoteo 3:5; I
Page 61
61
Atesalonika 2:14
Mpingo wa Mulungu wamoyo: I Timoteo 3:15
Mpingo wa Khristu: Aroma 16:16
Mpingo wa obadwa oyamba: Ahebri 12:23
Mpingo wa oyera mtima: I Akorinto 14:33
Anthu a Mulungu: Ahebri 4:9; I Petro 2:9-10
CHOLINGA CHA MPINGO MOLINGANA NDI MALEMBA
Pali zolinga zambiri za Mpingo molingana ndi mmene Baibulo limatiuzira:
MALAMBIRO A MULUNGU:
Cholinga chachikulu chimene muntu analengedwera ndicho kulambira Mulungu. Kulambira ndi
cholinga chachikulu cha Mpingo. Onani mavesiwa:
I Petro 2:5,9; I Akorinto 14:26-27; Yohane 4:23-24; Aefeso 2:19-22.
KUTUMIKIRA MU MPINGO:
Mamembala a mu Mpingo akuyenera kutumikirana zosowa za wina ndi mzake:
-Zikhoza kukhala zosowa za kuthupi: Machitidwe 11:27-30; 6:1-6.
-Mamembala ayenera kugawana mwa ufulu zinthuzawo: Machitidwe 2:44; 4:32, 34,37.
-Mamembala ayeneranso kusamalirana pa zosowa za ku uzimu mu thupi la Khristu: Yohane
15:1-7; Aroma 15:1-15; I Akorinto 3:9; Agalatiya 6:1; Akolose 2:16-23; I Atesalonika 2:7-16.
CHIYANJANO:
-Chiyanjano cha Mpingo chakhazikika pa umodzi wa mwa Khristu: Aefeso 4:4-6
-Mpingo umakhala umodzi mwa Khristu: Aefeso 2:11-18. Membala aliyense ndi wofanana
pamoso pa Ambuye: Aefeso 2:19-20.
Page 62
62
-Mpingo ukuyenera kukhala gulu la chiyanjano mmawu, mpemphero, ndi mu ntchito:
Machitidwe 2:41-47; 4:24,32-33; Aefeso 2:20-22; I Yohane.
-Chiyanjano chawo chikuyenera chikhale ndi cholinga chimodzi, maganizo amodzi, moyo
umodzi ndi mtima umodzi: Machitidwe 1:14; 2:46; 4:24,32; 5:12; 15:25
Chiyanjano sikuyenera chikhale kwa mpingo umodzi wokha ayi, komanso pakati pa mipingo ina.
Werengani mavesiwa amene akuonetsera ubale umenewu pakati pa mipingo:
-Amadziwa kuti ali amodzi mwa Khristu ndipo alumikizidwa pamodzi: Machitidwe 15:1; Aroma
15:26-27
-Amalankhulana pafupipafupi ndi wina: Aroma 16:16; I Akorinto 16:19-20; Afilipi 4:23
-Amathandizana wina ndi mzake: Aroma 15:26; I Akorinto 16:1-3.
-Anathandizira ntchito ya atumwi mmadera ena: Afilipi4:15-16
-Anagawana makalata a atumwi: Akolose 4:16.
-Amatumizirana nthumwi wina ndi mzake: Machitidwe 11:22,23,27; 15:1,2; I Akorinto16:3,4
-Amalimbikizana wina ndi mzake pa chikhulupiriro: II Akorinto 1:24; 9:2; I Atesalonika 1:7-10;
2:14
-Amalumikizana pa nkhani ya ulaliki: I Atesalonika 1:8
UTUMWI:
Mpingo cholinga chake ndiko kuchita utumwi osangoti kulambira komanso chiyanjano.
Cholinga cha ana a Israyeli mu Chipangano Chakale ndi Mpingo mu Chipangano Chatsopano
kunali kuulula Mulungu ku dziko lapansi.
Mu Chipangano Chakale, Israyeli anayenera kukhala mboni ku maiko osadziwa Mulungu.
Chimene Mulungu amafuna chinali choti maikowa afike poona Mulungu ndi mphamvu yake
kwa Israyeli. Mu Chipangano Chatsopano, cholingancha Mulungu chinali china. Chollinga
chake chinali kuti mpingo upite ku maiko ngati mboni. Utumwi weniweni wa mpingo ukupezeka
mu Aefeso:
Page 63
63
Kuti mu Eklesia azindikiritse tsopano kwa akulu ndi maulamuliro m'zakumwamba
nzeru ya mitundu mitundu ya Mulungu,
monga mwa citsimikizo mtima ca nthawi za nthawi, cimene anacita mwa Kristu
Yesu Ambuye wathu (Aefeso 3:10-11).
Anatizindikiritsa ife cinsinsi ca cifuniro cace, monga kunamkomera ndi monga
anatsimikiza mtima kale mwa iye,
kuti tikakonzedwe a makwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi zonse
mwa Kristu, za kumwamba, ndi za padziko (Aefeso 1:9-10).
Chidule cha utumwi wa mpingo ndi ichi:
1. Mpingo ukuyenera kuonetsera Yesu ku dziko lapansi ngati Ambuye ndi Mpulumutsi.
Mpingo ukuyenera kutsogolera anthu ku ubale wabwino ndi Yesu kuti athe
kukhululukidwa machimo awo ndi kuyambanso moyo watsopano.
2. Kupyolera mu chiphunzitso ndi ulaliki wa ubatizo wa mmadzi, mpingo ukuyenera
kukhazikitsa okhulupirra mu chiphunzitso, mfundo ndi makhalidwe a chikhristu.
Akuyenera kuphunzitsa anthu ongotembenuka kumene kuti “asunge zinthu zonse”
zimene analamulilidwa mmawu a Mulungu.
3. Mpingo ukuyenera kupanga dongosolo la okhulupirra atsopano kukhala ofunikira mu
chiyanjano cha mpingo.
4. Mipingo yokhazikikayi ikuyenera kubwereza ndondomekoyi kuti akhale ndi okhulupirira
ambiri ndi chiyanjano chochuluka.
Phunzirani zambiri zokhuza utumwi wa mpingo mmavesi awa:
Kufalisa uthenga wabwino kudziko lapansi: Mateyu 5:13-14; 28:18-20; Marko 16:15-16;
Luka 24:45-49; Yohane 20:19-23; Machitidwe 1:8.
Kukhala mchere ndi kuunika kwa dziko lapansi: Mateyu 5:13-16; Afilipi 2:14-16: I Yohane 4:1.
Kuphunzitsa okhulupirita atsopano: Mateyu 28:19-20; Machitidwe 20:27-28; Aefeso 4:11-16; I
Petro 5:1-3.
Page 64
64
MITUNDU YA KUKULA KWA MPINGO
Ngati mpingo ukukwaniritsa cholinga chake cha mmalemba, mitundu inayi yampingo
imapezeka:
KUKULA KWA MKATI:
Kukula kwa mkati ndi kukula kwa uzimu kwa anthu a mumpingo.
KUKULA KOCHULUKA:
Uku ndi kukula kwa mpingo mu chiwerengero kumene kumachitika pamene ntchito yolalikira
uthenga yachitika ndi mpingo. Okhulupirira achilendo amapezeka mkukhala gawo limodzi la
thupi la Khristu.
KUKULA MMADERA:
Mpingo umakula mmadera pamene wayambitsa mpingo wina mudera lina la anthu achikhlaidwe
chofanana.
KUKULA KOLUMIKIZANA:
Uku ndi kukula kwa mpingo pamene wayamba kugawana uthenga kupitilira malire ndi anthu a
dera lina osiyana mtundu, chikhalidwe.
MZIMU WOYERA NDI KUKULA KWA MPINGO
Mzimu Woyera ndi mphamvu ya uzimu imene imapangitsa kukula kwa konse kwa mpingo kwa
mitundu inayi:
Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo
mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi
kufikira malekezero ace a dziko. (Machitidwe 1:8).
Vesi limeneli limatiuza za mmene Mzimu Woyera amapangira:
Kukula kwa mkati: ophunzira alandira mphamvu ya Mzimu Woyera. Izi ziwapangisa iwo kuti
akachitire umboni mwamphamvu.
Kukula kochuluka: Mpingo udzachuluka ku Yerusalemu.
Page 65
65
Kukula mmadera: mpingo udzadzala mipingo ina kumadera a zikhalidwe zofanana.
Kukula kolumikizana: Mpingo udzalumikizitsa kusiyana kwa zikhalidwe pofuna kufikira ena
monga Samariya ndi “malekezero a dziko lapansi.”
Baibulo limaphunzitsa kuti Mzimu Woyera ali ndi mautumiki ambiri. Anali wochitachita pa
kulengedwa kwa dziko, amauzira mawu Mulungu. Analinso wochitachita mu nthawi ya utumiki
wa Yesu pansi pano, ndipo anagwira ntchito zambiri mmaalo mwa okhulupirira.
Mzimu Woyera amaulula choonadi cha uthenga wabwino ndi kuwakokera anthu kwa Mulungu
kuti apulumuke. Mzimu Woyera alinso ndi utumiki wokhudza Satana. Amaberetsa mphamvy ya
uzimu imene imaika malire pa mphamvu ya Satana (Yesaya 49:19). Mautumiki ake onse
akupezeka mu maphunziro a Harvestime International Institute otchedwa “Utumiki wa Mzimu
Woyera.”
Mzimu Woyera alinso ndi utumiki wapaderadera wokhudza kukula ndi kuumba mpingo:
MZIMU WOYERA ANAUMBA MPINGO:
Pa tsiku la pentekosite pa Machitidwe 2:1-4 Mzimu Woyera anapanga Mpingo. Baibulo
limaphunzitsa kuti Mpingo malo opezeka Mulungu omangidwa ndi Mzimu Woyera.
Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera, komatu muli a mudzi womwewo wa
oyera mtima ndi a banja la Mulungu
omangika pa maziko a atumwi ndi aneneri, pali Kristu Yesu mwini, mwala wa
pangondya;
mwa iye cimango conse, columikizika pamodzi bwino, cikula, cikhale kacisi
wopatulika mwa Ambuye;
cimene inunso mumangidwamo pamodzi, mukhale cokhalamo Mulungu mwa
Mzimu
(Aefeso 2:19).
MZIMU AMAKHUDZA MALAMBIRO
Kulambira kwa Mpingo kukuyenera kukhudzidwa ndi Mzimu Woyera:
Page 66
66
Koma ikudza nthawi, ndipo tsopano iripo, imene olambira oona adzalambira Atate
mumzimu ndi m'coonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ace.
Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira iye ayenera kumlambira mumzimu ndi
m'coonadi (Yohane 4:23-24).
Pakuti ife ndife mdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu,
nadzitamandira mwa Yesu Kristu, osakhulupirira m'thupi (Afilipi 3:3).
MZIMU WOYERA ANATSOGOLERA NTCHITO YA UTUMWI:
Izi zikuoneka mu ntchito ya utumwi ya mpingo woyamba:
Ndipo Mzimu anati kwa Filipo, Yandikira, nudziphatike ku gareta uyu (Machitidwe
8:29).
Ndipo anapita pa dziko la Frugiya ndi Galatiya, atawaletsa Mzimu Woyera kuti
asalalikire mau m'Asiya; pamene anafika kundunji kwa Musiya,
Anayesa kunka ku Bituniya; ndipo Mzimu wa Yesu sanawaloleza
Pamene anaona masomphenyawo, pomwepo tinayesa kuturukirakunka ku
Makedoniya, poganizira kuti Mulungu anaitanira ife kulalikira Uthenga Wabwino
kwa iwo (Machitidwe 16:6,7,10).
Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala cakudya, Mzimu Woyera anati,
Mundipatulire Ine Bamaba ndi Saulo ku nchito imene odinawaitanirako
Pamenepo iwo, otumidwa ndi Mzimu Woyera, anatsikira ku Selukeya; ndipo
pocokerapo anapita m'ngalawa ku Kupro (Machitdwe 13:2,4).
MZIMU WOYERA ANASANKHA ATUMIKI:
Mipingo ina imasankha atumiki otumikira mu mpingo. Anthu ambiri amapita ku sukulu
za koleji kapena ku seminale kukaphunzitsidwa ngati atumiki. Koma choyenereza chimene
malemba amanena ndi chakuti atumiki ayenera kuitanidwa ndi kusankhidwa ndi Mzimu
Woyera:
Page 67
67
Tadzicenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani
oyang'anira, kuti muwete Eklesia wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa iye
yekha (Machitidwe 20:28).
MZIMU AMADZODZA ALALIKI:
Paulo analemba kale: Ndipo mau anga ndi kulalikira kwanga sanakhala ndi mau
okopa a nzeru, koma m'cionetso ca Mzimu ndi ca mphamvu (I Akorinto 2:4).
MZIMU WOYERA AMATSOGOLERA ZIGANIZO:
Machitdwe chaputala cha 15 amakamba za mkumano wa atsogoleri umene amakambirana
mavuto osiyanasiyana amene mpingo umakumana nawo. Chiganizo chawo chomaliza
amatsogolera ndi Mzimu Woyera:
Pakuti cinakomer a Mzimu Woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu cothodwetsa
cacikuru cina coposa izi zoyenerazi (Machitidwe 15:28).
MZIMU AMABATIZA MPINGO NDI MPHAMVU:
Buku la Machitidwe limayamba ndi nkhani yaikulu kwambiri:
Ubatizo umenewu unali wamphamvu pa kukula kwa mpingo mkati, chiwerengero, mmadera,
mmalire kumene kukupezeka mbuku la Machitidwe.
Ndipo pakufika tsiku la Penteskoste, anali onse pamodzi pa malo amodzi.
Ndipo mwadzidzidzi anamveka mau ocokera Kumwamba ngati mkokomo wa
mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene analikukhalamo.
Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogawanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa
iwo onse wayekha wayekha.
Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime
ena, monga Mzimu anawalankhulitsa (Machitidwe 2:1-4).
Page 68
68
MAYESO ODZIYETSA NOKHA
1. Lembani Vesi Lotsogolera kuchokera pamtima.
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
2. Kodi Mpingo woona ndi wandani?
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
3. Kodi Mpingo unayamba bwanji?
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
4. Pali zitsanzo zambiri za Mbaibulo zimene zimakamba za Mpingo. Lembani zitsanzo
zitatu zokha.
___________________________ __________________________
____________________________________
5. Tchulani zolinga zinayi za Mpingo zimene mwaphunzira mu phunziroli.
________________ _________________ _____________________
______________________
6. Tchulani ndipo longosolani mwachidule mitundu inayi ya Mpingo.
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
7. Chaputalach chakambapo za zolinga 7 za Mzimu Woyera mogwirizana ndi kukula ndi
mapangidwe a Mpingo. Kodi mungatchule zingati?
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
(Mayankho a mafunsowa akupezeka kumapeto kwenikweni kwa bukuli)
Page 69
69
KUPITILIZA KUPHUNZIRA
1. Izi ndi zina mwa zotitsogolera zimene tingaziwire Mpingo woona. Ndi Mpingo
umene:
-umakhala wolondola mchiphunzitso. Ziphunzitso zonse zimakhazikika mu Mau
olembedwa ndi Mulungu.
-umakhala ndi mamembala obadwa mwatsopano: miyoyo ya mamembalayo imakhala
yosinthika ndi mphamvu ya Mulungu.
-wolambira: umalambira Mulungu mmodzi woonayo Atate, Mwana ndi Mzimu
Woyera.
-olalikira. Umakhala wochitachita mu utumwi ofikira dziko lapansi ndi uthenga
wabwino.
2. Izi ndi zina zotitsogolera kudziwa Mpingo wonama. Ndi Mpingo umene:
-umakhala wonama mchiphunzitso chake: Amasindika mawu ochepa okha ochokera
Mbaibulo ndi kuchotsako ena. Samatenga Mau a Mulungu mmene alili.
Amavomereza ziphunzitso za munthu zimene zimatsutsana ndi Mau a Mulungu.
-ogawikana: amakhala ndi magawano a mu Mpingo ndipo amalakalaka kuyambitsa
kuyambitsa mipatuko mu thupi la Khristu. Onani Aroma 16:17-18; Acts 20:29,30;
Aefeso 4.
-ulamuliro: mpingo wonama umayesera kulamulira miyoyo ndi ntchito za
mamembala mu njira yowalamulira.
-umakhala ndi mamembala osabadwanso: anthu amapitilira kukhala mmakhalidwe
akale a uchimo.
Page 70
70
CHAPUTALA CHA 6
KUKULA KWA MKATI
ZOLINGA:
Pakutha pa chaputalachi muyenera:
Kulemba Vesi Lotsogolera kuchokera pamtima.
Kulongosola za kukula kwa “mkati” kwa Mpingo.
Kupereka tanthauzo la “kukula mu uzimu.”
Kuzindikira zizindikiro za kukula mu uzimu.
Kulongosola utumiki wa Mzimu Woyera mogwirizana ndi kukula kwa Mpingo.
Kuzindikira nyengo za kakulidwe mu dziko lapansi molingana ndi kudziko la ku uzimu.
VESI LOTSOGOLERA:
Pakuti kunamkomera Atate kuti mwa iye cidzalo conse cikhalire (Akolose 1:19).
MAWU OYAMBA
Mu chaputala chomaliza munaphunzira kuti pali mitundi inayi ya kukula kwa dongosolo la
Mulungu pa kuchuluka kwa Mpingo. Mpingo ukuyenera kuchulukana mkati, muchiwerengero,
mmadera komanso mmalire. Phunziro ili tikhala tikukamba za kukula mkati kwa Mpingo.
KUKULA KWA MKATI
Tikamakamba za “kukula mkati” kwa Mpingo, timakamba za kukula ndi kuumbika kwa
mamembala. Mpingo umakula mu uzimu molingana ndi kukula kwa munthu kwa yekha.
Mpingo sukungoyenera kukula kokha mu chiwerengero kudzera ku mmadera, kuchuluka kwa
anthu kapena mmalire, ukuyeneranso kukula mmachitidwe. Kukula mmachitidwe ndiye kuti ndi
kukula mkati ndi kukula ku uzimu. Paulo anakamba za izi pofanizira za kukula mkati mu thupi:
Pakuti kunamkomera Atate kuti mwa iye cidzalo conse cikhalire (Akolose 1:19).
Ndiye kuti “kuchuluka kwa Mulungu” ndiye kuti ndi kukula kwa kuuzimu. Pamene mamembala
akukula mu uzimu, mpingo umakumanandi kukula kwa mkati. Moti thupi lonse la Khristu
limakula ndi kuchuluka kwa chidziwitso cha Mulungu.
Page 71
71
Kukula kwa ku uzimu ndi kuchuluka kwa kukhwima ku uzimu kumene kumatsatira ku kuumba
moyo wa mkhristu wa okhulupirira. Ndi kukula kwa chidziwitso cha Yesu:
Koma kulani n'cisomo ndi cizindikiritso ca Ambure wathu ndi Mpulumutsi Yesu
Khristu (II Petro 3:18)
Uku ndi kukula mwa Khristu:
Koma ndi kucita zoona mwa cikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira iye amene ali
mutu ndiye Kristu (Aefeso 4:15)
Kukula mu uzimu kumatanthauza kuchepetsa umwini ndi kukulitsa moyo wa Khristu mwa iwe:
Iyeyo ayenera kukula koma ine ndicepe (Yohane 3:30)
Kukula mu uzimu sikumabwera nthawi imodzi chifukwa cha kukhala nthawi yaitali ya mkhristu.
Ndi zotsatira za kukula kwa moyo wa chikhristu mwa okhulupirira.
Zizindikiro za kukula mu uzimu ndi:
1. Kuchuluka kwa chidziwitso cha uzimu
2. Kugwirtsa ntchito bwino chidziwitsocho pa moyo ndi utumiki.
3. Kukhala ndi kuya kwa zinthu za uzimu.
4. Kukhala ndi chikondi chachikulu pa Mulungu ndi anthu ena.
5. Kuumbika kwa moyo wa chikhristu mmakhalidwe a uzimu (zipatso za uzimu).
6. Kukula kwa khumbo ndi kuthekera kugawana uthenga wabwino ndi anthu ena.
7. Kukula ndi kugwiritsa ntchito mphatso za uzimu.
Kukula ndi zotsatira za moyo. Ngati pali moyo wa uzimu mu mpingo, kukula kwa mkati
kuzabweretsa kukula mu chiwerengero, mmadera, ngakhale kukula mmalire.
MZIMU WOYERA NDI KUKULA KWA MKATI
Mu chaputala chathachi munaphunzira za utumiki wa Mzimu Woyera ku mpingo. Mzimu
Woyera:
-amapanga Mpingo.
-amatakasa Mpingo.
-amatsogolera ntchito ya umishoni.
-amasankha atumiki.
-amadzodza alaliki ache.
-amatsogolera ziganizo.
Page 72
72
-amabatiza ndi mphamvu.
Kuonjezera zku mautumuki mu mpingo, Mzimu Woyera ali ndi ntchito zina mogwirizana ndi
makulidwe a mkati a mpingo. Izi ndi monga:
KUTSUTSA UCHIMO:
Kukula mu uzimu kumatchingidwa ndi uchimo. Motero Mzimu Woyera amatsutsa tchimo kwa
okhulupirira:
Ndipo atadza Iyeyo, adzatsutsa dziko lapansi za macimo, ndi za cilungamo, ndi za
ciweruziro;
za macimo, cifukwa sakhulupirira Ine;
za cilungamo, cifukwa ndinka kwa Atate, ndipo simundionanso;
za ciweruziro, cifukwa mkuru wa dziko ili lapansi waweruzidwa (Yohane 16:8-11).
Pamene Mzimu Woyera akutsutsa za uchimo, pamenepo ndiye kuti tikhoza kutsatira lamulo…
Ngati tibvomereza macimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama iye, kuti
atikhululukire macimo athu, ndi kutisambitsa kuticotsera cosalungama ciri conse (I
Yohane 1:9).
KUKONZEDWANSO:
Uku kumatanthauza “kusinthika.” Mzimu Woyera amasintha moyo wa okhulupirira. Kusintha
uku kumabweretsa kukula kwa mkati:
Zosati zocokera m'nchito za m'cilungamo, zimene tidazicita ife, komatu monga mwa
cifundo cace anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a
Mzimu Woyera (Tito 3:5).
CHIYERETSO:
Chiyeretso ndi “kupatulikira Mulungu.” Kupatulikaku kumabweretsa kukula ku uzimu:
Koma tiyenera ife tiziyamika Mulungu nthawi zonse cifukwa: ca inu, abale
okondedwa ndi Ambuye, kuti Mulungu anakusankhani inu kuyambira paciyambi,
Page 73
73
mulandire cipulumutso mwa ciyeretso ca Mzimu ndi cikhulupiriro ca coonadi (II
Atesalonika 2:13).
KUKHALA NAYE:
Mzimu Woyera amakhala mmoyo wa wa okhulupirira. Cholinga cha chimenechi ndi
kulimbikitsa chikhalidwe chatsopano chimene chinabwera chifukwa cha chipulumutso:
Kapena simudziwa kuti thupi lanu liri kacisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa
inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha (I A korinto
6:19).
Kodi simudziwa kuti muli Kacisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu
agonera mwa inu? (I Akorinto 3:16).
Cifukwa cace ngati munthu ali yense ali mwa Kristu ali wolengedwa watsopano;
zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano (II Akorinto 5:17).
Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse cilakolako ca thupi.
Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi;
pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazicite.
Ngati Mzimu akutsogolerani, simuli omvera lamulo (Agalatiya 5:16-18).
KULIMBIKITSA:
Kulimbitsa ndi kukula zimayendera limodzi. Umakhala wamphamvu pamene ukukula.
Zimatengera mphamvu kuti munthu ukule. Kukula kwa mkati kumabwera kudzera mu
kulimbikitsidwa kwa Mzimu Woyera:
Kuti monga mwa cuma ca ulemerero wace akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa
Mzimu wace, m'kati mwanu (Aefeso 3:16).
UMODZI:
Umodzi umabweretsa kukula mkati kwa Mpingo:
Koma iye wophatikidwa ndi Ambuye ali mzimu umodzi (I Akorinto 6:17).
Page 74
74
Pakuti monga thupi liri limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri; koma ziwalo zonse
za thupilo, pokhala zambiri, ziri thupi limodzi; momwemonso Kristu.
Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi,
ngakhale Ayuda, ngakhale Ahelene, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse
tinamwetsedwa Mzimu mmodzi (I Akorinto 12:12-13).
KUPEMBEDZERA:
Kupembedzera kwa Mzimu Woyera kumamanga moyo wa wokhulupirira ku uzimu:
Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufoka kwathu; pakuti cimene tizipempha
monga ciyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwiniatipempherera ndi zobuula
zosatheka kuneneka (Aroma 8:36).
Koma inu, okondedwa, podzimangirira nokha pa cikhulupiriro canu coyeretsetsa,
ndi 4 kupemphera mu Mzimu Woyera (Yuda 20).
Mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu,
ndipo poeezera pamenepo cicezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse (Aefeso
6:18).
CHITSOGOZO:
Mzimu Woyera amatsogoza okhulupirira ku choonadi chonse cha Mau a Mulungu chimene
chimabweretsa kukula kwa mu uzimu:
Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa coonadi, adzatsogolera inu m'coonadi conse; pakuti
sadzalankhula za iye mwini; koma zinthu ziri zonse adzazimva, adzazilankhula;
ndipo zinthu zirinkudza adzakulalikirani (Yohane 16:13).
Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a
Mulungu (Aroma 16:14).
MAVUMBULUTSO:
Mzimu Woyera amavumbulutsa choonadi cha Mau a Mulungu kwa okhulupirira chimene
chimabweretsa kukula mu uzimu:
Page 75
75
Koma kwa ife Mulungu anati onetsera izi mwa Mzimu; pakuti Mzimu asanthula
zonse, zakuya za Mulungu zomwe (I Akorinto 2:10).
CHIKONDI:
Anthu amakulu mu uzimu pamene akuonetsera chikondi:
Ndipo ciyembekezo sicicititsa manyazi; cifukwa cikondi ca Mulungu cinatsanulidwa
m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife (Aroma 5:5).
KUFANANA:
Mzimu Woyera amakhala pa yotifanizira ife ndi Yesu mkati mwathu:
Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole
ulemerero wa Ambuye, tisandulika m'cithunzihunzi comweci kucokera kuulenerero
kumka kuulemerero, monga ngati kucokera kwa Ambuye Mzimu (II Akorinto
3:18).
KUPHUNZITSA:
Timakula ku uzimu pamene tikukula mu chidziwitso cha Mulungu cha Mulungu. Mzimu
Woyera ndi mphunzitsi wathu.
Ndipo inu, kudzoza kumene munalandira kucokera kwa iye, kukhala mwa inu,
ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma 9 monga kudzoza kwace
kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga
kudaphunzitsa inu, mukhale mwa iye (I Yohane 2:27).
CHITSIMIKIZO:
Kukaika kumatchinga kukula kwa uzimu. Mzimu Woyera amachotsa kukaika paukutipatsa
chitsimikizo cha chipulumutso:
Mzimu yekha acita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu
(Aroma 8:16).
Ndipo 6 munthu amene asunga malamulo ace akhala mwa iye, ndi iye mwa
munthuyo. Ndipo 7 m'menemo tizindikira kuti akhala mwa ife, kucokera mwa
Mzimu amene anatipatsa ife (I Yohane 3:24).
Page 76
76
UFULU:
Zotchinga zimaika malire pa kukula. Mzimu Woyera amapatsa ufulu pa uchimo ndi
zikhulupiriro za anthu:
Pakuti cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine ku lamulo la
ucimo ndi la imfa (Aroma 8:2)
Koma Ambuye ndiye Mzimuyo; ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu
(II Akorinto 3:17).
KUTONTHOZA:
Nkhawa ndi kufooketsedwa kumatchinga kukula kwa moyo wa uzimu. Mzimu Woyera
amapereka chitonthozo:
…ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'citonthozo ca Mzimu Woyera,
nucuruka (Machitidwe 9:31).
Ndiye Mzimu wa coonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti
silimuona iye, kapena kumzindikira iye. Inu mumzindikira iye; cifukwa akhala ndi
inu nadzakhala mwa inu…
Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, Iyeyo
adzaphunzitsa Inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa
inu (Yohane 14:17,26).
KUDZUTSA:
Umodzi mwa mautumiki a Mzimu Woyera mmoyo wa Yesu unali kudzutsa Iye kwa akufa.
Koma ngati Mzimu wa iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, iye
amene adaukitsa Kristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa,
mwa Mzimu wace wakukhala mwa inu (Aroma 8:11).
Ngati simukukula ku moyo wanu wa uzimu, ndiye kuti mumakhala “wakufa” ku uzimu. Kukula
kumatha. Pakuti ndi mphamvu ya Mzimu Woyera imene imadzutsa inu moyo wanu wa uzimu.
KUONETSERA MPHAMVU:
Page 77
77
Paulo anati:
Ndipo mau anga ndi kulalikira kwanga sanakhala ndi mau okopa a nzeru, koma
m'cionetso ca Mzimu ndi ca mphamvu;
kuti cikhulupiriro canu cisakhale m'nzeru ya anthu, koma mu mphamvu ya
Mulungu (I Akorinto 2:4-5).
Chionetsero cha mphamvu ya Mzimu Woyera chimakulitsa chikhulupiriro chanu mwa Mulungu.
MPHAMVU YA KUCHITIRA UMBONI:
Mphamvu yapadera ya kuchitira umboni ndi chizindikiro kuti munthu wabatizidwa mwa Mzimu
Woyera:
Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo
mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi
kufikira malekezero ace a dziko (Machitdwe 1:8).
Akhristu okhwima mu uzimu adzachulukana pochitira umboni wa uthenga wabwino.
KUBATIZA:
Mpingo umakula mkati kudzera mu ubatizo wa Mzimu Woyera:
Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime
ena, monga Mzimu anawalankhulitsa (Machitidwe 2:4).
Ubatizo wa Mzimu Woyera kukula kwa mphatso za Mzimu ndi zipatso mmoyo wa okhulupirira.
KUPEREKA MPHATSO ZA MZIMU:
Mphatso za mzimu ndi zofunikira pa kukula kwa Mpingo chifukwa “zimalimbikitsa”
wokhulupirira. Moti “kulimbikitsa” kumatanthauza “kumanga ndi kukweza kukula kwa moyo
wa uzimu.” (Muphunzira za mphatso za mzimu muphunziro likubwerali).
KUKWEZA CHIPATSO ZA UZIMU:
Chipatso cha Mzimu ndi chikhalidwe cha Mzimu choululidwa mmoyo wa okhulupirira.
Zimenezi zimatanthauza makhalidwe a uzimu amene ndi zizindikiro mu moyo wa okhulupirira.
Page 78
78
Chipatso cha Mzimu ndi chizindikiro cha kukula mu uzimu. Monga chipatso cha dziko lapansi,
ndi zotsatira za makhalidwe a uzimu amene ndi zotsatira za moyowu. Monga chipatso
chimatenga nthawi kuti chikule mu dziko lapansi, chipatso cha mzimu chimatenganso nthawi
kuti chikule. Zimenezi ndi zotsatira za kukula kwa mkati kwa moyo wa okhulupirira.
Izi ndi zipatso Mzimu Woyera:
Koma cipatso ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza mtima,
cifundo, kukoma mtima, icikhulupirtro, cifatso, ciletso; pokana zimenezi palibe
lamulo (Agalatiya 5:22-23).
Mulungu amafuna inu kuti mukule mu:
Chikondi: chikondi cholama, chisamaliro, ndi kukhuzidwa
Chimwemwe: chisangalalo, kukondwa, kunyadira zimane sizimadalira zochitikaza moyo.
Mtendere: bata, chiyanjano, kudekha, kupanda nkhawa ndi madandaulo, maudani.
Kuleza mtima: kudikira-kuthekera kopilira mu nyengo yowawa, chipliro.
Kufatsa: ulemu kwa anthu ena, kupanda nkhanza, kudekha.
Ubwino: machitidwe a chiyero ndi chilungamo.
Chikhulupiriro: maganizo okhala ndi kudalira pa Mulungu.
Kudekha: kukhala ndi kuthekera koletsa mphamvu.
Kukhazikika: maganizo abwino, ntchito zabwino, kudziletsa.
ZOPANGITSA KUKULA
Mu dzikoli lapansi pali zinthu zimene zimapangitsa kukula kwa zipatso. Zinthu za chilengedwe
zimenezi zimafanana ndi za uzimu zofunika kukula kwa moyo wobereka chipatso. Izi ndi zina
zimene zimafanana:
MOYO:
Kukula mkosatheka popanda moyo. Kukula kwa chpiatso kumayamba kuchokera ku mbewu.
Pamayenera kukhala moyo mu mbewu, kupanda kutero zingakule. Pakufanizira fanizo la ofesa,
“mbewu” ndiye mau a Mulung. Kukula kumabwera kudzera mbewu ya Mau a Mulungu.
Lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda cinyengo, kuti mukakule
nao kufikira cipulumutso (I Petro 2:2).
Yesu anali ndi chionetsero cha Mau a Mulungu, mbewu, ndipo mwa Iye munali moyo:
Mwa iye munali moyo; ndi moyowu unali kuunika kwa anthu (Yohane 1:4).
Page 79
79
Pakuti monga Atate ali ndi moyo mwa iye yekha, momwemonso anapatsa kwa
Mwana kukhala ndi moyo mwa iye yekha (Yohane 5:26).
Yesu anadza kudzafeso mbewu ya moyo yopangitsa moyo wauzimu kukula.
Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga, Ndadza Ine kuti akhale
ndi moyo, ndi kukhala nao wocuruka (Yohane 10:10).
NTHAKA YABWINO:
Mbewu ya Mau a Mulungu imayenera kukhalandi nthaka yabwino kuti ikule bwinobwino.
Werengani fanizo la wofesa mu Marko 4. Mbewu yokhayo imene yagwera panthaka yabwino
imabweretsa kukula kwa ku uzimu:
Ndipo iwo ofesedwa pa nthaka yabwino ndiwo oterewa akumva mau, nawalandira,
nabala zipatso zakupindula makumi atatu, ndi makumi asanu ndi limodzi, ndi
makumi khumi (Marko 4:20).
Mukuyenera kukonzekeretsa “nthaka” ya mtima wanu ndi maganizo anu kuti mulandire Mau a
Mulungu.
MADZI:
Madzi ndi wofunika pa kukula kwa zinthu mu dzikoli. Mulungu analonjeza:
Pakuti ndidzathira madzi pa dziko limene liribe madzi, ndi mitsinje pa nthaka
youma (Yesaya 44:3).
Kutsanulira kumeneku ndi kudzodza kwa Mzimu Woyera kwa madzi amene ndi chizindikiro:
Iye wokhulupirira Ine, monga cilembo cinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda,
kuturuka m'kati mwace (Yohane 7:38).
Madzi a Mzimu Woyera amapangitsa mbewu ya Mawu a Mulungu kuzika mizu mmitima ya
anthu amene ndi okufa mu uzimu:
Pakuti akaulikha mtengo pali ciyembekezo kuti udzaphukanso,
Ndi kuti nthambi yace yanthete siidzasowa.
Ngakhale muzu wace wakalamba m'nthaka, Ndi tsinde lace likufa pansi;
Page 80
80
Koma pa mnunkho wa madzi udzaphuka, Nudzaswa nthambi ngati womera (Yobu
14:7-9).
KUWALA:
Uku ndi kuyankha kuwala kumene kumapangisa kukula mu dziko lapansi. Kukula ku uzimu
kumayamba polandira kuwala kwa uzimu. Kuwalaku ndi Yesu.
Mwa iye munali moyo; ndi moyowu unali kuunika kwa anthu (Yohane 1:4).
Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata ine sadzayenda mumdima,
koma adzakhala nako kuunika kwa moyo (Yohane 8:12).
MPWEYA:
Mpweya umabwera kuchokera ku chilengedwe cha zomera mulengalenga. Mpweya ndi
wofunika pa kukula. Mu Baibulo Mzimu Woyera amafanizidwa ngati mpweya kapena mphepo.
Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau ace, komavsudziwa, kumene
icokera, ndi kumene imuka; cotero ali yense wobadwa mwa Mzimu (Yohane 3:8).
Mzimu Woyera amapumuira mmoyo wa mbewu ya Mau a Mulungu. Kukula ku uzimu ndi
zipatso zimakhala zotsatira.
MPATA:
Mu fanizo la ofesa, kulimbirana mpata kumapangisa kuti mbewu zina zife:
Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mau; ndipo kulabadira
kwa dziko lapansi, ndi cinyengo ca cuma citsamwitsa mau, ndipo akhala wopanda
cipatso (Mateyu 13:22).
Mpikisano wa zinthu za dziko zimatsamwitsa mbewu ya Mau a Mulungu ndi kulepheretsa
kukula kwa uzimu.
MPUMULO:
Nthawi ya mpumulo (yotchedwa yongokhala) imakhala nyengo yapadera ya kubwerezeka kwa
zomera mu dziko lapansi. Imeneyi ndi nthawi ya mpumulo wa zomera ndi nyengo imene ndi
Page 81
81
yachisanu ya kukula kwambiri. Mu nthawi yongokhala, zomera zimaoneka ngati zafa. Koma
zimakhala zisanafe. Mbewu ya moyo imakhala ili mkati.
Nthawi zina munthu kapena mpingo umatha kuoneka ngati sukukula mu uzimu. Koma ngati
mbewu ya Mau a Mulungu yadzalidwa bwino, kukula kwa mkati kudzachitika (Masalmo 1).
Monga ngati mdziko, kungokhala mu uzimu kumabwera pambuyo pa kukula kwambiri ndi
kuumbika. Dikirani modekha pa kukula kwa mkati ndi kuchuluka ku zipatso za mzimu:
Taonani, wolima munda alindira cipatso cofunikatu ca dziko, ndi kuleza mtima
naco kufikira cikalandira mvula ya myundo ndi masika (Yakobo 5:7).
MIZU YAKE:
Mizu ndi yofunikira kulimbitsa ndi kupereka zofunika ku mtengo. Masalmo 1 amatuiza za
mmene mizu ilili mmoyo wa uzimu:
Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipawosakhala pansi pa bwalo la
onyoza.
Komatu m'cilamulo ca Yehova muli cikondwerero cace;
Ndipo m'cilamulo cace amalingima usana ndi usiku.
Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; Wakupatsa cipatso cace pa
nyengo yace,
Tsamba lace lomwe losafota; Ndipo zonse azicita apindula nazo (Masalmo1:1-3).
IMFA:
Nthawi yonse imene mudzala mbewu kti ibereke, zingakhale ndi moyo ngati siyamba yafa kaye:
Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati mbeu ya tirigu siigwa m'nthaka, nifa, ikhala
pa yokha iyo; koma ngati ifa, ibala cipatso cambiri (Yohane 12:24).
Wopusa iwe, cimene ucifesa wekha sicikhalitsidwanso camoyo, ngati sicifa (I
Akorinto 15:36).
Moyo wa uzimu umadalira kufa kwa zinthu zina za dziko lapansi. Umafuna kufa ku tchimo,
zokhumba za dziko, ndi zosangalasa. Kufa ku za dziko kumasatira kukula kwa moyo wachipatso
wofanana ndi Khristu mmoyo wanu.
Page 82
82
KULUMIKIZIKA KU MPESA:
Kuti mubale chipatso mu dziko lapansi nthambi iyenera kulumikizika ku mtengo. Ngati nthambi
yadulidwa ku mtengo umene umapereka moyo ndiye kuti idzafa.
Yesu ndiye mpesa ndipo ife ndi nthambi. Choncho kuti ife tikabale chipatso cha uzimu tiyenera
kusungabe ubale wathu ndi Iye:
Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye wam'munda.
Nthambi iri yonse ya mwa Ine yosabala cipatso, aicotsa; ndi iri y'onse yakubala
cipatso, aisadza, kuti ikabale cipatso cocuruka.
Mwakhala okonzeka tsopano inu cifukwa ca mau amene ndalankhula ndi inu,
Khalani mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Monga nthambi siingathe kubala cipatso pa
yokha, ngati siikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala mwa Ine.
Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zace: wakukhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye,
ameneyo abala cipatso cambiri; pakuti kopanda Ine simungathe kucita kanthu
(Yohane 15:1-5).
KUTSAZA:
Kutsaza ndi kofunikira mu dziko lapansi ngati tikufuna kuti zomera zikhale zoberekana zipatso.
Pamene mlimi atsanza mtengo amadula nthambi zosafunika ndi cholinga chopanga mtengowo
kuti ubale zipatso zambiri. Amachotsa chilichonse chimene chimatchinga makulidwe a mtengo.
Kutsanza ndi kofunikanso ku dziko la uzimu. Kutsanza ku uzimu ndi kukonzedwa ndi Mulungu.
Baibulo limatchula kuti chilango. Pamene Mulungu “atsanza” amachotsa chilichonse chimene
chilepheretsa kukula moyo wanu wa uzimu. Machitidwewa ndi ofunika ngati mufuna kuti
mubale chipatso:
Nthambi iri yonse ya mwa Ine yosabala cipatso, aicotsa; ndi iri y'onse yakubala
cipatso, aisadza, kuti ikabale cipatso cocuruka (Yohane 15:2).
Nthawi zina simukolola zotsatira za kutsanza chifukwa mumloza chala Satana pamene ali
Mulungu kubweretsa zinthu mmoyo wanu kuti akukonzeni (kutsanza). Cholinga cha kukonza
kwa Mulungu chikupezeka pa Hoseya 6:1:
Page 83
83
Tiyeni, tibwerere kunka kwa Yehova; pakuti wang'amba, nadzatipoletsera; wakantha,
nadzatimanga (Hoseya 6:1).
Chilango cha kutsanza chimatsatira kubwerera kwa Mulungu. Pokhapo pamene tabwerera kwa
Iye pamenepo mudzakhala ochitachita ku uzimu ndi kubala chipatso cha Mzimu Woyera.
NYENGO:
Nyengo ndi yofunika pa kukula kwa chipatso. Mu dziko lathuli zipatso za mitundu yambiri
zimakula mu nyengo imene imatetezedwa. Zimakula mnyumba zotchedwa “nyumba zotentha”
pamene pamakhala kutentha kwapadera. Zimatetezedwa ku nyengo imene ili pa dziko.
Mukatenga “nyumba yotentha” mkudzala ndi kuchotsa, mwamsanga chidzafa chifukwa chakhala
pa nyengo yotetezedwa. Sichingalimbe ndi nyengo imene ilipo mdziko. Kulankhula ku uzimu,
simufunika “nyumba yotentha” akhristu amene amaoneka abwino mu nyengo inayake koma
amafota akapezana ndi zenizeni za dziko.
Page 84
84
MAYESO ODIYETSA NOKHA
1. Lembani Vesi Lotsogolera kuchokera pamtima.
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
__________________________________________________________________________
2. Kodi timatanthauza chani tikamakamba za kukula kwa mkati kwa Mpingo?
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
__________________________________________________________________________
3. Kodi kukula mu uzimu ndi chiyani?
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
4. Lembani zizindikiro 7 za kukula mu uzimu.
_____________________ ______________________ ________________
___________________________
_______________________ ______________________ ________________
5. Mwaphunzira njira zambiri za mmene Mzimu Woyera amakhudzira kukula mkati kwa
mpingo. Lembani zimene mungathe:
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
__________________________________________________________________________
6. Mwaphunziranso za nyengo za kakulidwe ka moyo wa uzimu zimene ndi zofanana ndi za
mdziko lapansi. Lembani zimene mungathe.
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
(Mayankho a mafunsowa akupezeka kumapeto kwenikweni kwa bukuli)
Page 85
85
KUPITILIZA KUPHUNZIRA
1. Pamene mtengo wayandikira kufa mu dzikoli, umayenera kuti utsitsimudwe.
Momwemonso Mpingo ukayandikira kufa, chitsitsimutso chimafunika. Kutsitsimula
ndiye kuti “kukhala ndi moyo kawiri.” Werengani mawuwa:
Kulirira chitsitsimutso: Masalmo 85:6 Dongosolo la Mulungu la chitsitsimutso: II
Mbiri 7:14
Werengani mavesiwa amene akukamba za chitsitsimutso mu chipangano chatsopano.
Kodi ndi zinthu ziti zimene zinabweretsa chitsitsimutso? Nanga zotsatira za
chitsitsimutso zinali chiyani?
Chitsitsimutso ku Sinai: Eksodo 32:1-35; 33:1:23
Chitsitsimutso mu nthawi ya Samueli: I Samueli 7:1-17
Chitsitsimutso pa phiri la Karimeli: I Mafumu18:1-46
Chitsitsimutso ku Ninevi: Buku la Yona
Chitsitsimutso mu nthawi ya Asa: II Mbiri 15
Chitsitsimutso mu nthawi ya Hezekiya: II Mbiri 29:1-36; 30:1-27; 31:1-21
Chitsitsimutso mu nthawi ya Yosiya: II Mbiri 34:1-33; 35:1-19
Chitsitsimutso utatha ukapolo: Nehemiya 8:1-18
2. Muchaputala chomalizachi mwaphunzira kuti mpingo umafanizidwa ndi nyumba ya
uzimu yomangidwa pa maziko a Yesu Khristu. Kukula kwa mkati kwa uzimu ndi njira
yomanga pa maziko amenewa. Werengani magawowa:
KUKULA PA KUMANGA
MFUNDO ZIKULUZIKULU:
A. Kodi mukumanga chiyani ku uzimu?
1. Inu ndiye mamangidwe:
Inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu… (I Petro 2:5)
2. Inu ndi mamangidwe a muyaya:
Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tiri
naco cimango ca kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja,
yosatha, m'Mwamba (II Akorinto 5:1)
Page 86
86
3. Mpingo ndi mamangidwe:
…Omangika pa maziko a atumwi ndi aneneri, pali Kristu Yesu mwini, mwala
wa pangondya; mwa iye cimango conse, columikizika pamodzi bwino, cikula,
cikhale kacisi wopatulika mwa Ambuye; cimene inunso mumangidwamo
pamodzi, mukhale cokhalamo Mulungu mwa Mzimu (Aefeso 2:20-22)
B. Pali awiri amene akutenga nawo gawo:
1. Mulungu
…Koma wodzimanga zonse ndiye Mulungu. (Ahebri 3:4).
Akapanda kumanga nyumba Yehova, Akuimanga agwiritsa nchito cabe;
Akapanda kusunga mudzi Yehoya (Masalmo 127 :1)
…Ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la
akufa sadzaulaka uwo (Mateyu 16:18)
2. Munthu: Munthu, mu ubale ndi Mulungu, akuyenera kumanga:
Pakuti ife ndife anchito anzace a Mulungu; cilimo ca Mulungu, cimango ca Mulungu
ndi inu (I Akorinto 3:9)
podzimangirira nokha pa cikhulupiriro canu coyeretsetsa (Yuda 20)
Ndipo iwo amene adzakhala a iwe adzamanga malo akale abwinja; udzautsa maziko a
mibadwo yambiri; udzachedwa Wokonza pogumuka, Wakubwezera njira
zakukhalamo (Yesaya 58:12)
MUSANAYAMBE KUMANGA:
Musanaymbe kumanga muyenera:
1. Muwerengere mtengo wake:
Pakuti ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala
pansi, nawerengera mtengo wace, aone ngati ali nazo zakuimariza? 29Kuti
kungacitike, pamene atakhazika pansi miyala ya ku maziko ace, osakhoza
kuimariza, anthu onse akuyang'ana adzayamba kumseka iye, 30ndi kunena kuti,
Munthu uyu anayamba kumanga, koma sanathe kumariza (Luka 14:28-30)
Page 87
87
2. Khalani otsimikizika:
Ndipo a Solomo anati alimangire dzina la Yehova nyumba… (II Mbiri 2:1)
3. Khalani ndi malingaliro abwino:
Taonani, nditi ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba,
kumpatulira iyo, ndi kufukiza pamaso pace zonunkhira za pfungo lokoma (II
Mbiri 2:4)
4. Kukonzeka:
Pakuti Ezara adaikiratu mtima wace kucifuna cilamulo ca Yehova, ndi kucicita,
ndi kuphunzitsa m'Israyeli malemba ndi maweruzo… (Ezara 7:10)
Ndipo 4 kapolo uyo, wodziwa cifuniro ca mbuye wace, ndipo sanakonza, ndi
kusacita zonga za cifuniro caceco, (Luka 12:47)
TIMANGE BWANJI:
1. Mangani pa maziko abwino:
Munthu wamzeru amamanga pa maziko a Mau a Mulungu…amene simagwa
chifukwa imakhala pa thanthwe (Mateyu 7:24-27)
Maziko abwino ndiye Yesu ndi Mau ake:
omangika pa maziko a atumwi ndi aneneri, pali Kristu Yesu mwini, mwala wa
pangondya (Aefeso 2:20)
Ozika mizu ndi omangirika mwa iye, ndi okhazikika m'cikhulupiriro, monga
munaphunzitsidwa, ndi kucurukitsa ciiyamiko (Akolose 2:7)
Musamalitse mmene mukumangirapa mazikowa:
Monga mwa cisomo ca Mulungu cidapatsidwa kwa ine, ngati mwini mamangidwe
waluso, ndinaika maziko, koma wina amangapo. Koma yense ayang'anire umo
amangira pamenepo. 11Pakuti palibe munthu akhoza kuika maziko ena, koma
amene aikidwako, ndiwo Yesu Kristu.
Page 88
88
Koma ngati wina amanga pa mazikowo, golidi, siliva, miyala va mtengo wace,
mtengo, maudzu, dziputu,
nchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, cifukwa kuti
yabvumbuluka m'moto; ndipo mota wokha udzayesera nchito ya yense ikhala
yotani (I Akorinto 3:10-13)
2. Mangani molingana ndi dongosolo:
Mamangidwe ena aliwonse a Mbaibulo, pamakhala dongosolo la Mulungu. Onani Genesis 6:
Eksodo 25:1 Mbiri 22. Anthu anamvera dongosolo la Mulungu:
Cotero anacita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu,
momwemo anacita (Genesis 6:22)
Dongosolo linali losiyana, koma chomwechonso zinali ndi Mose, Davide, Solomoni, Ezarandi
Nehemiya molingana ndi mmene Ambuye anawalamulira.
Conseci, anati Davide, anandidziwitsa ndi kucilemba kucokera kwa dzanja la
Yehova; ndizo nchito zonse za cifaniziro ici (I Mbiri 28:19)
Ngati simukusatira dongosolo la Mulungu la moyo wanu pa Mau a Mulungu, simudzapambana:
Pakuti sasamala nchito za Yehova, Kapena macitidwe a manja ace,
Adzawapasula, osawamanganso (Masalmo 28:5)
3. Mangani molingana ndi kuthekera kwanu:
Pa zokhudza mamangidwe mu nthawi ya Chipangano Chakale, anthu anapereka molingana ndi
kutherekera kwawo:
Monga momwe anakhoza anapereka ku Cuma… (Ezara 2:69)
4. Mangani mofuna:
Funani kukula mu uzimu:
Anapereka caufulu kwa nyumba ya Mulungu cakulimika pakuzika pace (Ezara
2:68).
Page 89
89
5. Mangani mu mphamvu za Ambuye:
…Motero ndinalimbika mtima, monga umo dzanja la Yehova Mulungu
wanga linakhala pa ine (Ezara 7:28)
6. Mangani mu Umodzi:
…Popeza mitima ya anthu inalunjika kunchito (Nehemiya 4:6)
7. Mangani Mwanzeru:
Nzeru imangitsa nyumba; Luntha liikhazikitsa (Miyambo 24:3)
Mkazi yense wanzeru amanga banja lace; Koma wopusa alipasula ndi manja ace
(Miyambo 14:1)
Nzeru yamanga nyumba yace, Yasema zoimiritsa zace zisanu ndi ziwiri (Miyambo
9:1)
Mulungu adzakupatsa luntha:
Ndipo ndamdzaza nd mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi cidziwitso, ndi
m'nchito ziri zonse (Eksodo 31:3,6)
Nampatsa mfumu Davide mwana waluso, wodziwa nzeru ndi waluntha, ammangire
Yehova nyumba, ndiponso nyumba ya ufumu wace (II Mbiri 2:12)
Mwini luntha ndi Mulungu:
Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa
onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye (Yakobo 1:5)
Page 90
90
CHAPUTALA CHA 7
KUKULA MU CHIWERENGERO
ZOLINGA:
Pakutha pa chaputalachi muyenera:
Kulemba Vesi Lotsogolera kuchokera pamtima.
Kulongosola tanthauzo la kukula mu chiwerengero.
Kulemba chidule cha kukula mu chiwerengero kwa mpingo woyamba wa ku
Yerusalemu.
Lembani chidule cha njira za kukula kwa mpingo mu chipangano chatsopano.
VESI LOTSOGOLERA
Ndipo mau a Mulungu anakula; ndipo ciwerengero ca akuphunzira cidacurukatu
ku Yerusalemu (Machitidwe 6:7)
MAWU OYAMBA
Mu thupi lathuli, ziwalo zambiri zalumikizika ndi mutu. Ntchito zonse za thupi zimabwera
chifukwa zimachokera ku mutu. Yesu ndi mutu amene amapereka chitsogozo cha thupi lake la
uzimu, ndiye mpingo. Yesu anati, “ndizamanga mpingo wanga” (Mateyu 16:18). Mu Baibulo,
njira zake zofuna kukwaniritsa cholinga chake zaululika.
Njira zochulukitsa mpingo zikuyenera kuti zikhazikike pa zimene zinaphunzitsidwa ndi
kuonetsedwa Mmau a Mulungu. Ngati ziwalo za thupi la Khristu, okhulupirira akuyenera
kuchitapo kanthu pa zitsogozo zimene zimachokera ku mutu, ndiye Ambuye Yesu. Chaputala
ichi ndi chimodzi mwa machaputala atatu amene amaika chidwi pa kukula kwa mamembala mu
mpingo. Phunziro ili likukamba zambiri za kukula mu chiwerengero.
KUKULA MU CHIWERENGERO
Kukula mu chiwerengero kumachitika pamene okhulupirira atembenuza munthu kupita kwa
Khristu ndikumutengera ki chiyanjano cha mpingo. Zotsatira za izi ndi kukula kwa mpingo mu
chiwerengero. Kukula mu chiwerengero kukuyenera kuloza ku kuchulukitsa Ufumu wa
Mulungu.
Ngati mpingo wachiwiri unaonjezeka ndi anthu 100 kuchokera ku mpingo wina pa ma thiransifa,
pamenepo kukula mu chiwerengero sikunachitike. Pakhala pali kuchuluka kwa mamembala ku
Page 91
91
mpingo wachiwiri koma chiwerengero mu ufumu sichinachitike. Kukula kwa ufumu
kumachitika pamene membala watsopano akutengedwera kwa Yesu ndi kuphunzitsidwa kukhala
membala odalilika mu thupi la Khristu.
ZIMENE CHIPANGANO CHATSOPANO CHIMANENA
Buku la Machitidwe limakamba za kukula kwa mpingo woyamba ku Yerusalemu mu
chiwerengero. Izi ndi chidule cha mmene zinakhalira:
KAKULIDWE KAKE:
Ndipo m'masiku awa anaimirira Petro pakati pa abale, nati (gulu la anthu
losonkhana pamalo pomwe ndilo ngati zana limodzi ndi makumi awiri)
(Machitidwe 1:15)
Mpingo unayamba mu chipinda cha pamwamba ndi gulu lochepa la ophunzira okwana 120. Pa
tsiku la Pentekosite, anthu okwanira 3,000 anaonjezereka ku mpingo:
Pamenepo iwo amene analandira mau ace anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku
lomwelo anthu ngati zikwi zitatu (Machitidwe 2:41).
Itatha Pentekosite, kukula mu chiwerengero kumachitika tsiku ndi tsiku:
Chiwerengero cha anthu ku Yerusalemu chinakwera mkufika 5,000. Chiwerengerochi panalibe
akazi ndi ana amene analinso gawo limodzi la mpingo:
Koma ambiri a iwo amene adamva mau anakhulupira; ndipo ciwerengero ca
amuna cinali ngati zikwi zisanu (Machitidwe 4:4)
Kumapeto kwake, khamu la athu linaonjezereka:
Ndipo makamaka anaonjezedwa kwa Ambuye okhulupirira ambiri, ndiwo amuna
ndi akazi (Machitidwe 5:14)
Ngakhale iwo amene amatsutsa mpingo anazizwa ndi kukulaku:
Koma m'mene anamva mau awa mdindo wa Kacisi ndi ansembe akulu anathedwa
nzeru ndi iwo aja, kuti ici cidzatani (Machitidwe 5:24)
Page 92
92
Mawu oti anaonjezeredwa anagwiritsidwa ntchito polongosola kukula ku chiwerengero cha
mpingo. Mwamsanga kukula kuja kunakhala kwakukulu moti mawu oti kukuchuka anagwira
ntchito.
Ndipo mau a Mulungu anakula; ndipo ciwerengero ca akuphunzira cidacurukatu
ku Yerusalemu (Machitidwe 6:7)
Kuchokera pa nthawi imeneyi, buku la Machitidwe limatsindika za kuchuluka kwa mipingo
komanso mamembala a mpingo wa ku Yerusalemu. Mipingo yatsopano inadzalidwa mmalo onse
a anthu a mitundu amene ndi odziwika mdziko osachepera za 40. Mwachitsanzo, ku Samariya…
Koma pamene anakhulupirira Filipo wakulalikira Uthenga Wabwinowa Ufumu wa
Mulungu ndi dzina la Yesu Kristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi (Machitidwe
8:12)
Mipingo yaku Yudeya, Galileya, Ludda, Sarona ndi Yopa inakula mu chiwerengero cha anthu:
Pamenepo ndipo Mpingo wa m'Yudeya Ionse ndi Galileya ndi Samariya unali nao
mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'citonthozo ca
Mzimu Woyera, nucuruka (Machitidwe 9:31)
Ndipo anamuona iye onse akukhala ku Luda ndi ku Sarona, natembenukira kwa
Ambuye amenewa (Machitidwe 9:35,42)
Anthu “ambiri anaonjezereka” ku mpingo kudzera mu utumiki wa Myuda mmodzi
wotembenuka:
Cifukwa anali munthu wabwino, ndi wodzala ndi Mzimu Woyera ndi cikhulupiriro:
ndipo khamu lalikuru lidaonjezeka kwa Ambuye (Machitidwe 11:24)
Mavesi atatu akukamba za chiwerenero chachikulu chimene chinaonjezereka ku Antioki:
Ndipo dzanja la Ambuye linali nao; ndi unyinji wakukhulupira unatembenukira
kwa Ambuye.
ndipo m'mene anampeza, anadza naye ku Antiokeya. Ndipo kunali, kuti caka conse
anasonkhana pamodzi mu Mpingo, naphunzitsa anthu aunyinji; ndipo ophunzira
anayamba kuchedwa Akristu ku Antiokeya (Machitidwe 11:21, 24,26).
Pamene Mau a Ambuye amapitilira kulalikidwa ndi kuchuluka, okhulupirira atsopano
amaonjezereka ku mpingo:
Page 93
93
Koma mau a Mulungu anakula, nacurukitsa (Machitidwe 12:24)
KUCHULUKA KUPITILIRA:
Ndime zotsatirazi ndi chidule chabe cha kukula kwa mpingo kumadera ena:
Ndipo mau a Ambuye anabukitsidwa m'dziko lonse. Koma Ayuda anakakamiza
akazi opembedza ndi omveka, ndi akulu a mudziwo (Machitidwe 13:49-50)
Cotero mau a Ambuye anacuruka mwamphamvu nalakika (Machitidwe 19:20)
KUKULA KU IKONIYO
Ndipo kunali pa Ikoniyo kuti analowa pamodzi m'sunagoge wa Ayuda, nalankhula
kotero, kuti khamu lalikuru la Ayuda ndi Ahelene anakhulupira (Machitidwe 14:1)
KUKULA KU DEBE
Ku Debe, ophunzira anatsimikizidwa, kulimbikitsidwa ndi kukhala pamodzi ndi Paulo (Onani
Machitidwe 14:20-21)
KUKULA KU AGALATIYA:
Kotero Mipingoyo inalimbikitsidwa m'cikhulupiriro, nacuruka m'ciwerengo cao
tsiku ndi tsiku (Machitidwe 16:5)
KUKULA KU FILIPO:
Ndipo anatimva mkazi wina dzina lace Lidiya, wakugulitsa cibakuwa, wa ku mudzi
wa Tiyatira, amene anapembedza Mulungu; mtima wace Ambuye anatsegula, kuti
amvere zimene anazinena Paulo (Machitidwe 16:14)
KUKULA KU ATESALONIKA:
Ndipo ena a iwo anakopedwa, nadziphatika kwa Paulo ndi Sila; ndi Ahelene
akupembedza aunyinji ndithu, ndi akazi akuru osati owerengeka (Machitidwe 17:4)
Page 94
94
KUKULA KU BEREYA:
Ndipo ambiri a iwo anakhulupira; ndi akazi a Cihelene omveka, ndi amuna, osati
owerengeka (Machitidwe 17:12)
KUKULA KU AKORINTO:
Ambuye anati “Ndili ndi anthu ambiri mu mzindawu” (Onani Machitidwe 18:8-11). Buku la
Machitidwe limatha ndi Paulo akadali kukulitsabe mpingo, ngakhale anali wa mndende kwa
Aroma:
Ndipo anakhala zaka ziwiri zamphumphu m'nyumba yace yobwereka, nalandira
onse akufika kwa iye,
ndi kulalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Kristu ndi
kulimbika konse, wosamletsa munthu (Machitidwe 28:30-31)
Paulo nalemba kuti zikwi za Ayuda ambiri anabwera kwa Yesu nakhala gawo la
mipingo:
Ndipo pamene anazimva, analemekeza Mulungu; nati kwa iye, Uona, mbale, kuti
ambirimbiri mwa Ayuda akhulupira; ndipo ali naco cangu onsewa, ca pa cilamulo
(Machitidwe 21:20)
MMENE MPINGO UMAKULIRA
Pali njira zambiri zimene mpingo oyamba unakulira:
MASOMPHENYA A UZIMU:
Popanda masomphenya anthu amatayika. (Miyambo 29:18)
Popanda masomphenya a uzimu, anthu amafa ku uzimu. Mpingo woyamba unali ndi
masomphenya a uzimu. Anali masomphenya amene Yesu anapereka kwa ophunzira ake pamene
anawauza kuti….
Onani ndinena kwa inu, Kwezani maso anu, nimuyang'ane m'minda, kuti mwayera
kale kufikira kumweta (Yohane 4:35)
Page 95
95
Masomphenya a uzimu amalumikiza anthu pa cholinga. Masomphenya amatsogolera anthu
kuchitukuko cha machitidwe. Machitidwe monga kumvetsa cholinga, ndi kuwaniritsa
cholingacho komanso njira za kauniuni poonetsetsa kuti cholinga chikukwaniritsidwa.
Masomphenya amatsogolera kukhudzikwa. Pamene Yesu anaona khamu la anthu anakhudzika.
Chinali chikatundu cholemera molingana ndi chidziwitso cha chosowa chawo. Masomphenya
ndi kutukula kwa maonedwe a zinthu molingana ndi Baibulo, kumaliwona dziko molingana ndi
mmene Mulungu amalionera ndi kuvomereza pa zimenezo.
Mpingo woyamba unatenga masomphenya ochulukitsa mpingo kuchokera ku Yerusalemu kupita
ku Yudeya, Samariya ndi malekedzero onse a dziko lapansi. Anali masomphenya ophunzitsidwa
ndi atsogolera awo (Machitidwe 1:8). Pamene anthu ali ndi masomphenya a uzimu
chiyembekezo chimachotsa ulesi ndi umodzi wawo umachotsa mpikisano.
MALO NDI NTHAWI ZOLANDILIKA:
Yesu anaphunzitsa kuti malo ena adzalandilidwa kuposa ena:
Awa amene, khumi ndi awiriwa, Yesu anawatumiza, nawalangiza ndi kuti,
Musapite ku njira ya kwa anthu akunja, ndi m'mudzi wa Asamariya
musamalowamo:
koma makamaka mupite ku nkhosa zosokera za banja la Israyeli
Ndipo yemwe sadzakulandirani inu, kapena kusamva mau anu, pamene
mulikuturuka m'nyumbayo, kapena m'mudzimo, sansani pfumbi m'mapazi anu
(Mateyu 10:5-6,14)
Madera ena komanso magulu ena amalandira uthenga mu nthawi zina kuposa ena. Mpingo
woyamba unagwira ntchito pa zokolola za uzimu zimene zimalandira uthengawo. Pamene Paulo
anakanidwa ku Sunagoge, anaphunzitsa kwina (Machitidwe 9:20-31). Pamene amafuna kupita
ku M’ Asiya mu nthawi yoyamba, Mzimu Woyera anamuletsa (Machitidwe 16:6). Anadzapita
nthawi ina imene analandira uthenga.
Kukula ku chiwerengero kumachitika pamene taika chidwi pa zokolola za mmunda mu nyengo
yake. Izi sizitanthauza kuti mumasiya minda imene sinakonzeke ayi. Mumapitilizabe kufesa mau
a Mulungu, kudikira, kupemphera kuti Mulungu awapangise kulandira uthenga.
NDONDOMEKO YA “PITANI OSATI “BWERANI”
Page 96
96
Mpingo woyamba umagwiritsa ntchito njira “yopita” osati njira “yobwera” ya Chipangano
Chakale mu nthawi ya Israyeli.
Mu nthawi ya Chipangano Chakale mitundu ya anthu imayenera kubwera kwa Israyeli
kudzalandira vumbulutso la Mulungu. Koma mu Chipangano Chatsopano lamulo ndi lakuti
“pitani kudziko lonse lapansi.” Mu Chipangano Chatsopano okhulupirira amatsatira njira
imeneyi. samangokhala pansi kudikirira anthu kuti awapeza kumene iwo akukhala.
WOKHULUPIRIRA ALIYENSE ACHULUKITSE”
Wokhulupirira aliyense wa mpingo woyamba amachuluka pobweretsa okhulupirira atsopano:
Pamenepo ndipo iwo akubalalitsidwa anapitapita nalalikira mauwo (Machitidwe
8:4)
Mpingo ukuyenera kutumiza anthu (MUN ndi akazi) mmagawo onse a moyo. Anthu amene
amakhala ndi mwa chikhulupiriro osti kumangoyankhula. Anthu amene miyoyo yawo inasintha
ndi uthenga wabwino. Msilikali sapambana ku nkhondo pamene wangokhala ku malo
amaphunziro. Wokolola sangokhala mu nkhokwe ndipo nsodzi sangokhala kumtunda
kumadikira.
MAUBALE A ANTHU:
Mu nthawi ya Chipangano Chatsopano uthenga wabwino unafala mwamsanga mmalo amene
anthu anali pa ubale wa mbanja, ndi anzawo. Mwachitsanzo, Yesu anaitana Andreya kuti
amtsate. Mwamsanga Andreya anayamba kugawana uthenga wabwino kwa apabanja ake. Ndipo
anambweretsera Petro kwa Yesu.
Werengani ndimezi zimene zikuonetsera za mmene uthenga unafalikira pakati pa maubale a
anthu:
-Zakeyu ndi banja lake: Luka19
-Banja la mkulu wa ku Kapanawo: Yohane 4:53
-Abale ndi abwenzi a Koneliyo: Machitdwe 10:24,44
-Anthu awiri mnyumba ya Filipo: Machitdwe 16:15 ndi 27-34
-Banja la atsogoleri a Sunagoge: Machitidwe18:8
-Stefano ndi a mnyumba mwake: I Akorinto 1:16
-Amnyumba mwa of Aristobulo ndi Nakiso: Romans 16:10-11
-Onesifolo ndi banja lake: II Timoteo 1:16
-Filemoni ndi banja lake: Filemoni l
NJIRA ZA YESU
Page 97
97
Mu buku lonse la Machitidwe, mpingo woyamba unagwiritsa ntchito njira zimene Yesu
anaphunzitsa ndi kuonetsera. Analalikira uthenga, kuphunzitsa mau, kubatiza atsopano, ndi
kuphunzitsa ophunzira (Mateyu 28:19-20).
Pemphero ndi kuwerenga Mau zinali zofunika kwambiri pa kukula kwa mpingo mu
chiwerengero (Machitidwe 6:4).
Kuphatikiza Mau a Mulungu ndi kuonetsera mphamvu zinachulukitsanso mpingo. Pamene anthu
amachiritsidwa, zozizwa zimachitikanso, ziwanda zimathawa ndipo ambiri amabwera kwa
Ambuye.
(Kuonetsera mphamvu kunali kofunika moti a Harvestime International Institute ali ndi phunziro
lotchedwa “Mfundo Zamphamvu”).
MAGULU A CHIPANGANO CHATSOPANO:
Magulu anali ofunika mu Chipangano Chatsopano pa kukula mu chiwerengero. Mu Machitidwe
6:1-7 pamene vuto labwera, gulu lapadera linapangidwa kuthetsa vutoli. Paulo anaphunzitsa
zagulu lapadera la ophunzira pa sukulu ya mdera (Machitidwe 19:9). Mwanthawi, Paulo
amaphunzitsa gulu lapadera la Ayuda ndi a mitundu (Machitidwe 13:42). Magulu ochepa
amakumana mnyumba (Machitidwe 12).
Mipingo yambiri yapanga dongosolo la anthu amumpingo mwawo kuhkala magulu a ang’ono
kuti akwaniritse cholinga chimene sichingakwaniritsidwe ndi bwino ndi mikumano yaikulu ya
mpingo wonse. Magulu ang’ono amakhala pa ubale, oyendayenda ndi omasuka kutumikira
zosowa za anthu.
UTUMIKI WA MZIMU WOYERA:
Mzimu Woyera ndi mphamvu imene imatsutsa anthu ochimwa ndi kuwakopa kuti alandire
uthenga wabwino. Zotsatira za izi ndi kukhala ndi okhulupirira atsopano amene amakulitsa
mpingo.
Ndipo atadza Iyeyo, adzatsutsa dziko lapansi za macimo, ndi za cilungamo, ndi za
ciweruziro;
za macimo, cifukwa sakhulupirira Ine;
za cilungamo, cifukwa ndinka kwa Atate, ndipo simundionanso; 11za ciweruziro,
cifukwa mkuru wa dziko ili lapansi waweruzidwa (Yohane 16:8-11).
Page 98
98
MPHATSO ZA MZIMU:
Kukula kwa munthu kumafuna kukula kwa gawo lolimba pofuna kulimbitsa ndi kuthandiza
kuchulukana nkwa ma selo. Kuti thupi la Khristu likule, gawolinso ndi lofunika. Yesu ananena
kuti zokolola zapsa, koma ogwira ntchito ochepa. Ngati ogwira ntchito achepa, ndiye kuti
tigwirizane kuti tikolole zokolola.
Pa cholinga ichi, Mzimu Woyera amapereka mphatso ndi mautumiki osiyana mu mpingo ndi
cholinga chogwira ntchito ya utumiki. Mphatso za Mzimu ndi kuthekera kwa uzimu kopatsidwa
ndi Mzimu Woyera kopangitsa ntchito ya utumiki. Mukhoza kuwerenga mavesi awa:
Aroma 12:1-8, I Akorinto 12:1-31, Aefeso 4:1-16, I Petro 4:7-11
Mulungu ali ndi malo mu mpingo amene ali wokhulupirira:
Koma tsopano, Mulungu anaika ziwalo zonsezo m'thupi, monga anafuna (I
Akorinto 12:18)
Membala aliyense ali ndi malo amene Mulungu anamusankhira. Amapatsidwa mphamvu kuti
akwaniritse cholinga mu mpingo kudzera mu mphatso za Mzimu Woyera. Pamene okhulupirira
akupezeka pa malo amene Mulungu wamusankhira ndi kuyamba kugwiritsa mphatso yake,
mpingo umayamba kuyenda bwino. Mulungu amaufanizira ngati mmene thupi la munthu
limagwirira ntchito pamene chiwalo chilichonse chimachita ntchito yake. (I Akorinto 12:1-31).
Munthu aliyense ndi wofunika pa ntchito ya utumiki, monganso mmene lilili thupi lathu:
Ndipo dise silingathe kunena kwa dzanja, Sindikufuna iwe, kapenanso mutu kwa mapazi,
Sindikufunani inu. 22Koma makamakatu ziwalozo zoyesedwa zofoka m'thupi, zifunika (I
Akorinto 12:21-22).
Harvestime International Institute mu phunziro lawo amalitcha “Utumiki wa Mzimu Woyera”
limapereka tsatanetsatane wa mphatso za uzimu. Pa chifukwa ichi, chidule chokha
chaperekedwa:
Mphatso zapadera za utsogoleri:
Pali ma udindo a utsogoleri amene Mulungu amawaika ndi kuwasankha ena mu mpingo:
Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi enaaneneri; ndi ena alaliki; ndi ena
abusa, ndi ena aphunzitsi (Aefeso 4:11)
Atsogoleri apadera operekedwa ndi Mulungu ndi monga:
Atumwi:
Page 99
99
Mtumwi ndi amene ali ndi kuthekera kwapadera kutukula mpingo watsopano mmadera komanso
mu zikhalidwe osiyanasiyana ndipo amayang’anira mipingo ngati woyang’anira. Mtumwi ndiye
kuti “wotumidwa” amene watumidwa ndi mphamvu yonse komanso ulamuliro wochita mmalo
mwa wina.” Mtumwi ali ndi ulamuliro wapadera kapena kuthekera kofalisa uthenga wabwino
kumadera ambiri ku dziko lapansi popanga okhulupirira. Masiku ano mpingo ukuwatchula
atumwi ngati wodzala mipingo.
Aneneri:
Pali magawo awiri a uneneri. Loyamba ndi mphatso yapadera yokhala mneneri. Ina ndi mphatso
yolankhula uneneri. Mwachidule, uneneri ndi kulankhula pansi pa kuuzilidwa ndi Mulungu. Ndi
kuthekera kwapadera kolandira ndi kulankhula uthenga wa Mulungu kwa anthu ake. Munthu
amene ali mneneri ali ndi mphatso ya utsogoleri yapadera ya uneneri komanso mphatso
yolankhula uneneri.
Alaliki:
Mlaliki ali ndi kuthekera kwa kogawana ndi uthenga wabwino ndi anthu osakhulupirira ndi
cholinga kuti anthuwa akhale mu thupi la Yesu. Tanthauzo la “mlaliki” ndi amene amagawa
uthenga wabwino.
Abusa:
Abusa ndi atsogoleri amene amakhala nthawi yaitali yoyamg’anira moyo wa uzimu wa gulu la
okhulupirira.
Aphunzitsi:
Aphunzitsi ali ndi kuthekera kolankhula Mau a Mulungu cholinga choti adziwitse anthu ndi
kugwiritsa ntchito zimene aphunzirazo. Mphunzitsi ndi amene ali ndi mphatso yophunzitsa
komanso amakhala atsogoleri a mu mpingo.
Mphatso zisanu za utsogolerizi zimagwira ntchito pamodzi ndi cholinga chokulitsa mpingo.
Atumwi amakulitsa mpingo polalikira uthenga wabwino ku madera osiyanasiyana ndi kukhala
ndi okhulupirira atsopano. Mulungu amachita zozizwa ndi zodabwitsa pofuna kuthandiza kukula
kwa uthenga wabwino. Atumwi amapereka utsogoleri wapadera ku mpingo umene awudzutsa.
Udindo wenweni wa iwo amene ali ndi mphatso ndi kuthandiza okhulupirira ena kuzindikira ndi
kugwiritsa ntchito mphatso zawo za uzimu (Aefeso 4:11-16). Ntchito ya utumiki imafuna
kuchitachita kwa onse. Pamene thupi la Khristu siligwira ntchito moyenera, mamembala ofooka
amatengedwa ndi mosavuta ndi ziphunzitso zonama (Aefeso 4:14).
Ichi ndi chidule cha mphatso za uzimu zopatsidwa kwa okhulupirira:
Mphatso zolankhula:
Page 100
100
Mphatso izi zimatchedwa “zolankhula” chifukwa zimakhudza kulankhula momveka (mokweza).
Mphatsozi ndi monga uneneri, kuphunzitsa, chilimbikitso, mawu a nzeru (kuthekera kolandira
chidziwitso cha mmene zinthu zikhalire), mawu a chidziwitso (kuthekera komvetsa zinthu
zimene ena sadziwa ndipo sangamvetse ngakhale kutha kugawira kwa ena.
Mphatso zotumikira:
Mphatso izi zimatumikira mpingo pothandiza ndondomeko, dongosolo ndi chithandizo cha ku
uzimu kapena kuthupi.
Kutumira: kuthekera kogwira ntchito ya Ambuye, kumasula ena ndi zina.
Thandizo: kuthandiza ena mu ntchito za Ambuye powachulukitsa kuti azichita bwino.
Utsogoleri: kuthekera kokhala ndi zolinga zogwirizana ndi Mulungu ndi kuuza ena za izi.
Munthu amene ali ndi mphatso imeneyi amalimbiktsa ndi kutsogolera ena kuwaniritsa cholinga
cha Mulungu ku ulemerero wa dzina lake.
Dongosolo: mphatsoyi imatchedwa “maboma” Mbaibulo. Munthu amene ali ndi mphatsoyi
amakhala ndi kuthekera kotsogolera, kulongosola, ndi kupanga ziganizo mmalo mwa ena.
Kupereka: kuthekera kwapadera kopereka zinthu, ndalama, nthawi, mphamvu ndi luso ku ntchito
ya Mulungu.
Kuonetsa chifundo: chifundo chapadera ndi kuthekera kothandiza iwo akuvutika.
Kuzindikira mizimi: kuthekera kokhalandi kawuniwuni wa anthu, ziphunzitso ndi nyengo ndi
kutsimikiza ngati zikuchokera kwa Mulungu kapena Satana.
Chikhulupiriro: munthu wa chikhulupiriro amakhala ndi kuthekera kokhulupirira zinthu pa
kulimba mtima ndi kudalira Mulungu mu nyengo zovuta.
Kuchereza alendo: kuthekera kopereka chakudya ndi malo ndi zinthu zina kwa iwo amene ali ndi
zosowa.
Mphatso za zozizwa:
Izi ndi zozizwa za umulungu za mphamvu ya Mulungu kudzera mwa okhulupirira pofuna
kuwaniritsa Mau a Mulungu.
Malilime: kuthekera kolandira ndi kulankhula uthenga wa Mulungu kupita kwa anthu mwa
ziyankhulo zachilendo.
Kumasulira: kuthekera kodziwitsa uthenga mu chilankhulo chomveka cha amene alankhula ndi
malilime ena.
Page 101
101
Zozizwa: kudzera mwa munthu amene ali ndi mphatso ya kuchita zodabwitsa za Mulungu
amachita mwamphamvu ya Mulungu kuposa ya chilengedwe.
Machiritso: munthu ameneyi amakhala ndi kuthekera kolola mphamvu ya Mulungu kuwombola
moyo posagwiritsa ntchito njira zachilengedwe.
MAUTSOGOLERI ENA A MBAIBULO
Okhulupirira amene ali ndi mphatso zapadera si omwewa amene ali ndi utsogoleri mu Mbaibulo
kuti atumikire mu mpingo. Palinso ma udindi ena monga akulu a mpingo, oyanga’anira amene
akupezeka mu Chipangano Chatsopano. Maudindo amenewa ndi ofunikiranso pa kukula kwa
mpingo.
Maudindo amenewa ndi osiyana ndi mphatso za utsogoleri zimene mwaphunzira. Awa ndi
maudindo apadera amene anakhazikitsidwa ndi mpingo wakale othandizira kukula kwa mpingo
mu chiwerengero. Mukhoza kuwerenga Machitidwe 6:1-7 za mmene analili mu mpingo
woyamba.
Zimene mpingo wakale umachita zinali cholinga cha Mulungu kuti zikhale chitsanzo chathu.
Maudindowa akhoza kugwiranso ntchito lero lino. Cholinga cha maudindo amenewa ndi
kuthandiza iwo amene ali ndi mautumiki a mphatso zapadera monga za atumwi, aneneri, alaliki,
abusa ndi aphunzitsi.
Dziwani: mawu oti “akulu a mpingo” anayamba kugwiritsidwa ntchito mu Eksodo 3:16 pofuna
kunena za Israyeli. Pali mavesi ambiri amakamba za akulu a Israyeli mu Baibulo. Akuluwa ndi
osiyana ndi amene anali ndi utsogoleri wa mpingo woyamba.
ZOWAYENEREZA A BISHOPO NDI AKULU A MPINGO
Werengani mavesi ndipo phunzirani zina mwa zinthu zimene atumiki akuyenera kukhala:
I Timoteo 3:2-12, Tito 1:6-9 ndi Aroma 16:2
Page 102
102
MAYESO ODZIYETSA NOKHA
1. Lembani Vesi Lotsogolera kuchokera pamtima.
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
__________________________________________________________________________
2. Kodi chimachitika ndi chiyani pamene mpingo ukukula mu chiwerengero?
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
__________________________________________________________________________
3. Lembani chidule cha mmene mpingo woyamba unakulira ku Yerusalemu.
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
4. Pansipa pali njira za kukula kwa mpingo mu Chipangano Chatsopano. Lembani
mwachidule pa pepala lina za mmene zinagwirira ntchito kuti mpingo ukule ku
Yerusalemu.
-Masomphenya a uzimu
-Nthawi ndi malo amene uthenga wabwino umalandilidwa
-"Pitani" osati "bwerani" ngati njira
-Okhulupirira aliyense achulukane
-Maubale
-Njira za Yesu
-Magulu
-Khomo lililonse
-Utumiki wa Mzimu Woyera
-Mphatso ndi maudindo a uzimu
(Mayankho a mafunsowa akupezeka kumapeto kwenikweni kwa bukuli).
Page 103
103
KUPITILIZA KUPHUNZIRA
1. Pa nkhani ya kukula kwa mpingo mu chiwerengero pali zinthu zitatu zofunika. Mzimu
wa Mulungu (Machitidwe 1-11, Mau a Mulungu (Machitidwe 12:20) ndi munthu wa
Mulungu (Machitidwe 21-28).
2. Magulu a padera a uthumi anali amodzi amene amene anabweretsa kukula kwa mpingo
wakale. Awa ndi ena mwa magulu a padera a utumuki amene mukhoza
kumawapempherera mu mpingo mwanu:
-Kuphunzitsa obadwa mwatsopano
-Akazi atsopano ndi oyembekezera
-Ana
-Achinyamata
-Achikulire
-Mabanja atsopano
-Osakwatiwa / osakwatira
-Utumiki wa iwo amene ali mu msinga za mowa, fodya, mankhwala ozunguza bongo.
-Utumiki wa abambo
-Utumiki wa amayi
-Amasiye, osiidwa banja
-Olumala
3. Magulu onse amene ali mu mpingo amafuna mtsogoleri. Onetsetsani kuti mtsogoleri
amene akutsogolera ali ndi zomuyenereza kukhala mtsogoleri molingana ndi Baibulo.
4. Kafukufuku wa kukula kwa mpingo anachitika ku Amerika ndipo anapeza zinthu zimene
zimakuluitsa mpingo mu chiwerengero. Zina mwa izo ndi izi:
Utsogoleri wa uzimu wamphamvu
Ulaliki wa kathithi
Kuonetsera mphamvu za Mzimu woyera
Maziko a chuma amphamvu
Mphatso ndi zipatso za Mzimu
Pemphero
Mautumiki osiyanasiyana
Kugwiritsa ntchito Baibulo
Kukamba za Yesu yekha basi.
Page 104
104
CHAPUTALA CHA 8
KUKULA MMADERA
ZOLINGA:
Pakutha pa chaputalachi muyenera:
Kulemba Vesi Lotsogolera kuchokera pamtima.
Kupereka tanthauzo la “kukula mmadera”
Kupereka tanthauzo la “kudzala mpingo”
Kuomba mkota pa kukula mmadera kwa mpingo wa chipangano chatsopano.
Longosolani za mmene mpingo umachulukira kudzera mmadera.
Kudziwa njira zinayi zimene mpingo ungayambire
Kudziwa mitundu itatu ya kukula mmadera kwa mpingo.
Lembani zimene Baibulo limafuna posankha madera amene mungadzaleko mipingo
Longosolani uthenga umene ungayambitse mpingo.
VESI LOTSOGOLERA:
Kotero Mipingoyo inalimbikitsidwa m'cikhulupiriro, nacuruka m'ciwerengo cao
tsiku ndi tsiku (Machitidwe 16:5)
MAWU OYAMBA
Ophunzira analamulidwa ndi Yesu kuti akhale mboni ku Yerusalemu, Yudeya, Samariya ndi
malekedzero a dziko lapansi (Machitidwe 1:8).
Monga mwaphunzira chaputala changothachi, mpingo wa ku Yerusalemu unachuluka kwambiri.
Gawo lina mu dongosolo la Mulungu linali kukulitsa mmadera. Mpingo wa ku Yerusalemu
unayenera kuyambitsa mipingo ina mu mizinda ya Ayuda.
KUKULA MMADERA
Kukula mmadera kumayamba pamene mpingo wayambitsa mpingo wina mu dera la anthu a
chikhalidwe chofanana. Mpingo watsopanowo umakhala wina wochokera ku mpingo “waukulu”
monga ngati mwana akakhala ndi makolo ake mdzikoli.
Ngati mpingo “waukuluwo” uli wokhwima mu uzimu, mpingo watsopanowo udzakulanso
momwemo. Ngati pali mavuto mu mpingo “waukulu” mpingo watsopanowo udzakhalanso ndi
ndi mavutowo. Izi ndi chifukwa chake mkofunika kwa mpingo kuti uyambe wakula mkati
usanayambe kuganiza zoyambitsa mpingo kwina.
Mawu oti “Kudzala mpingo” ndi mawu amene timagwiritsa nchito pokamba za kukula mmadera
ndi kubweretsa kukula kwa mpingo. Mawuwa amagwiritsidwa ntchito chifukwa mmodzi
Page 105
105
“amadzala” mpingo watsopano ngati mlimi adzala mbewu munthaka. Mu dothi la nthaka,
mbewu idzakula ngati yatsopano monga ngati “makolo” amene mbewuyo inachokera.
Mawu oti “kudzala” amafunika chifukwa sizikwanira pa “kulongosola” mpingo umene suyenera
mu chikhalidwe cha anthu. Sizikwanira “kungoyambitsa” mpingo mkuwusiya kuti uzivutika.
Umayenera “kudzalidwa” zimene zikutanthauza kuti umaikizidwa, kukulitsidwa ndi kupitilira
moyo wa uzimu.
KUKULA KWA MPINGO MMADERA MCHIPANGANO CHATSOPANO
Kuchuluka kumachitika pogawana. Ndipo kugawana ndi njira yoyamba yofunika imene
Mulungu amachulukitsira. Ngati mwadala sitikusankha kugawana ndi kuchulukana, Mulungu
adzalola zinthu zina zipangise. Machitidwe 8 amakamba za chizunzo chachikulu pa okhulupirira
ku Yerusalemu. Chizunzochi chinabweretsa kugawana ku mpingo wa ku Yerusalemu pakuti
anthu anathawa kupita ku mizinda ina.
Pamene anthu amathawa ku Yerusalemu, “kumene amapitako amalalikira Mau” (Machitidwe
8:4). Obadwa mwatsopano amapezeka ndipo mipingo yatsopano imadzalidwa. Mipingo imrneyi
imakulitsa mpingo “waukulu” wa ku Yerusalemu.
Mpingo wa Chipangano Chatsopano sunakule mmadera podzala mipingo ina yokha ayi,
komanso unalumikiza danga loyambitsa mipingo yambiri mu madera ena. Muphunzira izi mu
phunziro la “kukula kwa mpingo kolumikiza maiko” mu chaputala chikubwerachi.
Mbiri ya kukula kwa mpingo mmadera mu buku la Machitidwe inayamba ku Yerusalemu,
Yudeya, Galileya, Ludda, Sarone ndi Ku Yopa. Awa anali madera a chikhalidwe cha Ayuda. Si
munthu wokhulupirira payekha amene akachuluka ku uzimu, koma mipingo inachulukanso mu
chiwerengero pamene mpingo wa ku Yerusalemu umakula pochitira umboni
mderalo...Machitidwe 16:5
MMENE MIPINGO INAKULIRA MMADERA
Pali njira zimene mpingo watsopano umayambira:
1. Mpingo wina umayambitsa mpingo umzake.
2. Mipingo kugwirizana kuyambitsa mpingo wina.
3. Mpingo waukulu kugawana kupanga mipingo iwiri kapena yoposera apo.
4. Wokhulupirira mmodzi akhoza kukuyambitsa mpingo. Amene ali ndi mphatso ya uzimu
ya utumwi angatero mosavuta. Munthu ameneyi nthawi zina amatchedwa “wodzala
mpingo.”
Muzonse izi, kuchulukana kumachitika kudzera mu kufalisa uthenga pokhala ndi
okhulupirira atsopano.
MITUNDU YA KUKULA KWA MPINGO MMADERA
Mipingo yatsopano imakhala ndi makulidwe osiyana a mmadera:
Page 106
106
1. MIPINGO KUMATUMIKIRA KU MADERA:
Iyi ndi mipingo yokhazikitsidwa ndi cholinga chotumikira ku madera, mmidzi, kapena mu
mzinda. Izi zikhoza kukhala zotsatira za ulaliki umene waitana gulu la anthu okhulupirira mdera.
Ikhoza kukhazikitsidwa kuti itumikire anthu amene sanafikilidwe ndi uthenga kapena ku malo
kumene uthenga sulandilidwa.
2. MIPINGO YOTUMIKIRA KU MAGULU A MITUNDU YA ANTHU:
Chiyanjano cha mautumiki awa amtumikira ku magulu a anthu amene ali ndi zikhalidwe,
ziyankhulo komanso mitundu yofanana. Mwachitsanzo mpingo ukhoza kuyamba kwa anthu
amene amalankhula Spanishi koma sangamve chingerezi ngati “chiyankhulo” chawo choyamba.
3. MIPINGO YOKHALA NDI CHOLINGA CHAPADERADERA:
Mpingo ukhoza kukhazikitsidwa ndi cholinga chapedera: Mwachitsanzo, mpingo ukhoza
kudzalidwe kufupi ndi malo amene ophunzira amachitirako maphunziro kuti azitumikira
ophunzira.
ZOFUNIKA TIKAMAYAMBA KUKULITSA MPINGO MMADERA
Baibulo limaphunzitsa zinthu zimene ndi zofunikira pokulitsa mpingo polalikira uthenga
wabwino pamene tikufuna kukhazikitsa mipingo. Zofunikirazo ndi izi:
OSAFIKILIDWA:
Chinthu choyambirira ndi anthu osafikilidwa. Paulo anati:
Pakuti, amene ali yense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.
Ndipo iwo adzaitana bwanji pa iye amene sanamkhulupirira? ndipo
adzakhulupirira bwanji iye amene sanamva za iye? ndipo adzamva bwanji
wopanda wolalikira (Aroma 10:13-14)
Kumalo kumene kulibe umboni wa uthenga wabwino kukuyeneran kukhala koyamba.
Werengani fanizo la nkhosa mu Luka 15:3-7. Chinthu choyamba chinali pa nkhosa yotaika, osati
pa zomwe zinali nkhola.
OLANDIRA:
Mwaphunzira mu phunziro lotsiriza za kufumikira kwa kulalikira kwa munda wa uzimu umene
uthenga umalandirika. Yesu anaphunzitsa mu Mateyu 10:13-15; Luka 8:5-15) ndi Paulo
analankhulanso (Machitidwe 13:42-51). Yesu ndi Paulo sanakane za malo osalandilika.
Anapitilira kulalikira uthenga kwa iwo ndikuchenjeza za chiwereuzo cha Mulungu. Koma
anayambirira kwa anthu amene amalandira uthenga.
Page 107
107
KUYAMBA MIZINDA, KENAKO MADERA A KUMUDZI:
Iyi inali njira imene Paulo anagwiritsa ntchito imene muphunzira zambiri mukafika mu chaputala
chikubwerachi. Mizindi ili ndi chiwerengero chambiri cha anthu. Anthu ambiri amapita ku
kukachita malonda ku mizinda. Anapitilira kulalikira uthenga ndi kuchenjeza za chiwereuzo cha
Mulungu. Pamene mukufikira anthu ambiri mi mizinda, iwowa amabwerera ku midzi
kumakagawira anthu uthenga wabwino ndi kudzala mipingo yatsopano.
Kaya ndi zokhuza za kusintha kwa zikhalidwe, machitidwe a moyo, malamulo, kusintha
kumeneku kumayamba ku mizinda kenako kumudzi. Pamene mwafikira mizinda ndi uthenga
wabwino, umafalikira kumalo konse kwa deralo mpakana ku midzi.
UTHENGA
Uthenga wa iwo amene amadzala mipingo ndi wakuti:
UTHENGA WA MBAIBULO:
Mipingo yatsopano inabadwa chifukwa cha iwo amene sanatembenuke mtima atatha kumva
uthenga wabwino ndi kulandira Yesu kukhala Mbuye ndi mpulumutsi wa moyo wawo. Pamene
kulalikira kuli kochokera Mbaibulo, kumakhala ndi ulamuliro wa Mulungu. Omvera amadziwa
ndi kuchitapo kanthu pa za mphamvu ya Mau a Mulungu.
WOKAMBA ZA MKRISTU:
Yesu ndiye mwini wa uthenga umene umachulukitsa mipingo. Anthu akuyenera kudziwa Yesu
ndi ndani, kufunikira kwa utumuki wake wa padziko lapansi, imfa yake, ndi kuuka kwake kwa
akufa. Akuyenera kuphunzitsaidwa za mmene angachitire ndi kulandira uthenga wabwino wa
chipulumutso ndi moyo wosatha.
UTHENGA WOKHAZIKIKA PA CHOSOWA:
Anthu amachitapo kanthu pa uthenga umene ukukumana ndi chosowa chawo. Chitsanzo cha ichi
ndi Yesu ndi mkazi pa chitsime (Yohane 4). Uthenga wake ukhakhazikika pa pa chosowa chake
pa madzi akumwa.
MMENE TIGZDZALIRE MPINGO WATSOPANO:
Maphunziro ambiri a Harvestime International Institute amakamba zambiri za mmene
tingadzalire mpingo watsopano. Ngati mukuphunzira phunziroli la Harvestime Institute mu
ndondomeko yawo, phunziro limene mukuphunzirali lili gawo limodzi la mapgunziro a Mfundo
za Baibulo za kuchulukitsa.
Pofuna kudzala ndi kulongosola mipingo, mukuyenera kuphunzira maphunzirowa. Pakadali pano
yambani kupemphera chitsogozo cha Mulungu cha kumene akufuna iye kuti mukule. Ngati muli
Page 108
108
mbusa wa mpingo, musadwabwe pa nkhani yoti muchulukane. Mwaphunzira kale kuti
kuchuluka ndi chifuniro cha Mulungu.
Pemphero lanu likhale pa kumene mukufuna kudzala mpingo watsopano ndi nthawi imene
muchite chifukwa nthawi ndi malo ndi zofunika pa zokolola za uzimu. Mukuyenera kuchulukana
ku malo oyenera komanso pa nthawi yabwino.
MIPINGO YATSOPANO IKUYENERA KUKULA
Monga mwana akabadwa mdzikoli, mpingo watsopano ukuyenera kudalira “kholo” la mpingo pa
kukula kwake. Koma pamene mpingo watsopano ukukula, ukuyenera kukhala osiyana, thupi la
okhulupirira lochitachita, ndi kuthekera kwa kuchulukana ku uzimu pa kuberekana. Ichi ndi
chitsanzo cha mipingo imene Paulo anadzala.
Mpingo wadera ukuyenera kukula kuchokera mu mfundo za Mmalemba zimene zimakamba za
“Kukula kwa Mpingo mu chiwerengero.” Kuti ukule bwino mpingo uliwonse watsopano
ukuyenera:
1. KUMVETSA CHOLINGA CHAKE:
Madongosolo onse a mu mpingo akuyenera kugwirizana ndi zolinga za Mpingo.
Harvestime International Institute ali ndi phunziro la “Dongosolo pa Zolinga” limene
limalongosola izi mwatsatane.
2. KUMVETSA MFUNDO ZA MMBAIBULO ZA DONGOSOLO:
Izi ndi monga mphatso za uzim ndi mautumiki a mumpingo ndi mpaphunziro a
okhulupirira atsopano kuti akhala atsogoleri a ku uzimu otha kugwiritsa ntchito mphatso
zawo. Harvestime International Institute ali ndi phunziro la “Dongosolo la Mfundo za
Mbaibulo” ndi “Dongosolo pa Zolinga” amene adzakuthandizani pophunzira.
3. KUMETSA ZOMUYENEREZA MTSOGOLERI ZA MBAIBULO:
Harvestime International Institute ali ndi phunziro la “Dongosolo la Mfundo za
Mbaibulo” limene lingakuthandizeni pa maphunziro anu.
4. KUPHUNZITSIDWA MAZIKO A CHIKHULUPIRIRO:
Maphunziro a Harvestime mu bukhu la “Kukhala Wachiwiri” a Harvestime International
Institute azakuthandizani kukwaniritsa zolinga zanu.
5. KHAZIKIKANI PA MAFUNSO ENIENI:
Mafunsowa ali ndi zinthu monga:
Page 109
109
-Kupanga chiphunzitso chimene alendo adzadziwa zikhulipiriro zanu za mpingo za
Mbaibulo.
-Malamulo amene boma limafuna pa za mpingo watsopano.
-Dongosolo la mpingo lokhuza utsogoleri, mautumiki, ndi ndondomeko za chuma cha
mpingo.
-Malo ndi umwini wake wa katundu wa mpingo.
-Ubale wake wa “likulu” la mpingo ndi mipingo yatsopano.
Page 110
110
MAYESO ODZIYETSA NOKHA
1. Lembaini Vesi Lotsogera kuchokera pamtima.
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
2. Kodi kukula kwa mpingo “mmadera ndi chiyani?
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
3. Kodi “kudzala mpingo” kumatanthauza chiyani?
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
4. Lembani chidule cha kukula kwa mpingo woyamba mmadera ku Yerusalemu.
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
5. Lembani njira zinayi zimene mpingo watsopano ungayambire.
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
6. Lembani mitundu itatu ya kukula mmadera kwa mpingo.
____________________________________ ____________________________
________________________________________________________
7. Ndi mfundo ziti zoyamba zimene Baibulo limanena posankha madera oyambitsako
mipingo?
______________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
8. Kodi ndi mtundu uti wa uthenga umene umayambitsa mpingo watsopano?
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
(Mayankho a mafunsowa akupezeka kumapeto kwenikweni kwa bukuli)
Page 111
111
KUPITILIZA KUPHUNZIRA
Popitiliza kuphunzira za mmene mungadzalire mpingo onani maphunziro awa a Harvestime
International Institute:
Dongosolo la mpingo la Mbaibulo lidzakutsogolerani posankha ndi kupanga atsogoleri a
mpingo.
Kusanthula Malo lidzakuthandizani kudziwa malo amene uthenga wabwino ungafikeko ndi
kudzalako mpingo.
Dongosolo la Zolinga lidzakuphunzitsani kukhazikitsa cholinga, kupanda zochita ndi
kulongosola mpingo.
Ndondomeko Zolimbikitsa zidzkuthandizani kulimbikitsa chiyanjano cha mpingo pa ulaliki.
Chotupisa ngati Ulaliki lidzabweretsa okhulupirira atsopano pa mpingo.
Page 112
112
CHAPUTALA CHA 9
KUKULA POLUMIKIZA
ZOLINGA:
Pakutha pa chaputalachi muyenera:
Kulemba Vesi Lotsogolera kuchokera pamtima.
Kulongosola tanthauza la “kukula polumikiza” mipingo.
Kupereka Vesi la Mbaibulo la dongosolo ma Mulungu la “kukula polumikiza”
mpingo.
Kudziwa Vesi Lotsogolera la mtsogoleri wa mu Chipangano Chatsopano pa nkhani
ya “kukula polumikiza”
Kulemba chidule cha njira zimene Paulo anagwiritsa ntchito pokulitsa uthenga
wabwino mmadera a zikhalidwe zina.
VESI LOTSOGOLERA:
… Kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kucokera kumdima, kulinga
kukuunika, ndi kucokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti
alandire iwo cikhululukiro ca macimo, ndi colowa mwa iwo akuyeretsedwa
ndi cikhulupiriro ca mwa Ine (Machitidwe 26:18)
MAWU OTSOGOLERA
Chaputala chomwe mwamalizirachi chikukamba za kukula kwa mpingo mmadera kumene
kumachitika podzala mipingo yatsopano mu madera ofanana chikhalidwe. Zikuyenera kukhala
limodzi ndi phunziro la kukula kwa mpingo polumikiza.
Mfundo zomwezo zofunikira pa kukula kwa mpingo mmadera zikugwiranso ntchito pa kukula
kwa mpingo polumikiza. Izi zikutanthauza kuti chilichonse chakambidwa mu phunziro lathali,
ndi chofunikanso mu phunziro lino. Koma kukulitsa polumikiza kumafuna njira zina zimene ndi
za chaputalachi basi.
KUKULA POLUMIKIZA
Kukula polumikiza kumachitika pamene mpingo uzikulitsa mmadera a dziko, chiyankhulo,
malire a mitundu podzala mpingo watsopano mu zikhalidwe zatsopano za anthu. Mawu oti
“kulumikiza” akugwiritsidwa ntchito chifukwa pamene ntchito ikuchitika “mlato” umaikidwa
kuchokera ku chikhalidwe china kupita ku chikhalidwe china polafalitsa uthenga. Njira
zatsopano za mayendedwe ndi zolumikizana zatukula kwambiri machitidwe a mpingo okula
polumikiza ngakhale ku malo akutali.
Page 113
113
KUKULA KOLUMIKIZA MCHIPANGANO CHATSOPANO
Kukula kolumikiza madera kunali gawo limodzi la dongosolo la Ambuye Yesu pofuna kufalitsa
uthenga wabwino mdziko lonse lapansi. Ophunzira amayenera kuyamba kuchitira umboni
mmadera a zikhalidwe zawo ku Yerusalemu keneko kukula popita ku madera ena ofanana nawo
zikhalidwe kukudzala mipingo.
Kenako, ophunzira amayenera kulumikiza maiko, zilankhulo ndi malire pofalisa uthenga
wabwino mu zikhalidwe zosiyana ndi zawo monga Samariya ndi “malekezero onse a dziko
lapansi” (Machitidwe 1:8). Ophunzira mwachangu anakwaniritsa lamuloli pochulukana pakati pa
anthu a zikhalidwe zawo (Machitidwe 2).
Kukula ku madera ena a zikhalidwe zawo kunabwera chifukwa cha chizunzo:
… Koma pamene atumwi a ku Yerusalemu anamva kuti Samariya adalandira mau
a Mulungu, anawatumizira Petro ndi Yohane; (Machitidwe 8:14).
Filipo koyamba analumikiza kusiyana kwa zikhalidwe pa chitsitsimutso cha ku Samariya pa
Machitidwe 8. Petro ndi Yohane anapitiliza utumiki mu dera lomwelo.
Mtumwi Petro anali ndi vuto polandira ntchito yotumidwa wa anthu osiyana zikhalidwe. Anali
mu Yuda wachipembedzo ndipo mwa kanthawi anali ndi malire polumikizana ndi Amitundu
(anthu amene sanali Ayuda). Mulungu analankhula kwa Petro mmasomphenya pa Machitidwe
10 ndipo Petro anatengera uthenga wabwino kwa amitundu ku Kaesareya.
Kukula kolumikiza mu Chipangano Chatsopano kukuonetsedwa bwino ndi utumiki wa mtumwi
Paulo. Mulungu akuitana Paulo ku utumuki umenewu. Paulo anali mu Yuda, koma Mulungu
anamuuza kuti anali:
Koma Ambuye anat kwa iye, Pita; pakuti iye ndiye cotengera canga cosankhika,
cakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israyeli
(Machitidwe 9:15).
Chifukwa Paulo anaitanidwa ndi Mulungu pa utumiki wopita kwa anthu a zikhalidwe zina, njira
zake ndi zofunika pofuna kumvetsetsa kukula kwa mpingo polumikiza. Werengani nkhani ya
kutembenuka mtima kwa Paulo mu Machitidwe 9. Zina zonse za buku la Machitidwe ndi nkhani
ya ntchito ya umishoni kwa mitundu ya dziko. Ambiri mwa mabuku a Chipangano chatsopano
ndi makalata otsatira kwa mipingo imene anadzala mmadera osiyanasiyana (Aroma ndi Aheleni).
NJIRA ZA MTUMWI PAULO
Paulo anasankhidwa ndi Mulungu ngati chitsanzo chathu:
Komatu mwa ici anandicitira cifundo, kuti mwa ine, woyamba, Yesu Kristu
akaonetsere kuleza mtima kwace konse kukhale citsanzo ca kwa iwo
adzakhulupirira pa iye m'tsogolo kufikira moyo wosatha (I Timoteo 1:16).
Page 114
114
Ichi ndi chifukwa njira za Paulo zikhoza kukhala ngati chitsanzo pa kukula kwa mpingo
polumikiza. Izi ndi zina mwa mfundo za kukula polumikiza mu utumiki wa Paulo:
CHOLINGA CHABWINO:
Paulo amalimbikitsidwa ndi nyengo za amitundu zopanda Yesu (Amitundu ndiye kuti mitundu
yonse imene si Israyeli).
Momwemo kumbukirani, kuti kale inu amitundu m'thupi, ochedwa kusadulidwa
ndi iwo ochedwa mdulidwe m'thupi, umene udacitika ndi manja; 12kuti nthawi ija
munali opanda Kristu, alendo a padera ndi mbumba ya Israyeli, ndi alendo alibe
kanthu ndi mapangano a malonjezano, opanda ciyembekezo, ndi opanda Mulungu
m'dziko lapansi (Aefeso 2:11-12).
Amaumilizidwa ndi chidwi cha lamulo:
Ine ndiri wamangawa wa Ahelene ndi wa akunja, wa anzeru ndi wa opusa.
15Cotero, momwe ndingakhoze ine, ndirikufuna kulalikira Uthenga Wabwino kwa
inunso a ku Roma (Aroma 1:14-15).
Paulo amalimbikitsidwa ndi khumbo lomvera masomphenya opatsidwa ndi Mulungu:
Potero, Mfumu Agripa, sindinakhala ine wosamvera masomphenya a Kumwamba
(Machitidwe 26:16)
Amalimbikitsidwa ndi changu ndi katundu wa pa Mulungu:
Pamene Paulo analindira iwo pa Atene, anabvutidwa mtima pamene anaona mudzi
wonse wadzala ndi mafano (Machitidwe 17:16)
Amalimbikitsidwa ndi chikondi choyera:
Koma m'zonse tidzitsimikfzira ife tokha monga atumiki a Mulungu, m'kupirira
kwambiri, m'zisautso, m'zikakamizo, m'zopsinja
M'mayeredwe, m'cidziwitso, m'cilekerero, m'kukoma mtima, mwa Mzimu Woyera,
m'cikondi cosanyenga (II Akorinto 6:4,6)
ZOFUKIKA KOYAMBIRIRA:
Paulo anali ndi zinthu zofunikira. Zinthu zimene zinali phindu kwa iye…maphunziro, katundu,
chuma, maudindo, ndi zina…anaziyesa zopanda kanthu ku uzimu. Chokhacho chimene
chinampindulira kwa Yesu chinali choyambirira:
Page 115
115
Komatu zonse zimene zinandipindulira, zomwezo ndinaziyesa citayiko cifukwa ca
Kristu.
Komatu zeni zeninso ndiyesa zonse zikhale citayiko cifukwa ca mapambanidwe a
cizindikiritso ca Kristu Yesu Ambuye wanga, cifukwa ca Iyeyu ndinatayikitsa
zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Kristu (Afilipi 3:7-8)
Zinthu zanu zofunikira zikuyenera kukhala:
1. Ubale wanu ndi Mulungu.
2. Ubale wanu ku thupi la Khristu (kuphatikizapo banja lanu ngati gawo la thupilo).
3. Utumiki wanu kwa Mulungu.
Ubale umabwera pambuyo pa utumiki pa zifukwa ziwiri:
1. Simungatumikire pamene ubale wanu siuli bwino ndi Mulungu.
2. Simungatumikire pamene ubale wanu siuli bwino ndi anthu ena. Ziwalo za thupi la
Khristu (kuphatikizapo banja lanu) sizingalandire utumiki wanu pamene ubale wanu ndi
ena siuli bwino.
MAWU A MULUNGU:
Utumiki wa Paulo unakhazikika pa Mau a Mulungu. Pamene Mau a Mulungu amafalikira ku
zikhalidwe za anthu ena, mipingo imafalikira:
Koma mau a Mulungu anakula, nacurukitsa (Machitidwe 12:24)
Cotero mau a Ambuye anacuruka mwamphamvu nalakika (Machitidwe 19:20)
Kotero Mipingoyo inalimbikitsidwa m'cikhulupiriro, nacuruka m'ciwerengo cao
tsiku ndi tsiku (Machitidwe 16:5)
UTHENGA WA UTHENGA WABWINO:
Uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu wa Paulo. Sanasemphanitse ndi ntchito za za
umishoni kwa maiko osowa ndi mphamvu ya kulalikira uthenga wabwino. Sanagwiritse ntchito
machitidwe ake kuti akope anthu ambiri. Anthu amakhuzidwa ndi mphamvu ya Mulungu.
Pakuti Uthenga Wabwino sundicititsa manyazi; pakuti uti mphamvu ya Mulungu
yakupulumutsa munthu ali yense wakukhulupira; kuyambira Myuda, ndiponso
Mhelene (Aroma 1:16).
PEMPHERO:
Page 116
116
Paulo anapempherera chitsogozo cha Mulungu polalikira uthenga wabwino kwa anthu a
zikhalidwe zina:
Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala cakudya, Mzimu Woyera anati,
Mundipatulire Ine Bamaba ndi Saulo ku nchito imene odinawaitanirako.
Pamenepo, m'mene adasala cakudya ndi kupemphera ndi kuika manja pa iwo,
anawatumiza amuke (Machitidwe 13:2-3)
MZIMU WOYERA:
Mzimu Woyera anali mtsogoleri wa utumwi wa Paulo. Mwachitsanzo, mu nyengo ina…
… atawaletsa Mzimu Woyera kuti asalalikire mau m'Asiya (Machitidwe 16:6)
ULALIKI, CHIPHUNZITSO, KUCHITIRA UMBONI:
Paulo anatsata malangizo a kutumwa kwakukulu kolalikira, kuphunzitsa ndi kuchitira umboni wa
uthenga wabwino.
Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate, Paulo
anawafotokozera mau, popeza anati acoke m'mawa mwace; ndipo ananena cinenere
kufikira pakati pa usiku… (Machitidwe 20:7)
Kuti sindinakubisirani zinthu zopindulira, osazilalikira kwa inu, ndi
kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m'nyumba m'nyumba, ndi kucitira umboni
Ayuda ndi Ahelene wa kutembenuza mtima kulinga kwa Mulungu, ndi
cikhulupiriro colinga kwa Ambuye wathu Yesu Kristu (Machitidwe 20:20-21).
Sizokwanira kulumikizana mu uthenga wabwino okha. Unthenga ukuyenera kuperekedwa mu
njira imene ingamveke kwa anthu omvera. Mawu, chilankhulo, machitidwe ena ofalisira
akuyenera kusinthidwa ndi cholinga chakuti uthenga umveke. Paulo anazindikira ndi kuchita izi
(onani Machitidwe 21:37-40 ndi 22:2). Ndipo 26:18 amapereka njira imene kulumikizana
kwamphamvu kungachitikire palalikira uthenga wabwino kw anthu ndi zikhalidwe zina.
Mulungu anatuma Paulo kwa amitundu…
…Kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kucokera kumdima, kulinga
kukuunika, ndi kucokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire
iwo cikhululukiro ca macimo, ndi colowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi cikhulupiriro
ca mwa Ine (Machitidwe 26:18).
Uthenga ukuyenera kuperekedwa mu njira yotha:
1. Kutsekula maso a anthu.
Page 117
117
2. Kuti atuluke mu mdima wa uzimu kulowa mu kuunika.
3. Kuti achoke ku mphamvu ya Satana mkupita kwa Mulungu.
4. Kuti alandire chikhululukiro cha machimo awo polandira chipulumutso.
5. Kuti alandire cholowa cha uzimu mwa chiyeretso cha chikhulupiriro.
Chikhalidwe chimene munthu wakhalamo chimalosera zinthu zisanu mmadera awa:
Chilankhulo chake: mmene amalankhulira ndi kulumikizana maganizo ake.
Maonedwe ake a dziko: mmene amalionera ndi kulimvetsa dzikoli.
Zikhulupiriro zake: chipembedzo mu za mphamvu za uzimu, njira ndi maganizo ake.
Zimene amayendera: makhalidwe ake ndi anthu ena, zilimbikitso ndi njira za mmene
amapangira ziganizo.
Makhalidwe ake: mmene amachitira, amakhalira, makhalidwe a zikhalidwe zawo
zoyenera.
Machitidwe 26:18 amakambapo za izi, mukhoza kuwerenga. Pali nkhani ya chiyankhulo,
maonedwe a dziko, zikhulupiriro ndi kusintha kwa makhalidwe.
KUONETSERA MPHAMVU
Paulo sanangolankhula za uthenga wabwino ayi, komanso amaonetsera mphamvu ya Mulungu:
Mu mphamvu ya zizindikilo ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera;
kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iluriko,
ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Kristu (Aroma 15:19)
KUDZALA MIPINGO:
Paulo sanangofalitsa uthenga wabwino keneko ndi kuwasiya okha obadwa mwatsopano.
Amapanga gulu la okhulupirira amene otembenuka mtima amakhala nawo. Amadzala mipingo
mmadera.
1. Ogwira ntchito atumidwa: Machitidwe 13:1-4; 15:39-40
Ogwira ntchito amaphunzitsaidwa ndi kutumidwa kukafika mmadera ena. Okhulupirira a
mmipingo ya pakhomo amathandiza, kutuma, ndi kuyanjana ndi iwo amene Mulungu
anawapatulira ku ntchito.
2. Anthu analumikizana: Machitidwe 13:14-16; 14:1; 16:13-15
Mmadera ambiri, Paulo anayetsetsa kulumikizana ndi atsogoleri a mu sunagoge. Anayesera
kukhala ndi chidziwitso ndi thandizo la atsogoleri a pamalo. Magulu komanso anthu anatsata
zolinga zokhala ndi gulu la anthu ambiri omvera uthenga wabwino.
3. Uthenga unaperekedwa: Machitidwe 13:17; 16:31
Page 118
118
Uthenga unaperekedwa mu ulaliki, chiphunzitso, kuchitira umboni ndi kuonetsera mphamvu ya
Mulungu. Njira zosiyana zinagwira ntchito molingana ndi mmene zinalili pofuna kulupereka
uthenga kwa anthu. Mmadera ena amalalikira mu sunagoge (Machitidwe 14:1). Pomwe ena,
anthu amene amalandira amaikidwa mmagulu ena apadera (Machitidwe 19:9). Mautumiki
osiyana kwa anthu amachitika mmadera ena (Machitidwe 13:42) ndipo chilankhulo
chimasinthidwa ponetsetsa kuti uthenga ukuperekedwa moyenera (Machitidwe 22:2).
4. Omvera amatembenuka: Machitidwe 13:48; 16:14-15
Kulumikizana bwino kwa uthenga wabwino kunachokera mu kutembenuka, ndi anthu amene
amalandira uthenga wa chipulumutso ndi kulapa kwa machimo awo.
5. Okhulupirira anasonkhana: Machitidwe 13:43
Paulo sanasite ulaliki ndi kutembenuza anthu. Amawasonkhanitsa okhulupirira kukhala pa
mpingo wad era. Okhulupirirawa amakhala mu thupi la chiyanjano ndi mwambo wa mpingo.
Nthawi komanso malo zimayikidwa zoti azisonkhana pamodzi ngati mpingo.
6. Chikhulupiriro chitsimikizidwa: Machitidwe 14:21, 22; 15:41
Monga zaonetsedwa pa kutuma kwakukulu mu Machitidwe 28:19-20, chiphunzitso chimatsatira
kutembenuka mtima. Chiphunzitso ichi, molingana ndi mpingo chinaumba okhulupirirawa pa
maziko a moyo wawo wa chikhristu mu ufumu wa Mulungu. Zokhuza “chitsimikizo cha
chikhulupiriro” zimalimbikitsa kukula mmoyo wauzimu, ndi kuthandiza okhulupirira kuzindikira
mphatso zawo za uzimu ndi kukhala ziwalo zamphamvu mu thupi la Khristu.
7. Atsogoleri apatulidwa: Machitidwe 14:23
Ngati okhulupirira okhwima, atsogoleri omwe akulitsidwa ndi Mulungu amayenerezedwa pa
utumiki wotsogolera mu mpingo. Akukuakulu anasankhidwa ku mpingo womwe amasonkhana
osti kutumizidwa kuchokra ku mpingo wina kapena ku dziko lina. Mpingo uliwonse umakhala
ndi madongosolo a kayendetsedwe ka mpingo kochokera Mbaibulo, kabwino ndi koyenera.
8. Mpingo unayamikiridwa: Machitidwe 14:23; 16:40
Pamene atsogoleri ali pamalo ndi kuyamba kugwira ntchito moyenera, kudalira “odzala mpingo”
kumatha. Pakuti kusintha koyenera kunachitika kuchokera ku likulu la mpingo kupita ku mpingo
watsopano. Mpingo “unayamikidwa” pochita bwino kwawo ngati thupi lokhulupirira.
9. Maubale anapitilira: Machitidwe 15:36; 18:23
Ubale unapitilira pakati pa okhulupirira ndi odzala mpingo (Paulo) ndi likulu la mpingo
(Yerusalemu). Maubalewa amakhazikikanso pakati pa chiyanjano chatsopano cha iwo ndi
mipingo ina mmadera ndi cholinga chofuna kufalitsa uthenga.
MASOMPHENYA A DZIKO LONSE:
Page 119
119
Paulo anali ndi dongosolo la lenileni la machitidwe ake. Baibulo limaulula kuti anali ndi chidwi
ku mAsiya, Galatiya, Makedoniya ndi ena amene anali ndi mmadera amenewo nthawi imeneyo:
Filipo: (Machitidwe 16) uwu unali mzinda wotsogolera ku Makedoniya.
Tesalonika: (Machitidwe17:1-10) uwu unali waukulu ndi wachumua.
Akorinto: (Machitidwe18:1-11) wa chuma wa Metulopolisi ku Helene.
Aefeso: (Machitidwe 19:1-10) kumene misewu yaikulu ya ufumu wa Chiroma unadutsa
kummawa. Madoko komanso malo a malonda.
Paulo anadziwa kutiangathe kufikira anthu ambiri mu mizinda. Anadziwanso kuti kusintha
kumayamba mu mzinda kenako ku malo akumudzi.
Mizinda ya malondayi ndi malo okopa alendo inali ndi anthu ambiri amalonda ndi zolinga zina.
Moti alendo amamva nawo uthenga wabwino pamene amapita kwawo. Paulo anayendera
mizinda mkukhazikitsa ntchito ua umishoni. Pamene amachoka ku Yerusalemu, anapita kudera
lina ku Tarisi ndi Antiokeya. Werengani mavesi awa: Machitidwe 11:25-30; 13:1-3; 19:1-20;
16:8; 19:21; 23:11; 28:14-31. Aroma 1:9-15; 15:24, 28).
MALO OLANDILIKA:
Njira za Paulo zokulitsa mpingo zinachitika chifukwa cha anthu amene amalandira uthenga wa
Paulo. Ku Mateyu 10, Yesu anawauza ophunzira ake kuti asapite ku Samariya kapena kwa anthu
a mitundu koma kwa Israyeli. Nthawiyi inali ya bwino koma kwa ana a Israyeli. Magulu ena a
anthu sinali nthawi yawo yolandira uthenga.
Ngakhale pakati pa Ayuda, ophunzira amayenera kulalikira kwa iwo amene akanalandira
uthenga. Amayenera kugawira iwo amene amalandira ndi kuchitabe choncho ngakhale
amakumana ndi osalandira uthenga. Amayenera apereke mphamvu zawo kwa madera amene
amalandira uthenga.
Paulo anatsata ndithu njira imeneyi. pamene ayuda amakana uthenga wabwino, Paulo amapita
kwa amitundu (Machitidwe 13:42-51). Pamene Atene sanakonzeke, Paulo amapita Kwa
Akorinto. Ndipo ku Akorinto Paulo anachoka kwa ayuda ndi amitundu. A Helene amene
amalandira uthenga anakondwera ndikubatizidwa atakhulupirira (Machitidwe 18:5-11). Mulungu
anavomereza ntchito ya Paulo mmasomphenya pomuuza kuti akhalebe ku Akorinto opanda
mantha ndi kulalikira Khristu (Machitidwe 18:5-11). Pamene mikumano ikuchitika
mmasunagoge mkuamamukana iye, Paulo anayamba mipingo imene imalandira mauthenga ake.
Pamene chizunzo chimamutulutsa kunja, amapita ku madera ena.
ANTHU AKE:
Paulo amaika chidwi pofikira anthu a mtundu wake ndi uthenga wabwino:
Page 120
120
Abale, kufunitsa kwa mtima wanga ndi pemphero langa limene ndiwapempherera
kwa Mulungu, ndilo, kuti apulumuke (Aroma 10:1).
ANTHU OSAFIKILIDWA:
Paulo anasankha madera amene uthenga wa Khristu sunafikeko:
Ndipo cotero ndinaciyesa cinthu caulemu kulalikira Uthenga Wabwino, pa malopo
Kristu asanachulldwe kale, kuti ndisamange nyumba pa maziko a munthu wina.
Koma monga kwalembedwa; Iwo amene uthenga wace sunawafikire, adzaona,
Ndipo iwo amene sanamve, adzadziwitsa (Aroma 15:20-21)
MAGULU A ANTHU
Paulo anagwira ntchito ndi magulu a anthu mkati mzinda ndi madera. Mwachitsanzo, analalikira
kwa Ahelene ndi ayuda ku Antiyokeya (Machitidwe 13:42). Gulu la anthu linali la mtundu wa
chikhalidwe, chiyankhulo chofanana. Ndi kofunikira kumaona mudzi kapena mzinda mu magulu
a zikhalidwe zawo ndi kupanga dongosolo la kukulitsa mu kulumikiza.
Mwachitsanzo, mzinda umodzi ku Amerika muli anthu ambiri olankhula chi spanishi, chingerezi
ndi chimwenye. Kukula pa kulumikiza kumanga mipingo mu mizinda imeneyi muyenera kuona
magulu onse a anthuwa. Kudala mipingo mkati mwa anthu a magulu osiyana kumapititsa
uthenga wabwino patsogolo. Pakuti anthu a maguluwa amalnkhula zilankhulo zosiyana ndipo
ndi a zikhalidwe zosiyananso. Choncho palibe chimene chingatchinge uthenga wabwino kaya
zilankhulo kapena zikhalidwe. Mu phunziro latha mwaphunzira kuti anthu amene amakhala
limodzi, amalamkhula zilankhulo zofanana ndipo ali ndi zikhalidwe zofanana.
Anthu amene ali ngati ife, akhoza kugawidwa mkukhala mmagulu a ang’ono ndi cholinga
chofalitsa uthenga. Mwachitsanzo, mumachita izi pokhala ndi magulu a maphunziro a sunde
sukulu molingana ndi zaka zawo. Mukhonzanso kuchita izi pamene mukufuna kufikira anthu
amabiri a mmagulu.
Harvestime international Institute ali ndi phunziro la “Kuzindikira Malo” limene limathandiza
kudziwa malo ofunika pa utumuki. Taganiza kuti mukhale ndi phunziroli pa kudzala mpingo.
Phunziroli likuthandizani mmalo:
1. Kudziwa anthu amene mukawafikire. Ndi anthu amagulu ati osiyana amene
mukawafikire mmizinda kapena mmadera. Ndi ndani amene mukufuna kukafikra?
Zipembedzo zawo, zikhalidwe ndi zilankhulo zawo.
2. Kudzindikira zosowa zawo za ku uzimu. Mwachitsanzo, kodi mkofunika kudzala mpingo
pakati pa anthu a chilankhulo cha chisena. Mwina zosowa zawo zikutumikiridwa koma
amene amalankhula zilankhulo zina sakuthandizidwa.
Page 121
121
3. Kudziwa kulandilidwa kwa uthenga wabwino:
4. Kudziwa njira zimene mukagwiritse ntchito pofikira anthu onse. Kodi afikilidwa bwanji?
Nanga ndi ndani amene afikire? Mukuyenera kuwafikira monse mmene angamvere ndi
kumvetsetsa mwa zikhalidwe zawo. Mwachtsanzo, ngati gulu lina silingawerenge,
kulalikira kowapatsa zowerenga sikungawathandize powafikira ndi uthenga.
KUFUNA KUSINTHA MALINGANA NDI ZIKHALIDWE:
Paulo anafunitsitsa kusintha kwa anthu osiyana zikhalidwe ndi muteso mmadera (onani I
Akorinto 9:16-23). Munthu amasunthika ndi chikhalidwe chimene wakulilamo. Anthu a
zikhalidwe zosiyana amasiyananso mu zochita.
KUSIYANA KWA ZIKHALIDWE
Paulo sanagofuna kusintha pa zikhalidwe zokha ayi, koma sanalole kuti uthenga wabwino
utchingidwe ndi zikhalidwe.
Ku maiko a aluya, ngati wokhulupirira watsopano afuna kusiya mpingo wa pabanja lake
chifukwa cha chikhulupiriro chake, amakhala limodzi ndi anthu ofanana naye chikhulupiriro mu
mpingo. Onse amalankhula chiyankhulo chimodzi ndi kukhala ndi makhalidwe amodzi. Koma
ku maiko ena kumene chikhristu chimati munthu ayenera kusiya chikhalidwe chake ndi kuyamba
kukhala ndi achikhulupiriro chimodzi, uthenga wabwino umafalikira mochedwa. Zikhalidwe
zina zimalemekezedwa kuposa za anthu ena. Mitundu, zikhalidwe zonsezi ndi zofunikira
kwambiri.
Mu Chipangano Chatsopano, pamene munthu wakhala khristu sizimatanthauza kuti wasiya
kukhala mu wosatira chi Yuda. Ngakhale wamitundu sayenera kulandira mdulidwe wa chiyuda.
Komayambiriro kunali mavuto pa ayuda amene amaika lamulo pa amitundu polalola kuti
azidulidwa ngati atembenuka mtima. Koma Paulo ananena kuti ameneyu anali katundu
wosayenera kusenza. Mukhoza kuwerenga za izi pa Machitidwe 15.
(Chidziwitso: tikamakamba za “chikhalidwe” timakamba za makhalalidwe osiyana potengera
zikhalidwe za anthu ndi mtundu zimene sizimaphwanya malamulo a Mulungu. Machitidwe a
uchimo samaloledwa.
NTHAWI:
Paulo amasinthanso nthawi imene amakhala nawo mu zikhalidwe za anthu malingana ndi
zosowa zawo. Mmalo ena amakhalamo masiku ochepa. Onani Machitidwe 21:4. Ndipo malo ena
amakhalako nthawi yaitali, onani Machitidwe 14:28. Anali woyendayenda ndipo dongosolo lake
limatsogozedwa ndi Mzimu Woyera.
KULANKHULA KWA ANTHU AMBIRI:
Page 122
122
Paulo amalankhula uthenga wake kwa anthu ambiri. Anagwiritsa ntchito mwayi wolankhula kwa
anthu ambiri:
Ndipo kunali pa Ikoniyo kuti analowa pamodzi m'sunagoge wa Ayuda, nalankhula
kotero, kuti khamu lalikuru la Ayuda ndi Ahelene anakhulupira (Machitidwe 14:1)
KUKHALA WOPHUNZIRA:
Paulo analalikira ku khamu la anthu komanso amadziwa kufunika kopereka moyo wake kwa
anthu ochepa amene anli ofunika okhala ndi kuthekera kophunzitsa ena. Timoteo anali mmodzi
wa anthuwa komanso Tito ndi Yohane Marko, amene nthawi ina anakanidwa pa maphunziro a
kukhala wophunzira (Machitidwe 15:36-40). Anali Paulo amene Mzimu Woyera anamuulira
zolinga za Mulungu pa wokhulupirira onse kuti achulukane mu uzimu (II Timoteo 2:2).
Kugwira ntchito limodzi ndi okhulupirira ena monga Banabasi ndi Sila, ndi ophunzira ena amene
anawaphunzitsa, kunachulukitsa utumiki wa Paulo mtumwi. Pa ulendo wake wachiwiri ndi
wachitatu, Paulo anlemba za thandizo la amene anagwira nawo ntchito limodzi amene anli mzika
za madera awo kumene anakonza kuti agwireko ntchito.
Iyi ndi mfundo yaikulu. Anthu a ku afilika akhoza kufikira anzawo a ku Afilika momwenso
anthu a mitundu ina. Chifukwa amalankhula chilankhulo chofanana, komanso zikhalidwe zawo
zofanana.
MIPINGO YOIMA PAWOKHA:
Paulo anadzala mipingo yoima pawokha. Ngakhale inali pa ubale ndi likulu la mpingowo
kumbali ya chiyanjano chawo ndi utsogoleri, simadalira mpingo waukulu. Paulo samatenga
thandizo la umishoni kapena iwo kuonetsa kuti Paulo antengako thandizo lopita ku mipingo ina
ya zikhalidwe zina. Amapeza yekha thandizo la mipingo imene amadzala imene inalinso
yokonzeka kuima payokha posadalira thandizo la kwina.
Nkhani zonse za chuma zothandizira kukula kwa mpingo zikuyenera kupanga anthu kuti
azizilamulira okha. Ngati mpingo ulandira thandizo kuchokera ku mipingo ina, ndiye kuti
mpingowo ukudalira amenewo. Ngati mpingo wothandizawo walephera, ndiye kuti mpingo
umene ukudalirawo udzalepheranso. Ngati ubale wa maiko suli bwino, mpingo udzakumana ndi
mavuto ngati thandizo lasiya kubwera.
Ambuye yemweyo amene anasandutsa madzi kukhala vinyo ndi kuchulukitsa mkate ndi nsomba
zimene anadyetsa khamu la anthu ndi wokuthanso kubweretsa chuma chofunikira kufalisira
uthenga.
Ulamuliro wogwiritsa ntchito mphatso za mzimu ukyenera kupatsidwa ku mpingo watsopano
kamodzi ndi utsogoleri umene ulipo pa mpingo watsopano. Pamene Paulo anasankha akulu a
mpingo, anasankhidwa kuchokera pakati pa anthu osati kuchokera kwina kwake.
Page 123
123
Cifukwa ca ici ndinakusiya iwe m'Krete, kuti ukalongosole zosowa, nukaike akuru
m'midzi yonse, monga ndinakulamulira (Tito 1:5)
Paulo anagwiritsa ntchito mipingo yatsopano mmadera onse amene amapita monga pemphero,
kupereka, ndi ngati ogwira ntchito limodzi okulitsa mpingo mchiwerengero, ndi polumikiza ndi
anthu ena. Onani Machitidwe 20:4, Aefeso 6:19 ndi Afilipi 1:5,7; 4:14-16.
Mpingo uliwonse umene Paulo anadzala unali likulu latsopano la kuchulukana ku uzimu.
Pakuti kuturuka kwa inu kudamveka mau a Ambuye, osati m'Makedoniya ndi
Akaya mokha, komatu m'malo monse cikhulupiriro canu ca kwa Mulungu
cidaturuka; kotero kuti sikufunika kwa ife kulankhula kanthu (I Atesalonika 1:8)
Paulo anadzala mipingo yambiri pa Mau a Mulungu ndi thanthwe, Yesu Khristu. Sanaikhazikitse
pa bungwe kapena mpingo kapena umunthu wake. Kubweretsa kudalira sikumaphunzitsa kuima
pawekha.
Page 124
124
MAYESO ODZIYETSA NOKHA
1. Lembani Vesi Lotsogolera kuchokera pamtima.
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
2. Lembani tanthauzo la mawu oti “kukula kwa mpingo kolumikiza”
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
__________________________________________________________________________
3. Tchulani vesi imene imakamba za dongosolo la Khristu la “kukulitsa mpingo
polumikiza”
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
4. Ndi ndani amene anali mtsogoleri mu Chipangano Chatsopano pa “kukulitsa mpingo
polumikiza” kwa amitundu?
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
5. Lembani chidule cha njira zimene Paulo angwiritsa ntchito pofalitsa uthenga wabwino
kwa anthu a zikhalidwe zina.
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
(Mayankho a mafunsowa akupezeka kumapeto kwenikweni kwa bukuli)
Page 125
125
KUPITILIZA KUPHUNZIRA
1. Mpingo wa ku Antiokeya unadzalidwa ndi mpingo wa ku Yerusalemu. Chitatha chizunzo
cha Stefano, okhulupirira ambiri anathawa ku Yerusalemu. Ena anabwera ku mzinda wa
Antiokeya ku Siriya, mzinda waukulu ku ufumu wa Chiroma. Kumeneko anakakhazikitsa
mpingo (Machitidwe 11:19-21).
Ophunzira kwa nthawi yoyamba anatchedwa akhristu ku Antiokeya. Uwu unali mpingo
woyamba kwa anthu amene sanali ayuda koma anli pd chiyanjano chabwino. Aheleni
amitundu ndiwo amene anali mu mpingowo. Antiokeya unakhalano mzinda waukulu wa
mipingo ya Chipangano Chatsopano. Utumiki umene tili nawo pano umachokera ku
Antiokeya, osati ku Yerusalemu kumene anthu ake anali a chikhalidwe cha chiyuda basi.
2. Kufala kwa uthenga wabwino kwa Paulo mu zikhalidwe za anthu ena chidule chake ndi
ichi mu maulendo wake wachitatu wa umishoni:
Ulendo woyamba: Machitidwe 13:1-14:28
Ulendo wachiwiri: Machitidwe 15:36-18:22
Ulendo wachitatu: Machitidwe 18:23-21:14
3. Werengani umboni wa Paulo mu Machitidwe 22:
Asanatembenukire kwa Khristu: Machitidwe 22:3-5
Kutembenuka mtima: Machitidwe 22:6-11
Utumiki wake: Machitidwe 22:12-16
Ntchito yake ya umishoni: Machitidwe 22:17-21
4. Werengani zambiri zokhuza Paulo mmene anayendera ulendo wake ku Aefeso:
Anthu anakumana: Machitidwe 18:19; 19:1,8,9
Uthenga wabwino unaperekedwa: Machitidwe 19:4,9,10
Omvera anatembenuka: Machitidwe 19:5,18
Okhulupirira anasonhkana: Machitidwe 19:9-10
Chikhulupiriro chinatsimikizidwa: Machitidwe 20:20, 27
Atsogoleri anapatulidwa: Machitidwe 20:17,28: I Timoteo 1:3,4;
Mpingo unayamikidwa: Machitidwe 20:17; Aefeso 1:1-3,15,16
5. Kodi kukula kwa mpingo polumikiza mu chipangano chatsopano kumachita bwino?
Onetsetsani izi:
… Ndipo panakhala cimwemwe cacikuru m'mudzimo (Samariya): Machitidwe 8:8
… Ndipo anamuona iye onse akukhala ku Luda ndi ku Sarona, natembenukira kwa
Ambuye amenewa: Machitidwe 9:35
… Koma mau a Mulungu anakula, nacurukitsa (Machitidwe 12:24).
Page 126
126
… Ndipo mau a Ambuye anabukitsidwa m'dziko lonse (Machitidwe 13:49)
… Kotero Mipingoyo inalimbikitsidwa m'cikhulupiriro, nacuruka m'ciwerengo cao tsiku
ndi tsiku (Machitidwe 16:5)
… Ndipo anacita comweco zaka ziwiri; kotero kuti onseakukhala m'Asiya anamva mau a
Ambuye, Ayuda ndi Ahelene (Machitidwe 19:10)
…Cotero mau a Ambuye anacuruka mwamphamvu nalakika (Machitidwe 19:20)
…mu mphamvu ya zizindikilo ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero
kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iluriko, ndinakwanitsa
Uthenga Wabwino wa Kristu; ndipo cotero ndinaciyesa cinthu caulemu kulalikira
Uthenga Wabwino, pa malopo Kristu asanachulldwe kale, kuti ndisamange nyumba pa
maziko a munthu wina (Aroma 15:19)
6. Muyeso wa anthu ndi malo a anthu amene anatembenuka mtima amaonetsera za mmene
mpingo wa chipangano chatsopano unalumikizana mmagulu, muzikhalidwe, ndi
mmadera ndi uthenga wabwino.
Page 127
127
CHAPUTALA CHA 10
ZISANKHO KAPENA OPHUNZIRA?
ZOLINGA:
Pakutha pa chaputalachi muyenera:
Kulemba Vesi Lotsogolera kuchokera pamtima.
Kupereka tanthauza la “kutembenuka.”
Kupereka tanthauzo la “wophunzira.”
Kulemba zinthu zitatu zofunika pa kukhala wophunzira.
Kudziwa mfundo 9 za kukhala wophunzira zimene zikuonetseredwa pa Yesu ndi
ophunzira ake.
Kulemba zinthu 9 za kukhala wophunzira weniweni.
Longosolani yesero lenileni la wophunzira.
VESI LOTSOGOLERA:
Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ace, Ngati munthu afuna kudza pambuyo
panga, adzikane yekha, natenge mtanda wace, nanditsate Ine (Mateyu 16:24)
MAWU OYAMBA
Mwamvapo zambiri za nkhani ya “Kutuma Kwakukulu” kwa Yesu, koma kodi mumamvetsa
zenizeni za umishoni umene Yesu anapatsa ophunzira ake? Kodi lamulo linali longokhala ndi
anthu atsopano? Kodi anawatsimikizira kuti atha kupanga maulendo mmizinda ndi kumanga
mipingo yaikulu? Kodi anawauza za zinthu zofunikira monga chakudya ndi zovala za a
umphawi?
Tiyeni tiwerengenso malangizowa kachiwiri:
Cifukwa cace mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo
m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:
ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo
onani, Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira cimariziro ca nthawi ya
pansi pano (Mateyu 28:19-20)
koyambirira kupita kunali kwa amitundu yonse, kuwaphunzitsa uthenga wabwino ndi
kuwabatiza ndi kukhala nawo pa ziphunzitso a zimene Yesu analamulira.
Page 128
128
Ichi chinali choyamba ndi chofunikira. Mukhoza kukhala moyo wanu mu njira zambiri.
Mukhoza kuchita ntchito zabwino ngati kuthandiza a umphawi. Mukhoza kumanga mipingo
yaikulu. Mukhoza kupanga misonkhano yaikulu ya chipembedzo.
Koma mukuyenera kuchita chinthu chimodzi ngati mukufuna kuwaniritsa zimene Yesu
amanena: Mukuyenera kuchita nawo pofikira dziko lapansi ndi uthenga wabwino. Zinthu zonse
ngati kutumikira osauka, kumanga mipingo ndi zina, ndi zofunika pakuti zingothandizira ku
chofunika chachikulu.
Koma kufikira anthu a mitundu yonse ndi kuposa kulumikiza anthu ku malo a chitsankho cha
Yesu. Pofuna kukwaniritsa kutuma kwakukuluku mukuyenera kupita chitsogolo kupitilira
kukhala wophunzira.
CHISANKHO KAPENA WOPHUNZIRA?
Mitundu iwiri ya ziphunzitso ikupezeka pa kutuma kwakukula kwa Yesu:
KOYAMBA: KUPHUNZITSA ANTHU KUTI APULUMUTSIDWE
Anthu akuyenera kumva Mau a Mulungu ndi cholinga choti achitepo kanthu, kulapa ku machimo
ndi kubadwa mwatsopano. Chipunzitso chimenechi ndi “uvangeli”:
Cifukwa cace mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo
m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera (Mateyu 28:19).
Okhulupirira atsopano nthawi zina amatchedwa “otembenuka mtima.” Munthu wotembenuka ndi
wokhulupirira mwa Yesu amene wabadwa mwatsopano mwa chikhulupiriro ndi kukhala gawo
limodzi la Ufumu wa Mulungu. (Harvestime International Institute ali ndi phunziro lotchedwa
“Chotupitsa ngati Ulaliki” limene limapereka maphunziro a ulaliki kwa anthu amene ndi
atsopano mu chikhulupiriro.
CHACHIWIRI: CHIPHUNZITSO PAMBUYO PA KUTEMBENUKA:
Mutatha kupnzitsidwa za Uthnega Wabwino ndipo mwabwera kwa Yesu, mukuyenera
kuphunzira za mmene mungamutsatire Iye.
Ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo
onani, Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira cimariziro ca nthawi ya
pansi pano (Mateyu 28:19-20)
Kutumwa kwa Yesu kumaulula kuti chiphunzitso chopitilira chimayenera kubwera munthu
atatha kutembenuka ndi kubatizidwa. Obadwa mwatsopano akuyenera kulangizidwa mmene
Yesu anaphunzitsira. Ntchito imeneyi imatchedwa “kuyendera anthu” kapena “kudyetsa nkhosa”
kapena “kupanga ophunzira.”
Page 129
129
TANTHAUZO LA KUPANGA OPHUNZIRA
Dongosolo la Yesu ndi lokuti mutsogolere otembenuka mtima kukhala ophunzira.
Wophunzirandiye amene watembenuka ndi kukhazikika pa maziko a chikhulupiriro cha
chikhristu ndi kuthekera kupanganso ophunzira ena ndi kuwatsogolera. Mawu oti “wophunzira”
ndiye kuti mwana, amene ali ku sukulu, amene amaphunzira potsatira. Zikuposa mzeru za
mmutu. Uku ndi kuphunzira kumene kumasintha makhalidwe a munthu.
CHISANKHO CHA WOPHUNZIRA
Chisankho ndi gawo lokhalo loyamba pa kukhala wophunzire woona. Otembenuka mtima
ayenera kupita chitsogolo pa chisankho chawo chokhala ziwalo za thupi la Yesu zokonzeka
kupanganso ophunzira ena. Kupeza ophunzira ena ndi zofunikira, koma kuwaphunzitsa kutsatira
ndi kukhala okhwima ku uzimu ndiye zofunikanso. Aliyense amene mukumphunzitsa,
mumpange kuti akhalale wophunzira weniweni kuti nayenso aphunzitse ena.
Ili ndi dongosolo la Mbaibulo la kukhala wophunzira molingana ndi mmene Yesu
anaphunzitsira. Anasankha ophunzira khumi ndi awiri, nawaphunzitsa kuti nawonso aphunzitse
ena. Pamene mukuphunzira chaputala cha 4 cha phunziro ili, dongosolo loti “aliyense
aphunzitse” limabweretsa kukulukana kwa okhulupirira, mipingo komanso zipembedzo.
Koma nthawi zonse dziwani zolinga zanu bwino. Sikuti mukuphunzitsa ndi cholinga chopanga
utumiki wanu kapena mpingo wanu. Cholinga ndi chakuti mufikire anthu a mitundu yonse
molingana ndi Yesu. Kukwaniritsa kutuma kwakukulu sikukutengera mzeru kapena luso
lapadera, komano pa kuumba ndi kudzipereka kwa ophunzira.
Ulaliki umabweretsa anthu kutembenuka mtima. Kupereka mwambo kumapanga ophunzira
amene akhoza kulalikira, ndi kutembenuza anthu ndi kuwapanga kukhala ophunzira. Ndipo izi
zimapitilira chonchi.
KUKHALA WOPHUNZIRA
Werengani Luka 9:57-62 mu Baibulo lanu. Mu ndimeyi anthu atatu anampeza Yesu ndi khumbo
lofuna kukhala ophunzira. Kwa yense, Yesu anaulula machitidwe osiyana okhala wophunzira
kuti amafuna:
1. KUWERENGERA MTENGO: Luka 9:57-58
Munthu woyamba akanamtsata Yesu opandapo kudikira kuti ayitanidwe. Anayesera kukhala
wophunzira mwakufuna kwa iye yekha. Koma Yesu anamuchenjeza kuti samvetsa bwino
tanthauzo la kukhala wophunzira. Kukhala wophunzira sikuti munthu umangozifunitsa kwa
Mulungu ayi, koma ndi maitanidwe a kwa Mulungu. Yesu anaati, “ukanditsata ine, izi ndi
zimene udzakumana nazo.” Analongosola kuti kukhala wophunzira umalipira mtengo wake.
Sizingakwaniritsidwe ndi kuchita mwa iwe wekha.
Page 130
130
2. KUCHITA ZOYENERA: Luka 9:59-60
Munthu wachiwiri amene anaitanidwa ndi Yesu kuti “amutsate.” Ku “mutsata” ndiye kuti
kubwera pambuyo pa wina amene ali patsogolo, kutsatira chitsanzo. Zimakhuza zomwe
umakhulupirira ndi kumvera. Pamene Yesu anaitana ophunzira ake 12, anawapempha kuti
amutsatire ndi kumutsata. Sanalongosole za mmene njira yake inalili. Sanawapatse tsatanetsatane
wa dongosolo la moyo.
Ophunzira akuyenera kusiya moyo wakale mbuyo chifukwa cha maitanidwe okha basi.
Zosankho ndi nsembe zimene izi zimatengera sizidziwika. Wotsatirayo amasiya moyo
wachitetezo ndi kukhala moyo wonga ngati wopanda chitetezo mmaso a dziko. Sikukhala
kudzipereka ku dongosolo koma kwa munthuyo. Munthuyo ndiye Yesu Khristu.
Mu ndime ya Luka, mmene munthuyu anayankhira ku maitanidwe omtsata Yesu anali “uyambe
wavutikira ine kaye…” amafuna kumutsata Yesu, koma sichinali chinthu choyamba pa moyo
wake. Yesu sanaganizirepo kuti wotsatira wa iye adzakana zosowa za makolo ake (onani Yohane
19:25-27). Ndi nkhani ya zinthu zoyamba zimene ndi zofunika mu nkhaniyi. Munthuyi amafuna
kukaika makolo ake koyamba. Mu nthawi yofunikira iyi ndi pamene Yesu anamuitana kuti
amutsatire iye, pasapezeke chinachake chotchinga maitanidwe usanayankhe.
Mu ndime ina Yesu analongosola mwachindunji pa nkhani ya “kutsatira” imene imafuna:
Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ace, Ngati munthu afuna kudza pambuyo
panga, adzikane yekha, natenge mtanda wace, nanditsate Ine (Mateyu 16:24).
Kudzikana wekha kukuyenera kukhala koyamba usanayambe kunyamula mtanda. Makhalidwe
akale ndi a uchimo akanidwe. (werengani Aroma 7-8 mmene Paulo anavutikira ndi moyo wake).
Keneko motha kutenga mtanda. Mtanda ndi chizindikiro cha nsembe, kuwawa, kukanidwa,
mavuto, chitonzo pochita chifuniro cha Mulungu. Mtanda ukhoza kukhalanso maitanidwe a kufa
chifukwa cha dzina la Khristu.
“kusenza mtanda sizimakamba za zomelera za moyo. Izi ndi za kwa anthu onse. Pakuti ndi
ziphinjo, mayesero, kukhumudwa, kuwawadwa chifukwa cha moyo wochimwa wa mdziko.
Wokhulupirira sanaikidwe kunja kwa zowawazi. Nayenso amamva kuwawa, amadwala,
kukumana ndi ngozi, moto, zopsa za dziko chifukwa cha uchimo. Koma zowawazi sizimatenga
mtanda. Kunyamula mtanda ndi kuchokera mu kufuna kwa munthu osti zokakamizidwa ndi
zophinja za dziko ayi. Ndipo ndi zopitilira (tsiku ndi tsiku) kusankha kudzikana ku zokhuma za
thupi ndi cholinga chomvera Mulungu.
Kunyamula mtanda ndi kofunikira pa kukhala wophunzira. Yesu anati, “Aliyense amene
sanyamula mtanda ndi kunditsata sayenera ine.” Kunyamula mtanda sikosangalasa chifukwa ndi
nkhani yodzikaniza. Koma ikuyenera kuchitika mwa ufulu chifukwa cha Yesu ndi cholinga
chofuna kukhala wophunzira. Kunyamula mtanda, kukupangiseni kusiya zonse za dziko lapansi.
Ngati mtima wanu uli pa ndalama ndi zinthu zina, ndiye kuti mwachulukidwa kuti
simungatengenso mtanda. Ngati nthawi yanu imatha ndi zinthu za dziko lapansi ndi za thupi,
ndiye kuti manja anu alemedwa sangatengenso mtanda. Mutatha kudzikana nokha ndi kutenga
Page 131
131
mtanda, chotstira ndiko kumutsata. Mukuyenera kusiya zonse za moyo wakale ndi maubale a
kale a uchimo.
Izi sizitanthauza kuti wophunzira aliyense asiye ntchito yake ayi mdi nymba yake. Koma
akutanthauza kusintha kwa makhalidwe a munthu. Mwa njira ina zikhoza kutanthauza kusiya
nyumba, ntchito kapena okondedwa chifukwa cha uthenga wabwino. Mukuyenera kutsatira
kumene Yesu akutsogolera. Kukhala wophunzira kukuyenera kukhala koyambirira.
ZOLINGA CHENICHENI: Luka 9:61-62
Munthu wachitatu mu buku la Luka 9:757-62 amafuna kumutsata Yesu, koma amafuna kutero
mu njira yake. Kupita kukatsanzika banja lake chinali chodziwika koma Yesu anamiutana kuti
amutsate. Kodi cholinga chenicheni chinali chani mmoyo wake? Kukhala wophunzira kapena
kuchita zinthu zake? Cholinga cha munthuyi chinali chosakhazikika. Amabwerera mbuyo ndi
zomwe amachita kale ndi zatsopano zimene Yesu anamuitanira.
NJIRA NDI UTHENGA WA OPHUNZIRA
Kuitanidwa kukhala wophunzira kumakhuza kutumidwa kuphunzitsa mitundu yonse. Njira ya
ophunzira inali yochitira umboni. Yesu anati, “mudzakhala mboni zanga” Machitidwe 1:8.
Kutsindika sikunali kwambiri pa zimene akadachita mkukhala. Koma zimene zikadakula mu
zimene akanakhala. Kumapeto, otsatira Yesu anadzitenga okha kukhala mboni. Kumapeto a
moyo wake, Paulo anati:
Pamenepo pothandizidwa ndi Mulungu, ndiimirira kufikira lero lino, ndi
kuwacitira umboni ang'ono ndi akuru, posanena kanthu kena koma zimene aneneri
ndi Mose ananenazidzafika; 23kuti Kristu akamve zowawa, kuti iye, woyamba mwa
kuuka kwa akufa, adzalalikira kuunika kwa anthu ndi kwa amitundu (Machitidwe
26:22-23)
Kuchitira umboni kwa ophunzira kunali kulalikira, kuphunzitsa ndi kuonetsera mphamvu ya
Mulungu mwa zozizwa ndi machiritso. Uthenga wa umboni wawo unali uthenga wabwino wa
ufumu wa Mulungu:
Ndipo uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi,
ukhale mboni kwa anthu h mitundu yonse; ndipo pomwepo cidzafika cimariziro
(Mateyu 24:14).
Pakuti ndinapereka kwa inu poyamba, cimenenso ndinalandira, kuti Kristuanafera
zoipa zathu, mongamwa malembo; 4ndi kuti anaikidwa; ndi kutianaukitsidwa tsiku
lacitatu, monga mwa malembo (I Akorinto 15:3-4)
Izi ndi zimene Paulo anazitcha kuti “choonadi cha uthenga wabwino” (Agalatiya 2:5). Uthenga
wina unali wosaloledwa (Agalatiya 1:8).
YESU NDI OPHUNZIRA
Page 132
132
Yesu anali ndi ophunzira ake kwa zaka zitatu ndi theka za utumiki wa ntchito imene Mulungu
anamutumira kuti akachite. Imeneyi inali ntchito yapamwamba kwambiri. Amakwanitsa
kuyendera malo ochepa mu nthawinso yochepayo ndi kufikira anthu ochepa.
Kufuna kutsimikiza mathero a ntchito yake, Yesu anapanga ophunzira ngati chofunikira
kwambiri. Amadziwa kuti ophunzira ake adzapanga ophunzira ena ndi kufikira anthu ambir ku
midzi ndi mizinda imene Yesu sanakhale ndi mwayi ofikako.
Yesu akanakhala ndi nthawi yonse yodyetsa ndi kuveka osauka. Akanamanga mpingo waukulu
ku Yerusalemu. Panali njira zambiri zimene akanatha kugwiritsa ntchito ntchito. Koma Yesu
anasankha mafungulo aakulu a kuchulukana ku uzimu. Anadziwa kuti kuika moyo wake mwa
okhulupirika ochepa ulendo wochulukitsa umene sudzatha uyamba. Chidwi chake sichinali
kufikira khamu, koma pa anthu amene anali ndi kuthekera kufikira makamu a anthu.
Sizitengera kuti mukukhala dera liti, khaya muli ku mzinda waukulu, kaya ku midzi yakytali,
munamva uthenga wabwino chifukwa cha kukhulupirika kwa ophunzira a Yesu. Titati tibwerere
mbuyo ku mbiri ya uthenga wabwino, unafalikira mpaka utakupezani, njirayo ndiye kuti
ikanabwerera kumene kunali ophunzira ake.
Yesu ndiye chitsanzo cha ophunzira. Ngati mutsata chitsanzo chake, mudzazindikira kuti
ophunzira woberekana sachokera ku maphunziro a atsogoleri. Yesu anaona kufunikira kwa
kupereka mwambo.
Powerenga ubale wa pakati pa Yesu ndi akuphunzira ake, mfundo zambiri za kukhala ophunzira
zimaonekera. Izi ndi zofunika pa nkhani ya kukhala ophunzira:
1. KUSANKHA:
Kusankhidwa kwa ophunzira 12 kukupezeka pa Mateyu 5:1; 10:2-4; Marko 3:13-19 ndi Luka
6:12-16. Kusankhidwa kwa 70 aja kukupezeka ku Luka 10:1-16. Kusankhaku chinali chinthu
choyamba mu dongosolo lopanga ophunzira. Pamene Yesu anasankha ophunzira, anaitana ngati
anthu wamba. Ena anali osaphunzira ndipo anali ndi zolakwika ndi zolephera.
Zakhala zikunenedwa kuti ngati ophunzira 12 aja anayamba awonedwa kaye ndi mpingo wa
utumwi mu nthawi yathu ino, sakapatsidwa ntchito yotumikira. Koma Yesu anakhazikika pa
kuthekera kwawo osati zoooka zawo. Sanawasankhe chifukwa cha mmene analili koma
chifukwa cha chimene akanakhala. Anayang’ana kutsogolo kupitilira mavuto awo.
Wokhulupirira aliyense ayenera kupatsidwa mwambo ndi wina wake, simungakwanitse kupanga
ophunzira wina aliyense. Ndinu munthu mmodzi yekha ndipo muli ndi malire ku chiwerengero
cha anthu ophunzira amene mungawapange mu nthawi imodzi. Ichi ndi chifukwa chake kupanga
ophunzira kukuyenera kuchitika mmalo amene mpingo wanu ulili. Mbusa aliyense amakhala ndi
chitsimikizo kuti wotembenuka mtima aliyense amaphunzitsidwa ndi okhulupirira okhwima mu
uzimu.
Kodi Yesu anasankha bwanji ophunzira:
Page 133
133
Koyamba, podalira ndi Mulungu:
Sindikhoza kucita kanthu kwa Ine ndekha; monga momwe ndimva ndiweruza;
ndipo maweruzidwe anga ali olungama; cifukwa kuti sinditsata cifuniro canga,
koma cifuniro ca Iye ondituma Ine (Yohane 5:30)
Kachiwiri, anapemphera, Luka 6:12-13 amakamba kuti Yesu anapereka nthawi yake yonse usiku
kupemphera asanasankhe ophunzira amene amawafuna.
Kachitatu, Yesu anayamba kuwaitana ophunzira ake. Anthu sadzabera kwa inu kuti mukhale
ophunzira wa Yesu. Mukuyenera kuchitapo kanthu powayitana. Mwa mphamvu ya Mulungu
mukuyenera “kupanga” ophunzira.
Kachinayi, Yesu analongosola za mmene kukhala ophunzira kumakhalira. Monga mwaphunzira,
ophunzira akuyenera awerengere mtengo wake, kuika zoyambirira, ndi kuipanga ntchitoyi
kukhala cholinga chenicheni pa moyo.
Kukhala wophunziranso kumafuna okhulupirika ndi kutha kuphunzitsa ena. Paulo anamuuza
Timoteo kuti asankhe anthu okhulupirika ndi odzipereka ku zinthu zimene anaphunzitsidwa.
Anthu amenewa akuyenera kukhala ndi kuthekera kophunzitsa ena. Zinthu ziwiri izi ndi
zofunika pa kuchulukitsa. Ngati munthu Sali okhulupirika, sangathe kukwaniritsa udindo
wochulukana ku uzimu. Ngati ali wokhulupirira koma sakwanitsa kuphunzitsa, ndiye kuti
adzalephera.
Paulo analankhula za okhulupirira amene akadali ndi kuthekera kophunzitsa ena koma
osakhwima ku uzimu kuti atha kutero. Anthuwa ndiye kuti sanakonzeke kukhala ophunzira
enieni. Akuyenera kulangizidwa mu maziko a chikhulupirio. Kukhala ophunzira kumafuna
“anthu okhulupirika” otha kuphunzitsa enanso.
Anthu okhulupirika sikuti amakhala opanda vuto. Musasokoneze kukhala ophunzira ndi
ungwiro. Musakhazikike pa mavuto a munthu amene akufuna kukhala ophunzira. Muyang’ane
kuthekera kwawo. Kukhala ophunzira kumatenga nthawi kuti munthu akhale “wangwiro” monga
mmene zilili pa Aefeso 4. Ngakhale anthu okhulupirika amakhalanso ndi zofooka zoti athane
nazo monga mmene analili oyamba aja.
Dziko limatenga anthu aluso mkuwapatsa zochita. Amakhazikika pa luko lawo la ntchito.
Mulungu anati kutenga okhulupirika a makhalidwe abwino ndipo amawapatsa maluso a uzimu
ndi kuthekera. Anthu okhulupirika amapezeka kuti akwaniritse cholinga cha Mulungu. Pamene
Yesu anaitana Simoni ndi Andreya, mwachangu anasiya maukonde awo. Mawu oti “mwachangu
amatanthauza kuoezeka kwawo.
Pamene mwasankha anthu oti akhale ophunzira ayenera kupezeka. Amayenera kufuna kupanga
ophunzira ndikukhala choyamba ku moyo wawo. Anthu okhulupirikawa amakhala
olimbikitsidwa ndi masomphenya a uzimu. Pamene Yesu anampatsa Petro ndi Andreya
masomphenya osodza anthu, zinawalimbikitsa kusiya maukonde awo. Anthu okhulupirika
Page 134
134
amakhala ndi njala ya Mau a Mulungu, ngati mmene Yesu anachitira ndi ophunzira ake. Mitima
yawo inatekeseka ndi iwo pamene amawagawira Malemba (Luka 24:32,45). Amafuna ndi
kukhumba kuphunzitsidwa.
2. MAGULU:
Pamene Yesu anaitana ophunzira ake, anwaitana kuti akhale ndi Iye. Amakhalira limodzi,
mmautumiki onse komanso mu nyengo zonse. Kukhala ophunzira sikubwera chifukwa cha
misonkhano kapena maphunziro tsiku lolambira. Mukuyenera kukhala pa ubale ndi iwo amene
ndi ophunziranso. Muyenera mugawane nawo moyo wanu ndi iwo.
3. KUDZIPATULA
Kuchokera mu chiyanjano chimene anali nacho ndi Yesu, kudzipatula kunayamba. Yesu
anaitana ophunzira ake kuti adzipatule ku umuthu osati ku mpingo kapena bungwe.
Kudzipatulira kwa Mulungu kumafuna kumvera kwatunthu ku Mau ndi cholinga chake. Onani
Yohane 4:34; 5:30; 15:10; 17:4; and Luka 22:42).
4. MASOMPHENYA:
Yesu anawalimbikitsa ophunzira ake pa kuwapatsa masomphenya a uzimu. Anawaitianira ku
ntchito yaikulu kwambiri kuposa imene iwo amaidziwa mmoyo wawo wa tsiku ndi tsiku.
Anawaitana ophunzira ake kukhala asodzi a anthu (Mateyu 4:19). Anawapatsa masomphenya a
dziko lonse pa zokolola za uzimu (Yohane 4:35). Anawatsimikizira ndi mavumbulutso a ufumu
wa Mulungu (Mateyu 13).
5. MALANGIZO:
Malangizo amene Yesu amawapatsa amagwirizana ndi masomphenya a uzimu. Ngati
wophuznira wa Yesu amayenera kuphunzitsa zimene Yesu anaphunzitsa. Ili ndi gawo limodzi la
kutuma kwakukulu kopezeka pa Mateyu 28:20. Chidwi chikuyenera kukhala pa chiphunzitso cha
Yesu ndipo zimene zimaululika pa ziphunzitsozi zikhale zimene mpingo uyenera kumachita.
Maphunziro a Harvestime International Institute amapereka maphunziro a kukhala wophunzira.
Ndipo ndi chaputala chomalizira pa phunziroli. Komanso ali ndi phunziro limene limatchedwa
“Luso pa Kaphunzitsidwe” limene limakuphunzitsani inu kuti muthenso kuphunzitsa anthu ena
monga mmene Yesu anaphunzitsira.
Pamene mukuphunzitsa zimene Yesu anaphunzitsa, mumaphunzitsa zonse zimene zili mu Mau a
Mulungu chifukwa choti zakhazikika pa Chipangano Chatsopano monga Yesu anati:
Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi
inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'cilamulo ca Mose, ndi
aneneri, ndi masalmo…
Page 135
135
ndipo anati kwa iwo, Kotero kwalembedwa, kuti Kristu amve zowawa, nauke kwa
akufa tsiku lacitatu;
ndi kuti kulalikidwe m'dzina lace kulapa ndi kukhululukidwa kwa macimo kwa
mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu (Luka 24:44, 46-47)
6. KUONETSERA:
Yesu sanaphunzitse kuchokera pa zolankhula zokha ayi. Amaonetseranso zimene amaphunzitsa
u machiritso kwa odwala. Anali ndi mphamvu yotulutsa ziwanda ndi ulamuliro pa Satana.
Anaika chidwi pa osauka nawapatsa chakudya. Ophunzira sanali ophunzira okha, komanso anali
mboni pa zimene Yesu amachita ndi mphamvu ya Mulungu. “Cimene cinaliko kuyambira
paciyambi, cimene tidacimva, cimene tidaciona m'maso mwathu, cimene tidacipenyerera, ndipo
manja athu adacigwira ca Mau a moyo (I Yohane 1:1).
Yesu anaphunzitsa nakhala chitsanzo. Anaonetsera zimene anaphunzitsa ndi mmene anakhalira
ndi kutumikira. Ndipo anati:
Pakuti ndakupatsani inu citsanzo, kuti, monga Ine ndakucitirani inu, inunso mucite
(Yohane 13:15)
Kuonetsera kwa mphamvu kumapangitsa anthu kuti akhale ndi chidwi ku uthenga:
Ndipo makamuwo ndi mtima umodzi anasamalira zonenedwa ndi Filipo, pamene
anamva, napenya zizindikilo zimene anazicita (Machitdwe 8:6)
Paulo sanalankhule za choonadi cha uthenga wokha (Agalatiya 2:5) komanso za mphamvu ya
uthenga wabwino (Aroma 1:16). Analengeza ndi kuonetsera uthenga (I Akorinto 2:1,4).
Chifukwa cha kufunika kwa kuonetsera mphamvu mu kuchulukitsa, Harvestime International
Institute ali ndi phunziro lotchedwa “Mfundo za Mphamvu” ku maphunziro amenewa.
7. KUTENGA NAWO MBALI:
Chidziwitso chokhal sichipindula. Kuti uchite bwino, chidziwitso chiyenera chigwire ntchito.
Keneko imafika nthawi yoti muchitepo kanthu. Ophunzira samangomvetsera ndi kuonera
ziphunzitso za Yesu ndi chionetsero cha mphamvu koma amtenga nawonso mbali. Kuphunzitsi
chithu sizikwanira kuti utha kuphunzira. Kuphunzitsa kokha kuli ngati kuyera opareshoni ya mu
ubongo powerenga mabuku.
Ophunzira akuyenera kukhala ndi luso kapena mzeru za kachitidwe ka zinthu ka zimene
akuphunzira. Akuyenera kudziwa za mmene angalalikire uthenga, kupempherera odwala, ndi
kutulutsa ziwanda. Yesu amapereka mwayi umenewu kwa ophunzira ake. Werengani pa Marko
6:7-13 ndi Luka 9:1-6. Yesu anawatuma ophunzra ake kuti akayesere zimene anawaphunzitsa.
Onetsetsani kuti ophunzira anu ali ochita mawu osati ongomva kokha.
8. KUYANG’ANIRA
Page 136
136
Pamene ophunzira a Yesu anabwerera ku utumiki umene Yesu anawatuma, Yesu anasanthula
ntchito yawo (Luka 9:10). Mu maphunziro onse amen anachita nawo Yesu amawayng’anira
ophunzira ake. Samawasiya wokha kuti azilimbana nazo zinthu. Amakhala nawo kuti awakonze,
kuwadzudzula ndi kuwalimbikitsa.
Simungayerekeze kuti ntchitoyi mukhoza kuichita chifukwa mwamuonetsera wogwira ntchito
machitidwe ake, ndi kutuma ndi chiyembekezo chonse. Mukuyenera kumuyang’anira. Monga
ophunzira amakumana ndi zokhumudwitsa ndi zoletsa, mukuyenera kuwaphunzitsa za mmene
angakumaire ndi zimenezi. Kuyang’anira nthawi zina kumatchedwa “kulondola.” Paulo
amayang’anira komanso “kulondola” ophunzira ake:
Atakhala kumeneko nthawi, anacoka, napita pa dziko la Galatiya ndi Frugiya
m'dziko m'dziko, nakhazikitsaakuphunzira onse (Machitidwe 18:23)
nalimbikitsa mitima ya akuphunzira, nadandauliraiwo kuti akhalebe
m'cikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa m'ufumu wa Mulungu ndi zisautso
zambiri (Machitdwe 14:22)
KUPATSA ENA NTCHITO:
Gawo lomaliza la kukhala wophunzira linali pamene Yesu amapatsa ophunzira ake chochita pa
kukhala anthu opanga ophunzira ena. Anawapatsa ntchito ya kuchulukitsa ku uzimu kudziko
lonse lapansi.
MAKHALIDWE A WOPHUNZIRA WENIWENI
Ophunzira ayesu akuyenera kukhala okhulupirira okhwima ndi kuonetsa chipatso cha Mzimu
Woyera ngati chizindikiro mmoyo wawo komanso mphatso za mzimu zikhale zochitachita
mmautumiki awo.
Pali makhalidwe ambiri a kukhala wophunzira weniweni wa Yesu pamene mukuona zimene
Mau a Mulungu akufotokozera, koma Yesu anakhazikika pa makhalidwe 9. Wophunzira ndiye
amene:
1. AMASIYA ZINTHU ZONSE:
Amasiya zonse ndi kuyamba kumutsata Yesu.
Cifukwa cace tsono, yense wa inu amene sakaniza zonse ali nazo, sakhoza kukhala
wophunzira wanga (Luka 14:33)
2. KUDZIKANA WEKHA:
Wophunzira woona ayenera kudzikaniza yekha ndi kunyamula mtanda mwaufulu:
Page 137
137
Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ace, Ngati munthu afuna kudza pambuyo
panga, adzikane yekha, natenge mtanda wace, nanditsate Ine (Mateyu 16:24)
Ndipo amene ali yense sasenza mtanda wace wa mwini yekha, ndi kudza pambuyo
panga, sakhoza kukhala wophunzira wanga (Mateyu 14:27)
3. KUTSATIRA YESU:
Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ace, Ngati munthu afuna kudza pambuyo
panga, adzikane yekha, natenge mtanda wace, nanditsate Ine (Mateyu 16:24)
4. KUPANGA UFUMU WA MULUNGU KUKHALA WOYAMBA:
Cifukwa cace musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya ciani? kapena, Tidzamwa
ciani? kapena, Tidzabvala ciani
Koma muthange mwafuna Ufumu wace ndi cilungamo cace, ndipo zonse zimenezo
zidzaonjezedwa kwa inu (Mateyu 6:31,33)
5. KUONETSERA CHIKONDI CHA MULUNGU:
Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzace; monga
ndakonda Inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzace. 351 Mwa ici adzazindikira
onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli naco cikondano wina ndi mnzace
(Yohane 13:34-35)
6. KUKHAMA MMAWU:
…Ngati mukhala inu m'mau anga, muli akuphunzira anga ndithu (Yohane 8:31)
Mawu oti “kukhala” amatanthauza kuti kupitilira. Wophunzira amakhala akuphunzira mopitilira
ndi kugwiritsa ntchito Mau a Mulungu.
7. NDI OMVERA:
Kukhala mu Mau kumaposa kuphunzira. Uku ndi kuchita zimene mwaphunzira. Ndiye kumvera.
Sizikwanira kuwerenga, kuphunzira kapena kuloweza Mau. Amayenera apange chikhalidwe cha
munthu. Kukhala mu Mau kumaphtikizapo kumvera.
8. NDI OTUMIKIRA:
Kumkwanira wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wace, ndi kapolo monga
mbuye (Mateyu 10:25)
Sikudzakhala comweco kwa inu ai; koma amene ali yense akafuna kukhala wamkuru
mwa inu, adzakhala mtumiki wanu;
Page 138
138
Ndipo amene ali yense akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu
Monga Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka
moyo wace dipo la anthu ambiri (Mateyu 20:26-28)
9. KULEMEKEZA MULUNGU MWA KUBEREKA ZIPATSO:
Wophunzira ayenera kulemekeza Mulungu pobereka zipatso:
Mwa ici alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale cipatso cambiri; ndipo
mudzakhala akuphunzira anga (Yohane 15:8)
Pamene mubala chipatso cha ku uzimu, mumakuza chipatso cha Mzimu Woyera mu moyo wanu
(Agalatiya 5:20-23). Mumabala chipatso poberekana ku uzimu (Yohane 15:1-16)
YESERO LENILENI LA WOPHUNZIRA
Yesero lenileni la wophunzira ndi zimene zimzchitika pamene simukupezeka ndi iwo amene
munawaphunzitsa. Kodi mumakhalabe okhulupirika ku zimene munaphunzitsidwa? Kodi
mumaphunzitsa ena amene ali ndi kuthekera kochulukana? Ngati ndi choncho ndiye kuti kukhala
wophunzira kwanu kuli kopambana:
Wophunzira saposa mphunzitsi wace; koma yense, m'mene atakonzedwa mtima,
adzafanana ndi mphunzitsi wace (Luka 6:40)
Mu maphunziro anu ndi ena, yembekezerani mavuto monga mmene Yesu anakumana nawo…
-Munthawi ina yake, Petro, Yakobo ndi Yohane anawonetsa maganizo a udani popempha
moto kuchokera kumwamba kuti uwononge mudzi wa Samariya umene sumalandira
uthenga (Luka 9:51-55).
-Petro anamkana Yesu katatu (Luka 22:54-62).
-Onse atatu amagona mmunda wa Getsemane pamene anauzidwa kuti apemphere (Luka
22:45-46).
Koma anthu ochepawa anali oyenera kupereka nthawi yawo ku utumiki wa Yesu. Yesu
anatsimikira kukhala anthu okhulupirika, posatengera zofooka ndi zolephera zawo. Panthawi
imene Yesu sanali ndi iwo anakhalabe ophunzira ochulukitsa ku maiko onse a dziko lapansi.
Yesu anati:
Zotuta zicurukadi koma anchito ali owerengeka (Mateyu 9:37)
Page 139
139
Anthu otuta zokolola oyenera kututa zokolola za uzimu ndi ochepa. Kodi mwakonzeka kupereka
moyo wanu kukhala gawo limodzi la ochepawa?
Page 140
140
MAYESO ODZIYETSA NOKHA
1. Lembani Vesi Lotsogolera kuchokera pamtima.
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
2. Kodi mawu oti “kutembenuka” akutanthauza chiyani?
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
3. Perekani tanthauzo la mawu oti “wophunzira.”
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
_
4. Lembani mfundo zitatu zachidule cha maitanidwe a kukhala wophunzira
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
____________________________________
5. Lembani mfundo 9 zimene ndi zofunika kukhala wophunzira zimene mwaphunzira
zokhuza Yesu ndi ophunzira ake.
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
6. Lembani makhalidwe 9 a kukhala wophunzira weniweni.
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
7. Kodi yesero lenileni la wophunzira ndi liti?
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
__________________________________________________________________________
(Mayankho a mafunsowa akupezeka kumapeto kwenikweni kwa bukuli)
Page 142
142
KUPITILIZA KUPHUNZIRA
1. Kupereka mwambo kuli ngatinso “kudyetsa nkhosa” mawu amene amaonetsedwa
Mbaibulo za mmene mbusa angasamalire nkhosa zake.
Mulungu ali ngati mbusa: Ahebri 13:20; Masalmo 80:1-2 ndi Ezekieli 34:11
Yesu ali ngati mbusa wa nkhosa: Yohane 10:11-18
Mbusa ndi wotsogolera, woyang’anira kapena mlonda wa nkhosa. Amazipulumutsa ku
choipa, namanga mabala, kuzikonda ndi kudzidyetsa. Werengani Mateyu 9:36-38; Marko
3:14- 15; Yohane 21:15-17; Machitidwe 20:28.
2. Kuitana kwambiri kwa Yesu Khristu ndi kobwerezabwereza. Mawu oti “unditsate”
agwiritsidwa ntchito koposa ka 20. Mwachitsanzo Simoni ndi Andreya; Mateyu 4:19;
Marko 1:17. Onani zitsanzo zina.
3. Mawu oti “ophunzira” sakupezeka Muchipangano Chakale, koma mfundo za kupereka
mwambo zikupezekamo. Mwachitsanzo Yoswa anali wophunzira kwa Mose
(Deuteronomo 3:28). Perekani zitsanzo zina.
4. Onani mmene Paulo anachitira kalondolondo kwa ophunzira ake:
Ndi kalata: I Atesalonika 1:1
Ndi pemphero: I Atesalonika 1:2; 3:10
Potuma nthumwi: I Atesalonika 3:1-5
Popita yekha I Atesalonika 2:18
Page 143
143
CHAPUTALA CHA 11
KUKULA MOPINIMBIRA
ZOLINGA:
Paakutha pa chaputalachi muyenera:
Kulemba Vesi Lotsogolera kuchokera pamtima.
Kupereka tanthauzo la mawu oti “kupinimbira.”
Kuzindikira zinthu zimene zimatchinga kukula ku uzimu ndi kuchulukana.
Kupereka zithandizo zimene Baibulo limapereka pokonza mavuto amenewa.
VESI LOTSOGOLERA:
Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, Kapena wosaimirira m'njira
ya ocimwa, Kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza.
Komatu m'cilamulo ca Yehova muli cikondwerero cace, Ndipo m'cilamulo cace
amalingima usana ndi usiku.
Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; Wakupatsa cipatso cace pa
nyengo yace, Tsamba lace lomwe losafota; Ndipo zonse azicita apindula nazo
(Masalmo 1:1-3)
MAWU OYAMBA
Pali zinthu zambiri zimene zimakhudza kukula kwa munthu. Kuperewera kwa chakudya
choyenera kumatchinga kukulaku. Matendanso a mitundumitundu amakhudza kukula. Pamene
kukula kukusowa mthupi, pakuyenera kukhala chopulumukirapo chimene chingakonze vutoli
kupanda kutero kukula kupinimbira. Pamene kukula kuli kopinimbira, thupi silikulanso bwino.
Pamene mukuphunzira phunziroli, Baibulo limaonetsera mpingo ngati thupi la munthu. Pokhala
thupi la munthu, makulidwe amakhudzidwa ndi zinthu zina. Nthawi zina mavuto amachitika mu
mpingo ndiwo amene amalepheretsa kukula ku uzimu. Pamene kukula mu uzimu kuli
kopinimbira, mpingo umalephera kukula. Pakusowa anthu ndi ophunzira ndi kusowa kwa
kukhwima mu uzimu.
Yesu anati, “ndidzamanga mpingo.” Sitingabweretse kuchulukana tokha, koma tikhoza kuchotsa
zinthu zimene zimalepheretsa kukula. Pamene tikutero, ndiye kuti tikupanga malo ati kukula
kungachitike. Chaputala ichi chikuonetsa mavuto amene amalepheretsa kuchulukana. Pa vuto
lililonse pali Vesi yake imene ingakonze vutolo.
KUKULA KOPINIMBIRA
VUTO: KUSOWA CHAKUDYA CHA UZIMU.
Page 144
144
Thupi la munthu liyenera kupatsidwa chakudya ndi madzi kupanda kutero limafa. Thupi la
uzimu liyenera kupatsidwanso chakudya ndi madzi kupanda kutero limafa. Mipingo ina
simaphunzitsa Mau a Mulungu koma amaphunzitsa ziphunzitso za anthu. Amanena zimene
anthu afuna kudzimva (II Timoteo 4:3). Kuperewera zakudya za ku uzimu kumabweretsa njala
ya Mau a Mulungu (Amosi 8:11-12). Ena amanh=gophunzita “mkaka” wa mau ndipo anthu
sakula ku uzimu. Okhulupirira amanyalanyaza kuwerenga Mau a Mulungu kapena sasanthula
maziko a choonadi cha ngati “nyama” ya Mau a Mulungu. Monga thupi limafa popanda
chakudya, thupi la uzimunsi limafa.
YANKHO:
Kutsindikanso kobwereza pa Mau a Mulungu (Aroma 10:17). Phunzitsani mkaka ndi nyama ya
Mau a Mulungu (I Akorinto 3:1, I Petro 2:22 ndi Ahebri 5:12-14). Thupi la munthu silingadalire
mkaka konse. Ngakhale mwana wang’ono ayenera kuphunzira kudya chakudya cholimba. Mau a
Mulungu ndi mkate wa moyo wa uzimu.
VUTO: KUSOWA MASOMPHENYA.
Baibulo limati “popanda masomphenya anthu amasochera” (Miyambo 29:18). Masomphenya a
uzimu a anthu ena ndi amalire kubanja ndi kudera lawo. Ena amatanganidwa ndi malo ena
akutali ndi zinthu za mayina a chilendo, pamene anthu kunja kwa mpingo akufa opanda Yesu.
YANKHO:
Pakuyenera kukhala kufanana masomphenya azochitika zathu ndi za uzimu. Mpingo ukuyenera
kukhala ndi masomphenya a dziko lonse koma osasiyanso iwo amene ali mdera lathu. Awa ndi
masomphenya amene Yesu anapatsa ophunzira ake a zokolola za uzimu zimene zapsa kale
mmunda. Mundawu ndi dziko. Werengani Yonane 4.
VUTO: KUKULA KOCHEPA.
Werengani fanizo la ofetsa mu Marko 4:1-20. Pamene mbewu ya Mau a Mulungu sikhala ndi
muzu mmoyo wanu, mumakhala ndi kukula kochepa. Pamene chizunzo ndi zovuta zabwera
mumafa ku uzimu (Marko 4:17).
YANKHO:
Phunzitsani anthu kuti kuwerenga, kumva ndi kuphunzitsa Mau a Mulungu sikokwanira.
Akuyenera kukhala ochita Mau a Mulungu. Akuyenera kusintha moyo wawo (Yakobo 1:22-25).
Ndi pakulowa kwa Mau mumtima kumene kumabweretsa kusintha (Masalmo 119:130).
VUTO: KUSOWA KUTSADZA
Mipingo kwanthawi yaitali yakhala yosabereka mu njira zawo ndi dongosolo lawo. Pamene
zochitikazi sizisadzidwa, kubala zipatso kumatha. Popanda kutsadza, Pang’ono ndi pang’ono
imfa imabwera imaononga moyo. Pamene mtengo sunatsadzidwe ukhoza kumakula moongoka
Page 145
145
koma uli wakufa. Palibe zipatso, kukula komanso kuchulukana. Mtengo kukhalapo koma opanda
moyo. Izi ndi chomodzimodzi ndi kudziko la uzimu.
YANKHO:
Nthambi zosabereka ziyenera kudulidwa ndi cholinga chofuna choti mtengowo ubereke zipatso
zambiri. Kudziko la uzimu tikuyenera kudula ntchito zosathandiza mmoyo wathu ndi mumpingo
wathu. Njira ndi ndondomeko zimene sizimabweretsa athu kwa Yesu ndi ophunzira zichotsedwe.
Mikumano iwonedwenso, kaya ndi ndondomeko ziunukilidwenso ngati ndi zothandiza.
VUTO: KULEPHERA KUDZIWA MALO AMENE ANGALANDIRE UTHENGA:
Mu fanizo la ofetsa mu Marko 4:1-20, panali dothi labwino ndi lina losakhala bwino. Kukula
kochepa kumachitika mu dothi losakhala bwino.
YANKHO:
Pali malo ena amene ali ndi mwayi wochepa wochulukana. Ndipo pali malo ena amene
amakhalaokonzeka pa zokolola za uzimu amene amapereka mwayi olalikira uthenga wabwino.
Anthu oyenera ayenera adziwike ndi kuchitapo kanthu kwa anthu amenewa. Pamene Paulo
anamva Mzimu Woyera kuti akubweretsa anthu amitundu kukhala ophunzira ku Antiokeya,
mwachangu anachoka ku Tarisi mkupita ku Antiokeya. Pamene nthawi inali isanakwane ku
mAsiya, Paulo anakhalabe kumene mpakana Mulungu anamutsekula maso. Khazikikani ku malo
kumene kuli kuthekera. Pitilizani kufesa ndi kudikira nthawi yoyenera kuti mudzatute zikapsa.
VUTO: ZOFUNIKA ZOLAKWIKA.
Atsogoleri a uzimu ali ndi zofunika zimene ndi zolakwika pamene ali ndi chidwi ndi zochita za
mpingo kuposa pemphero ndi kutumikira Mau a Mulungu. Zofunika zimakhala zachiwiri monga
mamangidwe ndi tchito zina. Kukoza mpingo kumakhala kofunika kuposa utumwi.
YANKHO:
Yesu sanalankhulepo za mamangidwe apamamba. Akhristu amapanga zochita zambiri. Ngakhale
izi sizolakwika, koma kuchulukana kumalephereka pamene chidwi chikukhala pa mamangidwe
osati kulalikira ndi kupanga ophunzira. Vuto la zofunika ndi ziti ndi mayankho ake zikupezeka
ku Machitidwe 6:1-6. Pamene atsogoleri aika chidwi pa pemphero ndi kutumikira Mau a
Mulungu kuchulukana kumabwera (Machitidwe 6:7).
VUTO: UTUMIKI WOSAGWIRIZANA NDI ANTHU
Mipingo ina yasiya kukula chifukwa choti utumiki sugwirizana ndi anthu. Mwina mtumiki
sakhala mmodzi wa anthuwo. Amakhala wa chikhalidwe china zimene ndi zovuta kupereka
uthenga mu chiyankhulo chimene angamve.
YANKHO:
Page 146
146
Atsogolera ayenera kuchokera ku mpingo umene akuchokera ngati kuli kotheka pamene mpingo
wadzalidwa (Tito 1:5). Atsogoleri a kudera amene ali ndi chikhalidwe ndi chiyankhulo cha
kumaloko amatha kulumikizana ndi anthu a kumeneko mosavuta.
VUTO: “BWERANI MUWONE” OSATI “PITANI MUKAWAUZE”
Mipingo yambiri yatenga njira ya “bwerani” osti “pitani” imene Yesu analamulira. Mipingoyi
imakhala ndi mikumano ndi dongosolo limene limakopa anthu osakhulupirira “kubwera” ku
mpingo. Sapita ku dziko kukawapeza ndi uthenga wabwino ndi kuwabweretsa ku mpingo.
Amatsekula zitseko mkumadikira anthu kuti abwere, koma palibe amene amabwera. Mu mpingo
umenewu mamembala amakangalika ndi mikumano, misonkhano, maphunziro mmalo mwa
maulaliki otuluka.
YANKHO:
Mpingo ukuyenera kukhala wogwirira ntchito Mulungu mdzikoli. Koma mpingo wakhala
okangalika kusiyana ndi kukhala maziko a Mulungu otumiza ophunzira mmunda wa dziko
kukachulukana. Mpingo ukuyenera kusiya kudzitumikira wokha ndi kuyamba kutumikira dziko.
Mpingo ukhale malo amene okhulupirira alandirapo maphunziro ndi kukonzekerdwa kupita ku
dziko lapansi kumene kuli ochimwa ndi kuwatengera kwa Yesu. Njira ya Yesu yopita iyenera
kutsindikizidwa (Mateyu 28:19; Machitidwe 1:8).
VUTO: TCHIMO LOSAVOMEREZA
Tchimo losavomereza mmoyo wa membala wa mpingo limatchinga kukula moyo wauzimu.
YANKHO:
Werengani malangizo a Paulo kwa mpingo wa kwa Akorinto othana ndi tchimo losavomereza
kwa munthu (I Akorinto 5:11-13). Ngati membalayi walapa, akuyenera kulandilidwanso (Onani
II Akorinto 2:4-8).
VUTO: MAVUTO A MUNTHU OSATHA:
Mikangano imakhala mu mpingo ngati membala wa mpingo akali ndi mangawa ndi munthu
wina. Ngati sakhala pamodzi kufuna kuthetsa magawano amayamba. Mavuto osatha
amalepheretsa kuchulukana.
YANKHO:
Mateyu 18:15-17 amapereka malangizo othetsa mavuto pakati pa anthu mu thupi la Yesu.
Werengani chitsanzo cha Paulo ndi Banaba mu Machitidwe 15:36-41. Ngati mabvutowa atha
bwinobwino, ngakhala kugawana kungabweretse kuchulukana mu ufumu wa Mulungu.
VUTO: UTSOGOLERI WA UZIMU WOSAYENERA:
Page 147
147
Kukula kumakhudzidwa ngati atsogoleri safikira makhalidwe a uzimu opezeka Mbaibulo.
Miyeso ya atsogoleri a mpingo oikidwa ndi Mulungu ndi zoyenereza ku uzimu. Sasamala za
maphunziro a munthu ndi kuthekera kwa munthu kuyerekeza ndi makhalidwe a uzimu wa
munthu (onani I Samueli 16:7).
YANKHO:
Mtaogoleri ayenera kusiya udindo wake kufikira aika “nyumba yake” (moyo wake wa uzimu ndi
banja lake) mmalo mwake. Atsogoleri ayenera kukhala ndi zowayenereza zomwe zili mu I
Timoteo 3 ndi Tito 1:5-9.
VUTO: KUKANA KUSINTHA.
Anthu ali ndi chikhalidwe chokana kusintha. Ambiri amakhutira ndi zinthu zimene zakhala
zikuyendera kwa zaka 40 zapitazo. Sakonda kuvomereza zinthu zatsopano.
YANKHO:
Kumbukirani kuti cholinga cha mpingo ndi kuchita maulaliki ndi kuchulukana ku uzimu
sikumasintha. Njira zokwaniritsa cholingachi zimatha. Ndi zoona kuti tiyenera kugwiritsa ntchito
njira za Mbaibulo za mpingo woyamba, koma dziko lasintha kuchokera nthawi imene ija.
Sitingakane njira zatsopano chifukwa sizimapezeka Mbaibulo. Monga makina a computer, ma
disiki a uthenga wabwino amene Paulo sanagwiritse ntchito. Pakuti kunalibe nthawi imeneyo.
VUTO: MAVUTO A KULUMIKIZANA
Kuchulukana kumalephereka ngati palibe kulumikizana bwino pa uthenga wabwino. Atumiki
amayeera kusangalasa anthu awo ndi mawu a pamwamba ndi kuonetsa chidziwitso cha
maphunziro awo a umulungu. Potero amalemphera kulumikizana ndi zosowa za anthu. Ntchito
zawo sizigwirizana ndi mawu awo.
YANKHO:
Uthenga ukuyenera kufalisidwa mu njira yoti anthu amvestere. Alaliki, aphunzitsi ndi avangeli
ayenera kupereka uthenga mu muyeso wa anthu amene akuwalalikira mmalo mwa mawu a akulu
ndi kuonetsa chidziwitso. Pamene Yesu amaphunzitsa, anthu amamvetsera ndi kumvetsetsa
(Marko 12:37).
Mmene uthenga ukuperekedwa uyenera kusinthidwa molingana ndi mmene anthu alili pa
maphunziro awo (Aroma 1:14). Kulumikizana kwa mmawu kuyenera kugwirizana ndi
makhalidwe a moyo. Tikuyenera kukhala ochita mawu ndi olengeza mawu. Kulengeza kwa
chikhulupiriro chathu kumakhala kopambana pamene zinthu za Mulungu zikuonekera mmoyo
wathu (Filemoni 6).
VUTO: KUSIYANA KWA ZIKHALIDWE, DERA NDI ZIPEMBEDZO.
Page 148
148
Mipingi ina simakwanitsa kufikira anthu mdera lawo chifukwa “Sali ngati ife.” Samatumikira
kwa iwo amene ndi osiyana chikhalidwe, mtundu, ngakhale chiyankhulo. Mpingo ina imakana
kuwoloka malire posafuna kuti anthu a dera lina akhale a mumpingo mwawo. Ena amakana
chiyanjano ndi mipingo ina. Ena anazipatula kudziko moti sangachulukane chifukwa
samalumikizana ndi osakhulupirira.
YANKHO:
Onani Aefeso 2:14. Palibe makoma a kusiyana mwa Yesu. Mpingo wamanga makoma a
kusiyana amene akuyenera kuchotsedwa. Tikuyenera kudutsa chikhalidwe chathu, chiyankhulo,
dera komanso zipembedzo ndi cholinga choti tikafikire anthu onse. Tikuyenera kusiya pambali
zomemera ndi machimo ndi kuyamba kuika chidwi pa kufikira anthu a dziko lonse ndi uthega
wabwino (Ahebri 12:1-2). Sitikuyenera kudzipatula kudziko, koma tikhale mdzikoli koma
osachita nawo ntchito za uchimo (Yohane 17:15). Kudzipatula kudziko sizitanthauza kusiyana
kapena kusalana.
VUTO: KUKHALA ONERERA OSATI OTENGA NAWO MBALI
Onera ndi anthu amene amangoyang’anira koma satenga now mbali mu zochitika za Mulungu.
Samaberekana mu uzimu. Amanyalanyaza kulalikira ndi kupanga ophunzira kwa atumiki
“ophunzira.” Mpingo wodzala ndi anthu ononerera sumakula.
YANKHO:
Munthu wina aliyense adziwe udindo wake pa lamulo la Yesu pa Mateyu 28:19-20. Anthu
akuyenera kutsogoleredwa kuti agwiritse ntchito mphatso zawo za uzimu ndi cholinga chakuti
mpingo ukule bwino (Timoteo 1:6). Atumiki ayenera kukonzekeretsa anthu ku utumiki (Aefeso
4:12). Munthu aliyense akhale wochitachita, ndi khomo lililonse likhale malo a ulakili (II Timote
2:2).
VUTO: OTEMBENUKA SAKHALA OPHUNZIRA
Okhulupirira atsopano sakula kukhala ophunzira. Amabwerera ku moyo wawo wakale kapena
kukhala ana mu uzimu amene sakwanitsa kuchulukana ku uzimu.
YANKHO:
Okhulupirira tsopano ayenera kuumbidwa ndi kukonzekeredwa ku utumiki ngati kuchulukana
kupitilire. Ulaliki sukhala okwanira kufikira wotembenuka mtima akhala wamphamvu wa Yesu.
Chiphuncityso chikuyenera kuchitika ukaliki pamene zikuchitika (Mateyu 28:19-20).
VUTO: MANTHA
Kuopa kulemphera ndi mdani wamkulu pa kuchulukana. Werengani fanizo la matalente pa
Mateyu 25:14-30. Kapolo amene amaopa sanachite bwino. Sanachulukane mu uzimu.
Page 149
149
YANKHO:
Khalani pa ubale ndi Mulungu mwachikondi osti mwa mantha (I Yohane 4:18).
VUTO: CHIDWI PA NTCHITO OSATI KULAMBIRA
Dongosolo, ndondomeko ndi zochitika za mpingo zikhoza kutenga malo a malambiro. Mwambo
wa mapemphero ukhoza kukhala wa zolemgeza, kupereka ndalama ndi zina.
YANKHO:
Ikani koyambirira zinthu zofunika mu mpingo. Chikondi ndi kulambira Mulungu zikhale
koyamba. Chikondi ndi utumiki kwa ena zibwere pambuyo. Mapulogalamu ena amabwera
pambuyo pa zochitika ziwiri zazakuluzi (Mateyu 12:29-31).
VUTO: KUTUMIKIRA DERA OSATI ANTHU.
Pali zosowa zambiri lero mu dziko lathupi. Pali osauka ambiri amene afunika chakudya, zovala,
ndi malo okhala. Pali anthu amene afunika mankhwala ndi ntchito. Pali mavuto ena a
kayendetsedwe ka boma, maphunziro amene akufunika kukonzedwa. Izi ndi zosowa zenizeni
zimene mpingo ungather kutumikira anthuwa mu dzina la Yesu. Koma nthawi zambiri chidwi
chathu chimakhala kutumikira dera osati kupulumutsa moyo wa anthu.
YANKHO:
Mkazi amene anali ndi Yesu pachitsime amafuna madzi a kuthupi koma Yesu anampatsa
chosowa chake chenicheni cha ku zuimu (onani Yohane 4). Maitanidwe a akulu a mpingo
sikutumikira dera, koma kupulumutsa anthu amene ndi ovutika ku uzimu. Kutenga nawo mbali
mu zochitika ndi kuchita mwa nzeru sikudzapangitsa anthu anjala kufuna mkate wa moyo.
VUTO: KUSAKHULUPIRIRA
Werengani nkhani ya Israyeli pa malire a dziko lolonjezedwa la Mulungu (Numeri 13). Israyeli
sanalowe mdziko la malonjezano chifukwa chosakhulupirira. Anabwerera mbuyo mu chipululu
muja ndipo mbadwo onse unatha kwa zaka 40.
Wokhulupirira aliyense ndi mpingo uliwonse ayenera afike pa “Kadesi” pa malo a uzimu.
Akhoza kupita chitsogolo mu chikhulupiriro mkufusa malonjezo a Mulungu, kapena abwerera
mbuyo mkusakhulupirira kwawo mkufa ku uzimu.
YANKHO:
Kusakhulupirira kumalepheretsa kukula komanso kuchulukana. Mpingo ukuyenera kukhulupirira
kuti kukwaniritsa chipambano pa ulaliki ndi kupanga phunzira kwagona pa chikhulupiriro
(Marko 6:15). Kukhulupirira kutenga malo a kusakhulupirira. Chikhulupiriro chimakula ndi Mau
Page 150
150
a Mulungu. Anthu ayenera kuchita zinthu mwachikhulupiriro. Ndipo chikhulupiriro chikhale ndi
ntchito yake (Yakobo 2:26).
VUTO: UNYINJI OSATI KHALIDWE
Chidwi pa unyinji osati khalidwe kumabweretsa nthu osakhwima mu uzimu. Zimatheka kukhala
ndi anthu ambiri koma olephera kukhala ophunzira ndi osakhwima.
YANKHO:
Onaninso chaputala cha 6 cha phunziroli. Gwiritsani ntchito mfundo kuti mukule ku uzimu.
VUTO: ANTHU AMASOCHERA MU KHAMU LA ANTHU.
Pamene mpingo ukukula, anthu “amataika mu gulu la anthu.” Amayamba kuzimvu kuti alipo
ambiri. Sipakhala kulumikizana, kusamalana ndi chidwi. Chidwi chimakhala pa khamu osati pa
munthu.
YANKHO:
Moyo umodzi ndi wopambana kuposa dziko lonse (Mateyu 16:26). Ngakhle tiyenera
kukhuzidwa ndi dziko lonse, koma tisachotse chidwi chathu pa munthu mu khamu. Anthu
amabadwa mu uzimu kwa nthawi imodzi koma amataika payekha.
Palibe chithu ngati kutembenuka mtima kwa gulu. Ngakhale gulu litembenuka ku ulaliki,
munthu aliyense amapnga chisankho yekha. Tisaike chidwi chathu pa khamu la anthu ndi
kuiwala munthu mmodzi. Yesu amaitana munthu mu khamu la anthu mkuyamba kumutumikira.
Kuyamba mautumiki ang’ono ndi njira imodzi yosunga utumiki wa anthu mu khamu ndipo
kuchulukana mumpingo kumatheka.
VUTO: TIMAGULU TA MUMPINGO
Nthawi zina “timagulu” tiyamba mu mpingo. Awa ndi magulu a ang’ono a anthu amene
amakhala pamodzi ndi cholinga chofuna kusiyanitsa kapena kukana kuyanjana ndi anzawo.
Gululi limalola anthu ena kukhala nawo koma ena amawakana.
YANKHO:
Baibulo limaphunzitsa kuti mchitidwe oterewo ndi wolakwika. Werengani Yakobo 2:1-10.
Chikhalidwe choterechi chimafuna kulapa chifukwa ndi tchimo.
VUTO: GULU LAMOYO, KOMA ANTHU AKUFA
Gulu ndi lofunika, koma kukula mu uzimu kumalephereka pamene chidwi chili pa gulu osati
kukhala ndi moyo wa Mulungu. Miyambo, malamulo, ndi zikhalidwe zimachotsa uzimu
Page 151
151
weniweni (Marko 7:13), gulu la mumpingo likhoza kukhala ndi moyo ndithu, koma anthu amene
ndi moyo weniweni wa uzimu mthupi umafa ngati palibe moyo wauzimu.
Mipingo yoterryi imakhala ndi ndondomeko zabwino ndipo amakhala ndi “dzina limene
amachitira izi” koma ku uzimu akufa (Chibvumbulutso 3:1). Moyo wa uzimu umafa. Amakhala
ndi maonekedwe a chipembedzo koma mphamvu yake adaikana (II Timoteo 3:5)
YANKHO:
Mpingo umafanizidwa ngati thupi. Thupi ndi lamoyo, osati chith cha ziwalo ayi. Gulu
silingapereke moyo. Koma chithu cha moyo chingathe kupereka moyo. Moyo wa thupi la
mpingo ukuyenera uphunzitsidwe ndipo utumiki utsindikidwe (I Akorinto 12).
VUTO: KUSOWA CHIKONDI
Mpingo ukhoza kukhala ndi machitichita a uzimu, koma opanda chikondi. Anthu samachezeka.
Samakondana wina ndi nzake. Pamakhala chiwawa, udani, malingaliro oyipa kwa wina.
YANKHO:
Utumiki uliwonse, mphatso iliyonse ndi ntchito iliyonse ya munthu kapena mpingo ili chabe
popanda chikondi. Werengani ndi kugwiritsa ntchito I Akorinto 13.
VUTO: KUSOWA KWA ZINTHU
Anthu ndi ndalama ndi zinthu zofunika pa kuchulukana. Kukula kukhoza kukhala kopinimbira
pamene palibe anthu odzipereka ku masomphenya. Kosowa kwa thandizo la ndalama
kungalepheretse kukula ndi kutukuka kwa mpingo.
YANKHO:
Tsindikani za Ufumu wa Mulungu osati kukamba za utumiki wa munthi. Yesu analonjeza kuti
zinthu zonse zimene tizifuna tidzapatsidwa tikachita zimene zili pa Mateyu 6:33. Pemphererani
anthu oyenera kugwira ntchito ya Mulungu kuti akakolole kholola la uzimu mmunda (Mateyu
9:37-38).
Page 152
152
MAYESO ODZIYETSA NOKHA
1. Lembani Vesi Lotsogolera kuchokera pamtima.
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
2. Perekani tanthauzo la kukula “mopinimbira.”
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
3. Werengani zitsanzo za nyengo za mipingo yambiri mmene zilili. Zindikirani mavuto ndi
kupereka mayankho ake a Mbaibulo.
Chitsanzo A. Akazi awiri mumpingo samalankhulana wina ndi mzake. Mkazi A
anayankhula zinthu zosakhala bwino kwa mkazi B. Kodi mungapereke yankho laotani?
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
Chitsanzo B. Usiku wa sabata iliyonse mpingo umakhala ndi zochitika, koma anthu
ochepa ndiwo amene amabwera kwa Ambuye. Kodi pamenepa vuto ndi chiyani? Yankho
ndi liti?
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
Chitsanzo C. Okhulupirira atsopano ochepa ndiwo amene amapezeka ku mpingo
mwakanthawi, kenako amabwereranso ku zintchito zawo zakale za uchimo. Ena
amakhalabe mu mpingo, koma makanda mu uzimu. Kodi vuto ndi chiyani? Nanga
yankho ndi liti?
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
________________________________________________________________________
(Mayankho a mafunsowa akupezeka kumapeto kwenikweni kwa bukuli)
Page 153
153
KUPITILIZA KUPHUNZIRA
1. Bwerezani mavuto a kukula mu uzimu amene akambidwa mu chaputalachi. Pangani
mndandanda wa zinthu za mumpingo wanu zimene zimalepheretsa kukula ndi
kuchulukana. Kodi mavutowa mungawakonza bwanji?
2. Onaninso phunziro ndi kudziwa zinthu zimene zimalepheretsa kukula kwa moyo wanu
wa uzimu. Kodi mavutowa mungawathetse bwanji?
3. Unguzani mpingo wanu ndi moyo wanu wa uzimu. Kodi zinthuzi zikulepheretsa kukula
kwa moyo wanu wa uzimu kupatula zimene zatchulidwa mu chaputalachi? Ngati ndi
choncho lembani mndandanda wa mavutowa ndi kupeza mayankho mu Baibulo.
4. Werengani makalata 7 a kumpingo mu Chibvumbulutso chaputala 2-3. Lembani
mndandanda wa mavuto omwe amene amapezeka mmipingoyi ndi mayankho ake
ochokera kwa Mzimu Woyera.
Page 154
154
CHAPUTALA CHA 12
MALO OCHITIRAPO MAPHUNZIRO
ZOLINGA:
Pakutha pa chaputalachi muyenera:
Kulemba Vesi Lotsogolera kuchokera pamtima.
Kudziwa njira zimene Paulo anagwiritsa ntchito pophunzitsa okhulupirira a ku Aefeso.
Kulongosolo malo ochitirapo maphunziro ku Aefeso.
Kulongosola cholinga chokhala ndi malo ochitirapo maphunziro.
Kulemba chidule cha malangizo oyambitsa malo achitirapo maphunziro.
Kuyambitsa malo ochitirapo maphunziro.
VESI LOTSOGOLERA:
Koma pamene ena anaumitsa mtima ndi kusamvera, nanenera zoipa Njirayo
pamaso pa anthu, anawacokera, napatutsa akuphunzira, nafotokozera masiku onse
m'sukulu ya Turano.
Ndipo anacita comweco zaka ziwiri; kotero kuti onseakukhala m'Asiya anamva
mau a Ambuye, Ayuda ndi Ahelene (Machitidwe 19:9-10).
MAWU OYAMBA
Musanayambe kuphunzira chaputalachi, werengani Machitidwe 19:1-20. Ndimeyi imakamba za
utumiki wa Paulo ku mzinda wa Aefeso kumene Paulo anagwiritsa ntchito njira zapadera za
kuchulukana ku uzimu. Anakhazikitsa malo ochitirapo maphunziro. Mu chaputala ichi
muphunzira mmene mungachulukanire kudzera mu utumiki okhala ndi malo ochitirapo
maphuziro.
NJIRA YA AEFESO
Pamene Paulo anafika ku Aefeso, anafufuza ophunzira amene analiko. Anthuwa amenewa anali
atamva kale ndi kulandira uthenga wabwino mkukhala otsatira Yesu (Machitidwe 19:1).
Okhulupirira atsopanowa amafunika kupitiliza maphunziro ndi cholinga choti akhale atumiki
amphamvu mu mzinda mwawo. Chidwi choyamba cha Paulo chinali kuphunzitsa ophunzirawa
zokhudza Ufumu wa Mulungu.
Paulo anawaphunzitsa kudzera mu zimene amadziwa ndipo chinthu choyamba chimene anachita
kunali kuwatsogolera ku moyo watsopano wa uzimu, ndiwo ubatizo wa Mzimu Woyera (onani
Machitidwe 19:2-8). Kudzera mu chionetsero cha mphamvu ya Mulunngu mmoyo wake, Paulo
Page 155
155
anawaphunzitsa chitsanzo chake. Anachitira umboni za mphamvu zambiri zimene anachita mu
dzina la Yesu (Machitidwe 19:11-12). Iwo amene sanali otsatira enieni a Yesu anafika poyera
mkulapa (Machitidwe 19:13-17). Otembenuka mtima amapezeka ambiri (Machitidwe 19:17-20).
Pamene panali chitsutso pa uthenga wabwino kuchokera kwa atsogoleri a malamulo, Paulo
anakhazikitsa malo ochitirapo maphunziro a ophunzira a Yesu ku Aefeso:
Koma pamene ena anaumitsa mtima ndi kusamvera, nanenera zoipa Njirayo
pamaso pa anthu, anawacokera, napatutsa akuphunzira, nafotokozera masiku onse
m'sukulu ya Turano (Machitidwe 19:9-10).
Malo amene Paulo anakhazikitsa amapereka maphunziro a zaka ziwiri kwa ophunzira. Cholinga
cha sukuluyi chinali kufuna kuchulukitsa ophunzira amene akhoza kufalitsa uthenga wabwino:
Ndipo anacita comweco zaka ziwiri; kotero kuti onseakukhala m'Asiya anamva
mau a Ambuye, Ayuda ndi Ahelene (Machitidwe 19:10).
Malo a maphunzirowa analibe malire pa chikhalidwe. Ophunzira amatumikira kwa ayuda ndi
amitundu omwe. Sukuluyi inalibenso malire pa dera. Ophunzira samatumikira mu mzinda wawo
wa Aefeso okha, koma anafika mu chigawo chonse cha m’Asiya. Malo amphunziro amene Paulo
nakhazikitsa anakwaniritsa cholingachi:
Ndipo anacita comweco zaka ziwiri; kotero kuti onseakukhala m'Asiya anamva
mau a Ambuye, Ayuda ndi Ahelene (Machitidwe 19:9-10).
Cotero mau a Ambuye anacuruka mwamphamvu nalakika (Machitidwe 19:20)
Sukulu yak u Aefeso inaphunzitsa okhulupirira kuti akhale atumiki amphamvu a uthenga
wabwino. Ophunzirawa anachulukana mu uzimu kufikira onse amene anali mu m’Asiya ndi Mau
a Mulungu. Pokhazikitsa malowa Paulo anachulukitsa utumiki wake.
NTCHITO YOPITILIRA
Werengani Machitidwe 19:23-41 ndi 20:1. Kupanga komanso kugulitsa kwa zinthu za matsenga,
mabuku, ndi zina anali malonda a akulu ku Aefeso. Pamene anthu analapa machimo awo ndi
kuyamba kutsata njira ya uthenga wabwino, sanagulenso katunduyi zimene zimagwira ntchito pa
chipembedzo cha mafano. Zonse zimene anagula kale anaziotcha.
Amalonda amene amapezamo phindu mu zogulisa zawo anakwiya. Moti mpungwepungwe
unayamba koma kumapeto, Paulo anachoka ku mzindako. Koma atngochoka Paulo, anasiya
chinachake chofunika kwambiri. Anasiya gulu limene linali ophunzira amene amafalitsa uthenga
wabwino. Anasiya malo ochitirapo maphunziro amene anapitilira kutsogoleraanthu obadwa
mwatsopano mkukhala ophunzira. Malo amene Paulo anakhazikitsa anapitilira kuchuluka
ngakhale mu nthawi imene sanali ku mzindako.
CHOSOWA CHALERO
Page 156
156
Chosowa chokhala ndi malo ochitira maphunziro chilipobe lero. Pamene anthu atembenuka
mtima mkuchuluka, ndi zofunikira kuti akuphunzitsaidwa. Ophunzirawa ayenera kupatsidwa
udindo wofikira anzawo ndi uthenga wabwino.
Pamene dziko likukumana ndi kusintha kwa maboma, atumiki ambiri amishoni amakakamizidwa
kuchoka dziko limene akutumikira. Ngati kuchulukana kupitilre mu nthawi imene iwo kulibe,
akuyenera kusiya malo ochitira maphunziro ngati mmene zinalili ku Aefeso.
Zotsalira za chaputalachi zikupereka malangizo okhazikitsa malowa. Akhoza kuyambika ndi ka
gulu kakang’ono ka mipingo kapena ndi munthu mmodzi amene ngati Paulo anagwira
masomphenya ochulukitsa mu njira imeneyi.
KODI TINGAKHAZIKITSE BWANJI MALO OCHITIRAPO MAPHUNZIRO
Pofuna kuyamba malo ochitirapo maphunziro:
1. FUNANI DONGOSOLO LA MULUNGU:
Ngakhale Paulo anaphunzitsa ophunzira kulikonse amatumikira, sanakhazikitsa malo a
maphuziro kulikonse amapita. Mwaphunzira njira zambiri za kuchulukana ku uzimu mu
phunziroli. Cholinga cha Mulungu cha kuchulukana kwa ophunzira ndiko kufalisa uthenga
wabwino basi. Njira zimene anagwiritsa ntchito pofuna kufikira cholingachi zinali zosiyana.
Gawo loyamba lokhazikitsa malo ochitita maphunziro ndi kufunafuna chifuniro cha Mulungu.
Harvestime International Institute amapereka phunziro mutu wake, “Kudziwa Kulankhula kwa
Mulungu” limene lingakuthandizeni kumvetsa mmene Mulungu amaululira chifuniro chake kwa
munthu. Podziwa kuti dongosolo la Mulungu limasiyana potengera malo, chikhalidwe, chosowa
komanso njira za dongosolo la malowo zimasiyana.
2. KUMVETSA CHOLINGA:
Mukuyenera kumvetsa bwino cholinga chokhala ndi malo ochitapo maphunziro molingana ndi
chitsanzo cha Aefeso. Cholinga cha sukuluyi sikuphunzitsa anthu kupeza mapepala a ntchito,
malonda, kampani kapena ulimi ayi. Makoleji ndi masukulu a maluso amapanga izi.
Sukulu yaku Aefeso inaphunzitsa ophunzira ndi kuwakonzekeretsa ku ntchito ya utumiki.
Cholinga chinali kufalisa uthenga wabwino ku dziko lonse ndi kwa anthu a mitundu yonse.
Okhulupirira atsopano anaphunzitsidwa kukhala ophunzira ndi kupitilira kuchulukana. Ena mwa
ophunzirawa anali ochita malonda kapena alimi. Koma sukuluyi sinawaphunzitse mu zimenezi
koma mu kukhala okhulupirira ochitachita kaya akugwira kumsika kapena ndinu otumikira
nthawi yonse.
Malo ochitira maphunziro sanatenge malo a mpingo. Okhulupirira amapitilira kusonkhana mu
sunagoge, amene anali malo amodzi osonkhanira a mpingo woyamba. Okhulupirira ayenera
kupitilira kusonkhana mmipingo ya kumadera ndi kunyumba kwawo. Sukulu ya Aefeso inali
Page 157
157
mbali yopitiliza ntchito ya mpingo. Sukuluyi sinatenge malo a utumiki wa mpingo, koma
kukulisa. Cholinga cha maphunzirowa si kuchotsa malo ena ophunzitsira bwino ayi pofalisa
uthenga.
Ndi cha nzeru kulemba cholinga cha sukuluyi. Izi zimatchedwa “Mawu a Cholinga.”
Zimakuthandizirani kukhala owona ku cholinga cha malo ochitira maphunzirowa. Harvestime
International Institute ali ndi phunziro lotchedwa “Dongosolo la Zolinga” limene lingathe
kukuthandizani kulemba mawu a cholinga.
3. KHALANI NDI DONGOSOLO LA NDALAMA
Ili ndi dongosolo loyerekeza mitengo ya katundu amene mudzafune. Znthu zimene mugwiritse
ntchito pa skuluyi, mmene mulengezere kwa anthu, ndi ndondomeko ya maphunziro anu. Izi
zimafuna ndalama imene mudzagwiritse ntchito. Ngati muli ndi ndalama yoyambisira sukulu,
mukuyenera kupanga dongosolo la ndalamazi. Pamenepa mukuyenera kulemba mitengo ya
zinthu imene mwakonza.
Ngati ndalama mulibe yoyambitsira sukulu, pempherani kuti Mulungu akupatseni ndalama.
Ngati gulu la mpingo ndi limene likufuna kuyambitsa malowa, mwina mpingo uliwonse utha
kupereka zimene angathe, komanso ophunzira atha kupereka imene angathe. Kusowa kwa
ndalama kusakupangiseni kusayambitsa sukuluyi. Gwiritsani ntchito maphunziro a Harvestime
International Institute ndipo yambani sukulu kunyumba kapena malo amene simupereka
ndalama. Aphunzitsi kapena othandizira akhoza kudzipereka kuphunzitsa ophunzira.
4. SANKHANI MALO
Mzinda wa ku Aefeso umene Paulo anasankha kuti ukhale malo ochitirapo maphunziro unali
wotanganidwa ndi malonda. Unali malo okopa alendo ndi likulu la zamatsenga ndi mafano a
Mulungu wa mkazi wotchedwa Diyana. Zinthu izi zinapangitsa kuti anthu ambiri azikakhala
kumeneko. Kufikira anthu a ku Aefeso ndi uthenga unali mwayi wawo wa maphunziro. Osati
chifukwa uthenga ukanalalikidwa kwa anthu ambiyi ayi, koma kunali mwayi wofikira anthu
zikwi amene amabwera kumeneko ngati alendo ndi amalonda amene amabwerera kwawo atamva
uthenga. Ngati ophunzira amatha kuphunzira mmene amachitira za matsenga ndi ziwanda ndiye
kuti akhoza kutumikira madera ena ndi mphamvu yaoipa ya Satana. Paulo sanawachotse
ophunzirawa mu nyengo zawo ndi cholinga choti alandire maphunziro. Anawaphunzitsa mu
nyengo imene inali yodziwika kwa iwo. Anakhalabe ku malo awo ndi mu chiyankhulo chawo.
Paulo anasankha malo oyenera a sukulu ya maphunziro. Mufunseni Mulungu akutsogolereni
pamene mukufuna malo ochitirapo maphunziro.
Pamene mukuganiza za malo, dzifunseni mafunsowa:
Koyamba: Kodi malowa anthu amafikapo kuti angalandire maphunziro?
Anthu akuyenera kutha kuzapedza maphunziro. Ngati mulu kumudzi sukuluyo ikhale malo oti
anthu atha kuyenda. Kaya ndi mu mzinda anthu ayende kappa pa galimoto. Kaya ndi malo a
zochitika, anthu ambiri athe kufikapo.
Page 158
158
Kachiwiri: Kodi malowo ali kwabwino?
Kwa Aefeso kunali malo abwino ochitira malonda. Ngati mkotheka malowo akhale kotero
amene anthu pachikhalidwe amatha kubwerako kudzapanga zinhtu zina. Makamaka kumene kuli
chiwerengero cha anthu ambiri. Musaope kaya malowo kuli malinga a Satana, pakuti izi
zidzathandiza ophunzira kuona zimene akuphunzira.
Kachitatu: Kodi ndi zipangizo zanji zimene mugwiritse ntchito?
Sizofunika kumanga malo a maphunziro a chilendo, Paulo anagwiritsa ntchito zipangizo zimene
zinalipo kale. Mungayambitse sukuluyi mmasukulu, mumpingo, ndi malo a zochitika. Ngati
mkotheka malo akhale opanda mbali. Malo amene si ampingo ayi pofuna kupereka mwayi kwa
anthu onse. Abusa ena amaopa kuti anthu awo apita ku mipingo ina. Mipingo ina simalola anthu
awo kupita ku mipingo ina. Maganizowa si abwino, ngakhale alipo.
5. SANKHANI DONGOSOLO LA MAPHUNZIRO OYENERA:
Dongosolo la maphunzira ndi maphunziro amene mwakonza kuti aziphunzitsidwa. Onentsetsani
kuti maphunzirowo akhale amene akwaniritsa cholinga chophunzitsa ndi kukonzekeretsa
atumuki. Mwachitsanzo phunziro la mmene mungamvere kulankhula kwa Mulungu ndi lofunika
pokwaniritsa cholinga cha sukulu kusiyana ndi phunziro la mbiri ya mpingo wanu.
Maphunzirowa aziika chidwi pa zimene Yesu anaphunzitsa kwa anthu wamba amene
anasanduka pohunzira oflaitsa uthenga wabwino. Ndipo akhale ochkera Mbaibulo. Maphunziro
amenewa akupezeka kudzera kwa Harvestime International Institute. Posasankha maphunzirowa
muonenso mpahunziro a anthu amene mukufuna kuwaphunzitsa. Kodi amatha kulemba ndi
kuwerenga? Nanga amalankhula chiyankhulo chanji, kulemba ndi kuwerenga? Kodi muzafuna
owamasulira ziyankhulo kapena ayi?
6. SANKHANI APHUNZITSI NDI OGWIRA NTCHITO ZINA
Mfuseni Mulungu akutsogoleleni posankha aphunzitsi. Onetsetsani kuti mukugwirizana ndi
cholinga cha sukuluyo ndi maphunziro amene mukuphunzitsa. Maphunziro a aphunzitsi ndi
ofunika kuwaonanso. Akhale okhoza kuphunzitsa ophunzira molingana ndi maphunziro awo.
Koma koposa zonse moyo wawo wa uzimu ndi mphatso zawo ndizofunikanso. Sankhani
okhulupirira amene ali ndi mphatso yophunzitsa.
Kupatula aphunzitsi sankhani ogwira ntchito ena amene azikonza malo ophunzirira. Amene
akuyenera kumalankhula zambiri za sukuluyo ndi ena.
7. LENGEZETSANI SUKULUYO
Anthu sangabwere kusukuluko ngati sanamvepo zoti ilipo. Mukuyenera kulengeza uthenga wa
sukuluyo ku mudzi, mzinda ndi kumene mufuna kutumikira. Mmene mungalengezere zitengera
ndala zimene muli nazo ndi malo. Ngati ndi mudzi wochepa ndiye kuti mokhoza
Page 159
159
kumangoyendera, momwemonso ku mpingo. Kaya mukhoza kulankhulana ndi abusa anzanu
zokhuza sukuluyo. Mu mzinda uthenga umavuta kufalisa chifukwa cha chiwerengero
chochuluka. Izi ndi zina mwa njira zimene mungasate kufalisa uthenga wa sukuluyo.
Kuyenda mmipingo. Pezani mipingo imene ili mdera lanu poimba mafoni kwa abusa kenako
awuzeni za masomphenya anu. Apempheni kuti awuze mpingo wonse za masomphenya anuwo
mu mwambo wa mapemphero.
Nkhani za mu mpingo: Ngati mpingo wanu umalengezetsa nkhani kwa mamembala anu,
konzekerani kukalengezetsako za sukuluyi.
Nkhani zoulutsidwa: Konzekeraninso kukasiya uthenga wa sukulu yaniyi ku nyumba imene
amalembako ndi kufalitsa nkhani.
Mauthenga ofalitsidwa: Mukhozanso kuika uthengawu mutaulemba bwino mmasukulu,
mmitengo komanso malo amene aanthu amapezekako ambiri. Pemphani chilolezo kwa
akuluakulu mmalowa.
Zochitika za akhristu: Ngati pali mwambo waukulu, umene waitana anthu ambiri a
mumpingowo, pemphani atsogoleri kuti alengezetse za sukulu yanuyo ku mwambo wa
zochitikazo.
Njira zina ndi monga kupereka makalata kwa anthu, kupezeka ku malo amene atsogoleri
amakhalako. Komanso tumizani mauthenga ku mipingo yosiyanasiyana kwa abusa. Kuonjezera
apo, gwiritsani ncthito mabungwe a chikhristu amene ali mdera lanu. Pamphani atsogoleri kuti
akupatseni mwayi wolengezetsa uthanga kwa anthu awo mu mikumano yawo.
8. CHITANI MKUMANO WOYAMBA:
Kukumana koyamba mkalasi ndi kofunika kwambiri. Kukuyenera kukhala kwa abusa ndi
okhulupirira onse opezeka mderalo. Zimene mungachite ndi monga:
a. Kuwalandira aphunzitsi ndi ogwira ntchito ena.
b. Kufotokoza cholinga cha sukulu ya maphunziro.
c. Kufotokozapo za dongosolo la maphunziro ake.
d. Kupemphera, kulambira ndi kuyimba.
e. Kuyesera kuphunzitsa ngati chitsanzo
f. Pemphero lotsekera zonse.
g. Kulembetsa kwa iwo amene awonetsa chidwi choyamba. Izi zichitike kumapeto koma
musanaseke. Ophunzira akumane ndi aphunzitsi awo ndi kutenga dongosolo la
maphunziro awo. Izi ziwalimbikitsa kulembetsa ndi kumaliza maphunziro awo.
9. MAPHUNZIRO OPITILIRA
Izi ndi zina zimene mungamachite pamene sukulu yayambika: kukonzekera, kusunga nthawi,
kupemphera, kubwereza zomwe mwaphunzitsa, kugwiritsa ntchito njira zophunzitsira
Page 160
160
zosiyanasiyana, lolerani kuyenda kwa Mzimu Woyera ndipo tsogolerani ophunzira kuti ayambe
kugwiritsa ntchito zimene aphunzira. Komanso apatseni ophunzira ntchito yokachita kwawo pa
zimene aphunzira
Kumbukirani: cholinga cha sukuluyi ndi kukonzekeretsa ophunzira kupita kulikonse ndi uthenga
wabwino.
Page 161
161
MAYESO ODZIYETSA NOKHA
1. Lembani Vesi Yotsogolera kuchokea pamtima
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
__________________________________________________________________________
2. Kodi ndi njira ziti zimene Paulo anagwiritsa ntchito kukphunzitsa okhulupirira a ku
Aefeso?
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
3. Fotokozani za malo ochitirapo maphunziro a ku Aefeso.
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
__________________________________________________________________________
4. Kodi cholinga cha kukhala ndi malo ochitira maphunziro ndi chiyani?
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
5. Perekani chidule cha malangizo amene aperekedwa pofuna kutsekula sukulu ya
maphunziro.
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
___________________________________________________________________________
(Mayankho a mafunsowa akupezeka kumapeto kwenikweni kwa bukuli)
Page 162
162
KUPITILIZA KUPHUNZIRA
1. Eliya anali ndi sukulu ya aneneri mu Chipangano Chatsopano ndipo anali otsogolera
(onani II Mafumu 2:4). Poganizira utumiki wa aneneri, kodi ndi maphunziro anji amene
akuyenera kukhala nawo?
2. Harvestime International Institute imapereka maphunziro amene akhoza kugwiritsidwa
ntchito ku sukulu yamaphunziro potenga maphunziro akewa. Sukuluyi ili ndi pulogalamu
yoyendayenda ya akhristu komanso iwo amene ali ndi njala yotumikira Mulungu.
Maphunzirowa amakamba za zimene Yesu anaphunzitsa ndi kusintha anthu wamba
kukhala okhulupirika potengera uthenga kudziko lapansi ndi kuonetsera mphamvu yake.
Maphunziro ake agawidwa mmagawo monga chiyambi cha maphunziro ndi mabuku
asanu ndi limodzi a maphunziro.
Page 163
163
MAYANKHO A MAFUNSO ODZIYETSA NOKHA
CHAPUTALA CHA 1:
1. Ndipo Yesu ananena nao, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a
anthu (Marko 1:17).
2. Lamulo loyamba ndi lomaliza la Yesu kwa ophunzira ake linali lowapanga kuti
achulukane. Onani Marko 1:17 ndi Machitidwe 1:8.
3. Kuchulukana ndi kukhala ambiri mu chiwerengero poberekana. Kuchulukana ndi njira
yochulukitsa. Pamene chinthu chikuchulukana chimachuluka nthawi ndi nthawi.
4. Kuchulukana ku uzimu kumachitikanso ku uzimu. Wokhulupirira amagawana uthenga
wabwibo ndi anthu ena, ndi kuwatsogolera kukhala okhazikika mwa Yesu.
5. Njira ndi ndongosolo lokwaniritsa cholinga chathu.
6. Ndondomeko ndi dongosolo la njira zimene zaikidwa pamodzi pofuna kufikira cholinga.
7. Ndondomeko za njira zochulukana mu uzimu ndi dongosolo la njira limene limapangitsa
okhulupirira kufikira cholinga chawo chochulukana ku uzimu.
8. Fananitsani chidule chanu ndi zimene mwaphunzira mu chaputala choyamba.
CHAPUTALA CHA 2:
1. Pakuti wapeputsa tsiku la tinthu tating'ono ndani? (Zakariya 4:10).
2. Fanizirani chidule chanu ndi zomwe mwaphunzira mu chaputala cha 2.
3. Kukula mmadera, mu chikhalidwe, mu chiwerengero ndi mu uzimu.
4. Ena mwa mavesi awa akhoza kugwiritsidwa ntchito: Numeri 1:1-3; 2:23-24; 26:1-4;
Mateyu 9:13; Luka 15:7; 19:10 Machitidwe 1:15; 2:41; 4:4; 6:7; 9:32; 12:24; 16:5; 19:20;
28:30-31; Yohane 3:16; II Petro 3:9
5. Fanizirani chidule chanu ndi zimene mwaphunzira mu chaputala cha 2.
6. a. Zonama b. Zonama
CHAPUTALA CHA 3:
Page 164
164
1. Ndipo ndi mafanizo otere ambiri analankhula nao mau, monga anakhoza kumva (Marko
4:33)
2. Fanizo ndi nkhani imene imachokera mu zochitika za anthu koma imakhala ndi tanthauzo
la kumwamba kapena la uzimu.
3. Kumvetsetsa choonadi cha uzimu chimene chimaphunzitsidwa mmapemphero
kunapatsidwa kwa ophunzira chifukwa anapatsidwa maganizo a uzimu. Iwo amene
analibe uzimu amalephera kumvetsa.
4. Onani zimene zili mu mafanizo mu chaputala cha 3.
CHAPUTALA CHA 4:
1. Ndipo zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zomwezi uikize kwa anthu
okhulupirika, amene adzadziwa kuphunzitsa enanso (II Timoteo 2:2)
2. Kuchitira umboni ndi kuwauza anthu zimene wazimva, ndi kukumana nazo. Mu nyumba
ya malamulo, mboni ndiye amene amanena za munthu kapena chinthu. Monga mboni,
timanena za Yesu ndi dongosolo la chipulumutso kwa anthu onse.
3. Atumiki amene sanasankhidwe ndi amene amapezeka mu mpingo wa Mulungu. Kapena
kuti ndi anthu onse a Mulungu. Ena amatchedwa otumikira koma osati nthawi zonse mu
mpingo.
4. Mawu oti “akulu a mpingo” ndi atumiki amene anasankhidwa kutumikira mumpingo.
Iwo amene utumiki umakhala gawo la moyo wawo amene amakhala olembedwa ndi
mpingo.
5. Maitanidwe a anthu amene satumikira nthawi yonse ndi a kwa okhulupirira onse amene
ndi “ansembe” kapena atumiki a uthenga wabwino.
6. Dongosolo la Mulungu likupezeka pa Machitidwe 1:8. Mzimu Woyera ndiye mphamvu
ypoangitsa kuchulukana, Yesu ndiye uthenga wopita kudziko lonse. Okhulupirira ndiwo
zotengera za uthengawu.
7. Andreya ndi Hananiya.
8. Yambani kugawana uthenga wabwino ndi achibale, anzanu ndi ogwira ntchito limodzi.
Uthenga umafala mwachangu kwa magulu amenewa.
CHAPUTALA CHA 5:
Page 165
165
1. Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili
ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzaulaka uwo (Mateyu
16:18-19).
2. Okhulupirira onse mwa Yesu abadwanso kachiwiri mu ufumu wa Mulungu.
3. Mpingo unabadwa mwa Mzimu Woyera pa tsiku la Pentekosite. Onani Machitidwe 4.
4. Fanizirani mayankho anu ndi zitsanzo za mu chaputala cha 5.
5. Kulambira, kutumikira, chiyanjano ndi utumwi.
6. Onani zokambirana za mu chaputala cha 5.
7. Onani zokhambira za mu chaputala cha 5.
CHAPUTALA CHA 6:
1. Pakuti kunamkomera Atate kuti mwa iye cidzalo conse cikhalire (Akolose 1:19).
2. Kukula mkati ndi kukula mu uzimu ndi kuumbika kwa mamembala a mpingo. Uku ndi
kukula kwa makhalidwe abwino osati kukula mu chiwerengero.
3. Kukula mu uzimu ndi kuchuluka kwa uzimu kumene kumabwera chifukwa chakukula
kwa moyo wa uzimu mmoyo wa okhulupirira.
4. Onani zokambirana za mu chaputala cha 6.
5. Onani zokambirana za mu chaputala cha 6.
6. Onani zokhambirana za mu chaputala cha 6.
CHAPUTALA CHA 7:
1. Ndipo mau a Mulungu anakula; ndipo ciwerengero ca akuphunzira cidacurukatu ku
Yerusalemu (Machitidwe 6:7).
2. Kukula mu chiwerengero ndi pamene okhulupirira apezera okhulupirira nzake kwa Yesu
ndi kuwabweretsa chiyanjano pa mpingo wawo. Zotsatira zake zimakhala kukula mu
chiwerengero cha mpingo.
3. Fanizirani ndi chidule chanu pa zokambirana za mu chaputala cha 7.
Page 166
166
4. Fanizirani ndi mayankho anu pa zokambirana za mu chaputala cha 7.
CHAPUTALA CHA 8:
1. Kotero Mipingoyo inalimbikitsidwa m'cikhulupiriro, nacuruka m'ciwerengo cao tsiku ndi
tsiku (Machitidwe 16:5).
2. Kukula mmadera kumachitika pamene mpingo uyambitsa mpingo wina mu zikhalidwe
zofanana. Mpingo watsopanowo ndi nthambi ina ya “likulu” la mpingo monga mmene
zimzkhalira mdziko kholo ndi mwana.
3. Kudzala mpingo ndi kukula ndi kulumikiza kwa mpingo. Mmodzi amadzala mpingo
watsopano monga mlimi wodzala mbeu. Mbue zimabereka mtengo watsopano wofanana
ndi kholo la mbeu ija.
4. Anthu a ku mpingo wa ku Yerusalemu anabalalikana chifukwa cha chizunzo. Anapita
mmalo osiyanasiyana kulalikira uthenga ndipo anthu amatembenuka mtima.
5. Izi ndi njira zokulitsira mpingo:
-mpingo kudzala mpingo wina
-mipingo kugwirizana kudzala mpingo
-mpingo waukulu kugawana mkupanga mipingo iwiri kapena yoposera apo.
-munthu wokhulupirira kupita kumalo ena kukayambitsa mpingo.
6. Pali mitundu ingapo ya kukula mmadera kwa mipingo:
-mipingo kukatumikira ku madera ena
-mipingo kukatumikira kumadera a mitundu ina
-mipingo ya cholinga chapadera.
7. Zofunikira za Mbaibulo ndi kudzala mipingo mmalo osafikilidwa, malo osalandilika,
mmizinda keneko mmidzi.
8. Uthenga umene umabadwitsa mipingo ndi wochokera Mbaibulo, wokamba za Khristu,
wofikira chosowa.
CHAPUTALA CHA 9:
1. …Kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kucokera kumdima, kulinga kukuunika,
ndi kucokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo cikhululukiro
ca macimo, ndi colowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi cikhulupiriro ca mwa Ine
(Machitdwe 26:18).
2. Kukula kolumikiza ndi pamene mpingo ukula polalikira ku madera ena, a zilankhulo
zina, mitundu ya anthu ena amene ndi osiyana zikhalidwe.
Page 167
167
3. Machitidwe 1:8. Uthenga wabwino umayenera kupita kutali kuchokera ku Yerusalemu
kufika ku “malekedzero a dziko” lapansi.
4. Mtumwi Paulo.
5. Fanizirani chidule chanu ndi zomwe zili mu chaputala cha 9.
CHAPUTALA CHA 10:
1. Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ace, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga,
adzikane yekha, natenge mtanda wace, nanditsate Ine (Mateyu 16:24).
2. Mawu oti “kutembenuka” amakamba za wokhulupirira watsopano mwa Yesu amene
wabadwa mwatsopano mwa chikhulupiriro mkukhala gawo la ufumu wa Mulungu.
3. Mawu oti “wophunzira” ndi munthu amene watembenuka mtima mkukhazikika pa
maziko a chikhristu ndipo amakhala wokonzeka kupanga ophunzira ena. Wophunzira ali
ngati mwana wa sukulu amene amaphuzira potsatira. Ndi kuposa kukhala ndi mzeru. Ndi
kuphunzira kumene kumasintha makhalidwe a moyo wamunthuyo.
4. Zinthu zofunika pa kukhala wophunzira ndi kuwerengera mtengo wake, kuchita zofunika,
ndi kukhala ndi cholinga chenicheni.
5. Mfundo 9 zofunika pa kukhala wophunzira ndi:
Kusankha malangizo chiyanjano
Chionetsero kudzipatula kutenga nawo mbali
Kuyang’anira kupatsa ena zochita masomphenya
6. Wophuzira ndiye amene:
Amazikaniza yekha amasiya zonse amakhala Mmau
Amatsatira Yesu amakhala womvera amakhala wotumikira
Ufumu umakhala choyamba amabala chipatso amaonetsera chikondi
7. Yesero lenileni la wophunzira ndi zimene zimachitika pamene simukupezeka ndi
ophunzira anu. Kodi amakhalabe okhulupirika ndi kuphunzitsa ena amene ali ndi
kuthekera kopitilira kuchulukana?
CHAPUTALA CHA 11:
1. Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, Kapena wosaimirira m'njira ya
ocimwa, Kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza. Komatu m'cilamulo ca Yehova
muli cikondwerero cace; Ndipo m'cilamulo cace amalingima usana ndi usiku. Ndiye
akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; Wakupatsa cipatso cace pa nyengo yace,
Tsamba lace lomwe losafota; Ndipo zonse azicita apindula nazo (Masalmo 1:1-3).
Page 168
168
2. Pamene kukula kuli kopinimbira kudziko, thupi silimakula moyenera. Pamene kuluka
kwa uzimu kuli kopinimbira, anthu sakula mu uzimu ndipo mpingo sukulanso.
3. Chitsanzo A: Mlongo wolakwiridwa ayenera atsatire malangizo amene ali pa Mateyu
18:15-17
Chitsanzo B: Mpingo ukuyenera kugwiritsa ntchito njira ya “bwerani” osati ya “pitani.”
Pakhoza kukhala ntchito zina zosayenera zimene ziyenera kusadzidwa.
Chitsanzo C: Mpingowo mkutheka sumaphunzitsa anthu atsopano mwa Yesu kuti akhale
ophunzira.
CHAPUTALA CHA 12:
1. Koma pamene ena anaumitsa mtima ndi kusamvera, nanenera zoipa Njirayo pamaso pa
anthu, anawacokera, napatutsa akuphunzira, nafotokozera masiku onse m'sukulu ya
Turano (Machitidwe 19:9-10).
2. Paulo anaphunzitsa zimene anakumana nazo (Machitidwe 19:2-8), poonetsa chitsanzo
(Machitidwe 19:11-12), ndi pochititsa maphunziro (Machitidwe 19:9).
3. Malo ochitira maphunziro a ku Aefeso amapereka maphunziro a zaka ziwiri amene
amaphunzitsa atumiki mu zikhalidwe ndi mmadera pofafalita uthenga wabwino
(Machitidwe 19:10-20).
4. Cholinga cha kukhala ndi malo ochitira maphunziro ndi kuphunzitsa ophunzira ndi
kuwakonzekeretsa ku ntchito ya utumiki.
5. Fanizirani chidule chanu ndi zomwe zili mu chaputala cha 12.