Top Banner
Yambirani apa kuwerenga Yambirani apa kuwerenga Zam'kati Thandodzo kwaowerenga Thandodzo kwaowerenga T N L M he ew ife ission KODI MWABADWADI MWATSOPANO MWA MADZI NDI MWA MZIMU WOYERA?
375

Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

Oct 04, 2014

Download

Documents

C Knox Jarmon
Welcome message from author
This document is posted to help you gain knowledge. Please leave a comment to let me know what you think about it! Share it to your friends and learn new things together.
Transcript
Page 1: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

Yambirani apa kuwerengaYambirani apa kuwerenga

Zam'kati

Thandodzo kwaowerengaThandodzo kwaowerenga

T N L Mhe ew ife ission

KODI MWABADWADI

MWATSOPANO

MWA MADZI NDI

MWA MZIMU WOYERA?

Page 2: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

◄ Zam'kati ►

KODI MWABADWADI MWATSOPANO

MWA MADZI NDI MWA MZIMU

WOYERA?

KODI MWABADWADI MWATSOPANO

MWA MADZI NDI MWA MZIMU

WOYERA?

PAUL C. JONG

Hephzibah Publishing House A Division of THE NEW LIFE MISSION

SEOUL, KOREA

Page 3: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

◄ Zam'kati ►

Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera? Copyright © 2004 by The New Life Mission Gawo lililonse labukuli siliyenera kusindikizidwa kapena kulilemba popanda chilolezo cha mwini wake. Mau a Mulungu amene agwiritsidwa ntchito m’bukuli achokera Mbuku Loyera. ISBN 89-8314-459-9

MAU OTHOKOZA Ife tili kupereka kuthokoza kwathu kwa

Mulungu potipatsa mau achipulumutso ndi potipatsa Uthenga Wabwino wakubadwanso mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu Woyera.

Tikuthokozanso atumiki onse a Mulungu, kuphatikizapo Rev. Samuel Jungsoo Kim ndi Rev. John Kyunghwan Shin amene adagwira ntchito yaikulu posindikiza bukuli; kwa Mrs. Jungpil Sul pomasulira bukuli, kwa abale ndi alongo ku nyumba yosindikizira mabuku ya Hephzi-bah. Tikuti zikomo kwa inu nonse.

Ine ndi kupemphera ndi kukhulupilira kuti bukuli ndi matepi lidzathandiza kuti mitima yambiri ibadwenso mwatsopano, ndipo ndikubwerezanso kuthokoza anthu amene anagwira nafe ntchito kuti buku lisindikizidwe.

Page 4: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

◄ Zam'kati ►

Ine ndikukhulupilira kuti Ambuye Mulungu adzatilora kuti ife tifalitse Uthenga Wabwino wa kubadwanso mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu Woyera kudziko lonse kudzera mwa anthu okhulupilira Yesu.

Ndi chikhulupiliro cha muyaya, ndikuthokoza Mulungu.

PAUL C. JONG

Page 5: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

5 MAU OYAMBIRA:

◄ Zam'kati ►

MAU OYAMBIRA:

TIYENERA KUBADWA MWATSOPANO MWA MADZI NDI MZIMU WOYERA

Pamene Mulungu adalenga kumwamba ndi

dziko lapansi poyamba pa nthaœi, iye adalenganso dziko la muyaya, kumwamba ndi gahena. Ndipo Iye analenganso munthu m’chifaniziro chake. Koma popeza munthu adachimwa pamaso pa Mulungu, munthu adayenera kufa kamodzi kokha: “munthu aliyense adzafa kamodzi kokha ndipo kenaka adzaœeruzidwa” (Ahebri 9:27).

Imfa ya thupi lathu ndi njira yokaloœera kumwamba. Anthu opanda uchimo adzaloœa ku dziko la muyaya mu Ufumu wa Mulungu ndipo adzakhala pa chikondwerero chakuti iwo ndi ana a Mulungu, pamene ochimwa adzaponyedwa

Page 6: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

6 MAU OYAMBIRA:

◄ Zam'kati ►

“M’nyanja ya moto yodzala ndi miyala ya Sulufule yoyaka” (Chivumbulutso 20:10).

Choncho nkoyenera kuti anthu onse abadwenso mwa tsopano. Tiyenera kubadwanso mwatsopano kudzera m’chikhulupiliro chathu, kuomboledwa ndi kukhala olungama. Pakuti ndi njira yokhayo imene tinga kaloœere ku ufumu wa muyaya wa kumwamba. Baibulo limatiuza zimenezi. “Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera sangathe kuloœa mu ufumu wa Mulungu” (Yohane 3:5). Mzimu Woyera ndi njira yokhayo imene ife tinga loœere mu ufumu wa Mulungu.

Nanga ‘madziœa’ ndi ‘Mzimu’ zimene zimatilora ife kubadwanso mwatsopano ndi chiyani? Mau a Mulungu akamanena madzi anena ubatizo wa Yesu.

Nchifukwa chiyani Yesu, amene ndi Mulungu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi? Kodi ndi kuonetsa kudzichepetsa kwake? Kodi kunali kufuna kudzionetsa kuti Iye ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja? Ai. Sichoncho.

Pamene Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi “Mwa njira yosanjika manja” (Levitiko 16:21), “Inali ntchito yolungama ya munthu m” modzi (Aroma 5:18), imene inachotsa machimo aanthu onse.

M’chipangano Chakale, Mulungu anapatsa Aisraele lamulo la chifundo la chiomboli pa Tsiku Lansembe yochotsera machimo onse a Aisraele anali kuperekedwa kudzera mwa wansembe wamkulu Aroni posanjika manja pamutu pa ‘mbuzi wonyamula’ machimo ndi kupereka machimo onse pa mbuziyo.

Awa anali mau a Chivumbulutso amene anali kunenedwa popereka nsembe ya muyaya yochotsera machimo imene inali kubwera kutsogolo. Idaulula choonadi chakuti machimo onse a anthu adzaperekedwa kwa Yesu Khristu kamodzi kokha malinga ndi chifuniro cha Atate. Iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi amene anali wa fuko la Aroni ndiponso woyimira anthu onse.

Page 7: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

7 MAU OYAMBIRA:

◄ Zam'kati ►

Pamene Yesu anali kubatizidwa adauza Yohane kuti, “Tsopano lino vomera chifukwa umu ndi m’mene tiyenera kuchitira zimene Mulungu akufuna” (Mateyu 3:15).

Pamenepa, mau akuti “chifukwa umu” atanthauza kuti mwanjira yosanjika manja, machimo onse anaperekedwa kwa Yesu kuti zimene Mulungu anali kufuna zichitikedi. Mau akuti ‘chilungamo’ ndi ‘dikauzine’ cha chi Giriki ndipo amatanthauza kukhala ‘oyenera’ m’makhalidwe.

Yesu adakwaniritsa chifuniro cha Mulungu m,malo mwa anthu onse kudzera mu ubatizo wakwe molingana ndiponso moyenera.

Chifukwa chakuti anatenga machimo onse aanthu, kudzera mu ubatizo wake, Yohane Mbatizi adachitira umboni, “Suuyu Mwana wa Nkhosa wa Mulungu amene anachotsa machimo adziko lapansi” (Yohane 1:29).

Ndi machimo onse aanthu pa mapewa pake Yesu anapachikidwa pa Mtanda. Ndipo Iye

analandira chiweruzo cha machimo amene Iye anadzitengera kudzera mu ubatizo wake. Iye anafa pa Mtanda ndikunena kuti, “Kwatha” (Yohane 19:30). Iye ananyamula machimo athu onse ndi kulandira chiweruzo chotsiriza.

UBATIZO WA YESU NDI MBALI YA CHIPULUMUTSO

Choncho, popanda kukhulupilira mu ubatizo wa

Yesu, sitingathe kupulumutsidwa. Nchifukwa chake Petro ananena kuti, “Ubatizo wake ufanizira ubatizo umene lero ukukhupulumutsani” (1 Petro 3:21).

Masiku ano, anthu amene amakhulupilira mwa Yesu Khristu, sakhulupiliranso ubatizo wake wa madzi ndi Mzimu Woyera, amangokhulupilira mu imfa yake ya pa Mtanda.

Kodi zimenezi adzapulumutsidwa nazo? Kodi tingapulumutsidwe pakungokhulupilira mu mwazi

Page 8: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

8 MAU OYAMBIRA:

◄ Zam'kati ►

wa Yesu wokha? Kodi mwa wokha ungatipatse chipulumutso?

Ai. Sitingapulumuke pa maso pa Mulungu pakungokhulupilira mu imfa ya Yesu pa Mtanda.

Pamene ana a Aisraele anali kupereka nsembe yao yochotsera machimo Mchipangano Chakale, sichikanakhala chinthu chabwino kupha nsembe ya uchimoyo popanda kusanjika manja pa mutu pa nsembeyo. Kapenanso tinganene kuti Aisraele aja akanapereka nsembeyo popanda kuyamba asanjika manja pamutu pa nsembeyo chikanakhala chintu cholakwika.

Momwemonso sibwino kukhulupilira mu Mtanda wa Yesu popanda kukhulupilira mu ubatizo wake.

Choncho, mtumwi Petro anati, “Ubatizo wake, ufanizira ubatizo umene lero ukukhupulumutsani, kupyolera mu kuuka kwakwe” (1 Petro 3:21).

Chimodzimodzinso anthu amene sanakhulupilire m’madzi oopsa aja (chigumula) munthaœi ya Nowa adaonongeka.

Chikhulupiliro chenicheni chimene chimatitengera ku chipulumutso ndi cha mwa Iye, “Amene anabwera mwa madzi ndi mwadzi Yesu Khristu” (1 Yohane 5:6). Tiyenera kukhulupilira mu zonse, ubatizo ndi Mtanda wa Yesu Khristu.

Choncho mtumwi Yohane ananena kuti kukhala ndi chikukhulupiliro choona ndi kukhulupilira mu, “Umboni wa Mzimu Woyera, madzi ndi mwazi” (1 Yohane 5:8).

Tidzakhala ndi chikhulupiliro choona ngati tikhulupilira zimenezi. “Yesu ndi Mulungu ndipo anabwera mu thupi la munthu mwa Mzimu Woyera kudzera m’thupi la Maria namwali ndipo Iye anachotsa machimo onse adziko lapansi pakubatizidwa mu Mtsinje wa Yorodani ndi Yohane Mbatizi, woyimira anthu onse. Ndipo Yesu ananyamula machimo onsewo.” Choncho Uthenga Wabwino sungakhale wokwanira popanda ‘ubatizo wa Yesu’ ‘madzi,’ kaya tikhulupilire motani, sitingapulumutsidwe popanda ubatizo wa Yesu.

Page 9: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

9 MAU OYAMBIRA:

◄ Zam'kati ►

MBIRI YA MPINGO IMENE NACHOTSA UTHENGA WABWINO M’CHALICHI

Kodi masiku ano zakhala bwanji kuti Uthenga

Wabwino wonena za ubatizo wa Yesu wakhala ngati uthenga wonama, pa Chigiriki ‘pseudo-gospel’ ndipo uli kufalitsidwa molakwa padziko lonse?

Yesu atauka kwakufa ndikukwera kumwamba, atumwi anali kulalika ‘Uthenga wonena za madzi ndi mwazi’ Ngati tiœerenga bwino Chipangano Chatsopano, tikhoza kuona kuti si olemba Baibulo okha, komanso atumwi onse ndi ogwira ntchito Mu mpingo woyamba wachikhristu, kuphatikizapo atumwi aœa: Paulo, Petro ndi Yohane analalika momveka bwino ‘Uthenga Wabwino wa madzi ndi mwazi wa Yesu.’

Pakadali pano, Satana wakhala ali kuyetsetsa kuchokera pachiyambi kuthetsa ndi kuchotsa

Uthenga umenewu wa mpingo. Kuchokera pa nthaœi ya msonkhano wa ku Milani wa m’chaka cha 313 A.D., mpingo wa chikhristu unagwidwa mu m’sampha wa Satana. Mphamvu za ndale za Boma la Aroma, posinthana ndi maganizo akuti chikhristu ndiwo uli ndi chipembedzo chovomerezeka, zinakhala zokhazikika.

Ndipo pamane lamulo lakuti ‘munthu akayamba mpingo abatizidwe linakhazikitsidwa,’ Boma la Aroma linali kuyanjanitsa anthu ogaœikana m’maboma onse amene anali pansi pa ulamuliro wawo.

Pambuyo pake anthu anayamba kuloœeza pamtima chikhulupiliro chatumwi kuti chikhale ngati maziko a maphunziro a chikhristu. Chifukwa chaichi, Uthenga Wabwino mogwirizana kwatunthu ndi Mau a Mulungu ‘Uthenga wonena za madzi ndi Mzimu Woyera’ – zimene zimatipatsa “Mphamvu za Mzimu Woyera, ndiponso mosakaika konse” (1 Atesalonika 1:5) – udasoœanso. Monga momwe Satana anakonzera,

Page 10: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

10 MAU OYAMBIRA:

◄ Zam'kati ►

uthenga wonama osalola munthu aliyense kubadwa mwatsopano unapita patsogolo pa dziko lonse.

Kwa zaka chikwi chimodzi (1000) utatha msonkhano waku Milani, kunafika nthaœi yoipitsitsa mu mpingo wa chikhristu ku maiko onse a azungu.

Ngakhale kuti magulu ofuna kukonzanso mpingo wachikhristu anayambidwa m’maiko ambiri, kupempha anthu kuti abwererenso ku ‘Mau, Chisomo ndi chikhulupiliro,’ palibe mmodzi wa iwo amene adapeza uthenga woona, uthenga wonena za madzi ndi Mzimu Woyera.’

Uthenga woonawu wakhala uli kusungidwa m’manja mwa anthu ochepa amene anatsatira mauœa kuyambira pa nthaœi ya atumwi. Ndipo monga dziœe limene labisika pansi pa nthaka ndikukaonekeranso tsidya lina, Uthenga Wabwino udaonekeranso M’masiku Otsiliza kuti ulalikidwe padziko lapansi.

ILI NDI BUKU LOYAMBA PADZIKO LINO LIMENE LIKULALIKA ZA UBATIZO WA YESU MONGA ZALEMBEDWA MU BAIBULO

Ili ndi buku loyamba munthaœi yathu ino

limene likulalika Uthenga Wabwino wa ubatizo ndi mwadzi wa Yesu monga zalembedwa m’Mau a Mulungu; Uthenga umene umatiuza kuti Iye anachotsa machimo athu onse pamene anafa pa Mtanda. Ndikhulupilira kuti palibenso buku lina limene likulalika ‘Uthenga wonena za madzi ndi mwadzi’ momveka bwino ngati ili.

Munthaœi yathu ino pamene zinthu zikufufuzidwa kudzera pa internet, ndayetsa kupeza anzanga amene akulalika Uthenga Wabwino monga momwe uthenga unalembedwera m’Baibulo, munthu amene amadziœa ndi kulalika mokhulupilika, chinsinsi cha ubatizo wa Yesu. Koma ndalephera kale. Choncho ndaganiza kuti

Page 11: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

11 MAU OYAMBIRA:

◄ Zam'kati ►

nditsindikize ‘bukuli la Uthenga Wabwino m’Chicheœa.’

Pamene madzi osefukira aphimba dziko lonse, madziwo sasiya dera ndiponso sakhala oyenera kumwa. Momwemonso, pali anthu ambiri amene akudzitchula kuti ndi ‘atumiki a Mulungu’ amene amafalitsa uthenga wonama, koma palibe ndi umodzi womwe umene ungatipatse ife moyo weniweni.

TIYENI TIKHALE ANTCHITO A MULUNGU, WOKONZATSO UBALE WATHU NDI MULUNGU

Tikukhala mu m’badwo moyandikina ndi kutha

kwa dziko. Iyi ndi nthaœi yimene machimo aanthu amakula, ndipo tiyitane chiweruzo cholungama cha Mulungu. Asayasi aulula kuti amaphatikiza

nzeru za m’mene anthu amabadwira ndi Mau a Mulungu.

Tikumanganso nsanja yina ya Baibulo matsiku ano matsiku otsiriza pamene anthu anayetsa izi, Mulungu anaœabalalitsa padziko lonse la kudzera mukusokoneza zilankhulo zao. Tsono, popanda chisomo cha Mulungu, mabvuto akulu okumana asanu ndi aœiri ndi chiweruzo chosatha chinafika pa anthu amene sanabadwetso kachiœiri.

Choncho ndikupemphera ndi kukupemphani kuti muœerenge buku ili ndidekha. Ndi ku pemphera kuti mwina, ‘mungabadwenso kachiœiri ndi madzi ndi Mzimu.’ Buku ili likulalika Uthenga Wabwino monga momwe udalembedwera mu Baibulo. Choncho Uthenga uwu ndi uwu. “Ngati m’mvera mau anga nthaœi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. Mudzadziœa zoona zenizeni, ndipo zoonazo zidzakusandutsani aufulu” (Yohane 8:31-32). Yetsani kudziœa mau achoona kudera mu buku ili kuti mumasuke ku machimo

Page 12: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

12 MAU OYAMBIRA:

◄ Zam'kati ►

ndi imfa. Kuti mupulumutsidwe ndi kupeza moyo wosatha mwa iye.

Tiyeni tigwire ntchito ya Atate pamodzi kuti tipulumutse mizimu ya anthu kudzera mukulalika ‘Uthenga Wabwino wa madzi ndi magazi.’ Ndikhulupilira moonadi kuti Uthenga woona uzawala ndi kutipatsa mphamvu kuti tigwire ntchito mozipereka kumanganso maziko muchikhulupiliro ndi mau achoona.

“Anthu anu adzamanganso nyumba zimene zakhala mabwinja nthaœi yaitali. Adzamanganso pa maziko akalekale. Apo mudzatchedwa anthu okonza makoma, omanganso nyumba zamabwinja, kuti anthu azikhalamo.” (Yesaya 58:12).

Ambiri ainu salikuziœabe za Uthenga Wabwino wobadwanso kachiœiri ndi madzi ndi Mzimu. Ndi chifukwa chake ndikutsindikiza za Uthenga Wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi Mtanda wake ukanakhala wopanda ntchito kwa ife tonse.

Ichi ndi chifukwa chake ndikutsindikiza za ubatizo wakwe kaœirikaœiri.

Ndikufuna kuti inu m’mvetse mpaka nonse mudalitsidwe ndi Uthenga Wabwino wa madzi (ubatizo wa Yesu) ndi Mzimu, ndifuna kubwerezanso chifukwa cha inu.

Ndikulakalaka kuti inu nonse mukhulupilire Uthenga Wabwino wa ubatizo ndi magazi ake kuti mupulumutsidwe ku uchimo. Ndipo ndikukhulupilira kuti maulaliki aœa akusandutseni kubadwatso kachiœiri.

Page 13: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

◄ Cover Page ►

ZAM’KATIMU

Chigawo choyamba – Maulaliki 1. Poyamba tiyenera kudziœa machimo

athu kuti tipulumutsidwe (Marko 7:8-9, 20-23) ------------------------ 15

2. Anthu amabadwa ali ochimwa

(Marko 7:20-23) ----------------------------- 32 3. Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo,

kodi tingapulumuke? (Luka 10:25-30) ----------------------------- 44

4. Chiombolo cha muyaya

(Yohane 8:1-12) ---------------------------- 65

5. Ubatizo wa Yesu ndi nsembe

yochotsera machimo (Mateo 3:13-17) ----------------------------- 97

6. Yesu anabwera mwa Madzi,

mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera (1 Yohane 5:1-12) ----- 149

7. Ubatizo wa Yesu ndi Chifanizo cha

Chipulumutso cha Ochimwa (1 Petro 3:20-22) --------------------------- 187

8. Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe

yochotsera machimo (Yohane 13:1-17) -------------------------- 206

Page 14: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

◄ Cover Page ►

Chigawo chachiœiri – Mau owonjezera 1. Maumboni achipulumutso ---------------- 278 2. Kulongosola kowonjezerapo ------------- 299 3. Funso & Yankho -------------------------- 333

Page 15: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

◄ Zam'kati ►

ULALIKI OYAMBA

Poyamba tiyenera kudziœa machimo

athu kuti tipulumutsidwe

Page 16: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

16 Poyamba tiyenera kudziœa machimo athu kuti tipulumutsidwe

◄ Zam'kati ►

Poyamba tiyenera kudziœa machimo athu

kuti tipulumutsidwe < Marko 7:8-9 >

“‘Chifukwa mwaika pambali malamulo a Mulungu, ndikusunga miyambo ya anthu monga – kusuka makapu ndi zinthu zina.’ Ananena kwaiwo, ‘Pazonsezi m’kukana malamulo a Mulungu, kuti m’sunge miyambo yanu’”

< Marko 7:20-23 >

“Ndipo anati, zimene zimatuluka mwa munthu ndizo zimamuipitsa chifukwa m’kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa za chiwerewere, za kuba, zakuphana, zigololo, masiriro, kuipa m’tima,

kunyenga, zonyansa, kaduka, kunyoza, kudzikuza, ndiponso kupusa. Zoipa zonsezi zimachokera m’kati mwa munthu, ndipo ndizo zimamuipitsa.”

Poyamba, ndikufuna kufotokoza tanthauzo la tchimo. Pali machimo amene afotokozedwa ndi Mulungu ndi machimo amene afotokozedwa ndi munthu. Mau oti tchimo, mu chiGiriki, atanthauza kulumpha malire. Kutanthauza kusakhoza. Ndi chimo ngati sitisatira malamulo a Mulungu molondola. Poyamba tiyeni tiyang’ane pa machimo ofotokozedwa ndi munthu.

Tchimo ndi chiyani?

Tchimo ndikusasunga malangizo a Mulungu

Page 17: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

17 Poyamba tiyenera kudziœa machimo athu kuti tipulumutsidwe

◄ Zam'kati ►

Timayesa machimo athu mu chikumbumtima munjira yina, sikulakwira malamulo a Mulungu, koma ndikuweruza molingana ndizimene munthu achita mumtima mwakwe.

Ndikuweruzidwa kwa payekha payekha. Choncho, ntchito yimodzi yimayesedwa tchimo malinga ndi m’mene munthu akuchitira. Ndichifukwa chake Mulungu anatipatsa ndime zokwanira 613 za malamulo ngati mu yeso wa chiweruzo chake.

Chithunzi ichi chikuonesta tchimo la munthu.

Malamulo a Mulungu

Chikumbumtima cha munthu Kuzisunga, myambo ya bwino

Malamulo adziko, makhalidwe

Choncho, tisayike muyeso pa chikumbum’tima chathu.

Tchimo la chikumbumtima chathu silifanana ndi zimene Mulungu akuti ndi tchimo. Choncho sitiyenera kumvera chikumbumtima chathu, koma tiyike ntchito zathu pa malamulo a Mulungu.

Aliyense wa ife ali ndi maganizo ake oti kodi tchimo ndi chiyani. Ena akuganiza kuti ndikulephera kwathu, ndipo ena akuganiza kuti maganizo athu. Poyamba tiyenera kudziœa machimo athu kuti tipulumutsidwe.

Mwa chitsanzo, ku Korea anthu aku phimba manda amakolo awo ndi udzu akuganiza kuti ndi ntchito yawo kudula udzu ndi kusamala mandawo mpaka iwo amwalire. Koma monga mwa umbuli wa mtundu wa Papua New Guinea, amalemekeza mitembo yamakolo awo pogaœana mumbanja awo ndi kudya (sindikutsimikiza kuti amaphika kapena ayi asanadye.) Chikuwonetsa kuteteza mtembo kuti usadyedwe nditizolombo. Miyambo iyi

Page 18: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

18 Poyamba tiyenera kudziœa machimo athu kuti tipulumutsidwe

◄ Zam'kati ►

yikuonetsa kuti maganizo aanthu pamachimo ndi osiyana.

Izi ndi m’mene ziliri pa zabwino ndi uchimo. Koma Baibulo limatiuza kuti ndikuchimwa kusamvera malamulo ake.

“Chifukwa mwaika pambali malamulo a Mulungu, ndikusunga miyambo ya anthu monga – kusuka makapu ndi zinthu zina. Ananena kwaiwo, ‘Pazonsezi m’kukana malamulo a Mulungu, kuti m’sunge miyambo yanu’”(Marko 7:8-9).

Mulungu sasamala m’mene tikuwonekera kunja. Akuyang’ana m’kati mum’tima yathu.

MULUNGU AKUWONA KUTI MUNTHU ALIYENSE NDIWOCHIMWA PA MASO PAKE

Kodi tchimo lalikulu ndi liti?

Ndikusalabadira mau a Mulungu Ndifuna kukuudza limene ndi tchimo pamaso

pa Mulungu. Ndikulephera kukhala muchifuniro chake sikukhulupilira mau ake. Mulungu akuti ndi tchimo kukhala ngati Afarisi amene akukana malamulo a Mulungu ndi kuika patsogolo ziphunzitso za miyambo yawo. Yesu anaona kuti Afarisi ndi anthu osakhulupilira.

Kodi mumakhulupilira mwa Mulungu uti? Kodi ndizoona mumandilemekezadi? Mumadzitukumula ndi dzina langa koma ndizoona

Page 19: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

19 Poyamba tiyenera kudziœa machimo athu kuti tipulumutsidwe

◄ Zam'kati ►

mumandilemekezadi? Anthu amayang’ ana kunja ndi kusalabadira mau ake uwu ndu uchimo pa maso pake. Tchimo loopya ndi kusalabadira mau ake. Kodi mukudziœa izi? Ili ndi tchimo la machimo onse.

Kulephera ndi vuto lathu la machimo. Kulakwa kumene tichita ndi machimo amene tichita sichifukwa cha machimo koma ndi vuto lathu. Mulungu amasiyanitsa machimo ndi kulephera kwathu. Amene salabadira mau ake ndi ochimwa ngakhale alibe mavuto. Ndi ochimwa kwambiri pa maso pa Mulungu. Ichi ndi chifukwa chake Yesu anawadzudzula Afarisi.

Mumabuku asanu a Mose kuchokera ku Genesisi mpaka Deuteronomo muli malamulo amene akutiuza zoti tichite ndi zimene sitiyenera kuchita. Awa ndi Mau a Mulungu, ndi malamulo ake. Sitingakwanitse kusunga onse mwangwiro (100%), kapena poyamba tiyenera kudziœa machimo athu kuti tipulumutsidwe.

“Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.” Tsono Mulungu adati, “Kuyere, ndipo kudayeradi.” Analenga zinthu zonse ndipo anakhadzikitsa malamulo.

“Wochedwa mau uja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu, iye ndi mau” (Yohane 1:1, 14) Kodi Mulungu amadzionetsa bwanji kwa ife? Iye amadzionetsa kwa ife kudzera mu malamulo ake. Mulungu ndi mau ndipo amadzionetsera mu malamulo. Mulungu ndi Mzimu. Kodi Baibulo timalitcha chiyani? Timalitcha kuti ndi Mau a Mulungu.

Kunalembedwa kuti, “Kuika malamulo a Mulungu pambali, ndi kusunga myambo ya anthu.” Kuli ndime zokwanira 613 mu malamulo ake. Chitani ichi koma musachite icho, lemekezani makolo anu… ndi zina zotere. Mubuku la Levitiko akuti akazi ndi amuna achitepo kanthu ngati choœeta chagwera mu dzenje. Pali ndime zokwana 613, zili mumalamulo ake.

Page 20: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

20 Poyamba tiyenera kudziœa machimo athu kuti tipulumutsidwe

◄ Zam'kati ►

Koma chifukwa simau a munthu, tiyenera kuganizira za zimenezi kaœiri-kaœiri. Tiyenera kumvera Mulungu ngakhale sitingasunge malamulo onse a Mulungu, koma tiyenera kuœadziœa.

Kodi pali mau a Mulungu amene ndi olakwika? Afarisi anayika pambali malamulo a Mulungu. Anasunga miyambi ya anthu mumalo mwa malamulo ake. Mau aakulu awo anawalemekeza kwambiri kusiyana ndi Mau a Mulungu. Zinali choncho pamene Yesu anabadwa. Yesu anadana nazo kwambiri pamene anthu sanakhulupilire Mau a Mulungu.

Mulungu anatipatsa ndime zokwana 613 za malamulo kuti tiphunzire zoona zake, ndi Mulungu wathu, kodi machimo athu ndichiyani pamaso pake ndikutionetsa chiyero chake. Choncho chifukwa tonse ndife ochimwa pamaso pake, tiyenera kukhulupira Yesu amene anatumizidwa kwa ife kuchokera kwa Mulungu

chifukwa cha chikondi chake pa ife tiyenera kukhala mwachikhulupiliro.

Amene amaika pambali mau ake, amene sakhulupilira ndi ochimwa. Ndipo amene sangasunge mau ake ndiochimwa, koma ndikuchimwa kwakukhulu kuika pambali mau ake. Ndi amenewo amene adzathera ku gahena. Kusakhulupilira ndi kuchimwa pamaso pa Mulungu.

CHIFUKWA CHIMENE MULUNGU ANATIPATSIRA MALAMULO

Kodi chifukwa nchiyani Mulungu anatipatsa

malamulo? Kuti tidziœe machimo athu ndikutembenukira kwa iye. Anatipatsa ndime 613 za malamulo kuti tidziœe machimo athu kuti tipulumuke kudzera mwa Yesu. Ichi ndi chifukwa chake Mulungu anatipatsa malamulo.

Page 21: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

21 Poyamba tiyenera kudziœa machimo athu kuti tipulumutsidwe

◄ Zam'kati ►

Nchifukwa chiyani Mulunngu atipatsa Malamulo?

Kuti tidziwe machimo athu

ndi chilango chake M’buku la Aroma 3:20 timawerenga kuti,

“Malamulo amangotizindikilitsa kuchimwa kwathu” choncho tidziœa Mulungu anatipatsa Malamulo mosatiumiliza kuti tidzikhala ndi malamulowo.

Kodi nzeru imene timayipeza kuchokera kumalamulo ndi iti? Ndi chifukwa chakuti tili ofooka kotheratu ndipo tilephea kusunga malamulo onse ndiponso kuti ndife ochimwa pamaso pake. Nanga tidziœanji kuchokera ku ndime 613 za malamulo ake? Zidziœa kulephera kwathu posasunga malamulo ake. Timadziœanso kuti ife olengedwa ake a Mulungu tilibe

mphamvu. Timadziœanso kuti ndife ochimwa pamaso pa Mulungu ndipo kuti tonse tidayenera kuponyedwa mugahena malinga ndi lamulo lake.

Kodi tikadziœa za machimo athu tiyenera kuchita chiyani? Kodi timafuna kupititsa patsogolo kulephera kwathuko? Iyayi chimene ife tingachite ndi kuvomereza kuti ndife ochimwa, ndikhulupilira mwa Ambuye Yesu kuti m’pulutsidwe kudzera muchipulumutso cha madzi ndi Mzimu Woyera, ndi kumuthokoza.

Chifukwa chimene Mulungu anatipatsira malamulo ndi chakuti ife tizindikire machimo athu ndi chilango chamachimowo kuti potero tidziœe kuti sitingapulumuke popanda Yesu. Ngati tikhulupilira mwaYesu monga Mpulumutsi wathu tidzaomboledwa.

Anatipatsa lamulo kuti tipulumutsidwe. Anatipatsa lamulo kuti tizindikire m’mene tiliri pa machimo athu ndi kutipulumutsa miyoyo yathu ku uchimo. Anatipatsa lamulo ndi kutuma Yesu kudzatipulumutsa. Anatumiza mwana wakwe

Page 22: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

22 Poyamba tiyenera kudziœa machimo athu kuti tipulumutsidwe

◄ Zam'kati ►

kudzatichotsera machimo athu kudzera mu ubatizo wake. Ndipo tikhoza kupulumutsidwa ngati tikhulupilira mwa Iye.

Tiyenera kudziœa kuti ndife anthu ochimwa ndi opanda chiyembekezo ndipo kuti tiyenera kukhulupilira kuti timasuke ku mphamvu ya uchimo, tikhale ana ake ndikubwezera ulemelero kwa Mulungu.

Tiyenera kumvetsa bwino Mau ake. Ziyambi zonse zinachokera m’mau ake. Tiyenera kuganiza ndi kuweruza kudzera m’mau ake. Ichi ndi chikhulupiliro choonadi.

KODI CHIMAKHALA MUM’TIMA WA MUNTHU NCHIYANI?

Tiyenera kuchita chiyani pa Maso pa Mulungu?

Tiyenera kuulura machimo athu Ndikupempha chipurumutso cha

Mulungu

Chikuhulupiliro chiyenera kuyamba ndi Mau ake ndipo tiyenera kukhulupilira Mulungu kudzera m’Mau ake. Kupanda kutero tidzalephera. Chidzakhala chikhulupiliro cholakwika.

Pamene a Farisi ndi alembi anaona ophunziro a Yesu alikudya m’kate ndi m’manja mosasamba sanathe kumvetsa chifukwa chimene anachitira zimenezi iwo ankayetsa kuti ophunzira aja sanali kudziœa Mau a Mulungu. Mau a Mulungu

Page 23: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

23 Poyamba tiyenera kudziœa machimo athu kuti tipulumutsidwe

◄ Zam'kati ►

amatiuza kuti chilichonse chilowa mwa munthu sichingathe kumuyipitsa chifukwa chimapita m’mimba mwake, osati mum’tima mwake ndipo chimatulukanso.

Monga pananenedwa pa Marko 7:20-23 “Adatinso ‘zimene zimatuluka mwa munthu ndizo zimamuipitsa.’ Chifukwa m’kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, zachiwerewere, zakuba, zakuphana, zigololo, masiliro, kuipa m’tima, kunyenga, zonyansa, kaduka ndiponso zopusa. Zoipa zonsezi zimachokera mkati mwa munthu, ndipo zimamuipitsa.” Adanena kuti anthu onse ndi ochimwa chifukwa amabadwa ndi uchimo.

Kodi mudziœa tanthauzo la zimenezi? Ife tonse ndife zidzukulu za Adamu. Sitingaone choona chenicheni chifukwa sitivomera kapenanso kukhulupilira Mau ake onse. Kodi chimakhala m’kati mwam’tima wa munthu nchiyani?

Tatiyeni tione pa Marko 7:21-22 “Chifukwa m’kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka

maganizo oipa, zachiwerewere, zakuba, zakuphana, zigololo, masiliro, kuipa m’tima, kunyenga, zonyansa, kaduka, kunyoza, kudzikuza ndiponso kupusa.” Zonsezi zimatuluka m’kati mwa m’tima wa munthu ndikumuipitsa ndi kuipitsanso anthu ena.

Pa Masalimo atiuza kuti “Ndikamayang’ana kuthambo lanu limene mudapanga ndi manja anu, ndikamaona mwezi ndi nyenyezi zimene mudazikhazika kumeneko, ndimadzifunsa kuti Kodi munthu nchiyani kuti muzim’kumbukila, mwana wa munthu nchiyani kuti muzim’samalira?”(Masalimo 8:3-4).

Nchifukwa chiyani amatiyendera? Amatiyendera chifukwa amatikonda. Ndiye anatilenga,kutikonda ndikutimvera chifundo ife anthu ochimwa. Anachotsa machimo athu onse ndikutipanga ife kukhla anthu ake ake. “Chauta Ambuye athu, dzina lanu ndilotchuka padziko lonse lapansi.” Mfumu Davide anayimba mu Chipangano Chakale pamene anadziœa kuti

Page 24: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

24 Poyamba tiyenera kudziœa machimo athu kuti tipulumutsidwe

◄ Zam'kati ►

Mulungu adzakhala Mpulumutsi wa anthu ochimwa.

Ndipo m’Chipangano Chatsopano, mtumwi Paulo adanena chimodzi modzi. Ndichinthu chodabwitsa kwambiri kuti ife olengedwa ndi Mulungu, tikhalenso ana ake. Izi zinachitika kudzera m’chifundo chake pa ife. Ichi ndi chikondi cha Mulungu.

Kuyesa kusunga malamulo onse, ndi njira yokhayo imene tingamuyesere Mulungu. Ilinso ndi ganizo limabwera chifukwa cha umbuli wathu. Nkulakwa kumakhala kutali ndi chikondi cha Mulungu pamene tili kuyetsa kusunga lamulo ndikupemphera. Ndi chifuniro cha Mulungu kuti ife tivomereze kuti ndife ochimwa kudzera mu malamulo ndi kukhulupilira mu chipulumutso cha madzi ndi mwazi (Mzimu).

Mau ake analembedwa mu Marko 7:20-23, “Zimene zimatuluka mwa munthu, ndizo zimamuipitsa. Chifukwa m’kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa,

zachiwerewere, zakuba, zakuphana, zigololo, masiliro, kuipa m’tima, kunyenga, zonyansa, kaduka, kunyoza, kudzikuza ndiponso zopusa. Zoipa zonsezi zimachokera m’kati mwa munthu, ndipo ndizo zimamuipitsa.”

Yesu anati zimene zimatuluka mwa munthu, amene ali nawo amaipitsidwa. Chakudya chimene Mulungu anatipatsa sichingaipitse munthu. Zolengedwa zonse ndi zabwino, koma zinthu zokhazo zimene zimatuluka mwa munthu, machimo athu, zimaipitsa munthu. Tonse tinabadwa monga zidzukulu za Adamu. Nanga tinabadwa bwanji? Tinabadwa ndi mitundu khumi ndi Iœiri ya machimo. Kodi sizoonadi zimenezi?

Tsono kodi tingakhale opanda tchimo? Tidzapitilizabe kuchimwa chifukwa tinabadwa ndi uchimo. Kodi mwa ife tokha tingaleke kuchimwa chifukwa chakuti Mulungu adatipatsa malamulo. Kodi tingasunge Malamulo onse khumi? Ayi.

Pamene tiyetsa kusunga malamulo ndi pamenenso tidzaona ndi ntchito yaikulu. Tidzaona

Page 25: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

25 Poyamba tiyenera kudziœa machimo athu kuti tipulumutsidwe

◄ Zam'kati ►

kuti talephera ndipo tidzaleka chabe. Ndipo ndi m’tima wodzichepetsa tingathe kuvomereza ubatizo ndi mwazi wa Yesu umene unatipulumutsa.

Ndime zonse 613 za malamulo ndi zoona. Koma anthu ndi ochimwa kuchokera pa nthaœi imene anapangidwa m’mimba mwa amayi awo. Tikavomera malamulo a Mulungu kuti ndi oonadi, koma ife ndi amene tinabadwa mu uchimo ndiponso sitingadziyeretse, timazindikira kuti tili oyenera kukhululukidwa mwa chifundo cha Mulungu ndikupulumutsidwa ndi chiombolo cha Yesu m’modzi, m’mwadzi ndi Mzimu. Pamene tizindikira kulephera kwathu – kuti, sitingadziyeretse mwa ife tokha ndipo tiyenera kulangidwa chifukwa chamachimo athu, palibe chomwe tingachite koma kudalira pa chiombolo cha Yesu.

Motero tingapulumutsidwe. Tiyenera kudziœa kuti sitingachite bwino pa maso pa Mulungu mwaife tokha. Choncho tiyenera kuvomera pa

maso pa Mulungu kuti ndife anthu ochimwa amene tiyembekezera chilango kugahena ndipo tikhoza kupempha Mulungu kuti atichitire chifundo, “Chonde Ambuye Mulungu khululukireni machimo anga onse ndichitireni chifundo.”

Taonani pemphero la Davide monga analembera pa Masalimo 51:4 “Motero mwakhoza ponditchula wolakwa, simudaleke pogamula mlandu wanga.”

Adadziœa kuti anali wodzala ndi uchimo ndi adaali woyenera kulangidwa kugahena komabe adaulura machimo ake pa maso pa Mulungu. Ngati sitikhululukira, palibe chimene tingachite koma kuponyedwa kugahena. Amenewa ndiwo malo athu.

Ichi ndico chikulupiliro chenicheni. N’mwamene tipulumukira. N’mwamene tiyenera kukhalira ngati tifuna kukonzekera kukulupirira muchiombolo chamwa Yesu.

Page 26: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

26 Poyamba tiyenera kudziœa machimo athu kuti tipulumutsidwe

◄ Zam'kati ►

TIYENERA KUDZIŒA M’MENE MACHIMO ATHU ALILI

Popeza ndife zidzikhukulu za Adamu, tonse

timasilira. Kodi nanga Mulungu amatiuza kuti chiyani? Iye amatiuza kuti tisachite chigololo. M’mitima mwathu timapha, koma Mulungu amatiuza kuti chiyani? Iye amatiuza kuti tisaphe. Tonse timanyoza makolo athu koma Mulungu amatiuza kuti tizilemekeza makolo athu. Tiyenera kudzindikira kuti Mau a Mulungu ndiwoona ndiponso abwino ndiponso kuti tonsefe tili ndi machimo m’kati mwa mitima yathu.

Kodi ndili kunena zoona kapena ayi? Tsono tiyenera kuchita chiyani pa maso pa Mulungu? Tiyenera kuvomera pa maso pake kuti ndife odzala ndi uchimo, opanda chiyembekezo. Sibwino kuganiza kuti tinali wolungama dzulo chifukwa tinachita zabwino, ndipo tachimwa lero chifukwa tachita zosayenera. Tinabadwa tili ochimwa. Mu chilichonse chimene timachita ndife

ochimwabe. Ichi nchifukwa chake tiyenera kuomboledwa kudzera mu ubatizo wa Yesu.

Sindife ochimwa chifukwa cha ntchito zathu monga kuchita chigololo, kupha ndi umbava… koma ndife ochimwa chifukwa chakuti timabadwa tili ochimwa pa maso pa Mulungu sitingakhale abwino muntchito zathu. Tikhoza kudziyerekeza kukhala abwino.

Tinabadwa ndi maganizo odzaza ndi uchimo monga kupha umbava ndi zina zotero. Nanga tingakhale bwanji olungama chifukwa sitichita machimo awa? Sitingakhale kukhala olungama pa maso pa Mulungu mwa ife tokha. Ngati tinena kuti ndife olungama, ndiye kuti ndife a chiphamaso. Yesu anawatcha Afarisi ndi Alembi kuti ndi achiphamaso. Anthu amabadwa ndi uchimo. Amachimwira Mulungu moyo wawo onse.

Aliyense amene anganene kuti sanamenyaneko ndi mnzake kapena ku vulaza wina aliyense kapena kuba ngakhale singano ya munthu wina pa

Page 27: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

27 Poyamba tiyenera kudziœa machimo athu kuti tipulumutsidwe

◄ Zam'kati ►

moyo wakwe wonse, alikunama chifukwa anthu amabadwa ndi uchimo. Ndi wabodza, wochimwa ndiponso Mkhristu wachiphamaso. Umu ndi m’mene Mulungu amamuonera.

Munabadwa muli ochimwa, ngakhale musachite tchimo lililonse mudzaponyedwa kugahena. Ngakhale munasunga lamulo kapena malamulo onse khumi ndinu ochimwabe ndipo mudzayenera kulangidwa kugahena.

Tsono tiyenera kuchita chiyani pa vuto monga ili? Tiyenera kupempha Mulungu kuti atichitire chifundo ndikudalira pa Iye kuti tipulumutsidwe ku machimo athu. Ngati satikhululikira, palibe chimene tingachite koma kuponyedwa kugahena. Amenewa ndiwo malo athu.

Amene avomera Mau ake, avomeranso kuti ndi ochimwa. Ndipo amadziœanso ndi olungama. Choncho amadziœa kuti kumva chabe Mau a Mulungu osadziœa chimene mauwo ali kunena, ndi kuchimwa. Anthu amene amavomera Mau ake ndi olungama ngakhale anali ochimwa pa maso pa

Mulungu. Anabadwanso mwatsopano mwa Mau ake ndikulandiranso chisomo chake. Ndi odalitsidwa kopambana.

AMENE AYESA KUDZIOMBOLA KUDZERA MU NTCHITO ZAWO AKADALI OCHIMWA

Ndi anthu ati amene akhalebe ochimwa nganga akhulupulire mwa Yesu?

Amene amayesa kudziombola

Kudzera muntchito zao Tiyeni tione pa Agalatia 3:10 ndi 11 “Onse

amene amadalira ntchito za malamulo a Mose kuti ziwapulumutse pa maso pa Mulungu,

Page 28: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

28 Poyamba tiyenera kudziœa machimo athu kuti tipulumutsidwe

◄ Zam'kati ►

ngotembereredwa. Pakuti Malembo akuti ngotembereredwa onse amene sasunga zonse zolembedwa m’buku la Malamulo tsono nchodziœikiratu kuti Mulungu salungamitsa munthu aliyense chifukwa chochita zimene Malamulo anena. Pakuti malembo akuti “Iye amene Mulungu wam’lungamitsa adzakhala ndi moyo.””

Mau a Mulungu akuti “Aliyense amene sasunga zonse zolembedwa m’buku la Malamulo ngwotembereredwa.”

Amene akhulupilira mwa Yesu namayesa kudzilungamitsa okha ndi ntchito zawo ndi otembereredwa. Kodi anthu amene alikuyetsa kudzilungamitsa ali kuti? Ali pansi pa tembererero.

Nchifukwa chiyani Mulungu anatipatsa lamulo? Anatipatsa lamulo kuti tidzindikire machimo athu (Aroma 3:20). Kuti ife tidzindikire kuti ndife ochimwa kotheratu ndiponso kuti tidzayenera kulangidwa kugahena.

Choncho, chomwe muyenera kuchita, ndikukhulupilira mu ubatizo wa Yesu Mwana wa Mulungu ndi kubadwa mwa tsopano mwa madzi ndi Mzimu.

Mukatero mudzapulumutsidwa ku machimo anu, kukhala olungama, kukhala moyo wosatha ndi kupita kumwamba. Khalani ndi chikhulupiliro m’mtima mwanu.

TCHIMO LOIPA KWAMBIRI PA DZIKO LAPANSI

Kodi tchimo loipa kwambiri pa dziko lonse ndi liti?

Kuyesa kukhala mwa lamulo

Page 29: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

29 Poyamba tiyenera kudziœa machimo athu kuti tipulumutsidwe

◄ Zam'kati ►

Palibe chimene chimawerengedwa koposa kukhulupilira mwa Mulungu. Timadalitsidwa pamene tikhulupilira m’madalitso ake. Iye anaganiza za kupulumutsa onse amene akhulupilira m’mau ake.

Koma lero, pakati pa okhulupilira, pali ambiri amene amayetsa kukhala mwa Lamulo lake. Akhristu ambiri alikuchita chimodzimodzi. Ndi chinthu chabwino kutero, koma nanga zingatheke bwanji?

Tiyenera kudziœa kuti nkupusa ngati munthu ayetsa kumakhala mwa Malamulo ake. Pamene tiyetsa kutero, tidzaonanso kuti nkosatheka. Iye anati “Chikhulupiliro chimabwera pa kumva Mau a Mulungu.” Tiyenera kuchotsa umbuni wathu kuti tipulumutsidwe.

TIYENERA KUTAYA MUYESO WATHU KUTI TIPULUMUTSIDWE

Tiyenera kuchita chiyani kuti tipulumutsidwe?

Tiyenera kutaya maganizo athu.

Kodi anthu angapulumutsidwe bwanji? Ayenera kudziœa kuti iwo ndi ochimwa. Pali ambiri amene mpaka pano sanapulumutsidwe chifukwa sangathe kuchotsa chikhulupiliro chawo cholakwika pa za m’mene angapulumutsidwe pa maso pa Mulungu.

Mulungu amatiuza kuti amene amakangamira pa buku la Malamulo ndi otembereredwa. Amene amakhulupilira kuti akhoza kukhala olungama pamene ali kukhulupilira mwa Yesu ndikuyetsa kukhala molingana ndi lamulo ali pansi pa

Page 30: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

30 Poyamba tiyenera kudziœa machimo athu kuti tipulumutsidwe

◄ Zam'kati ►

temberero lake. Amakhulupilira mwa Mulungu koma amadanabe kuti ayenera kukhala molingana ndi lamulo kuti apulumutsidwe.

Abwenzi okondedwa, kodi tingathe kukhala olungama muntchito zathu pamene tikadali ndi moyo padziko lapansi? Timakhala olungama pakukhulupilira kokha Mau a Yesu ndichipulumutso chimene iye anatipatsa. Pamene timakhala ndi chikhulupiliro mu ubatizo wa Yesu m’mwadzi wake, ndikukhulupiliranso kuti iye ndi Mulungu ndi m’ene amapezera chipulumutso.

Nchifukwa chake Mulungu anakonza lamulo la chikhulupiliro kwa ife ngati njira imene ingatipange ife kukhala olungama. Chiombolo cha madzi ndi Mzimu sichidalira ntchito zathu koma m’hikhulupiliro chokhazikika pa Mau a Mulungu. Ndipo Mulungu anatipumulutsa kudzera m’hikhulupiliro. Umu ndi m’mene Mulungu anakonzeratu ndipo wakwaniritsira cholinga chakechi.

Nchifukwa chiyani anthu amene adakhulupilira mwa Yesu sadaomboledwe? Nchifukwa chakuti sadalandire Mau achipulumutso amadzi ndi Mzimu. Koma ife, amene sitili oyera monga iwo aja taombœdwa chifukwa chakukhulupilira Mau a Mulungu.

Ngati anthu awiri ali kugwira ntchito pa chida chophwanyira miyala, mmodzi amene adzakhalira odzapitiliza kugwira ntchito ngakhale mmodzi wa iwo atatengedwa. Amene wakhalira uja ndi amene sadaomboledwe. Nchifukwa chiyani wina watengedwa wina wakhala?

Nchifukwa chakuti winayo adamvera ndi kukhulupilira Mau a Mulungu. Wina uja amene adayetsetsa kusunga malamulo adaponyedwa kugahena. Adayetsa ku kwawa kuti akafike kwa Mulungu, koma Mulungu adamugwedeza monga m’mene timagwedezera chikwama chikafuna kugwa pansi. Ngati munthu ayetsa kukwawa yekha kuti akafike kwa Mulungu pakusunga malamulo zoonadi adzaponyedwa kugahena.

Page 31: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

31 Poyamba tiyenera kudziœa machimo athu kuti tipulumutsidwe

◄ Zam'kati ►

Nchifukwa chake tiyenera kuomboledwa pakukhulupilira mwa madzi ndi Mzimu.

“Onse amene amadalira ntchito za Malamulo ndi otembereredwa. Paja Malembo akuti, ‘Ndi otembereredwa aliyense amene satsata zonse zolembedwa m’buku la malamulo. Komatu nchodziœikiratu palibe munthu amene angapezeke kuti ngwolungama pa maso pa Mulungu pakuchita ntchito zolamulidwa ndi Malamulo.’ “Olungama adzakhala ndi moyo pakukhulupilira”” (Agalatia 3:10-11; Aroma 1:17)

Kusakhulupilira Mau a Mulungu ndi tchimo pa maso pa Mulungu. Ndikuchimwanso kuphatikiza Mau a Mulungu ndimaganizo athu. Anthu sangakhale molingana ndi lamulo chifukwa tonse tidabadwa tili ochimwa. Ndipo timapitiliza kuchimwa pa moyo wathu onse. Timachimwa pang’ono pano, pang’ono uko ndi kwina kulikonse kumene ife tingapite. Tiyenera kudzindikira kuti ndife anthu chabe ndipo palibe chabwino mwaife koma uchimo.

Munthu alingati chidebe chonyamuliramo manyowa. Ngati tiyetsa kuchinyamula, timangowononga zimene zili m’katimo ulendo wathu wonse. Ife tili chomwecho. Timayenda ndi machimo kuli konse tingapite. Mungazimvese zimenezi?

Kodi mulikudziyerezabe kuti ndinu oyera? Ngati mungadzione nokha bwinobwino

mudzaleka kutaya nthaœi ndi kuyesa kuyeretsa nokha, m’malo mwa mungokhulupilira mwa madzi ndi mwazi wa Yesu.

Tifunika kuchotseratu maganizo athu ndikuvomera kuti ndife ochimwa pa maso pa Mulungu. Ndipo tikatero tibwererenso ku Mau ake ndi kudziœa m’mene Mulungu adatipulumutsira mwa madzi ndi Mzimu.

Page 32: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

◄ Zam'kati ►

ULALIKI WACHIŒIRI

Anthu amabadwa ali ochimwa

Page 33: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

33 Anthu amabadwa ali ochimwa

◄ Zam'kati ►

Anthu amabadwa ali ochimwa

< Marko 7:20-23 > “Adatinso, zimene zimatuluka mwa munthu,

ndizo zimamuipitsa. Chifukwa mkati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za chiwerewere, za kuba, zakuphana, zigololo, masiliro, kuipa mtima, kunyena, zonyansa, kaduka, kunyoza, kudzikuza ndiponso kupusa. Zoipa zonsezi zimachokera m’kati mwa munthu, ndipo ndizo zimamuipitsa.”

ANTHU ALI KUSOKONEZEDWA NDIKUKHALA ONAMIZIDWA

Ndani amene ali oyenera kupulumutsidwa?

Ndi amene amaganiza kuti ndi

munthu wochimwitsitsa Ndisanapilire, ndifuna ndikufunsani funso. Kodi

mumaganiza bwanji za inu nokha? Kodi mumaganiza kuti ndinu abwino kapena oipa? Mumaganiza bwanji?

Anthu onse amakhala modzinamiza. Sindinu oipitsitsa kapenanso abwino monga mumaganizira.

Nanga ndi ndani amene mukuganiza kuti angakhale ndi moyo wabwino wa chikhulupiliro? Kodi angakhale anthu amene amaganiza kuti ndi abwino kapena amene amaganiza kuti ndi oipa?

Page 34: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

34 Anthu amabadwa ali ochimwa

◄ Zam'kati ►

Aka nkachiœiri. Nanga ndi ndani amene oyenera kuomboledwa: Kodi amene achita machimo ambiri kapena ndi amene achita machimo ochepa? Amene achita machimo ambiri ndi amene angathe kuomboledwa chifukwa ali kudziœa okha kuti ndi ochimwa. Akhoza kuvomera chiombolo chimene Yesu anawakonzera.

Tikadziona bwinobwino tokha, tidzaona kuti ndife odzala ndi machimo. Kodi munthu ndi chiyani? Munthu ndi “mbeu ya anthu ochita zoipa.” Pa Yesaya 59 Mau a Mulungu akuti m’kati mwa mtima wa munthu muli modzala ndi uchimo. Choncho munthu ali odzaladi ndi uchimo. Koma ngati tinena kuti munthu ndi odzala ndi uchimo ambiri sadzavomereza. Kunena kuti munthu ndi “mbeu ya ochita zoipa” ndi kukhoza.

Ngati tidziyang’ana tokha mokhulupilika, tidzaona kuti mapeto ake tazindikira kuti ndife oipadi. Amene amadzikhulupilira ayenera kudziœa zimenezi.

Koma kuoneka kuti si anthu ambiri amene angavomere kuti iwo ndi odzala ndi uchimo. Ambiri amakhala omasuka chifukwa saona kuti iwo ndi ochimwa. Chifukwa chakuti ndife ochita zoipa, tapanganso ulamuliro woipa. Kukadakhala kuti palibe anthu ambiri amene amakana uchimo wawo ena akadakhala ndi manyazi kuti achimwe. Koma pali anthu ambiri onga ameneœa amene sachita manyazi ndi uchimo.

Koma chikumbumtima chawo chimadziœa. Munthu aliyense ali ndi chikumbumtima chimene chimamuuza kuti “Izi ndizochititsa manyazi.” Adamu ndi Hava adabisala pakati pa mitengo pamene anachimwa.

Lero lino anthu ochimwa alikubisala m’miyambo yawo yoipa-miyambo yathu ya uchimo. Anthu otere, amabisalanso pakati pa ochimwa anzawo kupewa chiweruzo cha Mulungu.

Anthu alikunamizidwa ndi maganizo awo oipa. Amaganiza kuti iwo ndi oyera kuposa ena. Anthu

Page 35: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

35 Anthu amabadwa ali ochimwa

◄ Zam'kati ►

amalira pamene adziœa kuti aputa mkwiyo wa Mulungu, “Munthu angachite bwanji zoterezi? Munthu wovala bwinobwino angachite bwanji zimenezi? Mwana angachite bwanji choipa kwa makolo ake?” Iwo amaganiza kuti sangachite zimenezi.

Okondedwa, ndi chinthu chovuta kwambiri kudziœa chilengedwe cha munthu. Ngati tikufuna kudziœa za m’mene ife tiliri, poyamba tiyenera kuomboledwa. Ndi chinthu chapatali kwambiri kudziœa zonsezi, ndi pali ambiri aife amene sitidzadziœa mpaka tidzamwalira.

MUZIDZIWE NOKHA

Kodi munthu amene sazidzila yekha amakhalabwanji?

Amayesa kudzibisa yekha

Nthaœi timaona munthu ndipo timaona kuti sadzidziœa yekha. Socrates anati, “Muzidziœe nokha.” Anthu ena sadziœa zimene zili mkati mwa mitima yawo, akupha, aumbava, kusilira, kuipa, kunyenga, diso ioipa…

Ali ndi ululu njoka mumtima mwake koma amakamba za ubwino. Ichi nchifukwa chakuti sadziœa kuti anabadwa ndi uchimo.

Pali anthu ambiri padziko lapansi amene sadziœa kudziona okha. Akudzinyenga okha ndipo amakhala okutidwa ndi chinyengo chaocho. Amadziponya okha kugahena. Ali kupita kugahena chifukwa chachinyengo chao.

Page 36: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

36 Anthu amabadwa ali ochimwa

◄ Zam'kati ►

MOPITIRIZA ANTHU AMAGWA MU UCHIMO PAMOYO WAWO ONSE

N’chifukwa chiyani ali kupita kugahena?

Chifukwa chakuti sali

kuzidzila okha Tatiyeni tionenso pa Marko 7:20-23. “Zimene

zimatuluka mumunthu ndizo zimamuipitsa. Chifukwa m’kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, zachiwerewere, zakuba, zakuphana, zigololo, masiliro, kuipa m’tima, kunyenga, zonyasa, kaduka, kunyoza, kudzikuza ndiponso kupusa. Zoipa zonsezi zimachokera m’kati mwa munthu, ndipo ndizo zimamuipitsa”. Mum’tima mwa munthu ndimodzala ndi maganizo oipa kuchokera pamene anali m’mimba mwa mayi wake.

Tiyerekeze kuti m’tima wa munthu unapangidwa ndi galasi ndi wodzazidwa ndi madzi oipa kunena kuti machimo athu. Chingachitike nchiyani ngati munthu uja abwerera m’mbuyo ndikupitanso pa tsogolo? Nchodziwikilatu kuti zoipa zija zili m’kati (tchimo) zidzasefukira. Pamene akuyenda uku ndi uko, zoipa zija zidzasefukira mopitilira.

Ife odzala ndi uchimo, miyoyo yathu ili chimodzimodzi. Timafalitsa machimo kulikonse kumene tikupita. Tidzakhala tikuchimwabe mpaka moyo wathu wonse chifukwa ndife odzala ndi uchimo.

Vuto ndi lakuti sitidziœa kuti ndife odzala ndi uchimo ndipo m’kati mwa mitima yathu muli machimo okhaokha. Umu ndi m’mene munthu alili.

Uchimo umene ndiokonzeka kusefukira. Tchimo la munthu ndi lakuti savomera kuti anabadwa ndi uchimo koma ndi anthu amene amakhala nawo ndi amene anamuipitsa choncho

Page 37: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

37 Anthu amabadwa ali ochimwa

◄ Zam'kati ►

sivuto lake ayi. Choncho ngakhale achimwe, amaganiza kuti

chimene iye angachite ndikuchotsa machimowo. Amayetsetsa kuchotsa tchimolo ngakhale lisefukire, ndipo mum’tima mwake amanena kuti sivuto lake. Pamene tili kuchotsa machimo kodi timaganiza kuti sitidzagwanso mu uchimowo? Komabe tiyenera kuchotsa machimo athu kaœiri kaœiri.

Pamene kapu yadzadza ndi uchimo, idzapitiriza kusefukira. Sidzithandiza kupukuta kunja kwake kokha. Masiku ambiri timapukuta kunja kwa makapu, ndi chinthu chopanda nzeru ngati kapu yadzadza ndi uchimo.

Munthu amabadwa ndi uchimo motero mum’tima wake simukhala mopanda tchimo ngakhale uchimo uchoke mwa iye. Choncho, timangopitilira kuchimwa mu moyo wathu.

Munthu ngati sadzindikira kuti ndiwodzadza ndi uchimo, amapitiriza kubisala. Uchimo uli mum’tima wa munthu, siumachoka ngati asamalira

kunja kokha. Amatulutsa pang’ono ndi kupukuta ndi nsalu, ndipo ngati atulutsa nthaœi ina, apukuta ndi nsalu. Amaganiza kuti ngati angapitirize kupukuta kachiœiri ndiye kuti idzayera koma imasefukira kaœiri kaœiri.

Kodi muganiza kuti izi zidzachitika mpaka liti? Zidzachitika mpaka iye atamwalira. Ichi nchifukwa chake tiyenera kukhulupilira Yesu kuti tipulumutsidwe kuti tipulumutsidwe tiyenera kudziœa tokha.

Kodi ndani angalandire Yesu mothokoza?

Ochimwa amene avomera kuti achimwa kwambiri

Tikhoza kunena kuti pali anthu aœiri monga

ngati makapu aœiri odzadza ndi madzi aoipa. Ena amaziyang’ana okha ndi kunena kuti, “Aa, ndine

Page 38: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

38 Anthu amabadwa ali ochimwa

◄ Zam'kati ►

munthu wochimwa.” Ndipo amafunafuna m’nzake kuti am’thandize.

Koma wina amaganiza kuti iye siwoipitsitsa. Samawona kukhula kwa uchimo umene uli mwa iye ndipo amaganiza kuti siwoipitsitsa. Masiku onse amoyo wake amapitiriza kupukuta zosefukira, amapukuta kumbali yina ndi kumbali yinatso mofulumira.

Pali ena ambiri amene amakhala ochenjera mu umoyo wawo ndi uchimo wochepa m’mitima motero kuti asefukira. Koma chifukwa amakhalabe ndi uchimo m’mitima yawo, kodi ubwino ndi uti? Kukhala osamala sikuzaœathandiza kuœafikitsa kumwamba. Kusamala kumakutengerani kugahena.

Abwenzi okondedwa, “kukhala osamala” kumakutengerani kugahena. Pamene akusamala, machimo awo samasefukira kwambiri. Ngakhale anamizire koma ndi ochimwabe.

Kodi ndi chiyani chimene chili mum’tima wa munthu? Uchimo? Makhalidwe oipa? Inde!

Maganizo oipa? Inde. Kodi kuli kuba? Inde! Kudzikudza? Inde!

Timadziœa kuti ndife anthu odzadza ndi uchimo pamene tikuona zimene tikuchita zosayenera ngakhale sitinapunzitsidwe za zomwe tichita. Ngakhale sipangaoneke umboni pa zimene tinkachita pa ubwana.

Koma zili bwanji pamene takula? Pamene tikupita kusekondale sukulu, kapena ku kolegi ndi kwina konse. Timawona kuti m’kati mwathu muli uchimo zoona? Ndi chimakhala chosatheka kubisa, zoona? Timapitiriza kusefuka. Ndipo timakhulupilira. “Sindikanachita izi,” koma sitimasintha, chifukwa chiyani? Chifukwa aliyense wa ife anabadwa ndi uchimo wochuluka.

Sitimakhala woyera chifukwa cha kusamala kwathu. Chimene tiyenera kudziœa ndi choti tinabadwa ndi uchimo wochuluka kuti tipulumutsidwe. Ndi okhawo ochimwa othokoza ndi kulandira chipulumutso chimene Yesu anakonza amapulumutsidwa, koma amene aganiza

Page 39: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

39 Anthu amabadwa ali ochimwa

◄ Zam'kati ►

kuti Sindinachite uchimo wambiri sapulumuka. Ngati muganiza kuti, “Sindinachimwe

kwambiri ndipo nditaomboledwa kutchimo lochepa” kodi muganiza kuti pamenepa ndiye kuti mwamasuka mpaka m’tsogolo? Palibe.

Amene angaomboledwa ku machimo ndimunthu amene amadziœa kuti iyeyo ndi odzala ndi machimo. Ndipo amakhulupilira kuti Yesu anamuchotsera machimo akewo pobatizidwa mu mtsinje wa Yorodani ndiponso kuti anasungunula machimowo pa Mtanda.

Kaya tinaomboledwa kapena ayi, tonsefe timakhala m’chinyengo. Ndife odzala ndi machimo. Umu ndi m’mene ife tonse tilili. Tingaomboledwe pokhapo pamene tidziœa kuti Yesu anachotsa machimo athu onse.

MULUNGU SANAOMBOLE ANTHU AMENE ALI NDI MACHIMO OCHEPA

Kodi ndani amene amanamiza Ambuye?

Amene amapempha chikhululukiro

cha machimo amene achita tsiku ndi tsiku

Mulungu sanaombole anthu amene ali ndi

machimo ochepa. Mulungu sayang’ana mwachangu pa anthu amene amati, “Mulungu, ndili ndi kachimo kochepaka.” Amene Mulungu amawayang’ana ndi amene amati “Mulungu, ine ndine odzala ndi machimo. Ndikupita ku gahena. Chonde ndipulumutseni.” Anthu ochimwa kotheratu amati “Mulungu, ine ndingapulumuke

Page 40: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

40 Anthu amabadwa ali ochimwa

◄ Zam'kati ►

ngati inu nokha mutandipulumutsa. Sindinga pempherenso molapa chifukwa sindidzachimwanso. Chonde mpulumutseni.”

Mulungu amapulumutsa anthu amene amamudalira kotheratu. Inenso ndinayesako. Koma mapemphero olapa satimasula ife ku machimo. “Mulungu, chonde nchitireni chifundo ndipo ndipulumutseni kumachimo anga.” Anthu amapephera chotere, adzapulumutsidwa.

Amakhulupilira m’chiombolo cha Mulungu, ubatizo wa Yesu amene anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Adzapulumutsidwa.

Mulungu amapulumutsa anthu okhawo amene amadziœa kuti ndi odzala ndi machimo, ndi mbeu ya tchimo. Anthu amene amati, “Ndachita tchimo lochepali. Chonde khululukireni tchimo limeneli,” akali ochimwabe ndipo Mulungu sangawapulumutse. Mulungu amapulumutsa anthu amene amadziœa kuti iwo ndi odzala kotheratu ndi machimo.

M’buku la Yesaya 59:1 pali mau awa: “Chauta

siwosowa mphamvu, kuti angalephere kukupulumutsani, ndipo si gonthi, kuti angapande kumva zimene mukupempha.”

Chifukwa chakuti amabadwa ali odzala ndi machimo, Mulungu sangamuyang’ane momukonda. Sichifukwa chakuti dzanja lake ndi lofunika, kapena khutu lake ndi lolemera kuti sangathe kumva pamene tikupempha chikhululukiro chake.

Mulungu ali kutiuza kuti, “Machimo anu adakulekanitsani ndi Mulungu wanu, ndipo Iye wakufulatilani chifukwa cha machimo anuwo. Choncho samva zimene inu mumanena.” Chifukwa chakuti mitima yathu ndiyodzala ndi machimo sitingathe kuloœa mu Ufumu wa Mulungu ngakhale zitseko zikhale zotsekula.

Ngati, amene ndi odzala ndi machimo, opempha chikhululukiro nthaœi zonse pamene achimwa, ndiye kuti naye Mulungu akanakhala akupha mwana wake nthaœi zonse. Mulungu safuna kuchita zimenezi. Choncho akunena kuti,

Page 41: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

41 Anthu amabadwa ali ochimwa

◄ Zam'kati ►

“Osabwera kwa ine ndi machimo tsiku ndi tsiku. Ndinakutumizirani Mwana Wanga kudzakuombolani ku machimo anu onse. Chimene inu muyenera kuchita ndi kuzindikira m’mene Mulungu anachotsera machimo anu ndipo muone ngati ndi zoonadi. Kenaka, mukhulupilire mu Uthenga wa chipulumutso kuti mupulumutsidwe. Ichi ndi chikondi changa chozama chimene ndili nacho pa inu, zolengedwa zanga.”

Izi ndi zimene iye amatiuza. “Khulupilirani Mwana Wanga kuti muomboledwe. Ine, Mulungu wanu, ndinatuma Mwana wanga kudzapereka nsembe ya machimo anu ndi mphulupulu zanu. Khulupilirani MwanaWanga kuti mupulumuke.”

Anthu amene sadziœa kuti ali odzala ndi machimo amangopempha chikhululukiro cha timachimo tawo tochepato. Amabwera kwa Mulungu popanda kudziœa kuchuluka kwa machimo awo ndi kupempha, “Chonde khululukirani katchimo kochepaka sindidzabwerezanso.”

Ali kuyesanso kunamiza Mulungu. Sitichimwa kamodzi kokha ayi koma timachimwa mosalekeza mpaka kumwalira. Anthu otere ayenera kupempha chikhululukiro nthaœi zonse kufikira patsiku lotsiliza la moyo wawo.

Kukhululukidwa kwa tchimo limodzi lokha sikungathetse vuto lililonse chifukwa timachimwa tsiku ndi tsiku kufikira tsiku la imfa. Choncho njira yekhayo imene ingatimasule ku tchimo ndi kupereka machimo athu onse kwa Yesu.

Kodi munthu ndi chiyani?

munthu ndi machimo okha

okha Baibulo limanena za machimo amunthu. Pa

Yesaya 59:3-8, “Manja anu ali psuu ndi magazi a anthu amene mudapha. Mudadziipitsa ndi

Page 42: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

42 Anthu amabadwa ali ochimwa

◄ Zam'kati ►

machimo anu ambiri. Pakamwa panu palankhula za bodza, pamanena zoipa. Palibe munthu amene amaimba mlandu molungama, palibe wopita kubwalo la milandu moona. Amadalira zopanda pake, amangonena mabodza. Amangolingalira za mphulupulu, nachitadi zoipa zimene akuganiza. Ziwembu zao nzoopsa ngati mazira amphiri, komanso nzasalimba konse ngati ukonde wa nkangaude. Wodya mazira ambiri amata. Likasweka dzira limodzi mumatuluka mphiri. Ukonde wa kangaude sungauvale ngati nsalu, chimene anthu amapangacho sangafunde konse. Ntchito zao nzoipa ndipo amakonda kuchita za ndeu ndi manja ao, amathamangira kukachita zoipa, sachedwa kupha anthu osalakwa. Maganizo ao onse ali pa zoipa. Kulikonse kumene kuli iwowo anthu sapeza mtendere. Zonse zimene amachita nzopanda chilungamo. Amayenda m’njira zokhotakhota, ndipo aliyense woyenda m’njira zimenezo sapeza mtendere.”

Zala za munthu, nzoipitsidwa ndi mphulupulu

ndipo zimagwira ntchito yoipa moyo wakwe wonse. Chilichonse chimene zalazo zingachite nchoipa. Ndipo malilime athu amalankhula zoipa. Chilichonse chotuluka m’kamwa mwathu nchabodza.

“Kunena mabodza ndiye khalidwe lake”(Yohane 8:44). Anthu amene abadwa mwatsopano, amakonda kunena kuti, “Ndili kukuuzani zoona…. Zoonadi ndili kukuuzani. Zimene ndikunenazi nzoonadi…” Koma zonsezi ndi mabodza. Zili monga kwalembedwa, “Kunena mabodza ndiye khalidwe lake.”

Munthu amakhulupilira m’mau opanda pake ndipo amanena mabodza. Munthu ndi odzala ndi mabodza ndipo amabala mphulupulu. Munthu amagogomola mazira amphiri ndikuluka ukonde wa kangaude. Mulungu akutiuza kuti, “Wodya mazira awo amafa. Likasweka dzira limodzi mumatuluka mphiri.” Iye akuti m’mitima yathu muli mazira a mphiri. Mazira amphiri! Muli zoipa mumitima mwanu. Khalani oomboledwa

Page 43: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

43 Anthu amabadwa ali ochimwa

◄ Zam'kati ►

pakukhulupilira mu uthenga wa madzi ndi mwazi. Nthaœi zambiri ndikayamba kunena za

Mulungu, pali anthu ena amene amati, “Ayi, osandiuza za Mulungu ine. Nthaœi zambiri ndikafuna kuchita kanthu, limayamba ndi tchimo kuchoka mwaine. Limafalikira. Sindingayende popanda kugwetsa tchimo paliponse. Sindingadzigwire chifukwa ndine odzala ndi machimo. Motero, osakambanane za Mulungu ayi.”

Munthu uyu akudziœadi kuti ndi odzala ndi machimo komanso kuti sakudziœa Uthenga umene ungamupulumutse. Anthu amene amazidziœa kuti ndi odzala ndi machimo akhoza kupulumutsidwa.

Tingonena kuti, aliyense ali chimodzimodzi. Aliyense akufalitsa tchimo. Limangosefukira chifukwa munthu ndi odzala ndi uchimo. Njira yopulumutsira munthu otere ndi kudzera mu mphamvu ya Mulungu. Kodi sizodabwitsa zimenezi? Amene amafalitsa uchimo pamene ali okumudwa, okondwa, omasuka….akhoza

kupulumuka kudzera mwa Ambuye athu okha Yesu. Yesu anabwera kudzapulumutsa anthu amenewa.

Ndipo anapereka nsembe ya machimo anu. Muzidziœe nokha kuti ndinu odzala ndi machimo kuti mupulumutsidwe.

Page 44: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

◄ Zam'kati ►

ULALIKI WACHITATU

Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi

tingapulumuke?

MALAMUL

MACHI

Page 45: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

45 Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi tingapulumuke?

◄ Zam'kati ►

Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi

tingapulumuke?

< Luka 10:25-30 > “Katswiri wina wa za malamulo adaimilira

kuti ayetse Yesu. Adamufunsa kuti, ‘Aphunzitsi, kodi ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?’ Yesu adamuyankha kuti, ‘Uzikonda Chauta Mulungu wako, ndi m’tima wako wonse, ndi mphamvu zako zonse ndi nzeru zako zonse, ndiponso mzako monga umadzikondera iwe weka.’ Yesu adati, ‘Mwayankha bwino. Kachiteni zimenezo ndipo udzakhala ndi moyo.’ Koma munthu uja pofuna kuzionetsa ngati wolungama, adafunsa Yesu kuti, ‘Nanga mnzanga ndani?’ Apo Yesu adati, ‘Munthu wina akatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Panjira achifwamba

adam’gwira. Adamuvula zovala, na m’menya, nkumusiya ali thasa, ali pafupi kufa.’”

Kodi vuto lalikulu la munthu ndi chiyani?

Amakhala molakwika chifukwa

chakulephera kwake Luka 10:28 “Kachiteni zimenezi ndipo

mudzakhala ndi moyo.” Anthu amakhala ndi makhalidwe oipa chifukwa

chakulephera kwawo. Zikuoneka ngati ali osauka. Aoneka ngati ali samalira koma amanyengezedwa mosavuta ndikukhala osadziœa kuipa kwawo. Timabadwa popanda kudzidziœa tokha koma timakhalabe ngati odziœa. Chifukwa chakuti anthu sadzidziœa okha, Baibulo limanena kuti ndife ochimwa.

Anthu amakamba zakukhazikika kwa machimo awo. Ndipo kuoneka ngati anthu satha kuchita

Page 46: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

46 Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi tingapulumuke?

◄ Zam'kati ►

zinthu zabwino ndipo nkosatheka kudzitchula kuti ndi anthu abwino. Amafuna kunyada chifukwa cha ntchito zawo zabwino ndipo amadzionetsera. Amati ndi ochimwa koma achita ngati ndi anthu abwino kwambiri.

Adziœa kuti mwa iwo mulibe chabwino ngakhale mphamvu yochitila zinthu zabwino koma amayetsa kunamiza anzawo ngakhale kudzinamiza okha kumene. “Sitingakhale oipa kotheratu. Muyenera kukhala china chake chabwino mwa ife.”

Ndipo amaona anzawo ndi kumadziuza kuti, kalanga ine! Iye anachitiranji zimenezi. Zikanakha bwino akanango siya osachita zimenezi. Ndikuganiza kuti ndi kwabwino kulalika mwa njira imeneyi. Anayamba ndiye kuomboledwa tsono ndikuganiza kuti nchabwino kuti azikhala monga munthu oomboledwa. Ine ndangoomboledwa posachedwapa, ndipo ngati ndi phunzira zambiri, ndidza bwino kwambiri kuposa iye.

Anthu akunora mipeni m’mitima mwao. “Iwe yamba wadikira. Udzaona kuti sindiwe wolingana nawe. Ndipo ukuganiza kuti ulipatsogolo panga tsopano, sichoncho? Angodikira chabe. Kunalembedwa m’Baibulo kuti amene abwera potsiliza, adzakhala oyambirira. Ndi kudziœa kuti izi zikukhudzanzo ine.” Yembekezani ndipo amadzinamiza.

Ngakhale achite monga mmene iwo amachitila, amawaweruza. Pamene aima ku gome amapezeka kuti mwadzidzi ali kubwerezabwereza ndipo amalepheranso kuti akonze zimene walakwitsa m’malo mwake amaganizira za chovala chimene wa vala pa nthaœiyo.

Olalikira ayenera kuyang’ana kwa Mulungu yekha osayamba kuganiza za zimene anthu ena angamaganize. Ngati achita zimenezi ndiye kuti sadzatha kulalika.

Anthu ambiri mukawafunsa ngati ali ndi mphamvu yakuchita zabwino, amayankha kuti alibe. Koma amadzinamiza kuti ali ndi mphamvu

Page 47: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

47 Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi tingapulumuke?

◄ Zam'kati ►

yakuchita zinthu zina. Kotero kuti amayetsetsa mpaka nthaœi ya kumwalira.

Amaganiza kuti m’mitima mwao, muli zabwino kuti angakhale ndi mphamvu kuchita zinthu za bwino. Iwo amaganizanso kuti iwowonso ndi anthu abwino. Posaganizira za nthaœi imene iwo anabadwa mwatsopano, ngakhale amene achita bwino muntchito ya Mulungu, amaganiza kuti

‘Ndikhoza kuwachitira ichi Ambuye.’ Koma ngati Ambuye salamulira miyoyo yathu,

kodi mukuganiza kuti tingachite zabwino? Kodi muli chabwino mwa munthu? Kodi angakhale ali kuchita ntchito zabwino? Munthu alibe mphamvu yochitila zinthu zabwino. Nthaœi zonse munthu akafuna kuchita zabwino mwa iye yekha, amachimwa.

Anthu ena amayika Yesu pambali ataomboledwa ndi kuyamba kuyetsa kuchita bwino paokha. Mwa ife muli zoipa zokha zokha. Timangochita zoipa. Mwa ife tokha, (ngakhalenso anthu opulumutsidwa kale), timangochimwa. Ichi

ndi choonadi cha thupi lathu.

Kodi timachita chiyani kawiri kawiri, zabwino

kapena zoipa?

Zoipa

M’buku lathu lotchedwa ‘Athokozedwe Ambuye’ muli nyimbo imene timayimba chotero, “♪Popanda Yesu ife timalephera. Tili ngati anthu osawa monga sitima imene imawoloka nyanja popanda chokakhira madzi♪.” Popanda Yesu ife timango chimwa. Ndife olungama chifukwa Yesu anatipulumusta, popanda Yesu ndife anthu oipa. Ngati tichita zinthu motsatira lamulo kodi tingapulumuke?

Mtumwi Paulo akunena kuti, “Ngakhale ndimafuna kuchita zabwino komabe sindizichita, koma ndimachita zoipa zimene sindifuna.” (Aroma

Page 48: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

48 Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi tingapulumuke?

◄ Zam'kati ►

7:19) Ngati munthu akhala ndi Yesu palibe vuto. Koma pamene alibe naye chochita, amafuna kuchita zabwino pa maso pa Mulungu. Koma pamene ayetsa kutero ndipamenenso amachita zoipira Mulungu.

Ngakhale Mfumu Davide anali ndi khalidwe longa lomweli. Pa mene dziko lake linali la mtendere ndi lachitukuko, anayamba kukhala ngati munthu amene amagulira zinthu pa zenela. Anagwa m’mayesero ofuna zinthu zosangalatsa moyo wake. Kodi iye anama bwanji pamane aiwala Ambuye! Kunena zoona anali munthu oipa. Iye anapha Uriya ndi kutenga mkazi wake. Sanathe kuona kuipa kumene kunali mwa iye. Anayamba kunena zifukwa za tchimo lakelo.

Koma tsiku lina, m’meneri Natani anabwera kwa iye namuuza kuti, “Mu m’zinda wina munali anthu aœiri, wina anali wolemera winayo anali wosauka. Wolemerayo anali ndi nkhosa zambiri ndi ng’ombenso zambiri. Koma wosauka uja analibe nkhanthu komwe kupatula kankhosa

kamodzi kakakazi, kamene adaagula. Tsiku lina ku nyumba kwa munthu wolemera uja kudafika mlendo. Munthu uja sadafune kutengako imodzi mwa nkhosa zake, kapena imodzi mwa ng’ombe zake kuti aphere mlendo wakeyo.”(2 Samuel 12:1-4)

Davide anati, “Munthu amene adachita zimeneziyu ayenera kuphedwa basi” Mkwiyo wakwe unakula kwambiri choncho anati alinazo zake zambiri zoti akanachotsapo imodzi.

Koma anatenga kankhosa ka munthu wosauka uja kuphera mlendo wakeyo. “Anayenera kuphedwa!” Ndipo Natani anamuuza kuti “Munthu wake ndi iwe amene.” Ngati sititsatila Yesu ndi kukhala naye ngakhale amene anabadwa mwatsopano akhoza kukhala ndi makhalidwe onga amenewa.

Ndi chimodzimodzi kwa anthu onse, ngakhale okhulupilika. Amalephere kaœirikaœiri ndipo popanda Yesu munthu amachita zoipa. Motero tili othokoza lero chifukwa Yesu anatipulumutsa

Page 49: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

49 Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi tingapulumuke?

◄ Zam'kati ►

osayang’ana kuipa kwathu. “♪Nchifukwa kupumula pansi pa mthunzi wa Mtanda.♪” Mitima yathu imapumula pansi pa mthunzi wa chiombolo cha Yesu. Koma ngati tisiya mthunzi ndi kudziyang’ana tokha, sitingapumule.

MULUNGU ANATIPATSA CHILUNGAMO CHA CHKHULUPILIRO ASANAPEREKE LAMULO

Kodi chiyamba n’chiyani chikhulupiliro kapena lamulo?

Chikhulupiliro

Mtumwi Paulo ananena kuti Mulungu

anatipatsa chilungamo cha chikhulupiliro

asanapereke lamulo. Chilungamo cha chikhulupiliro chinabwera poyamba. Anapereka kwa Adamu ndi Hava, kwa Kaini ndi Abele, kenaka kwa Seti ndi Enoki…. Kufikila kwa Nowa…, kenaka kwa Abrahamu ndi kufikira kwa Isake, kwa Yakobo ndi ana ake khumi ndi aœiri. Ngakhale panalibe lamulo anakhala olungama pa maso pa Mulungu kudzera m’chikhulupiliro chawo pa Mau Ake.

Ndipo patapita nthaœi adzukulu a Yakobo anakhala mu Egipito monga akapolo kwa zaka mazana anai (400) chifukwa cha Yosefe. Kenaka Mulungu anawatsogolera kuwatulutsa mu Egipito kudzera mwa Mose ndi kupita nawo kudziko la Kanani. Koma m’zaka 400 zaukapolozi anaiwala chilungamo cha chikhulupiliro.

Motero, Mulungu anawatsogolera kuoloka Nyanja Yofiira kudzera mzozizwitsa kufikira m’chipilulu. Pamene anafika pa chipululu cha tchimo, anawapatsa lamulo pa Phiri la Sinai. Anawapatsa Malamulo Khumi amene ndi ndime

Page 50: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

50 Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi tingapulumuke?

◄ Zam'kati ►

zokwana 613 za Lamulo. “Ine ndine Ambuye Mulungu wako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, Mulungu wa Yakobo. Mose akwere pa Phiri la Sinai, ndipo ndidzampatsani lamulo.” Mulungu anapereka lamulo kwa Israele.

Anawapatsa lamulo kuti “Adziœe kuchimwa kwawo”(Aroma 3:20). Mulungu anachita izi kuti Aisraele adziœe zimene Mulungu afuna ndi zimene Mulungu safuna ndi kuuluranso kuti Iye ndi wa chilungamo ndiponso oyera.

Anthu onse aku Israele amene anakhala mu ukapolo kwa zaka mazana anai (400) mu Egipito anawoloka Nyanja Yofiira. Sanakumaneko ndi Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, Mulungu wa Yakobo. Sanamudziœe.

Ndipo pamene anali kukhala mu ukapolowo, anaiwala chilungamo cha Mulungu. Ndipo sanakhale ndi mtsogoleri. Yakobo ndi Yosefe analephera kupereka chikhulupiliro kwa ana ake, Manase ndi Efulemu.

Motero anafuna kupezanso Mulungu wawo ndi

kukumana naye chifukwa anawapatsa la mulo ataiwala chikhulupiliro. Anawapatsa Lamulo kuti abwererenso kwa Iye.

Kupulumutsa a Israele, kuwapanga kuti akhale anthu ake, anthu a Abrahamu, Iye anawauza kuti aumbalidwe.

Cholinga chowaitanira chinali chakuti aœadziœitse kuti kuli Mulungu popanga lamulo ndi kuœadziœitsanso kuti iwo anali anthu ochimwa pa maso pake. Anafuna kuti iwo mu nsembe ya chiombolo imene Mulungu anawapatsa. Ndipo anawapanga kukhala anthu ake.

Ana a Israele anaomboledwa kudzera mu lamulo (njira ya nsembe) pakukhupilira mwa Mpulumutsi wolonjezedwa amene anali kubwera. Koma njira yoperekera nsembe inatha nthaœi yake. Tiyeni tione kuti zimenezi zinachitika liti.

Pa Luka 10:25, “Munthu wina wodziœa za malamulo anafuna kumuyetsa iye.” Mkulu wa za malamuloyo anali Mfarisi. Afarisi anali anthu amene anali kukhulupilira malamulo ndipo anali

Page 51: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

51 Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi tingapulumuke?

◄ Zam'kati ►

kuyetsa kugwiritsitsa Mau a Mulungu. Anali anthu amene anayetsetsa kuteteza dziko lawo ndiponso kusunga malamulo. Ndiponso kunali amene anali kulemekeza chipembedzo chawo koma anali anthu osaganiza pochita zinthu, anayetsa kuchita zionetsero pofuna kukwaniritsa masomphenya awo.

Kodi ndi anthu ati amene Yesu anafuna kukumana

nawo? Anthu ochimwa opanda

mbusa kumanena mau monga kunena kuti, “Samalani

anthu ozunzidwa m’dziko muno.” Amakhulupilira Yesu anabwera kudzapulumutsa anthu osauka ndi ozunzika. Motero, amaphunzira za Mau a Mulungu m’masukulu ophunzilirako za Mulungu, kutenga mbali mundale za dziko, ndikumayesa

kupulumutsa kunena kuti, “Tiyeni tonse tikhale mwa lamulo loyera ndi la chifundo…, tikhale mwa lamulo ndi Mau ake.” Koma sadziœa tanthauzo lenileni la Mau akuti Lamulo. Amayetsa kukhala ndi lemba la lamulo koma sazindikira cholinga cha lamulolo.

Motero tikhoza kunena kuti panalibe m’neneri, m’tumiki wa Mulungu, kwa zaka mazana anai (400) Yesu asanabadwe. Ndipo anakhala gulu la nkhosa zopanda mbusa.

Analibe lamulo kapena m’tsogoleri. Mulungu sanadziulure kudzera mwa atsogoleri achiphamaso a chpembedzo amasiku amenewo. Dziko linakhala pansi pa ulamuliro wa Boma la Aroma. Ndipo Yesu anati kwa anthu aku Israele amene anali ku m’tsata m’chipululu sadzawasiya ndi njala. Anawamvera chisoni anthu opanda mbusa. Panali ambiri amene anali kuvutika pa nthaœi imeneyo.

Ndipo anthu odziœa za malamulo ndi amene anali ndi mwayi; Afarisi anali zidzukulu za a Israele achipembedzo cha Chiuda. Anali anthu

Page 52: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

52 Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi tingapulumuke?

◄ Zam'kati ►

onyada kwambiri. Ndipo katswiri wa zamalamuloyu anafunsa

Yesu pa Luka 10:25 “Kodi ndingachite chiyani kuti ndi peze moyo wosatha?” Kwa iye ankaona ngati palibe munthu wina woposa iye ku Israele. Choncho m’kulu wa zamalamuloyu (amene anali asanaomboledwe) anafuna kuyetsa Yesu, anati “Kodi ndichite chiyani kuti ndipeze moyo wosatha?”

Mukulu wa zamalamuloyu ali ngati chidzudzulo pa ife lero. Anafunsa Yesu, “Kodi ndingachite chiyani kuti ndipeze moyo wosatha?” Yesu anati kwa iye, “Kodi mbuku la malamulo munalembedwa chiyani? Mumawerengamo zotani?”

Iye anayakha nati, “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi m’tima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse ndi nzeru zako zonse,” ndipo uzikonda m’nzako monga iwe mwini.

Ndipo Yesu anati kwa iye, “Mwayankha bwino;

Kachiteni zimenezi ndipo mudzakhala ndi moyo.” Anali kuyetsa Yesu osadziœa kuti anali woipa,

wodzala ndi machimo amene sangathe kuchita zabwino. Motero Yesu anamufunsa kuti, “Kodi mbuku la malamulo munalembedwa chiyani? Nanga mumawerengamo zotani?”

Kodi mmalamulo mumawerengamo zotani?

Ndife ochimwa amene sitingathe

kusunga malamulo “Kodi mbuku la malamulo mumawerengamo

zotani?” “Mwayankha bwino; kachite zimenezi ndipo mudzakhala ndi moyo.” “Kodi mbuku la malamulo mumawerengamo zotani?” Mau aœa atanthauza kuti kodi mumadziœa ndi kulizindikira lamulo.

Monga m’mene anthu ali kuchitira masiku ano,

Page 53: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

53 Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi tingapulumuke?

◄ Zam'kati ►

m’kulu wa za malamuloyu anali kuganiza kuti Mulungu anampatsa lamulo kuti azilisunga. Kotero anayankha, “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi m’tima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse ndi nzeru zako zonse ndiponso uzikonda m’nzako monga iwe mwini.”

Lamulo linalibe vuto. Anatipatsa lamulo langwiro. Anatiuza kuti tizikonda Ambuye ndi m’tima wonse ndi moyo wathu wonse, ndi mphamvu zathu zonse ndi nzeru zathu zonse ndi tizikonda anzathu monga momwe timadzikondera. Ndi chinthu chabwino kuti tizikonda Mulungu wathu ndi m’tima wathu wonse ndi mphamvu zathu zonse. Koma anali mau oyera amene sanathe kusungidwa.

“Kodi mumawerenga zotani?” Kunthauza kuti lamulo ndi lokhozeka koma mumalizindikira bwanji? Mkulu wa zamalamulo uja anali kuganiza kuti Mulungu anapereka lamulolo kuti iye azisunga. Koma lamulo la Mulungu linaperekedwa

kwa ife kuti tizidziœa kulephera kwathu, ndi kuonetsera mphulupulu zathu kotheratu. Limaonetsa machimo athu, “Munachimwa. Munapha pamene ndinakuuzani kuti musaphe. Nchifukwa chiyani simundimvera?”

Lamulo limaonetsa machimo mum’tima wa munthu. Tiyerekeze kuti pamene ndinali kuyenda, ndinaona zinanadzi zakupsa m’munda. Mulungu anadichenjeza mulamulo, usatenge zinanadzizo ndi kudya.

Ndidzachita manyazi ngati utenga ndi kudya. “Inde atate.” Mundau ndi wa uje, choncho suyenera kutenga zipatsozo “Inde Atate.”

Panthaœi imene tikumva mwa lamulo kuti tisatenge timakhala ndi ofuna kutenga ndithu chinthucho. Ngati tikankhadziœe pansi, limatikakhanso mobwezera. Machimo amunthu ali chimodzimodzinso.

Mulungu anatiuza kuti tisamachita zoipa. Mulungu akhoza kunena kuti chifukwa chakuti iye ndi Oyera, chifukwa iye ndi wokwanira chifukwa

Page 54: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

54 Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi tingapulumuke?

◄ Zam'kati ►

iye ali ndi mphamvu kuchita chilichonse. Kumbali inayi ife sitingathe kukhala osachimwa ndiponso sitingachite zinthu zabwino. M’mitima mwathu mulibe chinthu chabwino. Malamulo amati osachita (anali tsindika ndi mau akuti ‘Osachita’) chifukwa chiyani?

Chifukwa chakuti anthu amasilira m’mitima mwathu muli chigololo.

Tiyenera kumawerenga Mau a Mulungu mosamala. Pamene ndiyamba kukhulupilira mwa Yesu, ndinakhulupilira malinga ndi mau. Ndinawerenga kuti Yesu anafa pa mtanda chifukwa chaine ndipo sindinathe kuletsa misozi m’maso mwanga. Ndinali munthu woipa kwambiri ndipo Yesu anandifera pa mtanda… M’tima wanga unapweteka kwambiri moti ndinakhulupilira mwa Iye. Pamenepa ndinaganiza kuti, ‘Ndikanakhulupilira ndikanakhulupilira molingana ndi Mau’.

Pamene ndinawerenga buku la Eksodo 20 ndinamva kuti, “Usakhale nayo milungu yina

koma ine ndekha.” Ndinapemphera molapa chifukwa cha mau amenewa. Ndinayang’ana m’kati mwa m’tima wanga kuti ndione ngati ndidakhalapo ndi milungu yina. Ndipo ndinazindikira kuti zoonadi ndinali nditagwadirako milungu ina kwa nthaœi zambiri makamaka pa mwambo wolemekeza agogo anga. Ndinachita tchimo lokhala ndi milungu ina.

Motero, ndinapemphera molapa, “Ambuye, ndapembedza mafano. Niyenera kuweruzidwa. Chonde khululukireni machimo angawa. Sindidzachitanso.” Choncho tchimo limodzi ndithana nalo.

Ndipo ndinayamba kuganiza ngati ndinatchulako dzina lake pachabe. Pamenepo ndinakumbukira kuti ndinali kusuntha pamene ndinayamba kukhulupilira mwa Mulungu. Anzanga anali kundiuza kuti, “Kodi suchititsa manyazi Mulungu ukamasuntha. Mkhristu angasunthe bwanji?”

Uku kunali kutchula dzina la Mulungu pachabe,

Page 55: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

55 Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi tingapulumuke?

◄ Zam'kati ►

sichoncho? Motero ndinapempheranso, “Ambuye ndinatchula dzina lanu pachabe. Chonde khululukireni. Ndidzaleka kusuntha.” Ndipo ndinayesa kuleka kusuntha koma ndinapitiliza kuyatsa ndudu kwa chaka chimodzi. Chinali chinthu chovuta kwambiri, ndipo nkosatheka kuleka kusuntha. Koma potsiliza, ndinakwanitsa kulekelatu kusuntha. Ndinaona kuti tchimo linanso ndathana nalo.

Lamulo lina ndikuti “Uzikumbukira tsiku la Sabata likhale lopatulika.” Linatanthauza kuti osachita chilichonse pa tsiku la Mulungu; osachita malonda, kapena kupanga ndalama… Ndipo ndinalekanso zimenezo.

Ndipo panali lamulo lakuti, “Lemekeza atate ndi amako.” Ndinawalemekeza pamene ndinali kukhala kutali koma anali gwero la kutchera khutu langa pamene ndinali pafupi. “Chifukwa choona ubwino wanga, ndinachimwa pamaso pa Mulungu. Chonde khululukireni, Ambuye.” Ndipemphera molapa.

Koma sindinathe kulemekeza makolo anga chifukwa onse anali atamwalira nthaœi imeneyo. Ndikanachita chiyani? “Ambuye khululukireni wochimwa wopanda pake ine. Munapachikidwa pa mtanda chifukwa cha ine.” Ine ndinali munthu wothokoza kwambiri!

Mwa njira imeneyi ndiganiza kuti ndathana ndi machimo anga limodzi limodzi. Panali malamulo ena monga usaphe, usachite chigololo, usasilire…. Ndinazindikira kuti sindinasunge ngakhale limodzi mwa malamulowa. Ndinapemphera usiku ndi usana. Koma inu mukudziœa kuti kupemphera molapa, sichinthu chosangalatsa. Tiyeni tikambe kupemphera molapa.

Pamene ndiganiza za kupachikidwa kwa Yesu, ndinatha kumvetsa ululu umene Yesu anamva. Ndipo anafera ife amene sititha kumvera ndikutsatira Mau ake. Ndinakhala ndili kulira usiku wonse ndi kum’thokoza chifukwa chindipatsa chisangalalo chenicheni.

Chaka changa choyamba kukhala nawo pa

Page 56: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

56 Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi tingapulumuke?

◄ Zam'kati ►

mapemphero chinali chosavuta kwaine koma zaka zina zotsilazo zinakhala zovuta kwambiri chifukwa ndinali kuganiza kwambiri chifukwa cha misozi imene inali kuchoka m’maso mwanga chifukwa cha zimene ndinali kuchita.

Pamene misozi inaleka kuchoka m’maso mwanga, nthaœi zambiri ndinali kupita ku mapiri kukapemphera ndi kusala zakudya kwa masiku atatu. Misozi ija inayambanso kuchoka m’maso. Ndinanyikidwa m’misozi yanga, ndinabweranso kudzakhala ndi anzanga, ndikuyamba kulira m’tchalitchi.

Anthu amene anali kukhala nane anati, “Wakhala woyera chifukwa cha mapemphero ako kumapiri kuja?” Koma misozi ija inaumanso m’maso mwanga. M’chaka cha chitatu mpamene zinthu zinafika povuta kwambiri. Ndidayamba kuganiza za zoipa zimene ndinachitila anzanga ndi akhristu anzanga ndipo ndinayambanso kulira. M’maso mwanga munali misozi yambiri koma sinagwire ntchito.

Patapita zaka zisanu, ndinapilira osaliranso ngakhale kuti ndinali kuyetsa apa ndi apa. Zitapita izi mphuno zanga nazo ziyamba kukhala ngati ndili ndi chimfine. Zaka zambiri zitapita, ndikhala wodzikakamiza kuwerenga Mau a Mulungu.

LAMULO LIMATSA NZERU YA KUDZIŒA TCHIMO

Kodi lamulo limatizindikiritsa chiyani?

Kuti sitingathe kusunga

lamulo Pa Aroma 3:20 timawerenga kuti, “Malamulo

amangotizindikiritsa kuchimwa kwathu.” Mau amenewa anakhala ngati uthenga kwa ine wochokera kwa Mtumwi Paulo ndipo

Page 57: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

57 Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi tingapulumuke?

◄ Zam'kati ►

ndinakhulupilira mau okhawo amene ndinasankha. Koma pamene misozi inauma m’maso mwanga sindinathe kupitilira kukhala m’chikhulupiliro.

Motero, ndinachimwa mopitiliza ndipo ndinaona kuti ndili ndi machimo m’kati mwa mtima wanga ndiponso chinali chinthu chovuta kwa ine kukhala molingana ndi malamulo. Sindinathe kuwanyamula. Koma sindinathe kuwakana malamulowo chifukwa anapatsidwa kwa ife kuti tiziœamvera. Potsiliza ndinakhala katswiri wa za malamulo monga tionera m’Malembo Oyera. Chinakhala chovuta kwambiri kuti ndipitirire kukhala ndi moyo wokhulupilira.

Kotero kuti pofuna kuthetsa vuto limeneli, ndikhala ndili kufuna funa munthu wolalika, amene angalalikire za kubadwanso mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu. Ndinakumana ndi mlaliki amene analikulalikira kuti machimo athu onse ana omboledwa.

Pamene ndimva kuti ndilibe tchimo, chimakhala ngati mphweya wa tsopano ukuwomba

kum’tima wanga. Ndili ndimachimo ambiri moti pamene ndiwerenga m’malamulo ndimakumbikira machimo awa. Ndimachimwira malamulo onse khumi mum’tima wanga ku chimwira mum’tima nditchimo, sindinafune kukhala mokhulupilira mu malamulo.

Pamene ndinali kusunga malamulo ndinali wokondwa, koma pamene ndinalephera kusunga malamulo sindinali wokondwa, mokwiya ndi chisoni. Mosachedwa ndimaona zina zake ngati zichitika ndipo ndimatopanazo. Ndikanakhala kuti ndinaphunzitsidwa kuyambira pa chiyambi, “Ayi, ayi. Palitanthaunzo lina lamalumulo limawonetsa kuti ndinu odzadza ndi uchimo; mumakonda ndalama, chifukwa cha dama, ndi zinthu zina zimene zimawoneka ngati zokongola. Muli ndi zinthu zina zimene mukonda kwambiri kusiyana ndi Mulungu. Mufuna kutsatira zinthu za dziko. Malamulo anapatsidwa kwa inu, osati kuti musunge, koma kuti mudzindikire kuti ndinu ochimwa ndi zoipa mumitima yanu.”

Page 58: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

58 Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi tingapulumuke?

◄ Zam'kati ►

Pakadakhala wina akadandiphunzitsa kumbuyo sindikadavutika zaka zakumbuyo khumi. Ndakhala pansi pa malamulo zaka zakumbuyo khumi mpaka ntazindikira izi.

Lamulo la chinayi ndi ili “Sunga tsiku la Sabata likhale loyera.” Chimatanthauza kuti tisagwire ntchito patsiku la Sabata. Chimatanthauza kuti tiyenera kuyenda, osati kukwera pa ulendo wa utali. Ndipo ndinaganiza kuti ndiyende pansi kumalo okalalika kuti ndilemekezedwe.

Makamaka, pazosenzi ndinali kukalalika malamulo. Motero ndinaganiza kuti ndiziyetsa kulalika zomwe ndinalalika. Zinali zovuta motero ndinaganiza kuti ndisiye.

Monga zalembedwera, “Kodi mumawerenga izi?” Sindinali kumvetsa funsoli ndipo ndinavutika zaka zakumbuyo khumi. Katswiri wazamalamulo sanavetse izi. Anaganiza kuti ngati angasunge malamulo ndi kuœatsatira akhoza kudalitsidwa pamaso pa Mulungu.

Koma Yesu anamuuza kuti “Kodi uku ndi kuwerenga kwanu?” Inde, mwayankha bwino; mwachita monga momwe zinalembedwera. Yesani ndi kusunga izi, ngati m’chita choncho m’zakhala ndi moyo, koma m’mwalira ngati simutero, (ngati munthu sakhala ndi moyo amwalira, sichoncho?)

Koma m’kulu wa zamalamulo sanamvetse. Mukuluyu ndife, inu ndi ine. Ndinaphunzira za Mau a Mulungu zaka khumi, ndinayetsa zonse, kuœerenga ndi kuchita zonse, kutsala zakudya, mosadziœa kulankhula muzinenero zina… Ndinaœerenga Baibulo zaka khumi ndipo ndinaganiza kukwaniritsa chinthu china. Koma mu uzimu ndinali munthu wosawona.

Ndichifukwa chake wochimwa ayenera kukumana ndi wina wake kuti amuthandize kuti ayang’ane uyu ndi Ambuye athu Yesu Khristu. Ndipamene amadzindikira kuti Aa! Sitingathe kusunga malamulo. Ngakhale tiyetse bwanji, tidzamwalira tikadali kuyetsa. Koma Yesu anabwera kutipulumutsa ndi madzi ndi Mzimu!

Page 59: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

59 Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi tingapulumuke?

◄ Zam'kati ►

(“Hallelujah!”) “Tiyamike Mulungu” Tingathe kupulumutsidwa ndi madzi ndi magazi (mwadzi). Ndi mphatso ndi chisomo cha Mulungu. Tiyamike Ambuye.

Ndinali ndi mwayi waukulu kuti ndi tsirize maphunziro apamwamba ngakhale ndinali wotaya m’tima, koma ena anataya nthaœi yawo pa moyo wawo wonse kuphunzira Mau a Mulungu pachabe, sanadziœe chowona mpaka atamwalira. Ena anakhulupilira kwa zaka khumi sanabadwetso kachiœiri.

Tinachokako ku uchimo pamene tidzindikira kuti sitingathe kusunga malamulo, ndikuima pamaso pa Yesu ndi kumvetsera Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu Woyera. Pamene tikumana ndi Yesu, timachokako ku chiwerezo ndi chiwonongeko. Ndife wochimwitsitsa kwambiri koma timakhala woyera chifukwa anatipulumutsa ndi madzi ndi mwazi wake.

Yesu anatiuza kuti sitingakhale ndi moyo mu chifuniro chake. Ananena izi kwa m’kulu

wamalamulo koma sanamvetse. Yesu anamuuza kudzera munkhani kuti amvetse.

Kodi chipangitsa anthu kulephera m’moyo wa

chikhulupiliro nchiyani?

Tchimo

“Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu, panjira achifwamba adam’gwira. Adam’vula zovala, nam’menya, nkum’siya ali thasa, ali pafupi kufa” (Luka 10:30) Yesu anali kumuuza kuti anavutika moyo wake wonse monga ngati munthu amene achifwamba anam’menya pafupi kufa.

Munthu wina ankhatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Yeriko ndi mzinda chabe Yerusalemu nditanthauzo la m’zinda wa chipembezo; m’zinda wachikulupiliro, wonyadira

Page 60: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

60 Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi tingapulumuke?

◄ Zam'kati ►

malamulo. Chikutiuza kuti ngati tikhulupilira mwa Yesu ngati chipembezo chathu, sitingathe koma kuwonengeka.

“Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu, panjira achifwamba adam’gwira, adam’vula zovala, nam’menya, nkumusiya ali thasa, ali pafupi kufa.” Yerusalemu unali m’zinda wa anthu ambiri. Kunali wansembe wam’kulu, amene anali kulandira ansembe alendo ndi ena anthu odziœika a chipembezo. Kunali ena ambiri odziœa bwino malamulo. Kunali amene ankayetsa kusunga malamulo koma nalephera motero anachinzika ku Yeriko. Anapitirira kugwa mudziko (Yeriko) ndipo anakumana ndi akuba.

Munthu uyu anakumana ndi achifwamba kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Yeriko ndipo anamulanda zovala.

‘Kulandidwa zovala’ kutanthauza kuti anataya kulungama kwake. Ndi chinthu chosatheka kuti tikhale moyo ndi malamulo, kukhala ndi malamulo. Mtumwi Paulo mubuku la Aroma 7

akuti, “Ngakhale ndimafuna kuchita zabwino komabe sindizichita, sindichita zabwino zimene ndifuna, koma ndimachita zoipa zimene sindifuna.”

Ndifuna kuchita zabwino ndi kukhala mu Mau ake. Koma mumitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, zachiwerewere, zakuba, zakuphana, zigololo, masiriro, kuipa m’tima, kunyenga, zonyansa, kaduka, kunyoza, kudzikuza, ndiponso kupusa. Zoipa zonsezi zimachokera m’kati mwa munthu, ndipo ndizo zimamuipitsa (Marko 7:21-23).

Chifukwa zili mumitima yathu ndipo zimatuluka nthaœi ndi nthaœi, timachita zimene sitifuna kuchita ndi kusachita zimene tiyenera kuchita. Timapitiriza zoipa zimene zili m’kati mumitima yathu. Zimene Satana amachita amatipatsa chilakolako kuti tichimwe.

Page 61: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

61 Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi tingapulumuke?

◄ Zam'kati ►

UCHIMO UMENE ULI M’KATI MUM’TIMA WA MUNTHU

Kodi tingakhale ndi moyo posunga malamulo?

Ayi

Mubuku la Marko 7 akuti. “Palibe chinthu

chochokera kunja ndi kuloœa m’kati mwa munthu chimene chingathe kumuipitsa. Koma zimene zimatuluka mwa munthu ndizo zimamuipitsa.”

Akutiuza ife kuti kuli maganizo oipa, zachiwerewere, zakuba, zakuphana, zigololo, matsiriro, kuipa m’tima, kunyenga, zonyansa, kaduka, kunyoza, kudzikuza, ndiponso kupusa Mkati mum’tima wa munthu.

Palibe amene samapha. Makolo amaphyetsa m’tima ana awo, “ayi osachita izo. Ndinakuuza kuti usachite izo uzawonengeka. Ndinanena kuti

usachite izo ndipo ubwere kuno. Ndinakuuza ndipo ndinati usachite izo ndizakupha ngati uchita izo.” Uku ndi kupha. Mukhoza kupha ana anu ndi mau anu osaganizira.

Ana athu ayenera kukhala apenya chifukwa amathaœa kwa ife m’sanga; koma ngati tiwonetsa m’kwiyo wathu kwa iwo adzamwalira. Tizawapha pa maso pa Mulungu. Nthaœi zina timaziwophyeza tokha.

Aa Mulungu wanga! Chifukwa nchiyani ndinachita ichi? Timayang’ana pamene tinamenya mwana wathu ndipo timaganiza kuti tinasokonezeka pamene tinawamenya. Timachita izi chifukwa timakhala ndi kupha mumitima yathu.

Ndimachita zimene sindifuna kuchita, kutanthauza kuti timachita zoipa chifukwa ndife oipa. Ndichinthu chapafupi kuti Satana atiyetse kuti tichimwe.

Munthu amene sanapulumutsidwe afanana ndi munthu amene amakhala munyumba

Page 62: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

62 Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi tingapulumuke?

◄ Zam'kati ►

ndikuyang’ana chipupa za khumi ndikupemphera monga ngati mukulu wansembe Sungchol waku Korea. Ndibwino kukhala ndi kuyang’ana maso ku chipupa koma pafunika kuti wina abweretse chakudya ndi kuchotsa zoipa.

Ayenera kugwirizana ndi wina wake. Sichingakhale chovuta ngati angakhale mwamuna, tinganizire ngati angakhale mkazi wokongola. Ngati angamuone mwamwayi, kukhala kwake sikungakhale kwaphindu. Amaganiza, “Sindiyenera kuchita chigololo, ndili nacho mum’tima wanga koma sindiyenera kuwometsera. Ndiyenera kukuchumula. Ayi! Choka mumaganizo anga!”

Koma kuweruza, kugamula kwakwe kunachoka pamene anamuona. Pamene mkazi anachika, anayang’ana m’tima wakwe atagwira ntchito kwa zaka zisanu popanda phindu.

Ndichapafupi kuti Satana atenge chilungamo cha munthu chimene Satana amachita ndi kum’menya chibakera pang’ono. Munthu

amayetsa kuzipulumutsa popanda kupulumutsidwa, amangopitirira kugwa mu uchimo. Amapereka chakhumi mokhulupirika Sabata lililonse, kusala zakudya masiku makhumi anayi, ndikupemphera masiku makhumi khumi…. Koma Satana amayetsa munthu ndi zinthu zabwino pa moyo wake.

“Ndikufuna kukupatsa mpando wapamwamba pakamupani, koma ndiwe m’khristu siungagwire ntchito pamatsiku a Sabata, kodi ungathe? Ndi udindo wapamwamba. Mwina ungagwire ntchito masiku a Mulungu atatu ndipo m’mwezi upite ku tchalitchi kamodzi. Usatsangalala ndi kudyera udindo umenewu ndikukhala ndi ndalama zambiri. Ukuganiza bwanji?” Apa, zikuwoneka kuti uzagula zinthu makhumi khumi ndi makhumi khumi.

Ngati izi sizingagwire ntchito,ndikokuti iye ngofookera pa akazi. Satana amayika mkazi patsogolo pake, ndipo amagwa ndi kukondana naye nayiwala Mulungu pomwepo. Umu

Page 63: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

63 Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi tingapulumuke?

◄ Zam'kati ►

ndimumene chiyelo chamunthu chimawonongekera.

Ngati tiyetsa kukhala motsatira malamulo, pamapeto ake zotsatira zake ndi mabala auchimo, kuwawa ndi umphaœi; timataya chiyelo chilichonse.

“Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Panjira achifwamba adam’gwira. Adamuvula zovala, nam’menya, nkumusiya ali thasa, ali pafupi kufa.”

Ichi chitanthauza kuti ngakhale tikhala mu mzinda wa Yerusalemu muchifuniro cha Mulungu Woyera, kaœiri kaœiri timabwerera mumbuyo chifukwa cha kufooka kwathu kumene kudzatiwononga.

Kuyenda ulendo waku Yeriko kutanthauza kugwa mudziko lapansi ndi kuyandikirana ndi zadziko ndikutalikirana ndi Yerusalemu. Pachiyambi Yerusalemu amakhala pafupi. Koma pamene timachimwa ndi kutembenuka kaœirikaœiri timapeza kuti tikuima munjira ya ku

Yeriko; kugwa m’kati mu dziko la uchimo.

Ndani angapulumutsidwe?

Ndi iwo amene asiya kuyesa pa iwo okha

Kodi munthu uyu amakumana ndi ndani pa ulendo wopita ku Yeriko? Anakumana ndi a chifwamba. Munthu amene samatsatira malamulo amakhala ngati galu waumve. Amagona paliponse ndikumwa zonyasa. Galu uyu amadzuka m’mawa tsiku lina ndi kumwa kachiœiri. Galu waumve amadyanso zomwe watsadza. Ndichifukwa chake ndi galu. Amadziœa kuti sayenera kumwa. Amatembenuka m’mawa mwake ndi kumwanso kachiœiri.

Akufanana ndi munthu amene anakumana ndi achifwamba mnjira pa ulendo wopita ku Yeriko.

Page 64: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

64 Ngati tichita zinthu motsatila Lamulo, kodi tingapulumuke?

◄ Zam'kati ►

Anamusiya atamenyedwa pafupi kufa. Mum’tima mwake munali uchimo wokha. M’menemu ndi m’mene munthu alili.

Anthu amakhulupilira mwa Yesu ndikutsatiranso malamulo, koma zotsatira zake ndizakuti uchimo siumachoka m’mitima yawo. Zonse zimene amaonetsa ndi mabala a uchimo pa moyo wao wa “chipembezo.” Amene ndi mochimwa amaponyedwa kugahena. Amadziœa izi koma sadziœa chimene angachite. Kodi inu ndi ine sitinali choncho? Tonse tinali ofanana.

Mukulu wamalamulo amene sanamvetse malamulo a Mulungu anayetsetsa pamoyo wake wonse koma anaponyedwa kugahena, womvuladzidwa. Ameneyu ndife inu ndi ine.

Ndi Yesu yekha angatipulumutse. Pali anthu ambiri abwino otizungulira amene amaonetsera zimene amadziœa. Onseœa amayetsa kukhala wotsatira malamulo a Mulungu. Samadzikulupilira okha, sangathe kunena kuti ndiwochimwa koma amawona kuti ndi abwino ndi okhulupirika.

Pakati pa iwo panali ochimwa amene ali pa ulendo waku Yeriko, ndi amene amenyedwa ndi achifwamba ndipo iwo ndi omwalira kale. Tiyenera kudziœa kuti ndi osalimba pamaso pa Mulungu.

Timvomere pamaso pake, Ambuye ndikupita kugahena ngati simundipulumutsa ine. Chonde ndipulumutseni. Ndiyenera kupita kulikonse mufuna ngakhale kukhale mavuto ngati mwavomereza kuti ndimve Uthenga woona. Ngati mundisiya ndipita kugahena. Ndikukupemphani kuti mundipulumutse.

Kwa iwo amene akudziœa kuti akupita kugahena, amasiya kudalira pa iwo okha ndipo amaika chikhulupiliro pa Ambuye, awa ndi amene adzapulumutsidwa. Sitingadzipulumutse tokha.

Tiyenera kudzindikira kuti tili ngati munthu amene anagwa mumanja mwa achifwamba.

Page 65: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

◄ Zam'kati ►

ULALIKI WA CHINAYI

Chiombolo cha muyaya

Page 66: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

66 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

Chiombolo cha muyaya

< Yohane 8:1-12 > “Koma Yesu adapita kuphiri la Olivi.

M’mamawa adabweranso ku nyumba ya Mulungu. Anthu onse adadza kwa iye, iyeyo nkukhala pansi nayamba kuwaphunzitsa. Aphunzitsi a Malamulo pamodzi ndi Afarisi adabwera ndi mai amene adaamugwira akuchita chigololo, nkumukhalitsa pakati pao. Tsono adauza Yesu kuti, ‘Aphunzitsi mai uyu wagwidwa ali mkati mochita chigololo. Paja m’buku la malamulo a Mose adatilamula kuti tizipha pakumponya miyala. Nanga inuyo mukuti chiyani pamenepa?’ Adamufunsa funsoli kuti amuyetse ndikumpeza chifukwa. Koma Yesu adaœerema, nayamba kulemba pansi ndi chala chake. Popeza kuti iwo adapitilira kumufunsa, Yesu adaœeremuka nawauza kuti, ‘Pakati panupa amene

sadachimwepo konse, ayambe ndiye kumponya mwala maiyu.’

Atatero, adaœeremanso namalembanso pansi. Koma iwo adamva zimenezi adayamba kuchokapo mmodzi mmodzi kuyambira akulu akulu; Yesu nkutsalira yekha, mai uja ali chikhalire pakati pampaja. KenakaYesu adaœeramuka namufunsa kuti, ‘Kodi mai alikuti anthu aja? Kodi palibe ndi mmodzi yeme amene wakuzengani mlandu?’

Maiyo adati, ‘Inde Ambuye, palibe.’ Tsono Yesu adauza mai uja kuti, ‘Inenso sindikukuzengani mlandu. Pitani koma kuyambira tsopano musakachimwenso.’ Apo Yesu analankhulanso kwa iwo kuti, ‘Ndine ku unika kwa dziko. Uyo amene anditsata sadzayenda m’mdima konse, koma adzakhala mu ku unika.’”

Page 67: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

67 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

Ndi machimo angati

amene Yesu anachotsa?

Machimo onse adziko lapansi

Yesu anatipatsa chiombolo chamuyaya. Padziko lino lapansi palibe munthu amene sangapulumutsidwe ngati akhulupilira mwa Yesu ngati Mpulumutsi wake. Iye anaombola tonsefe. Ngati pali munthu wochimwa amene amadandaula ndi machimo ake, n’chifukwa chakuti sazindikira m’mene Yesu anachotsera machimo mu ubatizo wake.

Ife tiyenera kudziœa ndi kukhulupilira chinsinsi cha chipulumutso. Yesu anachotseratu machimo athu onse ndi ubatizo wake, ndipo ananyamula chilango chifukwa cha machimo athu ndipo anapachikidwa pa Mtanda.

Muyenera kukhulupilira mu chipulumutso cha

madzi ndi Mzimu; chipulumutso cha muyaya cha machimo athu. Muyeneranso kukhulupilira m,chikondi chake chachikulu chimene chakusandutsani kukhala olungama. Khulupilirani zimene Iye anachita ku Mtsinje wa Yolodani ndiponso pa Mtanda kuti mupulumuke.

Ndipo Yesu amadziœanso machimo athu obisika. Anthu ena amaganiza molakwika pa zamachimo. Iwo amaganiza kuti machimo ena sangathe kukhululukidwa. Yesu anafafaniza machimo onse.

Palibe tchimo ngakhale limodzi limene iye analisiya. Chifukwa chakuti Yesu anachotsa machimo onse padziko lino lapansi, palibenso munthu wochimwa. Kodi mumaudziœa Uthenga umene unachotsa machimo anu, ngakhale machimo anu a mtsogolo? Khulupilirani Uthenga umenewu kuti mupulumuke. Ndipo bwererani ku ulemelero wa Mulungu.

Page 68: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

68 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

MAI AMENE ANAGWIDWA AKUCHITA CHIGOLOLO

Kodi ndi anthu angati amene amachita

chigololo?

Anthu onse

Pa Yohane mutu wa 8 pali nkhani ya m’zimai wina amene anagwidwa ndi chigololo. Ndipo tikhoza kuona m’mene Yesu anapulumutsira mai ameneyu. Nkofunika kuti tigawane chisomo chimene maiyu anachilandira. Sichovuta kunena kuti anthu onse amachita chigololo pa moyo wawo wonse. Mzimu uliwonse umachita chigololo.

Ngati kwa ife sizioneka choncho, ndi chifukwa chakuti timachita zimenezi kaœirikaœiri kotero kuti zimaoneka ngati kuti sitichita. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti m’mitima mwathu muli chigololo.

Ndimayang’ana m’zimayi ndi kumaganiza ngati alipo amene chikhalire sanachiteko chigololo monga mai uja amene anagwidwa. Tonse timachita chigololo. Timango dziyerekeza ngati sitinachiteko.

Kodi inu mukuganiza kuti ndikulakwa? Ai sindikulakwa. Mutayang’ana bwinobwino m’mitima mwanu. Aliyense padziko lapansi anachitako chigololo. Anthu amachita chigololo pamene ali kuyang’ana m’kazi mosilira pa meso, m’maganizo ndi muntchito zawo, nthaœi iliyonse ndi kwina kulikonse.

Vuto ndi lakuti anthu sadziœa kuti akuchita tchimoli. Pali anthu ambiri amene sadziœa mpaka kufa kuti akhala ali kuchita chigololo kosawerengeka pamoyo wawo wonse. Osati anthu okhawo amene agwidwa, komanso tonse amene sitinagwidwe. Anthu onse amachita chigololo m’maganizo mwawo ndi muntchito zawo. Kodi limeneli sikhalidwe lathu?

Kodi muli kukhumudwa nazo zimene

Page 69: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

69 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

ndanenazi? Komabe ndizoona zimenezi. Tili kunena ngati tikukalipa chifukwa chakuti zimenezi ndizokhumudwitsa. Ndikhulupilira kuti masiku ano anthu ali kuchita chigololo koma osadziœa.

Anthu amachita chigololo ngakhale m’mitima mwawo. Ife amene tinalengedwa ndi Mulungu timakhala padziko lino lapansi osadziœa kuti tili kuchita chigololo m’miyoyo yathu. Kupembedza milungu ina, ndi chigololo chauzimu chifukwa Ambuye ndi mwamuna wa anthu onse.

Mai uja amene anagwidwa akuchita chigololo, ndi munthu ngati ife tomwe ndipo analandira chifundo cha Mulungu monga momwe tinalandilira ife amene tinaomboledwa. Koma Afarisi achiphamaso aja anamuika pakati pawo ndi kumamuloza zala ngati kuti iwo anali oweruza, ndipo anafuna kumuponya miyala. Anafuna kuyamba kumunyoza ndi kumuweruza ngati kuti iwo anali anthu angwiro kapenanso kuti sanachiteko chigololo.

Akhristu anzanga, anthu amene amadzidziœa

okha kuti ndi odzala ndi uchimo, saweruza anzawo pa maso pa Mulungu. M’malo mwake, chifukwa iwo amadziœa kuti iwonso anali kuchita chigololo pa moyo wao wonse, analandira chisomo cha Mulungu chimene chinatiombola ife tonse. Anthu okhawo amene amadziœa kuti ndi ochimwa ndi amene ali onena kuti apulumuka pa maso pa Mulungu.

KODI NDANI AMENE AYENERA KULANDIRA CHISOMO CHA MULUNGU?

Kodi anthu osachimwa kapena amene

sanachiteko chigololo amalandiranso chisomo cha Mulungu kapena munthu amene amachita chigololo ndiye amalandira chisomo? Munthu amene amachita zimenezi ndi amene amalandira chisomo chochuluka cha chipulumutso. Anthu

Page 70: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

70 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

amene sangathe kudzithandiza, amene ali ofooka amalandira chipulumutso. Ndi amene amakhala m’chisomo cha Mulungu.

Ndani amalandira chisomo cha Mulungu?

Anthu osayenera

Anthu amene amaganiza kuti alibe machimo

sangapulumuke. Iwo angalandire bwanji chipulumutso cha Mulungu pamene alibe tchimo lakuti Mulungu wakhululukire?

Afarisi ndi alembi aja anagwira mai wachigololo uja ndikuika pakati pawo nayamba kufunsa Yesu, “Aphunzitsi mai uyu tampeza akuchita chigololo. Nanga inu mukuti bwanji? Chifukwa chiyani iwo anabwera ndi mai uja kwa Iye ndikumamuyetsa?”

Iwo anakhala ali kuchita chigololo nthaœi zambiri, koma anali kuyetsa ku muweruza mai uja

ndi kumupha kudzera mwa Yesu ndi kufuna ku madzudzula Yesu.

Yesu anadziœa zimene anthu aja ankaganiza, ndipo anali nazo zonse zokhudza maiyo. Motero anauza anthu aja kuti, “Amene sanachimweko chikhalire ayambe kumponya miyala maiyu.” Ndipo alembi ndi Afarisi aja anayamba kuchoka mmodzi mmodzi ndikusiya Yesu ndi mai uja.

Anthu amene anachoka aja ndi Afarisi ndi alembi, atsogoleri ampingo. Anatsala pang’ono ku muweruza mai uja amene anagwidwa ali kuchita chigololo ngati kuti iwo sanali anthu ochimwa.

Yesu anali kulalika za chikondi chake pa dziko la pansi. Iye anali mwini chikondi. Yesu anali kupatsa anthu chakudya, kuukitsa anthu akufa, anaukitsa mwana wa m’kazi wa masiye, anaukitsa Lazaro, analikuchilitsa anthu akhate ndi kuchita zozizwitsa kwa anthu osauka. Ndiponso anachotsa machimo aanthu onse nawapatsanso chipulumutso.

Yesu amatikonda. Iye ndi wamphamvu zonse amene akhoza kuchita chilichonse, koma Afarisi

Page 71: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

71 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

ndi alembi anali kumuona Yesu ngati m’dani wawo. Nchifukwa chake anabwera ndi mai wachigololo uja kwa iye kuti a muyetse.

Iwo anafunsa Yesu kuti, “Aphunzitsi, m’malamulo a Mose amanena kuti munthu wotereyu aphedwe. Nanga inu mukuti chiyani?” Pamenepa iwo anali kuganiza kuti Yesu awalamula kuti amponye miyala. Chifukwa chiyani? Ngati tikadaweruzana molingana ndi malamlo a Mulungu, ndiye kuti anthu onse amene amachita chigololo akanaphedwa mosapatula.

Anthu onse ayenera kuponyedwa miyala ndipo anthu onse ayenera kupita kugahena. Mphotho ya uchimo ndi imfa. Koma Yesu sanauze anthu aja kuti amponye miyala mai uja m’malo mwake anati, “Pakati pa inu, amene sanachimweko chikhalire ayambe kumponya miyala maiyu.”

Nchifukwa chiyani Mulungu anatipatsa

ndime 613 za Malamulo?

Kuti tidziwe kuti ndife anthu ochimwa

Malamulo amationetsa m’kwiyo wa Mulungu.

Mulungu ndi oyera chimodzimodzinso Malamulo ake. Malamulo oyera a Mulungu anabwera kwa ife m’ndime zokwana 613. Chifukwa chimene Mulungu anatipatsira ndime zimenezi ndi chakuti ife tidziœe kuti ndife anthu ochimwa; ndiponso kuti ife ndife olephera.

Malamulo amatiphunzitsa kuti ife tiyenera kuyang’ana kwa Mulungu kuti tipulumuke. Ngati sitinadziœe zimenezi ndikuganizira zimene zinalembedwa, tonse tinayenera kuponyedwa miyala monga mai wogwidwa ndi chigololo uja.

Alembi ndi Afarisi amene sanadziœe zoonadi zake za Malamulo a Mulungu anali kuganiza kuti

Page 72: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

72 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

amponye miyala mai uja mwinanso ndi ife tomwe. Ndani amene angaponye miyala pa mai osowa thandizo. Ngakhale anagwidwa ndi chigololo palibe munthu ndi mmodzi yemwe anali oyenera kumuponya miyala.

Ngati mai uja ndi ife tomwe tingaweruzidwe molingana ndi malamulo okha, tikanalandira chiweruzo choopsa. Koma Yesu anatipulumutsa ife anthu ochimwa, kumachimo athu, ndiponso ku chiweruzo cholungama. Kodi ndi ndani amene angapulumuke ngati titaweruzidwa potsatila malamulo onse olembedwa m’buku la malamulo? Aliyense wa ife ndi oyenera kukaponyedwa kugahena.

Koma alembi ndi Afarisi aja anadziœa malamulo monga m’mene analembedwera basi. Malamulo amagwiritsidwa ntchito molondola, amene akuweruza m’nzake ndi oyeneranso kuphedwa pamodzi ndi amene akuweruzidwa. Zoona ndi zakuti lamulo linapatsidwa kwa munthu kuti anthu azidziœa za kuchimwa kwawo, koma

anthu ali kuvutika chifukwa sakulimvetsa ndiponso amaligwiritsa ntchito molakwika.

Afarisi amasiku ano, monga Afarisi am’Baibulo, amadziœa malamulo monga m’mene analembedwera basi. Iwo ayenera kumvetsa bwino za chisomo, chilungamo, ndi choonadi cha Mulungu. ayenera kuphunzitsidwa za Uthenga wabwino wa chipulumutso kuti apulumuke.

Afarisi ananena kuti, “Malamulo akunena kuti munthu oteroyu aphedwe. Inu mukuti chiyani?” Anafunsa miyala ili m’manja mwao. Iwo analikuganiza kuti Yesu sanenapo kanthu. Iwo ankayembekezera Yesu kuti atenge myambo yawoyo.

Yesu akanaweruza molinga ndi Lamulo, nayenso akanaponyedwa miyala. Cholinga chao chinali chakuti awaponye miyala Yesu ndi mai uja. Yesu akanalamula kuti mai uja amponye miyala iwo akanayamba kunena kuti Yesu wanyoza malamulo a Mulungu. Ichi chinali chiwembu choipa kwambiri.

Page 73: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

73 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

Koma Yesu anaweramira pansi namalemba pansi ndi chala chake koma iwo anapitiliza ku mufunsa, “Kodi inu mukuti chiyani? Nanga muli kulemba chiyani pansipa? Tangoyankhani mafunso athuwa. Mukuti chiyani?” Iwo nkuti akuloza zala pa Yesu ndikumanena mowopseza.

Yesu anaweramuka nawauza anthu aja kuti pakati pawo ngati alipo munthu amene sanachimweko ayambe ndiye kumuponya miyala. Kenaka anaweramiranso pansi n’malemba pansi ndi chala chake. Pamenepo amene anamva zimenezi anadzitsutsa m’mitima mwawo nayamba kuchoka mmodzi mmodzi kuyambira akulu akulu mpaka ku ang’ono ang’ono. Pamenepo Yesu anatsala yekha, ndi mai uja ali chiimire.

AMENE SANACHIMWENSO PAKATI PANU PA AYAMBE NDIYE KUMPONYA MIYALA MAIYO

Kodi machimo analembedwa kuti?

Mkati mwa mitima yathu ndi m’Mabuku a zintchito

Yesu anawauza kuti, Amene chikhalire

sanachimweko pakati panupa ayambe ndiye ku mponya miyala maiyu. Ndipo Yesu anapitilizabe kulemba pansi. Pamene akulu akulu anayamba kuchoka. Akulu akulu amene anali atachimwa kwambiri anali woyamba kuchoka. Ang’ono ang’ono anachokapo pa malopo. Tiyerekeze kuti Yesu ali kuimilira pakati pathu, ndipo ife tili kuima mozungilira m’zimai. Yesu akanatiuza ife

Page 74: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

74 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

kuti amene sanachimweko ayambe ndiye kumponya miyala maiyu, kodi inu munatani?

Kodi Yesu anali kulemba chiyani pansi paja? Mulungu amene anatilenga amalemba machimo athu mumalo osiyana ambiri.

Poyamba, iye amalemba machimo athu m’kati mwa mitima mwathu. “Uchimo wa Yuda ndi wolembedwa ndi cholembera chachitsulo, chansonga ya mwala wa daimondi. Uchimowo walembedwa pa mitima yao ndiponso pa maguwa ao.”(Yeremiya 17:1).

Mulungu ali kulankhula nafe kudzera mwa Yuda amene ali woimilira m’malo mwathu. Machimo a munthu amalembedwa pansi pa mitima yathu ndi cholembera chachitsulo, ndi cha nsonga ya mwala wa daimondi. Machimo a menewa amalembedwa pa mitima yathu. Yesu anaweramira pansi nayamba kulemba pansi kuti anthu ndi ochimwa.

Mulungu amadziœa ife timachimwa ndipo analemba machimo pansi pa mitima yathu. Pomba,

analemba zintchito zathu, machimo amene timachita chifukwa ndife osalimba pa Lamulo. Pamene machimo ali kulembedwa m’mitima yathu, timadziœa kuti ndife anthu ochimwa pamene tiyang’ana pa malamulo. Chifukwa chakuti Mulungu analemba machimowo m’mitima mwathu, mu chikumbumtima chathu, timadziœa kuti ndife ochimwa pamaso pake.

Ndipo Yesu anaweramira pansi kachiœiri namalemba pansi. Mau a Mulungu akunena kuti machimo athu onse analembedwanso m’Mabuku a Zintchito pamaso pa Mulungu. (Chivumbulutso 20:12). Dzina lamunthu ndi machimo ake zinalembedwa m’Buku. Ndipo zinalembedwanso pansi pa m’tima wa munthu. Machimo athu analembedwa kaœiri m’Mabuku a Zintchito ndi pansi pa mitima yathu.

Machimo analembedwa pa m’tima wa munthu, wamng’ono kapena wamkulu. Nchifukwa chake analibe chilichonse chonena chokhudza machimo awo pamaso pa Yesu. Iwo amene anali kuyetsa

Page 75: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

75 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

kumponya miyala mai uja analibe chonena pa mau ake.

Ndi nthawi iti imene machimo athu amene a nalembedwa mmalo awiri amachoka?

Pamene ife tivomereza chipulumutso

cha madzi ndi mwazi wa Yesu m’mitima yathu

Koma pamene mulandira chipulumutso,

machimo anu onse m’Buku la Zintchito amafutidwa ndipo dzina lanu lidzalembedwa m’Buku la moyo. Anthu amene maina awo analembedwa m’Buku la Moyo azapita kumwamba. Ntchito zao zabwino, zimene anali kuchita m’dziko lino lapansi chifukwa cha Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake zinalembedwa

m’Buku la Moyo ndipo ndi zovomerezeka kumwamba.

Anthu amene apulumutsidwa kumachimo ao amaloœa ku dziko la muyaya. Machimo aanthu onse analembedwa m’malo aœiri. Motero palibe amene anganamize Mulungu. Palibe anthu amene sanachimwe kapena kuchita chigololo mum’tima mwake. Onsefe ndife anthu ochimwa ndipo ndi odetsedwa ndi uchimo.

Anthu amene sanalandire chipulumutso cha Yesu m’mitima mwao, palibe chimene angachite koma kulira ndi machimo. Sali osangalala ayi. Iwo ali ndi mantha ndi Mulungu, mantha pa maso pa Mulungu komanso mantha pa maso pa anthu anzao chifukwa cha machimo awo. Koma panthaœi imene iwo avomereza chipulumutso cha madzi ndi Mzimu Woyera m’mitima mwawo machimo awo onse amene analembedwa m’mitima mwao ndiponso m’Buku la zintchito amafafanizidwa. Ndiye kuti apulumuka ku machimo awo.

Page 76: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

76 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

Kumwamba kuli Buku la Moyo. Maina a anthu amene amakhulupilira mu chipulumutso cha madzi ndi Mzimu amalembedwa m’buku, ndipo adzalowa kumwamba. Amalowa kumwamba osati chifukwa chakuti iwo sanachimweko padziko lino lapansi, koma chifukwa chakuti apulumutsidwa ku machimo awo pakukhulupilira m’chipulumutso cha madzi ndi Mzimu. “Chachikulu nkuti munthu azikhulupilira.” (Aroma 3:27).

Akhristu anzanga, alembi ndi Afarisi anali ochimwa monga ngati m’kazi amene anagwidwa pa chigololo.

Nzoona anachita machimo ambiri chifukwa anazinamiza kuti iwo sali ochimwa.

Akulu a chipembezo anali kutsatira njira yovomerezedwa. Anali kubera mizimu, ndi miyoyo ya anthu. Anali kuphunzitsa anzawo mokhulupirika ngakhale iwo sanali wopulumutsidwa.

Palibe amene alibe uchimo molingana ndi malamulo. Koma munthu amakhala wolungama,

osati chifukwa sachimwa, koma chifukwa anapulumutsidwa ku machimo ake onse ndipo dzina lake lidalembedwa m’buku la umoyo. Chofunika ndichakuti munthu dzina lake lilembedwa m’buku la umoyo. Chifukwa munthu sangakhale womasuka ku uchimo, ayenera kupulumutsidwa.

Ngati m’zalandiridwa kumwamba ndikofunika kuti mukhulupirire kapena ayi. Ngati mulandira chisomo cha Mulungu kapena ayi ndikofunika kuti mulandire chipulumutso kudzera mwa Yesu. Kodi chinachitika ndi chiyani kwa m’kazi amene anagwidwa? Iye anaima pamenepo maso ali otseka chifukwa anadziœa kuti ayenera kufa. Ndizoona anali kulira chifukwa cha mantha ndiponso kuonetsa kutembenuka. Anthu anaonetsa chilungamo chawo pamene anazolika nkhope zawo pansi.

“Aa, Mulungu, ndichoyenera kuti ndife. Chonde landirani m’zimu wanga mumanja anu, ndipo mundichitire chifundo. Chonde ndichitireni

Page 77: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

77 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

chifundo, a Yesu.” Anachonderera kwa Yesu chifukwa cha chikondi chachipulumutso. “Mulungu, ngati mundiweruza ndiweruzidwa, ndipo ngati munena kuti ndilibe uchimo apo machimo anga azafafanizika. Zonse zili ndi inu.” Anali kunena zinthu zonsezi. Zonse zinasiidwa mumanja mwa Yesu.

M’kazi amene anamubweretsa kwa Yesu sananene kanthu, “Ndinachimwa, chonde ndikhululukireni ndinalakwa ndinachita chigololo.” Anatero, chonde ndikhululukireni machimo anga. Ngati mungandiombole ku machimo anga, ndidzapulumutsidwa. Ngati si mutero ndipita kugehena. Ndikufuna chiombolo chanu. Ndikufuna chikondi cha Mulungu, ndipo ndikufuna inu kuti mundichitire chifundo. Anatseka maso ake ndi kuvomereza machimo ake.

Yesu anamufunsa anati, “Kodi amene amakutsutsa ali kuti? Kodi palibe amene akutsutsa?” Ndipo Yesu ananena ndi iye, “Ngakhale inenso sindingakutsutse.” Yesu

sanamutsutse chifukwa anachotsa kale machimo ake kudzera mu ubatizo wake mu mtsinje wa Yolodani, ndiponso anali oomboledwa kale. Tsopano, Yesu, osati m’kazi, anayenera kuweruzidwa chifukwa cha machimo ake.

IYE ANATI, NGAKHALE INENSO SINDIKUTSUTSA

Kodi anatsutsidwa ndi Yesu?

Ayi

M’kazi anadalitsidwa ndichipulumutso cha

Yesu. Anaomboledwa ku machimo ake onse. Ambuye athu Yesu akutiuza kuti anachotsa machimo athu onse, ndipo ndife olungama.

Akutiuza choncho ife kudzera muBaibulo.

Page 78: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

78 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

Anamwalira pa mtanda kuti alipire machimo athu onse, amene anachotsa kudzera mu ubatizo wake mu mtsinje wa Yolodani. Akutiuza momveka bwino kuti anatiombola onse amene akhulupilira mu chiombolo cha ubatizo ndi chiweruzo cha pamtanda. Onse aife tifuna mau a Yesu ndipo tikufuna kutsatira mau amenewo. Apo ife tonse tidzadalitsidwa ndi chiombolo.

“Mulungu wanga, ndilibe sindili woyenera pamaso panu sindili woyenera. Ndilibe chokuonetsani koma machimo anga. Koma ndikhulupilira kuti Ambuye ndimupulumutsi. Anachotsa machimo anga onse mu mtsinje wa Yolodani ndi pa mtanda. Anachotsa machimo anga mu ubatizo ndi mwazi wake. Ndikhulupilira mwa inu, Ambuye.”

Umu ndi m’mene munapulumutsidwira. Yesu samatitaya ife ayi. Anatipatsa ufulu khukhala ana a Mulungu: kwa iwo amene akhulupilira chipulumutso cha madzi ndi mzimu, amaœachotsera machimo awo onse ndi kuœatcha

wolungama. Wokondedwa abwenzi. Amene adziœa

machimo ake ndi kumpempha Mulungu kuti amuchitire chifundo, amene akhulupilira chipulumutso cha madzi ndi Mzimu Woyera mwa Yesu amalandira madalitso achipulumutso kuchokera kwa Mulungu. amene ali ndi uchimo ayenera kupulumutsidwa. Iwo amene achimwa ngati sazindikira machimo awo sangadalitsidwe ndi chipulumutso.

Yesu anachotsa machimo adziko lonse lapansi (Yohane 1:29) ochimwa onse angapulumutsidwe ngati akhulupilira Yesu. Yesu anati kwa m’kazi, “Inenso sindikutsutsa”. Anati inenso sindikutsutsa chifukwa machimo ako onse ali pa ine. Anasenza machimo athu onse, anayenera kuweruzidwa chifukwa cha ife.

Page 79: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

79 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

FENSO TIYENERA KUOMBOLEDWA NDI YESU

Kodi chachikulu ndi chiti chikondi cha Mulungu kapena

chiwerunzo chake?

Chikondi cha Mulungu Afarisi, ndi miyala imene yinali mumanja

mwao, ndiponso ndi akulu a chipembezo alero, anamasulira kuti malamulo ndi opambana. Anali kuganiza kuti chifukwa malamulo amatiuza kuti tisachite chigololo, ndipo amene achimwa ayenera kuponyedwa ndi miyala mpaka kufa. Anali kuyang’ana akazi mowasilira ndipo anali kuyetsa kuti sakuchita chigololo. Sangaomboledwe kapena kupulumutsidwa. Afarisi ndi alembi anali anthu ochimwitsitsa mudziko lapansi. Sanali anthu

amene Yesu anaitana. Anthu awa sanamve Mau a Yesu, “Sindikutsutsa ine.”

M’kazi yekhayo amene anagwidwa pachigololo ndiyekhayo amene anamva mau a chisangalalo. Inunso ngati muli wokhulupirika pamaso pake, mukhoza kudalitsidwa ngati m’kazi uja. “Mulungu, ndinali kuchita chigololo masiku onse amoyo wanga. Zikuwonetsa ngati sindichita koma ndimachita masiku onse. Ndimachimwa kaœiri kaœiri masiku onse.”

Pamene timalandira malamulo ngati anthu ochimwa akufa ndikuyang’ana kwa Mulungu mowona chikudzindikira m’mene tilili, ndikunena, Mulungu wanga, ndine wochimwa. Chonde ndipulumutseni, Mulungu adzatidalitsa ndi chiombolo.

Chikondi cha Mulungu, cha madzi ndi Mzimu Woyera chinapambana chiweruzo cha Mulungu. “Inenso sindikutsutsa.” Iye sanatitsutse ife ndipo akuti, Inu ndinu aomboledwa. Ambuye athu Yesu ndi Mulungu wa chifundo. Anatichotsa ku

Page 80: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

80 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

machimo onse adziko lapansi. Mulungu wathu ndi Mulungu wachilungamo

ndipo ndi Mulungu wa chikondi. Chikondi cha madzi ndi Mzimu Woyera ndi chachikulu kusiyana ndi chiweruzo chake.

CHIKONDI CHAKE NDICHACHIKULU KUSIYANA NDI CHIWERUZO CHAKE

Chifukwa nchiyani anatiombola ife tonse?

Chifukwa chikondi chake ndi chachikulu kusiyana

ndi chiweruzo chake

Mulungu akanakahala kuti aumiriza chiweruzo

chake kuti akwanirise chilungamo chake akanawerudza anthu onse ochimwa ndi kuwaponya kugahena. Koma chifukwa chikondi cha Yesu ndi chachikulu chimene chinatipulumutsa kuchiweruzo, Mulungu anatuma Mwana wake yekha Yesu. Yesu anachotsa machimo athu onse pa iye yekha ndikulandira chiweruzo cholungama mumalo mwathu. Tsopano aliyense okhulupilira Yesu ngati Mpulumutsi wake amasanduka mwana wake ndipo amakhala wolungama. Chifukwa chikondi chake ndichachikulu kusiyana ndichiweruzo chake, anatiombola ife tonse.

Tiyenera kuthokoza Mulungu chifukwa samatiweruza ndi chiweruzo chake chokha ayi. Monga Yesu anaœauza alembi, Afarisi, ndi ophunzira, Mulungu amafuna chifundo ndi kumuzindikira iye, osati zopereka zathu. Anthu ena amapha ng’ombe kapena mbuzi masiku onse ndi kupereka chopereka kwa Mulungu ndi kupemphera, “Mulungu amandikhululukira

Page 81: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

81 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

machimo anga masiku onse.” Mulungu safuna zopereka zathu, koma chikhulupiliro chathu mukuomboledwa kwa mu madzi ndi Mzimu Woyera. Amafuna ife kuti tiomboledwe ndi kupulumutsidwa. Akufuna kutipatsa chikondi chake ndi kulandira chikhulupiliro chathu. Kodi nonsenu mukuona izi? Yesu anatipatsa chipulumutso.

Yesu amadana ndi uchimo koma ali ndi chikondi chozama pa anthu ake, amene analengedwa m’chifanizo cha Mulungu.

Iye anaganiza isanayambike konse nthaœi kutisandutsa ana ake ndipo anachotsa machimo athu onse ndi ubatizo komanso mwazi wake. Mulungu anatilenga ndi kutiombola, kutiveka Yesu, ndi kutisandutsa ana ake. Ichi ndi chikondi chimene Iye ali nacho pa ife, zolengedwa zake.

Mulungu akanatiœeruza molingana ndi lamulo lake, ife anthu ochimwa, tikadafa tonse. Koma anatipulumutsa kudzera mu ubatizo ndi chiœeruzo cha Mwana wake pa Mtanda. Kodi inu

mumakhulupilira? Tiyeni tione m’Chipangano Chakale.

ARONI ANASANJIKA MANJA PA MUTU WA MBUZI YOTAMANGITSIDWADWA

Kodi adapereka machimo a Aisraele ku mbuzi ya

moyo ngati woimirira wao ndi ndani?

Wansembe wa mkulu

Machimo onse adziko lino la pansi

anachotsedwa ndi kudzoza kwa m’Chipangano Chakale ndiponso ubatizo wa m’Chipangano Chatsopano. M’chipangano Chakale, machimo onse achaka ndi chaka anali kuperekera nsembe

Page 82: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

82 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

kudzera kwa wansembe wamkulu, amene ankasanjika manja pa mutu pa mbuzi yopanda chilema.

“Tsono Aroni asanjike manja ake pa mutu pa mbuziyo, ndipo aulure pa mbuziyo zochimwa zonse za Aisraele pamodzi ndi kusamvera kwawo konse, ndiye kuti machimo ao onse. Machimowo aœaike pa mutu pa mbuzi ija, ndipo munthu amene adamusankhiratu aithamangitsire ku chipululu mbuziyo.” (Levitiko 16:21).

Umu ndi m’mene anayanjanirana mumasiku a Chipangano Chakale. Kuomboledwa ku machimo atsiku ndi tsiku, ena anapereka mwana wankhosa kapena mbuzi yopanda chilema mu kachisi kuti apereke nsembe pa guwa la nsembe. Anaika manja ake pa mutu pa chopereka, ndi machimo awo anali kupita mu nsembe. Nsembeyo inapedwa ndipo magazi ake wansembe anaœaika pa nyanga za guwa la nsembe.

Makona anayi aguwa la nsembe anali ndi nyanga zinayi. Nyanga zimenezi zinali kuimirira

ntchito za mabuku anayi amene anafotokozedwa mubuku la Chivumbulutso 20:12. Magazi osala anali ku œawaza pansi, nthaka yinali kuimirira mitima ya anthu chifukwa anthu anachokera ku fumbi. Anthu anali kuchotsa machimo awo munjira yimeneyi masiku ndi masiku.

Koma sanali kupereka nsembe yochotsa machimo masiku onse. Mulungu anaœalola kupereka nsembe yochotsa machimo onse pa chaka kamodzi. Ili linali tsiku la khumi la mwezi wa chisanu ndi kaœiri, latsiku lansembe yochotsa machimo. Patsikulo, onse oimirira anthu a Aisraele, m’kulu wa nsembe, anabweretsa mbuzi ziœiri ndikuika manja ake pa mitu ya mbuzizo kuti zitenge machimo onse aanthu ndikuzipereka kwa Mulungu kuti yikhale nsembe yochotsera machimo aanthu a Aisraele.

“Aroni anasanjika manja ake pa mutu wa mbuzi ya moyo, ndikulapa machimo onse aanthu a Aisraele, uchimo wao wonse, mokhuzana ndi machimo anaperekedwa pa mutu wa mbuzi.”

Page 83: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

83 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

Mulungu anasankha Aroni, mukulu wa nsembe wa Israeli kuimira anthuœa. M’malo moti aliyense asanjike manja pa nsembe, mukulu wa nsembe, anali kuimirira anthu onse, analikusanjika manja pa mutu wa mbuzi ya moyo ndi kuchotsa machimo aanthu kwa chaka chonse.

Amanena machimo onse a Aisraele pamaso pa Mulungu, “Mulungu, ana anu Aisraele achimwa. Tinapempheza mafano, tinaphwanya mabuku onse a malamulo, ndikutchula dzina lanu pa chabe, tipanga milungu ina ndi kuikonda koposa inu. Sitisunga tsiku la Sabata kukhala loyera, sikulemekeza makolo athu, timapha, tikuchita chigololo ndi kuba. Tikuchita nsanje ndi kukangana.”

Anawerenga machimo onse. “Mulungu, ngakhale anthu aIsraele kapena ine palibe amene anasunga ngakhale limodzi mwa malamulo anu, kuti ndiomboledwe kumachimo onse awa, ndinaika manja anga pa mutu wa mbuzi ndipo inatenga machimo anga onse.” M’kulu wa nsembe

anaika manja pa chopereka mumalo mwa anthu onse ndi kupereka machimo onse pa mutu wa mbuzi yachopereka. Mwambo wokhazikitsa, kapena kusanjika manja kutanthauza ‘kudutsa’ (Levitiko 1:1-4; 16:20-21).

Kodi kugwirizana kunakwamiritsidwa

bwanji mu Chipangano Chakale pakati pa anthu

ndi Mulungu?

Kudzera mu kusanjika manji pa mutu wa chopereka

chochotsa machimo Mulungu anapereka mwambo wachopereka

chochotsera machimo kwa anthu Aisraele kuti itenge machimo chopanda machimo ndipo kuti choperekachi chiyenera kufa m’malo mwa anthu. Patsiku la mwambo, mopha chopereka chochotsa

Page 84: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

84 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

machimo, magazi ake amapitanawo m’kati munyumba ya Mulungu pamalo oyera ndikuwaza mwaziwo pa mpando wa chifundo kasanu ndi kaœiri. Choncho Aisraele anachita mwambo woœayanganitsa ndi Mulungu chaka chonse patsiku la khumi la mwezi wa chisanu ndi kaœiri.

Wansembe wam’kulu adali kuloœa kumalo oyera opatulika kupereka nsembe, koma anthu adali kukhala kunja ndi kumvetsera mau a belu limene lidali m’manja a m’kulu wansembe kuti aimbe kasanu ndi kaœiri pamene magazi anali kuœazidwa pa mpando wachifundo. Anthu anali kusangalala kuti machimo awo onse akhululukidwa. Kumveka kwa mau abelu anali mau a chisangalalo cha uthenga wabwino.

Sizoona kuti Yesu anakonda anthu ena ndi kuœaombola okhao. Yesu anachotsa machimo onse adziko lapansi pa nthaœi yimodzi pa ubatizo wake. Anali kufuna kutipulumutsa ife tonse pa nthaœi yimodzi. Machimo aanthu sangaomboledwe tsiku lililonse; anaomboledwa pa

nthaœi yimodzi. Muchipangano Chakale nsembe yochotsa

machimo yinali kuperekedwa pa nthaœi yodzodza ndi kupereka nsembe yochotsa machimo. Aroni adali kusanjika manja pa mutu wa mbuzi pamaso aanthu ndi kunena machimo onse amene anthu analikuchita kwa chaka chonse. Adali kupereka machimo onse ku mbuzi pamaso pa anthu onse. Kodi machimo aanthu ali kuti tere? Onse anaperekedwa ku mbuzi.

Mbuzi anaitenga kwina ndi muthu woyera. Mbuzi yinanyamula machimo onse aa Israele, ndipo anaitsogolera ku chipululu kumene kunali madzi ndi udzu. Mbuzi, yinali kuyenda yenda m’chipululu dzuœa likuwomba ndipo pambuyo pake inafa. Mbuzi imafa chifukwa cha machimo aa Israele.

Ichi ndi chikondi cha Mulungu, chikondi cha chiombolo. Umu ndi m’mene anali kuchotsera machimo a chaka chonse m’masiku amenewo. Koma ife tikukhala mu nthaœi ya Chipangano

Page 85: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

85 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

Chatsopano. Papita zaka pafupi 2000 pamene Yesu anabwera padziko lapansi. Anabwera kukwaniritsa ulosi umene anachita mu Chipangano Chakale. Anabwera ndi kutiombola ku machimo aanthu onse.

KUOMBOLA IFE TONSE

Kodi tanthauzo la Yesu ndi chiyani?

Mupulumutsi amene a dzapulumutsa anthu

ake ku machimo Tiœerenge Mateo 1:20-21 “Akadali

m’malingariro ameneœa m’ngelo wa Ambuye anamuonekera m’maloto, nanena kuti, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kutenga Maria kuti

akhale m’kazi wako. Pakati ali napopa mpa Mzumu Woyera. Adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu, pakuti ndiye amene adzapulumutsa anthu ake kumachimo awo.” (Mateo 1:20-21).

Atate athu akumwamba anabwereka thupi la Maria amene sanakumanepo ndi mwamuna kuti atumizire mwana wake padziko lapansi kutichotsa machimo athu. Anatuma m’ngelo kwa Maria ndi kunena kuti, “Udzakhala ndi pakati ndipo udzabala mwana wamwamuna ndipo adzatchedwa dzina lake Yesu.” Kutanthauza kuti mwana wa Maria adzakhala Mupulumutsi. Yesu Khristu ndiko kuti Mupulumutsi wa anthu ake, munjira yina, ndi Mupulumutsi.

Njira yimene Yesu anachotsera machimo aanthu ndi ubatizo wake mum’tsinje wa Yolodani. Anabatizidwa ndi Yohane Mubatizi ndipo machimo onse aanthu anadza pa Iye. Tiœerenge Mateo 3:13-17.

““Pa nthaœi yomweyo Yesu anafika kwa

Page 86: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

86 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

Yohane ku m’tsinje wa Yolodani, kuchokera ku Galilea, kuti Yohane am’batize. Koma Yohane nayetsa kukana nati, “Bwanji mukubwera kwa ine? Ndine amene ndiyenera kubatizidwa ndi inu.” Koma Yesu anamuyankha kuti, pakali pano, lola, chifukwa pakutero tichita chonse zimene Mulungu afuna.” Apo Yohane analola. Yesu atangobatizidwa, anabvuuka m’madzimo. Pomwepo kuthambo kunatsekuka, ndipo anaona Mzimu wa Mulungu alikutsika ngati nkhunda ndikutera pa iye. Ndipo kuthamboko kunachokera mau akuti, “Uyu ndiye mwana wanga amene ndim’konda, ndimakondwera naye kwambiri.””

Yesu anapita kwa Yohane Mabatizi kuti atiombole ku machimo athu onse. Iye adayenda pa madzi ndi kumiza mutu wake pamaso pa Yohane. “Yohane, ndibatize tsopano. Umu ndi m’mene tiyenera kuchitira zimene Mulungu akufuna. Monga munthu amene ayenera kuchotsa machimo ao ndiyenera kuchotsa machimo ao pakubatizidwa. Ndibatize tsopano lino! Ndithu vomera!”

Umu ndi m’mene tiyenera kuchitira zimene Mulungu akufuna. Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Panthaœi yomweyo anakwaniritsa chifuniro chonse cha Mulungu.

Umu ndi m’mene iye adachotsera machimo athu. Machimo anu onse anaperekedwa kwa Yesu. Kodi mukumvetsa?

Khulupilirani chiombolo cha ubatizo wa Yesu ndi Mzimu Woyera kuti mupulumutsidwe.

Kodi chilungamo cha Mulungu chinakwaniritsidwa bwanji?

Kudzera mu ubatizo wa Yesu

Poyamba Mulungu adalonjeza Aisraele kuti machimo ao onse adzafafanizidwa pakusanjika manja ndi nsembe yoperekera machimo. Koma monga kunali kosatheka kuti aliyense asanjike manja ake pa mutu pambuziyo, Mulungu

Page 87: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

87 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

anasankha Aroni kuti akhale wansembe wam’kulu kuti azipereka nsembe m’malo mwa anthu onse. Motero ankapereka machimo ao achaka ndi chaka pa nsembe yoperekera machimo kamodzi. Iyi ndi nzeru ndiponso Mphamvu ya chiombolo. Mulungu ndi wanzeru ndiponso wodabwitsa.

Iye anatumiza Mwana wake kudzapulumutsa dziko lathuli. Motero nsembe ya machimo athu inali itakonzedwa. Koma tsopano kudayenera kuti kukhale woyimirira anthu onse amene akanasanjika manja pa mutu pa Yesu ndi kupereka machimo adziko lapansi kwa Iye. Woyimirira ameneyu ndi Yohane Mabatizi, wansembe wam’kulu womaliza wa anthu.

Monga Mau a Mulungu anenera pa Mateo 11:11 “Mwa anthu onse amene anabadwa pansi pano, palibe ndi m’modzi yemwe woposa Yohane Mbatizi.” Iye ndi yekhayo amene anaimirira anthu onse Yesu asanabwere. Mulungu anatuma Yohane Mbatizi kuti akhale woyimirira anthu onse ndi zolengedwa zonse ndipo anabatiza Yesu ndi kuika

machimo onse adziko lapansi pa Iye. Kodi ngati anthu 6 biliyoni amene ali pansi

pano atapita kalero nasanjika manja awo pa mutu pa Yesu ndi kuika machimo awo pa Iye, chingachitike n’chiyani pa mutu wakewo? Ngati anthu opitilira 6 biliyoni padziko lonse lapansi angasanjike manja pa mutu wa Yesu, sichingakhale chinthu chabwino. Anthu amaganizo oipa akhoza kuyamba kusanjika manja awo ndi mphamvu kotero kuti tsitsi lake likhoza kuchoka. Mulungu mwa nzeru zake, anasankha Yohane kukhala wotiimirira ndi kupereka machimo adziko lonse lapansi pa Iye kamodzi kokha.

M’buku la Mateo 3:13-17 Mau a Mulungu ali kunena kuti, “Yesu adachoka ku Galilea kubwera kwa Yohane ku M’tsinje wa Yolodani, kuti Yohaneyo amubatize.” Nthaœi imeneyi nkuti Yesu ali ndi zaka makumi atatu. Yesu anaumbalidwa patapita masiku asanu ndi atatu kuchokera patsiku limene iye anabadwa. Zambiri zimene Yesu anachita, kuchokera pa nthaœi imene anabadwa

Page 88: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

88 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

kufikira zaka makumi atatu sizinalembedwe. Mubuku la Chipangano Chatsopano la Mateo

3:13-15 akuti, “Panthaœi yomweyo Yesu anafika kwa Yohane ku m’tsinje wa Yolodani, kuchokera ku Galilea kuti Yohane ambatize. Koma Yohane anayetsa kukana nati, “Bwanji mukubwera kwa ine? Ndine amene ndiyenera kubatizidwa ndi inu.” Koma Yesu anamuyankha kuti, “Pakali pano, lola, chifukwa pakutero tichita zonse zimene Mulungu afuna.”” Apo Yohane analola. Kodi amene akuimirira anthu ndi ndani? Yohane M’batizi. Nanga kodi amene akuimirira kumwamba ndi ndani? Oimirira kumwamba ndi dziko lapansi anakumana. Nanga wam’kulu ndani? Ndizoona, ndioimirira kumwamba.

Yohane Mbatizi, anazipereka kunena choona kwa akulu akulu a chipembezo pa masiku ake. “Ana anjoka inu! Lapani!” Mwadzidzizi anazichepeka pa maso pa Yesu. “Ndiyenera kubatizidwa ndi inu, inu mukubwera kwa ine?”

Yesu anamuyankha kuti, pakali pano, lola,

chifukwa pakutero tichita zonse zimene Mulungu afuna. Yesu anabwera padziko lapansi kukwaniritsa zimene Mulungu afuna ndipo zinachitikadi pamene anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi.

“Anamulola iye. Yesu atangobatizidwa anavuuka m’madzimo. Pomwepo kuthambo kunatsekuka, ndipo anaona Mzimu wa Mulungu alikutsika ngati nkhunda ndi kutera pa Iye. Ndipo kuthamboko kunachokera mau akuti, “Uyu ndiye mwana wanga amene ndimukonda. Ndimakondwera naye kwambiri.””

Izi ndi zimene zinachitika pamene anabatizidwa. Khomo lakumwamba linasekuka pamene anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi anatenga machimo onse adziko lapansi.

“Kuyambira panthaœi ya Yohane Mbatizi mpaka tsopano anthu alikulimbana ndi Ufumu wa kumwamba, ndipo ochita chamuna alikuyetsa kuulanda.” (Mateo 11:12).

Tsono kumwambako kudamveka mau akuti,

Page 89: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

89 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

“Uyu ndiye Mwana wanga wa pam’tima. Ndimakondwera naye kwambiri.” Izi ndi zimene zinaachitika pamene Yesu adaali kubatizidwa. Khomo la kumwamba lidatsekuka pamene Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi ndipo anachotsa machimo onse adziko lapansi. “Kuyambira pa nthaœi ya Yohane Mbatizi mpaka tsopano anthu akhala akulimbana ndi Ufumu wa kumwamba, ndipo ochita chamuna ndiwo amene akuulanda” (Mateo 11:12).

Aneneri onse ndi malamulo a Mulungu anali kulosera mpaka nthaœi ya Yohane Mbatizi. Kuyambira nthaœi ya Yohane Mbatizi mpaka tsopano anthu akhala akulimbana ndi Ufumu wakumwamba ndipo ochita chamuna ndiwo amene akuulanda Aliyense wokhulupilira mu Ubatizo wa Yesu akhoza kuloœa mu Ufumu wa kumwamba popanda kusankha.

“INE SINDILI KUKUWERUZANI”

Kodi nchifukwa chiyani Yesu anaweruzidwa pa

mtanda?

Ndi chifukwa chakuti iye ananyamula machimo

onse Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi

ndikuchotsa machimo onse a dziko lapansi. Ndipo nthaœi zina adauza mai kuti, “Ine sindili kukuweruzani.” Iye sanaweruze mai uja chifukwa machimo onse adziko lapansi anachotsedwa pa m’tsinje wa Yolodani ndipo Yesu ndi amene anaweruzidwa osati mai uja.

Yesu Khristu anatenga machimo onse a dziko lapansi. Ndipo tikhoza kuona mantha amene anali nawo pa ululu umene anali kudzaumva pa mtanda chifukwa “Mphotho ya uchimo ndi imfa.” Iye

Page 90: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

90 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

anapemphera kwa Mulungu katatu pa Phiri la Olivi kuti Mulungu amchotsere chiweruzo chakecho. Yesu anali ndi thupi longa la munthu wina aliyense, choncho kunali koyenera kuti iye achite mantha ndi ululu. Yesu adayenera kukhetsa mwazi kuti akwaniritse chiweruzo.

Monga nsembe za uchimo Mchipangano Chakale zinali kukhetsa mwazi kuti machimo afafanizidwe, Iye anayenera kupereka nsembe ya machimo athu pa Mtanda. Iye anali atatenga kale machimo onse adziko lapansi koma tsopano kunali koyenera kuti Iye apereke moyo wake kuti tipulumitsidwe. Iye anadziœa kuti ayenera kuweruzidwa pa maso pa Mulungu.

Yesu analibe uchimo mum’tima mwake. Koma pamene Iye anatenga machimo athu onse kudzera mu Mwana wake.

“Inenso sindikuzengani mlandu, kapena kukuweruzani.” Machimo athu onse, ochita mwadala kapenanso ochitika mwa tsoka, odziœika anayenera kuti aweruzidwe ndi Mulungu.

Mulungu sanalange ife, koma analanga Mwana wake amene ananyamula machimo athu onse mu ubatizo wake. Mulungu sanafune kulanga ochimwa chifukwa cha chifundo ndi chikondi chake. Ubatizo ndi mwazi wake pa Mtanda chinali chikondi chimene iye anatipulumutsa nacho. “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kwambiri kotero anapereka Mwana wake umodzi yekha, kuti aliyense okhulupilira iyeyo asataike koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:16).

Ndani ondalitsidwa Kwambiri?

Osachimwa konse.

M’menemu ndi m’mene timadziœila za

chikondi cha Mulungu. Yesu sanamuzenge mlandu mai uja amene anagwidwa ndi chigololo.

Mulungu amatiuza za chisangalalo mbuku la Aroma 4:7 “Ngodala anthu amene Mulungu

Page 91: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

91 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

adawakhululukira machimo awo, amene Iye adawafafanizira machimo awo.” Tonse timachimwa kufikira nthaœi ya kufa kwathu. Ndife anthu osachitila Mulungu ulemu ndipo ndife anthu osakwanira pa maso pake. Timapitiriza kuchimwa ngakhale kuti timadziœa malamulo ake. Ndife anthu ofooka pa maso pa Mulungu.

Koma Mulungu anatipulumutsa kupyolera mu ubatizo ndi mwazi wa Mwana wake wobadwa yekha ndipo amatiuza inu ndi ine kuti sindifenso anthu ochimwa, koma ndi olungama pa maso pake. Mulungu amatiuza kuti ndife ana ake.

Uthenga Wabwino wonena za madzi ndi Mzimu ndi Uthenga Wabwino wa chiombolo. Kodi inu mumakhulupilira zimenezi? Anthu amene amakhulupilira uthenga umenewu Mulungu amawatcha kuti ndi ana ake, olungama ndi oomboledwa. Kodi munthu osangalala kwambiri pa dziko lonse la pansi ndi uti? Ndi munthu amene amakhulupilira ndipo wapulumutsidwa. Kodi inu mwapulumutsidwa.

Kodi Yesu anasiyako machimo anu? Iyayi, iye anachotsa machimo athu onse mu ubatizo wake. Khulupilirani zimenezi. Khulupilirani

kuti mupulumuke ku machimo anu. Tatiyeni tiwerenge Yohane 1:29.

KUNGO KHALA NGATI MMENE TIMASESELA NDI CHISESO

Kodi Yesu anachotsa machimo angati?

Machimo onse a dziko lapansi

“M’mawa mwake Yohane adaona Yesu

akubwera kwa iye, ndipo adati “Suuyu Mwana wa Nkhosa wa Mulungu uja, wochotsa machimo aanthu a pa dziko lonse lapansi.”” (Yohane 1:29)

Page 92: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

92 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

“Suuyu Mwana wa Nkhosa wa Mulungu uja wochotsa machimo aanthu onse pa dziko lapansi.”

Yohane Mbatizi anatula machimo adziko lonse lapansi pa Yesu ku M’tsinje wa Yolodani. M’mawa mwake iye adachitira umboni kuti Yesu ndi Mwana wa Nkhosa wa Mulungu amene achotsa machimo adziko la pansi. Iye ananyamula machimo athu pa mapewa pake.

Machimo onse adziko lapansi atanthauza kuti machimo onse amene anthu amachita pa dziko la pansi kuchokera pa nthaœi imene Mulungu adalenga zinthu mpaka kumathero. Zaka pafupifupi zikwi lapansi ndi kutipulumutsa. Monga Mwana wa Nkhosa wa Mulungu, anachotsa machimo athu ndikulangidwa chifukwa cha ife.

Tchimo lililonse limene munthu achita, linaperekedwa kwa Yesu. Ndi iye anakhala mwana wa Nkhosa wa Mulungu amene anachotsa machimo onse adziko lapansi.

Yesu adabwera pa dziko lino la pansi monga

munthu wodzichepetsa, monga munthu amene adaali ndi mphamvu yakuchotsa machimo awanthu wonse. Ife timachimwa chifukwa ndife anthu ofooka, chifukwa ndife oipa, chifukwa ndi mbuli ndiponso chifukwa ndi anthu olephera. Machimo onsewa anasezedwa ndi kuikidwa pa mutu pa Yesu mu ubatizo wake ku M’tsinje wa Yolodani. Mpaka ife anapachikidwa pa mtanda chifukwa cha machimo amene ife tidampatsa. Ndipo mkucha wake iye anauka kwa kufa.

Monga Mpulumutsi wa anthu onse ochimwa, monga mgonjetsi monga oweruza, iye amakhala pa dzanja la manja la Mulungu Atate. Iye safunika kutipulumutsanso ayi chifukwa anatipulumutsa kale ife tingokhulupilira kuti tipulumutsidwe. Moyo wosatha uli kutiyembekeza ife amene timakhulupilira, ndipo chionongeko chili kuyembekezera anthu osakhulupilira. Palibe chimene ife tingachite.

Yesu anapulumutsa inu nonse. Ndinu anthu osangalala kwambiri pa dziko lapansi. Machimo

Page 93: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

93 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

onse amene inu mudzachite kutsogolo chifukwa cha kufooka kwanu, Yesu anachotsa machimo onsewo. Inde anachotsadi!

Kodi kuli machimo amene Yesu anasiyako m’kati mwa m’tima wanu? -Iyayi.-

Kodi Yesu anachotsa machimo anu onse? -Inde.-

Anthu onse ali chimodzimodzi. Ndipo palibe munthu amene ndi oyera kuposa mnzake. Koma monga anthu ambiri ndi achiphamaso, amaganiza kuti alibe uchimo. Koma kunena zoona nawonso ndi ochimwa. Dziko lino lapansi lili ngati malo achonde amene tchimo limakula bwino.

Pamene azimayi asesa m’nyumba zao amapaka milomo yao m’nkhwala ofiilitsa, kuzola mafuta pa nkhope zao, kukonza tistsi lawo, kuvala zovala zao zokongola ndi kuvala nsapato zazitali…. Amuna amapita ku malo ometera kukameta tsitsi lawo, kudzikongoletsa, kuvala malaya ao abwino, matao abwino ndi kupukuta nsapato zao.

Koma ngakhale aoneke ngati ana amfumu

m’kati mwawo ali ngati nsanza, zopanda ntchito. Kodi ndalama zimapatsa munthu chisangalalo?

Kodi umoyo wabwino umapanga munthu kukhala osangalala? Iyayi. Chiombolo chokha ndi chimene chimamupanga munthu kukhala wosangalala. Komabe ngakhale munthu akhale osangalala m’maonekedwe, ngati ali ndi machimo mu m’tima mwake alibe chisangalalo. Iye amakhala mwa mantha kuopa chiweruzo.

Munthu amene wapulumutsidwa amakhala wokondwa ngati mkango ngakhale avale nsanza. Mulibe machimo mum’tima mwake. “Zikomo Ambuye, mudapulumutsa wochimwa monga ine, mudachotsa machimo anga onse. Ulemelero ukhale kwa Mulungu.”

Munthu amene wapulumutsidwa, zoonadi ndi munthu wosangalala. Munthu amene wadalitsidwa ndi chisomo cha Mulungu ndiye munthu wokondwadi.

Monga Yesu Mwana wa Nkhosa wa Mulungu wochotsa machimo onse adziko lapansi

Page 94: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

94 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

watichotsera machimo athu onse, ndipo tilibenso machimo. Iye anatsiliza ntchito yotipulumutsa pa Mtanda. Machimo athu onse, kuphatikizapo anu ndi anga ali kutchulidwanso machimo adziko la pansi, choncho tonse tinapulumutsidwa.

CHIFUKWA CHA CHIFUNIRO CHA MULUNGU

Kodi tili ndi uchimo m’mitima yathu mwa

Yesu Khristu?

Ayi, tilibe Okondedwa abwenzi, m’kazi amene anagwidwa

pa chigololo amakhulupilira mau a Yesu ndipo anapulumutsidwa. Nkhani yake yinalembedwa mu Baibulo chifukwa anadalitsidwa ndi chiombolo.

Koma onama aja alembi ndi Afarisi anamuthawa Yesu.

Ngati mukhulupilira Yesu, ndi kumwamba, koma ngati m’musiya Yesu ndi wakugahena. Ngati mukhulupilira mu ntchito zake, zikufanana ndi kumwamba, koma ngati simukhulupilira ntchito zake zikufanana ndi kugahena. Chiombolo sintchito ya munthu iye yekha, ndi chipulumutso cha Yesu.

Tiwerenge mubuku la Aheberi 10. “Malamulo a Mose ndiwo chithunzithunzi chabe cha madalitso amene analikudzabwera, osati madalitso enieniwo. Nsembe zimodzimodzi zimaperekedwa kosalekeza chaka ndi chaka. Nchifukwa chake malamulowo sangathe konse mwa nsembezo kuwasandutsa angwiro anthu obwera kwa Mulungu. Anthu opembedza Mulungu aja akadayeretsedwa kwathunthu, sibwenzi m’tima wawo ulikuœatsutsabe, ndipo akadaleka kumapereka nsembe. Koma monga zililimu, nsembezo zimakumbutsa anthu za machimo awo

Page 95: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

95 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

chaka ndi chaka. Magazi ang’ombe zamphongo ndi atonde sangathe konse kuchotsa machimo. Nchifukwa chake pamene Khristu anadza pansi pano, anati, ‘Inu Mulungu simunafune nsembe kapena chopereka, koma munandikonzera thupi. Nsembe zoocha kwathunthu ndiponso nsembe zoperekedwa chifukwa cha uchimo, simunakondwere nazo’. Tsopano ndinati, ‘Ndili pano Mulungu, kuti ndichite zimene mufuna, monga zinalembedwa za ine mubuku lamalamulo.’ Anena zimenezi ngakhale malamulo ndimo ananena kuti ziperekedwe. Koma pambuyo pake anati, ‘Ndili pano, Mulungu, kuti ndichite zimene mufuna.’ Motero Khristu anachotsa nsembe za mtundu zoyamba, kuti m’malo mwake aike nsembe ya mtundu wachiœiri. Chifukwa chakuti Yesu Khristu anachita zimene Mulungu anafuna kuti achite, ndife oyeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene iye anapereka kamodzi kokha” (Aheberi 10:1-10).

“Mwa chifuniro cha Mulungu” Yesu anapereka

moyo wake kuti achotse machimo athu onse pa nthaœi yimodzi ndi kuweruzidwa kamodzi ndi kukhala ndi moyo.

Choncho tinayeretsedwa. ‘Tinayeretsedwa,’ zinalembedwa kuti ntchito yinachitika kale. Chikutanthauza kuti kuomboledwa sichinthu choti tinganenetso kaœiri. Inu munayeretsedwa.

Aheberi 10:11-14 akuti, “Wansembe aliyense amakhala chiriri kutumikira tsiku ndi tsiku, ndipo amapereka nsembe yimodzi yimodzi mobwerezabwereza. Komabe nsembe zimenezi sizingathe konse kuchotsa machimo. Koma Khristu anapereka nsembe imodzi yokha yochotsera machimo onse. Nsembeyo njokwanira nthaœi zonse, ndipo ataipereka, anakakhala ku zanja lamanja la Mulungu. Kumeneko alikudikira tsono kuti Mulungu asandutse adani ake kukhala ngati poponderapo mapazi ake – mwa nsembe imodzi yomweyo wasandutsa angwiro kwamuyaya iwo amene Iye alikuwayeretsa.” (Aheberi 10:11-14).

Nonsenu munayetsedwa kwa muyaya. Ngati

Page 96: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

96 Chiombolo cha muyaya

◄ Zam'kati ►

mwachimwa mawa, muzakhalanso ochimwa kachiœiri? Kodi Yesu sanachotse machimo amenewo? Anachotsa. Iye anachotsa machimo am’tsogolonso.

“Mzimu Woyera yemwe atitsimikizira zimenezi. Poyamba Iye akuti, ‘Nalipangano limene ndidzachita nawo atapita masiku amenewo, akutero Ambuye: Ndidzaika malamulo anga m’mitima mwawo, ndipo ndidzaœalemba m’nzeru zawo.’ Ndipo akutins, “Sindidzakumbukiranso konse machimo awo ndi kusaweruzika kwao”” (Aheberi 10:15-18).

Mau akuti ‘kukhululukira’ akutanthauza kuti anatichotsera machimo onse adziko lapansi. Yesu ndi Mupulumutsi wathu. Mupulumutsi wanga ndi wanu. Tinapulumutsidwa chifukwa tinakhulupilira Yesu. Ichi ndi chiombolo cha Yesu ndipo ndi chisomo chachikulu ndi mphanso yayikulu yochokera kwa Mulungu. Inu ndi ine amene tinaomboledwa ku machimo ndife odalitsidwa koposa!

Page 97: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

◄ Zam'kati ►

ULALIKI WA CHISANU

Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera

machimo

Page 98: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

98 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

< Mateo 3:13-17 > “Pa masiku amenewo, Yesu adachoka ku

Galilea kubwera kwa Yohane ku Mtsinje wa Yolodani, kuti Yohaneyo a mubatize. Yohane poyesa kukana adati, “Ndine amene ndiyenera kubatizidwa ndi inuyo. Nanga mukubweranso kwa ine kodi?” Koma Yesu adamuyankha kuti, “Tsopano lino vomera, chifukwa ndi m’mene tiyenera kuchitira Mulungu akufuna.” Apo Yohane adavomera. Yesu atangobatizidwa, adatuluka m’madzimo. Pomwepo kuthambo kudatsekuka, ndipo adaona Mzimu wa Mulungu akutsika ngati nkhumba nkutera pa iye. Tsono kuthamboko kudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga wapamtima. Ndi makondwera naye kwambiri.””

KODI ALIPOBE MUNTHU AMENE ALI KUVUTIKA NDI MACHIMO?

Kodi ukapolo wathu wa uchimo unatah?

Inde

Ambuye Mulungu wathu anadula unyolo wa

machimo aanthu onse. Anthu onse amene alikulamulidwa ndi uchimo ndi akapolo. Chifukwa ndi chiombolo chake, Yesu anachotsa machimo onse ndikutisandutsa angwiro. Iye anachotsa machimo athu onse. Kodi alipobe munthu amene akadali kuvutika ndi machimo?

Tiyenera kuzindikira kuti nkhondo yathu yomenyana ndi machimo inatha. Sitidzalimbananso ndi uchimo ayi. Ukapolo wathu onse anatichotsera Mwana wa Mulungu. Mulungu adalipira machimo athu kupyolera mwa Yesu

Page 99: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

99 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

amene anatimasula kwa muyaya ku unyolo wa machimo athu.

Kodi inu mumadziœa kuchuluka kwa anthu amene amavutika ndi machimo ao? Izi zidayamba pa nthaœi ya Adamu ndi Eva. Anthu onse amavutika ndi machimo amene anatenga kwa Adamu.

Koma Mulungu anachita pangano limene linalembedwa mbuku la Genesis 3:15, ndipo panganolo linali lakuti Iye adzapulumutsa anthu onse ku machimo ao. Iye ananena kuti anthu onse adzapulumutsidwa ku machimo ao kupyolera mu nsembe imene ya Yesu imene adzaipereke mwa madzi ndi Mzimu. Ndipo nthaœi itakwana, Mulungu adatumiza Mpulumutsi Yesu amene anakhala pakati pathu.

Mulungu adalonjezanso kutuma Yohane Mbatizi patsogolo pa Yesu ndipo iye adasunga lonjezo lakelo.

M’buku la Marko 1:1-8 Mau a Mulungu akuti, “Uyu ndi Uthenga Wabwino wonena za Yesu

Khristu Mwana wa Mulungu. Udayamba monga mneneri Yesaya adalemba m’buku mwake kuti, “Mulungu akuti, Ndidzatuma wa mthenga wanga mtsogolo mwako kuti akakonzeretu njira iwe udzapitemo. Liu la munthu wofuula m’chipululu akunena kuti konzani mseu wodzapitamo Ambuye, ongolani njira zoti adzapitemo. Zimenezi zidachitikadi pamene Yohane Mbatizi adaafika ku chipululu, nayamba kulalika. Ankhauza anthu kuti, “Tembenukani m’tima, mubatizidwe, ndipo Mulungu adzakukhululukirani machimo anu.” Anthu ochokera ku dera lonse la Yudea ndi aku Yerusalemu ankadza kwa ine. Tsono ankati iwo akaulula machimo ao, iye nkumawabatiza mu m’tsinje wa Yolodani. Yohaneyo ankavala zovala za ubweya wa ngamira, ndipo ankamangira lamba wa chikopa m’chiuno. Chakudya chake chinali dzombe ndi uchi wa m’thengo. Kulalika kwake ankati, Pambuyo panga pakubwera wina wa mphamvu koposa ine, mwakuti ineyo ndine wosayenera ngakhale kuwerama nkumasula

Page 100: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

100 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

zingwe za nsapato zake. Ine ndili kukubatizani inu ndi madzi koma iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera.”

MBONI NDI MNENELI WA UTHENGA WABWINO, YOHANE MBATIZI

Kodi Yohane Mbatizi ndi ndani?

Wansembe wa mkulu ndi woimirira wa anthu onse

Anthu amene amakhulupilira mwa Yesu

anabatizidwa. Ubatizo utanthauza kuti; ‘kutsukidwa, kukwilirika, kumizidwa, kupereka machimo kwa Yesu.’ Pamene Yesu anabatizidwa, chifuniro cha Mulungu chinakwaniritsidwa.

Chilungamo ndi mau amene pa Chigiriki amati, ‘dikauzine’ ndipo mauwa amatanthauza ‘kukhala olungama, ndipo amatanthauzanso kuti ‘chinthu choyera kwambiri.’

Kubatizidwa kwa Yesu, kunapanga iye kukhala Mpulumutsi mwa njira yoyenera kwambiri. Choncho anthu amene amakhulupilira mwa Yesu amalandira chiombolo chake kuchokera kwa Mulungu pakukhulupilira mu ubatizo, Mtanda wake madzi ndi Mzimu Woyera.

Mu Chipangano Chatsopano, Yohane Mbatizi ndi wa nsembe wa m’kulu womaliza wa Chingapano Chakale. Onani pa Mateo 11:10-11. Mau a Mulungu amanena kuti Yohane Mbatizi ndi woimirira anthu. Ndipo monga wansembe wamkulu mu nthaœi ya Chipangano chatsopano, anapereka machimo onse adziko lapansi kwa Yesu; panthaœi yomweyo anali kugwiranso ntchito ya unsembe wa Chipangano Chakale.

Yesu adachitira umboni za Yohane. Iye adati, pa Mateo 11:13 “Aneneri onse ndiponso

Page 101: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

101 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Mumalamulo a Mose ankaneneratu za Ufumu umenewu mpaka nthaœi ya Yohane Mbatizi. Ndipo ngati mukufunadi kukhulupilira zimenezi, Yohaneyo ndiye Eliya uja amene ankati adzabwerayu.” Choncho Yohane Mbatizi, amene anabatiza Yesu, anali chidzukulu cha wansembe wam’kulu Aroni ndi wansembe wam’kulu wotsiliza. Baibulo limachitiranso umboni kuti Yohane, anali chidzukulu cha Aroni m’Chipangano Chakale (Luka 1:5; 1 Mbiri 24:10).

Nchifukwa chiyani Yohane Mbatizi anali kukhala mchipululu yekha, ndikumavala zovala zaubweya wa ngamira. Ndi chitsimikizo chakuti iye anali wansembe wam’kulu. Ndipo monga woimirira anthu onse, Yohane Mabatizi sanali kukhala ndi anthu. Motero anafuula kwa anthu “Lapani inu ana anjokanu” namawabatiza monga chipatso cha kulapa, chimene chinabwezera anthu kwa Yesu amene adachotsa machimo ao onse. Yohane Mbatizi anatulira machimo athu onse pa Yesu kuti tipulumutsidwe.

MITUNDU IŒIRI YA UBATIZO

Ndi chifukwa chiyani Yohane Mbatizi anali

kubatiza anthu?

Kuti anthu alape machimo awo ndi kukhulupilira mu

ubatizo wa Yesu kuti apulumutsidwe

Yohane Mbatizi anabatiza anthu kenaka

anabatiza Yesu. Ubatizo woyamba unali wa kuti anthu “alape machimo ao” umene udaitanira anthu kwa Mulungu. Anthu ambiri amene anamva Mau a Mulungu kudzera mwa Yohane adaleka machitidwe ao oipa ndi kubwera kwa Mulungu.

Ubatizo wachiœiri unali ubatizo wa Yesu, ubatizo umene udapereka machimo athu onse pa Yesu. Yohane Mbatizi adabatiza Yesu pofuna kukwaniritsa zonse zimene Mulungu anali kufuna.

Page 102: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

102 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi kuti anthu onse apulumutsidwe ku machimo ao (Mateo 3:15).

Ndi chifukwa chiyani kunali koyenera kuti Yesu abatizidwe. Kuti achotsedwe machimo athu onse Mulungu analola kuti Yohane apereke machimo onse kwa Yesu kuti anthu onse amene anakhulupilira mwa Yesu anapulumutsidwa.

Yohane Mbatizi anali mtumiki wa Mulungu amene ntchito yake inali yothandiza anthu onse kuti alape machimo ao onse ndipo anali woimirira anthu onse amene adachitira umboni za Uthenga Wabwino wa chiombolo. Choncho Yohane anayenera kukhala yekha m’chipululu. Pa nthaœi ya Yohane Mbatizi, Aisraele anali anthu aziphuphu ndiponso oipa kwambiri

Motero Mulungu adalankhula Mchipangano Chakale, pa Malaki 4:5-6, “Ndidzakutumizirani mneneri Eliya. Iyeyo adzayanjanitsa atate ndi ana ao, ana ndi atate ao, kuopa kuti ndingadzabwere kudzatembelera dziko lanu kuti liwonongeke.”

Pamaso pa Mulungu, anthu onse a ku Israele

amene anali kupembedza Yehova Mulungu anali ziphuphu. Palibe ngakhale mmodzi amene anali olungama pa maso pa Mulungu. Atsogoleri a chipembedzo, mwa chitsanzo ansembe, odziœa za malamulo, ndi alembi anali oipa kotheratu. Aisraele pamodzi ndi ansembe sanalikupereka nsembe zao motsatira lamulo la Mulungu.

Ansembe adatailira ntchito yao yosanjika manja ndi myambo yoperekera nsembe zochotsera machimo imene Mulungu adaœalamula. Kwalembedwa kuti ansembe pa nthaœi ya Malaki adatailira ntchito yao ya unsembe, kusanjika manja pansembe yokhetsa mwazi ndi miyambo ina.

Choncho Yohane Mbatizi sanali kukhala pamodzi ndi anthu. Motero Yohane Mbatizi adapita ku chipululu ndi kumafuula. Kodi ankati chiyani?

Kwalembedwa M’buku la Marko 1:2-3, mmau a mneneri Yesaya, “Ndidzatuma wam’thenga wanga m’tsogolo mwake kuti akakonzeretu njira

Page 103: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

103 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

yoti iwe udzapitemo.” Mau ofuula m’chipululu adali kuuza anthu kuti

alape machimo ao. Kodi ubatizo wa kulapa ndi chiyani umene Mau a Mulungu ali kunena? Ndi ubatizo umene Yohane Mbatizi anali kulalika kwa anthu, ubatizo woitanira anthu kwa Yesu kuti anthu athe kukhulupilira mwa Yesu kuti apulumutsidwe muimfa yake yapa Mtanda, kuti anthu abwerere kwa Mulungu.

“Ine ndili kukubatizani ndi madzi, koma amene ali kubwera pambuyo panga adzakubatizani ndi Mzimu Woyera”

“Adzakubatizani ndi Mzimu Woyera,” Mau awa atanthauza kuchotsa machimo anu onse. Kubatiza kutanthauza ‘kutsuka.’ Ubatizo wa Yesu mu m’tsinje wa Yolodani umatiuza kuti Mwana wa Mulungu anabatizidwa ndi kuchotsa machimo athu onse kuti tipulumutsidwe.

Choncho ife tiyenera kuleka machimo athu ndi kukhulupilira mwa Yesu. Iye ndi Mwana wa Nkhosa wa Mulungu amene anachotsa machimo

aanthu onse. Ndipo umenewu ndi Uthenga Wabwino wachipulumutso umene Yohane anali kuchitira umboni.

NTCHITO YA WANSEMBE WAMKULUYO INALI YOPEREKA NSEMBE YOCHOTSERA MACHIMO

Kodi ndani angakonze njira yoti ife tikalowere

kumwamba?

Yohane Mbatizi Mneneri Yesaya adaneneratu, “Mulankhule

mofatsa anthu aku Yerusalemu. Muwauze kuti nthaœi ya mavuto ao yatha, machimo ao akhululukidwa. Ndawalanga mowilikiza chifukwa

Page 104: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

104 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

cha machimo ao.” (Yesaya 40:2). Yesu Khristu adachotsa machimo anu ndi anga

ndi awina aliyense mpanda kusankha; machimo obadwa nawo, machimo amene ife timachita ngakhale machimo amene tidzachita kutsogolo anachotsedwa kudzera mu ubatizo wa Yesu. Iye anaombola ife tonse. Ife tonse tiyenera kudziœa za chiombolo chathu.

Pamene tapulumutsidwa ku machimo athu, tiyenera kukhulupilira mu Uthenga Wabwino umene Yohane Mbatizi anali kufalitsa wonena za kuperekedwa kwa machimo athu kwa Yesu Khristu kudzera mu ubatizo wake.

Tisasokonezeke, poganiza kuti popeza kuti Mulungu ndi wa chikondi, tikhoza kuloœa mu ufumu wa kumwamba pakungokhulupilira Yesu ngakhale tili ndi machimo m’mitima mwathu.

Kuti tiomboledwe ku machimo athu, tiyenera kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu umene Yohane anapereka machimo onse pa Yesu kudzera mu madzi, Yohane Mbatizi adapereka machimo onse

kwa Yesu. Chinthu choyamba chimene Mulungu adachita

kuti apulumutse anthu onse, ndi kutuma Yohane mudziko lino lapansi.

Wam’thenga wa Mulungu, Yohane Mbatizi, adatumizidwa kuti kazembe wa Mfumu, amene adatenga machimo onse aanthu ndi kupereka kwa Yesu kuti anthu onse athe kukhulupilira mwa Yesu Khristu kuti azapite kumwamba.

Mulungu anatilonjeza kuti adzatitumizira wam’thenga wake. “Ndidatumiza wa m’thenga wanga m’tsogolo mwako kuti adzakonzeretu njira yoti udzapitemo.” Mtsogolo mwako akutanthauza mtsogolo mwa Yesu. Kodi nchifukwa chiyani Mulungu adatumiza Yohane patsogolo pa Yesu? Chifukwa ndi chakuti machimo onse adziko lapansi aperekedwe kwa Yesu, Mwana wa Mulungu kudzera mu ubatizo wake “Kuti adzakonzeretu njira yoti uzapitemo.” Izi ndizimene iye anali kutanthauza.

Kodi ndani amene anakonza kuti anthu

Page 105: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

105 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

aomboledwe ndiponso kuti azapite kumwamba? Ndi Yohane Mbatizi. “Pako anena Yesu” ‘wanga’ atanthauza Mulungu mwini wake. Choncho pamene Mulungu ananena kuti, “Ndidzatumiza wam’thenga mtsogolo mwako kuti adzakonzeretu njira yoti uzapitemo.” Kodi anali kutanthauza chiyani?

Kodi ndani angakonze njira yoti ife tikalowere kumwamba? Yohane Mbatizi adapereka machimo onse kwa Yesu kuti tidziœe kuti Yesu adachotsa machimo athu onse; ntchito inali yopereka machimo ndi kubatiza Yesu Khristu. Anali Yesu ndi Yohane amene anachita chotheka kuti ife tikhulupilire mchoonadi ndi kuti tiomboledwe.

Kodi chipulumutso chathu chimadala chiyani? Chimadalira mu ntchito za Yesu, Mwana wa Mulungu ndiponso kuti wam’thenga wa Mulungu adapereka machimo onse adziko lapansi pa Iye. Tonse tiyenera kudziœa Uthenga Wabwino wokamba za chikhululukiro cha machimo. Mulungu Atate adatumiza wa m’thenga wake

patsogolo pa Yesu, anali kubwera kuti adzabatize Mwana wa Mulungu, ndiponso Mulungu adapanga Yohane kukhala woyimirira anthu. Ndipo anatsiliza ntchito yoombola anthu onse.

Mulungu adatumiza m’tumiki wake Yohane Mbatizi kudzabatiza Mwana wake, kuti potero Yohane Mbatizi akonze njira ya chipulumutso kwa anthu onse okhulupilira mwa Mwana wa Mulungu. Ichi ndicho cholinga cha ubatizo wa Yesu. Ubatizo wa Yohane umene Yesu anaulandira, unali wa chiombolo kudzera mu njira imene Yohane adatsatira yopereka machimo onse kwa Yesu kuti anthu onse akhulupilire kuti potero azapite ku mwamba.

Ngakhale machimo a mtsogolo anaperekedwa kwa Yesu kudzera mu ubatizo wake. Yesu ndi Yohane Mbatizi anatikonzera njira yokaloœera kumwamba. Mwa njira imeneyi Mulungu adaulura chinsinsi cha chiombolo kudzera mwa Yohane Mbatizi.

Monga woyimirira wa aliyense, Yohane

Page 106: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

106 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Mbatizi anabatiza Yesu kuti ife tikhulupilire m’chiombolo chathu kuti tizapite kumwamba. Adapereka machimo onse kwa Yesu kudzera mu ubatizo. Iyi ndi nkhani yokondweretsa ya chiombolo, Uthenga Wabwino.

KODI NCHIFUKWA CHIYANI YOHANE MBATIZI ANABADWA?

Kodi tikhoza kukhulupira mwa Yesu kudzera mwandani?

Yohane Mbatizi

Mbuku la Malaki 3:1 timaœerenga kuti,

“Ndidzatuma wam’thenga wanga kuti adzandikonzere njira.” Muyenera ku maœerenga Baibulo mosamala. Nchifukwa chiyani Mulungu adatumiza wam’thenga kwa ife? Nchifukwa

chiyani Yohane anabadwa miyezi isanu ndi umodzi Yesu asanabadwe?

Tiyenera kumamvetsa bwino cholinga cha Baibulo. Muli gawo lina Mchipangano Chakale limene limakamba za ntchito ya wansembe wamkulu Aroni. Aroni adaali mkulu wake wa Mose. Iye pamodzi ndi ana ake anadzozedwa ndi Mulungu kukhala ansembe. Alevi ena aja anali kugwira nthcito yao pansi pa ulamuliro wa Aroni ndi ana ake. Anali ngati ziœiya, kuphatikiza batala ndi buledi, pamene ana Aroni anali kupereka nsembe mkati mwa kachisi woyera wa Mulungu.

Motero ana a Aroni anadzozedwa kuti azigaœana ntchito molinganiza pakati pawo, koma Patsiku la Nsembe yochotsera machimo, tsiku la chikumi la mwezi wa chisanu ndi chiœiri wansembe wamkulu yekha ndi amene anali kupereka nsembe yochotsera machimo m’malo mwa anthu ake.

Pa Luka 1:5, pali nkhani yokamba za kubadwa kwa Yohane Mbatizi. Tiyenera kumvetsa bwino za

Page 107: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

107 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

wam’thenga wa Mulungu kuti timvetsenso bwino za Yesu. Timaganiza zambiri zokhudza Yesu, koma sitiganiza za Yohane Mbatizi amene anabwera poyamba Yesu asanabwere. Ndifuna ndikuthandizeni kuti mumvetse.

Uwu ndi Uthenga Wabwino wonena za Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu. Monga nam’neneri Yesaya adalemba m’buku lake kuti “Mulungu akuti, ‘Ndidzatuma wa m’thenga wanga m’tsogolo mwako kuti adzakonzeretu njira yoti iwe uzapitemo.” (Marko 1:1-2) Uthenga Wabwino wakumwamba umayamba ndi Yohane Mbatizi.

Ngati tidziœa bwino za Yohane Mbatizi ndiye kuti tidzadziœanso bwino ndi kukhulupilira Uthenga Wabwino wonena za chiombolo chimene Yesu anatipatsa. Ndi chimodzimodzi m’mene timavera akazembe amene anaikidwa m’maiko osiyanasiyana kuti tidziœe zimene zili kuchitika m’maiko ao. Pamene tidziœa bwino za Yohane Mbatizi, tikhoza kumvetsa za chikondi cha Mulungu.

Koma ndizomvetsa chisoni kuti anthu amene ndi akhristu sadziœa bwino za Yohane, ndi kufunika kwakwe. Mulungu sanatumize Yohane chifukwa analibe ntchito kapena chifukwa cha kuipidwa ayi. Mabuku onse anai a Uthenga Wabwino ‘Chipangano Chatsopano amayamba ndi kunena za Yohane Mbatizi asanayambe kukamba za ntchito yoombola anthu imene Yesu anaigwira.

Koma alaliki a masiku ano atayilira, sali kunenapo za Yohane Mbatizi iwo amauza anthu kuti chikhulupiliro chokha mwa Yesu nchokwanira kuti anthu apulumutsidwe. Motero iwo ali kutsogolera anthu kuti azikhalabe ochimwa pa moyo wao onse ndipo chotsatira ndi kupita kugahena.

Ngati mungokhulupilira Yesu osadziœa ntchito ya Yohane Mbatizi, chikhristu chimakhala ngati chipembedzo china kwa inu. Mungaomboledwe bwanji ngati simudziœa choonadi? Nkosatheka.

Uthenga Wabwino ukamba za chipulumutso siwovuta komanso ndi wovuta. Anthu ambiri

Page 108: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

108 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

amaganiza kuti chiombolo chao chagona mchikhulupiliro chathu pa Mtanda wa Yesu chifukwa chakuti Yesu anapachikidwa chifukwa cha ife. Koma ngati mungokhulupilira mu imfa yake yapa Mtanda osadziœa choonadi chakuti machimo onse anaperekedwa kwa iye, palibe chikhulupiliro chimene chingatitengere kuchiombolo.

Choncho Mulungu anatuma Yohane Mbatizi kuti adzalidziœitse dziko lonse lapansi m’mene chiombolo chidzakwaniritsidwe ndiponso m’mene Yesu adzachotsere machimo onse adziko lapansi. Tikadziœa choonadi, tidzadziœanso kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu amene anachotsa machimo onse adziko lonse lapansi.

Yohane Mbatizi amatiuza zoona zake za chiombolo. Iye anabwera pa dziko lapansi kudzachitila umboni za Umulungu wa Yesu; mmene anthu adzalepherere ku mulandira pamene kuwala kudzafika pa dziko lapansi. Iye adachitiranso umboni pa Yohane kuti ndi iye,

Yohane amene anakonza Uthenga Wabwino wa chiombolo pakubatiza Yesu Khristu.

Kodi Yohane akadapanda kubweretsa Uthenga Wabwino wa chiombolo, tikadakhulupira mwa Yesu? Yesu sitimuona, ndipo pamene ife tinakula ndi miyambo yosiyana ndi zipembedzo zosiyana tingathe bwanji kukhulupilira Yehova.

Pamene tili ndi zipembedzo zosiyana siyana, kodi tingakhulupilire mwa Yesu Khristu? Tingadziœe bwanji kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu amene anatiombola pakutenga machimo athu onse?

Choncho tiyenera kuyang’ana m’Chipangano Chakale kuti tipeze kuchokera pa chiyambi mau a chiombolo ndiponso kuti tidziœe kuti Yesu ndi Mpulumutsi wathu. Ife tiyenera kupeza nzeru yeniyeni kuti tikhulupilire moonadi. Palibe chimene ife tingachite popanda kudziœa. Kuti tikhulupilire mwa Yesu ndi kupulumutsidwa, tiyenera kudziœa bwino za Uthenga Wabwino wa chiombolo chimene Yohane Mbatizi adachitira

Page 109: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

109 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

umboni. Kukhala ndi chikhulupiriro choona mwa Yesu Khristu, tiyenera kudziœa choonadi cha chiombolo.

Choncho, monga Yesu adanena kuti, “Mudzadziœa zoona zenizeni, ndipo zoonadizo zidzakusandutsani aufulu.” Tiyenera kudziœa zoona za chiombolo chimene Yesu anatipatsa.

ZIMENE BAIBULO LIMATIUZA

Kodi mabuku onse a Uthenga Wabwino anai amayamba

ndi nkhani iti? Amayamba ndi nkhani ya

kubwera kwa Yohane Mbatizi

Tiyeni tipitilize kuona zimene Baibulo

limatiuza za chiombolo chimene chimapezeka mwa Yesu Khristu. Tiyeni tione zimene mabuku anai a Uthenga Wabwino aja amanena za Yohane Mbatizi, kodi iye anali ndani, nanga chifukwa chiyani tikunena kuti iye anali mkhalapakati wa anthu onse ndiponso wa nsembe wamkulu wotsiliza, nanga iye anapereka bwanji machimo onse kwa Yesu, ndipo tionenso ngati Yesu anasezadi machimo onse kapena ayi.

Mabuku onse anai a Uthenga Wabwino amayamba ndi nkhani ya Yohane Mbatizi. Yohane 1:6 amatiuza chinthu chofunika kwambiri mu Uthenga Wabwino. Yohane 1:6 akutiuzanso za munthu amene anagwira ntchito yopereka machimo onse kwa Yesu. “Mulungu adatuma munthu wina, dzina lake Yohane. Iyeyu adabwera ngati mboni, kudzachitira umboni kuwala kuja, kuti anthu onse akhulupilira chifukwa cha umboni wakewo.”

Mau tawerenga akuti, “Kuti anthu onse akhulupilire chifukwa cha umboni wakewo ndipo

Page 110: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

110 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Iye adadzachitira umboni za kuwalako.” Kuwalako ndi Yesu Khristu. Izi zikutanthauza kuti Yohane adadzachitira umboni za Yesu Khristu kuti anthu amukhulupilire Yesu kudzera mwa Iye. Tsopano tione mozama m’buku la Mateo.

M’buku la Mateo 3:13-17 pali mau awa, “Pamasiku amenewo, Yesu adachoka ku Galilea kubwera kwa Yohane ku Mtsinje wa Yolodani, kuti Yohaneyo amubatize. Yohane poyetsa kukana, adati, “Ndine amene ndiyenera kubatizidwa ndi inuyo. Nanga mukubweranso kwa ine kodi?” Koma Yesu adamuyankha kuti, Tsopano lino vomera, chifukwa ndi m’mene tiyenera kuchitira zimene Mulungu akufuna. Apo Yohane adavomera. Yesu atangobatizidwa, adatuluka m’madzimo. Pomwepo kuthambo kudatsekuka, ndipo adaona Mzimu wa Mulungu akutsika ngati nkhunda nkutera pa Iye. Tsono kuthamboko kudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga wapam’tima. Ndimakondwera naye kwambiri.””

Nchifukwa chiyani tiyenera

kudziwa fuko la Yohane Mbatizi?

Chifukwa chakuti Baibulo

limati uza kuti Yohane Mbatizi ndi wansembe wamkulu wa

anthu onse Tiyeni tione zimene mau akunena pa Luka 1:1-

14, “anthu ambiri adayetsa kulongosola mbiri ya zinthu zimene zidachitika pakati pathu. Iwo adalemba zimene adaatisimbira anthu oziona chamaso kuyambira pa chiyambi pake, nakhala akuzilalika. Tsono popeza kuti inenso ndalondola mosamala kwambiri m’mene zonsezo zidachitikira kuyambira pa chiyambi, ndaganiza kuti nkwabwino kuti ndikulembereni zimenezo mwatsatane tsatane. Ndatero kuti mudziœe ndithu kuti zimene adakuphunzitsanizo nzoonadi. Panthaœi imene Herode anali mfumu ya dziko la

Page 111: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

111 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Yudea, kunali wansembe wina, dzina lake Zakariya wagulu la nsembe la Abiya. M’kazi wake Elizabeti anali wa fuko la Aroni. Aœiri onsewo anali wolungama pa maso pa Mulungu, ndipo ankhatsata malangizo ndi malamulo onse a Ambuye. Adaalibe mwana, chifukwa Elizabeti anali wosabala, ndipo aœiri onsewo anali wakalamba. Tsiku lina Zakaliya ankagwira ntchito yake ya unsembe pa maso pa Mulungu. Inali nthaœi ya gulu lake la ansembe kutumikira. Potsata dongosolo lao la ansembe iye adasankhidwa mwa maere kuti akalowe mnyumba ya Mulungu kukafukiza lubani. Khamu lonse la anthu linkapemphera kunja pa nthaœi yofukiza lubaniyo. Tsono mngelo wa Ambuye adaonekera Zakariya. Mngeloyo adaimirira adadzidzimuka pomuona, nachita mantha. Koma mngeloyo adamuuza kuti, usaope Zakariya, Mulungu wamva pemphero lako. M’kazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wa mwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane. Udzakondwa ndi

kusangalala, anthu ambirinso adzakondwa chifukwa chakubadwa kwake.”

Luka ali kutiuza mwatsatanetsane za kubadwa kwa Yohane. Luka, amene ndi wophunzira wa Yesu, akufotokoza za kubadwa kwa Yohane kuyambira pa chiyambi. Luka anali kuphunzitsa Uthenga Wabwinowu munthu wina dzina lake Teofilo, amene anali wochokera ku miyambo ina ndipo sankadziœa Ambuye.

Motero, pofuna kuti amuphuzitse za Yesu Mpulumutsi wa ochimwa, Luka adaona kuti nkwabwino kuti afotokoze mwatsatane tsatane za kubadwa kwa Yohane Mbatizi.

Pa Luka 1:5-9 akunena kuti, “Pa nthaœi imene Herode anali mfumu ya dziko la Yudea, kunali wansembe wina dzina lake Zakariya, wagulu la ansembe la Abiya. M’kazi wake Elizabeti anali wafuko la Aroni. Aœiri onsewo anali wolungama pa maso pa Mulungu, ndipo ankatsata mokhulupirika malamulo ndi malangizo onse a Ambuye. Adaalibe mwana, chifukwa Elizabeti

Page 112: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

112 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

anali wosabala, ndi aœiri onsewo anali wokalamba. Tsiku lina Zakariya ankagwira ntchito yake ya unsembe pa maso pa Mulungu.”

Pamenepa, chinthu china chinachitika pamene Zakariya ankagwira ntchito yake ya unsembe. Ndipo Luka adachitira umboni kuti Zakariya anali wam’banja la Aroni. Nanga Zakariya anali wa gawo liti? Iyi ndi mfundo yofunika kwambiri kudziœa.

Luka adalongosola, “Tsiku lina Zakariya ankagwira ntchito yake yaunsembe pa maso pa Mulungu, linali tsiku la gulu lake la ansembe.” Pamenepa tikhoza kuwona kuti Luka adadziœa bwino zambiri ya Zakariya kotero kuti nchifukwa chake analongosola Uthenga wa chiombolo kudzera mwa Zakariya ndi Elizabeti.

Ife monga anthu amitundu yina sitingathe kumvetsa za chipulumutso cha Yesu ngati wina satilongololera mwatsatane tsatane. Tiyeni tione kuti kodi tsatane tsatane wake ndi wotani. Yohane Mbatizi anabadwa mwa Zakariya ndi Elizabeti

amene anali m’modzi mwa ana aakazi a Aroni. Tsopano tione mbadwo wa Zakariya ndi Yohane.

MBADWO WA YOHANE MBATIZI

Kodi Yohane Mbatizi anali wafuko la ndani?

Aroni, wansembe wamkulu

Kuti timvetse bwino za fuko la Yohane Mbatizi

tiyeni tione Mchipangano Chakale 1 Mbiri 24:1-19 “Zidzikulu za Aroni ndi izi. Ana a Aroni nawa: Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara. Koma Nadabu ndi Abihu adafa bambo wao akali moyo, ndipo analibe ana. Motero Eliazara ndi Itamara adaloœa unsembe. Zidzukulu za Aroni Mfumu Davide adazigawira ntchito molongosoka bwino,

Page 113: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

113 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

pothandizidwa ndi Zadiki, mmodzi mwa zidzukulu za Eleazara, ndiponso Ahimeleki, mmodzi mwa zidzukulu za Itamara. Adaœasankhula pochita maere, mosakondera poti panali atumiki a kunyumba ya Chauta ndi atsogoleri achipembedzo pakati pa zidzukhulu za Eleazara ndiponso pakati pa zidzukulu za Itamara. Magulu aœiri a zidzukulu adachita maerewo motsatana, ndipo mlembi Semaya, mwana wa Netanele, amene anali Mlevi, adalemba maina ao. Mboni zake zinali izi: Mfumu, nduna, wansembe Zadoki, Abimeleki mwana Abiyatara, ndiponso atsogoleri a mabanja aansembe ndi a Alevi. Maere oyamba adagwera Yehoyaribu, achiœiri adagwera Uedaya, achitatu adagwera Harimu, achinayi adagwera Seorimu, achisanu adagwera Malikiya, achisanu ndi chimodzi adagwera Miyamini, achisanu ndi chiœiri adagwera Hakozi, achisanu ndi chitatu adagwera Abiya, achisanu ndi chinai adagwera Yesuwa, achikhumi adagwera Sekaniya, a chikhumi ndi chimodzi adagwera Eliyasibu a

chikhumi ndi chiœiri adagwera Yakimu, a chikhumi ndi chitatu adagwera Hupa a chikhumi ndi chinayi adagwera Yesebeabu, achikhumi ndi chisanu adagwera Biliga, a 16 adagwera Imeri, a 17 adagwera Heziri, a 18 adagwera Hapizeze, a 19 adagwera Petahiya, a 20 adagwera Yehezikele, a 21 adagwera Yakini, a 22 adagwera Gamuli, a 23 adagwera Delaya, a 24 adagwera Maaziya. Ntchito yao ya anthu amenewa inali yotumikira mNyumba ya Mulungu potsata mwambo umene adaukhazikitsa Aroni kholo lao, monga momwe Chauta Mulungu wa Aisraele adaamlamulira.”

Tiyeni tionenso pa ndime ya 10, “A chisanu ndi chiœiri adagwera Hakozi, achisanu ndi chitatu adagwera Abiya.” Pamenepa chimene Davide anachita ndi kupereka ntchito yambiri kwa ana a Aroni kuti nsembe iperekedwe molongosoka. (monga nonse mukudziœa, Aroni anali mkulu wake wa Mose. Mulungu anadzoza Mose kukhala womuimirira wake, ndipo Aroni anakhala wansembe wamkulu mu Kachisi Woyera wa

Page 114: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

114 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Mulungu pa maso pa Aisraele). Alevi ena onse anawayika pansi pa ulamuliro

wa ansembe ndi Aroni ndi ana a Aroni anakhala oyendetsa ntchito yonse yopereka nsembe pa maso pa Mulungu. Davide asagawe ntchito yoti anthu agwire, ansembe, am’fuko la Aroni, anali kudzipatsa okha ntchito ndipo izi zidadzetsa msokonezo waukulu.

Choncho, Davide adathetsa msokonezowo pakuika gulu lililonse mundondomeko yake. Analipo magulu okwanira makumi aœiri ndi mphambu zinai (24) m’munandanda umene unachokera ku zidzukhulu za Aroni, ndipo wa chisanu ndi chitatu anali Abiya. Ndipo kwalembedwa kuti, “Wansembe wina wotchedwa Zakariya anali wagulu la ansembe a Abiya.” Motero Zakariya anali wansembe wa ’gulu la ansembe la Abiya, ndipo aœiri onsewa anali afuko la wansembe wamkulu Aroni.

Zakariya, wansembe wagulu la Abiya ndiye wa bambo wake wa Yohane Mbatizi. Timadziœa

kuchokera M’mau a Mulungu kuti anthu awa anali kukwatirana okhaokha.

Monga inu mukudziœa, Yakobo anaakwatira mwana wa amalume ake kumbali ya mai wake. Ndipo dongosolo la mbadwoli ndi lofunika kwambiri monga tawerengera kuti, “Zakariya adali wansembe wagulu la ansembe la Abiya.”

Choncho, Iye anali wa fuko la Aroni. Ndani? Zakariya bambo wake wa Yohane Mbatizi. Nkhani imeneyi ndi yofunika kwambiri pofuna kulongosola za chiombolo cha Yesu Khristu, ndi ntchito ya Yohane Mbatizi ndiponso kuperekedwa kwa machimo onse adziko lapansi kwa Yesu.

Page 115: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

115 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

ANA A ARONI NDI OKHAWO AMENE AZAGWIRA NTCHITO YA MULUNGU

Kodi ndani ankagwira ntchito ngati wansembe wa mkulu panthawi ya Chipangano Chakale

Aroni ndi abanja lake

Nanga mu Baibulo ndipati pamene akunena kuti

Aroni ndi ana ake ndi amene ayenera kugwira ntchito ya Mulungu? Tiyeni tione mubuku la Numeri 20:22-29.

“Tsono mpingo wonse wa Aisraele udanyamuka ku Kadesi kuja nukafika ku Phiri la Horo ku Phiri limenero, limene lili m’marire adziko la Edomu,

Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, “Aroni salowa nawo m’dziko limene ndidapatsa Aisraele. Adzafa, chifukwa choti nonse aœirinu simudamvere lamulo langa kumadzi aku Meriba kuja. Uthenge Aroni pamodzi ndi Eleazara mwana wake, ukwere nawo pamwamba pa Phiri la Horo. Kumeneko uvule Aroni zovala za unsembe ndikumveka mwana wake Eleazara. Ndipo Aroni adzafera komweko.” Mose adachitadi zimene Chauta adamulamula. Atatu onsewo adakwera Phiri la Horo, mpingo wonse ukupenya. Apo Mose adamuvula Aroni zovala zake zaunsembe, naveka Eleazara mwana wake. Ndipo Aroni adafera pamwamba pa phiri pomwepo. Tsono Mose ndi Eleazara adatsika phiri. Pamene mpingo udamva kuti Aroni wamwalira, mpingo wonse wa Israele udalira maliro a Aroni masiku makumi atatu.”

M’buku la Eksodo, malamulo a Mulungu akuti, ana a m’kulu wansembe ayenera kutenga malo a ukulu wansembe monga ngati atate awo analili.

Pa Eksodo 28:1-5, “Aroni ndi ana ake amuna

Page 116: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

116 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

apatulidwe pakati pa Aisraele ndipo abwere kwa iwe, kuti akhale ansembe onditumikira, abwere Aroni pamodzi ndi ana ake Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara. Um’sokere mukulu wako Aroni zovala zopatulika, kuti azioneka wolemera ndi wolemekezeka. Ulamule anthu onse aluso, onse amene ndaœapatsa nzeru, kuti asoke zovala za Aroni zoozavala pamene udzampatule kuti akhale wansembe wanga. Zovala zimene udzasokezo ndi izi: chovala chapachifuwa, chovala cha efodi, m’kanjo, mwinjiro wopetedwa bwino, nduœira ndi lamba. Asoke zovala zopatulikazo za m’bale wako Aroni ndi za ana ake, kuti akhale ansembe onditumikira. Zovala zimenezi anthu alusowo azisoke ndi nsalu yagolide, ndi nsalu yobiriœira, yofuurira ndi yofiira ndiponso ya bafuta wosalala wopikidwa bwino.”

Mulungu adatuma Aroni m’bale wake wa Mose kupita ku unsembe. Ntchito ya unsembe sinali ntchito ya munthu aliyense. Motero Mulungu adalamula Mose kuti adzoze Aroni monga wa

nsembe wam’kulu ndiponso ampangire zovala za ntchito yake. Tisaiwale konse Mau a Mulungu.

Komanso pa Eksodo 29:1-9, pali mau aœa: “Pofuna kumpatula Aroni ndi ana ake, kuti akhale ansembe onditumikira, uchite izi: Utenge ng’ombe ya mphongo ndi nkhosa za mphongo ziœiri zopanda chilema. Utengenso buledi wosafufumitsa, makeke osatupitsa osakaniza ndi mafuta, ndiponso mitanda ya buledi yopsyapyalala yopaka mafuta. Zimenezi uzipange ndi ufa watirigu. Uziike m'lichero, ndipo ubwere nazo kwa ine pamene naye Aroni ku khomo la chihema cha msonkhano pamodzi ndi ana ake aamuna, ndipo onsewo uœayeretse m’madzi. Tsono utenge zovala zija ndi kumveka Aroni mwinjiro ndi m’kanjo wautali wovala pa mwamba pa efodi, ndiponso chovala chapachifuwa. Ndipo umange lamba woluka mwaluso m’chiuno mwake. Umveke nduœira ku mutu kwake, ndi duœa lopatulika lija pa ndwirapo. Tsono utenge mafuta odzora aja ndi kuwatsanyumira ku mutu kwake kuti um’dzoze.

Page 117: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

117 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Kenaka ubwere ndi ana ake aamuna ndipo uwaveke mwinjiro. Uœavekenso lamba m’chiuno mwao ndi nduœira. Motero iwoœa adzakhala ansembe anga potsata lamulo langa losatha. Umu ndi m’mene um’dzozere Aroni ndi ana ake aamuna.”

Uœavekenso lamba m’chiuno mwao ndi nduœiri. Motero iwowa adzakhala ansembe anga potsata lamulo langa losatha. Pamene anaœasankha anati, “Ili linali lamulo losatha,” linali kugwira ntchito ngakhale pamene Yesu anabwera m’dziko lapansi.

Motero m’buku la Luka akufotokoza mozama akuti Zakariya anali wabanja la Aroni wam’kulu wansembe. Pamene Zakariya anali kugwirira ntchito monga wansembe munyumba ya Mulungu, m’ngelo anamuwonekera ndi kumuuza kuti pemphero lako lavomerezedwa kuti m’kazi wake Elizabeti azabala mwana wamwamuna.

Zakariya sanakhulupilire izi ndipo anati, “M’kazi wanga wakula muzaka, zingatheke bwanji

kuti akhale ndi mwana?” Chifukwa chakukaika kwake, Mulungu anamuseka pakamwa pakanthaœi kuwonetsa kuti mau ake ndi owona.

Pa nthaœi yake, m’kazi wake anakhala ndi pakati ndipo pakanthaœi, Maria mosaziœana ndi mwamuna analinso ndi pakati. Zonse zochitikazi zinali chikonzero cha Mulungu kuti atipulumutse. Kuti apulumutse anthu otayika, anayenera kutuma kapolo wake Yohane ndiponso Mwana wake m’modzi yekha Yesu kuti abadwe m’dziko la pansi.

Choncho mwana wakeyo anabatizidwa ndi Yohane kuti achotse machimo adziko lapansi kuti aliyense amene akhulupilira iye adzapulumutsidwa..

Page 118: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

118 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

MPHATSO YA PADERA YA MULUNGU!

Kodi ndani amene Mulungu anakonza poyambirira pa ntchito yoombola anthu?

Yohane Mbatizi

Ndi Mupulumutsi wa anthu, Yesu Khristu,

yemwe anabadwa ndi namwali Maria amene sanadziœane ndi mwamuna. Maria analonjezana kukwatirana ndi Yosefe m’zukulu wa Yuda. Yesu anayenera kubadwa kudzera m’zizukulu za Yuda kuti lonjezo la Mulungu likwaniritsidwe monga momwe Yohane Mbatizi anabadwira mu nyumba ya m’kulu wansembe Aroni.

Mulungu anakonza kuti onse aœiriœa abadwe m’dziko lapansi, Yohane woyamba ndipo

wotsatira Yesu. Yohane anabadwa kuti abatize Yesu ndi kutenga machimo onse adziko lapansi. M’zukulu wa ansembe wam’kulu anali kupereka nsembe yochotsera machimo kuti akwaniritse lamulo la Mulungu limene anakhazikitsa mu Chipangano Chakale ndi Chatsopano; kuti Uthenga Wabwino wa chiombolo wa Yesu kuti aukhulupilire moyenera.

M’buku la Eksodo, Mulungu anapereka Malamulo ake ndi malonjezo, malamulo a Mulungu ndi malamulo oœatsogolera popereka nsembe mu kachisi, pansi pazovala za ansembe, ndi dongosolo la nsembe. Mulungu anasankha Aroni ndi zizukulu zake kuti akhale ansembe kwamuyaya.

Choncho zizukulu zonse za Aroni zinali kupereka nsembe ndipo wam’kulu wansembe anayenera kuchokera mu nyumba ya Aroni yokha. Mukuona m’mene zinalili?

Koma mwa ambiri azizukulu za Aroni, Mulungu anasankha wansembe dzina lake

Page 119: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

119 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Zakariya ndi m’kazi wake Elizabeti. Iye anati, “Wona, ndikutumiza wa m’thenga wanga pamaso pako.” Pamene Mulungu anauza Zakariya kuti Elizabeti azakhala ndi mwana wamwamuna, ndipo dzina lake adzamutcha Yohane, iye anadabwa kwambiri moti anakhala osalankhula monga momwe analamulira mpaka mwana anabadwa.

Ndipo ndizoona, mwana anabadwa munyumba yake. Pamene nthaœi yinakwana yopereka dzina motsatira mwambo wa Aisraele, dzina linaperekedwa pambuyo pa abambo ake.

“Nthaœi yakuti Elizabeti achire idakwana, ndipo adabala mwana wamwamuna. Anzake ndi abale ake atamva kuti Ambuye am’chitira chifundo chachikulu chotere, adakondwera naye pamodzi. Patsiku lachisanu ndi chitatu mwanayo atabadwa, adadza naye kuti amuumbale, nafuna kumutcha dzina la bambo wake Zakariya. Koma mai wake adakana, adati, “Iyai, koma atchedwe Yohane.” Pamenepo anthuwo adamuuza kuti, “Koma pakati pa abale anu palibe amene ali ndi

dzina limeneli.” Tsopano adalankhula ndi bambo wake ndi manja, namufunsa kuti, “Mukufuna kuti timutche dzina lanji?” Zakariya adapempha cholemberapo, nalemba kuti, “Dzina lake ndi Yohane.” Anthu onse adazizwa. Pomwepo Zakariya adathanso kulankhula, nayamba kutamanda Mulungu. Anzao onse aja adagwidwa ndi mantha, ndipo mbiri ya zimenezi idawanda ku dera lonse la mapiri aku Yudea. Anthu onse amene ankazimva, ankazilingalira m’mitima mwao, ndi kumadzifunsa kuti, “Kodi mwana ameneyu adzakhala munthu wotani?” Pakuti zinkhachita kuonekeratu kuti Ambuye anali naye” (Luka 1:57-66).

Zakariya anali munthu wosalankhula nthaœi yina. Pamene nthaœi yinakwana kuti atche dzina mwana wake, abale ake adaganiza kuti dzina lake amutche Zakariya. Koma amayi ake analimbikira kuti dzina lake ndi Yohane. Apo, abale ake ananena kuti palibe ngakhale m’modzi wa banja lanu amene ali ndi dzina limeneli ndipo ayenera

Page 120: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

120 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

kumutcha dzina la bambo wake. Pamene Elizabeti anali akulimbikira pa dzinalo,

abale ake anapita kwa Zakariya namufunsa kuti kodi dzina la mwana litchedwa ndani? Zakariya anali woti sankhalankhula, anapempha cholembapo nalemba kuti ‘Yohane.’ Abale awo onse adadabwa ndi m’mene anasankhira dzina ili.

Koma atamutcha dzina, Zakariya analankhula nthaœi yomweyo. Anatamanda Mulungu ndipo anadzdzidwa ndi Mzimu Woyera ndipo ananenerathu.

M’buku la Luka akunena za kubadwa kwa Yohane Mbatizi mu nyumba ya Zakariya, wam’gulu la Abiya. Monga mwa mphatso yapadera ya Mulungu, Yohane Mbatizi, mbale wa m’badwo wa anthu anabadwa munyumba ya Zakariya, m’kulu wa Aroni.

Ndipo kudzera mwa Yohane Mbatizi ndi Yesu Khristu, Mulungu anakwaniritsa chipulumutso cha anthu. Tinapulumutsidwa kuchokera ku machimo chifukwa chokhulupilira ntchito za kuomboledwa

zimene zinachitidwa ndi Yohane ndi Yesu Khristu.

UBATIZO WA YESU

Yesu anabatizidwa

ndi Yohane?

Kuti achotse machimo onse adziko lapansi

Yohane Mbatizi analikuchitira umboni kuti Yesu anali Mwana wa Mulungu ndipo anachotsa machimo athu onse. Anali Yohane Mbatizi, kapolo wa Mulungu amene anachitira umboni zachipulumutso chathu. Osati kuti zikutanthauza kuti Mulungu sangathe kutiuza yekha kuti iye ndi mupulumutsi wathu. Mulungu amagwira ntchito kudzera mwa antchito ake mu matchalitchi, ndi

Page 121: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

121 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

kudzera m’kamwa mwa anthu ake onse amene anapulumutsidwa.

Mulungu akuti, “Muœalankhule mofatsa anthu aku Yerusalemu. Muwauze kuti nthaœi ya mavuto ao yatha, machimo ao akhululukidwa. Ndaœalanga moœirikiza chifukwa cha machimo ao. Udzu umauma, maluwa amafota, koma Mau a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka muyayaya.”(Yesaya 40:2,8)

“Sindinu ochimwa lero ayi. Ndinalipira machimo anu onse ndipo ntchito yonse inatha.” Awa ndi mau a Uthenga Wabwino wa chiombolo ukulalikidwa kwa ife. Uwu ndi Uthenga Wabwino umene unakonzedwa.

Ngati timvetsa ntchito za Yohane Mbatizi, ngati timvetsetsa kuti Yesu anatenga machimo onse adziko lapansi kudzera mwa Yohane Mbatizi, tikhoza kukhala womasuka ku machimo athu onse.

Muchipangano Chakale, ochimwa anali kusanjika manja awo pa mutu wa nsembe kuti apereke machimo awo pa mutu wake.

Ndipo anali kudula khosi ndipo ansembe analikutenga mwazi ndi kuika pa nyanja za guwa lootcherapo nsembe. Iyi inali njira yoperekera nsembe ya machimo amasiku onse.

Ndipo, kodi anali kuchita bwanji kuti achotse machimo a chaka chonse?

Aroni, wam’kulu wansembe anali kupereka nsembe ya anthu onse adziko la Aisraele. Chifukwa Yohane Mbatizi anabadwa ku banja la Aroni, chinali kuyenera kuti iye akhale m’kulu wansembe, ndipo Mulungu anamusankha iye kuti akhale m’kulu wansembe wotsiriza monga momwe m’mene Iye nakonzera za chiombolo.

Yohane Mbatizi anali woimirira anthu onse chifukwa Chipangano Chakale chinatha pamene Yesu Khristu anabadwa. Ndani winanso koma Yohane Mbatizi anapereka machimo onse adziko lapansi pa Yesu M’chipangano Chatsopano monga momwe Aroni anachotsera machimo aanthu ake M’chipangano Chakale? Monga wansembe wam’kulu wotsiriza wa Chipangano Chakale

Page 122: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

122 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

ndiponso woimirira anthu onse, Yohane Mbatizi anapereka machimo onse a dziko lapansi pa Yesu ndi ubatizo wa Yesu.

Chifukwa Yohane anapereka machimo onse pa Yesu, tsono tikhoza kuomboledwa kupsolera mu kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzumu Woyera. Yesu anakhala Mwana Wankhosa kuti atipulumutse ochimwa onse, motero anatenga ntchito ya chiombolo monga m’mene Mulungu anakonzera.

Yesu anatiuza kuti Yohane Mbatizi anali mneneri wotsiriza amene anapereka machimo onse adziko lapansi pa Iye.

Kodi chifukwa nchiyani Yesu sanachite izi Iye yekha? Chifukwa nchiyani anali kufuna Yohane Mbatizi? Panali chifukwa chimene Yohane Mbatizi anabadwira miyezi isanu ndi umodzi Yesu asanabadwe. Kunali kukwaniritsa lamulo la Chipangano Chakale, kuyeretsa Chipangano Chakale.

Yesu anabadwa kwa namwali wosadziœana ndi

mwamuna Maria, ndipo Yohane Mbatizi anabadwa kwa mayi amene anali wachikulire Elizabeti.

Iyi inali ntchito ya Mulungu, Iye anakonza kuti apulumutse anthu ochimwa, kutipulumutsa ku nkhondo ya uchimo, ndi masautso aanthu oipa, anatumiza kapolo wake Yohane, ndi Mwana wake Yesu. Yohane Mbatizi anatumizidwa kuimirira anthu, m’kulu wansembe wotsiriza.

MUNTHU WAMKULU WOBADWA NDI M’KAZI

munthu wamkulu padziko lapansi ?

Yohane Mbatizi

“Pamene amithenga a Yohane aja ankhachoka,

Page 123: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

123 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Yesu adayamba kufunsa makamu aanthu aja za Yohane kuti, Kodi m’mene mudaapita ku chipululu, m’daati mukaona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi? Nanga m’daati mukaona chiyani? Munthu wovala zofewa kodi? Iyai, anthu ovala zofewa amakhala m’nyumba za mafumu. Tanenatu, m’daati mukaona chiyani? M’neneri kodi? Zoonadi, ndipo ndikunenetsa kuti mudakaona woposa m’neneri amene. Ameneyu ndiye uja Malembo akunena zakeyu kuti, Nayitu ntumi yanga, ndi kuitima m’tsogolo mwako, kuti ikakonzeretu njira yodzadzeramo ine? Ndithu ndikunenetsa kuti mwa anthu onse amene adabadwa pansi pano, palibe ndi mmodzi yemwe woposa Yohane Mbatizi. Komabe ngakhale amene ali wam’ng’onong’ono mu ufumu wakumwamba amampambana. Kuyambira pa nthaœi ya Yohane Mbatizi mpaka tsopano anthu akhala akulimbana ndi umfumu wakumwamba, ndipo ochita chamuna ndiwo amene akuulanda. Aneneri onse ndiponso malamulo a Mose ankaneneratu za umfumu

umenewu mpaka nthaœi ya Yohane Mbatizi. Ndipo ngati mukufunadi kukhulupilira zimenezi, Yohaneyo ndiye Eliya uja ankati adzabwerayu”(Mateo 11:7-14).

Anthu anapita ku chipululu kuti akaone Yohane Mbatizi, amene anali kufuula kuti, “Tembenukani, ana anjoka inu!” Yesu anati, “Nanga munapita kuchipululu kukaona chiyani? Munthu wovala zofewa kodi? Nzoonadi anthu ovala zofewa amakhala m’nyumba za maufumu.”

Yesu yekha anachitira umboni za ukulu wa Yohane. Kodi munapita kuchipululu kukaona chiyani? Munthu wankhondo wovala zikopa za ngamira amene akulankhula mokweza mau? Ayenera kuvala zikopa za ngamira. Tanenanitu, m’daati mukaona chiyani? Munthu wovala zofewa kodi? Munthu wovala zofewa amakhala m’nyumba za maufumu. “Koma uyu ndi wam’kulu koposa mafumu.”

Yesu anachitira umboni. Nzoona, anthu ovala zofewa amakhala m’nyumba za maufumu.

Page 124: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

124 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Tanenanitu m’daati mukaona chiyani? M’neneri kodi? Zoonadi, ndipo ndikunenetsa kuti mudakaona woposa m’neneri amene.

Mumasiku akhale, aneneri anali oposa mafumu. Kodi mukumvetsa? Koma Yohane Mbatizi anali woposa mafumu, ndiponso ndi aneneri ena. Anali woposa aneneri onse a Muchipangano Chakale. Yohane m’kulu wansembe wotsiriza woimirira anthu, anali woposa Aroni woyamba wam’kulu wansembe. Yesu yekha anachitira umboni Yohane. Kodi woimirira anthu ndani?

Kuchotsapo Yesu Khristu yekha, kodi munthu wam’kulu pansi panopa ndani? Yohane Mbatizi. “Ndikunena kwa inu, woposa m’neneri, taonani, ndikutumiza wam’thenga wanga pamaso panu, amene adzakonza njira yanu.”

Yohane Mbatizi anachitira umboni kuti nkhondo yolimbana ndi uchimo yatha. “Wonani, Mwana Wakhosa wa Mulungu amene achotsa machimo adziko lapansi!” Anali Yohane Mbatizi amene anachitira umboni kuti Yesu anachotsa

machimo adziko lonse. M’buku la Mateo 11:11, akuti, Ndithu

ndikunenetsa kuti mwa anthu onse amene adabadwa pansi pano, palibe ndi mmodzi amene ali wam’ng’ono mu ufumu wakumwamba amampambana.

Kodi chitanthauza chiyani kubadwa kwa akazi? Chitanthauza anthu onse kuchotsapo Adamu, anthu onse anabadwa kwa akazi. Inde, mwaiwo obadwa kwa akazi palibe amene adali wamukulu nati Yohane Mbatizi. Choncho iye ndi wansembe wam’kulu wotsiriza woimirira anthu. Yohane Mbatizi adali wansembe wam’kulu, m’neneri, ndi wotiimirira.

M’buku la Chipangano Chakale, Aroni ndi ana ake adadzodzedwa ndi Mulungu kugwira ntchito yochotsa machimo. Machimo onse analikuchotsedwa kudzera mwa Aroni ndi ana ake.

Zinali momwe Mulungu adalamulira. Ngati wina wa Alevi wabwera kuchita izi anali kuyenera kufa mosachedwa. Iwo chimene ankhachita ndi

Page 125: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

125 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

kusakira nkhuni zokolezera moto pa guœa lansembe ndi kutsenda nyama, kusuka matumbo, ndikuchotsa mafuta. Ngati wina afunitsitsa kutsogolera ntchito ya wansembe,anali kuyenera kufa. Lidali lamulo la Mulungu. Sanali kuyenera kudutsa malire.

Padziko lapansi, panalibe amene anapeza wam’kulu ngati Yohane Mbatizi. Anali wam’kulu mwa onse amene anali kuyenera kufa. “Kuchokera mu masiku a Yohane Mbatizi mpaka lero ufumu wakumwamba ukuwonongedwa, ndipo kuwonongedwa uku ndikoumirizidwa.”

Ndipo kuwonongedwa uku ndikoumirizidwa pamene Yohane Mbatizi anabatiza Yesu, ndi ena onse amene amakhulupilira Yesu ndi oyenera kulowa mu ufumu wa kumwamba. Amakhala olungama. Tiyeni tione m’mene bambo wa Yohane anachitira umboni wa mwana wake.

UMBONI WA ZAKARIYA, BAMBO WA YOHANE

zotani zokhuza mwana wake?

Yohane adzakoza njira ya Ambuye kupereka nzeru za

chipulumutso kwa anthu ake

Tiwerenga mu Luka 1:67-80 kuti, “Tsopnao

Zakariya, bambo wa Yohaneyo, adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula mau ochokera kwa Mulungu. Adati, ‘Atamandike Ambuye, Mulungu wa Israele, chifukwa adadzayendera anthu ao, ndi kudzaœaombola. Adautsa wina, wafuko la m’tumiki wake Davide, kuti akhale Mpulumutsi wathu wamphamvu. Izi ndi zimene iye adaaneneratu kalekale kudzera mwa aneneri ake oyera m’tima. Adaalonjeza kuti

Page 126: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

126 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

adzatipulumutsa kwa adani athu, ndi kwa onse odana nafe. Choncho iye waœachitiradi chifundo makolo athu akale, ndipo wakumbukira chipangano chake choyera. Adalonjezanso Abrahamu, kholo lathu, molumbira, kuti adzatipulumutsa kwa adani athu, kuti tizimtumikira mopanda mantha, kuti tikhale oyera m’tima ndi molungama pamaso pake, masiku onse amoyo wathu. Tsono mwana iwe, udzatchedwa mneneri wa Mulungu wopambana zonse, chifukwa udzatsogolera pamaso pa Ambuye, kuti ukonzeretu njira zao. Udzadziœitsa anthu ao kuti Mulungu adzaœapulumutsa pakuœakhululukira machimo ao. Mulungu wathu ndi wachifundo chachikulu, adzatitumizira kuœala kwa dzuœa lam’maœa kuchokera kumwamba. Kuœala kwake kudzaunikira onse okhala mum’dima wabii ngati wa imfa, kudzatitsogolera panjira ya mtendere’. Mwana uja Yohane ankakula adzasanduka wankhalidwe wamphamvu. Pambuyo pake adakhala ku chipululu mpaka tsiku limene

adadziwonetsa poyera pakati pa Aisraele.” Zakariya ananeneratu zinthu ziœiri. Ananena

kuti maufumu onse aanthu anafika. Kuchokera pa ndime 68 kufika pa ndime 73, ananena ndi chimwemwe kuti Mulungu sanaiwale malonjezo ake kuti Yesu, monga Mulungu analonjeza Abrahamu, kuti adzabadwa kwa namwali wosadziœana ndi mwamuna Maria kuti athe kupulumutsa afuko lake m’manja aadani ao.

Ndipo kuchokera pa ndime 74 akuti, “Adzatipulumutsa mumanja aadani athu, kuti tizim’tumikira mopanda mantha.” Ichi chinali chikumbutso cha lonjezo la Mulungu kwa Abrahamu ndi anthu onse a fuko la Israele, ndipo ananeneratu kuti, “Anatipatsa mphamvu yogwira ntchito yake popanda mantha.”

Kuchokera pa ndime 76, ananeneratu kwa mwana wake. “Tsono mwana iwe, udzatchedwa m’neneri wa Mulungu wompambana zonse, chifukwa udzatsogolera pamaso pa Ambuye, kuti ukonzeretu njira zao. Udzadziœitsa anthu ao kuti

Page 127: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

127 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Mulungu adzaœapulumutsa pakuœakhululukira machimo ao. Mulungu wathu ndi wachifundo chachikulu, adzatitumizira kuœala kwa dzuwa lam’maœa kuchokera kumwamba. Kuœala kwake kudzaunikira onse okhala mumdima wabii ngati wa imfa, kudzatitsogolera pa njira ya mtendere.”

Akunenatso akuti, “Akupereka nzeru za chipulumutso kwa anthu ake kudzera mukukhululukira machimo ao.” Kodi ndani amene iye ananena kudzapereka nzeru za chipulumutso? Yohane Mbatizi, kudzera mu Mau a Mulungu, anatipatsa nzeru zoti Yesu ndi Mwana wa Mulungu amene anachotsa machimo adziko lonse.

Tsono tiyeni tione m’buku la Marko 1:1-5. “Uwu ndi Uthenga Wabwino wonena za Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu. Udayamba monga m’neneri Yesaya adalembera m’buku mwake kuti, Mulungu akuti, ‘Ndidzatuma wamthenga wanga m’tsogolo mwako kuti akakonzeretu njira yoti iwe udzapitemo.’ Liwu lamunthu wofuula m’chipululu: akunena kuti, ‘Konzani mseu wodzadzeramo

Ambuye, ongolani njira zoti adzapitemo.’ Zimenezi zidachitikadi pamene Yohane Mbatizi adaafika ku chipululu, ‘Tembenukani m’tima, mubatizidwe, ndipo Mulungu adzakukhululukirani machimo anu.’ Anthu ochokera ku dera lonse la Yudea ndi aku Yerusalemu ankhadza kwa iye. Tsono ankati iwo akaulula machimo ao, iye nkuwabatiza mu Mtsinje wa Yolodani.”

Anthu anatembenuka m’tima kupembedza mafano aanthu amitundu ndipo anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Koma Yohane achitira umboni, “Ndikum’batizani ndi madzi kuti m’tembenukire kwa Mulungu. Koma Mwana wa Mulungu adzabwera ndipo adzabatidwa ndi ine kuti machimo anu onse akhale pa iye. Ndipo ngati mukhulupilira monga m’mene mbatizidwa ndi ine, machimo anu onse adzakhala pa iye monga ngati m’mene machimo anatengedwera Mchipangano Chakale pamene anali kusanjika manja pa mbuzi.” Uwu unali umboni umene Yohane anali kuchita.

Kunena kuti Yesu anabatizidwa mu mtsinje wa

Page 128: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

128 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Yolodani kutanthauza kuti iye anabatizidwa mu mtsinje wa imfa. Timaimba pa maliro, “♪M’chimwemwe ndi chimwemwe, Tidzakumana mu mbali mwa mtsinje wokongola. Tidzakumana mu mbali mwa mtsinje wa Yolodani.” Mtsinje wa Yolodani ndi mtsinje imfa. Yesu anabatizidwa mu mtsinje wa imfa.

UBATIZO UMENE UNADUTSA PA MACHIMO ATHU

Kodi kusanjika manja M’chingapano

Chatsopano ndi chiyani?

Ubatizo wa Yesu Mu Mateo tiwerenga kuti, “Pa masiku

amenewo, Yesu adachoka kuGalilea kubwera kwa

Yohane ku mtsinje wa Yolodani, kuti Yohaneyo amubatize. Yohane poyetsa kukana, adati, ‘Ndine amene ndiyenera kubatizidwa ndi inuyo. Nanga mukubweranso kwa ine kodi?’ Koma Yesu adamuyankha kuti, ‘Tsopano lino vomera, chifukwa ndi m’mene tiyenera kuchitira zonse zimene Mulungu akufuna.’ Apo Yohane adavomera. Yesu atangobatizidwa, adatuluka m’madzimo. Pomwepo kuthambo kudatsekuka, ndipo adaona mzimu wa Mulungu akutsika ngati nkhunda nkutera pa Iye. Tsono kuthamboko kudamveka mau akuti, ‘Uyu ndiye mwana wanga wapam’tima ndimakondwera naye kwambiri.”’(Mateo 3:13-17)

Yesu anadza ku mtsinje wa Yolodani ndipo anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. “Undibatize.” “Koma ndiyenera kubatizidwa ndi inu, inunso mukubwera kwa ine?” Wam’kulu wansembe wakumwamba ndi wadziko lapansi anakumana.

Monga m’buku la Aheberi, Yesu Khristu ndi wam’kulu wa nsembe kwa muyaya monga mwa

Page 129: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

129 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Lamulo la Makezedzi. Ndiopanda fuko. Iye sanali wafuko la Aroni, kapena la munthu aliyense panso pano. Iye ndi Mwana wa Mulungu, M’lengi wathu. Iye ndiye Iye. Choncho Iye alibe fuko, koma anasiya ulemerero wakumwamba ndikubwera pa dziko lapansi kuti apulumutse anthu ake.

Chifukwa chimene Iye anadzera pa dziko lapansi kudzera mu ubatizo umene anambatiza Yohane Mbatizi. “Koma Yesu anayankha ndipo anati kwa iye, ‘tsono iwe lola, chifukwa ndikoyenera kuti tikwaniritse zimenezi. Apo iye analola.’”

“Tsono lola kuti zichitike.” Lola! Yesu nalamula onse oimirira anthu ndi kuweremitsa mutu wake. M’buku la Chipangano Chakale, pamene nsembe inalikuperekedwa kwa Mulungu, wochimwa kapena wam’kulu wansembe analukusanjika manja pamutu wansembe ndipo imatenga machimo. ‘Kusanjika manja’ kutanthauza ‘Kuperekedwa.’

Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Ichi chitanthauza kusanjika manja mu Chipangano Chakale. ‘Kuperekedwa,’ ‘kuikidwa m’manda,’ ‘kusambitsidwa’ ndi ‘kupereka nsembe’ ndi chimodzimodzi.

Chipangano Chatsopano ndi choona koma Chipangano Chakale chinali chithunzithunzi. Pamene munthu wochimwa wasanjika manja ake pa mutu wa mwana wankhosa M’chipangano Chakale, machimo ake anali kuperekedwa kwa manawa nkhosa ndipo nkhosayo imafa. Pamene mwana wankhosa anafa, anaikidwa mu manda! Machimo amaperekedwa ku mwana wankhosa a munthu amene wasanjika manja pa mutu wankhosa, motero nkhosayo imafa ndi machimo! Ngati machimo aperekedwa ku mwana wankhosa, kodi ndani amene anapereka mwana wankhosa popanda tchimo?

Tingathe kunena kuti mpango nditchimo nsembe yochotsera machimo, mwana wankhosa. Ndipo ngati ndisanjika manja pa nsembeyo,

Page 130: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

130 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

tchimolo liperekedwa pa nsembeyo, mwana wankhosa. Mulungu Iye mwini anaganiza kuti ziyenera kutero. “Sanjikani manja anu,” kuti mukhululukidwe machimo anu, munthu ayenera kusanjika manja ake. Akatero, akhala opanda tchimo. Ubatizo wa Yesu ndi wosambitsa, kuikidwa mumanda ndi kupereka machimo pa Iye. Ili ndi limene ndi tanthauzo lake.

Kodi mau otikwaniritsa chifuniro cha Mulungu kutanthauza chiyani?

Ndikusamba machimo

onse kudzera mukupereka machimo onse pa Yesu

Motero pamene Yesu anabatizidwa ananyamula

machimo onse adziko lapansi, ndizoona kuti machimo onse anaperekedwa pa Iye. Machimo

onse adziko la pansi anaperekedwa pa Yesu ndipo anthu onse naomboledwa. Ndichimodzimodzi monga mu Chipangano Chakale machimo anali kuperekedwa pa nsembe yonyamula machimo. Yesu anabwera mu dziko lapansi ndi kumtsinje wa Yolodani, ndipo Yesu anati, “Tsopano lino vomera, chifukwa ndi m’mene tiyenera kuchita zonse zimene Mulungu akufuna.” Apo Yohane adavomera. Matero 3:15.

Iye anavomereza Iye yekha kuti abatizidwe. Yesu anauza Yohane kuti ndikoyenera kuti iwo akwaniritse chiyero cha ubatizo wake. ‘Chiyero’ chitanthauza ‘chinthu chabwino ndi choyenera.’ ‘Choncho’ chinali choyenera kuti iwo akwaniritse chiyero. Ichi chitanthauza kuti chinali chabwino kuti Yohane abatize Yesu, ndipo kuti Yesu abatizidwe ndi Yohane kuti atenge machimo onse.

Mulungu anavomera chiombolo kudzera mu ubatizo wa Yesu, ndi nsembe yake, ndi chikhulupiliro chathu. “Anthu onse ovutika ndi uchimo ndipo anazunzidwa ndi Satana chifukwa

Page 131: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

131 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

cha machimo ao. Motero kuti, anthu apulumutsidwe ndi kupita kumwamba, iwe, monga ngati moirira anthu ndi badwo wa Aroni, uyenera kundibatiza m’malo mwa anthu onse. Ndiyenera kubatizidwa ndi iwe. Apo ntchito yachiombolo izakwanitsidwa.”

Yohane anabatiza Yesu. Anasanjika manja ake pa mutu wa Yesu ndi machimo onse adziko lapansi anatengedwa ndi Yesu. Yesu ndi Mpulumutsi amene anachotsa machimo athu onse. Tinapulumutsidwa kudzera mukukhulupilira izi.

Iye atabatizidwa, ntchito yoyamba ya Yesu pa gulu m’mtsinje wa Yolodani, kudzera mwa kuombola anthu onse. Anayenda ndi kulalika Uthenga Wabwino kwa zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi atasenza machimo adziko lapansi pa mutu wake.

Anauza m’kazi amene anagwidwa pa chigololo, “Inenso sindikutsutsa.” Iye sanamutsutse chifukwa Iye anatenga machimo ake onse ndipo anali pafupi kumwalira pa mtanda chifukwa cha

anthu, pamene anali kupemphera pa malo otchedwa Getitsemane, anapemphera katatu kupempha Atate kuti chikho chimupitirire posatchedwa anadzipereka ndikunena kuti, “Osati monga nchifukwa, koma m’mene mufunira.”

“SUUYU MWANA WANKHOSA WA MULUNGU UJA, WOCHOTSA MACHIMO A ANTHU APA DZIKO LONSE LAPANSI!”

Ndi machimo angati amene Yesu anatichotsera?

Machimo onse adziko

lapansi M’buku la Yohane 1:29, “M’mawa mwake

Page 132: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

132 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Yohane adaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo adatati, ‘Suuyu Mwana Wankhosa wa Mulungu uja, wochotsa machimo aanthu apa dziko lonse lapansi!’” Unali umboni wake.

Mwana wa Mulungu anadza pa dziko lapansi kuti achotse machimo onse adziko lapansi. Yohane Mbatizi anachitira umboni kachiœiri. M’buku la Yohane 1:35, “Tsiku lina, Yohane anaimirira ndi ophunzira aœiri, pamene anayang’ana Yesu pamene anali kuyenda, anati, ‘suuyu Mwana Wankhosa wa Mulungu!’”

Mwana Wankhosa wa Mulungu kutanthauza kuti Iye ndi nsembe yeniyeni ya Chipangano Chakale amene anafera machimo a Aisraele. Inu ndi ine, Mwana wa Mulungu, M’lengi wathu anabwera pa pansi pano kuti achotse machimo aanthu onse. Machimo onse kuchokera patsiku loyamba mpaka pa tsiku lotsiriza, kuchokera ku machimo oyamba mpaka machimo onse, kuchokera ku zochitika ndi zolakwa zathu. Anatiombola ndi ubatizo wake ndi mwazi wake pa

mtanda. Yesu anachotsa machimo athu onse ndikupatsa

chiombolo. Kodi mukumvetsa izi? “Mwana Wankhosa wa Mulungu uja, wochotsa machimo aanthu apa dziko lonse lapansi.”

Kodi chaka chimenechi ndi chiti? Ndipafupifupi zaka 2000. Izi zitanthauza kuti papita zaka 2000 kuchokera pa nthaœi imene Yesu adabwera pa dziko lino lapansi. Anthu ena akuti ndi m’chaka cha 1 A. chimene Yesu anabadwa. Nthaœi imene Yesu anali asanabadwe imatchedwa B.C. pa chingerezi. Motero patha zaka zikwi ziœiri (2000) kuchokera nthaœi imene Yesu anabwera pa dziko lino lapansi.

M’chaka cha 30 A.D., Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Ndipo tsiku lina Yohane anafuula kwa anthu, “Suuyu Mwana wa Nkhosa wa Mulungu amene anachotsa machimo onse adziko lapansi.” “Suuyu” Yohane anali kuuza anthu kuti akhulupilire mwa Yesu amene anachotsa machimo awo onse. Iye anali kuchitira

Page 133: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

133 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

umboni kuti Yesu anali Mwana Wankhosa wa Mulungu, amene anatipulumutsa ku machimo athu onse.

Yesu anachotsa machimo athu onse ndikuthetsa nkhondo yathu yolimbana ndi uchimo. Tsopano ndife anthu opanda uchimo chifukwa Yesu adachotsa machimo athu onse. Ngakhale Yohane Mbatizi anachitira umboni kuti Yesu anachotsa machimo athu onse, machimo anu ndi anga. “Iyeyu anabwera ngati mboni, kudzachitira umboni kuœala kuja, kuti anthu onse akhulupilire chifukwa cha umboni wakewo” (Yohane 1:7).

Kodi tikadadziœa bwanji Yohane akanapanda kuchitira umboni kuti Yesu anachotsa machimo athu onse? Baibulo limatiuza kuti Iye anafa chifukwa cha ife, koma ndi Yohane Mbatizi yekha amene amachitira umboni kuti Yesu anatichotsera machimo athu onse.

Kodi machimo adziko lapansi ndi angati?

Machimo onse amene amachita

kuchokera pa chiyambi ndi kutha kwa dziko

Anthu ambiri adachitira umboni Yesu atafa,

koma Yohane Mbatizi adachitira umboni Yesu akali moyo. Ngakhale ophunzira a Yesu adachitira umboni za ntchito yoombola anthu onse ku machimo awo. Iwo anachitira umboni kuti Iye anachotsa machimo athu onse, ndiponso kuti Iye ndiye Mpulumutsi wathu.

Yesu anachotsa machimo aanthu onse pa dziko lino lapansi. Inu simunakwane zaka 100, sichoncho kodi? Yesu anachotsa machimo onse adziko lapansi ali ndi zaka makumi atatu (30). Taonani chithunzi ichi.

Page 134: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

134 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Adamu→Abrahamu→Ubatizo wa Yesu→nthaœi ino→mapeto adziko 4000BC 2000 B.C. 30 AD 2000 A.D. ? A.D.

Machimo onse adziko lapansi

Tiyerekeze kuti panatha zaka 4000 Yesu asanabwere. Pasathe zaka 2000 kuchokera pa nthaœi ya Yesu. Sitikudziœa za nthaœi imene idzakhalire, koma chimaliziro chilipodi ndipo chidzachitika. “Alefa ndi Omega ndine. Ndiye kuti woyamba ndi wotsiliza, chiyambi ndi chimaliziro ndine.”(Chivumbulutso 22:13)

Motero kudzakhaladi chimalirizo. Ndipo ife tili pafupi kuloœa chaka cha 2003. Yesu anachotsa machimo athu m’chaka cha 30 A.D, nthaœi imeneyi nkuti kutatsala zaka zitatu kuti apachikidwe pa mtanda.

“Mwana Wankhosa wa Mulungu amene adachotsa machimo adziko lapansi.” Iye anachotsa machimo adziko lapansi, machimo anu ndi anga. Papita nthaœi yaitali kwambiri

kuchokera pamene Yesu aanabadwa. Pafupifupi zaka 2000. Tsopano tili kuganizira kuti patha zaka 2000 kuchokera pamene Yesu anachotsa machimo athu onse. Ndipo timachimwabe mpaka pano pamene tili ndi moyo. Yesu ndi Mwana Wankhosa wa Mulungu amene anachotsa machimo adziko lapansi.

Timayamba kukhala m’dziko lino lapansi pa nthaœi imene ife tangobadwa. Kodi tonse timachimwa tikangobadwa, kapena ai? —Inde timachimwa.— Tione nthaœi yonseyi. Kuchokera panthaœi imene ife tinabadwa kufikira zaka 10, kodi nthaœi imeneyi timachimwa kapena ai sitichimwa? —Inde timachimwa.— Nanga kodi machimo amenewo anaperekedwanso kwa Yesu? Kapena ai. —Inde anaperekedwa.— Chifukwa chakuti Yesu anasenza machimo athu, Iye ndi Mpulumutsi wathu? Machimo onse anaperekedwa kwa Yesu.

Kodi kuyambira pa msinkhu wa zaka humi kufikira 20, timachimwa? Inde. Timwachimwa

Page 135: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

135 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

mkati mwa mitima yathu, mu ntchito zathu… Timaika mtima kwambiri pa uchimo. Timaphunzitsidwa kuti tisamachimwe koma ife timachimwa ndipo timachita machimo mosavuta.

Ndipo Mulungu amatiuza kuti machimo athu onse anaperekedwa kwa Yesu Khristu. Iye adzaadziœa m’mene ife tiriri, nchifukwa chake Iye anatengelatu machimo athu.

Kodi pa dziko lino lapansi timakhalapo nthaœi yaitali bwanji? Tiyerekeze kuti timakhalapo zaka makumi asanu ndi aœiri (70). Ngati tiphatikiza machimo amene takhala tili kuchita pa zaka zonsenzi, kodi machimo athu akadakwana angati? Ndipo ngati tingaphatikize machimo athu amene takhala tikuchita zaka zonsezi mu galimoto imene imanyamula katundu wolemera matani 8, mudaona kuti machimo athu akhoza kudzala m’magalimoto okwana 100.

Tangoganizani zamachimo amene ife tidzachite pa moyo wathu wonse. Kodi amenewo ndi machimo adziko lapansi kapena ai? Amenewo ndi

machimo adziko lapansi. Timachimwa ngakhale pamene tiri ndi za 20 kapenanso zaka 30, ndipo amenewanso ndi machimo adziko lapansi.

MPULUMUTSI WA ANTHU, YESU KHRISTU

machimo angati mwa ife?

Machimo onse a makolo athu, machimo athu ndi machimo adzidzikulu zathu mpaka kutha

kwa dziko lino Yesu amatiuza kuti iye anachotseratu machimo

athu onse. Yesu sananene mwa Iye yekha kuti, ‘Ndibatize,’ motero Mulungu anatuma mtumiki

Page 136: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

136 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

wake, woimirira wa anthu amene anasankidwa ndi Mulungu. Ndipo adzamtchula dzina lake lakuti “Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate a Muyaya, Mfumu ya Mtendere,” mwa Iye yekha, mwa nzeru zake, mwa mphamvu zake Iye anatuma woimirira wa anthu, ndipo Iye mwini amene ndi mwini amene ndi Mwana wa Mulungu anabwera monga munthu nadzachotsa machimo onse adziko lapansi. Kodi ichi sichipulumutso chodabwitsa?

Ichi ndi chipulumutso chodabwitsa, sichoncho? Motero pamene Iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi anachotseratu machimo onse aanthu pa dziko lapansi ndi kuombola anthu ku machimo awo pakupachikidwa pa mtanda. Iye anaombola ife tonse. Taganizani. Machimo anu onse kuchokera pa m’sinkhu wa zaka 20 kufika 60, kufika 70 kudzafika pa zaka 100, ndipo palinso machimo aœana wanu. Kodi Yesu ananyamula machimo onsewa, kapena ai? Inde Iye anachotsa machimo onse. Iye ndi Yesu Khristu, Mpulumutsi

wa anthu onse. Tsono popeza kuti Yohane Mbatizi anapereka

machimo athu onse kwa Yesu, ndiponso popeza kuti Mulungu adazikonzeratu, tikhoza kupulumutsidwa ngati tikhulupilira mwa Yesu Khristu. Kodi inu ndi ine ndife anthu ochimwa? Kodi machimo athu anaperekedwa kwa Yesu kapena sanaperekedwe? —Sindifenso anthu ochimwa ai, ndipo machimo athu onse anaperekedwa kwa Yesu.—

Ndani amene anganene kuti padziko lapansi pali machimo? Yesu anachotsa machimo onse a dziko lapansi. Iye anadziœanso kuti tidzakhala tikuchimwa mtsogolo, ndi machimo onse amene tidzachite kutsogolo, Yesu anachotsanso. Ena mwa ife tisanafike zaka 50 zakubadwa, ndipo tisanafike theka la zaka zimenezi koma kamba ngati kuti takhalitsa pa dziko lino lapansi.

Alipo ambiri mwa ife amene ali kukhala ndi moyo wa chisokonezo. Kapena ndi longosole motere. Kodi thekala moyo wa duœa ndi chiyani?

Page 137: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

137 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Ndi pafupifupi maora khumi ndi aœiri. Mwa mwayi! Ndinakumana ndi munthu wakuti

wakuti amene anadziœa za madzi a duœa limeneli ndipo ndinali pafupi kufa. Komabe ndi nadziœa kuti silikhala nthaœi yaitali. Chifukwa linali litakwana kale theka la moyo wake.

Pokwana 7 kapena 8 madzulo limaona kuwala kwake kotsiliza, ndipo kwa nthaœi yochepa limafa. Ena amakhala kwa maora 20, ena amatha kukhala maora 21 kapenanso kufika maora 24. Akhoza kumaona ngati akhala ndi moyo nthaœi yaitali, koma kwa ife kodi muli kuona bwanji? Pamene tikwanitsa zaka 70 kapena 80 zakubadwa, mwina tikhoza kumanena kuti osamandiseketsa. Zimene akhala ali kuona pa moyo wawo kwa ife nzopanda ntchito m’maso mwathu.

Mulungu wa muyaya. Iye amakhala opanda mathero. Amaganiza za chiyambi ndi mapeto. Monga Mulungu wa muyaya, amakhala opanda malekezero. Monga Mulungu wa muyaya, Iye amatiyang’anira mwa mphamvu zake.

Ndipo nthaœi itakwana, Iye anachotsa machimo onse adziko lapansi, kufa pa mtanda, ndipo anati, “Kwatha.” Ndi Iye anauka kwakufa patsiku lachitatu ndipo anakwera kumwamba. Ndipo ali kukhala kumeneko kwa nthaœi zosatha. Tsopano alikutiona ife kuchokera kumene aliriko.

Ndipo munthu wina anaena kuti, “Aa, ndachimwa kwambiri. Ngakhale ndili ndi zaka 20 zokha zakubadwa.” “Ndakhala zaka 30 koma ndachimwa kwambiri, zanyanya. Kodi ndidzakhulukidwa bwanji?”

Koma Ambuye wa Mphamvu zonse adzanena kuti, “Musandiseketse. Ine sindinaombole machimo anu okha ai, ndi naombolanso makolo anu inu musanabadwe ku machimo awo, ndiponso ana anu amene adzabwera inu mutamwalira.” Ambuye ali kunena zimene kwa inu. Kodi mukuhulupilira zimenezi?

Khulupilirani. Kuti mulandire mphatso ya chipulumutso imene mudzapatsidwe mwa ulere. Ndi kukaloœa mu ufumu wakumwamba.

Page 138: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

138 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Musakhulupilire zimene inu m’maganiza, koma khulupilirani m’mau a Mulungu. Umu ndim’mene tiyenera kuchitira zimene Mulungu akufuna. Chifuniro chonse cha Mulungu chinakwaniritsidwa kale ndi Mwana Wankhosa wa Mulungu amene adachotsa machimo onse adziko lonse lapansi. Kodi Iye anachitadi zimenezi kapena ai? Inde anachita.

Kodi Yesu ananena kuti chiyani pamene

anali kufa pa Mtanda?

“Kwatha” Yesu Khristu ananyamula machimo onse a

dziko lapansi, ndipo bwalo la Pontiyo Pilato linalamula kuti Yesu aphedwe, ndipo anapachikidwa pa Mtanda.

“Iye adasenza mtanda wake, adatuluka naye

mu nzinda kupita ku malo otchedwa Malo a Chibade cha mutu wa Chiyuda amati Gologota. Kumeneko adampachika pa mtanda. Adapachikanso anthu ena aœiri, wina ku dzanja la manja, wina kudzanja lake la manzere, Yesu pakati. Pilato adalemba chidziœitso nachiika pa mtandapo. Adalembapo kuti, Yesu waku Nazarete, Mfumu ya Ayuda. Ayuda ambiri adachiœerenga chidziœitsocho, chifukwa pamalo pamene Yesu adaapachikidwapo panali pafupi ndi mzinda wa Yerusalemu; chidziœitsocho chidalembedwa m’chilakhulo cha Ayuda, cha Aroma ndiponso cha Agriki” (Yohane 19:17-20).

Tiyeni tione zimene zinachitika Yesu atapachikidwa pa mtanda. “Yesu adadziœa tsopano kuti zonse wakwaniritsa zimene Malembo adaanena.” Iye ananyamula machimo athu onse monga Malembo adaanena. Iye adati, “Ndili ndi ludzu. Pomwepo panali mbiya yodzaza ndi vinyo wosasa; asilikali aja adaviika chinkhupule m’vinyo

Page 139: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

139 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

wosasayo, nkuchitsomeka kuka mtengo ka hisope nachikitsa pa kamwa pake. Yesu atalandira vinyo wosasayo adati, “Zonse zakwaniritsidwa” kenaka adaœeramitsa mutu napereka mzimu.” (Yohane 19:28-30).

Iye atalandira vinyo yosasayo, adati ‘kwatha’ kenaka anaœeramitsa mutu napereka mzimu wake. Anafa. Koma Iye anaukanso mukucha wake nakwera kumwamba.

Tiyeni tiœerenge pa Ahebri 10:1-9. “Malamulo a Mose ndi chithunzi chabe cha madalitso amene alikudza, osati madalitso enieniwo, ngakhale nsembe zimodzimodzi zimaperekedwa kosalekeza chaka ndi chaka, Malamulowo sangathe konse mwa nsembezo kuœasandutsa angwiro anthu oyandikira pamenepo. Anthu opembedza Mulungu aja akadayeresedwa kwathunthu, sibwenzi m’tima monga zilirimu, nsembezo zimakumbutsa zamachimo ao chaka ndi chaka. Magazi ang’ombe zamphongo ndi atonde sangathe konse kuchotsa

machimo. Nchifukwa chake, pamene Khristu adadza pansi pano, adati, Inu Mulungu simudafune nsembe kapena zopereka, koma thupi mudandikonzera. Nsembe zootcha kwathunthu ndi nsembe zoperekera machimo, simudakondwere nazo. Tsono ine ndidati – Inu Mulungu ndibweratu kuti ndi chite zimene mukufuna, paja zidalembedwa choncho ponena zaine m’buku la Malamulo – motero poyamba adati, nsembe kapena zopereka, nsembe zopsereza kwathunthu kapenanso nsembe zoperekera machimo, simudazifune ndipo simudakondwere nazo. Zimenezi n’zimene Malamulo adanena kuti ziperekedwe. Koma pambuyo pake adati, ndabweratu kuti ndichite zimene mukufuna. Motero Khristu adathetsa mphamvu za nsembe za mtundu woyamba zija, kuti m’malo mwake akhazikitse nsembe ya mtundu wa chiœiriyo.”

Page 140: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

140 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

CHIOMBOLO CHA MUYAYA

Kodi tingathetse bwanji machimo athu atsiku ndi tsiku

titakhulupilira mwa Yesu?

Pakuvomera kuti Yesu ananyamula kale machimo athu kudzera mu

ubatizo wake Malamulo ali ndi chithunzithunzi cha zinthu

zabwino zimene zili kudza. Nsembe za M’chipangano Chakale, nkhosa, ndi mbuzi, zinaulura kuti Khristu adzabwera ndikudzachotsa machimo athu monga momwe adaali kuperekera nsembe M’chipangano Chakale.

Anthu onse a M’chipangano Chakale, monga Davide, Abrahamu ndi ena onse anadziœa ndi kukhulupilira zimene m’chitidwe wopereka nsembe unali kutanthauza kwa iwo.

Ichi chinaulura kuti Mesiya, Khristu (kutanthauza Mpulumutsi) adzabwera tsiku lina ndikudzachotsa machimo athu onse. Iwo anakhulupilira chiombolo chawo ndipo anapulumutsidwa mwa chikhulupiliro.

Malamulo anali chithunzithunzi cha zinthu zabwino zimene zinali kubwera kutsogolo. Kupereka nsembe za machimo awo tsiku ndi tsiku chaka ndi chaka sikunatiombole kotherathu. Choncho munthu wa ngwiro, amene alibe chilema, Mwana wa Mulungu anayenera kubwera ku dziko lino lapansi.

Ndipo Iye anati anabwera kudzachita chifuniro cha Atate ake monga zinalembedwa m’mabuku onena za Iye. Ndidati Inu Mulungu, ndabweratu kuti ndichite zimene mukufuna, paja zidalembedwa ponena zaine M’buku la Malamulo. Motero Khristu adathetsa za nsembe za mtundu woyamba zija, kuti m’malo mwake akhazikitse nsembe za mtundu wa chiœiriwo. Ife ndife anthu oomboledwa chifukwa Yesu Khristu anachotsa

Page 141: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

141 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

machimo onse monga zinalembedwa M’chipangano Chakale ndipo chifukwa chakuti timakhulupilira mwa Iye.

Tiyeni tionenso pa Ahebri 10:10 “Ife tidayeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake limene Iye adapereka kamodzi kokhako.” Tinayeretsedwa kudzera mu nsembe imene Yesu anaipereka ndi thupi lake, nsembeyi Yesu anaipereka kamodzi kokha. Kodi tinayeretsedwadi kapena ai? —Inde tinayeretsedwa.—

Kodi ichi chitanthauzanji? Mulungu Atate anatumiza Mwana wake ndikupereka machimo onse kwa Mwana wakeyo kudzera mu ubatizo wake ndi ku mulanga kamodzi kokha. Ndipo anaombola ife tonse amene tinali kuvutika ndi machimo. Ichi chinali chifuniro.

Pofuna kutipulumutsa, Yesu adadzipereka kamodzi kokha, kuti ife tiyeretsedwe. Zoonadi tinayeretsedwa. Yesu Khristu adapereka nsembe ya machimo athu popereka thupi lake ndipo anafa m’malo mwathu kuti ife tisaœeruzidwe.

Nsembe ya M’chipangano Chakale anali kupereka tsiku ndi tsiku kuti Machimo amene anthu anali kuchita tsiku ndi tsiku achotsedwe.

PALI NKHANI YA YESU ALI KUTSUKA MAPAZI A PETRO

amene ife tiyenera kulapa m’mapemphero?

Ai.

Pa Yohane 13, pali nkhani ya Yesu ali kutsuka

mapazi a Petro. Iye adatsuka mapazi a Petro kuti amuonetse kuti iye (Petro) adzachimwanso mtsogolo ndiponso kuti machimo ake a m’tsogolowo adakhululukidwa kale. Yesu anadziœa kuti Petro adzachimwanso m’tsogolo, motero iye anathira madzi m’mbale ndi kutsuka

Page 142: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

142 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

mapazi a Petroyo. Petro anayetsa kukana, koma Yesu adati,

“Zimene ndikuchitazi, sukuzidziœa tsopano, koma udzadzidziœa m’tsogolo muno.” Pamenepa Yesu ali kuuza Petro kuti udzachimwanso. Udzandikana ndikuchimwanso ngakhale kuti ndakuchotsera machimo ako onse. Udzachimwanso ine nditakwera kumwamba. Choncho ine ndikutsuka mapazi akowa kuchenjeza Satana kuti asadzakuyetse chifukwa ndakuchotsera kale machimo ako a m’tsogolo.

Kodi mukuganiza kuti Yesu anatsuka mapazi a Petro pofuna kutiuza kuti tiyenera kumalapa machimo athu tsiku ndi tsiku? Iai. Itakadati tizilapa machimo tsiku ndi tsiku kuti tiomboledwe, Yesu sakanachotsa machimo athu kamodzi kokha.

Koma Yesu anaena kuti Iye anatiyeretsa kamodzi kokha. Tikadati tizilapa machimo athu tsiku ndi tsiku, tikanabwereranso ku Chipangano Chakale. Nanga akadakhala olungama ndani? Akadapulumutsidwa ndani? Ngati tikhulupilira

Mulungu kodi ndani amene angakhale opanda uchimo?

Ndani akanayeretsedwa pakulapa? Ife timachimwa mosalekeza tsiku ndi tsiku, nanga tingapemphe bwanji chikhululukiro cha machimo amenewa? Ife timaœala machimo amene tachita m’maœa pakutha kwa tsiku limenelo, ndiponso machimo amene tachita usiku pakuyamba kwa tsiku lina. Nkosatheka kuti inu ndi ine tilape machimo athu onse kotheratu.

Choncho Yesu anabatizidwa kamodzi, anadzipereka Yekha pa mtanda kamodzi kokha kuti ife tiyeretsedwe. Kodi mukumvetsa zimenezi? Tinaomboledwa kamodzi kokha kumachimo athu onse. Sitipulumutsidwa pakulapa machimo athu tsiku ndi tsiku.

Tinapulumutsidwa pakukhulupilira kuti Yesu anatichotsera machimo athu onse, machimo anu, ndi anga.

“Wansembe aliyense amaimirira tsiku ndi tsiku nkumatumikira ndipo amapereka nsembe

Page 143: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

143 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

imodzimodzi mobwereza bwereza. Komabe nsembe zimenezi sizingathe konse kuchotsa machimo. Koma Khristu adapereka nsembe imodzi yokha yochotsera machimo onse. Ndipo ataipereka, adakakhala ku adzanja lamanja la Mulungu. Kumeneko akudikira tsono kuti Mulungu asandutse adani kukhala ngati chopondapo mapazi ake. Mwa nsembe imodzi yomweyo wasandutsa angwiro kwa muyaya onse amene iye akuœaretsa. Mzimu Woyera nayenso amatitimikizira zimenezi. Poyamba Iye akuti, Nachi chipangano chimene ndidzachita nawo atapita masiku amenewo, akutero Ambuye: Ndidzaika Malamulo anga m’mitima mwawo ndidzachita kuœalemba m’maganizo ao. Pambuyo pake akutinso sindidzaœakumbukiranso konse machimo ao. Pamene Mulungu wakhululukira zonsezi, sipafunikanso nsembe yoperekera machimo” (Ahebri 10:11-18).

Kodi Mau akuti “Pamene Mulungu wakhululukira” akutanthauza chiyani? Pa 10:18,

Mauwa akutanthauza kuti tchimo liri lonse linachotsedwa popanda kusiyanako. Mulungu anakhululukira machimo onse. Kodi mukulupilira zimenezi? “Pamene Mulungu wakhululukira zonsezi, sipafunikanso nsembe yoperekera machimo.”

Tiyeni tiyerekeze, ngati Yohane Mbatizi sanasanjike manja ake pa Yesu, mwina, ngati iye sanambatize Yesu, kodi tikanaomboledwa? Sitikanaomboledwa.

Tiganizire zakumbuyo. Ngati Yesu sanakasankha Yohane Mbatizi kuimirira anthu onse ndi kuchotsa machimo onse kudzera mwa iye. Kodi akanachotsa machimo athu onse? Iye sakanatha ai.

Malamulo a Mulungu ndi chilungamo. Ali olungama. Iye sakananena kuti Iye ndi Mpulumutsi wathu, kuti achotsa machimo athu onse. Iye analikuyenera kunyamula machimo athu mu thupi lake. Kodi chifukwa nchiyani Yesu, Mulungu, anabwera kwa ife mu thupi? Chifukwa

Page 144: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

144 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

analikudziœa machimo onse a munthu, machimo amu m’tima ndi machimo amu thupi kuti achotse machimo onse aanthu, Iye, Mwana wa Mulungu anali kuyenera kubwera kwa ife mu thupi.

Yesu akanakhala kuti sanabatizidwe, machimo athu sakanachoka. Akanapachikidwa asanachotse machimo athu, imfa yake ikanakhala yopanda ntchito.

Pamene anayamba ntchito yake pa zaka 30 anabwera kwa Yohane Mbatizi mu mtsinje wa Yolodani kuti abatizidwe. Ntchito yake ya pa gulu anayamba ali ndi zaka 30 ndipo anatsiriza pazaka 33. Pamene anali ndi zaka 30, anabwera kwa Yohane Mbatizi kuti ambatize. “Tsopano vomera kuti zichitike, chifukwa ndi koyenera kuti tichite zimenezi kuti anthu onse apulumutsidwe ndi kukhala olungama. Ndi chinthu choyenera kuchita. Tsono, ndibatize.” Inde, Yesu Khristu anabatizidwa kuti aombole anthu onse.

Chifukwa Yesu anabatizidwa ndikuchotsa machimo athu onse ndiponso machimo athu onse

anaperekedwa pa Iye kudzera mukusanjikidwa manja pa Iye ndi Yohane Mbatizi, Mulungu sanayang’anenso Yesu pamene anali kumwalira pa mtanda. Ngakhale kuti Yesu anali mwana wake Yekhayo, Iye anavomereza kuti amwalire.

Mulungu ndi chikondi, koma anavomera kuti Mwana wake amwalire. Motero kuti, maola atatu, kunali mdima pa dziko lonse. Yesu anafuura kwakukulu kuti, “Eli, Eli lama sabakatani?” Ndiye kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga mwandisiyiranji?” Yesu ananyamula machimo athu onse ndikulandira chiweruzo pa mtanda m’malo mwa ife. Motero anatipulumutsa. Popanda ubatizo wa Yesu, imfa yake yikanakhala yopanda phindu.

kapena wolungama?

Munthu wolungama ndi amene ali ndi

tchimo mum’tima wake.

Page 145: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

145 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Ngati Yesu akanafa pa mtanda popanda kuchotsa machimo athu onse, popanda kubatizidwa, imfa yake siikanatha kutiombola. Kuti atiombole Yesu analikuyenera kubatizidwa ndi Yohane, woimirira anthu onse ndikulandira chiweruzo pa mtanda kuti onse amene akhulupilira Iye athe kupulumutsidwa.

Choncho, kuchokera pa matsiku a Yohane Mbatizi mpaka lero, Ufumu wakumwamba umavutika ndi mphamvu ya Satana, chifukwa Yohane Mbatizi anapereka machimo athu onse pa Yesu, machimo anu ndi anga anachotsedwa. Choncho inu ndi ine tikhoza kuitana Mulungu kuti Atate ndi mosakaika tilowa mu Ufumu wakumwamba.

M’buku la Ahebri 10:18 akuti, “Pamene Mulungu wakhululukira zonsezi, sipafunikanso nsembe yoperekera machimo.” Yesu analipira ngongole yathu yonse ya machimo, kodi muyeneranso kulipira ngongole?

Panali munthu wina amene kumwa kwake

kolezera kunamuika mu ngongole zambiri. Tsiku lina mwana wake anamchitira chifundo ndi kumubwezera ngongole zake zonse. Bambo wake ngakhale amwe koma sanalitso ndi ngongole ai.

Ichi ndi chimene Yesu anachita kwa ife. Analipira mokwanira zonse zokhuza machimo athu. Osati machimo athu amoyo uno wokha, koma machimo adziko lonse lino. Onse anaperekedwa pa Yesu pamene anali kubatizidwa. Kodi inu ndinu ochimwa lero? Ai, simuli ochimwa.

Ngati tadziœa Uthenga Wabwino wachipulumutso kuchokera pachiyambi, ndi kotheka kuti tikhulupilire Ambuye athu Yesu. Koma m’mene ziliri zikumveka ngati za tsopano kuti anthu ambiri sakumvetsa izi.

Koma ichi sichinthu chatsopano. Zinaliko kuyambira pa chiyambi. Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu Woyera unalembedwa mu Mau a Mulungu ndipo masiku onse akugwira ntchito. Analipo nthaœi zonse. Analipo inu ndi ine

Page 146: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

146 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

tisanabadwe. Analipo kuyambira pamene dziko linalengedwa.

UTHENGA WABWINO WA KUOMBOLEDWA

Kodi tingachite chiyani pamaso pa

Mulungu? Tiyenera kukhulupilira Uthenga

Wabwino wamuyaya wakuomboledwa

Yesu Khristu, amene anachotsa machimo athu

onse, anachita izi inu ndi ine tisanabadwe. Iye anachotsa machimo athu onse. Kodi inu muli ndi uchimo? —Ai.— Nanga bwanji machimo amene mudza chimwa maœa? Awanso ndi machimo

amene akuphatikizidwa mu machimo adziko lapansi.

Tiyeni tiganizire za machimo amaœa. Machimo amene tinachimwa mpaka lero ndi machimo amene amaphatikizidwa mu machimo adziko lapansi, sichoncho? Kodi anaperekedwa pa Yesu kapena ai? Inde, anaperekedwa.

Kodi ndiye kuti machimo am’mawa nawo anaperekedwa pa iye? Inde, anachotsa onse, popanda kuchotsera. Sanasiye kumbuyo tchimo ngakhale limodzi. Uthenga Wabwino ukutiuuza kuti tiyenera kukhulupilira ndi m’tima wonse kuti Yesu anachotsa machimo athu onse, pa nthaœi imodzi, ndi kulipirira onse.

Chiyambi cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu! (Marko 1:1) Uthenga wa kumwamba ndi nkhani ya chisangalatso. Akutifunsa ife, Ndinachotsa machimo anu onse. Ndine Mpulumutsi wanu. Kodi mukundikhulupilira ine? Mwa anthu osaœerengeka ndi ochepa amene amayankha,

Page 147: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

147 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

“Inde, ndikhulupilira. Ndikhulupilira monga momwe munatiuzira. Ndichinthu chapafupi kuti ndimvetse msanga.” Onse amene amanena motero amakhala olungama ngati Abrahamu.

Koma ena akuti, “sindingakhulupilire izi. Inenso ndikuona kuti ndi chatsopano ndichachilendo.”

Iye anafunsa, “Ndiuzeni chabe, kodi ndinachotsa machimo anu onse kapena ai?”

“Ndinaphunzitsidwa kuti anachotsa machimo obadwa nayo okha, osati machimo a masiku onse.”

“Ndi kuona kuti umakhulupilira monga momwe anakuuzira. Uyenera kupita kuGahena chifukwa palibe chimene ndingakuuze.”

Tinapulumutsidwa kudzera mukukhulupilira mu ntchito yake yotiombola. Onse amene akulimbikira kuti ali ndi tchimo ayenera kupita kuGahena. Ndichifuniro chao.

Uthenga wachiombolo ukuyamba ku chokera mu umboni wa Yohane Mbatizi chifukwa Yesu

anachotsa machimo athu ku dzera mukubatizidwa ndi Yohane Mbatizi, timasanduka oyera pamene tikhulupilira.

Mtumwi Paulo ananena zambiri zokhuza ubatizo wa Yesu mu makalata yake. M’buku la a Galatia 3:27, akuti “Pakuti nonsenu amene munasanduka amodzi ndi Khristu pakubatizidwa, munachita ngati kubvala moyo wa Khristu.” Kubatizidwa mwa Khristu kutanthauza kuti tili mwa Khristu. Pamene Yesu anabatizidwa, machimo athu onse anaperekedwa pa Iye kudzera mwa Yohane Mbatizi ndipo machimo athu anachotsedwa.

M’buku la Petro woyamba mutu 3:21 akuti, “Madziwo afanizira ubatizo umene lero ukupulumutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Khristu. Osati chifukwa cha kuchotsa litsiro la m’thupi, koma chifukwa mulonjeza kwa Mulungu ndi m’tima woona kudzera mukuuka kwa Yesu kwa akufa.”

Okha amene akhulupilira mu umboni wa

Page 148: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

148 Ubatizo wa Yesu ndi nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Yohane Mbatizi, ubatizo wa Yesu, ndi kukhetsa mwazi pa mtanda, ali ndi chisomo cha chiombolo mwa iwo.

Page 149: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

◄ Zam'kati ►

ULALIKI WA CHISANU NDI CHIMODZI

Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi

ndi mwa Mzimu Woyera

Page 150: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

150 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi

ndi mwa Mzimu Woyera

< 1 Yohane 5:1-12 > “Pambuyo pake kunali chikondwerero

chachipembedzo cha Ayuda, ndipo Yesu adapitako ku Yerusalemuko. Kumeneko kuli dziœe, dzina lake pa Chiyuda ndi Betesida. Dziœeli lili pafupi ndi Chipata cha Nkhosa, ndipo nlozingidwa ndi makonde asanu. M’makondemo munkagona anthu ambiri odwala, akhungu, opunduka miyendo ndi opuwala ziwalo. [Iwoœa ankadikira kuti madzi agwedezeke. Pakuti nthaœi zina mngelo wa Ambuye ankatsikira m’dziœemo nkuvundula madziwo. Woyamba kuloœamo madzi atavundulidwa, ankachira ngakhale ankhale

ndi nthenda yanji.] Pakati pa anthu odwalawo panali wina amene adaadwala zaka 38. Yesu adamuwona ali gone, anadziœa kuti adaadwala nthaœi yaitali. Tsono adamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kuchira?” Wodwalayo adati, “Ambuye, ndilibe munthu wondiloœetsa m’dziœemu madzi akavundulidwa. Ndikati ndiloœemo, wina waloœa kale.” Yesu adamlamula kuti, “Dzuka, tenga mphasa yako, yamba kuyenda.” Pompo munthuyo adachiradi, nanyamula mphasa yake nkuyamba kuyenda.

Tsikulo linali la Sabata. Choncho Ayuda adauza munthu amene adachirayo kuti, “Lero mpa Sabata. Malamulo athu sakulola kunyamula mphasa yako.” Koma iye adati, “Amene wandichiritsa ndiye wandiwuza kuti, ‘Nyamula mphasa yako, yenda.’” Iwo adamufunsa kuti, “Munthuyo ndani amene wakuuza kuti unyamule mphasa yako, uyende?”

Page 151: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

151 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

Amene ali ndi Mwana wa Mulungu ali ndi moyo, amene alibe Mwana wa Mulungu alibe umoyo.”

Kodi Yesu anabwera bwanji?

Mwa madzi, magazi, ndi Mzumu woyera.

Kodi Yesu anabwera mwa mwadzi? Inde,

anabwera mwa madzi. Anabwera mwa ubatizo wake. Madzi ndi ubatizo wa Yesu kudzera mwa Yohane Mbatizi mu mtsinje wa Yolodani. Ndi ubatizo wachiombolo umene Iye anachotsera machimo adziko lonse lapansi.

Kodi Yesu anabwera mwa mwazi? Inde, anabwera mwa mwazi. Anabwera mu thupi la munthu ndi kubatizidwa kuti achotse machimo onse adziko lapansi, ndipo analipira mphoto ya

machimo kudzera mukukhetsa mwazi wake pa mtanda. Yesu anabwera mwa mwazi.

Kodi Yesu anabwera mwa Mzimu Woyera? Inde, anabwera mwa Mzimu Woyera mu thupi kuti akhale Mpulumutsi waanthu ochimwa.

Anthu ambiri ali ndichikulupiliro kuti Yesu anabwera mwa madzi, mwa mwazi ndi mwa Mzimu Woyera. Ndi ochepa amene amakhulupilira kuti Yesu ndi Mfumu ya mafumu, Mulungu wa milungu. Anthu ambiri amakaikabe; ‘Kodi ndizoona kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu kapena Mwana wa Munthu?’ Ndipo ambiri, kuphatikizapo odziœa za Mau a Mulungu ndi ogwira ntchito ya Mulungu, amakhulupilira kutiYesu ndi munthu osati kuti ndi Mulungu, Mpulumutsi weniweni.

Koma Mulungu anati aliyense amene akhulupilira kuti Yesu ndi Mfumu ya mafumu Mulungu weniweni, ndi Mpulumutsi woona adzabadwanso mwa Iye. Amene akonda Mulungu amakonda Yesu ndipo onse amene akhulupilira

Page 152: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

152 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

zoona mwa Mulungu amakondanso Yesu munjira yomweyo.

Munthu sangagonjetse dziko lapansi. Mtumwi Yohane anatiuza kuti akhristu oona ndi okhao amene angagonjtse dziko lapansi. Chifukwa chimene okhulupilira amagonjetsera dziko lapansi ndi chakuti ali ndi chikhulupiliro mwa madzi, mwa mwazi, ndi mwa Mzimu Woyera wa Yesu. Mphamvu yogonjetsa dziko si yochokera muchifuniro cha munthu, kapena kuyetsa ndi mphamvu zathu.

“Ngakhale nditamalankhula zilankhulo za anthu kapenanso za angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chitsulo chongolira, kapena chinganga chosokosera. Ngakhale nditakhala ndi mphatso ya uneneri ngakhale nditamadziœa zobitsika zonse, ndi kumamvetsa zinthu zonse, ngakhale nditakhala ndi chikulupuliro chachikhulu chakuti ndingathe kusuntha mapiri, koma ngati ndilibe chikondi, sindili kanthu konse. Ndipo ngakhale ndingagaœire chuma changa chonse,

kapena kupereka thupi langa kuti anthu alitenthe, koma ngati ndibe chikondi, ndiye kuti changa palibe.” (1 Akorinto 13:1-3) Chikondi chitanthauza Yesu, amene anabwera mwa madzi, mwa mwazi ndi mwa Mzimu Woyera.

NDI OKHA OKHULUPILIRA MWA MADZI NDI MWA MWAZI ANGAGONJETSE DZIKO LAPANSI

Ndani angagonjetse ndiko lapansi?

Ndi okhao okhulupilira

muchiombolo cha ubatizo wa Yesu, mwa mwazi ndi

mwa Mzimu Woyera “Ndani amagonjetsa dziko lapansi?

Page 153: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

153 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

Amaligonjetsa si wina ai, koma wokhulupilira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu. Yesu Khristu ndiye amene adabwera kudzera mwa madzi ndi mwa magazi.” (1 Yohane 5:5-6)

Akhristu anzanga, Munthu amene anagonjetsa dziko lapansi, amenenso anagonjetsa Satana ndi Yesu Khristu. Amene akhulupilira Mau onena za madzi, mwazi ndi Mzimu Woyera wa Yesu amagonjetsa dziko lapansi. Kodi Yesu analigonjetsa bwanji dziko lapansi? Kudzera m’chipulumutso cha madzi, mwazi ndi Mzimu Woyera.

Pamene Mau a Mulungu akunena za madzi, amatanthauza ubatizo wa Yesu Khristu (1 Petro 3:21). Yesu Khristu anabwera pa dziko lino lapansi m’thupi. Iye anabwera kuzapulumutsa anthu ochimwa adziko lapansi; Iye anabatizidwa kuti achotse machimo onse aanthu adziko lino lapansi ndipo anafa pa mtanda kupereka nsembe ya machimo athu.

Mwazi umene Iye anakhetsa pa Mtanda,

utanthauza kuti Iye anabwera padziko lino lapansi monga munthu. Yesu anabwera m’thupi la munthu kuti apulumutse anthu ochimwa ndipo anabatizidwa ndi madzi. Choncho Yesu Khristu anabwera mwa madzi ndi mwazi. Tikhozanso kunena kuti Iye anathana ndi uchimo kudzera m’madzi a ubatizo wake ndi mwazi mu imfa yake.

Kodi Satana anali kulamulira bwanji dziko lapansi? Satana anatembunuza mitima ya anthu poœanamiza kuti ayambe kunyozera Mau a Mulungu.

Koma Yesu anabwera pa dziko lino lapansi ndikuchotseratu machimo onse kudzera mu madzi a ubatizo wake ndi mwazi wake pa Mtanda: Iye anagonjetsa Satana ndi kuchotsa machimo onse adziko lapansi.

Izi zinachitika chifukwa chakuti Yesu ndiye Mpulumutsi wa anthu onse ochimwa. Iye anakhala Mpulumutsi chifukwa anabwera mwa madzi ndi mwazi.

Page 154: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

154 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

YESU ANACHOTSA MACHIMO A DZIKO LAPANSI KUDZERA MU UBATIZO WAKE CHIPULUMUTSO

Kodi mukutanthauza chiyani mukamanena kuti Yesu

anagonjetse dziko?

Kutanthauza kuti lye anachotsa machimo onse adziko lapansi

Chifukwa chakuti Yesu anabatizidwa kuti achotse machimo onse adziko lapansi ndipo anafa pa Mtanda monga munthu; Mwa njira imeneyi Iye anatipulumutsa ku machimo athu onse. Chifukwa chakuti Yesu anabatizidwa mu Mtsinje wa Yolodani ndi Yohane Mbatizi, amene ndi oyimirira wa anthu onse, machimo onse adziko

lapansi anaperekedwa kwa Iye. Ndipo Iye anapereka moyo wake pa Mtanda ngati mphoto ya machimo. Chifukwa chakuti Yesu anafa pa Mtanda ndipo anaukanso kwa akufa, Iye anagonjetsa Satana. Iye analipila photho ya machimo kudeza mu imfa yake. YESU ANABWERA KWA OCHIMWA MWA MADZI AUBATIZO WAKE NDI MWAZI MU IMFA YAKE PA MTANDA

Mtumwi Yohane adanena kuti chipulumutso

simadzi okha, koma madzi ndi mwazi. Choncho, monga Yesu anachotsera machimo onse kwa muyaya, anthu onse ochimwa adzapulumutsidwa pakukhulupilira mwa Iye ndi kukhala okhulupilika ku Mau ake.

Page 155: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

155 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

Kodi anaigonjetsa bwanji mphamvu ya Satana?

Kudzera mu ubtizo wake mwazi wake ndi Mzimu

Woyera Pamene Yesu anabwera pa dziko lapansi,

sanachotse machimo okha, komanso anatipulumutsa pakukhetsa mwazi wake ndi kufa pa Mtanda. Iye anachotsa machimo athu onse pakubatizidwa mu Mtsinje wa Yolodani ndi kulipira mphohto ya machimo anthu pa Mtanda; Iye analipira mphotho ya machimo athu pamene anafa pa Mtanda. Ndipo ulosi wa malamulo a Mulungu umene unanena kuti, “Mphotho ya uchimo ndi mfa” (Aroma 6:23) unakwaniritsidwa.

Kodi Yesu ankatanthauzanji ponena kuti anagonjetsa dziko lapansi, ndi chikhulupiliro chimene chimagonjetsa dziko lapansi, ndi

chikhulupiliro chimene chimakhazikika pachiombolo chimene Yesu anatipatsa pakubatizidwa ndi kukhetsa mwazi pa Mtanda. Iye anabwera monga munthu ndipo anatitsimikizira za chipulumutso ndi ubatizo wake wa madzi ndi imfa yake pa Mtanda.

Yesu amagonjetsa dziko lapansi, kunena kuti Satana. Atumwi ampingo woyambirira anaima njii pachikulupiliro chao posagonjetsa Boma la Aroma ndiponso mayesero adziko lino lapansi.

Zonsezi zinali zotsatira za chikhulupiliro chakuti Yesu anabwera mwa madzi (anabatizidwa kuti atichotsere machimo athu onse), ndipo ndi mwazi wake pa mtanda (analipira mphotho ya mchimo athu onse ndi imfa yake).

Yesu anabwera mwa Mzimu (anabwera muthupi la muntu), ndipo anachotsa machimo aanthu onse ochimwa ndi ubatizo wake ndiponso mwazi wake pa Mtanda kuti tonse ife amene tapulumutsidwa tigonjetsenso dziko lapansi.

Page 156: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

156 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

PALINSO CHIFANIZIRO CHIMENE CHIMATIPULUMUTSA, NDIWO UBATIZO, KUDZERA MU KUUKITSIDWA KWA YESU KHRISTU <1 Petro 3:21>

Kodi chifaniziro cha chipulumutso ndi chiyani?

Ubatizo wa Yesu khristu

Pa 1 Petro 3:21 pali mau aœa: “Madziœo akufanizira ubatizo umene masiku ano umakupulumutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Khristu. Kubatizidwa kuneneku si kuchotsedwa litsiro la m’thupi, koma kudzipereka kwa Mulungu ndi m’tima woona kudzera mwa Yesu Khristu.” Mtumwi Petro anachitira umboni wakuti Yesu ndi

Mpulumutsi ndiponso kuti Iye anabwera mwa madzi a ubatizo ndi mwazi.

Motero tiyenera kukhulupilira mwa Yesu amene anabwera mwa madzi ndi mwa mwazi. Ndipo tiyenera kudziœa kuti Yesu ndi amene anabwera mwa madzi amenenso akufanizira ubatizo umene masiku ano ukutipulumutsa. Kukhulupilira mu mwazi okha, nditheka chabe la chikhulupiliro choona. Mtumwi Petro akutiuza kuti ‘madzi’ aubatizo, mwazi ndi Mzimu Woyera ndizo zida zenizeni za chiombolo.

Palibe ophunzira amene anakhulupilira mwazi wa Yesu pa mtanda popanda ubatizo wake. Koma chikhulupilira cha anthu amene amakhulupilira Uthenga Wabwino wonena za madzi, mwazi ndi Mzimu Woyera chidzakula kwa nthaœi zonse.

Koma Uthenga wonena za mwazi okha ndi umene uli kufalitsidwa kwambiri. Chifukwa chiyani? Anthu sadziœa Mau a choonadi, chiombolo cha madzi ndi Mzimu Woyera motero sangathe kubadwanso mwatsopano.

Page 157: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

157 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

Nthaœi ina mpingo waku madzulo unagwa mu zikhulupiliro zonama. Anali kuoneka kulemera pa nthaœi yochepa, koma antchito a Satana anali kutembenuza chikhulupiliro chao mu zonama.

Maere ndi chikhulupiliro choti Satana amathaœa ngati wina alemba mtanda pa popeza kapena pa thabwa, ndiko kuti Satana athaœa ngati munthu okhulupilira mwa mwazi wa Yesu. Kudzera muchikhulupiliro cha maere ichi, Satana anali kunamiza anthu kuti akhulupilire kuti sayenera kukhulupilira mwa mwazi wa Yesu okha. Satana analikuyetsa kuopa mwazi wa Yesu, ndi kunena kuti mwaziwu unakhetsedwa chifukwa cha ochimwa.

Koma, Petro ndi ophunzira ena anachitira umboni Uthenga Wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake pa mtanda. Komabe, kodi a khristu masiku ano amachitira umboni ndani? Amachitira umboni mwazi wa Yesu.

Koma, tiyenera kukhulupilira mu Mau olembedwa mu Baibulo ndi khala ndi

chikhulupiliro mukupulumutsidwa mwa Mzimu Woyera, ndimu ubatizo wa Yesu, ndi mwa mwazi. Ngati sitisamala ubatizo wa Yesu ndi kuchitira umboni kuti Yesu anatifera pa mtanda, chipulumutso si chingakhale chokwanira. MAU AUMBONI WA MULUNGU A CHIPULUMUTSO CHA MADZI

Kodi zoona zake zoti Mulungu anatipulumutsa ndi ziti?

Ndi mwa madzi, mwa mwazi, ndi

mwa Mzimu Woyera 1 Yohane 5:8 Ambuye akuti, “Mzimu Woyera,

madzi ndi magazi, ndipo atatuœa amavomerezana.” Woyamba ndi Mzimu Woyera,

Page 158: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

158 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

a chiœiri ndi madzi a ubatizo wa Yesu, ndipo achitatu ndi magazi a pa Mtanda. Onse atatu ndi amodzi. Yesu anabwera pa dziko lapansi kupulumutsa ife tonse kuchoka ku machimo. Iye yekha anachita izi mu njira zitatu, mwa ubatizo, mwa mwazi, ndi mwa Mzimu Woyera Mzimu Woyera, madzi ndi magazi, ndipo atatuwa amavomerezana.

Pali zinthu zitatu zimene zimaonetsa kuti Yesu anatipulumutsa ife. Umboni uwu ndi madzi a ubatizo wa Yesu, ndi mwazi ndi Mzimu Woyera. Zinthu zitatu izi ndi zimene Yesu anatichitira mu dziko lino lapansi.

Ngati mwa zinthu zitatu izi chimodzi sichichitika, chipulumutso sichikanachitika. Mzimu Woyera, madzi ndi magazi ndipo atatuwa amavomerezana. Mzimu Woyera, ndi madzi ndipo ndi mwazi.

Yesu amene anabwera kwa ife mu thupi ndi Mulungu, ndi Mzimu Woyera, ndipo ndi Mwana wa Mulungu. Anabwera pa dziko lino monga ngati

mwa Mzimu Woyera m’thupi ndipo anabatizidwa ndi madzi kuti achotse machimo adziko lapansi. Anatenga machimo onse m’thupi lake kuti atipulumutse ife ochimwa kudzera mu kukhetsa mwazi wake pa Mtanda mpaka imfa. Analipira machimo athu onse mokwanira. Ndi Uthenga Wabwino wokwanira wachiombolo wa madzi, wa mwazi, ndi wa Mzimu Woyera.

Ngati palibe chimodzi cha izi, ndiye kuti palibe chipulumutso cha Mulungu chimene chinatipulumutsa ife ku machimo. Ngati tigwirizana ndi okhulupilira ambiri masiku ano, tiyenera kunena kuti, aœiri aœa akuchitira umboni mwazi ndi Mzimu Woyera.

Koma Mtumwi Yohane ananena kuti pali zinthu zitatu zimene zikuchitira umboni. Madzi a Yesu aubatizo, mwazi umene unakhetsedwa pa mtanda, ndipo ndi Mzimu Woyera. Mtumwi Yohane sanabise kanthu pochitira umboni wake.

Chikhulupiliro chimene chimaombola ochimwa ndi chikhulupiliro cha Mzimu Woyera, cha madzi

Page 159: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

159 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

ndipo ndi cha mwazi. Kodi chikhulupiliro chimene chimapanga munthu kuti agonjetse dziko lapansi chili kuti? Chilipompano. Ndikukhulupilira Yesu amene anabwera mwa madzi, mwa mwazi ndi mwa Mzimu woyera. Kodi mukhulupilira izi ndi kulandira chipulumutso cha moyo wosatha?

Kodi chipulumutso chingakhale chokwanira popanda ubatizo

wa Yesu? Ai

Kale kale, ndisanabadwenso kachiœiri, inenso

ndinali m’khristu amene anali kukhulupilira mwa mwazi wa pa mtanda ndiponso mwa Mzimu Woyera. Ndikhulupilira kuti anabwera mwa Mzimu Woyera ndi kumwalira pa mtanda kuti apulumutse ine ku machimo onse. Ndinali kukhulupilira zinthu ziœiri zokhazi ndipo ndinali patsogolo kulalika zonse kwa anthu onse.

Ndili ndi maganizo ophunzira za Mulungu kuti ndikhale mtumwi wa Mulungu kuti ndigwire ntchito anthu ndiœafere monga ngati m’mene anachitira Yesu. Ndinali wokonzekera zonse zapamwamba zimene zingachitika.

Koma, m’mene ndinali kukhulupilira zinthu ziœiri izi, nthaœi yonse ndinali ndi uchimo m’kati mu m’tima wanga. Tere, sindikagonjetsa dziko lapansi ndikanakhala womasuka ku uchimo.

Pamene ndikanakhulupilira mwa mwazi, ndi mwa magazi, ndi mwa Mzimu Woyera, ndikanakhalabe ndi uchimo m’tima wanga.

Chifukwa chimene ndikadali ndi uchimo mum’tima wanga ngakhale ndikulupilira mwa Yesu chinali chakuti sindinali kudziœa za madzi, aubatizo wa Yesu. Kupulumutsidwa kwanga sikunali kokwanira mpaka ntakhulupilira mu madzi aubatizo ndi mu mwazi ndipo ndi mwa Mzimu Woyera.

Chifukwa chimene si ndikanagonjetsa uchimo ndi chakuti si ndinalikudziœa tanthauzo la ubatizo

Page 160: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

160 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

wa Yesu. Ngakhale lero lomwe anthu ambiri sakhulupilira Yesu koma amachimwira thupi lao. Akadali ndimachimo mu mitima yao ndipo amayetsa njira yiliyonse kuti abwerezerepo chikondi cha Yesu chomwe anali nacho poyamba.

Sangabwerezepo chisomo choyamba ndi mphavu zao chifukwa machimo ao sanachotsedwe onse ndi mwadzi a ubatizo. Sakukumbukira kuti machimo ao onse anaperekedwa pa Yesu pamene anali kubatizidwa, ndipo sangabwezerepo chikhulupiliro chao kachiœiri pamene agwa.

Ndikufuna kuti nonse mumvetse izi. Tingakhale ndi chikhulupilire ndikugonjetsa dziko lapansi ngati tikhulupilira mwa Yesu. Komabe sitiri okwanira, timachimwabe mu dziko lapansi, koma ngati tikhulupilira kuti Yesu ndi mupulumutsi wathu amene anatipanga kuti tikhale omasuka ku uchimo wa ubatizo wake, tizagonjetsa Satana.

Koma ngati tikhulupilira Yesu popanda madzi a ubatizo. Sitingakhale opulumutsidwa mokwanira. Mtumwi Yohane akutiuza kuti chikhulupiliro

chimene chimagonjetsa dziko ndi chikhulupiliro cha mwa Yesu Khristu amene anabwera mwa ubatizo wa madzi, wa mwazi ndi wa Mzimu Woyera.

Mulungu anatumiza Mwana wake wobadwa yekhayo kuti aombole onse amene akhulupilira mu ubatizo ndi mu mwazi wake. Yesu anachotsa machimo athu onse mu ubatizo wake. Yesu, yekhayo Mwana wa Mulungu, anabwera kwa ife mwa Mzimu Woyera (m’thupi lamuntu). Ndipo anakhetsa mwazi pa mtanda kuti alipire mphoto ya uchimo. Motero Yesu anapulumutsa anthu onse ku uchimo.

Chikhulupiliro chimene chimatitsogolera ife kuti tigonjetse dziko lapansi chimapezeka mukukhulupilira kuti ndizoona Yesu anabwera mwa madzi, mwa mwazi, ndipo ndi mwa Mzimu Woyera kuti atipulumutse ife ku machimo onse.

Pakanakhala kuti palibe madzi aubatizo ndi mwazi pa mtanda, sipakanakhala chikhulupiliro choona. Ngati palibe chimodzi cha izi si

Page 161: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

161 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

tikanakhala ndi chikhulupiliro choona cha chipulumutso. Chipulumutso choona si chikanapezeka popanda madzi ndi mwazi ndi Mzimu Woyera. Choncho, tiyenera kukhulupilira mu madzi, mu mwazi, ndi Mzimu Woyera. Dziœani ichi ndipo mudzakhala ndi chikhulupiliro choona. NDIKUUDZANI KUTI SIZOONA CHIPULUMUTSO CHOPANDA UMBONI WA MADZI, WA MWAZI NDI WA MZIMU WOYERA

Kodi atatu amene amachitira umboni wa chipulumutso

ndi ati? Ndi madzi, ndi mwazi ndipo ndi

Mzimu Woyera

Wina akhoza kuganiza motere. “Yesu ndi Mpulumutsi wanga. Ndikulupilira mwazi wa pa Mtanda ndipo ndikufuna kuphedwa chifukwa chakukhulupilira. Ndikulupilira Yesu ngakhale ndili ndi uchimo mu m’tima wanga. Ndikulapa momvetsa ndikukonda ena masiku onse. Ndipereka moyo wanga ndi chuma changa kwa inu. Si ndinenso wokwanira. Kodi Mulungu sangandidziœe bwanji? Yesu anadifera pa Mtanda. Mulungu wathu Woyera anabwera ngati munthu ndi kutifera pa Mtanda. Ndikhulupilira ntchito yanga mokhulupilika. Ngakhale ndikhale wopanda ntchito, komabe ndili nditchimo pang’ono m’mtima wanga, kodi Yesu adzandiponya kugehena chifukwa cha ichi? Ai, sadzachita ichi.”

Pali anthu ambiri ofanana ndi uyu. Ndi amene sakhulupilira kuti Yesu anabatizidwa kuti achotse machimo adziko lapansi. Anthu amene akhulupilira Yesu ngati alinso ndi uchimo kodi amapita kuti? Amapita kugehena. Ndi ochimwa.

Page 162: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

162 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

Amene, akuganiza ngati akusangalatsa ndi kuti Mulungu akuganiza monga momwe iwo aganiza adzapita kugehena. Ndipo, ena akuganiza kuti chifukwa Yesu anachotsa machimo onse pamene anafa pa mtanda, ndiye kuti padziko palibe uchimo. Koma, akunena chabe za mwazi, ndi Mzimu Woyera. Ichi si chikhulupiliro chimene chimatsogolera anthu kuchiombolo.

Tiyenera kukhulupilira kuti Yesu anachotsa machimo kudzera mu ubatizo, anaweruzidwa, ndi kufa pa matnda patapita masiku atatu.

Popanda chikhulupiliro ichi, palibe kuombolodwa. Yesu Khristu anabatizigwa, anamwalira pa mtanda, ndipo anauka kwa akufa. Yesu Khristu anabwera kwa ife mwa madzi, mwa mwazi ndi mwa Mzimu Woyera. Anachotsa machimo onse a dziko lapansi.

Ndi atatu amene amachitira umboni dziko lapansi: Mzimu Woyera, madzi ndi mwazi.

Mzimu Woyera ukuchitira umboni kuti Yesu ndi Mulungu ndipo kuti anabwera kudzea m’thupi

la munthu. Kachiœiri ndi umboni wa ‘madzi.’ Madzi ndi

ubatizo wa Yesu mu mtsinje wa Yolodani ndi Yohane Mbatizi, ndipo machimo athu anaperekedwa pa Yesu. Machimo athu onse anaperekedwa pa Yesu pamene anali kubatizidwa (Mateo 3:15) koma Yesu adamuyakha kuti, “Tsopano lino vomera, chifukwa ndi m’mene tiyenera kuchitira zonse zimene Mulungu akufuna.”

Umboni wachitatu ndi wa ‘mwazi’ umene ukuimirira umoyo watsopano ndipo Yesu akutenga chiweruzo mumalo wa ife. Yesu anatifera ndi kutenga chiweruzo m’malo mwathu ndi kuuka kwa akufa patapita masiku atatu.

Mulungu Atate anatumiza Mzimu Woyera m’mitima ya amene akhulupilira ubatizo ndi mu mwazi wa Mwana wake umene kuchitira umboni za kuomboledwa kwathu.

Amene anabadwanso kachiœiri ali ndi mau amene amaœathandiza kugonjetsa dziko lapansi.

Page 163: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

163 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

Chiombolo chidzagonjetsa Satana, kunama kwa aneneri onyenga, ndi zolepheretsa kapena zinthu za dziko zimene zimatigonjetsa kaœirikaœiri. Tiri ndi mphamvu iyi chifukwa tiri ndi zinthu zitatu m’mitima yathu: madzi a Yesu, ndi mwazi ndipo ndi Mzimu Woyera.

Kodi timagonjetsa bwanji dziko lapansi ndi mphamvu

ya Santana?

Ngati tikhulupilira mu maumboni atatu

Timagonjetsa mphamvu ya Satana ndi dziko lapansi ngati tikhulupilira mwa Mzimu Woyera, madzi ndi mu mwazi. Amene akhulupilira mu ubatizo ndi mu mwazi. Amene akhulupilira mu ubatizo ndi mu mwazi wa Yesu agonjetsa aneneri onyenga.

Chikhulupiliro chathu, ndi mphamvu yogonjetsa Satana; ili mu madzi, mu mwazi ndi mwa Mzimu Woyera. Kodi mukhulupilira izi?

Simungabadwetso kachiœiri kapena kugonjetsa dziko lapansi ngati mulibe chikhulupiliro cha chiombolo kudzera mu ubatizo wa Yesu, mu mwazi wake, ndikukhupulira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu ndipo ndi Mpulumutsi wathu. Kodi mukumvetsa izi m’mitima yanu?

Kodi muli ndi Mzimu Woyera ndi madzi a ubatizo m’mitima yanu?

Mudzagonjetsa dziko lapansi ngati mukhala ndi madzi ndi mwazi wa Yesu m’mitima yanu, ndipo ngati mukhulupilira kuti Yesu anakuferani pa mtanda ndi kutenga chiweruzo mu malo mwa inu.

Mtumwi Yohane anagonjetsa dziko lapansi chifukwa anali nazo zonsezi m’tima wake. Ndipo anali kunena zachiombolo kwa okhulupilira onse amene anali kukumana ndi mavuto ndi kuopsezedwa. Anachitira umboni, umu ndi m’mene mungagonjetsere dziko lapansi pano.

Page 164: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

164 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

Yesu anabwera mwa Mzimu Woyera, mwa madzi, ndipo ndi mwa mwazi, monga momwe anagonjetsera dziko lapansi, momwemonso okhulupilira adzagonjetsa dziko lapansi. Iyi ndi njira yokhayo imene okhulupilira angagonjetsere dziko lapansi.

1 Yohane 5:8 akuti, “Mzimu Woyera, madzi ndi magazi, ndipo atatuœa amavomerezana.” Ambiri amanena za mwazi ndi Mzimu Woyera koma amachotsapo madzi aubatizo wa Yesu. Ngati achotsapo madzi, amanamizidwabe ndi Satana Ayenera kubwera poyera ndikulapa, ayenera kukhulupilira mu madzi, a Yesu aubatizo, kuti abadwenso kachiœiri.

Palibe amene angagonjetse dziko lapansi popanda kukhulupilira mu madzi ndi mu mwazi. Ndikunenatso ndikuti palibe ngakhale m’modzi! Tiyenera kumenya nkhondo pogwiritsa ntchito madzi ndi mwazi wa Yesu ngati zida zathu. Mau ake ndi zida za Mzimu Woyera, ounikira anthu.

Pali anthu ambiri amene sakhulupilira mu

ubatizo wa Yesu amene unachotsa machimo ao onse. Pali anthu ambiri amene akhulupilira zinthu ziœiri zokha. Pamene Yesu akuwauza kuti zukani ndipo œalani samaœala. Amakhalabe ndi uchimo m’mitima yao. Ngakhale akhulupilire mwa Yesu komabe apita kugehena.

UTHENGA WABWINO WA UBATIZO NDI WA MWAZI WA YESU UYENERA KUUCHITIRA UMBONI KUTI ANTHU AMVE NDI KUKHULUPILIRA NDI KUPULUMUTSIDWA

Pamene tichitira umboni Uthenga Wabwino,

tiyenera kutsimikiza. Yesu anabwera mwa Mzimu Woyera, mwa ubatizo (umene umachotsa machimo athu), ndi mwa mwazi umene analipira

Page 165: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

165 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

machimo athu). Tiyenera kukhulupilira zonse zitatu izi.

Kodi chikhulupiliro cha ubatizo ndi chikhulupiliro

chachabe?

Ai. Sichikhulupiliro chachabe. Ndi zoona.

Ngati sichoncho, ndiye kuti sitikulalikira

Uthenga Wabwino osati chipembezo. Akhristu mu dziko muno akunena chikhristu kuti ndi chipembezo. Chikhristu sichingathanthauzidwe kuti ndi chipembezo. Ndichikhulupiliro chimene chimamangidwa pa choona, chikhulupiliro chimene chimayang’ana kwa Mulungu. Sichipembezo ai.

Chipembezo ndi chinthu china chimene

chinapangidwa ndi anthu, koma chikhulupiliro ndi kuyang’ana kuchipulumutso chimene Mulungu amatipatsa. Uku ndiko kusiyana kwake. Ngati munyozera choona ichi, ndiye kuti mukutenga chikhristu ngati chipembezo china ndi kulalikira kudzera mu makhalidwe ndi njira zina, zakumwamba, Nirvana, ndi Paladizo.

Yesu sanabwere kudzayambitsa chipembezo china mu dziko lino. Sanayambitse chipembezo china chotchedwa chikhristu. Kodi chifukwa nchiyani mukukhulupilira kuti ndi chipembezo? Ngati ndi chimodzimodzi, chifukwa nchiyani simukhulupilira mu chibuda? Kodi mukuganiza kuti ndikulakwa ponena choncho?

Ena amakhulupilira Yesu ngati chipembezo ndi kunena kuti, “Kodi kusiyana kwake ndi kotani? Ndi zinthu zimodzi, koma zili ndi maina osiyana chabe. Tonse tifika ku malo amodzi.”

Akhristu anzanga, tiyenera kuyang’ana ku choona. Tiyenera kuzuka ndi kuœala. Tiyenera kunena choona popanda mantha.

Page 166: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

166 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

Pamene wina anena kuti, “Iyi siingakhale njira yokhao,” muyenera kunena ndi mau osabisa, “Inde! Ndi njira yokhayo mungathe kupita kumwamba ngati mukukhulupilira Yesu Khristu amene anabwera mwa madzi, mwa mwazi ndi mwa Mzimu Woyera.” Muyenera kuœala kwambiri kuti anthu ena amve mau achiombolo, kuti abadwenso ndi kupita ku mwamba.

KHALANI NDI CHIKHULUPILIRO CHOONA: AMENE SAMUKONDA YESU NDI AMENE SADZIŒA ZA CHIOMBOLO CHA UBATIZO WA YESU NDI MWAZI WAKE NDIWO ADZAWONONGEDWA

Ndani amene adzawonongedwa

ngakhale akhulupilire mwa Yesu?

Ndi amene sakhulupilira mu ubatizo wake

Kunena kokha kuti ndikhulupilira Yesu ndi

maganizo athu popanda chikondi ndi Yesu ndi kutenga chipembezo ngati masewero chabe.

Bwato limene linali kuwoloka nyanja yayikulu

Page 167: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

167 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

ya Pacific linagubuduka anthu ochepa anapulumuka. Ndipo anamanga mudzi wa SOS, koma mafunde anali kulepheretsa mabwato ena kufika ndi thandizo pa maloœa. Ndi ndeke yimene yimaima pali ponse inabwera ndi kuœagwetsera Ngati wina angathe kugwira ntchito ndi manja ake ndi kuzimanga kudzungulira thupi lake, afanana ndi munthu amene amagwa mu chikondi chonama ndi Yesu; kukhulupilira bwino, koma iye akuti, “Ndikukhulupilira. Ndipulumutseni. Ndikhulupilira ndipo ndikuganiza kuti ndidzapulumutsidwa.”

Amene samvetsa choona cha ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake amakhulupilira kuti iye adzapulumuka chifukwa iye agwiritsa chingwe.

Koma pamene adzakokedwa, manja ake sangalimbe kugwira chingwe. Adzakhala kuti akugwira ndi mphamvu zake zokha. Pamene mphamvu zake zidzachepa adzagwira mu nyanja.

Umu ndi m’mene zimakhalira ngati munthu sali mu chikondi chenicheni ndi Yesu. Ambiri

amanena kuti ndi okhulupilira Mulungu ndi Yesu, kuti amakhulupilira Yesu amene anabwera mwa Mzimu Woyera, koma ili ndi gawo limodzi chabe. Sangathe kukhala ndi chikhulupiliro chenicheni cha Uthenga Wabwino, ndipo iwo amapitiriza kunena kuti ndi okhulupilira.

Kukhulupilira ndi kuyetsa kukhulupilira sizikufanana ai. Amanena kuti akutsatira Yesu koma potsiriza adaponyedwa kunja chifukwa cha machimo amene ali m’mitima yao. Amakonda Yesu popanda kudziœa kuti Yesu anabwera mwa ubatizo, mwa mwazi, ndi mwa Mzimu Woyera. Ngati akonda Yesu chifukwa cha mwazi wake wokha, azapita kugehena.

Ikani Mzimu wanu mu ubatizo wa madzi wa Yesu, ndi mu mau a mwazi wa pa mtanda. Pamene Yesu anagwetsa chingwe cha chikulupiliro, amene anadzimanga ndi madzi ndi mwazi, ndipo ndi Mzimu Woyera adzapulumutsidwa.

Page 168: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

168 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

Wopulumutsa anthu anafuula kuchokera mu ndege, “Chonde mvetsani kwa ine. Pamene ndi gwetsa chingwe pansi, zimangirireni mozungulira ndi manja anu. Ndipo khalani monga munaliri. Osalendewera ndi manja anu kuchingwe. Mungozimanga ni kukhala ofatsa. Ndipo mudzapulumutsidwa.”

Atapereka malangizo ameneœa, munthu mu modzi amene anatsatira malangizo ameneœa anapulumutsidwa. Koma munthu wina amene anati, “Osadandaula. Ndili ndi mphamvu kwambiri. Ndinali kugwira ntchito kukhalabu ya za umoyo. Kodi mukuona thupi langa? Ndikhoza kulendewera makilometa angapo.” Ndipo anagwira chingwe ndi manja ake ndipo kulendewera m’mene chingwe chija chinali kupitira m’mwamba.

Anthu aœiriœa anapita mumwamba poyamba. Koma panali kusiyana. Amene anamvera malangizo ndi kuzimanga mozungulira ndi

chingwe analamulidwa popanda…… Ndipo analudza maganizo mu njira koma anapita mumwamba.

Yemwe anakhulupilira mphamvu zake mphamvu zinamuthera. Ndipo anafa chifukwa anakana kumvera malangizo.

Kupedza chiombolo, munthu ayenera kukhulupilira mu chiombolo cha madzi aubatizo wake ndi mwa mwazi umene unapulumutsa mizimu yonse kuchokera ku machimo. Chipumulutso chimakhalapo kwa iwo amene akhulupilira ndi m’tima wonse mu mau ake; “Ndinakupulumutsani ndi ubatizo wanga kudzera mwa Yohane Mbatizi ndi kudzera mu khetsa mwazi mpaka kufa pa mtanda.”

Onse amene akhulupilira mu mwazi wokha amati, “Osadandaula, ndikhulupilira. Ndidzakahala wothokoza mpaka ku mapeto amoyo wanga chifukwa cha mwazi wa Yesu. Ndidzatsatira Yesu mpaka ku mapeto a chikhulupiliro changa mu

Page 169: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

169 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

mwazi wokha ndi dzagonje dziko lapansi ndimachimo onse pa nthaœi yonse ya moyo wanga.”

Koma ichi sichokwanira. Amene Mulungu amawachirita umboni kuti ndi anthu ake ndi amene akhulupilira mwa zinthu zitatu izi: Kuti Yesu anabwera mwa Mzimu Woyera ndipo anabatizidwa (Yesu anachotsa machimo onse kudzera mu ubatizo wake mu mtsinje wa Yolodani), kuti anamwalira pa mtanda kuti alipire machimo athu onse, ndipo anauka kwa akufa.

Mzimu Woyera umabwera kwa okhawo amene akhulupilira mu zintu zonse zitatu ndi kuchitira umboni pa zimenezi. “Inde, Ndine Mpulumutsi wanu. Ndinakupulumutsani ndi madzi ndi mwazi. Ndine Mulungu wanu.”

Koma kwa iwo amene sakhulupilira mu zinthu zitatuzi, Mulungu samapereka chipulumutso. Ngakhale kuti muntu achotsepo chimodzi, Mulungu amati, “Ai, iwe sungapulumutsidwe.”

Ophunzira ake anakhulupilira mu zinthu zitatu izi. Yesu anati ubatizo wake ndi umboni wa chipulumutso, ndipo mwazi wake ndi chiweruzo.

ATUMWI AWA PAULO NDI PETRO NAWONSO ANACHITIRA UMBONI ZA UBATIZO NDI MWAZI WA YESU

Kodi ophunzira a Yesu anachitira umboni chayani?

Ubatizo wa Yesu ni mwazi

wake Kodi mtumwi Paulo ananena za ubatizo wa

Yesu? Tiyeni tione kodi ndi kangati anali kunena za ubatizo wa Yesu. M’buku la Arona 6:3 akuti,

Page 170: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

170 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

“Kodi inu, simukudziœa kuti tonse amene tidasanduka amodzi ndi Khristu Yesu pakubatizidwa, ndi Iye mu imfa yake?” Ndipo mu Aroma 6:5 akuti, “Ngati takhala amodzi ndi Khristu mu imfa yake, momwemonso tidzakhala amodzi naye pakuuka kwa akufa, monga momwe adaukira Iyeyo.”

Akutinso m’buku la Agalatia 3:27, “pajatu nonsenu amene mudasanduka amodzi ndi Khristu pakubatizidwa, mudachita ngati kuvala moyo wa Khristu.” Mtumwi wa Yesu anachitira umboni wa ‘madzi’ aubatizo wa Yesu.

“Madziwo akufanizira ubatizo umene masiku ano umakupulutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Khristu.” Kubatizidwa kumeneku sikuchotsedwa litsiro a m’thupi, koma kudzipereka kwa Mulungu ndi m’tima woona, kudzera mwa Yesu Khristu. (1 Petro 3:21).

CHIPULUMUTSO CHA CHIOMBOLO CHA AMBUYE CHINABWERA MWA MADZI NDI MWA MWAZI WA YESU

Kodi ndi ati amene Mulungu amalatcha kuti ndi olungama?

Ndi munthu amene alibe uchimo m’tima

wake Chipulumutso chimene Yesu anagulira anthu

chinali cha madzi a ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake umene unakhetsedwa pa mtanda. Kudzera mukuomboledwa kumeneku tiyenera ku dzuka ndi kuœala. Tichita bwanji? Kudzera mukuchitira umboni mu zinthu zitatu izi.

‘Dzukani ndipo œalani.’ “Iwe Yerusalemu

Page 171: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

171 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

dzuka, œala, kuœala kwako kwayamba. Ulemelero wa Chauta wakuœalira” (Yesaya 60:1). Mulungu aonetsa kuœala pa ife ndipo akutiuza kuti ifenso tiœale. Tiyeni titsatire lamulo limeneli.

Anthu ambiri samamvetsa. Tiyenera kulalika ndi mpamvu. Khulupilirani mwa Yesu ndipo mudzaomboledwa. Ndipo muzalungama. Ngati mukadali tchimo m’tima wanu, si muli olungama ai. Simunagonjetse machimo adziko lapansi.

Simungachotse machimo m’mtima wanu ngati simungakhulupilire madzi a Yesu (a aubatizo wa Yesu). Simungaletse kuweruzidwa ngati simukhulupilira mu mwazi wa Yesu. Simungapulumutsidwe ngati simukuhulupilira Yesu Khristu amene anabwera mwa Mzimu Woyera. Simungakhale olungama mpaka m’takhulupilira mu zinthu zitatu izi.

Kulungama kosakwanira kumatsogolera kuchilungamo chopanda chilungamo chenicheni. Ngati munthu akunena kuti ali ndi tchimo koma akuyetsa kuti ngolungama mwa iye yekha sali

mwa Yesu. Anthu ena masiku ano akuyetsa kulendewera mu chiombolo chodzilungamitsa okha. Amalemba matani ambiri a makalata opanda ntchito pa phunziro ili.

Kodi Mulungu amanena kuti munthu alibe uchimo pamene mu m’tima wake muli tchimo. Amanena m’mene Iye amaonera. Iye ali ndi mphamvu sanganame ai. Timanena kuti chinthu ichi ndi choyera pamene ndi choyera. Sitimanena kuti chinthu ndi choyera pamene chli ndi uchimo.

Mukhoza kuganiza kuti ndinu olungama ndi Yesu ngakhale mukhale ndi tchimo mu m’tima wanu. Izi sizoona ai ndi kulakwa.

Yesu amationa olungama pamene tikhulupilira Yesu ngati amene anabwera mwa Mzimu Woyera, ndiponso amene anabwera mwa madzi (kuti anachotsa machimo athu pamene Iye anali kubatizidwa), ndiponso ngati amene anabweranso mwa mwazi (anabwera m’thupi ndi kutifera ife.)

Akhristu anzanga, chilungamo chimene si chenicheni chilibe ntchito ndi Uthenga Wabwino

Page 172: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

172 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

wa madzi ndi wa mwazi. Kuzilungamitsa kapena kutchedwa wolungama ndi chipunzitso chimene chimachoka mwa munthu. Kodi Mulungu amatitcha wolungama pamene tili ndi uchimo mu mitima yathu? Mulungu sanamena kuti munthu ngolungama pamene ali ndi uchimo mu m’tima wake ngakhale akhale wokhulupilira mwa Yesu. Yesu sanganame ai.

Komabe, kodi mukuganiza kuti amanena kuti ngolungama pamene ali ndi tchimo mu m’tima wake? Izi ndi zimene munthu aganiza, Mulungu amadana ndi kunama. Kodi anganene kuti ndi olungama pamene mukuhulupilira mwa ‘Mzimu Woyera’ ndi mwa ‘mwazi?’ Sangathe kutero.

Pali munthu m’modzi yekha amene Mulungu anganene kuti ndi olungama. Ndi munthu amene alibe tchimo mu m’tima wake.

Iye amaganiza za anthu okhawo amene akhulupilira mwa zinthu zitatu izi: kuti Yesu, amene ndi Mulungu anabwera pansi pano m’thupi, ndi kuti anabatizidwa mu mtsinje wa Yolodani,

ndipo kuti anakhetsa mwazi wake pa mtanda kuchotsa machimo athu onse.

Ndiokhao amene akhulupilira mu Uthenga Wabwino wa chipulumutso ndi amene amadziœika ndi Mulungu. Ndi okhao amene amakhulupilira zoona. Amakhulupilira mu zinthu zitatu zimene anatichitira. Amakhulupilira kuti Yesu anabwera ndi kubatizidwa kuti achotse machimo athu onse, ndi kutitengera chiweruzo pamene anatifera pa mtanda, ndipo anauka kwa akufa.

Zonse izi zinachitika chifukwa chachikondi cha Mulungu. Yesu anabwera pansi pano kuchokera ku mwamba ndipo anati, “Bwerani kwa ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo ine ndidzakupatsani mpumulo.” (Mateo11:28). Anachita izi pochotsa machimo athu.

Mulungu samaganizira amene amakhulupilira mu mwazi wake wokha. Amene amakhulupilira mu mwazi wake wokha akadali ndi machimo m’mitima yao.

Ndani amene Yesu amamuona kuti

Page 173: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

173 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

ndiomboledwa? “Ndinachotsa machimo anu onse pamene ndinabwera pansi pano ndikubatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Ndikuchitira umboni kuti machimo onse adziko lapansi anaperekedwa pa ine. Ndinalipira mphoto ya machimo pa mtanda. Ndinakupulutsani.” Kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu, ndi mwazi wake, ndi kuti Iye ndi Mulungu. Onse ndi oyenera kupulumutsidwa.

Kwa iwo amene akhulupilira mu zinthu zitatu izi, Yesu akuti, “Inde, inu mwapulumutsidwa. Ndimu olungama ndinu ana a Mulungu.” Ndinu opulumutsidwa ngati mukhulupilira mu ubatizo wa Yesu, ndi mwazi wake ndiponso ndi mwa Mzimu Woyera. Amene akhulupilira mu mwadzi, ndi mwa Mzimu Woyera akadali ndi uchimo m’mitima yao.

Mu Ufumu wa Mulungu, muli choona chimodzi. Muli chilungamo, kukhulupilira ndi chikondi. Mulibe kenakake konama. Kunama ndi kunamizana kulibe kumwamba.

Kodi ndani amene akuyetsa kuchita zoipitsitsa?

Ndi amene sakhulupilira

mu ubatizo wa Yesu

M’buku la Mateo 7:22 akuti, “Paja tsiku lachiweruzo anthu ambiri adzanena kuti, Ambuye, Ambuye, kodi suja ife tinkhalalika Mau a Mulungu mzina lanu?”

Mulungu samakumbukira ntchito za munthu. “Apo Ine ndidzaœauza poyera kuti, ‘Sindidakuziœeni konse chokani apa, anthu ochita zoipa.’”(Mateo 7:23).

“Ndinapereka nyumba ziœiri kwa inu. Ndinapereka moyo wanga kwa inu. Kodi simunandione? Sindinakukaneni inu pa mtsinje wa Yalu ndinakupatsani moyo wanga. Kodi simunandione?”

Page 174: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

174 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

“Kodi mukadali ndi uchimo m’mitima yanu?” “Inde, Ambuye, ndikadali nawo.” “Ndiye kuti ndathana nanu.Palibe ochimwa amene amaloledwa kubwera kuno.” “Koma ndinaphedwa chifukwa cha inu!” “Kodi utanthauza chiyani, kufera ife?

Unamwalira chifukwa cha kupusa kwako. Kodi mumadziœa za ubatizo wanga ndi mwazi wanga? Kodi ndinachitira umboni kuti ndinu anthu anga? Kodi ndinachitira umboni m’mitima yanu kuti ndinu anthu anga? Simukhulupilira mu ubatizo wanga ndipo inenso sindichitira umboni kuti ndinu anthu anga, sindichitira umboni kuti ndinu anthu anga, koma mumapitilira kukhulupilira zanu ndipo mu mafa. Kodi ndi liti sindinachitire umboni kwa inu? Izi munadzitengera nokha. Mumakonda ndi kuyetsa kuziombola nokha. Kodi mukumvetsa? Tsono, khalani m’njira yoona.”

Yesu akutiuza kuti tidzuke ndi kuœala. Anthu oomboledwa sataya m’tima pamene sanakhale akhristu enieni ndi ambiri aneneri onama ndipo

amalephera kuœala kwambiri! Koma moto wochepa ungasanduke moto waukulu. Ngati m’modzi angaime pachoonadi ndi mphamvu ndi kuchitira umboni dziko lonse lingaœale kwambiri.

M’buku la Yesaya 60:1-2 akuti, “Iwe Yerusalemu dzuka, œala, kuœala kwako kwayamba. Ulemelero wa Chauta wakuœalira. M’dima udzaphimba dziko lapansi, m’dima wandiweyani udzagwa pa anthu amitundu ina. Koma iwe, Chauta adzakuœalira, ulemelero wake udzaoneka pa iwe.”

Ukulamula ife kuti tidzuke ndi kuœala chifukwa m’dima wopanda chilungamo ndi uthenga wonama udzaphimba dziko lapansi. Okhao okhulupilira Yesu ndi amene angamukonde Iye. Onse amene sanaomboledwe sangamukonde Yesu. Angamukonde bwanji? Amanena za chikondi koma sangamukonde zoona Iye mpaka atakhulupilira.

Page 175: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

175 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

PALI ZINTHU ZITATU ZIMENE ZIKUCHITIRA UMBONI WACHIPULUMUTSO CHA OCHIMWA

Kodi umboni wachipulumutso mu mitima yahtu ndi uti?

Ndi ubatizo wa Yesu

“Ndipo pali atatu amene akuchitira umboni padziko lapansi: Mzimu Woyera, madzi, ndi mwazi, ndi zitatu izi zigwirizana ngati ndi mumodzi.” Yesu anabwera pa dziko lapansi ndipo anachita ntchito yake kudzera mu madzi ndi mu mwazi. Anachita izi kuti atipulumutse ife.

“Ngati tilandira umboni wa anthu umboni wa Mulungu ndi wopambana; chifukwa uwu ndi umboni wa Mulungu umene anachitira Mwana

wake…” (1Yohane 5:9-12). Anthu obadwa mwatsopano amalandira umboni

wa anthu. Timaoneka kuti ndife olungama. Pamene anthu obadwa mwatsopano amene anaomboledwa akamba za chiombolo, anthu sangatsutane nawo. Koma amavomereza. Amanena kuti ife timakhulupilira moyenera, ndipo chikhulupiliro chathu nchoona. Pamene tiwafotokozera m’mene ife tinabadwira mwatsopano palibe amene amatsutsa zonena zathuzo.

Iwo amangovomereza kuti ndizoonadi. Motero timalandira umboni wa anthu ambiri. Koma m’ndime taœerengayi tamvanso “Umboni wa Mulungu ndi waukulu koposa; chifukwa umenewu ndi umboni wa Mulungu.” Ndime imeneyi ikutiuza kuti mboni ya Mulungu ndiye Mwana wake. Ndizoona eti? Nanga umboni wa Mwana wa Mulungu ndi chiyani? Chitsimikizo chakuti Mulungu atipulumutsa ndi chakuti Yesu anabwera mwa Mzimu Woyera, ndiponso Iye anabwera

Page 176: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

176 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

mwa madzi a chiombolo ndiponso anabwera ndi mwazi wake pa mtanda. Ndipo Mulungu akutitsimikizira kuti imeneyi ndiyo njira ya chipulumutso chathu, ndipo mwa njira imeneyi ife ndife ana ake chifukwa chakuti timakhulupilira m’chipulumutso chimenechi.

“Amene ali ndi mwanayo , ali nawo moyo, amene sali ndi Mwana wa Mulungu, alibe moyo”(1 Yohane 5:10).

Ndime iyi ikutiuza bwino lomwe za anthu amene ali opulumutsidwa. Ndime imeneyi ikutiuza kuti amene akhulupilira mwa Mwana wa Mulungu ali nawo moyo. Kodi inu moyo umenewu muli nawo? Moyo umenewu uli mwa inu ndiponso uli mwa ine. Mulungu anabwera pansi pano chifukwa cha ife. (Iye anabwera monga munthu kudzera mwa Maria). Pamene iye anali ndi zaka makumi atatu 30, anabatizidwa kuti asenze machimo athu onse, ndipo analangidwa pa matanda. Iye anaukitsidwa kwakufa patapita masiku atatu kuti atipatse moyo wosatha. Zoonandi Yesu

anatipulumutsa. Kodi chikadachitika nchiyani Yesu akadapanda

kuuka kwakufa? Nanga akanatitsimikizira bwanji za chipulumutso chatu ali m’manda? Ichi nchifukwa iye ni Mpulumutsi wathu. Izi ndi zimene ife tiyenera kukhulupilira.

Ndipo monga momwe Yesu ananenera, Iye anatipulutsa ndi ubatizo wake ndiponso mwazi wake. Ndipo chifukwa chakuti ife timakhulupilira, inu ndi ine ndife opulumutsidwa. Moyo umenewu uli mwa inu ndiponso mwa ine. Sichoncho? Anthu oomboledwa saiœala ‘madzi’ aubatizo wake. Sitisiyako zimene iye anachita kuti ife tipulumutsidwe.

“Umu ndi m’mene tiyenera kuchitira zimene Mulungu akufuna,” (Mateo 3:15). Ife sitingakane Yesu anasenza machimo athu onse mu mtsinje wa Yolodani pamene iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Anthu oomboledwa sangakane ‘madzi’ ubatizo wa Yesu.

Page 177: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

177 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

ANTHU AMENE AMAKHULUPILIRA KOMA SANAOMBOLEDWE AMAKANA UBATIZO WA YESU

Kodi ndani amene amapanga Mulungu

kukhala onama?

Amene sakhulupilira ubatizo wa Yesu Khristu

Kodi Yohane analikunena chiyani pamene Iye

anati, “Amene sakhulupilira Mulungu, amusandutsa onama.” Mtumwi Yohane akanakhala kuti alipo lero, akadatiuza chiyani ife akhristu? Iye akatifusa ngati Yesu anachotsadi machimo athu onse pamene iye anabatizidwa.

Kodi Yohane sanachitirenso umboni za Uthenga Wabwino wakuti Yesu anatiombola ndi ubatizo wake? Kodi machimo anu sanaperekedwe pamutu wa Yesu ndiponso kodi Yesu sananyamule machimo athu papheœa pake pamene ine ndinamubatiza? Yohane akutitsimikizira kuti Yesu anabatizidwa kuti inu mupulumutsidwe. (Yohane 1:29; 1 Yohane 5:4-8)

Amene sakhulupilira mwa Mulungu, amenenso sakhulupilira zonse zimene Iye anachita kuti ife tipulumutsidwe amamusandutsa onama. Ife tikamanena kuti Yesu anatichotsera machimo athu onse pamene anabatizidwa iwo anati, “Aa ine! Sanachotse machimo athu onse! Iye anachotsa machimo amene ife tinabadwa nawo, motero machimo amene ife timachita tsiku ndi tsiku alipobe.”

Iwo amalimbikira kunena kuti ‘tiyenera kumalapa machimo athu tsiku ndi ndikuti ife tipulumuke.’ Izi ndizimene iwo amakhulupilira. Kodi inunso mumanena zimenezi? Mumanenanso?

Page 178: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

178 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

Anthu amene sakhulupilira kuti machimo athu onse anachotsedwa mwa ife ndi ubatizo wa Yesu, amamusandutsa onama.

YESU ANATIOMBOLA KAMODZI KOKHA PAMENE ANABATIZIDWA NDI KUKHETSA MWAZI WAKE PA MTANDA

Kodi wonama ndani?

Munthu amene sakhulupilira mu ubatizo wa Yesu

Iye anabatizidwa ndi kutichotsera machimo

athu kamodzi kokha. Mulungu amapulumutsa anthu amene amakhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu, ndipo amasiya anthu amene

sakhulupilira. Anthu otereœa amapita kugehena. Choncho kaya ndife opulumutsidwa kapena ai izi zimachitika malinga ndi chikulupiliro chatu. Yesu anapulumutsa dziko lapansi ku machimo onse. Amene amakhulipira adzapulumutsidwa, ndipo amene sakhulupilira sadzapulumuka chifukwa asandutsa Mulungu kukhala onama.

Anthu sapita kugehena chifukwa cha kufooka kwawo, koma kusoœa chikhulupiliro. “Amene sakhulupilira Mulungu amusandutsa wonama”(1 Yohane 5:10). Amene sakhulupilira kuti machimo ake anaperekedwa kwa Yesu, ali kukhalabe ndi machimo mu m’tima mwake. Munthu otere sanganene kuti alibe uchimo.

Tsiku lina ndidakumana ndi m’kulu wa mpingo ndipo ndidamufunsa kuti, “Inu akulu ampingo kodi machimo anga adzachoka ndikakhulupilira Yesu?”

“Inde adzachoka.” “Nanga popeza Yesu anachotsa machimo onse

adziko lapansi ndipo anati kwatha, inu

Page 179: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

179 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

mwapulumutsidwa. Kodi sizoona zimenezi?” “Inde, ndapulumutsidwa.” “Kotero kuti mulibenso uchimo.” “Inde ndilibe.” “Nanga mukhadza chimwanso chidzachitike

nchiyani?” “Ife ndife anthu chabe. Tingaleke bwanji

kuchimwanso? Choncho tiyenera kulapa machimo athu tsiku ndi tsiku.”

M’kulu wa mpingoyu akadali ndi machimo mu m’tima mwake chifukwa sadziœa choonadi chenicheni cha chiombolo.

M’kulu wa mpingo ameneyu akugwirizana ndi anthu amene amanyoza Mulungu ndi kumusandutsa wa bodza. Kodi Yesu, amene ndi Mulungu analephera kuchotsa machimo onse adziko lapansi? Izi ndizokwiyitsa kwambiri. Kodi Yesu akadalephera kuchotsa machimo akadakhala bwanji Mulungu wa Chipulumutso? Akadatiuza bwanji kuti tizimukhulupilira? Kodi mukufuna kumusandutsa wonama? Ndiganiza kuti inu

simuchita zimenezi! Mau a Mulungu amatiuza kuti tisanyoze

Mulungu. Ichi chitanthauza kuti Mulungu tisamusandutse wonama ndipo tisayetse kunamiza Mulungu. Iye sali monga ife.

Mtumwi Yohane amatiuza moveka bwino za Uthengawu chiombolo. Anthu ambiri safuna kukhulupilira mu zinthu zimene Mulungu anatichitira (zakuti Yesu anabwera mwa madzi, mwazi ndi mwa Mzimu Woyera).

Ngati alipo ena amene sakhulupilira zimene amauzidwa ndiponso amene sakhulupilira zonse zimene Mulungu watichitira (anthu amene amadziona kuti “Ndi ochimwa”), Kodi mwa onsewa ali kunena zoona ndi uti?

Anthu amene sakhulupilira zonse zimene Mulungu anaœachitira akunama. Ndipo ali ndi chikhulupiliro chonama. Anthu amene sakhulupilira ali kumusandutsa Mulungu kukhala wonama.

Musamusandutse wonama Mulungu. Yesu

Page 180: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

180 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

anabwera ku mtsinje wa Yolodani ndipo anabatizidwa kuti achite zimene Mulungu anali kufuna (anachotsa machimo onse adziko lapansi).

MOYO WA MUNTHU OSAKHULUPILIRA UMAKANA UBATIZO WA YESU NDI CHIYERO CHAKE

Kodi Satana ndi M’dierekezi amakana

chiyani?

Ubatizo wa Yesu ndi chiyero chake

Munthu amene amakhulupilira Mwana wa

Mulungu amachitira umboni za Iye. Munthu oomboledwa akhulupilira kuti machimo ake

anaperekedwa kwa Yesu pamene iye anabatizidwa ndiponso kuti anapulumutsidwa ndi madzi ndi mwazi wa Yesu. Ndipo amakhulupiliranso kuti Yesu anabadwa pano mwa Maria; Iye anabatizidwa mu mtsinje wa Yolodani asanapachikidwe pa mtanda; Iye anafa ndipo anauka kwakufa.

Anthu olungama ali ndi umboni. Chitsimikizo cha chipulumutso chatu, ndi chikulupiliro chimene ife tili nacho mwa Yesu, amene anabwera mwa madzi, mwazi ndi mwa Mzimu Woyera. Moyo umenewu uli mwa inu. ‘Mukhale nawo moyo umenewu m’kati mwa mitima yanu.’ Ndili kunena zimenezi kwa inu. Ngati palibe umboni ndiye kuti palibenso chipulumutso, chitsimikizo cha moyo wosatha chili mwa inu.

Mtumwi Yohane adati, “amene akhulupilira mwa Mwana wa Mulungu ali nawo moyo” (1 Yohane 5:10). Kodi kukhulupilira mwazi wake okha ndiko kukhala ndi moyo? Muyenera kukhulupilira mu zinthu zonse zitatu kuti mukhale

Page 181: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

181 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

ovomerezeka pa maso pa Mulungu. Ndipokhapo pamene Yesu adakuvomerezani

kuti ndinu ‘opumulutsidwa.’ Kodi mukunena kuti mungakhale ndi moyo ngati mukhulupilira zinthu ziœiri zokha? Kumeneku ndi kukhulupilira Mulungu mwa njira yodziœa inu nokha. Kumeneku ‘ndikudzichitira umboni nokha.’

Alipo anthu ambiri amene amakhulupilira mwa njira imeneyi. Pa dziko lapansi pali anthu ambiri amene amakhulupilira zinthu ziœiri zokha mwa zitatuzi. Iwo amakhala ndi chitsimikizo chakuti anapulumutsidwa ndipo amalemba mabuku onena za chipulumutso chawo. Bwanji anthu ameneœa amafulumira kulankula! Ndiponso ndi okhumudwitsa kwambiri. Iwo amadzitchula kuti ndi athu olalika Uthenga moona. Iwo amadzionanso ngati olungama. Sakhulupilira ‘madzi’ koma amanyadira chipulumutso chao! Koma akamakamba munthu akhoza kukhulupilira kuti mwina ndi zoonadi! Koma chodziœika nchakuti anthu otereœa alibe chitsimikizo

chochokera kwa Mulungu. Ichi ndi chikhulupiliro chopanda umboni.

Munganene bwanji kuti chimechi ndi chipulumutso? Anthu okhawo amakhulupilira Yesu Khristu, amene anabwera mwa Mzimu Woyera, madzi ndi mwazi ali ndi umboni wa Mulungu ndi anthu.

Mtumwi Paulo adati, “Paja Uthenga Wabwino umene tidadza nawo kwa inu sunali wapakamwa chabe, koma tinkaulalika ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndiponso mosakaika konse.” (1 Atesalonika 1:5). Satana amakondwera ngati anthu akhulupilira mu mwazi okha wa Yesu.

Iye amati, “Aa! Anthu opusa inu ndinakunamizani…” Pali anthu ambiri amene amaganiza kuti ngati munthu atamanda mwazi wa Yesu okha, Satana amachoka mwaiwo. Iwo amaganiza kuti Satana amaopa Mtanda wa Yesu. Satana akufuna kutionetsa mphamvu yake. Choncho tisanamizidwe ndi mphamvu yakeyi.

Landirani ubatizo wa Yesu m’mitima yanu,

Page 182: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

182 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

ndipo mu dzapulumutsidwa. Satana akaloœa mwa munthu, munthuyo amakhala ngati wachita misala ndipo amalankhula zodziœa yenkha. Satana akafuna kuloœa mwa munthu savutika ayi. Iye ali nayo mphamvu yakumupanga munthu kuchita chinthu chili chonse. Satana amagwiritsa ntchito mbali imodzi ya bongo wake. Mulungu anapereka mphamvu kwa Satana yakuchita chilichonse kupatulapo kupha. Satana akhoza kumugwedeza munthu ngati masamba am’tengo.

Izi zikachitika, anthu okhulupilira amafuula, “Choka! M’dzina la Yesu ndikukulamula kuti choka!” Ndipo pamene munthu uja ayamba kukhala bwino, iwo amati ndi mwazi wa Yesu umene wapereka mphamvu imeneyi. Koma imeneyi si mphamvu ya mwazi wake ayi. Ndi Satana amene akungofuna kuonetsa mphamvu ‘yake.’

Satana amaopa anthu amene amakhulupilira mwa Yesu amene adatitsuka ndi ubatizo wake, ndiponso amene analandira chilango m’malo

mwathu ndi kukhetsa mwazi wake pa mtanda ndi kuukanso. Satana sakhala pafupi ndi mboni ya ubatizo wa Yesu ndi chipulumutso cha mwazi wake.

Monga inu mukudziœa ansembe a chikatolika amayendetsa mdyelekezi. Takhala tikuziona zimene m’makanema. Mu kanema yotchedwa ‘The Omen,’ wansembe ananyamula mtanda wa mtengo ndi kumauvinitsa koma wa nsembeyo adafa. Munthu amene adabadwa mwatsopano sangagonje mwa njira imeneyi.

Iye akhoza kukamba za mwazi ndi madzi aubatizo wa Yesu. Pamene Satana anali kufuna kumuyetsa, iye akadafunsa satanayo kuti, “Kodi ukudziœa kuti Yesu anandichotsera kale machimo anga onse?”

Pamenepo Satana akadathaœa. Satana safuna kukhala pafupi ndi muntu amene anabadwa mwatsopano. Iye akakhala pafupi ndi munthu amene ‘anabadwa mwatsopano’ amathawa. Kunalembedwa kuti amene sakhulupilira Mwana

Page 183: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

183 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

wa Mulungu amamusandutsa wonama. Iwo sakhulupilira mu umboni wa Mwana wake, umboni wonena za madzi ndi mwazi wake.

Kodi ya Mwana wa Mulungu ndi chiyani?

Ubatizo wake, mwazi

wake ndi Mzimu woyera Kodi mboni ya Mwana wa Mulungu ndi

chiyani? Umboni wake ndi wakuti Iye anabwera mwa Mzimu Woyera ndi kuchotsa machimo athu onse ndi madzi. Iye anasenza machimo athu onse ndipo anakhetsa mwazi wake pa mtanda chifukwa cha ife. Kodi chimenechi sichiombolo cha madzi, mwazi ndi Mzimu Woyera?

Anthu amanena zonama pa maso pa Mulungu chifukwa chakuti iwo sakhulupilira Uthenga Wabwino wonena za madzi, ndi mwazi, Uthenga

wa chipulumutso. Zikhulupiliro zaozo ndi zonama, ndipo zimangopititsa patsogolo chiphunzitso chonama.

Tiyeni tione pa 1 Yohane 5 ndime ya 11, “Umboniwo tsono ndiwakuti Mulungu adatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowo umapezeka mwa Mwana wake.” Ndime imeneyi ikutiuza kuti Mulungu anatipatsa mwa anthu amene amaulandira. Ndiponso moyowo uli mwa Mwana wake.

Anthu amene amalandira moyo wosatha ndi amene anaomboledwa pakukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake. Anthu oomboledwa amalandira moyo wosatha ndipo amaulandira kwa muyaya. Kodi inu mudalandira moyo wosatha?

Pa ndime ya 12, “Amene ali ndi Mwanayo ali nawo moyo, amene sali ndi Mwana wa Mulungu, alibe moyo.” Tinganenenso kuti amene amakhulupilira mu zonse zimene Yesu anachita pansi pano: Pakubatizidwa ndi kufa pa mtanda ndi kuuka kwake, ali nawo moyo. Koma amene

Page 184: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

184 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

apatulapo chimodzi mwa zitatuzi sadza upeza moyo wosatha, ndipo sadzapulumutsidwa.

Mtumwi Yohane ananena za anthu a Mulungu amene amakhulupilira mu zinthu zonse zimene Yesu anachita: Madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera. Zonsezi zimatiuza bwino ngati ali kupatula anthu oomboledwa pa chikhulupiliro chawo mu madzi aubatizo wa Yesu, mwazi wake ndi Mzimu Woyera.

MUNTHU AMENE SANABADWENSO MWATSOPANO SANGATHE KUSIYANITSA PAKATI PA NKHOSA NDI MBUZI

Kodi ndani angathe kusiyanitsa pakati

pa anthu oomboledwa ndi osaomboledwa

Munthu amene wabadwa

mwatsopano Mtumwi Yohane adasiyanitsa bwino anthu

olungama amene anaomboledwa. Nayenso Paulo adachita chimodzimodzi. Kodi atumiki a Mulungu amasiyanitsa bwanji nkhosa ndi mbuzi? Kodi amasiyanitsa bwanji pakati pa atumiki oona a Mulungu ndi amene amangodzifanizira? Anthu

Page 185: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

185 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

amene anaomboledwa pakukhulupilira madzi ndi mwazi wa Yesu amalandira mphamvu ya kutha kuona.

Kaya munthu ndi mbusa, m’laliki kapenanso m’kulu wa mpingo ngati sangathe kudziœa munthu oomboledwa ngati sangathe kusiyanitsa nkhosa ndi mbuzi, ndiye kuti nayenso sanaomboledwe ndipo mwa iye mulibe moyo wosatha. Koma anthu amene anaomboledwa akhoza kuona kusiyana kwake. Anthu amene sanaomboledwe sangathe kusiyanitsa ngakhale kuziœa kumene.

Kuli ngati kusiyanitsa mitundu yosiyana siyana mu m’dima. Chinthu chobiliœira ndi chobiliœira ndithu ndipo choyera ndi choyera ndithu. Mutatseka maso anu, simungaone kapenanso kudziœa mtundu wa chinthu.

Koma anthu amene ali kupenya akhoza kusiyanitsa bwino mitundu ya zinthu. Angathe kuona kuti ichi nchobiliœira ndipo ichi nchoyera. Momwemonso, pali kusiyana koonekeratu pakati

pa anthu oomboledwa ndi anthu amene sanaomboledwe.

Tiyenera kulalika Uthenga Wabwino wa chiombolo, Uthenga wa madzi, mwazi wake ndi Mzimu Woyera. Tiyenera kuuka ndi kuœala. Pamene tasonkhanitsa anthu kuti tilalike za chikulupiliro, sitalankhula mau a munthu. M’baibulo pa 1 Yohane 5 akufotokozera bwino tanthauzo lake. Tiyenera kufotokozera pan’ono pang’ono kuti pasakhale chisokonezo.

Mau amene timalalika, Mau onena za madzi, mwazi ndi Mzimu Woyera wa Yesu ndi kuœala kwa chiombolo. Kufalitsa Uthenga wonena za ‘madzi’ a Yesu ndiko kuunika kwathunthu. Kufalitsa Uthenga wa mwazi wa Yesu ndiko kuunika kwenikeni. Tiyenera kufotokozera momveka bwino kuti pasakhale munthu padziko lino amene sadziœa zimenezi.

Ngati anthu oomboledwa sa uka ndi kuœala, anthu ambiri adzafa popanda chiombolo, ndipo Mulungu sadzakondwera. Iye adzatitcha antchito

Page 186: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

186 Yesu anabwera mwa Madzi, mwa magadzi ndi mwa Mzimu Woyera

◄ Zam'kati ►

aulesi. Tiyenera kufalitsa Uthenga wa madzi ndi mwazi wa Yesu Khristu.

Chimene ndili kunena mobwerezabwereza ndi chakuti ubatizo wa Yesu ndi wofunika kwambiri kuti ife tipulumutsidwe. Pamene tili kulankhula ndi ana, tiyenera kufotokozera mobwereza bwereza kuti titsimikize kuti anawo amvetsadi.

Page 187: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

◄ Zam'kati ►

ULALIKI ŒA CHISANI NDI CHIŒIRI

Ubatizo wa Yesu ndi Chifanizo cha

Chipulumutso cha Ochimwa

Page 188: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

188 Ubatizo wa Yesu ndi Chifanizo cha Chipulumutso cha Ochimwa

◄ Zam'kati ►

Ubatizo wa Yesu ndi Chifanizo cha

Chipulumutso cha Ochimwa

< 1 Petro 3:20-22 > “M’chombomo anthu oœerengeka okha, asanu

ndi atatu, adapumuluka ndi madzi. Madziwo akufanizira ubatizo umene masiku ano umakupulumutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Kristu. Kubatizidwa kumeneku (sikuchotsa litsiro la mthupi, koma kudzipereka kwa Mulungu ndi adapita kumwamba ndipo ali kudzanja la manja la Mulungu, kumeneko angelo ndi maulamuliro ndi zimphamvu zimamvera Iye.”

Kodi tinalungamitsidwa bwanji?

Mwa chisomo cha

Mulungu Ife tinabadwa pa dziko lino lapansi, koma

tisanabadwe Mulungu anali kutidziœa kale. Iye anadziœa kuti tidzabadwa ndi uchimo ndipo nchifukwa chake Iye adatipulumutsa kudzera mu ubatizo wa Yesu, umene unachotsa machimo athu onse. Anapulumutsa anthu onse okhulupilira ndi kuwasandutsa kukhala anthu ake.

Zonsezi zinachitika chifukwa cha chisomo cha Mulungu, monga adanena wolemba Masalimo 8:4, “Kodi munthu nchiyani kuti mukumbukira?” Anthu oomboledwa amenenso apulumutsidwa ku machimo awo onse ndi zipatso za chikondi cha’mtengo wapatali cha Mulungu. Iwo ndi ana

Page 189: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

189 Ubatizo wa Yesu ndi Chifanizo cha Chipulumutso cha Ochimwa

◄ Zam'kati ►

ake. Kodi ife tinali yani, amene timakhulupilira

madzi okha ndi Mzimu Woyera, tisanakhale ana a Mulungu, tisanakhale olungama, ndiponso tisanapulumutsidwe ndi kulandira ufulu wakumutchula Iye kuti Atate? Tinali anthu ochimwa, amene tinabadwa ndi kukhala pa dziko lino zaka 60 ndi 70 kapekanso zaka 70 mpaka 80 ngati tili ndi moyo wathanzi.

Tisana tsukidwe machimo athu, ndipo tisana khulupilire mu Uthenga wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake, tinali anthu osalungama amene tinali woyera kulangidwa.

Mtumwi Paulo adanena kuti chinali chisomo cha Mulungu kuti iye akhale mtumwi. Ife tiyenera kuthokoza Mulungu kuti tili kuoneka monga m’mene tilili. Tiyenera kumuthokoza chifukwa cha chisomo chake. Mlengi anabwera pa dziko lino ndi kutipulumutsa, kutisandutsa ana ake, anthu ake. Tikumuthokoza chifukwa chachipulumutso chimene anatikonzera mwa

chisomo chake mwa madzi ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chiyani Iye anatilola kukhala ana

ake, olungama? Kodi nchifukwa chakuti ndife ooneka bwino? Kapena chifukwa chakuti ndife oyenera? Kapena chifukwa chakuti ndife abwino? Tatiyeni tiganizire zimenezi ndipo tikapeza chifukwacho tithokoze Mulungu.

Chifukwa chake nchakuti Mulungu anatilenga kuti tikhale anthu ake ndipo anatilola kuti tikhale naye mu ufumu wa kumwamba. Mulungu anatisandutsa ana ake kuti tikakhale naye mu ufumu wake kwa muyaya. Palibe chifukwa china chimene Mulungu anatidalitsira ndi moyo wosatha. Sizoona kunena kuti Iye anatisandutsa ana ake chifukwa chakuti timaoneka bwino, kapena popeza ndife oyenera, kapena kuti tili ndi moyo wabwino kupambana zolengedwa zonse. Koma chifukwa chake nchakuti Iye amatikonda.

“Madziwo akufanizira ubatizo umene masiku ano umakhupulumutsani” (1 Petro 3:21). “M’chombomo anthu oœerengeka okha, asanu ndi

Page 190: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

190 Ubatizo wa Yesu ndi Chifanizo cha Chipulumutso cha Ochimwa

◄ Zam'kati ►

atatu, adapulumuka ndi madzi” (1 Petro 3:20). Anthu ochepa okha, m’modzi wa mu m’zinda

ndipo aœiri a banja limodzi anapulumutsidwa. Kodi ife ndife abwino kuposa ena? Ayi ndithu. Sindife anthu opatulika koma tinapulumutsidwa pakukhulupilira mu madzi ndi Mzimu Woyera.

Ndi chinthu chozizwitsa kuti ife tapulumutsidwa, ndipo ndi mphatso yosayembekezeka ndipo dalitso lalikulu kuti timutchule Mulungu kuti Atate, Ambuye athu. Ife sitingakane zimenezi. Kodi tinga tinganene bwanji Mulungu ndi atate kapenanso Ambuye athu ngati tikadali anthu ochimwa?

Pamene tili kuganiza zakupulumutsidwa kwathu, timadziœanso kuti ife ndife okondedwa ake a Mulungu. Kodi sitingathe kumuthokoza? Ife tikanabadwa ndi kufa popanda tanthauzo, ndipo tikanapita kugehena akadakhala kuti Mulungu satikonda. Timathokoza Mulungu nthaœi ndi nthaœi chifukwa cha madalitso amene Iye amatipatsa, ndiponso chikondi chake potisandutsa

ana ake ndi oyenera pa maso pake.

CHIPULUMUTSO CHA MTENGO WAPALI KUDZERA MU UBATIZO WA YESU

Nchifukwa chiyani anthu mu nthawi ya Nowa

anaonongeka?

Nchifukwa chakuti sanakhulupilire mu madzi

(ubatizo wa Yesu) “Madziwo akufanizira ubatizo umene masiku

ano umakupulumutsani” Petro analemba kuti anthu asanu ndi atatu okha adapulumuka ndi madzi. Kodi mu nthaœi ya Nowa anthu adalipo

Page 191: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

191 Ubatizo wa Yesu ndi Chifanizo cha Chipulumutso cha Ochimwa

◄ Zam'kati ►

angati? Sitidziœa kuchuluka kwa anthu amene adaalipo pa nthaœiyo, koma tatiyeni tiyerekeze kuti adaalipo okwana 1 Miliyoni. Anthu asanu ndi atatu okha mwa anthu 1 Miliyoni ndi amene adapulumuka.

Kuchuluka kwa anthu kukanakhala chimodzi modzi lero. Anthu akunena kuti padziko lonse lapansi pali anthu 6 biliyoni ndikunena pano. Ndi angati amene atsukidwa machimo awo mwa anthu okhulupilira mwa Yesu? Titayang’ayana anthu amu mzinda umodzi wokha tidzaona kuti ndi anthu ochepa okha.

Mu mzinda umene uli ndi anthu 250,000 kodi ndi angati amene aomboledwa ku machimo ao kapena 200 okha. Kodi zimenezi zitanthauza chiyani? Izi zikutanthauza kuti m’modzi mwa anthu 1000 analandira madalitso a chiombolo.

Pali chikhulupiliro chakuti m’dziko la Korea muli akhristu okwana 12 miliyoni, kuphatikizapo a Katolika. Kodi mwa anthu onseœa ndi angati amene anabadwa mwatsopano mwa madzi ndi

mwa Mzimu Woyera? Tiyenera kukumbukira kuti anthu asanu ndi atatu okha adapulumuka mwa anthu onse amene analipo pa nthaœi ya Nowa. Dziœani kuti Yesu anatichotsera machimo onse aanthu okhulupilira mu ubatizo wake.

Si anthu ambiri amene amakhulupilira kuti Yesu anaœaombola ndi ubatizo wake ndiponso mwazi wake pa Mtanda. Taonani pa chithunzi chotchuka chotchedwa, ‘The Resurrection of Jesus.’ Kodi pamenepo mumaona anthu angati ouka kwakufa? Mukhoza kuœaona akuchokera ku Yerusalemu kubwera pafupi ndi Yesu, amene watambasula manja ake. Koma ndi angati mwa iwo amene akudziœa za Mulungu?

Masiku ano padziko lapansi pali anthu ambiri ophunzira za Mau a Mulungu, koma mudzaona kuti ndi anthu ochepa okha amene amadziœa ndi kukhulupilira ubatizo wa chiombolo. Ena mwa iwowa amanena kuti Yesu anabatizidwa pofuna kuonetsa kudzichepetsa kwake, koma ena amati Yesu anabatizidwa kuti akhale ngati munthu wina

Page 192: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

192 Ubatizo wa Yesu ndi Chifanizo cha Chipulumutso cha Ochimwa

◄ Zam'kati ►

aliyense. Baibulo limanena kuti atumwi onse,

kuphatikizapo Petro ndi Yohane anatitsimikizira kuti za kuchotsedwa kwa machimo athu kudzera mu ubatizo wa Yesu.

Umenewu ndi Uthenga wodabwitsa wa chisomo cha Mulungu kotero kuti ife tikhoza kupulumuka pakungokhulupilira Uthenga umenewu.

PALIBE KUNENA KUTI ‘MWINA’ PA ZA UBATIZO WA CHIOMBOLO

Kodi amalandira chikondi cha Mulungu

ndani?

lye amene amakhulupilira mu ubatizo ndi mwazi

wa Yesu

Nthaœi zina timaganiza kuti tikhoza kupulumutsidwa pa kungokhulupilira Yesu yekha. Mipingo yonse ikudalira pa zikhulupiliro zao, ndi anthu ambiri amaganiza kuti ubatizo wa Yesu ndi umodzi mwa izo. Koma zimenezi sizoona. Mwa mabuku ambiri mbiri amene ndakhala ndikuœerenga, sindinathe kupeza buku lonena za chipulumutso limene limafotokoza mwa tchutchutchu kugwirizana kwa chiombolo cha ubatizo ndi mwazi wa Yesu ndi chipulumutso.

Anthu asanu ndi atatu okha adapulumuka pa nthaœi ya Nowa. Si ndidziœa kuti ndi anthu angati akadapulumuka masiku ano, komabe si ambiri. Anthu amene adzapulumuke ndi okhawo amene amakhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake. Nditayendera mipingo ya mbiri, ndidaona pali mipingo yochepa yokha imene ikulalika za ubatizo wa Yesu, umene uli Uthenga woona.

Ngati sitikhulupilira ubatizo wa chiombolo ndi mwazi wake, tikadali anthu ochimwa. (Palibe kanthu kuti timapita ku tchalichi kaœirikaœiri).

Page 193: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

193 Ubatizo wa Yesu ndi Chifanizo cha Chipulumutso cha Ochimwa

◄ Zam'kati ►

Tikhoza kumapemphera mokhulupilika moyo wathu wonse. Koma ngati machimo alipobe m’mitima mwathu tili ndi tsoka.

Ngati takhala tili kupita ku tchalichi kwa zaka makumi asanu (50) ndikumakhalabe ndi uchimo m’mitima mwathu, ndiye kuti chikhulupiliro chimene takhala nacho zaka 50 ndi chopanda ntchito, ndiponso ndi chinyengo chabe. Kuli bwino kukhala ndi chikhulupiliro choona cha tsiku limodzi lokha. Mwa anthu amene amakhulupilira Yesu, anthu okhawo amene amakhulupilira moonadi tanthauzo la ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake ndi amene adzaloledwe kuloœa kumwamba.

Chikhulupiliro choona ndi chimene chimakhazikika mwa Mwana wa Mulungu amene anabwera pansi pano ndi kubatizidwa kuti achotse machimo athu onse. Chikhulupiliro chimemechi ndicho chimatitengera ku moyo wosatha kumwamba. Tiyeneranso kukhulupilira kuti Yesu anakhetsa mwazi pa mtanda chifukwa cha inu ndi ine. Ndipo chifukwa cha ichi tiyenera kuthokoza

Mulungu. Kodi ife ndife yani? Ndife ana a munthu amene

Yesu adamupulumutsa ndi ubatizo ndi mwazi wake. Tingalephere bwanji kumuthokoza? Yesu anabatizidwa mu Mtsinje wa Yolodani ali ndi zaka makumi atatu (30) kuti atipulumutse. Mwa ichi, Iye anachotsa machimo onse ndi kulandira chilango pa mtanda chifukwa cha ife.

Pamene tikuganiza zimenezi, tiyenera kumuthokoza. Tiyeneranso kudziœa kuti Yesu anachita zonsezi pa dziko lino lapansi kuti ife tipulumutsidwe. Poyamba Iye anabwera padziko lino la pansi. Iye anabatizidwa, ndipo anapachikidwa pa mtanda ndiponso anauka kwakufa pastiku la chitatu, ndipo ali kukhala kudzanja la manja la Mulungu.

Chiombolo cha Mulungu ndi cha wina aliyense popanda kusankha. Chipulumutso cha Yesu ndi cha inu ndi ine. Timayamika Mulungu chifukwa cha chikondi chake ndi madalitso ake.

Pali nyimbo ya uzimu imene imati, “♫Kuli

Page 194: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

194 Ubatizo wa Yesu ndi Chifanizo cha Chipulumutso cha Ochimwa

◄ Zam'kati ►

kankhani kabwino. ♫Mwa anthu onse pa dziko lapansi, ndine ndekha amene ndikhala m’chikondi chake. ♫A chikondi chodabwitsadi! ♫Chikondi chake paine. Pali kankhani ka bwino. ♫Mwa anthu onse pa dziko lino, ndife tokha opulumutsidwa, amene tidasanduka ana ake. Tikuvala chikondi chake. ♫A chikondi cha Mulungu, chisomo cha Mulungu. Chikondi chodabwatsadi! Chikondi chake pa ine. ♫”

Yesu anabwera pansi pano kudzapulumutsa inu ndi ine, ndipo chiombolo cha ubatizo wake ndi cha inu ndi ine. Uthenga umenewu si nthano chabe ai, koma ndi choonadi chimene chimatichotsa m’moyo wa mavuto uno ndi kutitengera ku Ufumu wa kumwamba. Chikhulupiliro chimenechi ndi ubale pakati pa inu ndi Mulungu.

Iye anabwera pansi pano kudzatipulumutsa. Iye anabatizidwa ndi kulandira chilango cha pa mtanda kuti atichotsere machimo athu onse.

Ndi dalitso lalikulu anthu okhulupilira azitchula

Mulungu kuti Atate! Kodi tingakhulupilire bwanji Yesu ngati Mpulumutsi ndi kupulumutsidwa ku machimo ndi chikhulupiliro chathu? Zonse ndi zotheka chifukwa cha chikondi chake pa ife. Tapulumutsidwa chifukwa cha chikondi cha Iye amene anatikonda poyambilira.

YESU KHRISTU ANACHOTSA MACHIMO ATHU ONSE KAMODZI KOKHA

“Paja nayenso Khristu adafera machimo

aanthu kamodzi kokha, kuti atifikitse kwa Mulungu” (1Petro 3:18). Yesu Khristu anabatizidwa ndi kufa pa mtanda kamodzi kokha kuti apulumutse inu ndi ine, anthu osayenera konse.

Page 195: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

195 Ubatizo wa Yesu ndi Chifanizo cha Chipulumutso cha Ochimwa

◄ Zam'kati ►

Kodi tinapulumutsidwa kamodzi kokha, kapena

mopitiliza?

Kamodzi kokha Pofuna kuchotsa chiœeruzo chathu pa maso pa

Mulungu, Iye anafa kamodzi kokha padziko lino lapansi. Kuti ife tidzakhale nawo mu Umufu wa Mulungu, Iye anabwera pansi pano monga munthu ndi ku chotseratu machimo athu onse kamodzi kokha ndi ubatizo wake, imfa yake pa mtanda ndi kuuka kwake.

Kodi inu mumakhulupilira kuti Yesu Khristu anatipulumutsa ndi ubatizo wake ndiponso mwazi wake? Ngati simukhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wake, simungapulumuke. Chifukwa cha kuti ndife ofooka, sitingabadwe mwatsopano ngati sitikhulupilira kuti Yesu anachotseratu machimo

athu onse kamodzi kokha mwa ubatizo ndi mwazi wake.

Iye anabatizidwa kutichotsera machimo athu onse ndipo analangidwa pa mtanda chifukwa cha ife kamodzi kokha. Yesu anachotsa machimo onse adziko lapansi ndi ubatizo wake wa chiombolo, ndi mwazi wake.

Chikadakhala chovuta kuti ife tiomboledwe pakulapa machimo athu nthaœi ndi nthaœi pamene tachimwa, kapenanso pakukhala anthu abwino ngakhalenso pakupereka zopereka ku tchalichi.

Choncho kuika chikhulupiliro mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu ndi chinthu choyenera pa chipulumutso chathu. Tiyenera kukhulupilira madzi ndi mwazi wake. Sitingachite ntchito zabwino zokha kuti tibadwenso mwatsopano.

Sitingazithandiza kugulira zovala anthu osauka kukonza chakudya chabwino cha abusa. Yesu amapulumutsa anthu amene amakhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wake. Ngati tikhulupilira kuti Mulungu anatipulumutsa kudzera mwa Yesu ndi

Page 196: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

196 Ubatizo wa Yesu ndi Chifanizo cha Chipulumutso cha Ochimwa

◄ Zam'kati ►

ubatizo wake ndiponso mwazi wake kamodzi kokha, tidzapulumuka.

Ena akhoza kumaganiza kuti ngakhale Mulungu ananena kale m’Baibulo, Iwo akhoza kuyamba kuikapo maganizo awo. Izi zili kwa iwo. Koma ife tiyenera kukhulupilira zonse zimene Mau a Mulungu amanena.

Pa Ahebri 10:1-10, timaœerenga kuti Iye anatipulumutsa kamodzi. Ndi zoonadi kuti Mulungu anapulumutsa anthu onse amene amakhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake kamodzi. Ife tiyenera kukhulupiliranso zimenezi. “♫ Iye anafa kamodzi, anatipulumutsa kamodzi. A! abale khulupilirani, kuti muomboledwe. Ikani magoli anu pansi pa ubatizo wa Yesu.♫” Yesu anatichotsera kusalungama kwathu ndi machimo athu onse pakubatizidwa kamodzi, ndi kukhetsa mwazi kamodzi.

‘Wolungama chifukwa cha osalungama’ (1 Petro 3:18). Yesu ndi Mulungu ndipo alibe uchimo, ndiponso sanachimweko. Iye anabwera

kwa ife monga munthu kuti adzachotse machimo aanthu onse. Iye anabatizidwa ndi kuchotsa machimo onse aanthu osalungama. Iye anatipulumutsa ku machimo ndi kusalungama kwathu.

Machimo onse amunthu kuchokera pa nthaœi imene iye anabadwa kufikira nthaœi ya kufa kwake, anaperekedwa kwa Yesu pamene anabatizidwa, ndipo anthu onse anapulumutsidwa ku chilango pamene Iye anakhetsa mwazi ndi kufa pa Mtanda. Iye anabatizidwa chifukwa cha anthu ochimwa ndipo anafa m’malo mwa ochimwa.

Ichi ndicho chiombolo cha ubatizo wake. Yesu anapulumutsa ife tonse ochimwa kamodzi kokha. Ife tonse ndife ofooka! Yesu anaombola ife tonse kuchokera pa nthaœi imene ife tinabadwa kufikira pa nthaœi ya kufa kwthu ndiponso adadzipereka ku chilango cha pa mtanda.

Ife okhulupilira mwa Yesu tiyenera kukhulupilira kuti Iye anatipulumutsa ndi ubatizo komanso mwazi wake kamodzi kokha.

Page 197: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

197 Ubatizo wa Yesu ndi Chifanizo cha Chipulumutso cha Ochimwa

◄ Zam'kati ►

Ife ndife ofooka, koma Yesu si ofooka. Ife ndife osakhulupilika, koma Yesu ndi okhulupilika. Mulungu adatipulumutsa kamodzi kokha. “Mulungutu adaœakonda kambiri anthu apa dziko lonse lapansi, anali naye Mwana mmodzi yekha komabe adampereka kuti aliyense wokhulupilira iyeyo asataike koma akhale ndi moyo wosatha” (Yohane 3:16). Mulungu adatipatsa Mwana wake wobadwa yekha. Iye analola kuti Mwana wake abatizidwe kuti machimo onse adziko lapansi aperekedwe kwa iye ndi kulandira chilango chifukwa cha anthu onse.

Ichi ndi chikondi chodabwitsadi! Timuthokoze Mulungu chifukwa cha chipulumutsochi. Mulungu amapulumutsa anthu okhawo amene amakhulupilira madzi ndi mwazi wa Yesu Khristu ndiponso choonadi chakuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu.

Choncho, anthu amene amakhulupilira Yesu akhoza kupumulutsidwa pakukhulupilira choonadi cha ubatizo ndi mwazi wa Yesu kukhala ndi moyo

wosatha monga anthu olungama. Ife tonse tiyenera kukhulupilira zimenezi.

Kodi adatipulumutsa ndani? Kodi Mulungu amene adatipulumutsa, kapena ndi chimodzi mwa zolengedwa zake? Adatipulumutsa ndi Yesu Khristu, yemwenso ndi Mulungu. Ife tinapulumutsidwa chifukwa tidakhulupilira chiombolo cha Mulungu, ndipo ichi ndi chipulumutso cha chiombolo.

YESU NDI AMBUYE WA CHIPULUMUTSO

Kodi mau akuti Khristu atanthauza chiyani?

Wansembe, Mfumu, Mneneri

Yesu Khristu ndi Mulungu. Dzina la Yesu

litanthauza Mpulumutsi, ndipo Khristu atanthauza

Page 198: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

198 Ubatizo wa Yesu ndi Chifanizo cha Chipulumutso cha Ochimwa

◄ Zam'kati ►

‘Wodzozedwa’. Monga Samuele adadzoza Saulo m’Chipangano Chakale, mafumu ankadzozedwa, ansembenso ankadzozedwa ndiponso aneneri kuti agwire bwino ntchito ya uneneri anali kudzozedwanso.

Yesu anabwera pa dziko lino lapansi ndipo anadzozedwa pa maudindo atatu: Ya wansembe, Mfumu ndiponso Mneneri. Monga wansembe wa kumwamba, Iye anabatizidwa kuchotsa machimo aanthu m’malo zolengedwa zonse.

Pakumvera chifuniro cha Atate ake, Iye adazipereka ngati nsembe ya uchimo pa maso pa Atate ake. “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu wodza kwa Atate popanda kudzera mwa ine.” Yesu adapulumutsa anthu amene amakhulupilira Iye pakuchotsa machimo awo kudzera mu ubatizo wake ndiponso pakupachikidwa.

“Pa kuti moyo wa chinthu cholengedwa chilichonse uli m’magazi” (Levitiko 17:11). Yesu anakhetsa mwazi wa pa Mtanda atabatizidwa kale;

Motero adapereka moyo wake kwa Mulungu monga mphotho ya machimo athu kuti ife okhulupilira tipulumutsidwe.

Iye anauka kwakufa masiku atatu atafa pa Mtanda ndipo anakalalikira mizimu imene inali ku ndende. Anthu amene pakadali pano sanaomboledwe ali ngati mizimu yoikidwa m’ndende ya machimo, ndipo Yesu amalalikira Uthenga wa choonadi kwa iwo: Uthenga wa madzi ndi mwazi.

Mulungu watipatsa Uthenga wa madzi ndi Mzimu Woyera kuti atipulumutse. Aliyense wokhulupilira Uthengayu adzabadwa mwatsopano.

UBATIZO NDI MWAZI WA YESU KHRISTU UMAPULUMUTSA ANTHU OCHIMWA

Yesu Khristu ndi Mpulumutsi wathu, Petro

Page 199: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

199 Ubatizo wa Yesu ndi Chifanizo cha Chipulumutso cha Ochimwa

◄ Zam'kati ►

adatitsimikizira pa 1 Petro 3:21-22 “Madziwo akufanizira ubatizo umene masiku ano umakupulumutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Khristu. Kubatizidwa kumeneku (sikuchotsa litsiro la m’thupi koma kudzipereka kwa Mulungu ndi m’tima woona).” Madzi aubatizo wa Yesu ndi ofunika kwambiri pa chipulumutso cha anthu ochimwa.

Tingakhale nawo bwanji moyo wabwino pa maso

pa Mulungu?

Pakukhala ndi chikhulupiliro mu ubatizo ndi mwazi

wa Yesu Yesu anachotsa machimo aanthu ochimwa

pakunyamula machimowo kudzera mu ubatizo wake. Kodi inu mumakhulupilira ubatizo wa

Yesu? Kodi inu mumakhulupilira kuti mitima yanu inatsukidwa kudzera mu ubatizo wa Yesu? Mitima inatsukidwa koma thupi lathu limapitilirabe kuchimwa.

‘Munthu akaomboledwa’ sizitanthauza kuti munthuyo sadzachimwanso. Timachimwa. Koma mitima yathu imakhala yopanda tchimo chifukwa timakhulupilira mu ubatizo wake. Ubatizowu sutanthauza “kuchotsedwa litsiro la m’thupi koma kudzipereka kwa Mulungu ndi m’tima woona” (1 Petro 3:21).

Popeza kuti Yesu adandichotsera machimo anga, ndipo popeza kuti Mulungu anavomera kulandira chilango chifukwa cha ine, ndingalephere bwanji kumukhulupilira! Podziœa kuti Yesu, yemwenso ndi Mulungu, adandipulumutsa kudzera mu ubatizo wake ndiponso mwazi wake, ndingalephere bwanji kumukhulupilira! Tinapulumutsidwa pa maso pa Mulungu ndipo panopa mitima yathu ndi yoyera. Sitinganenenso pa maso pa Mulungu kuti Yesu

Page 200: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

200 Ubatizo wa Yesu ndi Chifanizo cha Chipulumutso cha Ochimwa

◄ Zam'kati ►

sadachotseretu machimo ndiponso kunena kuti Mulungu satikonda.

Mitima yathu ili ndi tcheru ndipo imatidzudzula tikachita zinthu zoipa. M’tima wathu ukanyansidwa pang’ono, sitingakhale omasuka popanda kukhulupilira ubatizo wa Yesu. Iyi ndi njira yokhayo imene tingakhalire ndi m’tima wabwino.

Pamene m’tima wathu ukutitsutsa, ndiye kuti china chake chalakwika. Madzi a ubatizo wa Yesu adatsuka litsiro lonse la uchimo m’mitima mwathu. Yesu anachotsa machimo athu onse ndi ubatizo wake ndi kuchotsa litsiro la uchimo m’mitima mwathu. Tikakhulupilira zimenezi, m’tima wathu ukhoza kukhala woyera. Kodi m’tima wathu ungatsukidwe bwanji? Pakukhulupilira ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Munthu aliyense ali ndi m’tima woipa ndi wa litsiro la uchimo kuchokera pa nthaœi imene iye adabadwa. Koma ngati tikhulupilira kuti machimo athu anaperekedwa kwa Yesu, litsiro lonse la

uchimo lidzachoka m’mitima mwathu. Ichi ndi chikhulupiliro cha anthu obadwa

mwatsopano. Sichinthu chimene inu mungavomere mwa kufuna kwanu. Kodi m’tima wanu ndi woyera? Kodi ndi woyera chifukwa chakuti inu mwakhala ndi makhalidwe abwino? Kapena ndi woyera chifukwa chakuti inu mumakhulupilira mwa iye? Ndi kudzera m’chikhulupiliro chokha m’mene inu mungapezere moyo umenewu.

Pali mau a moyo ndiponso mau opanda moyo. Kodi mitima ya anthu onse ingatsukidwe bwanji? Njira yokhayo imene ife tingakhalire wolungama ndi kukhala ndi m’tima woyera ndi kukhulupilira mu chipulumutso chathunthu kudzera mwa Yesu.

Pamene tayeretsedwa pakukhulupilira mu ubatizo wake, sizithanthauza kuchotsedwa kwa litsiro la m’thupi koma kudzipereka kwa Mulungu ndi m’tima woona. Nchifukwa chake Iye anabwera ndi kubatizidwa ndiponso anafa pa matanda ndi kuukanso kwa akufa ndipo ali kukhala ku dzanja la manja la Mulungu.

Page 201: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

201 Ubatizo wa Yesu ndi Chifanizo cha Chipulumutso cha Ochimwa

◄ Zam'kati ►

Ndipo nthaœi ikadzakwana, Iye adzabweranso. “Adzaonekanso kachiœiri, osati kuti adzachotsenso uchimo ai, koma kuti adzapulumutse anthu amene akumuyembekeza.” (Ahebri 9:28). Ife timakhulupilira kuti iye adzabweranso kudzatenga anthu amene akumuyembekeza mokonzeka, amene amakhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wake.

KUPIMA CHIKHULUPILIRO NGATI KU CHIPATALA

Kodi tingapulumuke popanda ubatizo wa Yesu?

Ai ndithu

Tinachita kufukufuku wachipatala

mosayembekezera pa tchalichi chathu cha Taejon. Mbusa Park waku Taejon Church anauza banja

lina pa dziko lapansi palibenso uchimo koma adalephera kufotokoza tanthauzo la ubatizo wa Yesu. Mwamuna wa m’kaziyo anali kugona pa nthaœi ya ulaliki akapita kukapemphera nawo ku mipingo ina chifukwa abusa ampingoyo sankakambapo za chiombolo kudzera mu ubatizo wa Yesu, zimenenso zina mupangitsa kuti azilapa machimo ake tsiku ndi tsiku.

Koma ku mpingo wathu wa Taejon, munthu ameneyu anali kukhala tcheru kumvera ulaliki chifukwa anauzidwa kudzera mu ulaliki umene mbusa anali kulalika anauzidwa kuti machimo ake onse anaperekedwa kwa Yesu. Ndipo chinakhala chinthu chosavuta kuti m’kazi wake amuumirize kuti ayambe kupemphera ku mpingo umodzi.

Tsiku lina, munthu uja anakhala pa mwambo wa mapemphero m’tchalichi ndipo adamva mau ochokera pa Aroma 8:1 “Motero tsopano palibiletu mlandu wotsutsa anthu amene amakhala

Page 202: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

202 Ubatizo wa Yesu ndi Chifanizo cha Chipulumutso cha Ochimwa

◄ Zam'kati ►

mwa Khristu Yesu.” Pa nthaœi yomweyo iye anati, ‘A, Ngati munthu akhulupilira Yesu, ndiye kuti alibe uchimo. Popeza ine ndi makhulupilira Yesu ndilibenso uchimo.’

Motero iye anaimba foni kwa m’lamu wake ndi anzake onse mmodzi mmodzi ndipo adaœafunsa kuti, “Kodi inu muli ndi uchimo mu mtima mwanu? Ndiye kuti chikhulupiliro chanu si choona.” Pamenepa mbusa Park ndiye kuti anatayika. Mwamuna uja sankadziœa ubatizo wa Yesu koma anali kulimbikira kuuza anzake kuti iye alibe uchimo.

Pambuyo pake banja lija lidayamba kukhala ndi mavuto. M’kazi uja anali wokhulupilika komabe mu m’tima mwake anali ndi uchimo pamene mwamuna wake anali kunena kuti alibe uchimo. Mwamuna anapita ku tchalichi kwa nthaœi yochepa yokha koma anakhala kale wopanda uchimo.

M’kazi uja adaali ndi chitsimikizo chakuti onsewo (iye ndi mwamuna wake) anali ndi

uchimo m’mitima mwao. Pamenepa aœiriwa anayamba kutsutsana. Mwamuna adalimbikira kunena kuti alibe uchimo chifukwa, “Tsopano palibiretu mlandu wotsutsa anthu amene amakhala mwa Khristu Yesu.” Koma m’kazi uja adanenetsa kuti iye ali ndi uchimo mu m’tima mwake.

Tsiku lina, m’kazi wake sanamve bwino mu m’tima mwake motero anaganiza zopita kukafunsa kwa mbusa wake zimene ankatanthauza ponena kuti machimo athu onse anaperekedwa kwa Yesu.

Tsiku lina mwambo wa mapemphero utatha, anauza mwamuna wake kuti apite ku nyumba ndipo m’kaziyo adakhalira ku tchalichi ndipo adayamba kufunsa Rev. Park. Iye adati, “Ndikudziœa kuti inu abusa muli ndi mau, ndipo ndikudziœa kuti mau amene muli nawo ndi ofunika kwambiri. Chonde ndiuzeni.” Pamenepo mbusa uja adauza mai uja za kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu Woyera.

Pambuyo pake mai uja anazindikira chifukwa

Page 203: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

203 Ubatizo wa Yesu ndi Chifanizo cha Chipulumutso cha Ochimwa

◄ Zam'kati ►

chimene Paulo adalembera pa Aroma 8:1, “Motero tsopano palibiletu mlandu wotsutsa anthu amene amakhala mwa Yesu.” Iye adakhulupilira pa nthaœi yomweyo ndipo adapumulutsidwa. Ndipo anamvetsa bwino kuti machimo athu onse anaperekedwa kwa Yesu Khristu kudzera mu ubatizo wake kuti onse okhala mwa Khristu asataike.

Iye adayamba kumvetsa mau olembedwa. Potsiliza pake iye adazindikira kuti khomo la ku chiombolo ndi ubatizo wa Yesu ndi kuti kudzera mu ubatizo wakewo tikhoza kukhala olungama.

Mwamuna wakeyo sadapite kunyumba koma adali kumuyembekezera panja., Mwamuna uja adafunsa m’kazi wakeyo kuti, “Kodi waomboledwa tsopano?”

Tsopano mwamuna uja adasokonezekanso poganizira zimene mbusa wake anali kunena. Iye anali sanamveko za uthenga wa ubatizo wa Yesu. Iye anali kuona ngati alibe uchimo mu m’tima popanda ubatizo wa Yesu. Ndipo kunyumba

aœiriwo adakayamba kutsutsananso. Panthaœi imeneyi, kutsutsana kuja

kudatembenuka. M’kazi adafunsa mwamuna ngati anali ndi uchimo mu m’tima mwake kapena ai. Iye anafunsa ngati nkutheka munthu kukhala opanda uchimo ngati sakhulupilira ubatizo wa Yesu. Iye adauza mwamuna wakeyo kuti adzione bwino mu m’tima mwake. Atadziona bwino mwamunayo adapeza kuti ali ndi uchimo mu m’tima mwake.

Motero mwamunayo adapita kwa mbusa Park kukavomereza kuti iye ali ndi uchimo mu m’tima mwake. Iye adafunsa mbusayo kuti, “Kodi mbuzi yokaphedwa ija ankaipha asanasanjike manja pa mutu pake?” Iye adali asanamveko za uthenga wa madzi ndi Mzimu woyera. Motero iye adasokonezeka kwambiri.

Imeneyi ndiyo inali mfundo ya kafukufuku wa uzimu. Yesu adaayenera kubatizidwa kuti anyamule machimo onse adziko lapansi. Mwa njira imeneyi Yesu anayenera kufa popeza mphotho ya uchimo ndi imfa.

Page 204: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

204 Ubatizo wa Yesu ndi Chifanizo cha Chipulumutso cha Ochimwa

◄ Zam'kati ►

“Kodi anali kusanjika manja pa mutu pa nsembeyo isanaphedwe kapena itaphedwa kale?” Iye adafunsa zimenezi chifukwa chakuti adali atasokonezeka pa nkhani ya kusanjika manja ndi ubatizo wa Yesu. Ndipo mbusa Park anamulongosolera za chiombolo cha ubatizo wa Yesu.

Patsiku limenelo, mwamuna uja adamva kwa nthaœi yoyamba za uthenga wa madzi ndi Mzimu Woyera ndipo adapulumuka.

Kumeneku ndiko kufufuza kwa zimene zimachitika ngati sikamba za ubatizo wa Yesu. Tikhoza kunena kuti tilibe uchimo koma kunena zoona popanda ubatizo wa Yesu uchimo umakhalamo m’mitima mwathu. Kaœiri kaœiri anthu amanena kuti Yesu anachotsa machimo aathu onse pamene anafa pa mtanda, koma anthu amene amakhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake akhoza kunena kuti alibe uchimo pa maso pa Mulungu.

Mbusa Park adatsimikizira banja limeneli kuti

singapulumuke ku machimo athu popanda chiombolo cha ubatizo wa Yesu. CHIFANIZO CHA CHIPULUMUTSO: UBATIZO WA YESU KHRISTU

Kodi chifanizo cha chipulumutso ndi chiyani?

Ubatizo wa Yesu

“Madziwo akufanizira ubatizo umene masiku ano umakupulumutsani.” Yesu anabwera pansi pano kudzachotsa machimo onse adziko lapansi, kuti mitima yathu iyere ngati matalala. Tatsukidwa machimo athu chifukwa Yesu anasenza machimo athu kudzera mu ubatizo wake. Iye adatipulumutsa ndi ubatizo wake ndiponso mwazi wake. Choncho

Page 205: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

205 Ubatizo wa Yesu ndi Chifanizo cha Chipulumutso cha Ochimwa

◄ Zam'kati ►

zolengedwa zonse ziyenera ku m’gwadira. Tidzapulumuka pakukhulupilira Yesu Khristu.

Timatchedwa ana a Mulungu ndi kupita kumwamba pa kukulupilira Yesu. Ndife ansembe ake. Tikhoza kunena kuti Mulungu ndi Atate athu. Timakhala pa dziko lino lapansi koma ndife mafumu.

Kodi inu mumakhulupiliradi kuti Mulungu anatipulumutsa ife amene timakhulupilira chiombolo cha madzi ndi Mzimu Woyera? Chiombolo chathu sichingakhale chokwanira popanda ubatizo wa Yesu. Chikhulupiliro choona chimene Mulungu ndi Yesu amavomereza ndi chimene chakhazikika pa chipulumutso cha Yesu kudzera mu ubatizo wake, Mtanda wake ndi Mzimu Woyera. Chimenechi ndicho chikhulupiliro choona.

Machimo athu anatsukidwa pamene Yesu anasenza machimowo ndi ubatizo wake ndipo mphotho ya machimo athu inaperekedwa pamene

Iye anakhetsa mwazi pa Mtanda. Khristu Yesu adatipulumutsa ndi ubatizo wake wa madzi ndi Mzimu woyera. Inde! Timakhulupilira uthenga umenewu!

Page 206: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

◄ Zam'kati ►

ULALIKI WA CHISANU NDI CHITATU

Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe

yochotsera machimo

Page 207: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

207 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe

yochotsera machimo

< Yohane 13:1-17 > “Chikondwerero cha Paska chili pafupi,

Yesu adaadziœiratu kuti nthaœi yake yafika yakuti achoke panso pano kupita kwa Atate. Iye ankaœakonda amene anali ake panso pano, ndipo adaaœakonda kotheratu. Tsono Yesu ndi ophunzira ake ankadya chakudya chamadzulo. Satana nkuti ataika kale mu m’tima mwa Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote, maganizo akuti apekere Yesu kwa adani ake. Yesu ankadziœa kuti Atate adapereka zinthu zonse m’manja mwake. Ankadziœanso kuti adachokera kwa Mulungu, ndipo kuti akubwerera kwa Mulungu. Choncho pamene analikudya, Yesu adaimilira, adavula mwinjiro

wake, natenga nsalu yopukutira nkuimanga m’chiwuno. Atatero adathira madzi m’beseni, nayamba kutsuka mapazi a ophunzira ake, nkumaœapukuta ndi nsalu yopukutira ija imene adaaimanga m’chiwuno. Pamene adafika pa Simoni Petro, iyeyo adati, ‘Ambuye, Inuyo nkundisambitsa ine mapazi?’ Yesu adamuyankha kuti, ‘Zimene ndikuchitazi, sukudziœa tsopano, koma udzadzidziœa mtsogolo muno. Ngati sindikusambitsa, ndiye kuti chako palibe.’ Simoni Petro adati, ‘Ambuye, ngati ndi choncho, mutsuke osati mapazi anga okha, komanso manja anga ndi mutu womwe.’ Yesu adamuuza kuti, ‘Munthu amene wasamba, wayera yense. Palibe chifukwa choti asambenso, koma kungosamba mapazi okha basi. Tsono inu mwayera, koma osati nonsenu ai.’ Yesu ankamudziœa munthu wodzampereka kwa adani ake, nchifukwa chake adaati, ‘Sinonsenu muli oyera.’ Yesu atatsuka mapazi a ophunzira ake, adavalanso

Page 208: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

208 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

mwinjiro wake nakakhalanso podyera paja. Kenaka adaœafunsa kuti, ‘Kodi mwazimvetsa zimene ndakuchitiranizi? Paja inu mumaditchula kuti, Aphunzitsi ndiponso, Ambuye. Apo mumalondola, pakuti ndine amene. Tsono ngati ine Mbuye wanu ndi Mphunzitsi wanu ndakusambitsani mapazi anu, ndiye kuti inunso muyenera kumasambitsana mapazi. Ndakupatsani chitsanzo, kuti inunso muzichita monga momwe Ine ndakuchitirani inu. Kunena zoona, wantchito saposa mbuye wake, nthumwinso siiposa woituma. Ngati mudziœa zimenezi, ndinu odala mukamazichita.’”

Kodi chifukwa nchiyani Yesu anasambitsa

mapazi a Petro pa tsiku la chikondwerero cha Pasika? Pamene analikusambitsa mapazi ake, Yesu anati, “Tsono siungamvetse, koma ngati zachitika uzamvetsa.” Simoni Petro anali wophunzira wa pa

m’tima. Anakhulupilira kuti Yesu anali Mwana wa

Mulungu ndipo anachitira umboni kuti Yesu ndi Mpulumutsi. Ndipo pamene Yesu anali kusambitsa mapazi ake, panali kuyenera kukhala chifukwa chenicheni chochitira zimenezo. Pamene Petro anamvomereza chikhulupiliro chake kuti Yesu ndi Mpulumutsi, anali kutanthauza kuti akhulupilira kuti Yesu ndi Mpulumutsi amene angampulumutse ku machimo ake onse.

Kodi chifukwa nchiyani Yesu anasambitsa mapazi

a ophunzira ake asanapachikidwe pa mtanda?

Chifukwa anali kufuna kuti ophunzira

ake amvetse za chipulumutso chenicheni

Page 209: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

209 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Kodi chifukwa nchiyani anasambitsa mapazi Petro? Yesu anadziœa kuti Petro adzamkana katatu, kuti adzachita machimo ambiri mtsogolo.

Ngati, pamene Yesu anakwera kumwamba, Petro analinso ndi uchimo mu m’tima wake, sakanakhala pamodzi ndi Yesu. Koma Yesu anali kudziœa kufooka konse kwa ophunzira ake, ndipo sanali kufuna kuti machimo awo akhale pakati pa Iye ndi ophunzira ake. Choncho Iye analikufuna kuœaphunzitsa kuti machimo awo anakhululukidwa.

Ichi nchifukwa chake Iye anasambitsa mapazi a ophunzira ake. Yesu, asanamwalire ndi kuwasiya iwo, anafuna kuti adzindikire ndi kumvetsa za Uthenga Wabwino waubatizo ndi kuti machimo awo amoyo wonse anakhululukidwa.

Yohane 13 akunena za chipulumutso chikwanira kuti Yesu anaœauza za nzeru za anthu onse kuti machimo awo anachotsedwa.

“Musanamizidwe ndi Satana mtsogolomu. Ndinachotsa machimo anu onse ndi ubatizo wanga

mu mtsinje wa Yolodani ndipo ndinatenga chiweruzo pa mtanda chifukwa cha iwo. Ndipo ndidzauka kwa akufa kuti ndikwaniritse chipulumutso chakubadwanso kachiœiri chifukwa cha inu. Kukuphunzitsani kuti ndinachotsa kale machimo anu amasiku onse kukuphunzitsani za Uthenga Woyamba wochotsa machimo, ndi nakusambitsani mapazi anu ndisanapachikidwe pa mtanda. Ichi ndi chinsinsi cha Uthenga Wabwino wakubadwanso kachiœiri. Nonse muyenera kukhulupilira izi.”

Tonse tiyenera kumvetsa chifukwa chimene Yesu anasambitsira mapazi a ophunzira ake ndikuziœa chifukwa chimene ananenera kuti, “Chimene ndi kuchita tsono si mungamvetse tsono, koma m’nzimvetsa ngati zachitika.” Apo ndi pamene mukhoza kukhulupilira Uthenga Wabwino wakubadwanso kachiœiri ndipo tibadwenso kachiœiri ife tomwe.

Page 210: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

210 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

M’BUKU LA YOHANE 13:12 AKUTI

Kodi machimo ndi chiyani?

Ndi mahimo amene timachimwa masiku onse chifukwa

ndife ofooka Asanamwalire pa mtanda, Yesu anachita

chikondwerero cha Pasika ndi ophunzira ake ndipo anaœaonetsa Uthenga wachikhulupiliro cha machimo awo kudzera mukuœasambitsa mapazi awo ndi manja ake.

“Ankadziœanso kuti adachokera kwa Mulungu, ndipo kuti akubwerera kwa Mulungu, choncho pamene analikudya, Yesu adaimirira, adavula mwinjiro wake, natenga nsalu yopukutira nkuimanga m’chiwuno. Atatero adathira madzi m’beseni, nayamba kusuka mapazi a ophunzira ake, nkumaœapukuta ndi nsalu yopukutira ija

imene adaaimanga m’chiwuno. Pamene adafika pa Simoni Petro, iyeyo adati, “Ambuye Inuyo nkundisambitsa ine mapazi?” Yesu adamuyankha kuti, ‘Zimene ndikuchitazi, sukuzidziœa tsopano, koma udzazidziœa mtsogolo muno.’”(Yohane 13:3-7)

Anaphunzitsa ophunzira ake Uthenga Wabwino wa ubatizo ndi nsembe yochotsera machimo kudzera mu madzi ake a ubatizo.

Panthaœi ija, atakhala wokhulupilika kwa Yesu, Petro sanali kumvetsa chifukwa chimene Yesu anali kusambitsira mapazi ake. Pamene Yesu anena ndi iye, munjira imene iye ankakhulupilira Yesu anasintha maganizo ake. Yesu anali kufuna kumuphunzitsa za njira yachipulumutso yochotsera machimo, ya Uthenga Wabwino wa madzi aubatizo wake.

Anali ndi nkhaœa kuti mwina Petro sangathe kubwera kwa Iye chifukwa cha machimo am’tsogolo, makamaka machimo ake a thupi m’tsogolomu. Yesu anatsuka mapazi awo kuti

Page 211: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

211 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Satana asatenge, asalande chikhulupiliro cha ophunzira ake. Pambuyo pake Petro anamvetsa zimenezi.

Yesu anakonza njira kuti aliyense amene akhulupilira mu ubatizo wa madzi ndi mwazi adzaomboledwa ku machimo awo kwamuyaya.

M’buku la Yohane 13 Mau amene ananena pamene analikutsuka mapazi a ophunzira ake anatsindikizidwa. Ndi Mau ofunika kwambiri ndipo ndi okha amene anabadwanso kachiœiri amene angaœamvetse bwino.

Chifukwa chimene Yesu anatsukira mapazi a ophunzira ake atadya chikondwerero cha Pasika anali kufuna kuœathandiza ophunzira ake kuti adzindikire kuti machimo awo amoyo wonse akhululukidwa. Yesu anati, “Chifukwa chimene ndi kutsukira mapazi anu si mungamvetse tsopano, koma mudzamvetsa m’tsogolomu.” Mau aœa kwa Petro anali ndi tanthauzo lenileni la kubadwanso kachiœiri.

Ife tonse tiyenera kudziœa ndi kukhulupilira mu

ubatizo wa Yesu, umene unachotsa machimo athu onse. Ubatizo wa Yesu mu mtsinje wa Yolodani unali Uthenga Wabwino wochotsera machimo kudzera mukusanjika manja. Ife tonse tiyenera kukhulupilira mu Mau a Yesu. Anachotsa machimo onse adziko lapansi kudzera mu ubatizo ndi kutichotsera machimo pa kuweruzidwa ndi kupachikidwa pa mtanda. Yesu anabatizidwa kuti atichotsere machimo athu onse.

Page 212: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

212 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

KUKHULULUKIDWA KWA MACHIMO ONSE KUNAKWANITSIDWA KUDZERA MU UBATIZO NDI MWAZI WA YESU

Kodi msampha wa Satana kwa olungama ndi chiyani?

Satana amayesetsa kunamiza

anthu olungama kuti awasandutsenso ochimwa

Yesu anali kudziœa bwino kuti pamene iye

atapachikidwa pa mtanda, kuti adzauka ndi kupita kumwamba, ndipo kuti Satana ndi ena osadziœa choona adzabwera ndi kuyeretsa kunamiza ophunzira ake. Tikhoza kuona izi pa umboni wa Petro. Komabe Yesu anafuna kuphunzitsa Petro za

chikhululukiro cha machimo. Uthenga umenewu ndi wa ubatizo wa Yesu, umene adachotsera nawo machimo onse adziko lapansi. Yesu anafuna kuphunzitsa Petro ndi ophunzira ena aja ndiponso ife, amene tinali kubwera patsogolo pake. “Zimene ndili kuchitazi, suli kuzidziœa tsopano, koma udzadzidziœa m’tsogolo muno.” (Yohane 13:7).

Ophunzira a Yesu akachimwa Satana anali kuœayetsa ndi kuœadzudzula, ponena kuti, “Ngati mukuchimwa, nanga mungakhale bwanji opanda uchimo! Ndiye kuti simunapulumutsidwe. Ndinu ochimwabe.” Pofuna kupeœa zimenezi, Yesu adaœauza kuti popeza amakhulupilira mu ubatizo wake machimo awo onse anachotsedwa kale mwa iwo.

“Inu nonse mukudziœa kuti ine ndinabatizidwa! Cholinga cha ubatizo wanga nchakuti machimo amene munachita pa moyo wanu wonse afafanizidwe kuonjezerapo machimo amene inu munabadwa nawo. Kodi mwadziœa tsopano chifukwa chimene ine ndinabatizidwira ndi kufa

Page 213: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

213 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

pa mtanda?” Yesu anachotsa machimo a ophunzira ake kudzera mu ubatizo wake, ndiponso analandira chilango ndi kufa pa mtanda.

Tsopano, inu ndi ine taomboledwa ku machimo, machimo athu onse pakukhulupilira uthenga ndi chikhululukiro cha machimo athu. Yesu anabatizidwa ndi kufa chifukwa cha ife. Iye anatichotsera machimo ndi ubatizo wake ndi mwazi wake. Aliyense amene amadziœa za Uthenga wa nsembe yochotsera machimo, ndiponso aliyense amene akhulupilira m’choonadi cha Uthenga umenewu, adzaomboledwa ku machimo ake onse.

Kodi munthu ayenera kuchita chiyani akapulumutsidwa? Ayenera kuvomereza kuchimwa kwake tsiku ndi tsiku di kukhulupilira chipumulutso cha ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake, uthenga wa chiombolo cha machimo onse. Ayenera kuika uthenga umenewu m’kati mwa m’tima wake

Kodi chifukwa chakuti mudzachimwanso, ndiye

kuti mudzakhalabe anthu ochimwa? Iai. Nanga popeza Yesu anatichotsera kale machimo athu onse tingakhalenso ochimwa bwanji? Ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake pa Mtanda ndiwo uthenga wa nsembe yoperekera wachikhululukiro chamachimo adzabadwanso mwatsopano ‘monga munthu wolungama.’

ANTHU OLUNGAMA SANGAKHALENSO ANTHU OCHIMWA

Nchifukwa chiyani anthu olungama sangakhalenso

ochimwa?

Chifukwa Yesu adapereka kale mphoto ya machimo

amoyo wao onse.

Page 214: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

214 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Ngati mukhulupilira uthenga wonena za chikhululukiro cha machimo, uthenga wa madzi ndi Mzimu Woyera, ndi kumadziona ngati ndinu anthu ochimwabe chifukwa chakuti mumachimwa tsiku ndi tsiku, ndiye kuti muyenera kupita nokha ku Mtsinje wa Yolodani kumene Yesu anabatizidwa kuti achotse machimo anu onse. Ngati ndinu munthu wchimwabe ngakhale kuti mudalandira chiombolo, ndiye kuti Yesu anayeneranso kumabatizidwa tsiku ndi tsiku. Muyenera khukhulupilira kuti machimo anu onse anakhululukidwa kudzera mu uthenga wa ubatizo wa Yesu Khristu. Msaiœale kuti Yesu anakumasulani ku machimo anu onse mu ubatizo wake. Musakhale ndi chikhulupiliro chogwedezeka mwa Mpulumutsi wanu Yesu Khristu.

Kukhulupilira Yesu monga Mpulumutsi wanu, kutanthauza kuti inu mumakhululupilira mu ubatizo wake, umene unachotsanso machimo amene tidzachite kutsogolo, ngakhale machimo

amene ife timachita chifukwa cha kufooka kwathu. Ndipo chifukwa chakuti Yesu anadanena motsindika za kufunika wa ubatizo wake, Iye anatsuka mapazi a ophunzira ake ndi madzi kufanizira uthenga wa chikhululukiro cha machimo, ubatizo wake.

Yesu Khristu anabatizidwa, anapachikidwa pa mtanda, anauka kwakufa ndipo anakwera kumwamba kukwaniritsa lonjezo la Mulungu la kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo onse adziko lapansi ndi kupumulutsa anthu onse. Motero, ophunzira analalika Uthenga wanonena za nsembe yochotsera machimo, ubatizo wa Yesu, mtanda wake ndi kuuka kwake mpaka kumathero a moyo wawo.

Page 215: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

215 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

KUFOOKA KWA THUPI LA PETRO

Kodi nchifukwa chiyani Petro adakana Yesu?

Nchifukwa chakuti iye

anali ofooka Baibulo limatiuza kuti pamene Petro analandira

mafunso ndi kumudzudzula kuti iye anali m’modzi mwa ophunzira a Yesu, anakana kaœiri, ponena kuti, “Ntheradi, munthu amene mukunenayu sindikumudziœa.” Ndipo adatemberera ndi kulumbira kachitatu.

Tiyeni tiwerengenso mau opereka pa Mateo 26:69, “Petro adaakhala kunja m’bwalo la nyumba ija. Mtsikana wina wa ntchito adabwera namuuza kuti ‘Inunsotu munali ndi Yesu wa ku Nazareteyu.’ Koma iye adakana pamaso pa anthu onse, adaati sindidziœa zimenezo ine. Pamene

Petro ankatuluka ku mapita ku chipata, mtsikana winanso wantchito adamuona nayamba kuuza amene adaali pamenepo kuti ‘Akulu ameneœa anali ndi Yesu waku Nazaretetu.’ Petro adakananso molumbira kuti ‘Ndithudi sindikumudziœa munthu ameneyo.’ Ndipo patangopita kanthaœi, anthu amene adali pamenepo adadza nauza Petro kuti Ndithudi iwenso ndiwe wa gulu lomweli tadziwira kalankhulidwe kakoka. Apo Petro adayamba kulumbira nkumanena kuti ‘Mulungu andilange munthu mukunenayu ine sindimam’dziœa konse.’ Tsono Petro adakumbukira mau aja a Yesu kuti, ‘Tambala asanalire ukhala utanena katatu kuti sindidziœa,’ pomwepo adatuluka, nakalira misozi ndi chisoni chachikulu” (Mateo 26:69-75).

Zoonadi Petro anali kukhulupilira Yesu ndi kumamutsatira mokhulupilika. Iye anakhulupilira kuti Yesu ndi Mbuye ndi Mpulumutsi wake, ‘Mneneri.’ Koma pamene Yesu anatengedwa kupita kubwalo la Pilato, pamene chinakhala

Page 216: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

216 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

chintu choopsa kuyenda ndi Yesu iye anamukana ndi kum’temberera.

Petro sadadziœe kuti adzakana Yesu. Koma Yesu adaadziœa. Yesu anadziœa kuti Petro ndi ofooka. Choncho Yesu adatsuka mapazi a Petro ndikumuphunzitsa Uthenga wachipulumutso wolembedwa pa Yohane 13, “Mudzachimwanso m’tsogolo, koma ine ndachotsa machimo anu a’mtsogolo.”

Petro anakana Yesu chifukwa chakuti moyo wake unali pa chiopsezo, ndiponso china nchakuti thupi lake linali lofooka. Choncho pofuna kuchotsa mphulupulu zawo za m’tsogolo, Yesu adatsuka mapazi a ophunzira ake.

“Ndidzachotsanso machimo anu am’tsogolo. Ndiyenera kupachikidwa chifukwa ndinabatizidwa ndi kuchotsa machimo anu onse, ndipo ndidalipira mulandu umeneyu kuti ndi khale Mpulumutsi wanu woona. Ine ndine Mulungu wanu, ndiponso Mpulumutsi wanu. Ndidzalipira zonse chifukwa cha machimo anu, ndipo didzakhala Mbusa wa

chipulumutso chanu.” Pofuna kulimbitsa Uthenga umenewu m’mitima

mwawo, Yesu adatsuka mapazi awo chitatha chikondwerero cha Paska. Ichi ndicho choonadi cha uthengawu.

Chifukwa chakuti thupi lathu ndi lofooka ngakhale kuti tinabadwa mwatsopano, tidzakhala tikuchimwabe. Komabe sitiyenera kuchimwa, koma pamene tachimwa ndikuona zotsatira za uchimowo monga adaonera Petro, timachimwa ngakhale kuti sitidafune kutero. Chifukwa chakuti timakhala ndi thupi lathu la uchimo. Nthaœi zina timapita ku chionongeko. Thupi lathu lidzakhala likuchimwabe pamene tili kukhala m’moyo uno, koma Yesu anakhululukira machimo amenewo ndi ubatizo ndiponso mwazi wake pa Mtanda.

Sitikana kuti Yesu ndi Mpulumutsi wathu, koma pamene tikukhala m’moyo uno, timachita zinthu zosiyana ndi chifuniro cha Mulungu. Ichi nchifukwa chakuti ndife obadwa mwa munthu chabe.

Page 217: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

217 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Koma Yesu anadziœa kuti ndife anthu ochimwa m’thupi lathu. Yesu adakhala Mpulumutsi polipira m’landu wa machimo athu ndi ubatizo ndi mwazi wake. Iye watichotsera machimo athu onse ife amene timakhulupilira chipulumutso chake ndiponso kuuka kwake.

Ma buku onse anai a Uthenga Wabwino amayamba ndi nkhani ya ubatizo wa Yesu kudzera mwa Yohane Mbatizi. Cholinga chake chimene iye ankhalira ndi moyo wa umunthu chinali chakuti akwaniritse Uthenga wonena za kubadwa mwatsopano, Uthenga wa chipulumutso.

Kodi thupi lathu limachimwa nthali yaitali bwanji?

Timachimwa pa moyo wathu

wonse mpaka kufa

Pamene Petro adakana Yesu katatu tambala asanalire kodi iye anamva bwanji mum’tima mwake? Kodi iye sadachite manyazi? Iye adaalumbira pa maso pa Yesu kuti sadzam’kana konse. Iye anachimwa chifukwa cha kufooka kwa thupi lake, koma kodi iye adamva bwanji pamene agonjera zofuna za thupi lake pokana Yesu katatu? Kodi iye ankhamuona bwanji Yesu?

Kunena zoona, Yesu adadziœa zimenezi. Choncho iye adati, “Ndikudziœa kuti iwe udzachimwanso. Koma ine ndakuchotsera kale machimo amene iwe udzachite m’tsogolo ndi ubatizo wanga, kuti machimo akowo asakusandutsenso munthu wochimwa, kuti chisakhale chinthu chovuta kubwereranso kwa ine. Ine ndakhalanso Mpulumutsi wako weniweni pakubatizidwa ndiponso pakulandira chilango pa Mtanda. Ndakhala Mulungu wako, Mbusa wako. Khulupilira Uthenga wachikhululukiro cha machimo ako. Ine ndidzapitiriza kukukonda ngakhale uchimwenso. Ndidakuchotsera kale

Page 218: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

218 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

mphulupulu zako zam’tsogolo. Uthenga wa chikhululukiro cha machimo ako ndi wanthaœi zonse. Chikondi changa pa iwe nchakusambitsa ndiye kuti chako palibe.”

Chifukwa chimene Yesu anakambira mau amenewa pa Yohane 13 chinali chakuti kunali kofunika kuti anthu abadwenso mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera. Kodi ndime ya 9, “Simoni Petro adati Ambuye ngati ndi choncho, mutsuke osati mapazi anga okha komanso manja anga ndi mutu womwe. Yesu adamuuza kuti munthu amene wasamba wayera yense.”

Abwenzi anga okondedwa, kodi mudzagonjeranso kuzofuna za moyo wanu ndi kuchimwanso m’tsogolo kapena ai? Inde mudzachimwa. Koma Yesu anati Iye adachotsa ngakhale machimo athu a m’tsogolo, mphulupulu zonse za thupi lathu ndi adzazichotsa kale ndi ubatizo wake ndiponso mwazi wake ndipo Iye adauza ophunzira ake momveka bwino za choonadi cha Uthenga wansense imene iye

adzapereke chifukwa cha machimo athu, Iye adanena zimenezi kwa ophunzira ake asanapachikidwe pa Mtanda.

Chifukwa chakuti timakhala muthupi lathu lofookali, timafuna kuchimwa kaœiri kaœiri. Yesu anachotsa machimo adziko lonse lapansi ndi ubatizo wake. Iye sanatsuke mutu kapena thupi loka, koma anatsukanso mapazi athu, ndiponso machimo athu a m’tsogolo. Umenewu ndi Uthenga wa kubadwanso mwatsopano mwa ubatizo wa Yesu Khristu.

Yesu atabatizidwa, Yohane Mbatizi adachitira umboni, “Suuyu Mwana Wankhosa wa Mulungu uja wochotsa machimo aanthu apa dziko lonse lapansi.” (Yohane 1:29). Ife tiyenera kukhulupilira kuti machimo onse adziko lapansi anaperekedwa kwa Yesu pamene Iye anabatizidwa.

Pamene anthu akukhala pa dziko lino lapansi, khalidwe lawo ndi lauchimo. Ife tiyenera kuvomera kuti zimenezi ndi zoona. Nthaœi zonse pamene zilakolako zathupi zafika tiyenera

Page 219: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

219 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

kukumbukira Yesu anachotsa machimo athu onse ndiponso machimo adziko lonse lapansi kudzera mu Uthenga wonena za chikhululukiro cha machimo ndi kulipira mlandu wamachimowo kudzera m’mwazi wake. Tiyenera kumuthokoza ndi m’tima wathu wonse. Tiyeni tivomereze mwa chikhulupiliro kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wathu ndiponso Mulungu wathu. Lemekezani Mulungu.

Munthu aliyense pansi pano amachimwa m’thupi lake. Anthu ambiri amamwalira ali ndi mathupi auchimo. Anthu amachimwa m’mathupi mwawo.

MAGANIZO OIPA M’MITIMA MWA ANTHU

Kodi chimaipitsa munthu nchiyani?

Machimo osiyana siyana

ndi maganizo oipa Pa Mateyu 15:19-20, Yesu akuti, “Chifukwa

m’kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, zakuphana, za chigololo, za chiwerewere, za kuba, maumboni onama ndiponso za chipongwe. Zimenezi ndizo zimaipitsa munthu, koma kudya chakudya osasamba m’manja, sikungaipitse munthu.” Chifukwa chakuti machimo osiyana siyana m’kati mwa m’tima wa munthu amamuipitsa, munthuyo ndi wodetsedwa.

Page 220: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

220 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

MUNTHU AYENERA KUDZIŒA ZA KUIPA KWAKE

Nichiyani chiri m’mutima Wamunthu ali yense?

Ndimachimo amitundu

Khumi ndi awiri (Marko 7:21-23)

Ife tiyenera kutha kunena kuti, “Mitundu khumi

ndi iœiri ya machimoyo ili m’kati mwa m’tima wa munthu. Ndiponso ine ndili nayo mitundu imeneyi mu m’tima mwanga. Ine ndili ndi mitundu khumi ndi iœiri mum’tima mwanga imenenso yalembedwa m’Baibulo.” Tisanabadwe mwatsopano, tiyenera kuvomera kuti ife tili nawo machimo m’mitima mwathu. Tiyenera kuvomereza kuti ndife anthu ochimwa kotheratu

pa maso pa Mulungu. Ambiri mwa ife timapereka zifukwa zosiyana siyana za machimo athu ponena kuti, “Ine ndinali osachimwa maganizo oipawa asanaloœe mwa ine, kotero kuti ndangosokonezedwa basi.”

Kodi nanga Yesu ananena kuti chiyani za m’mene muntu alili? Iye adanena momveka bwino kuti, zimene zimatuluka mwa munthu ndizo maganizo oipa mum’tima mwake. Kodi inu mukuganiza chiyani? Kodi ndinu wabwino kapena ai? Kodi mukudziœa kuti munthu aliyense ali ndi maganizo aoipa? Inde, maganizo a munthu ngoipa.

Zaka zingapo zapitazo, itolo la Sampoong ku Seoul lidagwa mwadzidzidzi. Ma banja amene anataya okondedwa awo anali pa chisoni chachikhulu. Koma anthu ambiri adapita kumaloko kusangalala ndi chionetsero choopsacho.

Ena anayamba kuganiza, ‘Ndi anthu angati amene afa? 200 kodi? Ai, chiœerengero chimenechi chachepa. Kapena 300, mwina?

Page 221: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

221 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Komabe chikanakhala chintu chochititsa chidwi ngati chiœerengero cha anthu akufa chikadafika pa 2000…’

M’tima wa munthu aliyense ukhoza kukhala ndi maganizo ngati amenewa. Tiyenera kuvomera. Kumeneku kunali kusalemekeza mathupi aanthu akufawo! Ndipo ngozi imeneyi inali yopweteka ku mabanja aanthu ofedwawo! Ndipo ambiri anatayanso chuma chawo.

Koma ena mwa anthu amene anaona ngoziyo sanali ndi chisoni. Chikandakhala chintu chochititsa chidwi chiœerengero cha anthu akufawo cikadakwera. Aœa ndi maganizo oipa. Kodi ngozi imeneyi ikadachitikira pa bwalo la za maseœero ampira akadafa anthu angati? Anthu zikwi akadakwiririka, sichoncho? Inde, zinakanakhala zochititsa chidwi kuposa ngozi yimeneyi. Mwina ena anali ndi maganizo otere.

Ndiponso ife tikudziœa kuti nthaœi zina timakhala ndi maganizo onyansa. Aa, iwo sakananena mokweza. Ndipo mwina akhoza ku

magwedeza malilime awo kukhala ngati ali kumva chifundo. Anthu otere amafuna kuti ngozi zotere zizichitika kuti anthu ambiri mbiri aziphedwa malinga iwo sakukhudzidwa. Umu ndi m’mene moyo wa munthu umagwirira ntchito. Ndiponso ambiri aife tili monga anthu amenewa tisanabadwe mwatsopano.

MAGANIZO AKUPHA MU M’TIMA MWA MUNTHU ALIYENSE

Nchifukwa chiyani timachimwa?

Nchifukwa chakuti ife tili ndi

maganizo oipa m’mitima mwathu

Page 222: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

222 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Mulungu adatiuza kuti muli maganizo akupha m’kati mwa mitima yathu. Koma ambiri amatsutsa zimenezi. “Munganene bwanji zimenezi! Ine ndilibe maganizo akupha mu m’tima mwanga Inu mungaganize bwanji zimenezi!” Iwo amaganiza kuti anthu amene amapha anzawo, si anthu onga iwowo.

“Chigawenga chimene tidamva pa nkhani tsiku lina, ndiponso gulu la anthu achiwembu limene lidazunza ndi kupha anthu pansi pa nyumba yosanjikizana, ndi anthu amene ali ndi maganizo akupha m’mitima mwawo! Iwo ndi anthu ambadwo wina. Ine sindingakhale monga iwo! Iwo ndi zigawenga! Ndiponso a chifwamba!” Iwo amakhala ngati anthu aukali ndiponso okwiya, “Anthu amene anabadwa ndi makhalidwe otere ayenera kuchoka pansi pano! Anthu otere ayenera kulandira chilango chokapedwa.”

Koma mwatsoka, maganizo akupha ali m’kati mwa mitima ya anthu amene amaoneka aukali ndiponso zigawenga. Mulungu akutiuza kuti

m’mitima ya anthu amenewa muli maganizo akupha okha. Ife tiyenera kuvomereza Mau a Mulungu amene amaona m’kati mwa mitima yathu. Ife tiyenera kuvomera, kunena kuti, “Ine ndili nawo maganizo akupha mu m’tima mwanga.”

Inde, Mulungu anatiuza kuti kuli maganizo oipa kuphatikizapo akupha mumitima ya anthu. Tiyeni tivomere Mau a Mulungu monga momwe mibadwo ya anthu yikukhala yoipitsitsa, zonse zida zimene anthu amazitetedzera ndi zida zophera anthu. Ichi ndi chifukwa cha kupha kumene kuli mumitima yathu.

Chifukwa anthu anabadwa ndi maganizo oipa mumitima yao ife tonse tili chimodzimodzi. Ena amapha, osati chifukwa anabadwa akupha, koma chifukwa ife tonse tikulakalaka kukhala akupha. Mulungu amatiuza kuti tili ndi maganizo oipa ndi kupha mumitima yathu. Izi ndi zoona. Palibe wa ife amene anga kane choona ichi.

Choncho njira yoyenera yoti titsatire ndi

Page 223: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

223 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

kumvomera Mau a Mulungu ndi kuœasunga. Timachimwa mu dziko lino chifukwa tili ndi maganizo oipa mumitima yathu.

CHIWEREWERE CHILI MU MITIMA YATHU

Mulungu akunena kuti tili ndi chiwerewere mu

m’tima wa munthu aliyense. Kodi mukuvomereza? Kodi mukuvomera kuti muli ndi chiwerewere mu mitima yathu? Inde, muli chiwerewere mu m’tima wa munthu aliyense.

Ndi chifukwa chake chigololo ndi maganizo ena oipa amakula pakati pathu. Ndi njira imodzi yoyangira ndarama mu mubadwo uli wonse. Mabizinesi ena angathe kugwa, koma bizinesi iyi yoipa siimagwa ai chifukwa mu m’tima wa munthu aliyense muli chiwerewere.

MPHOTO YA WOCHIMWA NDI TCHIMO

Kodi munthu angalinganitsidwe chiyani?

Ndi mtengo umene umabwereka zipatso za uchimo

Monga momwe m’tengo wazinanazi umabereka

zinanazi, m’tengo wapapaya umabereka mapapaya, m’tengo wakanjeza umaberaka zipatso zakanjeza, ife amene tinabadwa ndi mitundu ya machimo okwana khumi ndi aœiri m’mitima yathu timabereka zipatso za uchimo.

Yesu adati chimene chimachokera mum’tima wa munthu ndicho chimamudetsa munthu. Kodi mukuvomereza izi? Tiyenera kugwirizana ndi Mau a Yesu ndikunenena kuti, “Inde ndife ochimwa ochita zoipa. Inde, ndizoona, Ambuye.” Inde,

Page 224: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

224 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

tiyenera kuvomera kuti tili ndi uchimo. Tiyenera kuvomera zoona ife tokha pa maso pa Mulungu.

Monga momwe Yesu Khristu anasungira chifuniro cha Mulungu, tiyenera kuvomera Mau a Mulungu ndi kumutsatira Iye. Ndi njira yokhayo imene ingatipulumutse ku machimo athu kupsolera mu madzi ndi mwa Mzimu Woyera. Izi ndi mphatso zochokera kwa Mulungu.

Dziko lathu ndi lodalitsidwa ndi mvula yabwino. Ngati mvula yabwino yipitiriza, mitengo yosiyana siyana ibala zipatso. Choncho, machimo khumi ndi aœiri mu mitima yathu, mawa mwina chidzakhala chiwerewere.

Ndipo tsiku lina, maganizo oipa ndiponso chigololo kapena kuba, mwina umboni onama ndi zina zotere. Ndipo timapitilira kuchimwa chaka chonse, mwezi uli wonse, tsiku lililonse, ndi ola lililonse. Palibe tsiku limene limadutsa popanda kuchimwa tchimo lina lililonse. Timalumbira kuti sitizachimwa koma palibe chabwino chimene timachita koma kuchimwa chifukwa ndi m’mene

tinabadwira. Kodi munayamba mwaona kuti mtengo

wazinanazi umakana kuberaka zinanazi chifukwa siufuna? Sindifuna kubereka zinanazi. Ngakhale kuti utafuna kuti usabereke zipatso, kodi zingatheke bwanji kuti usabereke zinanazi? Maluwa akhoza kuoneka panthaœi ya chilimwe, ndipo zipatso zimatcholedwa ndi kudyedwa.

Umu ndi m’mene chilengedwe chimakhalira, ndipo moyo waochimwa nawonso umatsatira chilengendwe. Ochimwa sangazithandize okha koma kupitiriza kubereka zipatso za uchimo.

Page 225: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

225 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

UBATIZO NDI MTANDA WA YESU ZINALI KUTICHOTSERA MACHIMO ATHU

Kodi mutanthauza chiyani ndi zansembe yochotsera machimo?

Ndi malipiro a mphoto ya uchimo

kudzera mu ubatizo wa Yesu (kusanjika manja) ndikukhetsa

mwazi wake pa mtanda Tiyeni tiœerenge mu Baibulo kuti tione m’mene

ochimwa, ochita zoipa, amakhalira olungama pa maso pa Mulungu ndi kukhala moyo wachisangalalo. Umu ndi Uthenga wansembe yochotsera machimo.

Levitiko 4:27-31 akuti, “Ngati munthu wamba

aliyense achimwa mosadziœa, pochita china chilichonse chimene Chauta amaletsa, napalamula pakutero, tchimo lakelo akalizindikira, apereke nsembe ya mbuzi yaikazi yopanda chilema, chifukwa cha tchimo lakelo. Tsono asanjike dzanja lake pamutu pa mbuzi ya nsembe yopepesera machimoyo, ndipo aipereke pa malo amene amaperekera nsembe yopsereza. Atatero, wansembe atengeko magazi ndi chala chake, ndi kuœapaka pa nyanga za guwa la nsembe zopsereza, ndipo magazi otsalawo aœathire patsinde pa guwa lomwelo. Tsono achotse mafuta ake onse, monga momwe amachotsera mafuta ansembe yachiyanjano, ndipo wansembe aœatenthe pa guwalo, kuti atulutse fungo lokomera Chauta. Wansembeyo atachita mwambo wopepesera machimo amunthu wamba uja, munthuyo adzakhululukidwa.”

Panthaœi ya chipangano chakhale, kodi anthu analikuchotsa bwanji machimo awo? Anali kusanjika manja awo pa mutu wansembe

Page 226: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

226 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

yochotsera machimo ndipo analikupereka machimo awo pansembeyo.

M’buku la Levitiko 1:2-4 akuti, “Uza Aisraele kuti, munthu aliyense akabwera ndi chopereka kwa Chauta, azitenga �ombe kapena nkhosa kapena mbuzi. Ngati munthu apereka nsembe yopsereza kwathunthu, aziipereka pakhomo la chihema cham’sonkhano, kuti Chauta ailandire. Tsono asanjike dzanja lake pamutu pa �ombeyo, ndipo idzalandilidwa kuti ikhale yopepesera machimo ake.”

Mulungu anawauza kuti akonze nsembe yochotsera machimo a Aisraele. Ndipo anaœauza kuti ‘asanjike manja awo’ pa mutu wansembeyo, kuti itenge machimo awo. M’kati mwachihema munali guwa loperekerapo nsembe yochotsera machimo. Linali bokosi kukula kwake ngati thebulo lolalikirapo ndipo linali ndi minyanga inayi mu makona. Anthu a Aisraele analikuchotsa machimo awo kudzera mukupereka machimo awo pa mutu wansembe yochotsera machimo ndipo

anali kuotcha nyamayo pa guwa lansembe. Mulungu akuti m’buku la Levitiko kwa anthu,

“Perekani ndi m’tima wanu wonse mukufuna kwanu pa khomo la chihema pamaso pa Ambuye.” Machimo awo analikuperekedwa pa nsembe yochotsera machimo pamene asanjika manja awo pa mutu wake, ndipo wochimwa anali kudula khosi la nsembeyo ndipo anali kuika magazi ake pa nyanga za guœa lootchera nsembe.

Atachita zimenezi, nyama yansembe yochotsera machimo inali kuyeretsedwa, ndipo nyama yake analikuidula pa�onopa�ono nkusanduka phulusa pa guœa loperekerapo nsembe. Ndipo fungo labwino la Aroma la nyama linali kupita kwa Mulungu kuti achotse machimo ao. Umu ndi m’mene anali kuchotsera machimo awo a tsiku ndi tsiku.

Apa panalinso nsembe yochotsera machimo awo a chaka chonse. Panali kusiyana kwa nsembe yochotsera machimo a masiku onse moti wansembe wam’kulu analikusanjika manja ake pa

Page 227: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

227 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

mutu wansembe yochotsa machimo mu malo mwa anthu a fuko la Israele ndipo analikuwaza magazi m’mawa kwa mpando wachifundo kasanu ndi kaœiri. Ndiponso , kusanjika manja pa mutu wa mbuzi yamoyo zinali kuchitika pamaso pa anthu a Asraele patsiku la khumi la mwezi wachisanu ndi chiœiri mu chaka chonse (Levitiko 16:5-27).

Tsono, tiyeni tione m’mene nsembe yochotsera machimo inasinthira mu Chipangano Chatsopano ndiponso m’mene chipulumutso cha Mulungu chinakhalira nokhazikika kwa zaka zonsezi.

Kodi ndani amene anali kuimira nsembe yamachimo mu

Chipangano Chakale?

Yesu Khristu

Kodi chifukwa nchiyani Yesu anamwalira pa mtanda? Kodi anachita chiyani choipa padziko lapansi kuti Mulungu alole kuti Mwana wake amwalire pa mtanda? Pamene ochimwa onse adziko lapansi, kutanthauza kuti tonse ife tinagwa mu uchimo, Yesu anabwera pa dzikali kuti atipulumutse.

Anabatizidwa ndi Yohane M’batizi mu mtsinje wa Yolodani ndi kutenga weruzo pa mtanda amachimo onse mumalo mwathu. Njira imene Yesu anabatizidwa, njira yimene anakhetsera magazi pa mtanda ndi chimodzimodzi ndi m’mene anali kuperekera nsembe yochotsera machimo mu Chipangano Chakale, kusanjika manja pa mutu wansembe yochotsera machimo ndi kukhetsa mwazi wake.

Inali njira monga njira imene analikuchita mu Chipangano Chakale. Wochimwa anali kusanjika manja pa mutu wansembe yochotsera machimo ndi kuvomereza machimo ake, kuti, “Ambuye, ndine wochimwa. Ndinapha ndi kuchita

Page 228: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

228 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

chiwerewere.” Apo machimo ake anali kuperekedwa pa mutu wasembe yochotsera machimo.

Pamene wochimwa akadula khosi lansembe yochotsera machimo ndikuipereka pamaso pa Mulungu, Yesu nayenso anaperekedwa munjira yomweyi kuti achotse machimo athu onse. Yesu anabatizidwa ndi kukhetsa mwazi pa mtanda kuti apulumutse inu ndi ine ndi kuti achotse machimo athu onse kudzera mu nsembe yake.

Nzoona, Yesu anafa chifukwa cha ife. Pamene tiganizira zimenezi, kodi tanthauzo lopereka nsembe zanyama zopanda chilema monga nsembe za machimo a anthu onse? Kodi nyama zonsezo zinali kudziœa kuti tchimo ndi chiyani? Nyama sizingadziœe tchimo. Sizingachotse machimo onse aanthu.

Monga ngati nyama zopanda chilema, Yesu anali wopanda tchimo. Iye ndi Mulungu Woyera, Mwana wa Mulungu, ndipo Iye sanachimwepo. Choncho anachotsa machimo athu onse kudzera

mu ubatizo mu mtsinje wa Yolodani pamene anali ndi zaka makhumi atatu.

Kunali kutenga machimo athu onse, ndipo anafa pa mtanda kuti achotse machimo athu. Iyi yinali ntchito yake kuti atipulumutse pa kuchotsa machimo aanthu onse. Izi zinalembedwa m’buku la Mateo 3.

CHIYAMBI CHA UTHENGA WABWINO WANSEMBE YOCHOTSERA MACHIMO

Kodi chifukwa nchiyani Yesu anabatizidwa ndi

Yohane Mbatizi mutsinje wa Yolodane?

Kuti akwaniritse chilungamo

Page 229: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

229 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

M’buku la (Mateo 3:13-15) akuti pa masiku amenewo, Yesu adachoka ku Galilea kubwera kwa Yohane ku mtsinje wa Yolodani, kuti Yohane amubatize. Yohane poyetsa kukana, adati, “Ndine amene ndiyenera kubatizidwa ndi Inuyo. Nanga mukubwera kwa ine kodi?” Koma Yesu adamuyankha kuti, “Tsopano lino vomera, chifukwa ndi m’mene tiyenera kuchitira zonse zimene Mulungu akufuna.” Apo Yohane adavomera.

Tiyenera kudziœa chifukwa chimene Yesu anabatizidwa pamene anali ndi zaka makumi atatu. Anabatizidwa kuti achotse machimo aanthu onse ndikukwaniritsa chilungamo cha Mulungu. Kupulumutsa anthu onse ku machimo awo, Yesu Khristu, amene analibe chilema, anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi.

Choncho anachotsa machimo adziko lonse lapansi ndi kuzipereka Iye yekha ngati nsembe yochotsera machimo aanthu onse. Kuti pakutero machimo awo akhululukidwe, ife tonse tiyenera

kudziœa choona ndi kukhulupilira choona. Zili ndi ife kukhulupilira mu chipumulutso chake kuti tipulumutsidwe.

Kodi ubatizo wa Yesu ukutanthauza chiyani? Ndi chimodzimodzi ndi kusanjika manja M’chipangano chakale. Mu Chipangano Chakale, machimo aanthu anali kuperekedwa pa mutu wansembe yochotsera machimo kudzera mukusanjika manja, ndipo M’chipangano Chatsopano, Yesu anachotsa machimo aanthu onse pa dziko lapansi podzipereka Iye yekha ngati nsembe yochotsera machimo ndi kubatizidwa ndi Yohane M’batizi.

Yohane M’batizi anali munthu wamphamvu pakati pa anthu, oimirira anthu onse wozodzedwa ndi Mulungu, monga oimirira anthu onse, m’kulu wansembe onse, anasanjika manja ake pa mutu wa Yesu ndikupereka machimo adziko lonse lapansi pa Iye. ‘Ubatizo’ utanthauza, kupereka kuikidwa mumanda ndi kutsukidwa.

Tsono, kodi mukudziœa chifukwa chimene

Page 230: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

230 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Yesu anabwerera padziko lapansi ndi kubatizidwa ndi Yohane M’batizi? Kodi mukhulupilira Yesu, ndi kudzindikira tanthauzo la ubatizo wake? Ubatizo wa Yesu unali wochotsa machimo athu onse, machimo amene tirinawo, khalidwe lakuchita zoipa, zimene timachita pa moyo wathu wonse. Yesu anabatizidwa ndi Yohane M’batizi kuti akwanitse Uthenga Wabwino wansembe yakale yochotsera machimo athu onse.

M’buku la Mateo 3:13-17 analemba kuti, ‘pa nthaœiyo’ ndipo chitanthauza nthaœi imene Yesu anabatizidwa, nthaœi imene machimo aanthu onse anaperekedwa pa Iye.

‘Panthaœiyo,’ Yesu anachotsa machimo aanthu, pomwalira pa mtanda ndipo patapita masiku atatu anauuka kwakufa. Kuti achotse machimo aanthu onse adziko lapansi, anabatizidwa kamodzi kokha ndi kumwalira pa mtanda kamodzi kokha kufera anthu onse. Onse amene akufuna kuomboledwa ku machimo awo onse pa maso pa Mulungu, anapulumutsa onse kamodzi kokha.

Kodi chifukwa nchiyani Yesu anayenera kubatizidwa? Chifukwa nchiyani Iye ankhavala chisoti chaminga ndikuweruzidwa ndi Pilato monga ngati mbala? Kodi chifukwa nchiyani anapachikidwa pa mtanda ndi kukhetsa mwazi ndikufa? Chifukwa anachotsa machimo onse adziko lapansi, machimo ainu ndi ine, anaperekedwa pa Iye kudzera mu ubatizo wake. Ndipo chifukwa cha machimo athu anayenera kufa pa mtanda.

Tiyenera kukhulupilira mu Mau a Chipulumutso kuti Mulungu anatipulumutsa ife ndipo timuthokoze Iye. Popanda ubatizo wa Yesu, ndi imfa yake ya pa mtanda, ndiponso ndikuuka kwakwe kwa akufa, sitikanapulumutsidwa.

Tiyenera kukhulupilira mu Mau a Chipulumutso kuti Yesu anatipulumutsa ife ndi kumuthokoza Iye. Popanda ubatizo wa Yesu, imfa yake pa mtanda, ndikuuka kwake kwa akufa, pakadakhala kuti palibe chipulumutso pa ife.

Pamene Yesu anabatizidwa ndi Yohane

Page 231: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

231 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

M’batizi kuti achotse machimo onse adziko lapansi, anachotsa machimo athu onse kotero kuti ife amene tikhulupilira Uthenga wake wachipulumutso ndife opulumutsidwa. Pali anthu ena amene amaganiza kuti, ‘koma anachotsa machimo obadwa nao okha, kodi nzoona?’ Iwo ndi wolakwa.

Zinalembedwa bwino bwino M’baibulo kuti Yesu anachotsa machimo onse adziko lapansi kamodzi kokha pamene anabatizidwa. Machimo athu onse, kuphatikizapo machimo obadwa nao, anachotsedwa. M’buku la Mateo 3:15 akuti, “Koma Yesu adamuyankha kuti, Tsopano lino vomera, chifukwa ndi m’mene tiyenera kuchitira zonse zimene Mulungu akufuna.” Apo Yohane anavomera kukwaniritsa chilungamo kutanthauza kuti machimo onse, popanda kuchotsa ena anachotsedwa kwa ife.

Kodi nzoona Yesu anachotsa machimo athu amoyo wathu wonse. Inde, anachotsadi. Tiyeni tione umboni wake M’buku la Levitiko poyamba.

Likunena za wansembe wam’kulu ndi nsembe yochotsera machimo patsiku lochotsera machimo.

NSEMBE YOCHOTSERA MACHIMO YA CHAKA CHONSE YA ANTHU AM’TUNDU WA AISRAELE

Kodi anthu a Israele Ankanayeretsedwa ndi nsembe

Yamachimo ya dziko lino?

Ai “Aroni apereke �ombe ya mphongo kuti ikhale

nsembe yopepesera machimo a iye mwini wake, kuti achite mwambo wopepesera machimo ake ndi banja lake. Tsono atenge mbuzi ziœiri zija, ndipo aziike pamaso pa Chauta pakhomo pachihema cha m’sonkhano. Pompo Aroni achite maere pambuzi

Page 232: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

232 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

ziœirizo, kuti imodzi ikhale ya Chauta, ndipo ina ikhale ya Azazele. Aroniyo abwere ndi mbuzi imene maere aonetsa kuti ndi ya Chauta, ndipo aipereke kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. Koma mbuzi imene maere aonetsa kuti ndi ya Azazele, abwere nayo yamoyo pamaso pa Chauta, kuti achite mwambo wopepesera machimo pa mbuziyo, ndi kuitumiza ku chipululu kwa Azazele.” (Levitiko 16:6-10.) Apo Aroni anatenga mbuzi ziœiri pakhomo la chihema la m’sonkhano kuti achotsere machimo a Aisraele achaka chonse.

“Ndipo Aroni analikuchita maere pambuzi ziœirizo: Kuti imodzi ikhale ya Chauta, ndipo ina ikhale ya Azazele.” Mbuzi ya Azazele inali yochotsera machimo.

Iyi inali nsembe yochotsera machimo amasiku awo onse, wochimwa amasanjika manja ake pa mutu wansembeyo kuti apereke machimo ake. Koma machimo achaka chonse a anthu, m’kulu wansembe, mumalo mwa anthu onse, anali kupereka machimo a chaka chonse pa nsembe

yochotsa machimo pa tisku la khumi la mwezi pa mwezi wa chisanu ndi kaœiri chaka chonse.

Levitiko 16:29-31 akuti, “Limeneli likhale lamulo lanu lamuyaya kuti mwezi wachisanu ndi wachiœiri, pa tsiku lakhumi la mwezi, muzisala zakudya ndipo musagwire ntchito iliyonse, inu mbadwa, ndiponso alendo wokhala nao pakati panu. Pajatu pa tsiku limenelo padzakhala mwambo wopepesera machimo anu, kuti machimo anu achotsedwe. Choncho mudzakhala oyera pamaso pa Chauta. Limeneli lidzakhala tsiku lanu lalikulu la Sabata lopumula, ndipo mudzasale zakudya. Limeneli likhale lamulo lanu lamuyaya.”

M’Chipangano Chakale, anthu afuko la Aisraele anali kupereka nsembe yochotsera machimo amasiku onse ndipo analikupereka machimo amasiku onse ndipo analikupereka machimo awo pa mutu wansembeyo, ndi kuvomereza machimo awo, kwa Ambuye, “ndachimwa machimo akuti ndi akuti: Chonde mundikhululukire.”

Page 233: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

233 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Pamenepo anali kudula khosi la nsembeyo, ndikupereka magazi ake kwa m’kulu wansembe, ndi kupita ku mudzi, ndi kukhulupilira kuti machimo ake akhululukidwa. Machimo ansembe yachopereka inalikufa mumalo mwa ochimwa, ndi uchimo pa mutu wake. Nsembe ya machimo inali kuphedwa mumalo mwa olakwa. M’chipangano Chakale nsembe yamachimo inali monga mbuzi, mwana wa�ombe, �ombe ya mphongo ndi nyama zonse zoyeretsedwa zimene Mulungu anasankha.

Mumalo moti wochimwa afe chifukwa cha machimo ake, Mulungu, mwa chikondi chake analola kuti nyama iphedwe mumalo mwake.

Munjira imeneyi M’chipangano Chakale, ochimwa anali kuchotsa machimo awo kudzera ku nsembe yochotsera machimo. Machimo a wochimwa anali kuperekedwa pa nsembe yochotsera machimo kudzera mu kusanjika manja, ndipo magazi ake anali kuperekedwa kwa wansembe kuti achotse machimo awochimwa.

Koma kunali kovuta kuti apereke nsembe

yochotsa machimo masiku onse. Choncho Mulungu analola kuti m’kulu wansembe apereke nsembe yochotsa machimo a chaka chonse, pa mwezi uli wonse wa chisanu ndikaœiri patsiku la khumi. Mumalo mwa anthu onse a Aisraele.

Kodi ntchito ya m’kulu wansembe patsiku la kupereka nsembe chinali chiyani? Poyamba, Aroni m’kulu wansembe anali kusanjika manja ake pa mutu wansembe, ndikuvomereza machimo aanthu onse a Aisraele, “Ambuye, anthu a Aisraele achimwa machimo akuti ndi akuti, kupha, chigololo, chiwerewere, kuba, umboni wonama, ndikunyoza Mulungu.”

Ndipo anali kudula khosi la nsembe yochotsera machimo, ndikutenga magazi amene anaœawaza kasanu ndi kaœiri pa mpando wachifundo m’kati mu chihema cham’sonkhano. (M’baibulo 7 ndi nambala imene ndi yokwanira).

Yinali ntchito yake kupereka machimo achaka chonse pa mutu wansembe yochotsera machimo mumalo mwa anthu onse, ndipo nsembe

Page 234: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

234 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

yochotsera machimo mumalo mwa anthu onse, ndipo nsembe yochotsera machimo inali kuperekedwa mumalo mwao.

Chifukwa Chauta ndi wolungama kupulumutsa anthu onse kumachimo awo, analola kuti nsembe yochotsera machimo imfe mu malo mwa anthu. Chifukwa Mulungu ndizoona alindi chikondi, Analola kuti anthu apereke moyo wansembe mumalo mwao. Apo m’kulu wansembe anali kuwaza magazi chakum’awa kwa malo a mampando wachifundo kuti achotse machimo anthu achaka chatha pa tsiku loperekera nsembe, patsiku la khumi la mwezi wa chisanu ndi kaœiri.

Kodi nsembe ya Mwana Wankhosa M’chipangano Chakale

nindani?

Yesu amene ndiopanda chilema

M’kulu wansembe analikupereka mbuzi ziœiri patsiku lopereka nsembe kwa anthu a Aisraele. Imodzi mwa iyo inali kutchedwa mbuzi ya Azazele, ndikokuti, ‘kuika kunja.’ Momwenso Azazele, M’chipangano Chatsopano ndi Yesu Khristu. Yohane 3:16 akuti, “Mulungutu adaœakonda kwambiri anthu adziko lapansi. Anali naye Mwana m’modzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupilira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha” (Yohane 3:16).

Mulungu anapereka Mwana wake yekhayo monga Mwana Wakhosa wansembe. Ndipo ngati nsembe ya Mwana Wakhosa ya anthu onse, Iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi ndipo anakhala Mpulumutsi, Mpulumutsi wadziko lonse lapansi. Mesiya ndikokuti Mpulumutsi; ndipo Yesu Khristu ndiko kuti, Mfumu imene inabwera kupulumutsa anthu ake!

Choncho, monga momwe machimo aanthu onse amachotsedwa patsiku lochotsera machimo M’chipangano Chakale, Yesu Khristu, anabwera

Page 235: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

235 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

pa dziko lapansi zaka 200 zaku mbuyozo, kuti abatizidwe ndi kukhetsa mwazi wake pa mtanda kuti akwaniritse Uthenga Wabwino wochotsa machimo aanthu onse.

Pano, tiyeni tiœerenge m’buku la (Levitiko 16:21-22) Tsono Aroni asanjike manja ake pa mutu wambuziyo, ndipo aululire pa mbuzi imeneyo zochimwa zonse za Aisraele pamodzi ndi kusamvera kwao konse, ndiye kuti machimo ao onse. Machimowo awaike pa mutu pa mbuzi ija, ndipo munthu amene adamusankhiratu aithamangitsire kuchipululu mbuziyo.

Mbuziyo itsenze machimo ao onse ndi kumankha nawo kuchipululu. Munthuyo aileke mbuzi imeneyo kuti ipite kuchipululu.

Kunalembedwa kuti machimo aanthu onse anaperekedwa pa mutu wambuzi monga momwe ananenera m’buku la Levitiko pa mutu woyamba. ‘Machimo awo onse’ kutanthauza kuti machimo awo onse amene

Anachimwa m’mitima yao, machimo onse

amene anachimwa ndi mathupi awo. Ndipo ‘machimo awo onse’ anaperekedwa pa mutu wambuzi yonyamula machimo awo imene amaisanjika manja pa mutu.

KUDZERA MUMALAMULO AMULUNGU TIYENERA KUDZINDIKIRA MACHIMO ATHU ONSE NDI ZOTSATIRA ZAKE

Kodi chifukwa nchiyani Mulungu anatipatsa

malamulo?

Kuti tidziwe uchimo Malamulo a Mulungu ndi okwananira ndime

613. Koma, pamene tiganiza za izi tichita zimene

Page 236: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

236 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Iye sanatiuze kuti tichite. Kodi ndizimene anatiuza kuti tichite?

Choncho, ndife ochimwa, M’baibulo analemba kuti Mulungu anatipatsa ife malamulo kuti tidzindikire machimo (Aroma 3:20). Zitanthauza kuti anatipatsa malamulo ake kuti tiphunzire kuti ndife ochimwa. Sanatipatse kuti tisunge malamulowa koma kuti tidziœe machimo athu.

Sanatipatse malamulo ake kuti tiœasunga. Simungayembekezere kuti galu angakhale ngati munthu. Momwemonso, sitingathe kusunga malamulo a Mulungu koma kuti tidzindikire machimo athu kudzera mu malamulo ake.

Mulungu anapereka kwa ife chifukwa ndife anthu ochimwa, koma patokha sitingathe kudziœa. “Ndinu akupha, achigololo, ndipo ochita zoipa.” Iye anatiuza kuti tisaphe, koma timapha m’mitima yathu nthaœi zina kupha kwenikweni.

Koma chifukwa munalembedwa mumalamulo kuti musaphe, tikudziœa kuti ndife akupha, ndipo tinena, “Aa, ndine wochimwa.”

Choncho, kuti apulumutse anthu onse a Aisraele ku machimo, Mulungu analola Aroni kuti apereke nsembe yochotsera machimo patsiku lochotsera machimo M’chipangano Chakale, ndipo anali Aroni amene ankhapereka nsembe ya anthu a Aisraele chaka chonse.

M’chipangano Chakale, nsembe ziœiri zinali kuperekedwa kwa Mulungu pa tsiku lopereka nsembe yochotsera machimo. Ina inali kuperekedwa kwa Mulungu, ina inali kuperekedwa ku chipululu ataisanjika manja, kuti inyamule machimo achaka chonse aanthu. Mbuzi asanaipititse kuchipululu ndi manja a munthu woyenera, m’kulu wansembe analikusanjika manja ake pa mutu wambuzi ndikuvomereza machimo onse aAisraele. “Ambuye, anthu anapha, anachita chigololo, akuba, akupembeza mafano….Tinachimwa.”

Dziko la Palestine ndi lachipululu cha mchenga. Mbuzi ya Azazele inali kuperekedwa kumalo opanda malire kuchipululu ndi kufa komweko. Pamene amaipititsa, anthu a Aisraele anali kuona,

Page 237: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

237 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

ndikukhulupilira kuti machimo awo akhululukidwa. Anthu analikupeza mtendere m’mitima yao, ndipo mbuzi ya Azazele inali kufera m’chipilili chifukwa chamachimo aanthu onse.

Mulungu anachotsa machimo athu kudzera mu Mwana Wankhosa wa Mulungu, Yesu Khristu. Machimo athu onse anachotsedwa kotheratu kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi kukhetsa mwazi wake pa mtanda.

Yesu ndi Mulungu ndipo ndi Mupulumutsi wathu. Iye ndi Mwana wa Mulungu amene anabwera kupulumutsa anthu onse ku machimo awo ndipo ndi amene anatilenga m’chifanizo chake. Iye anabwera pansi pano kuti atipulumutse kumachimo.

Osati kumachimo amene ndi machimwa masiku onse ndi mathupi athu, komanso ndi machimo athu am’tsogolo, machimo athu onse am’mitima ndi muthupi anaperekedwa pa Yesu. Anali kuyenera kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi kuti

akwanitse chilungamo cha Mulungu, nsembe yokwanira yochotsera machimo adziko lapansi.

Zaka zitatu Yesu asanapachikidwe pa mtanda, pamene anayamba ntchito yake, anachotsa machimo onse a dziko lapansi kudzera mukubatizidwa ndi Yohane Mbatizi mu mutsinje wa Yolodani. Chipulumutso chake cha anthu onse kudzera mu nsembe yochotsera machimo chinayambika pamene Iye anabatizidwa.

Mu mtsinje wa Yolodani, pamalo madzi analikufika m’chiuno, Yohane Mbatizi anaika manja ake pa mutu wa Yesu ndikumumiza mumadzi. Ubatizo uwu unali ngati kusanjika manja M’chipangano Chakale ndipo ntchito yake inali imodzi yopereka machimo onse.

Kumiza mumadzi kutanthauza kufa, ndipo kuchoka mumadzi kutanthauza kuuka ku akufa. Choncho kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi, Yesu anakwanitsa ndi kuonetsa zinthu zitatu: Kuchotsa machimo onse, kupachikidwa, ndi kuuka kwa akufa.

Page 238: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

238 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Tingapulumutsidwe ngati timvera Mau okhao amene Yesu anatipulumutsa nawo kumachimo. Mulungu anaganiza kutipulumutsa kudzera mwa Yesu, ndi pangano limene Iye anapangana M’chipangano Chakale ngati lakwaniritsidwa. Ndipo Yesu anapita pa mtanda ndi machimo athu onse pa mutu wake.

Kodi ndi ntchito bwanji inasala kwa ife poti Yesu anachotsa

machimo athu onse?

Tiyenera kumvera Mau a Mulungu

Yohane 1:29 akuti, “M’maœa mwake Yohane adaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo adati, “Suuyu Mwana Wankhosa wa Mulungu uja, wochotsa machimo aanthu apa dziko lapansi.”” Yohane Mbatizi anachitira umboni. “Suuyu

Mwana Wankhosa wa Mulungu uja, wochotsa machimo aanthu apa dziko lapansi.” Machimo onse aanthu anaperekedwa pa Yesu pamene Iye anabatizidwa mu mtsinje wa Yolodani. Khulupilirani! Ndipo mudadalitsidwa ndi nsembe yochotsera machimo anu onse.

Ife anthu tiyenera kukhala ndichikhulupiliro ndi Mau a Mulungu. Tiyenera kuika kumbali maganizo osamvetsa ndi kungokhulupilira chabe kuti Yesu anachotsa machimo adziko lapansi, ndipo titsatire Mau olembedwa a Mulungu.

Kunena kuti Yesu anachotsa machimo onse adziko lapansi, ndikunena kuti Iye anakwaniritsa chilungamo cha Mulungu kudzera mu kuchotsa machimo athu ndi chinthu chimodzimodzi. Ndipo kusanjika manja, ndi kubatizidwa, ndi chinthu chimodzi.

Ngakhale tisanene zonse, kapena ayi koma tanthauzo ndi limodzi. Tanthauzo la Mau, kusanjika manja M’chipangano Chakale ndi chimodzimodzi ndi M’chipangano Chatsopano,

Page 239: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

239 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

kusiyana ndikoti Mau oti ubatizo ndi amene amagwiritsa ntchito.

Ndizoona kuti Yesu anabatizidwa ndi kuweruzidwa pa mtanda kuti atichotsere machimo athu onse. Ndipo kuti tipulumutsidwe ngati tikhulupilira mu Uthenga Wabwino wa machimo athu obadwanao.

Pamene tinena kuti Yesu anachotsa machimo adziko lonse lapansi (Yohane1:29), kodi timatanthauza chiyani pamene tikunena kuti machimo adziko lapansi? Timatanthauza machimo obadwanao, maganizo onse oipa, kuba, chigololo, kunyenga, kufooka, kunyoza, kuzikuuza, ndi makhalidwe oipa m’mitima yathu. Chitanthauza machimo athu ndi zolakwa zathu mu thupi ndi mum’tima. (Aroma 6:23) akuti, Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa, koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu. (Aheberi 9:22) akuti malinga ndi malamulo a Mosewo pafupifupi zonse zimayeretsedwa ndi magazi, ndipo machimo

sakhululukidwa popanda kukhetsa magazi. Monga momwe akunenera mu ndime izi, machimo onse ayenera kulipidwa. Ndipo Yesu Khristu, kuti apulumutse anthu onse kumachimo, anapereka moyo wake ndikulipira mphoto ya machimo athu pa nthaœi imodzi.

Choncho chimene tiyenera kuchita ndi kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi magazi ake, Uthenga Wabwino oyamba, ndi mwa Yesu monga ngati Mulungu wathu ndi Mpulumutsi wakumachimo onse.

Page 240: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

240 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

NSEMBE YOCHOTSERA MACHIMO ATHU AMAŒA

Kodi tiyenera kupereka nsembe ya machimo

athu kachiwiri?

Ai sitiyenera

Machimo am’maœa ndi amasiku na apatsogolo, ‘ndi machimo amene tizachimwa tisanamwalire amaphatikizidwa ndi machimo adziko lapansi’ monga machimo atsiku lalero, adzulo, ndiponso amatsiku akumbuyo kwa dzulo amaphatikidwa ‘mumachimo adziko lapansi’, ndipo machimo adziko lapansi anaperekedwa pa Yesu pa nthaœi ya ubatizo wake. Choncho machimo amene tichita kufikira patsiku loti timwalire anachotsedwa kale pa ife.

Tiyenera kukhulupilira mu Uthenga Wabwino woyamba, Mau olembedwa a Mulungu, ndi kuœasunga kuti tipulumutsidwe. Tiyenera kuika pambali maganizo athu kuti tipulumutsidwe ku machimo onse. Mwina mukhoza kufunsa, “Kodi angachotse bwanji machimo amene sanachitike?” Inenso ndikhoza kukufunsani inu, “Kodi Yesu angabwere pansi pano nthaœi yonse imene tichimwa ndi kukhetsa mwazi kaœirikaœiri?”

Mu Uthenga Wabwino wakubadwanso kachiœiri, pali lamulo la nsembe yochotsera machimo athu. (Aheberi 9:22) akuti, “Ndipo machimo sakhululukidwa popanda kukhetsa magazi.” Pamene munthu akufuna kuti aomboledwe kumachimo ake, ayenera kupereka machimo ake potsanjika manja ake pa mutu wansembe yochotsera machimo, ndipo nsembe yochotsera machimo iyenera kufa m’malo ake.

Monga momwe, Mwana wa Mulungu anadzera pa dzikoli ndi kupulumutsa anthu onse. Anabatizidwa kuti achotse machimo athu onse

Page 241: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

241 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

ndipo anakhetsa mwazi pa mtanda kuti alipilire mphoto ya machimo athu, ndikunena kuti “kwatha.” Anauka kwa aufa patapita masiku atatu ndipo tsono akukhala kudzanja lamanja la Mulungu. Ndipo ndi Mpulumutsi wathu kwamuyaya.

Kuti tikhululukidwe machimo athu onse, tiyenera kutaya maganizo athu ndi kusiya chipembezo choti tiyenera kuomboledwa ku machimo athu masiku onse. Kuti machimo aanthu akhululukidwe, nsembe iyenera kuperekedwa, kamodzi kokha. Mulungu kumwamba anapereka machimo onse adziko lapansi pa Mwana wake kudzera mu ubatizo ndi kumwalira pa mtanda mumalo mwathu. Ndipo pamene anauka kwa akufa, chipulumutso chathu chinakwaniritsidwa.

Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu, chilango chimene chidam’gwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa. Akunena kuti zolakwa zonse ndi machimo adziko lapansi,

aanthu onse anaperekedwa pa Yesu Khristu. Ndipo M’chipangano Chatsopano, M’buku la

Aefeso 1:4 akuti kunalembedwa kuti, “Mulungu asanalenge dziko lapansi, adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera m’tima ndi opanda cholakwa pamaso pake.” Ichi chitanthauza kuti anatisankha mwa Iye yekha dziko lisanalengedwe. Dziko lisanalengedwe, Mulungu anasakha kulenga ife anthu ake, olungama opanda chilema mwa Yesu. Chimene tingaganize poyamba, tsono tiyenera kukhulupilira ndi kutsatira Mau a Mulungu, Mau a ubatizo, ndi mwazi, ndipo ndi Mzimu woyera.

Mulungu akutiuza ife kuti Mwana Wakhosa Yesu Khristu, anachotsa machimo adziko lonse lapansi ndi aanthu onse. (Aheberi 10:1) akuti, “Malamulo a Mose ndi chithunzi chabe cha madalitso amene alikudza, osati madalizo enieniwo. Ngakhale nsembe zimodzimodzi zimaperekedwa kosalekeza chaka ndi chaka, malamulowo sangathe konse mwansembezo

Page 242: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

242 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

kuœasandutsa angwiro anthu oyandikira pamenepo.”

Apa akunena kuti kupereka nsembe yimodzi modzi chaka ndi chaka sikungatipange ife kukhala woyera. Malamulo ndi chithunzithunzi cha zinthu zabwino zimene zikubwera osati fanizo chabe la zinthu. Yesu Khristu Mpulumutsi amene anabwera, anapanga ife kukhala oyera kamodzi kokha (monga momwe nsembe ya Aisraele yinali kuperekedwa kamodzi ndi kuchotsa machimo achaka chonse) kudzera mu ubatizo ndikupachikidwa pa mtanda kuti achotse machimo athu onse.

Choncho m’buku pambuyo la Aheberi 10:9-18 Yesu akunena kuti, “Koma pambuyo pake adati, “Ndabweratu, kuti ndichite zimene mukufuna.” Motero Khristu adathetsa mphamvu za nsembe zakhale zija, kuti m’malo mwake akhazikitse nsembe ya mtundu wachiœiriyo. Chifukwa cha kuti Yesu Khristu atachita zimene Mulungu adaafuna kuti achite, ife tidayeretsedwa ndi nsembe ya thupi

lake, limene Iye adapereka kamodzi kokhako. Wansembe aliyense amaimirira tsiku ndi tsiku nkumatumikira, ndipo amapereka nsembe yimodzimodzi mobwereza bwereza. Komabe nsembe zimenezi sizingathe konse kuchotsa machimo. Koma Khristu adapereka nsembe imodzi yokha yochotsera machimo onse. Ndipo ataipereka, adakakhala ku dzanja lamanja la Mulungu. Kumeneko akudikira tsono kuti Mulungu asandutse adani ake kukhala ngati chopondapo mapazi ake. Mwansembe yimodzi yomweyo wasandutsa angwiro kwamuyaya onse amene Iye akuœayeretsa. Mzimu Woyera nayenso amatitsimikizira zimenezi. Poyamba Iye akuti, “Nachi chipangano chimene ndizachita nawo atapita masiku amenenwo, akutero Ambuye: Ndidzaika malamulo anga m’mitima mwao, ndidzachita kuœalemba m’maganizo ao.” Pambuyo pake akutinso, “Sindidzaœakumbukiranso konse machimo ao ndi zolakwa zao.” Pamene Mulungu wakhululukira zonsezi, sipafunikanso

Page 243: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

243 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

nsembe yoperekera machimo.” Timakhulupilira kuti Yesu anatipulumutsa

pochotsa machimo athu onse adziko lapansi kudzera mu ubatizo wake ndi mwazi amene anakhetsa pa mtanda.

CHIPULUMUTSO CHA KUBADWANSO KACHIŒIRI NDI MADZI NDIPONSO NDI MZIMU WOYERA UMENE UMAKHALA MU MITIMA YATHU NDI MU MITU YATHU

Kodi ndife olungama chifukwa sitichimwanso

lero?

Ai, ndife olungama chifukwa Yesu anachotsa machimo athu onse pokhulupilira

mwa lye

Kodi nonsenu mukhulupilira izi? —Amen— kodi mukumvera ndi chikhulupiliro Mau a Mulungu kuti Yesu Khristu anabatizidwa ndi kukhetsa mwazi pa mtanda kuti apulumutse ife?

Page 244: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

244 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Tiyenera kumvera kuti tibadwenso kachiœiri. Ngati tikhulupilira kuti Yesu Khristu, kudzera mu Uthenga Wabwino wochotsa machimo anachotsa machimo athu onse, ndi machimo adziko lonse lapansi, apo tingathe kupulumutsidwa.

Sitingakhale olungama posunga malamulo a Mulungu koma kudzera mu chikhulupiliro m’ntchito za Mulungu. Yesu Khristu anachotsa machimo athu onse kudzera mu ubatizo mu mtsinje wa Yolodani ndi kudzudzidwa ndi chilango mumalo mwa machimo athu pa mtanda. Pokhulupilira Uthenga uwu ndi mitima yathu yonse, tingaomboledwe kumachimo athu onse ndi kukhala olungama. Kodi mukhulupilira izi?

Ubatizo wa Yesu, kupachikidwa kwake pa mtanda, ndi kuuka kwa akufa kunali achipulumutso akuima pa chikondi cha Mulungu. Mulungu amatikonda ife monga m’mene tiliri ndipo Iye ndi olungama, ndipo anatithenga ife olungama poyamba. Anatilungamitsa ife popereka machimo athu pa Yesu pa nthaœi ya ubatizo wake.

Kuchotsa machimo athu onse, anatuma Mwana wake m’modzi yekha, Yesu, padziko lino lapansi mumalo mwathu. Analola kuti Yesu achotse machimo onse adziko lapansi kudzera mu ubatizo wa Yesu ndipo anapereka chiweruzo pa Iye mumalo mwathu chifukwa cha machimo athu onse. Anatipanga ife ana ake olungama kudzera muchipulumutso cha madzi ndi mwazi, chikondi chopanda malire cha Mulungu.

M’buku la Aheberi 10:16 akuti, “Nali pangano limene ndidzachita nawo atapita masiku amenewo, akutero Ambuye: Ndidzaika malamulo anga m’mitima mwawo, ndipo ndidzaœalemba m’nzeru yawo.”

M’mitima yathu ndi maganizo athu, kodi ndife ochimwa pamasio pa Mulungu kapena olungama. Yesu Khristu anachotsa machimo athu onse ndi chiweruzo chake. Yesu Khristu ndi Mpulumutsi wathu. Tikhoza kuganiza, “chifukwa timachimwa masiku onse, kodi tingakhale bwanji olungama? Nzoona ndife ochimwitsitsa.” Koma ngati

Page 245: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

245 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

tingasunge Mau a Mulungu monga momwe Yesu Khristu anamverera Atate, timakhala olungama.

Nzoona, monga momwe ndinanenera poyamba, tili ndi machimo m’mitima yathu tisanabadwenso kachiœiri. Pamene tatenga Uthenga Wabwino m’mitima yathu wachikhululukiro cha machimo, timapulumutsidwa kumachimo timakhala ochimwa. Koma timakhala wolungama pamene tiyamba kukhulupilira mu chipulumutso cha Yesu, ndiponso pamene tikhala ana olungama a Mulungu. Ichi ndichikhulupiliro chimene Mtumwi Paulo anali kunena. Chikhulupiliro cha Uthenga Wabwino wa chikhululukiro cha machimo chimatilungamitsa.

Mtumwi Paulo angakhale olungama kapena makolo achikhulupiliro sanakhale olungama chifukwa cha ntchito zao koma chifukwa cha chikhulupiliro ndi kusunga Mau a Mulungu, Mau amadalitso ake.

Aheberi 10:18 akuti, “Pamene Mulungu wakhululukira zonsezi, sipafunikanso nsembe

yoperekera machimo.” Monga momwe kunalembedwera, Mulungu anatipulumutsa kuti tisafe chifukwa cha machimo athu. Kodi mukhulupilira zimenezi? —Amen.—

M’buku la Afilipi 2:5-11 akuti, “Motero nonse mukhale ndi m’tima womwe uja umene adaalinawonso Khristu Yesu. Iyeyu anali ndi Mulungu chikhalire, komabe sadayetse kuti kulingana ndi Mulungu ndi chinthu choti achigwiritsitse. Koma adadzitsitsa kotheratu pakudzitengera umphaœi wa kapolo, ndi kukhala munthu monga anthu onse. Ali munthu choncho adadzichepetsa, adakhala momvera mpaka imfa, imfa yake yapa mtanda. Chifukwa cha chimenechi Mulungu adam’kweza kopambana, nampatsa dzina lopambana dzina lina lililonse. Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza, zonse zidzavomereze poyera kuti, Yesu Khristu ndi Ambuye, ndipo pakutero zilemekeze Mulungu

Page 246: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

246 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Atate.” Yesu Khristu sanazipangire yekha mbiri,

anakhala ngati wantchito, anabwera ngati munthu. Anadzitsitsa yekha ndipo nakhala omvera kufikira mpaka kufa kuti apulumutse ife.

Choncho tikuthokoza Yesu, “Iye ndi Mulungu wathu, Mpulumutsi ndiponso Mfumu.” Chifukwa chimene tikulemekezera Mulungu ndi kuthoza Yesu ndi choti Yesu anamvera chifuniro cha Atate ake mpaka pa mapeto. Ngati Iye sanamvere, sitikanalemekeza Mwana wa Mulungu lero. Koma chifukwa Mwana wa Mulungu anamvera chifuniro cha Atate ake mpaka kufa. Zolengedwa zonse ndi anthu onse pa dziko lapansi amamulemekeza Iye ndipo adachita choncho kalekale.

Yesu Khristu ndi Mwana Wankhosa wa Mulungu amene anachotsa machimo adziko lapansi, ndipo kunalembedwa kuti anachotsa machimowo kudzera mu ubatizo wake. Tsono, papita zaka zokwanira 2000 kuchokera pamene Iye anachotsera machimo adziko lapansi. Ndipo

chifukwa inu ndi ine tikukhala m’dziko limeneli kuyambira titabadwa, machimo athu onse akuphatikizidwa ndi machimo adziko lapansi.

Kodi ndife ochimwa ngakhale tidzachimwe

mawa?

Ai. Chifukwa Yesu anachotsa machimo athu onse akhale alero, ndiponso am’tsogolo

Popanda kusiyanitsa machimo obadwa nawo

ndi zolakwa zathu, za moyo wonse, kodi sitinachimwe kuchokera pamene tinabadwa?

Yesu anali kudziœa kuti tikhoza kuchimwa kuyambira pa nthaœi imene tinabadwa kufikira pa tsiku loti timwalire ndipo anachotsa machimo athu poyambirira. Kodi m’kuona izi tsono? Ngati tingathe kukhala kwa zaka 70, machimo athu ndi

Page 247: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

247 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

okwanira kudzadza magalimoto opitirira 100. Koma Yesu anachotsa machimo athu onse panthaœi yimodzi kudzera mu ubatizo wake. Anachotsa machimo athu onse pa mtanda.

Ngati Yesu anachotsa machimo obadwa nawo okha, ife tonse tikanafa ndikupita ku gehena. Ngakhale tikanaona kuti Iye sanachotse machimo athu onse, sichikanasintha mfundo yoti Yesu anachotsa machimo athu onse.

Kodi ndi machimo angati amene ife tachimwa mu dzikoli? Machimo onse amene tachimwa akuphatikizidwa pa machimo onse adziko lapansi.

Pamene Yesu anamuuza Yohane kuti am’batize Iye, ichi ndi chimene Iye analikutanthauza. Yesu anachitira umboni kuti Iye wachotsa machimo athu onse. Mulungu anatuma kapolo wake Yesu sanabwere kuti Yesu abatizidwe ndi Iye. Ndipo kudzera mukubatizidwa ndi Yohane amene naimirira anthu onse, ndi kuœerama mutu wake pamaso pake kuti abatizidwe, Yesu anachotsa machimo onse aanthu.

Tsono, machimo athu onse kuyambira pa 20 kufukira 30, kuchokera pa 30 kufikira 40, mpaka choncho, mpaka machimo aana athu anali kuphatikizidwa pa machimo adziko lonse amene Yesu anachotsa kudzera mu ubatizo wake.

Kodi ndani anganene kuti pali machimo pa dzikoli? Yesu Khristu anachotsa kale machimo adziko lino, ndipo ife tonse tingapulumutsidwe ngati tingakhulupilire m’mitima yathu, popanda kukhala wokaika, pa zimene Yesu anachita kuti achotse machimo athu onse: Ubatizo wake ndiponso ndi kukhetsa mwazi amakhala moyo woononga mumaganizo awo, kunena za moyo wao ngati kuti moyo wao ndi opambana zonse. Koma pali ena amene amakhala moyo ovutika. Anthu ambiri, kuphatikizapo ine, ambiri akukhala moyo woononga. Kodi mungakhale bwanji wosamvetsa kapena kulandira Uthenga Wabwino wachipulumutso, wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake?

Page 248: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

248 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

CHIPULUMUTSO CHA OCHIMWA CHA KWANIRITSIDWA

Kodi chifukwa nchiyani Yesu natsuka mapazi

a Petro?

Chifukwa anali kufuna kuti Petro akhale ndi chikhulupiliro

cholimba kuti lye anachotsa kale machimo onse ake onse

m’tsogolo

Yohane 19:17-20 akuti, “Iye atasenza mtanda wake, adatuluka naye mu mzinda kupita kumalo otchedwa “Malo achibade cha mutu” (pa Chiyuda amati “Gologota”) kumeneko adampachika pa mtanda. Adapachikanso anthu ena aœiri, wina ku dzanja lamanja, wina kudzanja lamanzere, Yesu pakati. Pilato adalemba chidziœitso nachiika pa

mtandapo. Adaalembapo kuti, “YESU WAKU NAZARETE MFUMU YA AYUDA.” Ayuda ambiri adachiœerenga chidziœitsocho, chifukwa pa malo pamene Yesu adaapachikidwapo panali pafupi ndi mzinda wa Yerusalemu. Chidziœitsocho chidalembedwa m’chilankhulo cha Ayuda, cha Aroma, ndiponso cha Agriki.”

Wokondedwa abwenzi, Yesu Khristu anachotsa machimo onse adziko lapansi ndipo anaweruzidwa kuti apachikidwe kubwalo la Pilato. Tsono tiyeni tiganizire za nkhani iyi pamodzi.

Yohane 19:28-30 akuti, “Yesu adaadziœa kuti tsopano zonse wakwaniritsa. Tsono kuti zipherezere zimene malembo adaanena, Iye adati, “ndili ndi ludzu.” Pomwepo panali mbiya yodzadza ndi vinyo wosasa. Asilikali aja adaviika chinkhupule m’vinyo wosasayo, nkuchitsomeka ku m’tengo ka hisope, nachifikitsa pa kamwa pake. Yesu atalandira vinyo wosasayo adati, “Zonse ndakwaniritsa” kenaka adaœeramitsa mutu, napereka mzimu.”

Page 249: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

249 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Ndipo patapita masiku atatu, Iye adauka kwa akufa ndipo anakwera kumwamba. Ubatizo wa Yesu ndi Yohane Mbatizi ni mfa yake pa mtanda zinali zokhuzana kwambira, chimodzi sichikanachitika popanda chinzake. Choncho tiyeni tithokoze Ambuye Yesu chifukwa chopulumutsa ife ndi Uthenga wake wochotsa machimo.

Thupi la munthu nthaœi zonse limatsatira zofuna zathupi, koma sitingathandize koma kupitiriza kuchimwa ndi thupi lathu – Yesu Khristu anatipatsa ife ubatizo wake ndi mwazi wake kuti atipulumutse kumachimo athupi. Anatipulumutsa ku machimo amathupi athu ndi Uthenga wake Wabwino.

Ndipo onse amene akwaniritsa chikhululukiro chamachimo ao angathe kulowa mu ufumu wakumwamba panthaœi iliyonse pokhulupilira Yesu, amene anabadwira mu Betelehemu, amene anabatizidwa mu mtsinje wa Yolodani, ndipo amene anafa mpa mtanda ndiponso anauka kwa

akufa patapita masiku atatu. Choncho tithokoze Ambuye ndi kutamanda dzina lake kwamuyaya.

M’mutu wotsiriza wa buku la Yohane, Yesu anapita ku Galilea atauka kwa akufa. Anapita kwa Petro ndikunena kuti, “Simoni, mwana wa Yona, kodi umandikonda kwambiri kusiyana ndi onseœa?” Ndipo Petro anamuyankha kuti, “Inde Ambuye; mukudziœa kuti ndimakukondani.” Apo Yesu anati, “Dyetsa ana ankhosa zanga.”

Petro anakumbukira zonse, Uthenga Wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake, wa chipulumutso cha machimo. Tsopano chifukwa akhulupilira mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi wa mwazi, wochotsa machimo ndipo akumbukira chifukwa chimene Yesu anatsukira mapazi ake, chikhulupiliro chake mwa Yesu chinachulukirapo.

Tiœerenge Yohane 21:15 akuti, “Iwo atafilusa, Yesu adafunsa Simoni Petro kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikonda koposa m’mene amandikondera aœa?” Iye adati, Inde Ambuye, mukudziœa kuti ndimakukondani. Yesu

Page 250: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

250 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

adamuuza kuti, samala anaankhosa anga.” Iye adauza Petro kuti asamale ana ankhosa zake chifukwa Petro anali wophunzira wake, chifukwa Petro anapulumutsidwa kwathunthu ndipo chifukwa Petro anali wolungama ndi wantchito wokhulupilira pamaso pa Mulungu.

Ngati Petro akadakhala wochimwa chifukwa cha machimo ake atsiku ndi tsiku, Yesu sakadamuuza kuti alalikire Uthenga Wabwino wochotsa machimo, chifukwa Iye, ndi ophunzira ena, sakanathandizira kulakwa ma tsiku onse m’thupi, koma Yesu anaœauza kulalika Uthenga Wabwino wochotsa machimo ao onse chifukwa anakhulupilira ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake umene unakhetsedwa pa mtanda, Uthenga Wabwino wochotsa machimo.

AMBUYE, MUKUDZIŒA KUTI NDIMAKUKONDANI

Kodi mzakhalanso ‘ochimwa’ pamene

mzachimwanso kachiwiri

Ai. Yesu anachotsa machimo anu onse am’tsogolo mu mtsinje

wa Yolodane

Tiyeni tiganizire za Mau a Yesu kwa Petro. “Simoni,mwana wa Yona, kodi umandikonda koposa ena onse?” “Inde, Ambuye, mukudziœa kuti ndimakukondani.” Kuvomeza chikondi chake chinali choona, kuchokera pa chikhulupiliro cha Uthenga wansembe yochotsa machimo.

Ngati Yesu sakanaphunzitsa Petro ndi

Page 251: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

251 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

ophunzira ena Uthenga wachipulumutso cha machimo kudzera mukutsuka mapazi awo, sakanatha kuvomereza chikondi chao m’njira imeneyi.

Koma, pamene Yesu anabwera kwa iwo ndi kufunsa kuti, “Kodi mumandikonda koposa ena aœa?” Petro akanati, “Ambuye, sindiliwokwanira ndipo ndine wochimwa. Ndine wochimwa amene sangathe kukukondani koposa ena aœa. Chonde ndi siyeni.” Ndipo Petro akanathawa ndi kubisala pamaso pa Yesu. Anadalitsidwa ndi Uthenga Wabwino wochotsa machimo, aubatizo wa Yesu ndi wa mwazi wake umene unapulumutsa anthu onse.

Koma ife tiyeni tiganizire za yankho la Petro. Iye anadalitsidwa ndi Uthenga Wabwino wochotsa machimo, wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake umene unapulumutsa athu onse.

Ndipo iye anati, “Inde, Ambuye, mukudziœa kuti ndimakukondani.” Kuvomereza kwa chikondi chake kunachokera pa chikhulupiliro cha Uthenga

Wabwino wa Yesu wochotsa machimo. Petro anali kukhulupilira Uthenga Wabwino woona wochotsa machimo onse adziko lapansi, ngakhale machimo awo am’tsogolo amene anthu adzachimwa chifukwa cha chikhulupiliro chochepa ndi kufooka kwa thupi.

Chifukwa Petro anali okhulupilira wa mphamvu wa Uthenga Wabwino wochotsa machimo, ndipo chifukwa anali kukhulupilira kuti Yesu ndi Mwana Wankhosa wa Mulungu, iye anali kuyenera kunena kuti Ambuye popanda kukaika. Chipulumutso cha Yesu chinachokera ku Uthenga Wabwino wochotsa machimo. Petro anapulumutsidwa ku machimo ake a tsiku ndi tsiku. Petro anakhulupilira mu chipulumutso kupyolera mu Uthenga Wabwino wochotsa machimo onse adziko lapansi.

Kodi inunso muli choncho? Kodi mungathe kukonda ndi kukhulupilira Yesu amene anachotsa machimo adziko lapansi chifukwa cha ife ndi Uthenga wake Wabwino wochotsa machimo, ndi

Page 252: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

252 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

ubatizo wake ndiponso mwazi wake? Kodi mungathe bwanji kusamukhulupilira ndi kumukonda Iye.

Ngati Yesu anachotsa machimo akale okha kapena alero, ndi kusiya machimo a m’tsogolo mumanja athu, sitikana m’lemekeza Iye monga m’mene tichitira lero. Choncho tiyenera kuvomera tonse kuti tinapulumutsidwa chifukwa cha kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wochuluka wansembe yochotsa machimo umene Yesu anatipatsa ife wa ubatizo ndi mwazi wake.

Ngati sitikhulupilira mu Uthenga Wabwino wochotsa machimo, wa ubatizo ndiponso ndi wa mwazi wa Yesu, palibe wokhulupilira amene angapulumuke ku machimo amoyo wake wonse. Ndipo ngati tinaomboledwa ku machimo amoyo wathu wonse kudzera mukuvomereza ndikulapa nthaœi yonse, tikhoza kukhala aulesi kuti tikhale olungama nthaœi zonse ndipo tikhoza kukhala ndi uchimo nthaœi zonse ndipo m’mitima yathu.

Ngati ndi choncho, ndiye kuti tibwerera ku

machimo ndipo sitingathe kukonda Yesu kapena kubwera pafupi ndi Iye. Apo sitingathe kukhulupilira mu chipulumutso cha Yesu ndipo sitingamutsatire Iye mpaka kumapeto amoyo wathu.

Koma Yesu anatipatsa Uthenga Wabwino wachikhululukiro cha machimo ndikupulumutsa onse okhulupilira. Anali Mpulumutsi wokwanira ndipo anachotsa zolakwa zonse zimene tinachimwa masiku onse amoyo wathu kuti timukonde Iye moona.

Tsono, ife okhulupilira sitingathandize koma kukonda Uthenga wa ubatizo ndi wa mwazi wa Yesu, wa chikhululukiro cha machimo anthu. Okhulupilira onse akhoza kukonda Yesu kwamuyaya ndipo angakhale akapolo achikondi cha chipulumutso kudzera mu Uthenga Wabwino wochotsa machimo umene Yesu anapereka kwa ife.

Abwenzi wokondedwa. Ngati Yesu anasiyako tchimo lina lochepa kumbuyo. Simungathe

Page 253: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

253 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

kukhulupilira mwa Yesu, kapena kuti simungathe kuchitira umboni Uthenga wakuchotsa machimo. Simungathe kugwira ntchito ngati a ntchito a Mulungu.

Koma ngati mukhulupilira Uthenga Wabwino wochotsa machimo, mukhoza kupulumutsidwa kumachimo onse adziko lapansi. Amalola kuti mupulumutsidwe kumachimo onse adziko lapansi pamene muzindikira Uthenga Wabwino wochotsa machimo amene unalembedwa mu Mau a Yesu.

KODI UMANDIKONDA KWAMBIRI KOPOSA AMENEŒA?

Kodi ndi chiyani chimene chimatipanga kuti tikonde Yesu koposa zinthu zina?

Chikondi chake pa ife kudzera

mu ubatizo wake wochotsa machimo athu onse ngakhale machimo

athu am’tsogolo Mulungu anapereka ana ake ankhosa kwa

kapolo wake, amene anakhulupilira mu Uthenga Wabwino wochotsa machimo. Yesu anafunsa katatu, “Simoni, mwana wa Yona, kodi umandikonda kwambiri koposa enaœa?” Nthaœi yonse Petro anayankha, “Inde, Ambuye, mukudziœa kuti ndimakukondani.” Tsopano, tiyeni tiganizire zamayankho a Petro. Tikhoza kuona kuti

Page 254: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

254 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

iye sanalikunena za chifuniro chake, koma chikhulupiliro cha Uthenga Wabwino wochotsa machimo adziko lapansi.

Pamene tikonda wina wake, ndipo ngati chikondi chimenechi chichoka pa chifuniro chathu chikhoza kubwerera pansi ngati tafooka. Koma ngati chikondi chimachokera mu mphamvu yachikondi chake, ndiye kuti chikhala kwamuyaya. Chikondi chake, ndiye kuti chikhala kwamuyaya. Chikondi cha Mulungu, tinena za, kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo athu onse, chipumulutso cha madzi ndi ubatizo wa Yesu ndiponso ndi Mzimu woyera ndi chimodzi modzi.

Chikhulupiliro chathu cha Uthenga wochotsa machimo adziko lapansi chiyenera kukhala madziko ntchito zathu za Ambuye ndi chikondi chathu pa Iye. Ngati timukonda Iye ndi chifuniro chathu ngati madziko athu, tizalephera mawa ndipo tisathera pozida ife tokha chifukwa cha machimo athu. Koma Yesu anachotsa machimo

athu onse. Machimo obadwanao, machimo athu amasiku onse akale, machimo amawa, ndi machimo amoyo wathu wonse. Iye sanasiye ngakhale m’modzi pa dziko lapansi kunja kwa chipulumutso chake.

Inde. Ngati chikondi chathu ndi chikhulupiliro chathu ziima pa chifuniro chathu. Koma, sitizakhoza mu chikhulupiliro chathu. Koma, chifukwa chikondi chathu ndi chikhulupiliro chathu chidzaima pa Uthenga Wabwino wochotsa machimo wa Yesu umene unaperekedwa kwa ife, ndife kale ana a Mulungu, olungama. Chifukwa tikhulupilira mu chipulumutso cha ubatizo wamadzi ndi Mzimu Woyera, ndife opanda tchimo.

Ndipo chifukwa chipulumutso chathu chafika, osati kuchokera ku chikondi cha Mulungu, malamulo ake oona achipulumutso kudzera mukuchotsa machimo athu, ndife olungama ngakhale sitiri okwanira kapena ofooka m’moyo wathu onse. Tidzapita ku ufumu wakumwamba

Page 255: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

255 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

ndipo tidzathokoza Mulungu kwa muyaya. Kodi mukhulupilira izi?

Yesu anati, “Osati chifukwa munandikonda, koma chifukwa Ine ndinakukondani.” Muchikondi ichi, osati chifukwa munandikonda ine, koma kudzera mu ubatizo wamadzi ndi Mzimu Woyera, tsopano tiyenera kukhala ndi chikhulupiliro cha Uthenga Wabwino wochotsa machimo, ubatizo wa Yesu ndi kukhetsa mwazi wake pa mtanda.

Ngati Mulungu sanatipulumutse ndi Uthenga Wabwino wochotsa machimo, sitikanapulumuka ngakhale tikhulupilire motani. Koma Yesu anachotsa machimo athu onse amene tinachimwa m’mitima yathu ndi mumathupi athu.

Kuti ife tikhulupilire mwa Mulungu, kuti tikhale olungama, tiyenera kukhla wokhazikika pa chipulumutso chathu, kudzera mu chikhulupiliro cha Mau ndi madzi aubatizo ndi Mzimu Woyera, Uthenga wochotsa machimo. Uthenga wochotsa machimo onse adziko lapansi ndi kukhala ndi chikhulupiliro mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi

wake. Uthenga wochotsa machimo ndi chikhulupiliro choona, ndi madziko oona achipulumutso, ndi khomo la Uthenga Wabwino wa Mulungu.

MUNTHU AYENERA KUKANA CHIKHULUPILIRO CHOBWERA CHIFUKWA CHA KUFUNA KWAKE

Kodi chikhulupiliro choona

chimachokera kuti?

Chimachokera ku chikondi cha Mulungu amene anatichotsera

kale machimo athu a m’tsogolo

Page 256: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

256 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Chikhulupiliro, kapena chikondi chobwera mwa kufuna kwa munthu, si chikondi kapenanso chikhulupiliro choona. Pali anthu ambiri pa dziko lino lapansi amene poyamba anakhulupilira Yesu ndi m’tima wao onse, koma pambuyo pake adataya chikhulupiliro chao chonse chifukwa cha machimo amene ali m’mitima mwao.

Koma ife tiyenera kudziœa kuti Yesu adachotsa machimo onse a dziko lapansi: Osati mphulupulu zosaonekera zokha, komanso machimo akulu akulu amene timachita chifukwa cha umbuli.

Pa Yohane mutu 13, Yesu adasonkhanitsa ophunzira ake kuti aaphunzitse za m’mene chipulumutso chake chiliri, Iye adasonkhanitsa ophunzirawo asanapachikidwe pa mtanda. Asanadye chakudya cha madzulo, Yesu adatsuka mapazi a ophunzira pofuna kuœaonetsa cholinga cha chipulumutso chake. Ife tonse tiyenera kudziœa ndiponso kukhulupilira Uthenga wa chikhululukiro cha machimo umene Yesu adaphunzitsa ophunzira ake pa kutsuka mapazi ao.

Koma poyamba Petro adakana kuti Yesu amutsuke mapazi ake, “Simudzandisambitsa konse mapazi anga.” Uku kunali kuonetsa chikhulupiliro chobwera mwa kufuna kwake. Koma Yesu adamuuza kuti, “Zimene ndi kuchitazi, sukuzidziœa tsopano koma udzazidziœa m’tsogolo muno.”

Tsopano, chifukwa cha Uthenga wa madzi ndi Mzimu Woyera, tikhoza kumvetsa bwino za Yesu Khristu. Aœa ndi mau a choonadi, Uthenga wa madzi ndi Mzimu Woyera wa chikhululukiro cha machimo, umene umasandutsa munthu kukhala olungama pa kukhulupilira ndi m’tima wake wonse.

Petro ndi ophunzira ena adapita kukapha nsomba. Iwo anali kupha nsomba monga momwe anachitira asanakumane ndi Yesu. Kenaka Yesu adaonekera kwa iwo ndikuwaitana. Pa nthaœiyo Yesu adakonza chakudya cha m’maœa, ndipo pamene iwo anali kudya cha kudyacho Petro anazindikira tanthauzo la mau amene ananena

Page 257: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

257 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Yesu kuti, “Zimene ndikuchitazi sukuzidziœa tsopano koma udzadzidziœa m’tsogolo muno.” Iye adazindikira pambuyo pake mau amene Yesu adanena pamene ankamutsuka mapazi.

“Ambuye adatsuka machimo anga onse. Machimo onse amene ine ndi machita chifukwa cha kufooka kwanga kuphatikizapo machimo onse amene ndidzachite m’tsogolo.” Choncho Petro adachotsa chikhulupiliro chobwera mwa kufuna kwake ndikuyamba kukhulupilira ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake, Uthenga wa chikhululukiro cha machimo.

Atatha kudya, Yesu adafunsa Petro kuti, “Kodi umandikonda kuposa aœa?” Modzazidwa ndi chikhulupiliro ndiponso chikondi, Petro adanena zimenezi chifukwa adakumbukira mau a Yesu akuti, “Koma udzazidziœa m’tsogolo muno.” Petro analandira chikhulupiliro choona, chikhulupiliro mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu Khristu, Uthenga wa chikhululukiro cha machimo.

PAMBUYO PAKE PETRO ADAKHALA MTUMIKI WOONA WA MULUNGU

Choncho, pambuyo pake, Petro ndi ophunzira

ena aja adalalika Uthenga Wabwino mpaka ku mapeto kwa moyo wao. Ngakhale Paulo, amene ankhazunza akhristu mopanda chifundo, adachitira umboni za Uthenga Wabwino m’masiku ovuta aja a Boma la Aroma.

Kodi mungakhale bwanji mtumiki woona wa Mulungu?

Pakukhulupilira nsembe ya

muyaya yochotsera machimo anu

Mwa ophunzira khumi ndi aœiri a Yesu,

Yudasi adagulitsa Yesu ndipo pambuyo pake

Page 258: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

258 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

adadzipha yekha. Motero, Mtumwi Paulo ndi amene analoœa m’malo mwake. Ophunzirawo asankha Matiyasi, koma Mulungu anasankha Paulo, ndi iye adakhala mtumiki wa Yesu ndipo anayamba kulalika Uthenga wa chikhululukiro cha machimo pamodzi ndi ophunzira ena aja.

Ambiri mwa ophunzira a Yesu, adafa monga anthu ofera chipembedzo chao. Ngakhale pamene anali kuopsezedwa kuti adzaphedwa, Iwo adapitiriza kulalika Uthenga woona.

“Yesu Khristu anachotsa machimo athupi lanu ndi ubatizo wake ndiponso mwazi wake, Uthenga wa chikhululukiro cha machimo. Yesu adachotsa machimo anu onse pakubatizidwa mu m’tsinje wa Yolodane ndi ku landira chilango cha imfa ya pa Mtanda. Khulupilirani Uthenga wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake pa mtanda kuti mpulumutsidwe.”

Ndipo anthu ambiri anapulumutsidwa pakumva Uthenga umenewu ndi kukhulupilira. Inali mphamvu ya kukhulupilira mu Uthenga wa

ubatizo wa Yesu, mwazi wake ndi Mzimu Woyera.

Ophunzira a Yesu adalalika Uthenga wa madzi ndi Mzimu Woyera, “Yesu ndi Mulungu ndiponso Mpulumutsi.” Tsono popeza iwo adachitira umboni za Uthenga wa madzi ndi Mzimu Woyera, Inu ndi ine tsopano tikhoza kumva Uthenga wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake, wa chipulumutso kuti tipulumuke ku machimo athu. Chifukwa cha chikondi cha Mulungu ndi chipulumutso chathunthu cha Yesu Khristu, ife tonse takhala ophunzira ake.

Kodi inu nonse mumakhulupilira? Yesu anatikonda kwambiri motero nchifukwa chake iye anatipatsa Uthenga wa madzi ndi Mzimu Woyera, wa chikhululukiro ndipo kudzera mu Uthenga umenewu timakhala ophunzira olungama a Yesu. Tsono pofuna kuœaphunzitsa Uthenga woona wa chikhululukiro cha machimo, Yesu adasambitsa mapazi a ophunzira ake.

Yesu adasambitsa mapazi a ophunzira ake kuti

Page 259: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

259 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

aœaphunzitse iwo ndiponso ife kuti machimo adatsukidwa kotheratu pamene Yesu anabatizidwa ndi kukhetsa mwazi wake pa mtanda. Ndipo ife tiyenera kuthokoza Yesu chifukwa cha chikondi chake ndiponso potipatsa ife uthenga wachikhululukiro cha machimo.

Yesu adatiphunzitsa zinthu ziœiri pamene adatsuka mapazi a ophunzira ake. Poyamba, iye anafuna kuphunzitsa ophunzirawo monga ananenera poyamba paja kuti, “Zimene ndikuchitazi, sukuzidziœa tsopano koma udzazidziœa m’tsogolo muno,” kuti machimo athu onse anachotsedwa ndi Uthenga wa chikhululukiro cha machimo kudzera mu ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake.

Kunali kuœaphunzitsa kuti monga Yesu anadzichepetsa kuti apulumutse anthu ochimwa ndi kuwasandutsa olungama, ifenso obadwa mwatsopano, tiyenera kuuza anzathu Uthenga wachikhululukiro cha machimo. Ndi chinthu chabwino kuti ife amene tinabadwa kale

mwatsopano tiphunzitse iwo amene akufuna kubadwa mwatsopano.

Zifukwa ziœiri zimene Yesu adasambitsira mapazi a ophunzira ake ndi zomveka bwino. Ndipo mpaka lero zikadalipobe mu mpingo.

Ophunzira sangapose mphunzitsi wake. Choncho timalalika Uthenga Wabwino ku dziko lonse lapansi ndi kulitumikira ngati tikutumikira Yesu. Ndipo ife amene tidapulumutsidwa poyambirira, tiyenera kutumikira anthu amene akubwera pambuyo pathu. Pofuna kuphunzitsa zimenezi, Yesu adasambitsa mapazi a ophunzira ake. Ndiponso pamene anatsuka mapazi a Petro, anationetsa kuti Iye ndiye Mpulumutsi wangwiro wa ife tonse kuti potero tisanyengedwenso ndi Satana.

Inu nonse mungapulumutsidwe pamene mukhulupilira Uthenga wa chikhululukiro cha machimo, Uthenga wa madzi ndi Mzimu Woyera. Yesu adatsuka machimo athu onse ndi ubatizo wake, kupachikidwa pa mtanda ndi kuuka

Page 260: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

260 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

kwakufa, motero anthu okhawo amene amakhulupilira Uthenga wake adzapulumitsidwa kwa muyaya ku machimo onse a dziko lapansi.

KUKHALA NDI CHIKHULUPILIRO MU UTHENGA UMENE UDACHOTSA MACHIMO ATHU A TSIKU NDI TSIKU

Tikhoza kuthetsa mabodza onse a M’dierekezi

pakukhulupilira Uthenga wa chikhululukiro cha machimo, mau a madzi ndi Mzimu Woyera. Anthu amanyengedwa mosavuta ndi Satana ndipo Satanayo amapitiriza ku nong’oneza m’makutu athu. Podziœa kuti thupi la munthu limakhalira kuchimwa, nanga angakhale bwanji opanda machimo? Anthu onse ndi ochimwa.

Tikudziœa yankho lake. “Podziœa kuti Yesu anachotsa machimo onse athupi lathu ndi ubatizo

wake, nanga munthu okhulupilira angakhale bwanji ndi uchimo? Popeza Yesu analipira mphotho ya machimo athu onse, nanga ndi tchimo lanji latsala kuti ife tilipire?”

Ngati sitikhulupilira Uthenga wa madzi ndi mwazi, mau a M’dierekezi amaoneka ngati oona. Koma ngati tili ndi Uthenga Wabwino, tikhoza kukhala ndi chikhulupiliro chosagwedezeka pa choona cha Mau a Mulungu.

Choncho ife tiyenera kukhala ndi chikhulupiliro mu Uthenga wa kubadwa mwatsopano mwa madzi ndi mwazi.

Chikhulupiliro choona ndicho kukhulupilira Uthenga wa ubatizo wa Yesu, mwazi wake pa Mtanda, ndiponso kuuka kwake.

Kodi mudachiona chithunzi cha m’mene Kachisi Woyera anamangidwira? Ndi nyumba yaing’ono. Nyumbayi anayigaœa m’zigawo ziœiri, gawo la kunja ndi malo oyera pamene gawo la m’kati ndi Malo Oyera kwambiri limene liri ndi mpando wa chifundo.

Page 261: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

261 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Pali mizati yokwana 60 kunja kwa kwachisiyo ndipo malo oyera ali ndi makhoma 48. Tiyenera kukhala ndi chithunzi cha Kachisi Woyera m’mitima mwathu pofuna kumvetsa bwino Mau a Mulungu.

KODI CHIPATA CHA KACHISI WOYERA ANACHIKONZA NDI CHIYANI?

Kodi chipata cha bwalo la kachisi woyerayo anachikonza

ndi chiyani?

Nsalu yobiliwira, yofiilira ndi yofiira ndi nsalu yabafuta yosalala

Chipata cha bwalo la Kachisi Woyera ali kufotokoza kamangidwe kake pa Eksodo 27:16, “Pa chipata cha bwalolo pakhale nsalu yochinga yobiliœira, yofiirira ndi yofiira, ndi yabafuta wosalala, wopikidwa bwino ndi wopetedwa mwaluso. Kutalika kwake kukhale mamita asanu ndi anayi. Ikhale ndi nsanamira zinai zomangidwa pa masinde anai.” Zinthu zimene anagwiritsa ntchito pomanga chipata chabwalo la kachisi woyera zinali zobiliœira, zofiirira, zofiira ndi zabafuta wosalala. Ndipo kachisi ameneyi anali wooneka bwino ndiponso wokongola.

Mulungu adalamula Mose a penthe bwino zochingira pa chipata cha bwalo la Kachisi Woyerayo ndi nsalu yobiriœira, yofiirira ndiponso yofiira kuti munthu aliyense aziona bwino chipata cha kachisiyo. Ndipo chipata chopenthedwa bwino ndi nsalu yobiriœira, yofiirira, yofiira ndipo yabafuta wosalala anali kuchiika pa nsanamira zinai.

Ndipo zipangizo zinai zonsezi zikufanizira

Page 262: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

262 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

chipulumutso chimene Mulungu adatikonzera kudzera mwa Mwana wake yemwenso ndi Mulungu.

Chinthu chilichonse chimene anachigwiritsa ntchito pomanga Kachisi Woyerayo chili ndi tanthauzo lake ndiponso chikuimirira Mau a Mulungu ndi chikonzero chake chopulumutsa anthu kudzera mwa Yesu Khristu.

Kodi ndi mitundu ingati ya zipangizo zimene anazigwiritsa ntchito pomanga chipata cha Kachisi Woyerayo? Wobiriœira, wofiirira, wofiira ndiponso bafuta wosalala Motero mitundu inai imeneyi ndiyothandiza kulimbikitsa chikhulupiliro chathu mu Uthenga wa kubadwanso mwatsopano. Zimenezi zikanakhala zopanda ntchito, sizikadalembedwa m’Baibulo mwatsatanetsatane.

Tsono popeza kuti chilichonse chimene anachigwiritsa ntchito pomanga chipata cha bwalo la Kachisi Woyera ndi chofunika pa chipulumutso chathu chimene chinachotsa machimo athu atsiku ndi tsiku, machimo amene tidabadwa nayo ndi

machimo athu a m’tsogolo chipatacho chinayenera kumangidwa ndi nsalu yobiriœira, yofiirira, yofiira ndi bafuta wosalala.

Choncho Mulungu adaulula zinthu zonsezi kwa Mose ndi kumuuza zonse zimene adzachite popanga kachisiyo.

KODI NSALU YOBIRIŒIRA, YOFIIRIRA, YOFIIRA NDI BAFUTA WOSALALA IKUTANTHAUZANJI NDI UTHENGA WA MULUNGU?

M’kati mwa Kachisi Woyera, nsalu yobiriœira,

yofiirira, yofiira ndi bafuta wosalala anali kupangira chochinga chimene anali kuchiika pakati pa Malo Oyera ndi Malo Oyera kwambiri. Ndipo nsalu yomweyi anali kupangira mikanjo ya wansembe amene ankatumikira m’kachisimo.

Page 263: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

263 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Kodi zipangizo zonse zomangira kachisi

zinkatanthauza chiyani?

Chipulumutso cha Yesu kudzera mu ubatizo wake

Nsalu yobiriœira ikutanthauza ubatizo wa Yesu.

Pa 1 Petro 3:21 mau akuti, “Madziwo akufanizira ubatizo umene masiku ano umakupulumutsani.” Ubatizo wa Yesu umene anachotsa nawo machimo onse adziko lapansi, Petro anatitsimikizira kuti ndi chifanizo cha nsembe ya chipulumutso. Machimo athu onse, machimo onse a dziko lapansi anaperekedwa kwa Yesu pa nthaœi ya ubatizo wake. Choncho nsalu yobiriœira, ubatizo wa Yesu ndi gawo lalikulu kwambiri M’mau a Mulungu, Mau a chipulumutso.

Nsalu yofiira ikufanizira mwazi wa Yesu,

pamene nsalu yofiirira ikufanizira ulemelero wake monga Mfumu, ndiponso Mulungu. Choncho mitundu itatu ya nsaluyi inali yofunika kwambiri pa chikhulupiliro chathu mwa Yesu Khristu ndi chipulumutso chake.

M’kanjo wokongola umene wansembe ankavala unkatchedwa mwinjiro, ndipo mwinjiro umenewu unkakhala wobiriœira. Wansembe wam’kulu ankavala nsalu mozungulira mutu wake ndi pankakhala chintu ngati mbale ya chitsulo cha m’tengo wapatali pamene panali mau akuti, ‘CHIYERO KWA AMBUYE’ ndipo mbale imeneyi ikankhala ndi maonekedwe obiriœira. ZOONA ZA CHIMENE NSALU YOBIRIŒIRA INKATANTHAUZA

Ndinayang’ana tanthauzo la nsalu yobiriœira

m’Baibulo. Kodi Baibulo limanena kuti chiyani za mtundu wobiriœira? Tiyenera kumvetsa za

Page 264: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

264 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

mitundu imeneyi wobiriœira, wofiirira, ndiponso wofiira.

Kodi nsalu yobiriwira ikufanizira chiyani?

Ubatizo wa Yesu

Nsalu yobiriœira itanthauza ubatizo wa Yesu.

Yesu Khristu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi kuti achotse machimo onse adziko lapansi (Mateo 3:15).

Yesu akadapanda kubatizidwa ndi kuchotsa machimo onse adziko lapansi, ife okhulupilira sitikanakhala oyera pa maso pa Mulungu. Motero, Yesu anayenera kubwera pa dziko lino lapansi kudzabatizidwa mu m’tsinje wa Yolodane ndi Yohane Mbatizi kuti adzachotse machimo onse adziko lapansi.

Chifukwa chimene ankaikira nsalu yobiriœira

pa chipata cha bwalo la Kachisi Woyera ndi chakuti ife sitikadatha kuyeretsedwa popanda ubatizo wa Yesu.

Nsalu yofiira inkatanthauza Mzimu Woyera, ndiponso Yesu monga “Mfumu ya mafumu onse ndiponso Mbuye wa ambuye onse.” (1 Timoteo 6:15).

Nsalu yofiira inkatanthauza mwazi wa Yesu Khristu umene anaukhetsa pa mtanda kuti apereke dipo la machimo athu. Yesu Khristu anabwera pa dziko lino lapansi monga munthu kuti adzanyamule machimo aanthu onse, asanapereke nsembe ya machimo pa mtanda. Ubatizo wa Yesu ndi uthenga woona wa chikhululukiro cha machimo umene ulosi wake unaonekera pa mitundu inai imene inakongoletsa Kachisi Woyera uja M’chipangano Chakale.

Nsanamira za kachisi zinali za mtengo wakesiyasi, zochingira zake zinali za mkuwa, zochinga za mkuwazi anachiphimba ndi zinthu za siliva.

Page 265: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

265 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Anthu onse ochimwa anayenera kulangidwa chifukwa mphotho ya uchimo ndi imfa. Munthu asana dalitsidwe nd Mulungu kuti apeze moyo wina ayenera kuweruzidwa chifukwa cha machimo ake.

Koma ubatizo wa Yesu M’chipangano Chatsopano, umene unafanizidwa ndi nsalu yobiriœira M’kachisi Woyera M’chipangano Chakale, udachotsa machimo athu onse. Iye ananyamula machimo onse mu imfa yake pa mtanda ndikukhetsa mwazi chifukwa cha machimowo ndi kupulumutsa ife tonse ndi Uthenga wake wa chikhululukiro. Iye ndi Mfumu ya mafumu ndiponso Mulungu Woyera.

Okondedwa, ubatizo wa Yesu ndiwo chipulumutso chathu chimene anatipatsa potichotsera machimo athu onse. Yesu Khristu, yemwenso ndi Mulungu, anabwera pansi pano monga munthu; Iye anapachikidwa pa mtanda ndi kukhetsa mwazi wake kulangidwa chifukwa cha ife. Ndipo ubatizo wa Yesu umatiuza mosakaika

konse kuti Iye ndiye Mpulumutsi woona wa anthu a mitundu yonse.

Tikhoza kuona zimenezi poyang’ana mitundu ya nsalu zija zimene adazigwiritsa ntchito pomanga Kachisi Woyera. Bafuta wosalala utanthauza kuti Yesu anatipulumutsa popanda kupatula munthu.

Popanda Kachisi Woyera ndi mitundu yonseyo kunali kufuna kutionetsa choonadi cha chipulumutso chimene Mulungu anatipatsa kudzera mwa Mwana wake. Ichi chinali chintu choyenera pa nsembe ya chipulumutso.

Tikhoza kuona kuti mitundu imene anaigwiritsa ntchito popanga chipata cha bwalo la Kachisi Woyera itanthauza kuti Yesu Khristu sanatipulumutse popanda kukonzekera. Iye anatipulumutsa potsatira chikonzero chimene Mulungu anachikonza mwa tsatane tsatane, iye anapachikidwa ndipo anaukanso kwa kufa kukwaniritsa chipulumutso cha anthu onse. Yesu anatipulumutsa kudzera mu Uthenga wa

Page 266: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

266 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

chikhululukiro umene unali kufanizidwa ndi mitundu inai ija. Yesu anapulumutsa onse okhulupilira mu Uthenga wake wa chipulumutso.

CHOCHINGA CHA MKUWA M’CHIPANGANO CHAKALE CHINALI CHITHUNZI THUNZI CHA UBATIZO WA M’CHIPANGANO CHATSOPANO

Nchifukwa chiyani wansembe ankasamba m’manja ndi mapzi

asanalowe malo oyera?

Chifukwa chakuti ankayenera kuima pa maso pa Mulungu

opanda uchimo

Cholinga chake ankachipanga ndi mkuwa. Mkuwa unali kuimirira chilango chimene Yesu analandira chifukwa cha ife. Mbale ya madzi inkafanizira Uthenga umene umatiuza kuti machimo athu anatsukidwa.

Mbale ya madzi itionetsanso m’mene machimo athu anachokera mwa ife kudzera mu ubatizo wake. Ichi n’chithunzithunzi cha choonadi chakuti machimo atsiku ndi tsiku aanthu onse anatsukidwa pakukhulupilira Mau a Uthenga wa ubatizo wa Yesu.

Gome loperekera nsembe yopsereza lifanizira chiœeruzo. Pamene madzi a Yesu, nsalu yobiriœira ndi Uthenga wa nsembe yochotsera machimo, ubatizo wa Yesu (Mateo 3:15, 1 Yohane 5:5-10). Aœa ndi mau aumboni wa Uthenga wa chipulumutso kudzera mu nsembe yochotsera machimo.

Pa 1 Yohane 5, akunena kuti, “Chimene timagonjetsera dziko lapansi ndi chikhulupiliro chathu, motero pali atatu aœa ochitira umboni:

Page 267: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

267 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Mzimu Woyera, madzi ndi magazi, ndipo atatuœa amavomerezana.” Ndipo adatiuzanso kuti amene amakhulupilira Mwana wa Mulungu ali nawo umboni wa madzi, mwazi ndi Mzimu Woyera.

Mulungu adalola kuti ife tiyeretsedwe pakukhulupilira Uthenga wa nsembe yochotsera machimo kuti tikaloœe M’kachisi Woyera. Motero, tsopano ife tingathe kukhala m’chikhulupiliro, ndi kulandira moyo wolungama, kudyetsedwa mau ake, ndikulandira madalitso. Kukhala ana a Mulungu kutanthauza kupulumutsidwa pa kukhulupilira Uthenga wa nsembe yochotsera machimo ndiponso kukhala M’kachisi Woyera.

Anthu ambiri amaganiza kuti kukhulupilira popanda kudziœa tanthauzo la mitundu inai imene anagwiritsa ntchito popanga Kachisi Woyera uja nkokwanira. Ngati munthu akhulupilira Yesu popanda kudziœa zimenezi ndiye kuti chikhulupiliro chakecho sichoona chifukwa mu m’tima mwake mukadali uchimo. Munthu amene

sakhulupilira Uthenga wa kubadwa mwatsopano mwa madzi, mwazi, ndi Mzimu Woyera ndiye kuti akadali ndi uchimo mu m’tima mwake.

Kodi munthu atafunsidwa kuti afotokozere za munthu amene sakumudziœa, ndipo pofuna ku sangalatsa womverayo akunena kuti, “Inde ndimam’khulupilira.” Kodi muganiza kuti munthu wofunsa uja adzakondwera? Mwina inu mungakondwere koma kukhulupilira uku sikumene Mulungu amafuna.

Mulungu akufuna ife tikhulupilire Uthenga wa chikhululukiro cha machimo, chipulumutso chimene Yesu adatipatsa kudzera mu ubatizo wake, ndiponso mwazi wake. Tiyenera kudziœa tisanakhulupilire m’mene Yesu anatipulumutsira ku machimo athu onse.

Pamene tikukhulupilira Yesu, tifunikanso kudziœa m’mene iye anatipulumutsira kumachimo athu onse kudzera m’madzi (ubatizo wake) ndiponso mwazi wake (imfa yake) ndi Mzimu Woyera (Yesu monga Mulungu).

Page 268: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

268 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Pamene timvetsa bwino zimenezi tikhoza kukhala ndi chikhulupiliro chenicheni. Chikhulupiliro chathu nchosakwanira ngati sitidziœa choonadi. Chikhulupiliro choona chimabwera pakumvetsa bwino umboni wa chipulumutso cha mwa Yesu, Uthenga wachikhululukiro, ndiponso Yesu monga Mpulumutsi woona wa anthu onse.

Kodi nanga chikhulupiliro chimene chimanyoza Yesu ndi chiti? Tiyeni tione.

CHIKHULUPILIRO CHIMENE CHIMANYOZA YESU

Kodi chofunika kwambiri pa chikhulupiliro ndi

chiyani?

Kudziwa choona chenicheni cha ubatizo wa Yesu

Muyenera kudziœa kuti kukhulupilira Yesu pakuganiza mwa inu nokha, ndikunyoza Yesu. Ngati mukuganiza kuti, “Nkovuta kukhulupilira, koma popeza Iye ndi Mulungu ndipo ndi Mwana wa Mulungu, ndiyenera ku m’khulupilira,” ndiye kuti mukunyoza Yesu. Muyenera kukhulupilira ubatizo ndi mwazi wa Yesu, imene ndi nsembe yochotsera machimo.

Kukhulupilira Yesu osadziœa Uthenga wa nsembe yochotsera machimo ndi choipa kwambiri kuposa kungokhala osakhulupilira. Kulalika Uthenga pamene wina akungokhulupilira mwazi wa Yesu wokha ndi kuvutika chabe ndipo palibe kudziœa choona.

Yesu safuna kuti munthu azimukhulupilira chifukwa chakuti iye wafuna kapenanso kukhulupilira iye popanda chifukwa chenicheni. Iye akufuna kuti ife tizimukhulupilira pakudziœa Uthenga wa nsembe yochotsera machimo.

Pamene tikhulupilira Yesu, timadziœanso kuti Uthenga wa nsembe yochotsera machimo ndi

Page 269: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

269 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

ubatizo ndiponso mwazi wake. Pamene tikukhulupilira Yesu, tiyeneranso kuzindikira Uthenga wa nsembe yochotsera machimo kudzera M’mau ake, ndi kudziœa bwino lomwe za m’mene Iye adachotsera machimo athu onse.

Ndiponso tiyenera kudziœa kuti mitundu yobiriœira, yofiirira, yofiira ndi bafuta wosalala imene anagwiritsa ntchito pa chipata chabwalo la Kachisi Woyera inali kufanizira chipulumutso chimene Mwana wa Mulungu adatipatsa. Pakutero tingathe kukhala ndi chikhulupiliro choona ndiponso cha muyaya.

SITINGABADWE MWATSOPANO POPANDA KUKHULUPILIRA YESU, AMENE ANAKWANIRITSA ZONSE ZIMENE NSALU YOBIRIŒIRA, YOFIIRIRA, YOFIIRA NDI BAFUTA WOSALALA ZINKAFANIZIRA

Kodi ansembe ankachita chiyani asanalowe m’kachisi

woyera?

Iwo ankasamba m’manja ndi kutsuka mapazi awo m’madzi ochokera ku chochinga cha

mkuwa Ambuye athu Yesu Khristu anatipulumutsa. Ife

tiyenera kutamanda Mulungu pamene tikuganizira za momwe Iye adatipulumutsira. Tiyenera

Page 270: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

270 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

kuyang’ana pa Kachisi Woyera uja. Iye adatipatsa Mau a Uthenga Wabwino wa nsembe yochotsera machimo kudzera m’mitundu inai ija ya M’kachisi Woyera ndi kutipulumutsa. Ife tikuthokoza ndi kutamanda Ambuye.

Anthu ochimwa sankaloœa M’kachisi Woyera popanda kulandira chiœeruzo. Nanga munthu akanaloœa bwanji M’kachisi woyera asanalandire chiœeruzo cha machimo ake? Sakadaloœa. Munthu otere akanaloœa, akanaphedwa nthaœi yomweyo. Ili silikanakhala dalitso koma chitaiko. Munthu ochimwa sankaloledwa kuloœa kapenanso kukhala M’kachisi Woyera.

Ambuye athu anatipulumutsa kudzera mu chinsinsi chobisika pa chipata cha bwalo la Kachisi Woyera. Ndi mtundu uja wobiriœira, wofiirira, wofiira ndi bafuta wosalala anatipulumutsa. Ndipo Iye anatiuza chinsinsi cha chipulumutso kudzera m’mitundu imeneyi.

Nanga inu ndi ine, kodi tinapulumutsidwa mwanjira imeneyi? Ngati ife sitikhulupilira mau

amenewa, sipangakhale chipulumutso kudzera mu Uthenga wansembe yochotsera machimo. Mtumdu wobiriœira sutanthauza ubatizo wa Yesu amene anachotsa machimo athu onse.

Munthu akhoza kuloœa mu gome loperekera nsembe yopsereza popanda kukhulupilira mtundu wa nsalu yobiriœira ija. Koma sangathe kuloœa Kumalo Oyera kumene Mulungu akulamulira.

Motero, tisanaloœe pa chipata cha Kachisi Woyera, tiyenera kukhulupilira ubatizo wa Yesu (nsalu yobiriœira) yofiira (mwazi wake pa mtanda) ndiponso nsalu yofiirira (Mwana wa Mulungu yemwenso ndi Mulungu). Ndipokhapo pamene ife tikhulupilira pamene Mulungu amativomereza kuloœa ku Malo Oyera kwambiri.

Anthu ena amaloœa bwalo la kunja kwa Kachisi woyera poganiza kuti ali m’kati. Koma ichi sichipulumutso konse ai. Kodi ife tingapite pa ulendo wautali bwanji kuti tipulumutsidwe? Tiyenera kuloœa ku Malo Oyera kwambiri.

Kuti tiloœe ku Malo Oyera kwambiri, tiyenera

Page 271: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

271 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

kuloœa podutsa pa chochinga cha m’kuwa. Chochinga cha m’kuwachi chikutanthauza ubatizo wa Yesu, ndipo tiyenera kuchotsa machimo athu atsiku ndi tsiku ndi ubatizo wa Yesu kuyeretsedwa kuti tikaloœe ku Malo Oyera.

M’chipangano Chakale ansembe anali kusamba asanaloœe M’kachisi Woyera, ndipo M’chipangano Chatsopano Yesu anatsuka mapazi a ophunzira ake kufanizira kuchotsedwa ku machimo awo.

Lamulo la Mulungu limanena kuti, “Mphotho ya uchimo ndi imfa, koma mphatso ya Mulungu ndiyo moyo wosatha mwa Yesu Ambuye athu”(Aroma 6:23). Mulungu amaœeruza machimo a munthu mopanda tsankho koma machimo athu anaœapereka kwa Yesu Mwana wake ndi ku muœeruza chifukwa cha machimowo. Ichi ndi chikondi cha Mulungu, ndiponso chipulumutso chimene Iye adatipatsa. Chipulumutso chenicheni timachipeza ngati tikhulupilira Uthenga wa nsembe wochotsera machimo, imene ndi ubatizo

wa Yesu, mwazi wake, imfa yake ndi kuuka kwake.

KUTI MUNTHU ABADWENSO MWATSOPANO, SAYENERA KUTAYA MAU A MULUNGU, UTHENGA WA NSEMBE YOCHOTSERA MACHIMO

Kodi chatsala nchiyani kuti ife tichite?

Ndi kukhulupilira Mau olembedwa a Mulungu

Ine sindinyoza anthu ena. Ngati akamba za

chinthu chimene ine sindikuchidziœa, ndi mamupempha kuti andiphunzitse. Koma pamene

Page 272: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

272 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

ndidafunsa tanthauzo la Kachisi Woyera palibe ndi m’modzi yemwe amene anandiyankha.

Nanga nkadachita chiyani? Ndinayenera kuœerenganso m’Baibulo. Tsono m’Baibulomo ndi pati pamene akukamba za Kachisi Woyera? Nkhani imeneyi ili mwatsatane tsatane m’buku la Eksodo. Kotero kuti ngati munthu aœerenga mosamala angathe kumvetsa tanthauzo lake kudzera M’mau olembedwa a Mulungu.

Okondedwa, simungapulumutsidwe pakukhulupilira Yesu popanda kudziœa zimene mukuchita. Simungabadwe mwatsopano pakupita kutchalichi kaœiri kaœiri. Tikudziœa zimene Yesu anauza Nikodemo. “Kodi iwe sindiwe mphunzitsi wodziœika pakati pa Aisraele, nanga sukumvetsa bwanji zimenezi? Ndithu ndikunenetsa kuti ngati munthu sabadwa m’madzi ndi mwa Mzimu Woyera sangathe kuloœa mu Ufumu wa Mulungu” (Yohane 3:5,10).

Onse amene amakhulupilira mtundu wobiriœira (umene uthanthauza kuti machimo athu

anaperekedwa kwa Yesu pamene adabatizidwa) ndiponso imfa yake ndi kukhulupilira kuti iye ndi Mulungu ndiponso Mpulumutsi adzapulumutsidwa.

Tiyenera kukhulupilira kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wa anthu onse ochimwa pa dziko lapansi. Popanda chikhulupiliro chimenechi, munthu sangathe kubadwanso mwatsopano ndiponso sangaloœe mu Ufumu wa Mulungu. Palibe munthu amene angathe kukhala wokhulupilira popanda Uthenga umenewu.

Kodi sichikadakhala chinthu chosavuta kubadwa mwatsopano pakukhulupilira Yesu? —Inde.— “♫Mwapulumutsidwa. Ine ndinapulumutsidwa. Ife tonse tinapulumutsidwa.♫” Zabwino kwambiri. Koma pali anthu ambiri okhulupilira Yesu koma ‘sanabadwenso mwatsopano.’

Munthu ayenera kudziœa choonadi m’Baibulo ndiponso kukhala ndi chikhulupiliro Uthenga wa chikhululukiro cha machimo ndiponso tanthauzo

Page 273: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

273 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

la nsalu yobiriœira, yofiirira, yofiira, bafuta wosalala kuti aloœe M’kachisi Woyera ndi kukakhala ndi Mulungu kudziko la chikhulupiliro. M’kati mwa kachisi wachikhulupiliro tikhoza kukhala wokondwa kufikira nthaœi imene ife tidzadziœe m’mene tingakhulupilire Yesu moyenera.

UTHENGA WABWINO UMABALA CHIYERO NDI NSALU YOBIRIŒIRA

Kodi chofunika nchiyani pa chipulumutso?

Ubatizo wa Yesu

Nthaœi zina munthu amaganiza kuti angathe kukhala ndi moyo wangwiro osalakwitsa. Pamene akuchita china chake, ndipamene amadziœa

kulephera kwake. Anthu ndi olephera, kotero kuti nkosatheka kukhala opanda uchimo. Koma popeza kuti Yesu anatipulumutsa ndi ubatizo, imfa ndi mwazi wake, womwenso ndi Uthenga wa nsembe yochotsera machimo tikhoza kuyeretsedwa ndi kuloœa M’kachisi Woyera wa Mulungu.

Mulungu akadapanda kutipulumutsa ndi nsalu yobiriœira, yofiirira, yofiira ndiponso bafuta wosalala, sitikanatha kuloœa ku Malo Oyera mwa ife tokha. Chifukwa chiyani? Ngati anthu okhawo amene ali ndi moyo wangwiro angakaloœe, panalibe munthu amene ali woyenera. Ngati munthu akhulupilira Yesu popanda Uthenga Wabwino, ndiye akungowonjezera machimo mu m’tima mwake.

Yesu anatipulumutsa ndi chikonzero chake cha chipulumutso, chipulumutso cha nsalu yobiriœira, yofiirira, yofiira ndiponso ya bafuta wosalala. Iye anachotsa machimo athu onse. Kodi inu mumakhululupilira zimenezi? —Inde.— Kodi inu muli ndi Uthenga wa chikhululukiro mu m’tima

Page 274: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

274 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

mwanu ndipo mulindi umboni wake? —Inde.— Pamene muchitira umboni za Uthenga

Wabwino mungathe kuika lamba wa nsalu wolembedwa kuti, ‘CHIYERO KWA AMBUYE’ ndikukhala pamodzi ndi ‘Ansembe achifumu’ (1 Petro 2:9). Ndipokhapo pamene mungathe kuima pa maso anthu ndi kuœauza kuti inu ndinu mtumiki wa Mulungu, kugwira ntchito monga wansembe wam’kulu.

Nsalu imene wansembe ankamanga kumutu inali ndi mbale ya golide ndipo chithunzi cha mbale ya golideyo ankachimanga ndi nsalu yobiriœira. Nchifukwa chiyani ankasankha mtundu wobiriœira. Chifukwa chakuti Yesu adatipulumutsa ndi Uthenga wa chikhululukiro, chifukwa chakuti Iye anachotsa machimo athu onse ndi kutisandutsa opanda uchimo ndi ubatizo wake (kusanjika manja kwa M’chipangano Chakale, ndiponso ubatizo wa M’chipangano Chatsopano).

Ngakhale tikhulupilire Yesu, sitingapeze

chithunzi cha mbale yolembedwa kuti, ‘CHIYERO KWA AMBUYE’ popanda chinsinsi cha Mau a mtundu wobiriœira, wofiirira, ndi yofiira

Kodi ife tinasanduka olungama bwanji? Pa Mateo 3:15, akunena kuti, “Umu ndi m’mene tiyenera kuchitira zimene Mulungu akufuna.” Yesu anabatizidwa ndi kutipulumutsa ku machimo athu onse adziko lapansi. Ndipo chifukwa chakuti Iye anabatizidwa ndi kutichotsera machimo athu onse, ife okhulupilira tinasanduka olungama.

Kodi tikananena bwanji kuti tilibe uchimo Yesu akadapanda kubatizidwa? Ngakhale tikanakhulupilira Yesu, ngakhale tikanalira pakuganizira imfa ya Yesu, misozi yathuyo sikanachotsa machimo athu. Ai. Ngakhale tikanalira, ndi kulapa, machimo akanakhalamo ndithu mwa ife.

‘CHIYERO KWA AMBUYE.’ Chifukwa chakuti Iye ananyamula machimo athu ndi ubatizo wake ndiponso mwazi wa anthu onse aperekedwa kwa Yesu ndiponso chifukwa chakuti Mau a

Page 275: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

275 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

chipulumutso analembedwa m’Baibulo, ife tasanduka olungama pakukhulupilira posaœerengera kuchooka kwathu.

Motero tikhoza kuima pa maso pa Mulungu tsopano. Tsopano tingathe kukhala monga anthu olungama ndi kulalika Uthenga Wabwino pa dziko lapansi. “♪A, ndapulumutsidwa. Inunso mwapulumutsidwa. Ife tapulumutsidwa.♪” Tinapulumutsidwa molingana ndi chikonzero cha Mulungu.

Popanda Mau a Uthenga Wabwino wansembe yochotsera machimo mu m’tima wanu, pali chipulumutso ngakhale muyetse bwanji. Ndichimodzi modzi ndi nyimbo yoziœika kwambiri ya Korean yokhuza chikondi chosabwedza. “♫Aa, m’tima wanga ukumenya m’sanga popanda chifukwa pamene ndimamuona iye, nthaœi zonse pamene ndili pafupi naye. Ndiyenera kukhala naye pa chibwenzi.♫” M’tima wanga umamenya m’sanga, koma osati wake. Koma chikondi changa sichobwezedwa.

Anthu ambiri akuganiza kuti chipulumutso chimabwera mu njira zambiri kwa anthu osiyana siyana. Amafunsa, “Kodi chifukwa nchiyani chimabwera kupsolera mu Uthenga Wabwino wa ubatizo wokha?” Ngati sichingabwere kupsolera mu Uthenga Wabwino wa ubatizo wa Yesu, ndiye kuti sichipulumutso chokwanira. Ndi njira yokhayo yimene tingakhalire wolungama kwenikweni pamaso pa Mulungu chifukwa ndi njira yokhayo yimene ingachotse machimo athu onse.

Page 276: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

276 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

KODI NDI CHIPULUMUTSO CHA NSALU YOBIRIŒIRA CHIMENE YESU ANATIPATSA IFE?

Kodi, chinatilungamitsa ife ndi chiyani?

Uthenga wa nsalu yobiriwira,

ndi yobiwira ndikufiira pang’ono ndi yofiira

Ndichipulumutso chopsolera mu Uthenga

Wabwino wansalu yobiriœira, yofiirira ndi yofiira ndi mphatso ya Mulungu ya anthu onse. Mphatso iyi inatilola ife kuloœa M’kachisi Woyera ndi kukhala ndi mtendere. Inatipanga ife kuti tikhale olungama. Yinatipanga ife kukhala olungama ndi kutilola ife kukhala munyumba ya Mulungu, ndi kuphunzira Mau Oyera m’kati mu nyumba ya Mulungu.

Pamene tikupita pamaso pa Mulungu kuti tipemphere, Uthenga Wabwino umatidalitsa ndi chikondi chake. Ichi ndi chifukwa chake chipulumutso ndi chofunika pa ife. Yesu akutiuza kuti timange nyumba zathu pa madziko olimba. Ndipo madziko olimba ndi ubatizo wa Yesu. Ife tonse tiyenera kupulumutsidwa, ndikukhala ndi chipulumutso kuti tipite ku mwamba, ndikupeza moyo wosatha, kuti tikhale ana a Mulungu.

Okondedwa abwenzi, chifukwa cha Uthenga Wabwino wansembe yochotsera machimo, tiri oyenera kuloœa M’kachisi Woyera ndi chikhulupiliro. Chifukwa machimo athu onse anachotsedwa (chifukwa cha ubatizo wa Yesu) ndi kuweruzidwa pa mtanda, tiri kupulumutsidwa chifukwa chokhulupilira mu Uthenga Wabwino wa ubatizo wa Yesu.

Nsembe yochuluka yochotsera machimo athu onse, ubatizo ndi mwazi wa Yesu ndi Uthenga Wabwino umene unachotsa machimo athu onse. Kodi mukhulupilira zimenezi? Uthenga oona ndi

Page 277: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

277 Uthenga œa kuchuluka kwa nsembe yochotsera machimo

◄ Zam'kati ►

Uthenga wakumwamba wansembe yochotsera machimo athu onse.

Tinabadwanso kachiœiri chifukwa chokulupilira Uthenga Wabwino wansembe yochotsera machimo. Yesu anatipatsa nsembe yochotsera machimo imene imachotsa machimo athu amasiku onse. Yamikani Ambuye. Aleluya! Yamikani Ambuye.

Uthenga wa madzi aubatizo ndi Mzimu Woyera (Uthenga Wabwino wa madzi ndi mwazi) ndi Uthenga Wabwino oona umene unanenedwa ndi Yesu Khristu. Buku ili linalembedwa kuti lionetse Uthenga Wabwino wa Yesu Uthenga wa madzi aubatizo ndi Mzimu Woyera.

Chifukwa anthu ambiri amakhulupilira mwa Yesu popanda kudziœa zoona zenizeni, ameneœa ali m’chipembezo cha chikhristu chabe, chipembezo chabe, ndi chipembezo choona, ndi chotsokoneza. Choncho tiyenera kubwereratso kumbuyo mu Uthenga Wabwino. Sitinachedwe ai.

Ndikufuna kuti tiyende mwatsatane tsatane

m’buku lachiœiri chifukwa cha amene ali ndi mafunso okhuza Uthenga Wabwino wakubadwanso kachiœiri wamadzi ndi Mzimu Woyera.

Page 278: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

◄ Zam'kati ►

MAU OYAMBA OONJEZERA

Maumboni

achipulumutso

Page 279: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

279 Maumboni achipulumutso

◄ Zam'kati ►

Maumboni achipulumutso

Mlongo Eun-Young Hwang Alemekezeke Mulungu amene anandipulumutsa

kukumangidwa ndi machimo. Ndinakula ngati m’khristu, koma osati m’khristu oona. M’mene ndinali kukula, kupita ku tchalichi chinali ngati khalidwe chabe. Ndinali kubwerera m’mbuyo chifukwa cha za dziko. Ndinali kuyetsa kufuna nzeru za dziko lapansi kwambiri kusiyana ndi Mulungu. Ndinayamba kusapita kutchalichi kukapembeza masiku onse ndipo ndinali kupembezera chikhululukiro cha machimo amenewo. Khalidwe ili loipa linatenga nthaœi. Masiku amenewo kunali mavuto ambiri kusiyana ndi chisangalalo.

Pamene ndinatsiriza maphunziro anga aku sekondale sukulu, sindinapite ku koleji. Pamene anzanga anali kukodzekera mayeso oloœera ku

koleji ndinali kufunafuna ntchito, pamene ndinali kugwira ganyu. Inali nthaœi yovuta kwambiri. Sindinali kuthakukhala osakhumudwa.

Koma ndinali ndi mwai womva Mau a Mulungu. Ndinali kukumana ndi abwenzi ndi alongo muchikhulupiliro kupsolera kwa m’kulu wanga, ndikumva kwa nthaœi yoyamba Uthenga Wabwino woona. Ndinali kudziœa mauwa, koma osati kudziœa tanthauzo lake loona.

“Koma Yesu adamuyankha kuti, ‘Tsopano lino vomera, chifukwa ndi m’mene tiyenera kuchitira zonse zimene Mulungu akufuna’” (Mateo3:15). Apo Yohane adavomera. Sizinali kundisangalasa poyamba koma pamene masiku anapitapo ndiyamba kumvetsa Uthenga Wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake. Uthenga Wabwino umene unadzudza mzimu wanga ku imfa kupsolera mu chikhulupiliro. Ndinakumbikira kuti sindiyenera kukaika. Ndinali wosamvetsa. Ndinayamba kuganiza kuti Mau ake ndi ofunika kwambiri. Ndipo ndinakhulupilira kuti Mulungu

Page 280: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

280 Maumboni achipulumutso

◄ Zam'kati ►

ndi wamoyo. Ndine wokondwa kuti ndikhala moyo woona wokhulupilika. Ndimakhulupilira zoona kuti mu m’tima wanga mulibe uchimo.

Alemekezeke Mulungu amene anandipulumutsa ku machimo.

M’bale Jae –dong Park Koma Yesu adamuyankha kuti, “Tsopano lino

vomera, chifukwa ndi m’mene tiyenera kuchitira zonse zimene Mulungu akufuna.” Apo Yohane adavomera. (Mateo 3:15)

Amene anazodzedwa kuti afere machimo ake anapulumutsidwa. Alemekezedwe Mulungu.

“Khala nazo nyanga zako ndi matsenga ako. Wakhala ukuzigwiritsa ntchito chiyambire cha ubwana wako. Mwina mwake zingakuthandize kapena nkuopsanazo adani ako.” (Yesaya 47:12). Ndinachitanso zimenezi.

Ndinabadwa m’banja lokonda banja lawo kwa amayi okonda chipembezo cha chibuda. Pamene ndinali kukula, ndinali kutsirira chipembezo cha chibuda mumisasa yao ndi kusunga pa m’tima mau a chipembezo cha chibuda ndi kupita ku tchalichi masiku onse. Ndinali kusakhulupilira miyambo imene akazi ambiri achibuda anali kutsatira ndi nali kuyetsa kupedza zinthu zina

Page 281: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

281 Maumboni achipulumutso

◄ Zam'kati ►

zimene zingandipatse tanthauzo la umoyo. Ndinali kuona kulema ndi uchimo mu m’tima wanga, ndipo ndinali kuyetsa kuongola khalidwe langa, ndipo ndinali kulemekezedwa ndi anthu ondizungulira.

Pamene ndinali kupita ku koleji ku mzinda wa Sokcho, ndinakumana ndi m’zanga amene anali mkhristu. Iyi yinali nthaœi imene ndinasintha moyo wanga. Mulungu ndiye anakonza kuti tikumane. Pambuyo pake ndinaona kuti m’zanga, amene ndinali kugwirizana naye anagwa m’chipembezo cha miyambo ndi mphamvu koma osapeza mtendere mu moyo wake; ndinali ndi chitsoni kwambiri ndi iye. Mu tchalichi, ndinakumbukira ntchito zanga zabwino zoumiriza zinali uchimo.

(Marko 7:21-22) akuti, “Chifukwa m’kati mwamitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za chiwerewere, zakuba, zakupha, zigololo, matsiriro, kuipa m’tima, kunyenga, zonyansa, kaduka, kunyoza, kudzikuza, ndiponso kupusa.”

Ndinazindikira kuti sindinali kuchita zabwino chifukwa maganizo anga anali ozadza ndi zinthu zoipa, ndipo vuto langa la uchimo silinathe. Ndinali kupita kugehena. Kuchokera pamenepo ndinayamba kuganizira za machimo anga ndipo ndifunafuna thandizo kwa m’busa Samuel Jungsoo Kim. Anandiphunzitsa kutiYesu ndi amene Yohane 1:29 wochotsa machimo aanthu a pa dziko lonse lapansi” ndipo kuti anachotsa machimo anga ndikulipila mumalo mwanga. Ichi chinachipeputsa ndipo maganizo anga anali pa mtendere.

Pambuyo pake ndinakumana ndi m’busa Paulo Jong ndi kuphunzira m’mene Yesu anachotsera machimo athu onse ndi m’mene ana Aisraele anali kuperekera nsembe M’chipangano Chakale. Ndipo ndinakumbukira chifukwa chimene Yesu, amene anabadwa mwa mphamvu ya Mzimu Woyera (Mateo 1:20), anali kuyenera kunyozedwa ndi kupachikidwa pam’tengo (Agalatia 3:13).

“Tsopano lino vomera, chifukwa ndi m’mene tiyenera kuchitaira.” Apo Yohane adavomera

Page 282: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

282 Maumboni achipulumutso

◄ Zam'kati ►

(Mateo 3:15). Yohane Mbatizi, monga wansembe wam’kulu, anabatiza ndi kupereka machimo onse pa Yesu Khristu, Mwana Wankhosa wa Mulungu wopanda banga. Yesu analipira machimo onse pa mtanda.

Uwu ndi Uthenga Wabwino woona umene unandidzudza ndi kundipatsa chilungamo.

(2 Akorinto 5:17) akuti, “Choncho ngati munthu ali mwa khristu, ngwolengedwa kwatsopano.” Zakal zapita, zimene zilipo nzatsopano. Izi zinali chimodzi modzi kwa ine. Ndinalapa chifukwa cha moyo wanga (Ntchito 11:18) ndipo anabatizidwa mwa Khristu, ndipo sipadzakhala kutsutsidwa kwa ife (Aroma 8:1). Ndikuonekera m’chisomo chake ndipo ndi kuyamika Mulungu chifukwa chondipulumutsa. Ndipemphera kuti onse amene akuvutika ndi uchimo ndi kupedza Yesu apedze Uthenga Wabwino wa chiombolo mwa Iye! Aleluya.

Mlongo Sung-Yuh kim

Ndinakwatira pamene ndinali ndi zaka khumi ndi zisanu ndi zinai, ndipo banja la mwamuna wanga linali losauka kwambiri. Kuchokera pamenepo sindinali wotha kulankhula kapena kukondedwa ndi mwamuna wanga. Nthaœi zonse ndinali kuchita nsanje ndi akazi ena amene anali ndi amuna achikondi ndi osamala mabanja awo. Banja la mwamuna wanga linali lokhulupilira milungu ya mapari, ndi bambo wa mwamuna wanga anali sing’anga waulosi. Mwamuna wanga analoœa ntchito ya usilikali patangopita masiku atatu titangokwatirana, ndipo mung’ono wa mwamuna wanga anasokonozeka bongo pa msinkhu wa zaka makumi aœiri ndi ziœiri. Kuposa pamenepo amai amwamuna wanga anakhala osaona pamene anali ndi zaka makumi asanu.

Ndipo chifukwa sindinali ophunzira ndiponso osakongola kapena kukhala ndinzeru., ndinali

Page 283: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

283 Maumboni achipulumutso

◄ Zam'kati ►

kuganiza kuti moyo wanga uyenera kukhala choncho. Mai wa mwamuna wanga analikuyenera kuchitika opalechoni, koma sindina atengere ku chipatala ndipo sindinafunenso kuti ndiœagulire mankhwala. Ndinali kuganiza kuti ayenera kudwala ndikufa basi.

Topanso ndili ndi zaka makumi asanu ndi zinai ndipo a mai a mwamuna wanga anafa zaka ziœiri zapitazo. Pali mau akuti sibwino kuika munthu wakufa ndi chotsamira chake.

Kuyambira pamenepo analikubwera kwa ine mu maloto, ndipo ndili ndi chisoni chifukwa ndinaika chotsamira chao mu bokosi lamaliro ndipo kuti ndinali waukali kwa iwo pamene anali ndi moyo. Anthu ena amaoneka abwino kwa makolo a amuna awo, koma ine masiku onse sindinali nawo ndi chikondi. Ndinavutika ndi maloto ndikhala ngati munthu wakufa nthaœi zina chifukwa cha zimenezi.

Ndili ndi mwana wamwamuna ndi akazi anai. Ndinali ndi mantha kuti mwina zinthu zina zoipa

zingathe kuchitika kwa mwana ameneyu. Pamene ndinauza anzathu okhala nawo pamodzi za maloto anga anzathu anandiuza kuti mizimu yoipa iyenera kuchotsedwa. Ndinapita kukaonana ndi Shamans ndipo ndinapita ku nyumba yamapemphero ndi kugwada pansi ndi kupempha kuti zisiye koma sizinathandize. Ndinali kuona ngati ndi tsiriza moyo wanga kuti ndikhale bwino mukulefuka kwanga.

Ngati sindinamupeze Yesu kapena kuomboledwa, sindikanakhala ndi moyo masiku ano. Tsiku lina ndinathaœa panyumba yanga ndi kupita kunyumba ya mwana wanga wa m’kazi kuti ndikapume ndi kutenga mankhwala azisamba. Inali nthaœi imene Mulungu anadionetsa njira ya umoyo. Mwana wanga ndim’khristu wobadwanso kachiœiri ndipo anaitana m’kazi wa m’busa wake ndipo akazi angapo anabwera ndipo analankhula nane.

Sindinali kudziœa kanthu ndiza Mulungu. Koma pamene ananena kuti Yesu anachotsa

Page 284: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

284 Maumboni achipulumutso

◄ Zam'kati ►

machimo anga onse, ndiyamba kuganiza kukhulupilira mu Mau ake. Ndinali kuletsa ana anga kupita ku tchalichi chifukwa ndinali kuganiza kuti angabweretse mavuto okhala ndi milungu iœiri pa nyumba. Koma sindinali kuganiza kuti zinthu zingaipe koposa izi ndipo sindinali kufuna kumwalira ngati ochimwa ai.

M’kazi wa m’busa anandiuza kuti anthu onse ndi obadwa ndi uchimo koma Mulungu anachotsa machimo athu onse kupsolera mwa Yesu ndipo sitingakhalenso ochimwa ai ngati tikhulupilira mwa Yesu. Ndinayamba kupita ku tchalichi ndi kuyetsa ku mvetsa Mau a Mulungu koma sindinali kumvetsa. Koma pamene masiku anali kupita Mau ake anayamba kumveka kwa ine. Ndinadzindikira kuti ndinabadwa ndi uchimo ndipo sindingazithandize monga munthu wochimwa chifukwa cha machimo obadwa nawo. Ndipo ndinaona kuti maganizo oipa mumutu mwanga anali amachimo pamaso pa Mulungu.

Kupereka nsembe M’chipangano Chatsopano

inali njira yake yotisonyeza zimene zinali kubwera. Ndipo Yesu, monga momwe zinali kuchitikira M’chipangano Chakale, anabatizidwa ndipo machimo anga onse anaperekedwa pa Iye mu m’tsinje wa Yolodane. Anachotsa machimo anga onse ndikukhetsa mwazi wake pa Mtanda kuti alipire mu malo mwanga.

Pambuyo pake ndinamvetsa kuti ndilibe tchimo, ndipo palibe amene anganditsutse ine. Ndipo ndidzagona mu mtendere.

(Aroma 8:1) akuti, “Motero tsopano palibiretu mlandu wotsutsa anthu amene amakhala mwa Khristu Yesu.” Ndinavutika kwambiri ndi uchimo mu m’tima wanga ndipo tsopano uchimo wachoka. Ndilibe tsopano kuchita maloto.

Sindingakwanitse kulemba zimene ndiganiza chifukwa sindidziœa kuœerenga mokwanira koma ndingathe kufotokozera anthu za Ambuye athu Yesu Khristu m’mene anachotsera machimo anga mu m’tima wanga. Ndikupembeza kuti Yesu adzapulumutsa mwamuna wanga ndi ena am’banja

Page 285: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

285 Maumboni achipulumutso

◄ Zam'kati ►

langa monga momwe anandipulumutsa ine. Ndipo ndi kukhulupilira kuti umboni uwu udzathandiza ena kuti apeze chiombolo mwa Yesu.

Ndikuthokoza Mulungu chifukwa chondipulumutsa ndipo tsopano ndili okondwa kuti ndili oyenera kufalitsa Uthenga Wabwino kwa anthu ena ambiri. Tsopano sindikuchitira nsanje olemera ndi anthu ena abwino.

Mubale Sung-min Choi Aleluya! Alemekezeke Mulungu amene anandipulumutsa

kuchokera kugehena kupsolera mwa Yesu ndikundipanga olungama ndi opanda tchimo. Sindinali kudzindikira kuti ndinali ochimwa ofooka kwambiri mpaka ntalandira chiombolo cha Uthenga Wabwino. “Ndinamva kuti ife tonse tili pansi pa uchimo,” ndipo kuti, “palibe munthu wolungama, ai ndithu ndi m’modzi yemwe” (Aroma 3:10) ndipo ndiganiza kuti zingakhale zoona. Ndinali kuganiza kuti ndine ochimwa chifukwa anthu onse ankandiuza choncho, kupsolera m’Baibulo. Ndinakumana ndi m’busa Paulo Jong pamene anabwera ku tchalichi kwathu.

Poyamba sindinali kumumvetsa. Maphunziro ake anali achilendo kwa ine, ndi m’tima wanga unasokonezeka nawo motero makutu anga anatsekeka ku Uthenga Wabwino woona. Koma chikhulupiliro chinali kubwera pomvetsera Mau a

Page 286: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

286 Maumboni achipulumutso

◄ Zam'kati ►

Mulungu. Pamene ndinali kupitiriza kumvetsa, ndinayamba kumvetsa Uthenga Wabwino woona ndipo ndinayamba kukhulupilira. Potsiriza ndinavomera mu m’tima wanga mfundo yoti Yesu anachotsa machimo anga onse pamene anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi ndi kufa pa mtanda kuti alipire machimo anga onse.

Tsopano, chimene chingabwere, sindikuonanso kuti ndingatsutsidwe ndipo ndinena zoona kuti ndine olungama. Sindikudziœa tsiku lenileni limene Ambuye azabwera koma ndikhulupilira kuti ndine wopulumutsidwa. Ndinatenga Mau amumabuku aœa Levitiko 1:4; Mateyu 3:15; ndiponso Yohane 1:29 mu m’tima wanga.

Mu masiku a Chipangano Chakale, anthu afuko la Israele anali kupereka ng’ombe yamphongo kapena mwana wankhosa wopanda chilema, ndi kusanjika manja awo pa mutu wansembe yochotsera machimo kuti apereke machimo awo ndipo machimo awo analikuchoka. Koma nsembe yochotsera machimo siinali yokwanira kuti ichotse

machimo athu onse. Sitingathe kulapa machimo athu onse amene timalakwa masiku onse.

Yesu anadzipereka yekha ngati nsembe yochotsera machimo onse pa nthaœi imodzi. Yesu anali wopanda tchimo, munjira yina, anali nsembe yolungama, yopanda chilema. Iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi kuti achotse machimo onse adziko lapansi. Machimo onse amene ndinachimwa pa moyo wanga anaperekedwa pa Iye. Koma, popanda kukhetsa mwazi, sipakanakhala chikhululukiro cha machimo (Aheberi 9:21). Choncho Yesu anafera pa mtanda.

Uthenga Wabwino unakhala chikhulupiliro mu m’tima wanga, ndipo tsopano ndikhulupilira kuti machimo anga anakhululukidwa. Ndinabadwanso kachiœiri ngati mwana wakhanda ngati wabadwa kuchokera m’mimba mwa amai ake. Tsopano ndine wolungama. Chikhulupiliro changa pakati pano sicholimba ndipo ndikadali kuchimwa, koma pamene ndiganiza kuti Yesu anachotsa kale

Page 287: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

287 Maumboni achipulumutso

◄ Zam'kati ►

kufooka kwanga, ndimakondwera ndi kuthokoza Mulungu.

Kaœirikaœiri, sindinali kusangalala ndi maulaliki, koma tsopano akubwera kwa ine ngati Mau ake a Mulungu. Ndipameza kuti ndimafuna kumvetsera. Ndiponso ndili ndi m’tima wofuna kufalitsa Uthenga Wabwino kwa iwo amene sanapulumutsidwe. Ndimadzindikira kuti ndikofunika kukhala ku gawo la tchalichi. M’tima wanga ndiwomvera ndi mozaza ndi kuthokoza. Tsopano ndimapewa kupembeza mafano amene ndinali kupemphera ndikuyang’anga kwa Mulungu.

Ndimadzichepetsa ndikukhulupilira kuti Mulungu adzanditsogolera ndi dzanja lake ndi kundigwiritsa ntchito kuti ndifalitse Uthenga wake. Ndikuthokoza Mulungu amene anandipulumutsa ndi kundipanga kuti ndikhale mwana wake.

Mtumwi Sang-duk Choi Ndinayang’ana masiku akumbuyo pamene ndi

sanaomboledwe. Ndinali mkhristu chabe. Nzoona ndinali ndi tchimo, koma zinalikuoneka ngati ndinalibe mavuto ambiri. Monga ngati anthu ena, ndinali wodzadza ndi chikhululukiro pamene ndioona machimo anga.

Monga m’mene analembera m’Baibulo, “Paja Malembo akuti, ‘Palibe munthu wolungama, ai ndithu ndi m’modzi yemwe’”(Aroma 3:10), ndinali kudziganizira ine ndekha kuti ndine wochimwa ndipo ndinali kupemphera kuti ndikhululukidwe, kupempha chikhululukiro nthaœi zonse. Ndinali kukonda kugwiritsa ntchito mau awa, “Bwerani kwa ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo” ndinali kuyetsa kudzipumitsa ndekha ku machimo anga.

Koma machimo anga anali kukulirakulira masiku onse. Ndinali kudabwa kuti kodi mpumulo umene anadilonjedza uli kuti, ndinali kuganiza

Page 288: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

288 Maumboni achipulumutso

◄ Zam'kati ►

kuti ndiyenera kunyamula machimo anga moyo wanga wonse. Sindinali kupuma chifukwa sindinali kudziœa choona.

Ndinali kupita ku misonkhano ili yonse ya chitsitsimutso ndipo poyamba ndinali ngati ndikusintha pomva Mau okweza apa zolankhulirapo. Pamene ndinali kumva Mau okweza anyimbo ndi mau okweza aabusa pamalo otentha, pamenepo, ndinali kuona ngati tonse ndife ochimwabe ndipo ochimwa sangapite ku mwamba. M’busa ndi am’sonkhano wachitsitsimutso anali kunena kuti ndiyenera kulapa masiku ali onse, ndikulemekeza abusa, ndikugwira ntchito mwa mphamvu m’mpingo, ndikupereka zopereka panthaœi yake nokhulupilira, ndi kukhala wolalika modzipereka. Iyi ndiyo inali njira yoti ndinali kuyenera kukhalira pa moyo wanga wa chikhristu ndiponso njira yoti ndidalitsidwe ndi Mulungu. Zonse zinali kumveka ngati zili bwino ndipo sindinali kuchitira mwina koma kutsatira malamulo awo mokhulupirika.

Anali kundiyamikira chifukwa cha ubwino ndikukhala mkhristu wokhulupirika ndipo kwa chaka kokha ntakhala pa mapemphero kwa nthaœi yoyamba, anandisankha kukhala wantchito wa Mulungu ngati wachiœiri kwa wansembe. Ndinali kuganiza kuti ndikuchita bwino. Koma pamene masiku anali kupita, sindinali kudzindikira zoona za chipulumutso changa, kapena mpumulo nawonso panalibe pa ine.

Kunalembedwa m’Baibulo, (Mateo 24:40) “Pa nthaœi imeneyo anthu aœiri adzakhala ali m’munda, m’modzi adzamtenga, winayo nkumusiya.” Mantha sanali kuchoka mumaganizo anga. Ntadzuka m’maœa ndinali kuyang’ana kuti mwina m’kazi wanga atengedwa okha mumwamba. Ndinayamba manjenje ndi kukaika za chipulumutso changa mu m’tima wanga. Komabe Mulungu anali kundikonda kwambiri ndipo ananditsogolera ku tchalichi yaku Whapyong mu m’zinda wa Sokcho.

Ndinakumana ndi alaliki otchuka ambiri ndi

Page 289: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

289 Maumboni achipulumutso

◄ Zam'kati ►

abusa pa moyo wanga wonse wa chikhristu, koma madalitso amene ndinalandira kwa iwo sanakhalitse. Sanali kuthandiza pa mavuto a uchimo, koma Mulungu anatumiza m’busa Paulo Jong kwa ine, ndipo Uthenga Wabwino wachiombolo unadzadza mutchalitchi.

Koma Satana anayetsetsa kwambiri kuti andibwezere mumbuyo. Ndinayamba kuuma m’tima ndi kukana kumva Uthenga Wabwino pamenepo m’busa Jong analalika. Koma ndinapitiriza kupita kutchalichi mokhulupirika. Ndinkaona ngati ulaliki umodzi ankabwereza kaœirikaœiri.

Anali kunditenga ngati m’khristu wokhulupirika ndipo ankandiyetsa kuti ngati ndilibe tchimo pamene ndinatembenuka. Koma apa, ndinkadziona ndekha m’mene ndinalili ndipo ndinali ndi chisoni chifukwa cha machimo anga onse ngakhale amene anali obisika mu m’tma wanga.

Monga momwe analembera (Marko 7:21) chifukwa m’kati mwa mitima ya anthu ndiye

mumatuluka maganizo oipa za chiwerewere, zakuba, zakuphana, zigololo, masiriro, kaduka, kunyonza, kudzikuza ndiponso kupusa. Ndina kumbukira kuti m’tima wanga ndiwodzadza ndi uchimo.

Monga momwe analemberanso m’buku la (Aroma 6:23) mphoto ya uchimo ndi imfa. Apo ndinadzindikira kuti sindingaime pamaso pa Mulungu ndi machimo anga onse awa, ndipo m’tima wanga unali wolema ndikukhumudwa.

Koma tsiku lina, Mulungu anandiunikira. Anali Mau odziœika, koma tanthauzo lake loona linandipanga kwa nthaœi yoyamba kuti ndikhulupilire (Yohane 1:29) Suuyu Mwana Wankhosa wa Mulungu uja, wochotsa machimo a pa dziko lonse lapansi atanthauza machimo onse, ndi anga omwe. Sanachotse machimo adzulo okha ndi alero ayi koma ndi machimo amaœa omwe. Yesu anachotsa machimo onse adziko lapansi pamene anabatizidwa.

(Mateo 3:15) koma Yesu adamuyankha kuti,

Page 290: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

290 Maumboni achipulumutso

◄ Zam'kati ►

“Tsopano lino vomera, chifukwa ndi m’mene tiyenera kuchitira zonse zimene Mulungu akufuna.” Apo Yohane adavomera.

Apo ndinakhulupilira kuti machimo anga onse anaperekedwa pa Yesu pamene anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi ndipo machimo anga onse analipidwa pamene Iye anamwalira pa mtanda.

(Levitiko 17:11) Pakuti moyo wake wa cholengedwa chilichonse uli m’magazi, ndipo ndaœapereka kwa inu kuti muzichitire mwambo wopepesera machimo amoyo wanu pa guwa. Pajatu magazi ndiwo amene amachotsa machimo, chifukwa cha moyo umene umakhala m’magazimo. Yesu sanamwalire kokha koma anati, “Kwatha!” Yohane 19:30. Ndipo anamubaya m’nthiti ndipo magazi ndi madzi anatuluka (Yohane 19:34), kubweretsa pansi chipupa chimene chinali kulekanitsa Mulungu ndi anthu. Tsono ndikhoza kuima pa maso pa Mulungu. Masiku amene ndinali wosakhulupilira anatayika chabe.

Tsopano nzoona ndaomboledwa. Sindilitso pansi pa zinthu za dziko koma munthu womasuka ndi wokondwa ndiponso wolungama. Ndikuthokoza Mulungu chifukwa tsono ndikhoza kutsatira munthu wolungama Abrahamu amene ali m’njira yopita ku Bethel.

Ndikuthokoza Mulungu kuti tsopano ndikhoza kulandira mana masiku onse ndikukhala mpampando wa kumwamba. Ameni.

Page 291: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

291 Maumboni achipulumutso

◄ Zam'kati ►

Mlongo Jung-soon Lee Ndinali kulota, ndikuganiza chifukwa chimene

ndinalengedwera. “Kodi ndine ndani? Chifukwa nchiyani ndinabadwa ndipo ndikupita kuti? Kodi kutha kwamoyo wanga ndi manda chabe? Ngati ndi m’mene ziriri ndiye kuti moyo wanga ulibe ntchito, ndipo zinali bwino kuti sindikanabadwa.” M’mene ndinali kukula, mu m’tima wanga munalibe ndipo ndinali ndi chisoni chosatha mu m’tima wanga. Pamene ndinakwatiriwa, ndinali kuona ngati ndalowa mumavuto aakulu kuti ndidzindikira zonse kwa mwamuna wanga ndi kuti ndikhale mai. Ndinali ndi mantha pamene ndinali kuganiza za moyo wanga wam’tsogolo.

Ndinali ndi mavuto ambiri kuchokera kwa mwamuna wake ndi mai ake. Kaœiriwiri mavuto amenewo anali aakulu kuti ndithane nawo. Ndipo ndinali kuona kuti sakundikonda. Ndinali kufuna kumwalira nthaœi zambiri motero kuti ndinali kuwonderawondera. Ndinali kufuna kupeza

mpumulo. Ndipo ndinapita ku mpingo wa Katolika. Pamene ndinakhala kumeneko, ndinali kupeza mtendere. Ndinaitana Mulungu ndikupembeza kwambiri.

Koma pamene panapita zaka zitatu, ndinaona kuti panalibe chimene chinali kuchitika. Kunja ndinali wokhulupilika ndi wodzipereka koma ndinali ndichisoni m’kati mwanga. Chikhulupiliro chinali chinthu china chimene ndinali kuvala ngati choonjezera chabe, koma m’kati ndinali kugwa kwambiri mu uchimo. Ndnali ku dzindikira kuti Mulungu anali kuyang’ana m’kati mwanga ndipo ndinali kungopembeza chabe kuti Iye asanditaye ine.

Ndinayamba kuœerenga Baibulo ndipo ndinadzindikira kuti mpingo wa Katolika siunali kuphunzitsa Mau a Mulungu monga m’mene analemberamu Baibulo. Ndinasiya tchalichi ndi anthu ena ambiri. Tinali kukumana pamodzi tsiku lililonse ndi kupembeza ndikumvera mau. Pamene ndiœerenga ndipamene ndidzindikira kuti ndi

Page 292: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

292 Maumboni achipulumutso

◄ Zam'kati ►

wochimwa kwambiri pa maso pa Mulungu. Ndinachimwa masiku onse ndipo maganizo anga ndi wodzadza ndi uchimo.

Baibulo limatiuza kuti Yesu anafa pa mtanda chifukwa cha machimo athu, komabe ndinali kuvutika ndi machimo anga. Ndipo pamene ndinali kupembeza ndinali kulapa machimo anga. Kupotsera theka la mapemphero anga ndinali kuvomera machimo anga, kufuna chikhululukiro chake. Ndinali kupempha kwa Mulungu m’mawa ali onse kuti ndisachimwetso tsikulo.

Kodi muli zinthu zingati m’Baibulo zimene Mulungu akutiuza kuti tisachite? Pamene ndikuyetsa kukhala motsatira Mau ake, ndi pamene ndikuona kuti ndimachimwabe. Ndinali kunena ndekha kaœiriœiri kuti ndingathe kuchita bwino ngati ndiyetsabe. Ngati sindinapite ku tchalichi, ndinali kudankhaœa kwambiri chifukwa cha machimo ndipo ndinali kufooka.

Pali muyambi wa a Korean umene ukuti, “Pamene mbewa ikuthamangitsidwa ndi mphaka

kumalo amene kulibe kothaœira, imabwerera ndi kumenyana ndi mphaka.” Ndinayetsa kwambiri kuti ndilandire madalitso a Mulungu koma madalitso sanabwere. Mosiyana, ndinali ndimantha ndikunditaya kwa Mulungu. Ndinayamba kudandaula kwa Mulungu. Ndinadandaula kuti Iye akufuna kuti ndichite zinthu zambiri ndipo ndinakwiya ndi Iye chifukwa chovutika ndi Iye. Ndinali kuchita zimene sindinali kuyenera kuchita.

Pamene Yesu atauka kwa akufa, anaœauza ophunzira ake katatu kuti “Mtendere ukhale nanu.” Ndinali kudikira Iye kuti anenetso kwa ine chimodzimodzi. Koma panalibe mtendere pa ine. Yesu anafa pa mtanda chifukwa cha ine ndipo anauka kwa akufa. Iye anati amene aitana dzina lake adzapulumutsidwa. Ndinakhulupilira mwa Iye ndikuitana dzina lake, nanga chifukwa nchiyani panalibe mtendere pa ine? Ndinali kudziœa kuti Baibulo linali loona ndikukhulupilira, nanga chifukwa nchiyani sandipatsa mtendere ine?

Page 293: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

293 Maumboni achipulumutso

◄ Zam'kati ►

Ndinapembeza masiku onse kuti asalole kuti nigwe mu uchimo ndipo ndinali kuganiza kuti adzamva mapemphero anga. Koma sanali kundiyankha. Ndinakhulupilira Mulungu chifukwa ndimaganiza kuti ndi wamphamvu amene angathe kundisintha ine kuti ndisachimwetso. Ngati sachita izi, nanga ndikhala bwanji? Ndinadzindikira kuti ndinali ofooka kwambiri ndipo moyo wanga uli mumanja mwake. Ngati sandipulumutsa ine kumachimo anga, kodi ndidzachita chiyani?

Mulungu anandichitira chifundo ndipo anatumiza kapolo wake, m’busa Paulo Jong, ku tchalichi langa “Paja ifenso tidaumva Uthenga Wabwino, monga iwo aja. Koma iwowo sadapindule nawo mau olalikidwawo, popeza kuti adangoœamva, koma osaœakhulupilira” (Aheberi 4:2).

Ndinayamba kuœerenga Mau a Mulungu. Ndinali kuœerenga za nsembe yochotsera machimo m’buku la Levitiko, ndinayamba kudzindikira kuti Yesu anali nsembe motsatira

malamulo ndipo kuti anachotsa machimo anga onse ndi ubatizo wake. Mpaka nthaœi iyi ndinali kudziœa za mwazi wa Yesu wokha ndipo sizinali kuthetsa vutola machimo.

Pamene Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi, Iye anati, “Tsopano lino vomera, chifukwa ndi m’mene tiyenera kuchitira zonse zimene Mulungu akufuna.” Apo Yohane adavomera (Mateo 3:15). Ndipo Yohane Mbatizi m’maœa mwake anati, “Suuyu Mwana Wankhosa ochotsa machimo aanthu onse dziko lapansi!”

Pamene ndiyamba kukhulupilira kuti anachotsa machimo anga onse, ngakhale machimo am’tsogolo, ndi kuti anaweruzidwa chifukwa cha ine ndikuuka kwa akufa ndi kuti machimo anga onse anachotsedwa, ndinayamba kupeza mtendere umene ndinali kuufuna. Machimo anga anachoka. Tsopano ndine wolungama machimo onse amene ndinali kuyenera kulapa anachoka.

Tsopano ndidzindikira chifukwa chimene ndinaliri mudziko lino. Ndinabadwanso kachiœiri

Page 294: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

294 Maumboni achipulumutso

◄ Zam'kati ►

ndipo ndi wolungama ndi khala ndi Mulungu kwa muyaya. Iye analola kuti ndibadwenso kachiœiri kuti ndifalitse Uthenga Wabwino. Sindili ndi mantha ni uchimo pakati pano. Mulungu amene analenga dziko lino anatenga moyo wanga mu manja ake ndipo akunditeteza. Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene anapulumutsa ine ku uchimo.

M’bale Gae-jin Umm “Mudzadziœa zoona zenizeni, ndipo zoonazo

zidzakusandutsani a Mulungu” (Yohane 8:32). Ndikuthokoza Mulungu amene anaonetsa

‘kuunika kwa zoona’ pa ine, amene anasowa mu m’dima. Pamene ndinafika kumapeto azaka ziœiri ku sukulu ya sekondale, ndinagogoda pa chitseko cha nyumba ya Mulungu (tchalichi) nkufunafuna Mulungu. Patapita zaka zisanu ndi zitatu, ndinagwira ntchito mokhulupirika mu bungwe la achinyamata ndi atsikana ndiponso ndi kugwira ntchito zina za tchalichi. Ngakhale ndinali kudziœa kuti ndingapulumutsidwe ‘chifukwa chosunga mau ake,’ komabe ndi kalimbika kuonetsa ntchito zanga, zimene zinali kuyetsedwa ndi ine ndemwe.

Pamene ndinali kuona kuti ndachita chintu cholungama, kapena pamene ndikumva kuti ndachita bwino kwambiri, ndinali ku lakwitsa kuti ndinapulumutsidwa. Anthu ondidzungulira nthaœi

Page 295: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

295 Maumboni achipulumutso

◄ Zam'kati ►

zambiri anali kundilemekeza chifukwa cha ntchito zabwino ndipo anali kundilimbikitsa chifukwa cha chikhulupiliro cholimba.

Chikhulupiliro chiyenera kuima pa mau ake. Koma ndinali kulemekezedwa chifukwa cha ntchito zanga ndipo zinali zosamveka. Chifukwa ndinali kudziœa bwino ndekha koposa wina aliyense za kunyenga kumene ndinali nako, ndinali kudabwa ngati anali kundidziœa bwino, ndipo m’tima wanga unali kudzadza ndi chisoni. Ndinayetsa njira zambiri kuti ndithetse ludzu langa la mwa Mulungu, koma chifukwa ndinalibe madziko olimba a Mau ake, ‘chikhulupiliro’ chinali ngati sichingachitike pa kumva kwanga.

Patapita nthaœi, m’mene ndinali kukonda zinthu zosangalasa, ndiloœa mu maphunziro aza Mulungu. Monga momwe ndinali kukonda ntchito zabwino panthaœiyo, onse amene anali kunena zoti kondani, kondani, kondani abale anu anali kuoneka ngati ndi onyenga kwa ine. Ndinali kudana ndi amene anali kunena zachikondi koma

anali kulephera kuthandiza osauka. Koma pamene ndinaomboledwa, ndinadzindikira kuti palibe china chopambana ndi mzimu wopulumutsidwa.

Ndinali kufuna kuphunzira zinthu zambiri nthaœi imene ndinali pa maphunziro aubusa, zambiri koposa zina zonse, ndinali kufuna kudzindikira tanthauzo lenileni la chikhulupiliro, chimene sichikuoneka ndiponso ngati chosamveka bwino. Ndinali kulira ndi kulapa m’mapemphero anga, ndinali kuœerenga Baibulo ndi mabuku ena olembedwa ndi anthu otchuka a Mau a Mulungu, koma zonsezi sizinali ku thandiza. Ndinakumbukira kuti abusa ambiri anali kugwiritsa ntchito mabuku othandidzira polalika koma sizinali kukometsera pa Mau ake. Ndipo ndinali wokhumudwa kwambiri, komabe chilakolako chofuna kudziœa zoona chinalikukulira kulira.

Pa nthaœiyo, ndinakumana ndikapolo wa Mulungu mu kalasi ndinamva za nsembe yochotsera machimo monga m’mene

Page 296: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

296 Maumboni achipulumutso

◄ Zam'kati ►

anafotokozera m’buku la Levitiko M’chipangano Chakale. Ndisanaomboledwe, linalikuoneka kutopetsa ndi lovuta kuœerenga Mau ake osatha obwereza bwereza onena zakupha nyama. Sindinali kudziœa kuti tanthauzo lobisika lili mu Mau amene adzatenga malo ansembe yochotsera machimo imene inafotokozedwa m’Chipangano Chakale ndi kuchotsa machimo anga onse ndi kundiyeretsa ngati matalala. Mateo 3:15 akuti, “Tsopano lino vomera, chifukwa ndi m’mene tiyenera kuchitira zonse zimene Mulungu akufuna.” Apo Yohane adavomera. Pamene Yesu anatenga thupi la munthu anali wopanda chilema, Yesu Khristu anabwera pa dziko lapansi monga ngati nsembe yamoyo ndipo anabatizidwa machimo anga onse anadza pa Iye. Mwataya machimo anga onse kumbuyo kwanu (Yesaya 38:17).

Anachotsa machimo onse adziko lapansi (Yohane 1:29) ndi kufa pa mtanda kuti aœeruzidwe chifukwa cha ife ndi anatipulumutsa

ku malamulo amachimo ndi imfa. Chifukwa machimo anga onse anapatsidwa pa Iye kupsolera mu ubatizo wake, ndi kumvetsa ndi maganizo anga onse chimene mtumwi Paulo anali kutanthauza pamene ankati, “Ndipachikidwa pamodzi ndi Khristu, sindine amene ndikhala moyo, koma Khristu amakhala mwa ine.” Ndinali kuona mtsinje wa madzi amoyo akuyenda mu m’tima wanga wouma. Nzoona Mau ake ali ndi moyo ndipo ndi amphamvu. Maganizo onse osaoneka ndi opanda ntchito amene ndinali nawo ‘achikhulupiliro’ anali oona.

Pamene ndimayang’ana kumbuyo kwa moyo wanga, panali nthaœi ya zoœaœa ndi nthaœi ya mtendere. Koma ndimathokoza Iye chifukwa cha izi. Tsono ndi kudziœa kuti Yesu ndi amene ananditsogolera ku malo amene ndili tsono. Ngakhale sindingathe kulongosola ndi mau aza chisomo ndi chikondi cha Mulungu, ndidzakhala moyo wanga wonse ngati kapolo wake ndi kudikira kuti ndidzakhala wothandiza kwa Iye.

Page 297: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

297 Maumboni achipulumutso

◄ Zam'kati ►

Ndikufuna kutsogolera amene akuyendayenda mu m’dima ku kuunika koona. Ndikuthokoza ndi kubwerera ku ulemerero wa Mulungu amene anandipulumutsa ku malamulo a uchimo ndi imfa ndi kundipatsa moyo wosatha. Aleluya!

Mlongo Belova Lyssa Moscow Ndifuna kunena kuti ndi akatswiri onse abusa aku

Korea mu dzina la Yesu ndi kugaœana ndi inu chisangalalo chimene chinachitika ndi kusintha moyo wanga kwathunthu.

Pa maphunziro amene anachitika ku Moscow zaka zopitazo, ndi namva Mau abwino a Mulungu. Pamene ndinachita nawo maphunziro am’sonkhano wa Mulungu ku Korea chaka china, ndinamva ziphunzitso zambiri za Mau a Mulungu za kubadwanso kachiœiri ndi madzi aubatizo ndi Mzimu Woyera. Nzoona ndi chosangalasa kuti ndione bwino bwino kuti ndili womasauka ku machimo anga onse!

Papita zaka zisanu ndi chimodzi kuchokera pamene ndinayamba kukhulupilira Yesu. Ndikofunika kuti “Nzoona ndibadwe kachiœiri,” ndinaphunzitsidwa kuti ndine wochimwitsitsa kwambiri ndipo ndiyenera kulapa kaœiri kaœiri. Ndinali kupemphera ndi kulapa masiku onse

Page 298: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

298 Maumboni achipulumutso

◄ Zam'kati ►

mobwereza bwereza. Ndinabatizidwa ndi madzi aubatizo komabe sindinali wobadwanso kachiœiri.

Ndinalikukhulupilira kuti ndinali wochimwa ndipo kuti ndinali ndi uchimo wambiri mu m’tima wanga. Ndinali kuyenera kupempha chikhululukiro nthaœi yonse. Nthaœi yonse ndinali kuvutika ndi machimo anga. Komabe nzoona ndimakhulupilira kuti Mulungu sankana nditaya mu chisoni changa koma akanandipulumutsa ine pa mapeto.

Mulungu anaditsogolera kwa kapolo ake amene analiwobadwanso kachiœiri. Kupsolera mwa iye ndinali kumva Uthenga Wabwino wofunika kwambiri mu dziko lino lapansi, Uthenga woona wa chipulumutso.

Ndinaphunzira kuti ndilibe uchimo ndi kuti Yesu anachotsa machimo anga onse kupsolera mu ubatizo wake ndi imfa ya pa mtanda.

Tsono sindinenso wochimwa ai, ndipo m’tima wanga wadzadza ndi chimwemwe. Tsono, kuti ndipereke mapemphero akulapa, ndimapereka

mapemphero amphamvu othokoza Mulungu masiku onse, ndipo moyo wanga uli pa mtendere ndi chimwemwe. Ndidziœa tsono kuti kulibe Uthenga wina, kulibe chikhulupiliro china choona ngati ichi. Ndikupemphera kuti chikhulupiliro changa chikhala cholimba. Ndikupereka mapemphero anga kwa Mulungu masiku onse ndipo ndimakhulupilira kuti palibe chikhulupiliro choposa ichi.

Ndili pa mtendere chifukwa chodziœa kuti ndidzalowa mu ufumu wa kumwamba pamene moyo wanga wapansi pano udzatha. Tsono ndigwire ntchito ya Mulungu ndipo ndimalalika Uthenga Wabwino kwa anthu ondidzungulira. Ndimakhala ndi chimwemwe chosatha, ndikugaœana chikondi cha Mulungu ndi anthu onse adziko lapansi.

Page 299: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

◄ Zam'kati ►

MAU ACHIŒIRI OONJEZERA

Kulongosola

kowonjezerapo

Page 300: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

300 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

Kulongosola kowonjezerapo

MALIPIRO Malipiro amene amapereka poombola munthu

amene wabadwa, kupereka katundu chifukwa chofuna kufafaniza ngongole, njira yothetsera mavuto ndi ndalama. Anali kugwiritsa kaœirikaœiri pofuna kuombola (Eksodo 21:30, ngati ndalama; Numeri 35:31-32; Yesaya 43:3; ‘malipiro’).

M’chipangano Chatsopano, Mateo 20:28 ndi Marko 10:45 akufotokozera zamalipiro ngati malipiro a ndalama.

KUGWIRIZANA, KUGWIRIZANA KWA MULUNGU NDI ANTHU Mwambo wopereka machimo onse aanthu pa

Yesu. M’chipangano Chakale nsembe yochotsera machimo kunali kupereka machimo pa nsembe kupsolera mukusanjika manja pa mutu wansembe. M’chipangano Chatsopano, zitanthauza ubatizo wa Yesu ndi Yohane Mbatizi. Mu Chiheberi ndi Chigiriki, Mau awa atanthauza kupereka machimo pa Yesu Khristu kuti wochimwa mwina angathe kukhala pa chibale ndi Mulungu.

M’chipangano Chatsopano akupereka chitsadzo cha nsembe yochotsera machimo: ubatizo wa Yesu ndi imfa yake pa mtanda.

M’CHIPANGANO CHAKALE: Mau ansembe yochotsera machimo agwiritsidwa ntchito makumi khumi (100) M’chipangano Chakale ndi nthaœi zambiri amatanthauziridwa monga ngati (Levitiko 23:27; 25:9; Numeri 5:8) ‘Kapha’ mu Chigiriki (kaœiri kaœiri amalembedwa ngati

Page 301: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

301 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

‘kupanga nsembe yochotsera machimo’). Nsembe ndi Mau ochokera ku Chiheberi amene atanthauza kupereka machimo posanjika manja pa mutu wa mbuzi ya moyo ndi kuvomera machimo onse ndi zolakwa za ana Aisraele (Levitiko 16:20).

M’CHIPANGANO CHATSOPANO: Nsembe

ndi chimodzimodzi mu Aramaic ‘Kpr’ ndikokuti kutseka. Ichi chitanthauza kuti ubatizo wa chiombolo wa Yesu M’chipangano Chatsopano. Yesu anadza pa dziko lapansi ndi kubatizidwa pamene anali ndi zaka makumi atatu (30) kuti akwaniritse chipulumutso cha anthu. NSEMBE YA M’BAIBULO

A. M’chipangano Chakale, nsembe inali

kuperekedwa kupsolera mu nsembe ya nyama Eksodo 30:10; Levitiko 1:3-5; 4:20-21; 16:6-22.

B. M’chipangano Chatsopano, maganizo ansembe yochotsera machimo a Chipangano Chakale analipo, koma kuomboledwa kwa munthu kukuchokera kwa Yesu Khristu. Monga momwe mtumwi Paulo ananenera kuti Yesu Khristu anafa chifukwa cha machimo athu (1 Akorinto 15:3).

Au oti nsembe sanagwiritsidwe ntchito kutsatira imfa ya Khristu kuchotsa machimo obadwanawo okha, koma kuchotsa machimo onse aanthu. Ndipo pamene anabatizidwa kupsolera mukuchotsedwa kwa machimo athu ndikuperekedwa pa Yesu (Mateo 3:15), Iye anapulumutsa anthu onse kupsolera mukukhetsa mwazi wake pa mtanda (Levitiko 1:1-5; Yohane 19:30).

Mtumwi Paulo analongosola m’buku la 2 Akorinto 5:14 kuti, Munthu m’modzi adafera anthu onse; ndipo pa ndime yoyamba akuti, chifukwa cha ife; mu Agalatia 3:13, akuti, ‘pakusanduka wotembereredwa m’malo mwathu.’ Pa ndime zambiri M’chipangano Chatsopano zimene zikusonyeza kwa Yesu monga nsembe

Page 302: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

302 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

(Aefeso 5:2), zina ndi Yohane 1:29,36 (Mwana Wankhosa’ – Yohane Mbatizi) ndi 1 Akorinto 5:7 (‘mphwando lathu’ – mtumwi Paulo akutero).

Koma Paulo anatsimikiza kuti ubatizo wa Yesu mu mtsinje wa Yolodane unali wochotsa machimo onse adziko lapansi. Analongosola m’buku la Aroma 6 kuti machimo onse aanthu anaperekedwa pa Yesu kupsolera mu ubatizo wa Yesu ndi Yohane Mbatizi.

Anapitiriza ndi kulongosola kuti kupachikidwa kwa Yesu pa mtanda unali weruzo ndi malipiro a machimo, kuti nsembe yochotsera machimo inaperekedwa chifukwa cha mizimu ya anthu onse.

Imfa ya Yesu ikusonyeza kwa ife nsembe yochotsera machimo M’chipangano Chakale, kusanjika manja M’chipangano Chakale ndi ubatizo wa Yesu M’chipangano Chatsopano zili m’njira ya malamulo a Mulungu (Yesaya 53:10; Mateo 3:13-17; Aheberi 7:1-10, 18; 1 Petro 3:21).

Chipangano Chatsopano sichimathera ndi

ubatizo ndi imfa ya Yesu koma kupita ndikunena kwa ife za kukwaniritsidwa kwa chipulumutso ndi m’mene tinabatizidwa mwa Yesu ndikufa naye pamodzi (Aroma 6:3-7, Agalatia 2:19-20).

Umatiuza ife kuti Yesu Khristu, kupsolera mu ubatizo wake ndi mwazi osati kuti anachotsa machimo athu ndi kumva zowawa, komanso anapulumutsa anthu ku mphamvu ya Satana ndi kutibwezeranso ku mphamvu ya Mulungu kupsolera mukulandira chilango mumala mwathu.

Choncho choombolo cha Yesu chinathetsa vuto la machimo limene linali kutipatula ndi Mulungu, kotero mtendere unabwera ndi ubale pakati pa anthu ndi Mulungu, kubweretsa chipulumutso, chimwemwe (Aroma 5:11), umoyo (Aroma 5:17-18), ndi chiombolo Mateo 3:15; Yohane 1:19; Aheberi 10:1-20; Aefeso 1:7; Akolose 1:14 panthaœi imodzi.

Page 303: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

303 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

TSIKU LANSEMBE YOCHOTSERA MACHIMO Mu Chiheberi, chitanthauza tsiku ‘lotseka.’

Kapena ‘kuyanjana.’ Tsiku lolemekezeka kwa Ayuda linali tsiku lansembe yochotsera machimo pa tsiku khumi la mwezi wa chisanu ndi kaœiri Levitiko 23:27; 25:9). Tikhoza kuona m’buku la Levitiko 16 kuti ngakhale wansembe wam’kulu sankalowa m’malo oyera akachisi kupatula pa mwambo wopatulika.

Malo Oyera iwo okha anali kufuna nsembe yochotsera machimo ndiponso anthu afuko la Aisraele anali kuganizira za kuyera kwa Mulungu ndi machimo awo patsiku lopereka nsembe yochotsa machimo.

Ndipo nsembe zokwanira mwina khumi ndi zisanu kuphatikiza mbuzi zochotsera machimo), nsembe zootcha khumi ndi ziœiri ndi nsembe zochotsera machimo zinali kuperekedwa pa maso pa Mulungu (Levitiko 16:5-29; Numeri 29:7-11).

Ngati tingaœerenge ana a nkhosa ‘ena’ amene anatchulidwa m’buku la Numeri 28:8, panali nsembe zootcha khumi ndi zitatu ndiponso nsembe zochotsera machimo zinai.

Tsiku limene Aisraele anali kupereka nsembe ya machimo achaka chonse linali tsiku la khumi la mwezi wa kasanu ndi kaœiri. Kupsolera mu njjira yomweyo tsiku la dziko lonse la nsembe yochotsera machimo linalitsiku limene Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Linali tsiku la nsembe yochotsera machimo (Mateo 3:13-17). Linali tsiku limene Yesu anachotsa machimo onse adziko lapansi (Mateo 3:13-17). Linali tsiku la nsembe yochotsera machimo pamene Mulungu “Chifukwa cha ife anakwaniritsa chilungamo chonse.”

Page 304: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

304 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

NSEMBE YOCHOTSERA MACHIMO M’CHIPANGANO CHAKALE: Monga ngati

nsembe zina, nsembe za chiyero zinali kuperekedwa mu Chihema. Wansembe wam’kulu amadziyeretsa ndi kuvala zovala za ntchito yake mumalo movala za masiku onse, ndi kusankha ng’ombe yamphongo kuti yikhale nsembe ndi nsembe yootcha ya Mwana Wankhosa ya iye yekha ndi banja lake (Levitiko 16:3-4). M’kulu wansembe anali kusanjika manja ake pa mutu wansembe kuti apereke machimo pa nsembeyo.

Kusanjika manja chinali chinthu chofunika pa tsiku lopereka nsembe yochotsa machimo. Ngati sizinachitike m’njira imeneyi, kupereka nsembe sikunakachitika chifukwa kuchotsa machimo sikunakwanira popanda kusanjika manja, motero nkupereka machimo a chaka chonse a Aisraele pa nsembeyo.

M’buku la Levitiko 16:21 akuti, “Tsono Aroni

asanjike manja ake pa mutu pa mbuziyo, ndipo aululire pa mbuzi imeneyo zochimwa zonse za Aisraele pamodzi ndi kusamvera kwao konse, ndiye kuti machimo awo onse. Machimowo aœaike pa mutu pa mbuzi ija, ndipo munthu amene adamusankhiratu aithamangitsire ku Chipululu mbuziyo.”

Anatenga mbuzi ziœiri za nsembe ya machimo ndi mwana wakhosa ngati nsembe yootcha kuchoka kwa anthu (Levitiko 16:5). Ndipo amapereka mbuzi ziœiri pa maso pa Ambuye pa khomo la chihema ndipo anachita maere kuti asankhe imodzi ikhale ya “Ambuye” ndipo ina imagwira ntchito “yochotsa machimo.”

Mbuzi ina ya Ambuye inaperekedwa ngati nsembe yochotsera machimo, ndipo mbuzi ya Ambuye kuti ichotse machimo achaka chonse a Aisraele ndipo amaipitikisa m’chipululu (Levitiko 16:7-10).

Machimo a Aisraele anali kuyenera kuperekedwa pa mbuzi yochotsa machimo

Page 305: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

305 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

kupsolera mukusanjika manja. Apo mbuzi ija yochotsa machimo onse a Aisraele inaperekedwa ku chipululu kuti pakhale mtendere pakati pa anthu ndi Mulungu. Choncho machimo achaka chonse a Aisraele anachotsedwa.

M’CHIPANGANO CHATSOPANO: Munjira

yomweyo M’chipangano Chatsopano, Yesu Khristu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi (kusanjika manja M’chipangano Chakale) ndi kuchotsa machimo onse aanthu monga ngati nsembe ya mwana wankhosa kukwaniritsa chipulumutso cha Mulungu (Levitiko 20:22; Mateo 3:15, Yohane 1:29, 36).

M’chipangano Chakale, asanachite maere, Aroni anapha ng’ombe yaying’ono ya mphongo ngati nsembe yochotsera machimo ya iye ndi nyumba yake (Levitiko 16:11). Ndipo anatenga moto wa makala kuchoka pa guwa nabwera pamaso pa Ambuye m’manja atanyamula lubani ndipo anapitirira nsalu imene inali kuguœa Malo

Oyera. Anaika lubani pamoto pamaso pa Ambuye kuti usi wa lubani ukhudze mpando wachifundo. Anatenganso magazi ena a ng’ombe ya mphongo nawadza ndi dzanja lake kasanu ndi kaœiri pampando wachifundo (Levitiko 16:12-19).

Patsiku lochotsera machimo, kusanjika manja kwa Aroni pa mutu wansembe sikunasiyidwa. Aroni anasanjika manja pa mutu wa mbuzi ndi kupereka machimo onse ndi zolakwa zonse za Aisraele pa mutu wake. Apo munthu amene anam’sankhiratu anatenga mbuziyo nayitsogolera m’chipululu kuti ikafere komweko. Mbuzi yonyamula machimo a Aisraele ndipo pambuyo pake imafa ndi machimowo. Iyi inali njira yoperekera nsembe M’chipangano Chakale.

Ndi chimodzimodzi M’chipangapo Chatsopano chosiyana ndi choti Yesu Khristu, anali ngati mbuzi yochotsera machimo, amene anathenga machimo onse aanthu pa Iye yekha kupsolera mu ubatizo wake ndi kukhetsa mwazi ndi kufa pa mtanda chifukwa cha ife.

Page 306: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

306 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

Choncho tsono, chikulukiliro cha machimo onse sichingakhalepo popanda ubatizo ndikupachikidwa kwa wansembe wam’kulu wa kumwamba, Yesu Khristu. Uku ndikukwaniritsa chipulumutso cha kubadwanso kachiœiri ndi madzi ndi Mzimu Woyera.

KUSANJIKA MANJA, NDI KUDZODZA Iyi ndi njira imene amaperekera machimo pa

mutu wansembe yochotsera machimo M’chipangano Chakale (Levitiko 4:29; 16:21). Mumasiku a Chipangano Chakale, Mulungu analamula anthu kuti apereke nsembe chifukwa cha machimo awo kupsolera mu kusanjika manja pa mutu wansembe yochotsera machimo mukati mu chihema. Ndipo chimaonetsa ubatizo wa Yesu umene unaoneka M’chipangano Chatsopano.

UBATIZO Ubatizo umatanthauza (1) kutsukidwa (2)

kuikidwa (kumidzidwa) ndipo mu Uzimu atanthauza, (3) kupereka machimo kupsolera mukusanjika manja, monga m’mene anachitira M’chipangano Chakale.

M’chipangano Chatsopano, kubatizidwa kwa Yesu ndi Yohane Mbatizi kunali kuchotsa machimo aanthu onse. Ubatizo wa Yesu uli ndi tanthauzo lochotsa machimo lapansi.

Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi, woimirira anthu onse ndi wansembe wam’kulu wa mwambo wa Aroni, ndipo anatenga machimo onse aanthu pa Iye yekha. Ichi ndicho chinali chifukwa cha ubatizo wake.

Mu Mau ‘ubatizo wa Yesu’ ndi tanthauzo la uzimu lakupereka, ndikuikidwa mumanda! Izi zitanthauza kuti machimo onse anaperekedwa pa Yesu ndiponso kuti anaweruzidwa mumalo mwathu. Kuti apulumutse anthu onse, Yesu

Page 307: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

307 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

analikuyenera kuchotsa machimo aanthu ndi kuœafera.

Choncho imfa yake ndi imfanso yanu ndi ine, ndi onse ochimwa adziko lapansi, ndipo kuuka kwake ndi kuuka kwa anthu onse. Nsembe yake ndi chipulumutso cha ochimwa, ndipo ubatizo wake ndi umboni wochotsera machimo aanthu onse.

Baibulo limatiuza kuti, “Madziwo akufanizira ubatizo umene masiku ano umakupulumutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Khristu”(1 Petro 3:21). Ubatizo wa Yesu ndi njira ya chilungamo imene munthu amapulumukira ku machimo ake onse.

TCHIMO Zinthu zonse zotsutsana ndi Mulungu,

kuphatikiza machimo obadwanawo ndi zolakwa zina zimene timachita ife pa moyo wathu.

Tchimo mu Chigiriki ndi ‘Lamartia.’ Ndipo ‘kuchimwa’ ndi ‘hamatano’ chimene chikutanthauza kusiya njira, ‘m’njira mau ena, ndi mphamvu yopulumukira. Kusadziœa kapena kusakhulupilira mu choona ndi kuphwanya malamulo ndi kunyoza Mulungu.

Ngati munthu sakufuna kuchimwa pa maso pa Mulungu, ayenera kumvetsa Mau a Mulungu ndi kudzindikira choona choti Yesu anakhala Mpulumutsi wake.

Tiyenera kukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mtanda wake kupsolera mu Mau a Mulungu. Ndi tchimo kusalandira Mau a Mulungu ndi kuchoka mu choona ndikukhulupilira zinthu zonama.

Baibulo silimatiuza kuti tchimo loipa kwambiri ndi kusakhulupilira kuti Mulungu anachotsa machimo onse adziko lapansi. Tiyenera kukhulupilira mukubadwa kwa Yesu, mukuchotsa kwake kwa machimo kupsolera mu ubatizo wake, ndi kutipatsa umoyo ndi mwazi wake umene unakhetsedwa pa mtanda. Ndi tchimo ngati

Page 308: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

308 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

munthu sakhulupilira mu Mau olembedwa amene akuti Yesu anabatidzidwa, ndiponso anamwalira pa mtanda ndikuuka kwa akufa kuti atimasule ife ku machimo athu.

KULAPA Pamene munthu amene achoka pamaso pa

Mulungu akumbukira machimo ake ndi kuyamika Yesu chifukwa anachotsa machimo ndikubweranso kwa Mulungu, ndiye kuti alapa.

Anthu onse ndi odzadza ndi uchimo. Kulapa kulandira Yesu pokhulupilira kuti anabwera pa dziko lapansi kuti apulumutse ochimwa, kuti anachotsa machimo onse (kupsolera mu ubatizo wake) ndipo anafa ndi kuuka kwa akufa kuti atipulumutse. Kulapa kwenikweni ndikupereka maganizo athu ndi kubwerera kwa Mulungu (Ntchito 2:38).

Kulapa ndikuvomera machimo athu ndi

kubwerera ku Mau a Mulungu, kulandira chipulumutso cha madzi aubatizo ndi mwazi ndi m’tima wathu wonse (1 Yohane 5:6).

Kulapa kwenikweni ndi kuvomera munthu pa yekha kuti ndine wochimwa ndi kukhulupilira mwa Yesu, Mwana wa Mulungu monga ngati Mpulumutsi wake amene anamupulumutsa ku machimo onse. Kuti tipulumutsidwe ndi kuchotseredwa machimo athu onse, tiyenera kusadalira pa ntchito zathu kuti tiyere ndipo tivomere kuti nzoona ndife ochimwitsitsa pamaso pa Mulungu ndi malamulo ake. Apo ndiye kuti tavomera choona, chipulumutso cha madzi aubatizo ndi Mzimu Woyera, chipulumutso chimene Yesu anatipatsa ndi ubatizo wake ndi mwazi wake.

Ochimwa ayenera kusiya maganizo ake onse ndipo angathe kubweranso kwa Yesu kwathunthu. Ndipo adzapulumutsidwa pamene adzakhulupilira kuti ubatizo wa Yesu unali kutenga machimo ake pa Iye.

Page 309: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

309 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

M’njira ina, kukhulupilira mfundo yoti ubatizo wa Yesu, kupachikidwa pa mtanda ndi kuuka kwa akufa inali njira yopulumutsira ochimwa. Yesu anabwera mwa thupi ndipo anabatizidwa ndiponso anapachikidwa pa mtanda kuti achotse machimo onse aanthu. Kukhala ndi chikhulupiliro chokwana muzonsezi ndi kukhulupilira kuti Yesu anauka kwakufa kuti akhale Mupulumutsi wa onse okhulupilira mwa Iye ndi kulapa koona ndiponso ndi chikhulupiliro chenicheni.

CHIPULUMUTSO Chipulumutso chitanthauza ‘kupulumutsidwa

kuchoka mu kumira!’ Munthu amalandira chipulumutso pamene avomera kuti sangathe kudzipulumutsa koma kupita kugehena chifukwa cha machimo ake ndikukhulupilira kuti Yesu anamupulumutsa ku machimo ake onse kupsolera mukubadwa kwake ndi ubatizo ndi mwazi wake

umene unakhetsedwa pa mtanda. Anthu amene anayeretsedwa ku machimo

chifukwa chokhulupilira mu chipulumutso cha Yesu, ndi ubatizo ndi mwazi wa Yesu amatchedwa ‘opulumutsidwa, obadwanso kachiœiri, olungama.’

Tikhoza kugwiritsa ntchito mau oti ‘chipulumutso’ kwa iwo amene anapulumutsidwa ku machimo awo onse, kuphatikizanso machimo obadwa nawo ndi machimo awo amasiku onse, chifukwa chokhulupilira mwa Yesu. Monga momwe munthu amene akumira anapulumukira, munthu amene akumira mumachimo a dziko lapansi angathe kupulumutsidwa kupsolera mukukhulupilira mwa Yesu ngati Mpulumutsi wake, kupsolera mukukhulupilira mu ubatizo wake ndi mwazi wake, kupsolera m’mau a uzimu oona.

Page 310: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

310 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

KUBADWANSO KACHIŒIRI ‘Kubadwanso kachiœiri.’ Ochimwa ndi

obadwanso kachiœiri ngati apulumutsidwa ku uzimu kupsolera mukukhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi imfa yake ya pa mtanda.

Munthu amakhala obadwanso kachiœiri ngati akhulupilira mu ubatizo ndi mwa mwazi wa Yesu. Obadwa kachiœiri ndi amene machimo awo achotsedwa ndipo akudikira kubwera kwa Yesu popanda tchimo. (Aheberi 9:28)

NSEMBE YOCHOTSERA MACHIMO Kapena chikhululukiro cha machimo, machimo

amakhululukidwa pamene timatsukidwa machimo onse kamodzi kokha kupsolera mu Uthenga Wabwino wa madzi aubatizo ndi Mzimu Woyera.

Chikhulupiliro cha madzi aubatizo ndi Mzimu Woyera ndi kukhulupilira mwa Yesu kuti ndi Mwana wa Mulungu, ndipo anadza padziko lapansi ngati munthu, ubatizo wake ndikupachikidwa kuti apulumutse anthu.

Chiombolo chimene Yesu anapereka kwa anthu chikupsolera mu chikhulupiliro cha ubatizo ndi mwazi wake (monga momwe analembera M’chipangano Chakale) kuti Yesu adzapulumutsa anthu onse kumachimo awo. Chiombolo m’Baibulo chikutsonyeza kuchotsedwa kwa machimo kupsolera mu chikhulupiliro mu ubatizo wa Yesu, kotero kuti tsopano mulibe tchimo m’mitima ya anthu.

Tsono tikhoza kunena kuti ndife oomboledwa ndi olungama ngati titapereka machimo athu onse kwa Yesu kupsolera mu ubatizo wake.

Page 311: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

311 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

KULONGOSOLA KOWONJEZERAPO YESU KHRISTU: ‘Mpulumutsi amene

anapulumutsa athu onse ku machimo awo ndi kuchilango cha uchimo.’ Yesu chitanthuza kuti Mpulumutsi , amene adzapulumutsa anthu onse kumachimo awo.

KHRISTU: ‘Wodzodzedwa’ panali zinthu zitatu

zenizeni zimene anthu anali kudzodzedwa nazo ndi Mulungu. Ndipo Yesu anakwaniritsa zonse.

1) Ngati mfumu 2) Ngati m’neneri 3) Ngati wansembe Yesu Khristu zonsezi anali nazo. Anachita

ntchito za zinthu zonsezi. Tiyenera kukhulupilira mwa Yesu ngati Mfumu, ngati M’neneri, ndiponso ngati Wansembe amene anatiphunzitsa ife za chiombolo ndi chipulumutso, motero tibwera kwa Iye ndikunena kuti, ‘Yesu Khristu.’ Iye anali

Wansembe Wam’kulu wakumwamba amene anatipulumutsa ife ku machimo onse adziko lapansi ndi ubatizo wake ndiponso ndi mwazi wake.

Choncho Iye ndi Mfumu ya onse amene amakhulupilira mwa Iye. Ndipo amatidzindikiritsa machimo athu pamene tibwerera kwa Iye. Amatiphunzitsa kuti tili wochimwa kuchokera kwa makolo athu, motero ngati m’badwo wochokera kwa wochimwa timagwanso mu uchimo ndipo pa chifukwa ichi tili oyenera kuweruzidwa ndi Mulungu.

Iye anatipulumutsanso kuti machimo athu onse anachotsedwa kupsolera mu ubatizo ndi mwazi wake. Anachita ntchito yonseyi chifukwa cha ife anthu ochimwa.

Page 312: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

312 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

KODI NCHIFUKWA CHIYANI MWANA WA MULUNGU ANAKHALA MUNTHU? Anakhala munthu kuti akhale Mpulumutsi

ndipo kuti apulumutse ochimwa onse kuchokera ku machimo, kuchiweruzo, ndiponso ndikugehena.

Kondi Yesu nindani? Monga momwe munalembedwa m’buku la

Genesisi 1:3. Iye ndi Mlengi, Mulungu woona, Mulungu wa dziko lonse amene anapulumutsa ochimwa onse ku machimo adziko lonse lapansi (Afilipi 2:6, “Iyeyu anali ndi Mulungu chikhalire.” Yohane 1:2 akuti, “Anali kwa Mulungu chikhalire. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo palibe chilichonse chimene chidalengedwa popanda Iye”). Yesu ndi

Mulungu wazolengedwa, katswiri wa dziko lonse la kumwamba.

Koma anthu ambiri analephera kupulumutsidwa kupsolera kosakhulupilira mu chikondi ndiponso mu chipulumutso chodzera mwa Yesu pamene Iye anadza pansi pano muthupi. Koma ena ambiri analandira chipulumutso anakhala anthu a Mulungu ndipo anapedza moyo wosatha chifukwa chokhulupilira mwa Iye. Ndipo anakhala olungama.

KODI MALAMULO ANAKHADZIKITSIDWA NDI MULUNGU? Mulungu ndiye amakoza zonse, Mulungu

yokhayo woona, ndi yekhayo. Choncho anakhazikitsa malamulo m’dziko.

1) Naœapatsa wochimwa malamulo ake kuti

Page 313: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

313 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

apulumutsidwe ku machimo awo (Aroma 3:20). 2) Lamulo lachiœiri anatipatsa ife lamulo la chikhulupiliro limene limapulumutsa ochimwa. Ndi lamulo limene limatipatsa chipulumutso kupsolera muchikhulupiliro mwa Yesu ngati Mpulumutsi wathu (Aroma 5:1-2). Yesu anadza padziko lapansi kuti akwaniritse malamulo amene ankhadzikitsa ndipo anabatizidwa ndi kukhetsa mwazi pa mtanda ndipo anauka kwa akufa. Yesu anakhadzikitsa malamulo achipulumutso kuti apulumutse ochimwa onse adziko lapansi. 3) Mulungu anakhadzikitsa lamulo la chikhulupiliro chifukwa cha omwe akhulupilira mu chipulumutso cha madzi aubatizo ndiponso ndi Mzimu Woyera. Aliyense amene akufuna kupulumutsidwa ndi kukhala Mwana wa Mulungu ayenera kukhulupilira mumalamulo la chikhulupiliro limene linakhadzikitsidwa ndi Mulungu. Ndi njira yokhayo ya chipulumutso. 4) Analola kumwamba okhao amene

akhulupilira mu chipulumutso chamuzimu wa choona.

LAMULO LA MULUNGU (MALAMULO KHUMI) Zinthu zofunika zimene tiyenera kusunga

pamaso pa Mulungu ndi malamulo khumi, ndipo pali ndime 613 zokhuza moyo watsiku ndi tsiku. Palinso malamulo oti, Chitani ichi ndipo osachita ichi ndipo chitani icho. Awa ndi malamulo amene tiyenera kutsatira ndipo malamulo khumi a Mulungu anaperekedwa kwa anthu kuti adzindikire machimo awo. Kudzera mukulembedwa kwa malamulo khumi a Mulungu, tikhoza kuona m’mene timamulakwira Mulungu (Aroma 3:19-20).

Chifukwa chimene Mulungu anatipatsira malamulo ake ndi choti tidzindikire machimo athu. Sitingasunge onse malamulo ake, ndipo

Page 314: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

314 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

tizichepetse ndi kuvomera kuti ndife ochimwa pamaso pa Yesu. Sitiyenera kuchimwa chifukwa cho dzikuza pa kuyetsa kukhala mosatira malamulo ake. Anthu onse ndi ochimwa ndipo Mulungu akudziœa kuti sangatsatire malamulo ake. Ndichifukwa chake anabwera padziko lino monga ngati munthu ndi kubatizidwa ndi kuweruzidwa pa mtanda.

Kumaonetsa m’mene malamulo a Mulungu alili olungama, ndiponso m’mene anthu alili ofooka. Ndiponso pa nthaœi yomweyo chiyero ndi chilungama cha Mulungu chimaoneka mumalamulo a Mulungu.

KODI TIYENERA KUKHULUPILIRA MWA YESU? Inde, tiyenera. “Ndipo palibe wina aliyense

amene angathe kupulumutsa anthu, pakuti pa dziko lonse lapansi palibe dzina lina limene

Mulungu adapatsa anthu kuti tipulumuke nalo.”(Ntchito 4:12) Chifukwa ndi Ambuye anthu, chifukwa Iye ndi wolungama, chifukwa ndi chifuniro chake, chifukwa palibe Mpulumutsi wina, chifukwa Yesu ndiye yekha Mpulumutsi wathu, chifukwa ife tingathe kuomboledwa ndi kubadwanso kaœiri ngati tingakhulupilire mwa Iye, tiyenera kukhulupilira mwa Iye.

KODI CHIFUKWA NCHIYANI TIKHULUPILIRA MWA YESU? Tiyenera kukhulupilira mwa Yesu chifukwa:

Kuti tikwaniritse chifuniro cha Mulungu Kuti tipulumutsidwe kumachimo athu Kuti tipulumutsidwe ndi kuloœa mu Ufumu

wakumwamba kuti tikhale kwamuyaya ndi Ambuye.

Page 315: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

315 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

KODI IFE OKHULUPILIRA YESU, TINGATHE KUKHALA OCHIMWABE? Ai. Mtumwi Paulo ananena kuti pokumbukira

masiku aja asakumane ndi Yesu pa 1 Timoteo 1:15, “Ndipo mwa iwowo ine ndiye ochimwa koposa.” Masiku ano kuli anthu ambiri amene amaganiza iwo ndi anthu ochimwambe ngakhale kuti amakhulupilirira Yesu. Koma izi sizoona ai. Anthu onse amakhala ochimwa asanayambe kukhulupilira Yesu Khristu. Koma pamene akhulupilira mwa Yesu monga momwe iye afunira, iwo amasanduka olungama pa nthaœi yomweyo. Mtumwi Paulo anakumbukira za m’mene Iye analili asanakumane ndi Yesu adavomera kuti iye anali wochimwa koposa.

Koma Paulo, akadali kudziœika ndi dzina lakuti Saulo adakumana ndi Yesu pa njira yopita ku Damasiko ndipo adazindikira kuti Yesu ndiye

Mpulumutsi wake ndipo anayamba kukhulupilira ndi kuthokoza Yesu. Ndipo pa moyo wake wonse anachitira umboni kuti chifuniro cha Mulungu, ubatizo wa Yesu ndi umene unachotsa machimo onse adziko lapansi, ndiponso Iye anayenera kufa kuti afafanize machimo onse adziko lapansi.

Motero tikhoza kunena iye adakhala mtumiki wa Mulungu amene ankhalalika Uthenga wa madzi ndi Mzimu Woyera. Anthu ambiri chifukwa cha kusamvetsa amanena kuti pamene Paulo ananena kuti ndi wochimwa koposa, ndiye kuti anali wochimwa ngakhale adakhulupilira Yesu.

Koma kunena zoona iye sanalinso ochimwa pamene adakhulupilira Yesu, koma anali munthu amene ankakhumana ndi Yesu nthaœi iliyonse akafuna. Iye anakhala ali kufalitsa Uthenga wachipulumutso, chiombolo cha ubatizo ndi mwazi wa Yesu Khristu. Ngakhale iye adapita kwa Mulungu, makalata ake tili nawo mpaka lero m’Baibulo kutitsimikizira kuti Uthenga wa madzi ndi Mzimu Woyera unali Uthenga umene mpingo

Page 316: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

316 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

woyamba wa chikhristu unkalalika. Kuvomereza kwa Pauloku chinali chikumbutso cha masiku amenewo ndiponso chopereka chake chothokozera Ambuye.

Kodi Paulo anali wochimwa atakhulupilira Yesu? Ai. Iye anali wochimwa asanabadwe mwatsopano, koma pamene iye anakhulupilira Yesu ngati Mpulumutsi wake, pamene iye anazindikira kuti machimo onse adziko lapansi anaperekedwa kwa Yesu kudzera mu ubatizo wake, pa nthaœi imene anakhulupilira mwazi ndi imfa ya Yesu pa mtanda, iye anasanduka olungama.

Chifukwa chimene Paulo akhudzitchula kuti ndiye wochimwa koposa ndi chakuti iye anali kukumbukira nthaœi ya imene iye ankazunza akhristu ndiponso ankathokoza Mulungu pakupulumutsa munthu wochimwa chotere.

Tsono ndani amene anganene kuti Paulo anali wochimwa? Izi sizingapindule kanthu. Anthu okhawo amene sadziœa za chiombolo cha Yesu

Khristu angathe kunena zimenezi. Kodi munthu wochimwa angalalikire Uthenga

Wabwino kwa anthu ena? Nzosatheka. Munthu sangalalike chimene iye sadziœa! Ngati munthu sanapulumutsidwe, angapulumutse bwanji anthu ena!

Ngati munthu akumira pa madzi nafunanso kuthandiza mnzake nzodziœikiratu onsewo adzamira. Tsono munthu wochimwa kodi angapulumutse anzake? Ndiye kuti adzaœatengera ku gehena anzake onsewo. Kodi munthu wodwala angachize bwanji wodwala mnzake? Nanga munthu wonyengedwa ndi Satana angapulumutse mnzake?

Mtumwi Paulo anali wochimwa koma adasanduka olungama pamene iye anakhulupilira ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Motero, iye adasanduka Mtumwi wa Mulungu ndi kuyamba kulalika Uthenga Wabwino kwa anthu ochimwa adziko lapansi. Iye adapulumutsa anthu ambiri ndichifuniro cha Mulungu. Ndipo iye sanali

Page 317: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

317 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

wochimwa. Iye anabadwa mwatsopano ndikukhala

m’chifuniro cha Mulungu. Iye adasanduka Mlaliki wa Mau a Mulungu amene anabweretsa anthu ambiri kwa Mulungu. Iye sanali Mlaliki wolalikira za kukhosi kwake koma ankhalalika chifuniro cha Mulungu.

Kodi iye anali wochimwa? Ai. Iye anali wolungama. Monga munthu wolungama, iye anakhala Mtumwi wa choonadi cha Mau a Mulungu. Kumutchula wochimwa nkunyoza Mulungu ndiponso kusamvetsa choonadi. Iye anali wolungama. Pakutero sitikunyoza Yesu kapenanso Paulo.

Ngati tinena kuti Paulo anali wochimwa ngakhale adakumana ndi Yesu, ndiye kuti tili kusandutsa Yesu ngati wonama. Yesu ndi amene adasandutsa Paulo kukhala wolungama, ndiponso Yesu yemweyo ndi amene anasandutsa Paulo kukhala Mtumwi weniweni.

KODI MACHIMO ATHU ANGACHOKE MWA IFE PAKULAPA? Machimo athu sangachotsedwe pakupemphera

kapenanso kulapa popeza chiombolo sintchito ya munthu kapenanso mapemphero amunthu. Koma kuti machimo athu afafanizidwe kwathunthu ndiponso kwa muyaya, tiyenera kukhulupilira ubatizo ndi mwazi wa Yesu ndiponso kuvomereza kuti Yesu ndi Mulungu. Chiombolo chenicheni chimaperekedwa kwa anthu amene amakhulupilira kuti Yesu adatichotsera machimo athu onse pakubatizidwa ndipo pakukhetsa mwazi wake pa Mtanda kuti atipatse moyo watsopano.

Tsono kodi tingachotse machimo athu atsiku ndi tsiku pakupemphera ndi chilapa? Ai. Machimo onse amene timachita pa moyo wathu onse adaœachotsa kale zaka 2000 zapitazo pamene Yesu anabatizidwa.

Page 318: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

318 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

Tinatsukidwa machimo athu kwa muyaya ndi ubatizo wa Yesu ndiponso pakukhetsa mwazi pa mtanda. Iye anakhala Mwana Wankhosa woperekera nsembe ya machimo athu, anachotsa machimo athu, ndi kulipira ndipo machimowo ndi ubatizo wa Yesu ndiponso pakukhetsa mwazi pa mtanda. Iye anakhala Mwana Wankhosa woperekera nsembe ya machimo athu, anachotsa machimo athu, ndi kulipira ndipo machimowo ndi ubatizo ndiponso mwazi wake.

Ngakhale machimo amene timachita tidakhulupilira mwa Yesu ayenera kutsukidwa mu kasupe wa chipulumutso cha Yesu choonadi cha chiombolo; Yesu adakhala kale Mpulumutsi ndipo anachotsa kale machimo amene timachita mpaka kufa kwathu. Yesu anabwera pa dziko lapansi ndi kubatizidwa “Umu ndim’mene…” (Mateo 3:15). Ndipo anakwaniritsa chifuniro chonse cha Mulungu pakuchotsa machimo athu onse. Mwana wa Mulungu anatenga machimo athu onse pakubatizidwa.

Ubatizo wa Yesu uli ndi tanthauzo “Kutsukidwa.” Popeza machimo athu onse anaperekedwa kwa Yesu pamene anabatizidwa, tinatsukidwa machimo athu onse ndiponso tinamasulidwa ku machimo onse.

Ubatizo umatanthauzanso kuti ‘Kumizidwa, kukwiriridwa.’ Chifukwa chakuti machimo athu onse anaperekedwa kwa Yesu, Iye anafa chifukwa cha ife ochimwa. Motero anthu onse amene amakhulupilira kuti machimo ao anaperekedwa kwa Yesu kudzera mu ubatizo wake adzayeretsedwa kwa muyaya.

Chikhulupiliro choona ndicho kukhulupilira m’mitima mwathu kuti machimo athu, ngakhalenso machimo amene tikuchita panopa, anaperekedwa kwa Yesu zaka 2000 zapitazo pamene iye anachotsa machimo athu onse pakutero anakwaniritsa chifuniro cha Mulungu.

Akadapanda kuchotsa machimo athu onse zaka zapitazo ndi ubatizo wake, sikukapezekanso njira ina yochotsera machimo athu. Kumbukirani kuti

Page 319: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

319 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

machimo athu onse anachotsedwa mwa ife kale kalelo.

Chikhulupiliro choona ndiponso chipulumutso cha moyo wa uzimu chitanthauza kupereka machimo athu kwa Yesu kuonetsetsa kuti machimowo achotsedwadi, kunena kuti, ‘Mwachotsadi tchimo ili, sichoncho kodi?’ Ndiponso kukhulupilira iye ndi ku m’thokoza. Nchifukwa chake Iye anabwera, kubatizidwa ndi kufa pa mtanda ndiponso anaukitsidwa kwakufa patatha masiku atatu, pakutero Iye adakhala Mpulumutsi wathu..

Ndi odala anthu amene amachotsa machimo ao ndi kukhulupilira ubatizo wa Yesu umene udachotsa machimo athu onse. Chikhulupiliro choona ndicho kukhulupilira Yesu amene adachotsa machimo onse adziko lapansi ndi ubatizo wake.

AROMA 8:30 ATIUZA KUTI, “MULUNGU SADANGOWPATULA, KOMANSO ADAŒAITANA, SADANGOŒAITANA, KOMANSO ADAŒAONA KUTI NGOLUNGAMA PA MASO PAKE, SADANGOONA KUTI NGOLUNGAMA PA MASO PAKE, KOMANSO ADAŒAGAŒIRAKO ULEMELERO WAKE.” KODI MAU AŒA AKUNENA ZA CHIYERO CHODZIPATSA TOKHA? Mau aœa sakunena za kudziyeretsa. Anthu

ambiri amene adaphunzira za Mau a Mulungu ndipo alaliki onama akhala ali kuphunzitsa kuti, “Anthu okhulupilira Yesu adzasintha ndi kuyera pa iwo okha m’thupi ndiponso mu uzimu,” ndipo

Page 320: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

320 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

anthu ambiri amakhulupilira zimenezi. Kunena zoona, anthu oterewa

amangowonjezera kuipa kulephera kwao. Ndipo machimo ao amakula pamene iwonso akukula. Kodi chiyero cha munthu chagona pa nthaœi? Chiyero chimene chimabwera pa nthaœi imene munthu wafuna Mulungu sakondwera nacho ndipo Satana ndi amene amakondwera nacho.

Anthu angathe kusanduka olungama machimo m’mitima mwawo mulibe chifukwa Yesu adachotsa machimo onse indi ubatizo wake ndiponso pamene iye adadzipereka monga nsembe yoperekera machimo. Anthu amasanduka olungma chifukwa cha ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Anthu amakhala olungama pakukhulupilira choonadi chakuti Yesu anasenza machimo athu onse.

Anthu akuti, ‘chiyero’ atanthauza kukhala opanda uchimo. Kuyesa yesa kukhala oyera mwa kufuna kwathu, sindiye kuti tikukhulupilira choonadi, koma ndi kukopeka ndi zofuna za thupi lathu lofokali.

Chiyero chobwera mwa kufuna kwa munthu chimachokera ku zilakolako zoipa za thupi lake. Zipembedzo zonse zili nawo mau akuti chiyero, koma ife okhulupilira mwa Yesu sitiyenera kuseœeretsa mau amenewa.

Sitisanduka olungama pa kungokhulupilira ubatizo ndi wazi wa Yesu Khristu, Uthenga wa chipulumutso cha moyo wathu wa uzimu. Anthu olungama moonadi amabadwa mu chikhulupiliro cha Uthenga wa ubatizo ndi mwazi wa Yesu Khristu.

KODI KUVOMEREZA MACHIMO ATHU KUNGACHOTSE MACHIMO MWA IFE? Ai. Machimo sabisika chifukwa cha kulapa,

koma amachoka ndi chikhulupiliro mu Uthenga wa madzi ndi Mzimu oyera. Machimo angachoke

Page 321: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

321 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

mwa ife ngati tikhulupilira ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake, umene udachotseratu machimo athu onse. Umenewu ndi Uthenga wa chipulumutso cha moyo wa Uzimu mwa Yesu, amene anachotsa machimo athu onse indi ubatizo wake mu mtsinje wa Yolodane.

Kulapa machimo ndiko kuvomereza malamulo a Mulungu, koma chiombolo chimabwera kwa ife pamene tikhulupilira ubatizi ndi mtanda wa Yesu Khristu.

Madzi a ubatizo ndiponso mwazi wa Khristu ndiwo choonadi chochokera kumwamba chimene chinapulumutsa anthu onse ku machimo ao, ndipo chipulumutso sichibwera chifukwa cha kuvomereza machimo, koma pakukhulupilira kuti Yesu anasenza machimo onse a munthu ndi anthu onse pakubatizidwa. Kupachikidwa kwa Yesu pa mtanda chidali chilango chifukwa cha machimo amene anatenga kwa anthu ochimwa.

Choncho chipulumutso chenicheni cha munthu chagona pa ubatizo wa Yesu Khristu mu mtsinje

wa Yolodane ndi mwazi wake pa mtanda. Chimene tidapulumukira ku machimo athu nchakuti Yesu adatisambitsa ndi mwazi wake.

Ngati alipo anthu amene amalalika kuti tingathe kuomboledwa pakuvomereza machimo athu, ndiye ali kukana chipulumutso cha Mulungu.

Motero, tiyenera kukhulupilira ubatizo ndi mwazi wa Yesu, chipulumutso chimene Yesu adatipatsa. Musayese kuganiza kuti machimo athu angachoke pa kuvomereza machimo athu kwa Mulungu.

Dziœani kuti machimo athu adzatitengera kugehena koma machimo angachoke m’mitima mwathu ngati tikhulupilira Yesu, ubatizo wake ndiponso mwazi wake, umene umatiombola ndi kutisandutsa olungama pa maso pa Mulungu. Iyi ndi njira yokhayo imene tingapulumukire nayo kumachimo athu anachotsedwa kamodzi kokha pakukhulupilira mau a choonadi, madzi ndi mwazi wa Yesu Khristu (1 Yohane 5:4-8).

Machimo sachotsedwa pa kulapa nthaœi ndi

Page 322: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

322 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

nthaœi. Ngati mulimbikira kunena kuti machimo anu adzachoka pakulapa nthaœi ndi nthaœi, mapeto ake mukapezeka muli kugehena. Tiyeni tikhulupilire Uthenga woona kuti machimo amene ali m’mitima mwathu afafanizidwe. Khulupilirani ndi m’tima wanu wonse, osati ndi mutu wanu, kuti mumasuke kumachimo anu kwa nthaœi zonse.

KODI UTHENGA WOONADI NDI UTI? Uthenga woonadi ndi umene umatimasula ku

machimo athu pamene takhulupilira uthengawo. Uthenga wa Mulungu ndi wamphamvu kwambiri.

Uthenga wa Mulungu ndi wakuti, “Yesu Khristu adabweza ngongole ya munthu amene adakongola (wochimwa), amene analephera kubweza ngongole yake.” Chifukwa chimene tkunenera kut Uthenga wa Mulungu ndi wamphamvu ndi chakuti pamene tinayenera kufa

chifukwa cha machimo athu ndikupita kugehena, pamene tinali woyenera kuœeruzidwa, Mwana wa Mulungu anakhala nsembe yoperekera machimo aanthu a padziko lonse.

Uye anabwera pansi pano kamodzi ndi kusenza machimo adziko lonse lapansi kudzera mu ubatizo wake mu mtsinje wa Yolodane ndi kutisambitsa kuti machimo athu afafanizidwe kwa muyaya.

Iye adalipira mphotho (dipo) ya machimo athu ndi ubatizo wake ndiponso ndi imfa yake pa mtanda. Yesu adaphulitsa machimo athu ngati bomba ndi ubatizo wake ndiponso mwazi wake. Uwu ndiwo uthenga woonadi.

Uthenga woonadi ndi wakuti Yesu anabwera pa dziko lino lapansi ndipo kuti pakubatizidwa ndiponso pakukhetsa mwazi wake pa mtanda anapulumutsa anthu onse okhulupilira iye.

Monga adalembera Yohane pa 1 Yohane 5:6, “Yesu Khristu ndiye amene adabwera kudzera mwa madzi ndi mwa magazi. Sadabwere mwa madzi okha, koma mwa madzi ndi mwa magazi

Page 323: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

323 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

omwe. Ndipo Mzimu Woyera ndiye amachitirapo umboni pakuti Mzimuyo ndiye choona.”

KODI NCHIFUKWA CHIYANI YESU ANADZIPEREKA PA MTANDA? Nsembe ya Yesu inali yoperekera machimo

aanthu amene anachotsa kudzera mu ubatizo wake. Iye anapereka thupi lake mwa anthu kulipira machimo a munthu kuti potero anthu amasulidwe ku chilango cha machimo ao.

Chimene tiyenera kudziœa nchakuti Yesu anabatizidwa mu mtsinje wa Yolodane kuchotsa machimo a munthu. Ndipo tiyenera kukhulupilira kuti Yesu anapachikidwa pa mtanda chifukwa cha machimo athu.

Yesu akadapanda kubatizidwa asanapachikidwe pa mtanda, akadapanda kufa pa mtanda machimo

athu sakadachotsedwa. Motero tiyenera kukhulupilira ubatizo ndi mwazi wa Yesu Khristu. Tsono popeza Yesu ndi Mwana wa Mulungu, nsembe ya machimo athu, Iye adapereka nsembeyo kuchotsa machimo onse.

Ife tonse tiyenera kukhulupilira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, ndi kuti Iye adabtizidwa kuti achotse machimo onse aanthu. Yesu anapachikidwa kuti achotse machimo onse aanthu. Yesu anapachikidwa pa mtanda kuti ife anthu ochimwa tipulumutsidwe ku machimo athu onse ndiponso ku chilango.

KODI YOHANE MBATIZI NDANI AMENENSO ANABATIZA YESU? Mulungu anapereka malamulo ake kudzera kwa

Mose ndiponso nsembe ya machimo kuti munthu akhale omasuka ku machimo ndi mphulupulu wake.

Page 324: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

324 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

Iye adzoza Aroni, mbale wake wa Mose ngati wa nsembe wa m’kulu ndipo analola kuti iye apereke nsembe ya machimo pa tsiku la chikhumi la mwezi wa chisanu ndi chiœiri, Ttsiku Lopereka nsense ya machimo kuti machimo amene Aisraele anachita chaka chimenecho afafanizidwe (Levitiko 16).

Iye adatsindika kunena kuti nsembe ya Tsiku Lopereka nsembe kuperekedwa ndi anthu afuko la Aroni. Mulungu adapanga tsiku lakuti Aisreale azipereka nsembe yochotsera machimo ao pakusanjika manja, pa nsembe yoperekedwa ndi amfuko la Aroni. Ili ndi lamulo la kaperekedwe ka nsembe lokhazikutsidwa ndi Mulungu.

Mulungu adafuna kuti anthu onse adziœe kuti Yesu ndiye Mpulumutsi. Ndipo pa nthaœi ya Chipangano Chatsopano Yohane Mbatizi anali wa m’banja la Aroni ndiponso (1 Mbiri 24:10, Luka 1:5) wansembe wamkulu wotsiliza wa m’Chipangano Chakale (Mateo 11:11-13). Yohane Mbatizi monga Mneneri wa Mulungu ndiponso

wansembe wam’kulu anabatiza Yesu, Mwana wa Mulungu amene anabwera kudzapulumutsa wochimwa, ndi kunyamula machimo onse a anthu pa mutu pake.

Anthu onse ndi odala chifukwa Yesu anasenza machimo ao kudzera mwa Yohane Mbatizi; ntchito ya Yohane Mbatizi inali ya wansembe wam’kulu komanso anali mkhala pakati wa anthu onse; mtumiki wa Mulungu amene adatenga machimo aanthu ndi kupatsa Yesu Khristu.

Yohane Mbatizi ndi woimirira ndiponso wansembe wamkulu wa anthu amene anatumidwa ndi Mulungu ndi wam’thenga amene anatumidwa miyezi isanu ndi umodzi Yesu asanabwere. Ndipo kumbali inayi, Yesu anali Mwana Wankhosa wa Mulungu amene anachotsa, achimo onse a dziko lapansi pamene Yohane Mbatizi anali wansembe wam’kulu amene anapereka machimo onse aanthu kwa Yesu Khristu kudzera mu ubatizo. Yohane Mbatizi anali mtumiki wa Mulungu.

Page 325: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

325 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

MU YOLODANE M’MENE YESU ANABATIZIDWIRA Mtsinje wa Yolodane umathira m’Njanya

Yakufa m’mene simukhala chinthu cha moyo. Nyanja Yakufa ndiyozama kwambiri. Motero madzi a m’Nyanja Yakufa sayenda kulikonse, anangoima m’Nyanjamo.

Yesu Khristu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi m’tsinje wa imfa (m’tsinje wa Yolodane).

Mtsinje umenewu utanthauza kuti anthu onse kupatula amene alibe machimo m’mitima adzataika kwa muyaya pamapeto pake.

Choncho mtsinje wa Yolodani ndi mtsinje umene ntchito yake nkusambamo kuti litsiro la uchimo lichoke, mtsinje kumene wochimwa amaferako. Mwadule, mtsinje umenewu ndi mtsinje wa chiombolo kumene machimo onse anachotsedwa kudzera mu ubatizo wake, kuperekedwa kwa machimo athu kwa Yesu.

KODI NSEMBE IMENE ANKAPEREKA PA TCHIMO LIMENE ANTHU ACHITA M’CHIPANGANO CHAKALE NDI CHIYANI? Panali nsembe yoperekera machimo amene

anthu achita pa tsiku limenelo. Pofuna kupereka nsembe ya machimo amene pa tsikulo, munthu aliyense ankayenera kubweretsa Mwana Wankhosa, nkosa, mtheno wa ng’ombe kapanenso nkhunda kukachisi ndi kusanjika manja kupereka machimo ake pa nsembeyo. Iyi inali nsembe yoperekera machimo amene anthu achita patsiku limenelo monga adanenera m’malamulo a Mulungu (Levitiko 3:1-11)

Page 326: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

326 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

NANGA NSEMBE YOPEREKERA MACHIMO A PA CHAKA M’CHIPANGANO CHAKALE NDI CHIYANI? Inali nsembe yoperekera machimo amene anthu

achita m’chaka chimenecho imene ankapereka kamodzi. Wansembe wam’kulu ankasanjika manja pa mutu pa mbuzi ndi kupereka machimo onse a chaka chimenecho amene Aisraele ankachita kamodzi (Levitiko 16:1-34).

Nsembe ya machimo apatsiku ndiponso machimo apachaka adaikwaniritsa ndi Yesu Khristu pamene Iye anakhala Mwana Wankhosa wa Mulungu kusenza machimo onse pa mutu pake kudzera mu ubatizo wake.

NANGA NSEMBE YOPEREKERA MACHIMO ANTHAŒI ZONSE INALI CHIYANI? Iyi ndinsembe yoperekera machimo onse

adziko la pansi yoperekedwa kamodzi kokha pakukhulupilira Yesu Khristu. Tsono popeza kuti Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu ndiponso Ambuye athu wa chikhalire, akhoza kuchotsa machimo amunthu kwa muyaya. Kodi Iye anachotsa bwanji kwa muyaya machimo athu?

1) Pakubadwa m’thupi la umunthu 2) Pakubatizidwa ndi Yohane Mbatizi mu

Yolodane 3) Pa kulandira chilango pa mtanda Mwana wa Mulungu anabwera pa dziko lino

lapansi m’thupi la umunthu ndipo anabatizidwa kuchotsa machimo amunthu kudzera mwa Yohane Mbatizi, kenaka anakhetsa mwazi wake pa mtanda, kupulumutsa anthu ku machimo ao kwa

Page 327: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

327 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

nthaœi zonse (Levitiko 16:6-22; Mateo 3:13-17; Yohane 1:29; Aheberi 9:12; 10:1-18).

KODI CHIOMBOLO CHINAPEREKEDWA KAMODZI KOKHA KAPENA MOPITIRIZA? Chimaperekedwa kamodzi popeza Yesu

anachotsa machimo aanthu kamodzi kokha pa kubatizidwa kamodzi ndi kulangidwa kamodzi kokha. Iye ananena pa Mateo 3:15, “Tsopano lino vomera, chifukwa umu ndi m’mene tiyenera kuchitira zimene Mulungu akufuna.”

Pa Yohane 1:29, Yohane Mbatizi adanena kuti, “Suuyu Mwana Wankhosa wa Mulungu amene anachotsa machimo onse adziko lapansi!” Ndipo pa Yohane 19:30, Yesu adanena kuti, “Kwatha.”

Pa Aheberi 10:9-18, “Koma pambuyo pake adati, ‘Ndabweratu kuti ndi chite chimene

mukufuna.’ Motero Khristu adathetsa mphamvu za nsembe za mtundu woyamba zija, kuti m’malo mwake akhazikitse nsembe ya mtundu wachiœiriyo. Chifukwa chakuti Khristu adachita zimene Mulungu adaafuna kuti achite, ife tidayeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene Iye adapereka kamodzi kokhako. Wansembe aliyense amaimirira tsiku ndi tsiku nkumatumikira, ndipo amapereka nsembe imodzi mozi mobwereza bwereza. Komabe nsembe zimenezi sizingathe konse kuchotsa machimo. Koma Khristu adapereka nsembe imodzi yokha yochotsa machimo onse. Ndipo ataipereka adakakhala ku dzanja la manja la Mulungu, kumeneko tsono akudikira kuti Mulungu asandutse adani kukhala ngati chopondapo mapazi ake. Mwa nsembe imodzi yomweyo wasandutsa angwiro kwa muyaya onse amene Iye akuœayeretsa. Mzimu Woyera nayenso amatitsimikizira zimenezi, poyamba Iye akuti, ‘Nachi chipangano chimene ndidzachita nawo atapita masiku amenewo’ akutero Ambuye:

Page 328: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

328 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

‘Ndidzaika malamulo anga m’mitima mwao, ndidzachita kuœalemba m’maganizo ao.’ Pambuyo pake akutinso, ‘Sindidzaœakumbukiranso konse machimo ao ndi zolakwa zao. Pamene Mulungu wakhululukira zonsezi, sipafunikanso nsembe yoperekera machimo.’”

Machimo onse amunthu anaomboledwa kamodzi ndi ubatizo ndiponso mwazi wa Yesu Khristu.

KODI MPHOTHO YA MACHIMO NDI CHIYANI? Mphotho ya uchimo ndi imfa. Posaœerengera

m’mene tchimo liliri, tchimo lililonse la munthu liyenera kuœeruzidwa pama pa Mulungu, ndi chiœeruzo cha machimo onse ndi imfa. Pofuna kupereka nsembe ya machimo onse munthu unkapereka nkhosa yopanda chilema kwa Mulungu.

Motero, Mulungu anapereka Mwana Wankhosa kuombola anthu onse ku machimo ao. Mwana Wankhosa ankamusanjika mwanj apa mutu pake kum’senzetsa machimo ndipo ankafa m’malo mwa anthu.

M’chipangano Chatsopano, Yesu anachotsa machimo onse a munthu kudzera mu ubatizo wake mu Yolodane monga Mwana Wankhosa ndipo anafa m’malo mwa munthu. “Mphotho ya uchimo ndi imfa, koma mphatso ya Mulungu ndi mo wosatha mwa Khristu Yesu” (Aroma 6:23).

Mphotho ya uchimo ndi imfa, koma Yesu adaonetsa chikondi chake pa kufa m’malo mwa munthu ndi kupereka mphatso ya moyo wosatha kwa anthu onse ochimwa a dziko lapansi.

Page 329: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

329 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

KODI NCHIFUKWA CHIYANI YESU ANAYENERA KUFA PA MTANDA? Imfa ya Yesu inali malipiro amachimo onse

aanthu amene anaœachotsa ndi ubatizo wake. Anthu onse ankhayembekezera imfa mu ng’anjo ya moto wa kugehena chifukwa cha machimo ao. Tsono popeza Yesu anatikonda, adavomera ubatizo pa mtanda kutipulumutsa.

Iye adadzipereka monga nsembe ya machimo athu kuti atipulumutse – ku machimo athu, ndiponso temberero lakugehena. Imfa yake inali malipiro a machimo aanthu onse. Iye anabatizidwa kuchotsa machimo aanthu onse. Iye anabatizidwa a munthu ndipo adadzipereka ku chilango pa mtanda kuti apulumutse anthu onse ku machimo, imfa, chilango ndiponso ku chiwonongeko.

Imfa ya Yesu inali yolipilira malndu wa munthu chifukwa cha machimo ake amene Yesu

anaœasenza ku Yolodani ndi kulandira chilango chifukwa cha machimowo. Iye anafa pa mtanda ndipo anaukanso kwa kufa kuti ifenso tikhale ndi moyo monga anthu olungama.

KODI TIMAPINDULANJI PAMENE TIKUKHULUPILIRA YESU?

1) Timaomboledwa ku machimo athu ndi kusanduka olungama (Aroma 8:1-2). 2) Timalandira Mzimu wake Woyera ndi moyo wosatha (Nchito 2:38, 1 Yohane 5:11-12). 3) Timalandira ufulu wakukhala ana a Mulungu (Yohane 1:12). 4) Timalandira chilolezo choloœera mu ufumu wa Mulungu, ufumu wa kumwamba (Chivumbulutso 21,22). 5) Timalandira madalitso onse a Mulungu (Aefeso 1:3-23).

Page 330: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

330 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

KODI NCHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUKHULUPILIRA YESU? Ife tonse ndife ochimwa amene akadaponyedwa

kugehena popanda kukhulupilira Yesu Mpulumutsi wathu. Yesu yekha ndiye Mpulumutsi wathu amene angatiteteze ku chilango cha kugehena. Ife tiyenera kukhulupilira Yesu chifukwa Iye ndiye Mpulumutsi wathu weniweni. Kodi anthu onse aomboledwa ndi okhulupilira

Yesu amapita kuti —Kumwamba.— Kodi anthu amene sanakhulupilire ndi

kuomboledwa adzapita kuti pakutha moyo wao? —Kugehena; nyanja imene imayaka ndi kulilima (Chivumbulutso 21:8).— Kodi nkhosa za Mulungu ndani? —Ndi

anthu amene amalandira chipulumutso cha moyo wao wa uzimu mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu Khristu. —

Ndipo “Nkhosa zina zimene sizili za m’khola lino” (Yohane 10:16), ndi mbuzi zimene chifukwa chakuti zimakhulupilira chimene zakonda, chifukwa chakuti zikadali ndi uchimo pamene anthu onse okhulupilira ubatizo ndi mwazi wa Yesu amapulumutsidwa kamodzi kokha ndipo iwo ndi nkhosa za Mulungu.

KODI MPINGO WOONA WA MULUNGU NDI UTI? Mpingo wa Mulungu ndi kumene anthu

olungama, amene anaomboledwa ndiponso amene anaœaperekera nsembe ya machimo ao, anthu amene anapulumutsidwa pa kukhulupilira ubatizo ndi mwazi wake amasonkhana ndi kupembedza Mulungu (1 Akorinto 1:2). Mpingo woona wa Mulungu monga analembera pa Aefeso 4:5 ndi malo amene ziœalo zako zimakhulupilira “Ambuye mmodzi, chikhulupiliro chimodzi,

Page 331: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

331 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

ubatizo umodzi; Mulungu mmodzi ndi Atate wa onse.”

KODI MUNTHU OSATSATA ZIMENE MAU AKUNENA M’BAIBULO NDANI? Munthu osatsatira zolembedwa m’Baibulo ndi

munthu amene ali ndi uchimo mu m’tima mwake ngakhale akukhulupilira Yesu. A Tito 3:11, akunena kuti, “Paja ukudziœa kuti munthu wotere ngwosokonezeka ndipo ngwochimwa. Mwini wake yemwe amadziimba mlandu yekha.”

Yesu Khristu adasenza machimo athu onse ndi ubatizo wake, koma munthu wosatsata Mau a Mulungu sakhulupilira Uthenga wodalitsidwa, madzi (ubatizo wa Yesu, ubatizo wa chipulumutso) umen ndi mphatso ya chisomo cha Mulungu koma m’malo mwake amakana

chipulumutsochi ndipo amadziœeruza monga munthu ochimwa.

Mulungu amaœatchula anthu amenewa kuti ndi wochimwa (Tito 3:11). Inu muyenera kuganiza ngati muli monga anthu ameneœa kapena ai. Ngati mumakhulupilira Yesu ndi kumadzitchanso kuti ndinu wochimwa ndiye kuti simudziœa choonadi cha Uthenga wa madzi ndi Mzimu Woyera.

Ngati mukhulupilira Yesu koma nkumaganizanso kuti mukadali ndi uchimo, ndiye kuti ndinu munthu wosakhulupilira zimene malemba akunena, sichipulumutso chokwanira kukhulupilira Yesu nkumaganizanso kuti mukadali ndi uchimo.

Ngati ndinu mmodzi wa anthu amene amavomereza machimo pa maso pa Mulungu ndi kumaganiza kuti ndinu wochimwabe, ndiye kuti muyenera kuganizira bwinobwino za chikhulupiliro chanu.

Mungakhale ochimwa bwanji pamene Yesu adachotsa kale machimo anu onse? Nchifukwa

Page 332: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

332 Kulongosola kowonjezerapo

◄ Zam'kati ►

chiyani mukufuna kubweza ngongole imene Yesu adapereka kale ngati mphatso yanu. Ngati mulimbikira kubweza ngongole imene Yesu adalipira kale ndiye kuti ndinu wosakhulupilira chifukwa mukusiyana ndi Mulungu.

Munthu aliyense wokhulupilira Yesu koma sanabadwe mwatsopano ndi wachipha maso. Inu muyenera kudziœa choonadi. Chifukwa Mulungu adachotsa machimo onse adziko lapansi, ngati munyalanyaza chipulumutso chake ndinu a chiphamaso.

Munthu wachipha maso, ndi munthu amene amadzitcha wochimwa ngakhale akhulupilire Yesu Khristu. Ngati mudzitchula wochimwa pamene mukukhulupilira mwa Mulungu Woyera, ndinu a chipha maso. Kuti musakhale achipha maso, muyeyenra kukhulupilira ubatizo wa Yesu ndiponso mwazi wake pa mtanda.

Mungathe kupulumutsidwa ngati mukhulupilira zonsezi: ubatizo wa Yesu ndi mwazi wake.

Page 333: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

◄ Zam'kati ►

Mafunso ndi Mayankho ake

Funso & Yankho

Page 334: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

334 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

Funso & Yankho Funso 1: Ine ndakhala ndikuœerenga

mabuku onse amene mwakhala mukunditumizira ndipo ndachita chidwi ndi nkhani ya ubatizo wa Yesu. Tandiuzani, kodi mumaphunzitsa chiyani pa za ubatizo wathu, ndi imfa ndiponso kuuka kwa Yesu Khristu kodi zimenezi zikugwirizana bwanji?

Yankho: Poyamba tiyenera kumvetsa bwino

“ziphunzitso za ubatizo” monga nalamembera pa Ahebri 6:2. Baibulo limatiuza kuti pali mitundu itatu ya ubatizo; ubatizo wa Yohane Mbatizi wa kulapa machimo, ubatizo wa Yesu Khristu ndiponso ubatizo wathu.

Ubatizo umene ife timalandira ndi kuvomereza chikhulupiliro chathu mu ubatizo wa Yesu. Ndiko kunena kuti timabatizidwa kuti tivomereze kuti

anabatizidwa kuti achotse machimo athu onse ndiponso anafa pa mtanda kupereka nsembe ya machimowo. Tsopano mukhoza kumvetsa mau amene ali pa Mateo 3:15 pamene akunena kuti, “Tsopano lino vomera pakuti umu ndi m’mene tiyenera kuchita zimene Mulungu akufuna.” Ndi mau amenewa Yesu akutanthauza kuti Iye anasenza machimo onse adziko lapansi pakubatizidwa ndi Yohane Mbatizi, woimirira anthu onse.

Chinali cholinga cha Mulungu kutipulumutsa ku msampha wa uchimo. “Ndipo Chauta adamsenzetsa iyeyo machimo athu.” (Yesaya 53:6) ndipo anatipatsa chilungamo chake. ‘Chilungamo’ m’Chigriki ndiye kuti “daukzine” ndipo chitanthauza kukhala okhulupirika pa malonjezo ake.

Mau anenewa akutiuza kuti Yesu anasenza mphulupulu za anthu onse adziko lapansi mwanjira ya chilungamo pa kubatizidwa mwa njira yosanjika manja.

Page 335: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

335 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

Tinapulumutsidwa ndi chikhulupiliro cha mphamvu mu ubatizo wa Yesu, imfa yake pa mtanda, ndiponso kuuka kwake.

Kuumbalidwa kwa m’tima (Aroma 2:29) kumene kunachotseratu machimo onse m’kati mwa mitima yathu. N’chifukwa chake mtumwi Petro anauza anthu aja kuti “Lapani, ndipo aliyense wainu abatizidwe m’dzina la Yesu ndipo mudalandira mphatso za Mzimu Woyera” (Ntchito 2:38) pa tsiku la Pentekositi.

Anthu onse ochimwa ayenera kupeza chikhululukiro cha machimo ao pakukhulupilira m’dzina la Yesu. Kodi tanthauzo la dzina lakeli ndi chiyani? “Iye adzapulumutsa anthu onse ku machimo awo” (Mateo 1:21). Dzina lakuti Yesu litanthauza Mpulumutsi amene amapulumutsa anthu ake ku machimo ao. Kodi Iye anatipulumutsa bwanji ku machimo anthu onse? Yesu Khristu anatipulumutsa ku machimo athu onse pakubatizidwa ndiponso ndi imfa yake ya pa mtanda.

Pamene ophunzira a Yesu anali kulalika Uthenga Wabwino anali kuonetsetsa kuti anthu ali kumvetsa za ubatizo wa Yesu ndiponso mtanda wake pambuyo pake unkabatiza anthu amene akhulupilira zimenezi. Mwanjira yomweyi, ifenso tinabatizidwa kuti tivomereze kuti timakhulupilira ubatizo ndi imfa ya Yesu. Pamene tinabatizidwa timamuuza Yesu kuti “Zikomo Ambuye. Munasenza machimo anga onse mwa ubatizo ndiponso mudafa pa mtanda ndi kuuka kwakufa chifukwa cha ine. Ndi makhulupilira Uthenga wanu.” Timabatizidwa ndi antchito a Mulungu ngati chizindikiro cha chikhulupiliro chathu mu ubatizo wa Yesu ndi imfa yake pa mtanda, monganso m’mene Iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Chimodzimodzi anthu okhulupilira akale ankabatizidwa pofuna ku tsimikiza chikhulupiliro chawo mwa Yesu, ankachita izi akaphunzitsidwa Mau a Mulungu ndikulandira chiombolo ndiponso chikhululukiro cha machimo.

Miyambo ya ubatizo imachitika popanda ku

Page 336: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

336 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

umirizidwa, koma ngakhale nkofunika kutero, madzi a ubatizo sagwirizana ndi chipulumutso. Timapulumutsidwa pa kukhulupilira mu ubatizo ndi mwazi wa Yesu. Baibulo limatiuza kuti timabatizidwa mwa Khristu Yesu (Aroma 6:3; Agalatia 3:27).

Kodi nanga tinga batizidwe bwanji m’dzina lake? Izi nzotheka ngati tikhulupilira mu ubatizo wake popeza thupi lathu ndi khalidwe lathu lokonda uchimo limalumikizana ndi Yesu ndiponso linapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Yesu kudzera muubatizo wake. Zoonadi, popeza Yesu anasenza machimo athu ndi ubatizo wake, imfa yake inakhala chilango cha mphulupulu zathu. Choncho ifenso tinapachikidwa naye limodzi, thupi lathu, gawo la thupi lathu lokonda zoipa tinafa pamtanda pamodzi ndi Yesu ndi tinapulumutsidwa ku mphulupulu zathu zonse.

Anthu amene analumikizana ndi Yesu kudzera mu ubatizo wake ndiponso imfa yake akhoza kulumikizana nayenso m’kuuka kwake. Kuuka

kwake sikuukitsidwa ku imfa kokha, komanso kumatipanga ife kubadwanso mwatsopano monga mwana wa Mulungu, wangwiro ndi opanda uchimo pa maso pa Mulungu.

Tikadapanda kupereka machimo athu kwa Yesu pakusakhulupilira ubatizo wake, imfa ndi kuuka kwake zikadakhala zopanda tanthauzo, ndipo pakadakhala popanda chipulumutso. Anthu amene anatula machimo awo pa Yesu ndi chikhulupiliro ayenera kugwirizana nayenso mu imfa ndi kuuka kwake.

Ubatizo wa anthu okhulupilira uli ndi mphamvu monga momwe mwamuna ndi mkazi amamangira ukwati wawo wovomerezeka pa tsiku la ukwati. Ubatizo wa anthu okhulupilira akale aja unali ngati njira yovomereza chikhulupiliro chawo. Pamene tilalika za chikhulupiliro chathu mu ubatizo wake ndiponso mtanda pa maso pa Mulungu, chikhulupiliro, chimakhala chenicheni.

Tikapanda kumvetsa bwino tanthauzo lenileni la ubatizo wa Yesu ndi Yohane Mbatizi, sitinga

Page 337: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

337 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

khulupilirenso kuti tikhoza kupulumutsidwa ngakhale tisakhulupilire ubatizo wa Yesu ndiponso kufunika kwake. Imeneyi ndi nzeru chabe ya Satana. Timalandira chikhululukiro ndipo timalandiridwa kumwamba ndikukhulupilira moonadi ubatizo wa Yesu m’malo mokhulupilira ubatizo wathu.

Funso 2: Kodi ndinganene bwanji kuti ndine

olungama pamene ndi machimwa tsiku ndi tsiku?

Yankho: Ife anthu, timachimwa kuchokera pa

nthaœi yakufa kwathu. Kunena zoona izi zimachitika chifukwa cha maganizo athu amene amakhala ndi uchimo. Motero, Baibulo limatiuza kuti “Palibe munthu wolungama” (Aroma 3:10). Ichi nchifukwa chake Paulo adavomereza pa maso pa Mulungu kuti, “Awa ndi mau otsimikizika akuti Yesu adabwera pansi pano kuti adzapulumutse

anthu ochimwa ndipo mwa iwowo ine ndiye wochimwa koposa” (1 Timoteo 1:15).

“Koma tsopano yaonekera njira yopezera chilungamo pamaso pa Mulungu, ndipo njira yake sikutsata malamulo ai, Malamulowo ndi aneneri womwe amachitira umboni Njira yake yomwe anthu amaonekera ngwolungama pa maso pa Mulungu ndi yakuti anthuwo akhulupilire Yesu Khristu. Zimenezi Mulungu amachitira anthu onse okhulupilira Khristu. Paja palibe kusiyana pakati pa anthu ai popeza kuti onse adachimwa nalephera kufika ku ulemelero umene Mulungu adawakonzera. Koma mwakukoma m’tima kwake, kwa ulere anthu amapezeka kuti ngwolungama pa maso pa Mulungu, chifukwa cha Yesu amene adaœaombola” (Aroma 3:21-24).

“Chilungamo” cha Mulunguchi chitanthauza kuti Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi mu m’tsinje wa Yolodane. Pamene anali kubatizidwa Yesu adauza Yohane kuti, “Tsopano lino vomera pakuti umu ndi m’mene tiyenera kuchita zimene

Page 338: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

338 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

Mulungu akufuna” (Mateo 3:15). “Iye anasenza machimo a dziko lapansi” (Yohne 1:29) ndi m’mawa mwake iye anabatiza Yesu.

Kodi mau akuti ‘machimo adziko lapansi’ akutanthauza chiyani? Mau amenewa atanthauza machimo aanthu onse kuchokera pa nthaœi ya Adamu ndi Hava, munthu woyamba pa dziko lapansi, kufikira ku munthu wotsiliza pa dziko lonse lapansi. Kale kunali dziko lapansi, panopa lilipo ndipo kutsogoloko lidzakhalakobe. Yesu, Alefa ndi Omega, adapereka nsembe imodzi kwa nthaœi zonse, ndipo adanyamula machimo onse a dziko lapansi kamodzi kokha kudzera mu ubatizo wake ndiponso imfa yake pa mtanda. Ndipo ife tinayeretsedwa.

Dziœani kuti mau akuti tayeretsedwa akunena za nthaœi ino imene tilimo. Tiyeretsedwa kuchokera pa nthaœi imene tidayamba kukhulupilira Mulungu mpaka pano ndipo zidzakhala chimodzimodzi mpaka kale. Pakuti Ambuye ndi Mulungu wamphamvu zonse, ali

kuona ndi diso ngati lambalame dziko lapansi kuchokera pa chiyambi mpaka kutha kwa dziko lapansi. Ngakhale patha zaka 2000 pamene Yesu anabatizidwa, anachotsa machimo aanthu kuchokera pa chiyambi mpaka kumathero adziko lapansi. Choncho Iye asanafe pa mtanda adati ‘kwatha’ (Yohane 19:30). Iye anachotsa machimo onse adziko lapansi zaka 2000 zapitazo ndipo anafa pa mtanda kuchotsa machimo onse.

Timachimwabe ngakhale tinapulumutsidwa chifukwa thupi lathu ndi lofooka. Koma Yesu anatiombola ku machimo athu onse amene tikuchita ndiponso amene tidzachite kutsogolo potula machimo pa iye kudzera mu ubatizo wake ndi kulandira chilango cha machimowo pa mtanda. Ichi ndicho chipulumutso chenicheni ndiponso chipulumutso cha chilungamo cha Mulungu.

Yesu akadapanda kunyamula machimo athu am’tsoglo palibe munthu ndi m’modzi yemwe amene akadapulumutsidwa ku machimo ake a

Page 339: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

339 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

tsiku ndi tsiku, “Pakuti mphotho ya uchimo ndi imfa” (Aroma 6:23). Pamene Yakobo ndi Esau anali m’mimba mwa mayi wawo, Mulungu adawapatula kukhala mitundu iœiri asanachite choipa chilichonse kapena chabwino, ndipo anakonda Yakobo kuposa Esau, ndipo adati “Wam’kulu adzakhala wotumikira wam’ng’ono” (Genesis 25:23).

Ife anthu timakhala mu uchimo wobadwa nawo mpaka ku mwalira, koma Mulungu adaadziœiratu machimo ndipo adachotseratu machimo athu kamodzi kokha ndi ubatizo wake ndiponso imfa yake pa mtanda chifukwa anatikonda kwambiri. Tili kukhala mu nthaœi ya madalitso. Mneneri Yesaya anati, “Muœayankhule mofatsa anthu a Yerusalemu. Muœauze kuti nthaœi ya mavuto ao yatha, machimo ao akhululukidwa. Ndaœalanga moœilikiza chifukwa cha machimo ao.” (Yesaya 40:2). Nthaœi yokhala akapolo a uchimo yatha kudzera mu uthenga wa ubatizo wa Yesu, ndi mtanda, motero aliyense wokhulupilira uthenga

umenewu angathe kupulumutsidwa ku machimo ake. “Nachi chipangano chimene ndidzachita nawo atapita masiku amenewo akutero Ambuye, ndidzaika malamulo anga m’mitima mwao. Pambuyo pake akutinso sindidzawakumbukiranso konse zolakwa zao, pamene Mulungu œakhululukira zonse sipafunikanso nsembe yoperekera machimo” (Ahebri 10:16-18).

Mulungu satiœeruzanso chifukwa cha machimo onse, ndi kuœeruza Yesu m’malo mwathu.

Chotsatira chake ife tiyembekezere Yesu kuti adzabwere ndi kumasunga mau ake, monga anthu olungama opanda uchimo, ngakhale timapitilira kuchimwa pa moyo wathu.

Funso 3: Kodi ubatizo wolapa machimo wa

Yohane uja utanthauzanji? Yankho: Yohane Mbatizi anali mtumiki wa

Ambuye, amene anabadwa miyezi isanu ndi

Page 340: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

340 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

umodzi Yesu asanabwere, ndipo ananeratu m’buku la Malaki, mneneri wotsiliza m’Chipangano Chakale, “Kumbukirani Malamulo a Mose, mtumiki wanga, amene ndidamula ku Horebi, kwa Aisiraele onse ndiwo malemba ndi chiœeruzo. Ndipo ndidzabwezera mitima ya atate kwa ana ndipo ya ana kwa atate ao kuti ndisatike ndi kuononga dziko lonse” (Malaki 4:4-6).

Yesu atabadwa ana Aisraele anatailira mau a m’Chipangano cha Mulungu ndi kuyamba kupembedza milungu ina. Ankapereka akhungu ndiponso achilema monga nsembe ndipo adapa kachisi wa Mulungu ngati malo ochitira malonda. Malamulo a Mose ndi m’mabuku aneneri ananeneratu za wochimwa (Aroma 3:20). Nkuchimwila Mulungu kutsasatira zolembedwa m’mabuku a Malamulo.

M’chipangano Chakale, wochimwa amene walephera kutsata malamulo ankapereka nsembe ya uchimo patsogolo pa Kachisi Woyera, ndi kusanjika manja pa mutu wansembeyo kutula

machimo ake pa nsembeyo, anali kuchitazi kuti machimo ake akhululukidwe ndi kuyanjananso ndi Mulungu. Pambuyo pake wansembe ankatenga magazi ansembeyo ndi kupaka pa guwa la mkachisimo.

Komabe, Aisraele sanali kupulumutsidwa kotheratu ngakhale kuti ankapereka nsembe ya machimo awo a tsiku ndi tisku. Motero Mulungu anapanga tsiku lapadera Tsiku Loperekera Nsembe ya Machimo. Pa nthaœi imeneyi mpamene Mulungu ankaœakhululukira machimo ao a chaka ndi chaka patsiku lachikhumi la mwezi wa chisanu ndi chiœiri.

Pa tisku limenelo Aroni ankatenga mbuzi ziœiri, imodzi ya Ambuye imodzi yoperekera machimo. Ndipo ankasanjika manja pa mutu pa mbuzi yokaphedwayo kuti potero Ambuye atule machimo onse apa chaka pa mbuziyo. Akatero Aroni, wa nsembe wam’kulu ankapha mbuziyo ndikutenga magazi ake kupaka pa mpando wa chifundo.

Page 341: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

341 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

Akatsiliza kupereka nsembe ya uchimoyo anali kusanjika manja ake mbuzi ya moyo ija, ndi kuulula machimo onse apa chaka a Aisraele pambuziyo, ndipo ankaithamangitsa ku chipululu. Aisraele ankapulumutsidwa ku machimo awo achaka ndi chaka mwanjira imeneyi.

Komabe, nsembe yoperekedwa potsatira malamulo a M’chipangano Chakale sinali kuchotseratu machimo onse aanthu. Chinali chithunzithunzi chabe cha (Mpulumutsi wolonjezedwa uja) (Ahebri 10:1). Anthu aku Israele sanayembekezere kubwera kwa Yesu Khristu Mpulumutsi. M’malo mwake ankapembedza milungu ya chilendo m’dziko uchimo, kuleka mau a neneri M’chipangano Chakale.

Koma Mulungu adaaneneratu kuti adzatuma Yohane Mbatizi kuti abwezere mitima ya Aisraele kwa Mulungu, ndikukonza mitima ya anthu kuti ilandire Yesu Khristu, anapereka ubatizo wakuvomereza machimo kwa Aisraele ku Yudea.

Cholinga chake pakuwabatiza ndi madzi chinali chakuti akhulupilire Yesu amene adzabatizidwe ndi Yohane Mbatizi mwa njira yosanjika manja kuchotsa machimo onse aanthu ndi kupachikidwa kupulumutsa anthu onse. Iye adati Yesu adzabwera kudzakwaniritsa nsembe zimene sizinkakwaniritsa kuchotsa machimo onse, monga Aisraele ankapulumukira pakupereka nsembe yopanda chilema, pakusanjika manja pa mutu pa nsembeyo ndiponso poyipereka motsatira malamulo a M’chipangano Chakale.

Aisraele ambiri ankaulula machimo ao, kulapa ndipo ankabatizidwa ndi iye. Kulapa kutanthauza kutembenuka m’tima ndi kuupereka kwa Ambuye. Anali kubwera kwa Yohane, ndipo pokumbukira malamulo a Mose iwo ankalapa machimo ao ndi kuvomera kuti iwo ndi ochimwa kufikira nthaœi ya kufa kwao. Adavomeranso kuti sangaloœe ku ufumu wa Mulungu posunga malamulo, ndipo anasintha maganizo ao ndi kupereka mitima yao kwa Yesu Khristu amene adanyamula machimo oa

Page 342: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

342 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

onse ndi kutsekula khomo la kumwamba. Ubatizo umene Yohane ankapereka kwa anthu

aku Israele unali chinthu chotsatira. Akufuna kuti anthuwo aulure machimo ao ndi kulapa machimowo ndikuyang’ana kwa Yesu Khristu, amene akanabatizidwa ndi iye, wansembe wam’kulu ndiponso woimirira wa anthu onse, ndi kupachikidwa kuti awapulumutse ku machimo ao, monga momwe anawabatizira. Uku ndiko kulapa kovomerezeka ndi Baibulo.

Motero, Yohane anafuula kwa anthu, “Ine ndimakhubatizani ndi madzi, kusonyeza kuti mwatembenukadi, koma amene akubwera pambuyo panga ndi wamphamvu kuposa ine ameneyo ine ndine wosayenera ngakhale kunyamula nsapato zake, Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera ndi moto” (Mateo 3:11).

Yohane Mbatizi adatembenuzira mitima ya anthu kwa Yesu ndipo adaœatsimikizira kuti Yesu adachotsa machimo aanthu onse pa dziko lapansi (Yohane 1:29). Ndipo adafa monga munthu

wokhulupilira . Funso 4: Kodi simukuganiza kuti

kukhulupilira ubatizo wa Yesu kwambiri kukhoza kusandutsa imfa yake kukhala yopanda phindu?

Yankho: Ubatizo wa Yesu ndi imfa yake pa

mtanda ndi zofunika kwambiri. Sitinganene kuti chimodzi ndi chofunika kuposa china. Komabe, vuto ndi lakuti akhristu ambiri masiku ano amangodziœa mwazi wa Yesu wokha pa mtanda. Iwo amakhulupilira kuti anakhululukidwa chifukwa chakuti Yesu anafa pa mtanda, koma si mtanda wokha umene Yesu anachotsera nawo machimo athu. Popeza kuti iye anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi ndi kutula machimo athu pa Iye imfa yake pa mtanda inali chilango cha machimo athu.

Kukhulupilira mtanda wokha, popanda

Page 343: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

343 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

kusanjika manja pa mutu wa nsembeyo. Anthu amene ankapereka nsembe yotere sankapulumutsidwa ku machimo ao chifukwa inali nsembe yoperekedwa posatsata malamulo.

Mulungu adaitana Mose ndi kulankhula naye kuchokera m’kachisi ndi kunena kuti, “Ngati munthu apereka nsembe yopsereza kwathunthu azipereka ng’ombe ya mphongo yopanda chilema. Aziipereka pa khomo la chihema cha msonkhano kuti Chauta alandire. Tsono asanjike dzanja lake pa mutu pa ng’ombeyo ndipo idzalandiridwa kuti ikhale yopepesera machimo ake” (Levitiko 1:3-4).

Chauta ndi wolungama ndiponso wa malamulo. Iye anakhazikitsa malamulo achilungamo pofuna kupulumutsa anthu onse ku machimo ao. Pamene tipereka nsembe motsatira malamulo, nsembeyo imakhala yovomerezeka pa maso pa Mulungu kupepesera machimo athu. Koma chimene anthu amalakwa nchakuti iwo amangokhulupilira kuti akhoza kupulumutsidwa pa kuvomereza kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wao, pakuti Ambuye ndi

chikondi. Baibulo limatiuza kuti, “Pamenepo aliyense

amene adzatama dzina langa mopemba adzapulumuka” (Ntchito 2:21, Aroma 10:13), ndipo limatiuzanso kuti, “Simunthu aliyense womanditi Ambuye Ambuye amene adzaloœe mu ufumu wakumwamba ai” (Mateo 7:21).

Pofuna kuvomera kuti Yesu ndi Mpulumutsi, tiyenera malamulo a chipulumutso chimene Mulungu adapereka. Tikadapulumutsidwa pakungokhulupilira m’dzina la Yesu pakadakhala popanda chifukwa chakuti tikhale ndi Malembo oyera okamba za mwambo woperekera nsembe M’chipangano Chakale ndiponso amene akunenedwa pa Mateo 7:21.

Komabe, njira yodabwitsa ndi yangwiro ya chipulumutso cha Ambuye inalembedwa m’Baibulo. Zoonadi, tikhoza kuona tokha pa Levitiko 3 ndi 4 kuti wochimwa ankasanjika manja ake pa mutu pa nsembeyo ndipo magazi ake ankawaza mozungulira pa malopo. Kupereka

Page 344: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

344 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

nsembe popanda kusanjika manja kapena kupereka nsembe imene ili ndi chilema kunali kopanda phindu ndipo sikunkachotsa machimo.

Mau a M’chipangano Chakale ndi Chatsopano amagwirizana (Yesaya 34:16). Ubatizo wa Yesu mu m’tsinje wa Yolodane umafanana ndi kusanjika manja pa mutu pa nsembe m’Chipangano Chakale. Pamene anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi mu Yolodane adati, “Tsopano lino vomera pakuti umu ndi m’mene tiyenera kuchitira zimene Mulungu akufuna” (Mateo 3:15).

Pamenepa mau akuti ‘zimene Mulungu akufuna’ zitanthauza “Chilungamo cha Mulungu.” Izi zitanthauza kuti kunali koyenera kuti Yesu abatizidwe ndi Yohane Mbatizi kuti akhale ngati nsembe yochotsera machimo aanthu onse. Kunalinso koyenera kuti asanjikidwe manja ndi Yohane Mbatizi kuchotsa machimo athu onse motstira malamulo woperekera nsembe a M’chipangano Chakale, omwe ndi mwambo woperekera nsembe amene Mulungu

adakhazikitsa. Chikadakhala chinthu chosapindulitsa

kungokhulupilira mtanda wa Yesu wokha osati ubatizo wa Yesu. Uku kumakhala ngati kuseœeretsa mwazi wa Yesu Khristu (Ahebri 10:29).

Choncho mwazi wake ungakhale waphindu kuchotsa machimo m’mitima mwa anthu okhulupilira, pokhapokha atakakhulupilira kuti machimo ao onse akhululukidwa poœatula pa Yesu pamene adabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Mtumwi Yohane adachitira umboni kuti munthu amene amagonjetsa dziko lapansi ndi amene amakhulupilira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu amene anabwera mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera ndiponso mwa mwazi. Yesu anabwera mwa madzi ndi mwazi osati ndi mwazi wokha (1 Yohane 5:4-6).

Iye adafokozera ophunzira ake za zinthu zokudza iye mwini Mmalembo Oyera, kuyambira Mose ndi aneneri ndipo anationetsa kuti nsembe

Page 345: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

345 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

yopepesera machimo ya Chipangano Chakale ndi iye amene. Ndipo Davide ananena pa Masalimo, “Tsono ndidati ndilipo ndikubwera monga zidalembedwa za ine m’buku la malamulo.” (Masalimo 40:2, Ahebri 10:7).

N’chifukwa chake ubatizo wake suwononga mphamvu ya mtanda, koma ndi Uthenga Wabwino wa Mulungu umene umakwaniritsa tanthauzo ndi kufunika kwake kwa mtanda. Uthenga umenewu umatiphuzitsanso kuti sitingaomboledwe popanda ubatizo ndi mwazi wam’tengo wapatali wa Yesu Khristu. Chimene mutanthauza mukati kupulumutsidwa nchakuti mwalandira chikhululukiro cha machimo anu pakukhulupilira ubatizo ndi mwazi wa Yesu pa mtanda ndi kulandira mphatso za Mzimu Woyera (1 Yohane 5:8; Nchito 2:38).

Funso 5: Tandiuzani tanthauzo la Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu Woyera?

Yankho: Ngati tataya singano timayang’ana

kumalo amene taitaila. Sichingakhale bwino kuyang’ana kumalo amene sinasoœere chifukwa sitidzaipeza. Ndimapeza anthu otere m’mipingo yambiri masiku ano. Ngakhale kuti ali pakati pa kutsutsana pa za madzi aubatizo wathu komanso chifukwa chimene Yesu anabatizidwira ndi Yohane Mbatizi, sadzifunsa mafunso ofunikawa. Chifukwa cha machitidwe umenewu pali kugaœikana pakati pa mipingo masiku ano.

Pofuna kuthetsa timikangano topanda paketi, tiyenera kupita kuja kumene kunataikira singano kuja. Ngati tikufuna kupeza choonadi sitiyenera kukhala ndi maganizo osiyana chifukwa sitingapeze choona chake cha chipembedzo. Nchifukwa chiyani atumwi ankanena motsindika za Uthenga wa madzi ndi Mzimu Woyera ndiponso za ubatizo wa Yesu? Ichi ndi chinsinsi

Page 346: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

346 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

cha Uthenga wa madzi ndi Mzimu Woyera chimene iwo anachilandira kwa Yesu Khristu ndi kulalika pa dziko lonse lapansi.

Yesu anati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati munthu sabadwa m’madzi ndi mwa Mzimu Woyera sangathe kuloœa mu ufumu wa Mulungu.”(Yohane 3:5). Baibulo limatiuza kuti Yesu anabwera mwa madzi ndi mwazi kuti atichotsere machimo athu onse (1 Yohane 5:6) Tanthauzo la mwazi ndi mtanda. Nanga madzi atanthauzanji? Nchifukwa chiyani Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi? Nchifukwa chiyani anati, “Tsopano lino vomera pakuti umu ndi m’mene tiyenera kuchitira zimene Mulungu akufuna” (Mateo 3:15) pa nthaœi ya ubatizo wake?

Ndifuna kumvetsa tanthauzo la Uthenga wa madzi ndi Mzimu Woyera ndi ubatizo wa Yesu womwe Iye adapereka kwa ophunzira ake. Atumwi ankatsindika kwambiri za ubatizo wa Yesu mu ulaliki wao. Mtumwi Paulo adati, “Paja

mau akulu amene ndidakupatsani ndi omweo amene inenso ndidaœalandira. Mauwo ndi akuti Khristu adafera machimo athu, monga Malembo ananenera. Adaikidwa m’manda, ndipo m’kucha kwake adauka monga Malembo anenera” (1 Korinto 15:3-4).

Kodi Mau akuti Yesu adafera machimo athu monga Malembo anenera akutanthauzanji? Izi ndi zochokera M’chipangano Chakale. Iye anafa chifukwa cha ife monga momwe anenera M’chipangano Chakale. Pa Ahebri 10:1 akuti, “Malamulo a Mose ndi chithunzi chabe cha madalitso amene ali kudza osati madalitso enieniwo.” Tiyeni tione ina mwa miyambo yoperekera nsembe pa Levitiko 1:3-5. Wochimwa ankaonetsetsa kuti wakwaniritsa zonse zofunika kuti apereke bwino nsembe yopepesera machimo ake.

1) Ankapereka nsembe yopanda chilema (Levitiko 1:3).

2) Ankasanjika dzanja lake pa mutu pa

Page 347: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

347 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

nsembeyo (Levitiko 1:4). Apa tiyenera tifotokoza bwino lamulo la Mulungu: Kusanjika dzanja pa mutu wa nsembe kunali kutula machimo ake pa nsembeyo.

3) Ankaipha kupepesera machimo ake (Levitiko 1:5).

Pa Tsiku Lopereka nsembe yopepesera machimo, Aroni ankasanjika manja ake pa mutu wa mbuzi ya moyo, ndi kuulula mpulupulu za Aisraele ndi machimo, potula machimo ao pa mutu pa mbuziyo (Levitiko 16:21). Pa nthaœi imeneyo Aroni anali woimirira Aisraele. Iye ankasanjika manja ake okha pa mutu wa mbuzi kutula machimo aanthu okwana (2-3) miliyoni. Nsembe yoperekera machimo M’chipangano Chakale chinali chithunzi chabe zinthu zimene zinali kudza. Yesu anadzipereka yekha mwa chifuniro cha Mulungu kuti atiyeretse molingana ndi Malembo Oyera.

Poyamba, Yesu anabadwa monga munthu ngati Mwana Wankhosa wa Mulungu wopanda chilema.

Iye ndi Mwana m’modzi yenkha wa Mulungu ndipo ali kukhala monga Mulungu. Komanso ndi woyenera kukhala nsembe yopepesera machimo athu.

Kachiœiri, Yesu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi mu mtsinje wa Yolodane. Ubatizo umaperekedwa ‘posanjika manja’ ndipo Yohane Mbatizi ndi chidzukulu cha Aroni. Pamene Yohane anasanjika mwanja ake pa mutu wa Yesu, machimo onse aanthu anatulira pa Iye molingana ndi malamulo a Ambuye. Yesu adauza Yohane kuti, “Tsopano lino vomera” ndipo anam’batiza. Machimo athu onse tatulira Yesu Khristu. Tsiku lina Yohane anafuula kuti, “Suuyu Mwana Wankhosa wa Mulungu uja amene amachotsa machimo onse adziko lapansi” (Yohane 1:29).

Kachitatu, Yesu anafa pa mtanda kukhululukira machimo athu onse ndipo anati, “Kwatha” (Yohane 19:30) ndipo anauka kwa kufa kutilungamitsa pa maso pa Mulungu. Kumbukirani nsembe ija imene anthu ankapereka kupepesera

Page 348: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

348 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

machimo ao. Wochimwayo ankasanjika manja ake pa mutu pa nsembeyo kutula machimo ake. Munthu akaiwala kusanjika manja ake, machimo ake ankakhala chikhalire chifukwa chakuti wapereka nsembeyo mosatsatira malamulo. Ngati m’khristu sadziœa chifukwa chimene analandirira ubatizo, sangapulumutsidwe chifukwa alinawobe uchimo mu m’tima mwake.

Akhristu ambiri amangodziœa theka la ntchito ya Yesu. Mtumwi Yohane akufotokozera bwino m’kalata yake yoyamba: “Yesu Khristu ndiye amene anabwera kudzera mwa madzi ndi magazi omwe. Ndipo Mzimu Woyera ndiye amachitira umboni pakuti Mzimuyo ndiye choona” (1 Yohane 5:6). Muli mau ambiri M’baibulo amatitsimikizira za kufunika kwa ubatizo wake mu ntchito yake ya chipulumutso. Akhristu onse ayenera kubwerera ku Uthenga wa madzi ndi Mzimu Woyera.

Funso 6: Kodi ndi mau ati M’baibulo amene akutitsimikizira kuti atumwi ankatsindikapo pa za ubatizo wa Yesu?

Yankho: Chofunika ndi kusiyanitsa pakati pa

ubatizo wa Yesu ndi ubatizo wathu. Sitingabadwe mwatsoapno pakungo landira madzi a ubatizo. Tikhoza kubadwa mwatsopano pa kukhulupilira Yesu Khristu. Miyambo yowonjezerapo monga ubatizo kapena m’dulidwe zilibe mbali kwenikweni kuchipulumutso cha Mulungu. Baibulo silikamba za madzi aubatizo okha amene okhulupilira amalandira. M’malo mwake limakamba kaœiri kaœiri za ubatizo umene Yesu anaulandira kwa Yohane Mbatizi.

Kunena zoona M’baibulo muli ndime zambiri zimene zimatiuza kuti ubatizo wa Yesu ndi ofunika kwambiri pa chipulumutso chathu. M’mabuku onse anai a Uthenga Wabwino ubatizo wa Yesu ali kusimba moœilikiza. Uthenga wa Marko ukuyamba ndi nkhani ya ubatizo wa Yesu,

Page 349: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

349 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

ndipo Yohane analemba nkhani yomweyi pogwiritsa ntchito mau monga, “tsiku lina” (Yohane 1:29) “m’kucha kwake” (Yohane 2:1) pa nkhani ya tsiku limene Yesu anabatizidwa.

Yohane Mbatizi ananena Mau a Mulungu pa tsiku limene anabatiza Yesu, “Suuyu Mwana Wankhosa wa Mulungu uja amene amachotsa machimo onse adziko lapansi” (Yohane 1:29). Machimo onse adziko lapansi anaperekedwa kwa Yesu pamene Yohane anamubatiza. Ndipo kenaka Yesu anapachikidwa pa mtanda kupereka nsembe ya machimo athu, ndipo anati, “Kwatha” (Yohane 19:30), ndipo anaukanso kwakufa pa tsiku la chitatu.

Mtumwi Paulo anati, “Khristu anafa chifukwa cha machimo athu monga Malembo anenera” (1 Korinto 15:3). Malembo Oyera atanthauza Chipangano Chakale. Kodi munthu wochimwa ankapereka bwanji nsembe yake kuti machimo ake akhululukidwe? Munthu wotereyu ankasanjika manja ake pa mutu pa nsembe yakeyo sanaiphe.

Akaiwala kusanjika manja ake pa mutu wa nsembeyo sanali kukhululukidwa machimo ake chifukwa wapereka nsembe mosatsira malamulo.

Mtumwi Paulo anati, “Ndipo ndi ubatizo womwewo tidasanduka amodzi ndi Iye mu imfa yake?” (Aroma 6:3). Kubatizidwa m’dzina la Yesu kutanthauza kukhulupilira ubatizo wa Yesu mu Yolodane, osati madzi aubatizo wathu wokha. Kodi kungatheke bwanji kubatizidwa mwa Yesu? Izi zingatheke ngati tikhulupilira kuti Yohane anatulira Yesu machimo athu onse pamene Yesu anabatizidwa, tikhoza kubatizidwa m’dzina lake.

“Pajatu nonsenu amene mudasanduka amodzi ndi Khristu pakubatizidwa, mudachita ngati kuvala moyo wa Khristu” (Agalatia 3:27). Anthu onse amene adatula machimo ao pa Yesu kudzera mu ubatizo wake asanduka opanda uchimo ndipo ana oyera a Mulungu.

“Mwa Iyeyu mudachita ngati kuumbalidwa, osatitu kuumbala kwa anthu ai, koma kuvula khalidwe lanu lokonda zoipa, kuumbala kumene

Page 350: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

350 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

amachita Khristu nkumeneku” (Akolose 2:11). Njira yaku pulumukira ku machimo ndiyo ya kuumbalidwa osati kuumbalidwa ndi manja ai koma kuumbalidwa kwa mu m’tima (Aroma 2:29), uku ndiko kukhulupilira ubatizo wa Yesu umene umadula uchimo m’mitima mwathu, mtumwi Paulo akutero.

“Madziwo akufanizira ubatizo umene masiku ano umakupulumutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Khristu. Kubatizidwa kumeneku sikuchotsa litsiro la m’thupi koma kudzipereka kwa Mulungu ndi m’tima woona kudzera mwa Yesu Khristu” (1 Petro 3:21). Ubatizo ndi chifanizo chimene chimatipulumutsa. Monga tonse tikudziœa kale kuti anthu anawonongeka pa nthaœi ya Nowa, chifukwa chakusakhulupilira madzi, ngakhale lero alipobe anthu osamvera amene adzaonongeka ngakhale akuti amakhulupilira Yesu chifukwa sakhulupilira ubatizo wa Yesu, umene ndi madzi.

Mtumwi Yohane anaulula zonse zokhuza Uthenga Wabwino mu kalata yake yoyamba (1

Yohane 5:6 akuti, “Yesu Khristu ndiye amene adabwera kudzera mwa madzi okha, koma mwa madzi ndi mwa magazi omwe”). Yesu anabwera kwa ife mwa ubatizo ndi pa mtanda kuti atipulumutse ife kuchokera ku machimo. Yohane akutinso, “Mzimu Woyera, madzi ndi magazi, ndipo atatuœo amavomerezana.” (1 Yohane 5:8). Izi zikutiuza kuti ubatizo wa Yesu, mtanda, ndi Mzimu Woyera onse pamodzi akupanga chipulumutso kukhala chokwanira.

Yesu anati kwa Nikodemo, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati munthu sabadwa m’madzi ndi mwa Mzimu Woyera sangathe kuloœa mu Ufumu wa Mulungu” (Yohane 3:5). Ndife obadwanso, mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera. Chikhulupiliro cha ubatizo wake wa madzi ndi mtanda ndizofunika kuti tiomboledwe ndi kulandira Mzimu Woyera ngati mphatso. “Ichi ndi chimene Baibulo linena zokhuza zakubadwanso kachiœiri.”

Choncho mtumwi Petro anati, “Tembenukani

Page 351: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

351 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

m’tima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m’dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera” (Nchito 2:38). Chifukwa cha chikhululukiro chamachimo onse ndi mphatso ya Mzimu Woyera nthaœi zonse muyenera kukhala ndi chikhulupiliro chotsatsintha cha ubatizo wa Yesu m’mitima yanu. Kodi palitso china chimene tinganene? Pali mau ambiri amene akutsimikiza za ubatizo wake monga ngati chilungamo choyenera kudzera mu Uthenga Wabwino wa mwadzi ndi Mzimu Woyera.

Tsono tisangoima pa maphunziro oyamba enieni a Khristu. Tisachite kubwerezanso kuphunzitsa zomwe zili ngati maziko, monga za kutembunuka m’tima kusiya ntchito zosapindulitsa moyo wosatha, zakukhulupilira Mulungu za maubatizo, za kusanjika manja za kuuka kwa akufa, ndi za chiweruzo chotsiriza. Koma tiyeni tipitirire mpaka tikafike pakukhwima kwenikweni (Ahebri 6:1-2). Apa, tikhoza kupeza njira

yoperekera Uthenga Wabwino woyamba wa mpingo woyamba. Anali kuphunzitsa chiphunzitso cha ubatizo, wosanjika manja, akuuka kwa akufa, ndi chiweruzo chamuyaya kwa iwo amene atangokhala akhristu. Ife tonse tiyenera kukhulupilira m’mitima yathu kuti Yesu anatichotsera machimo athu onse kudzera mu ubatizo wake ndi imfa yake ya pa mtanda kuti aweruzidwe chifukwa cha machimo athu molingana ndi chilungamo cha malamulo a Mulungu.

Funso 7: Ndi chinthu chimene

ndimakhulupilira ndi kuphunzitsa mwina ngati inu mumawonjezera kutsimikiza kuzimene ena sakhulupilira za ubatizo wa Yesu. Kodi cha chilendo cha Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu Woyera ndi chiti?

Yankho: “Kupulumutsidwa” kutanthauza

Page 352: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

352 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

kukhala ndi chipulumutso, chikhululukiro cha machimo. Kutanthauzanso kubadwanso kachiœiri chifukwa wochimwa amakhala wolungama kudzera mukukhulupilira Uthenga Wabwino wa umoyo, umene umamupanga kuti abadwenso kachiœiri mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera kudzera m’chipulumutso cha Yesu. Mzimu Woyera umadza pa iwo amene anaomboledwa ndi kubadwanso kachiœiri ndi kuchitira umboni kuti iwo ndi ana a Mulungu. Choncho, ichi ndi chimodzi nthaœi zonse; kulandira Mzimu Woyera, kuomboledwa, ndi kubadwanso kachiœiri, kukhala mwana wa Mulungu ndi kukhala wolungama.

Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa ine.” (Yohane 14:6) chimatanthauza kuti kudzera mwa Yesu yake, mwana yekhayo wobadwa wa Mulungu, tingathe kuloœa mu ufumu wa Mulungu. Motero, tiyenera kudziœa m’mene Yesu anachotsera machimo athu onse ndi kutipanga ife

kuti tikhale oyenera kuloœa mu ufumu wake. Ngakhale, akhristu ambiri akuganiza kuti

kungotchula kokha dzina la Mulungu akhoza kupulumutsidwa. Amakhulupilira mwa Yesu popanda kutsegula mu Baibulo, popanda kudziœa zimene anachita kuti atipulumutse ku machimo athu onse. Mulungu ndi Mzimu ndipo ndi woyera mwa Iye mulibe kutsintha kapena kutsintha chithunzi, koma timakhala moyo wochimwa. Kuloœa mu ufumu wa Ambuye ndi chapafupi kudzera mwa Yesu yekha, ndipo tiyenera kukhulupilira mwa Iye mu chikhulupiliro cha malamulo a Mzimu Woyera wa moyo mwa Yesu Khristu.

Anthu ambiri sadziœa zimene Yesu anachita zokhuza chipulumutso, koma mosapenya amakhulupilira mwa Iye, ndinena “Ambuye, Ambuye!” Akuganiza kuti apulumutsidwa komabe amakhalabe ndi machimo m’mitima yao. Ngati mukadali ndi tchimo m’mitima yanu ngakhale mukhulupilire mwa Yesu, ndi kuchokera kuti

Page 353: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

353 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

kumene inu kwa kupulumutsani? Ngati wina akufunsani, “Kodi Yesu anachotsa bwanji machimo athu?” Anthu ambiri amayankha kuti, “Iye anachotsa machimoœa pamene anali pa mtanda.” Ndipo pa funso lina, “Kodi muli ndi machimo m’mitima wanu?” Amati “inde ndizoona.” Dzina la Yesu limatanthauza Mpulumutsi amene adzapulumutsa anthu ake ku machimo ao. (Mateo 1:21). Timakhulupilira mwa Yesu kuti tipulumutsidwe kuchoka ku machimo.

Komabe, ngati tikadali ndi uchimo m’mitima yathu ngakhale tikhulupilire mwa Yesu, ndife ochimwa, ogulidwa mu ukapolo wa uchimo ndipo tidzaweruzidwa. Mtumwi Paulo anati, “Motero tsopano paliberetu mlandu wotsutsa anthu amene amakhala mwa Khristu Yesu” (Aroma 8:1). Ndichodziœika kuti amene amakhalabe ndi uchimo mum’tima wake sali m’modzi wa Khrsitu Yesu. Kodi chifukwa nchiyani amakhalabe ochimwa ngati sioomboledwa ndikugura ku chipulumutso ngakhale amakhulupilira mwa

Yesu? Chifukwa ndi choti amakhulupilira mu mwazi wokha wokhetsedwa pa mtanda popanda kusanjika machimo awo pa ubatizo wa Yesu. Motero, amakhalabe ndi uchimo m’mitima yao komabe Yesu anamwalira pa mtanda chifukwa cha machimo awo.

Pali kusiyana kwakukulu pakati pa kukhulupilira ubatizo wa Yesu ndi kusakhulupilira ena ali ndi chiombolo ndikukhala olungama kudzera mukukhulupilira mu ubatizo wa Yesu, komabe ena amakhalabe ochimwa chifukwa chopanda chikhulupiliro. Mzimu Woyera sangabwere pa anthu ochimwa. Amabwera pa okhawo olungama amene anaomboledwa ndi madzi ndiponso ndi Mzimu Woyera.

Choncho, mtumwi Paulo anati, “Kodi inu simukudziœa kuti tonse amene tidasanduka amodzi ndi Khristu Yesu pakubatizidwa, ndi ubatizo womwewo tidasandukanso amodzi ndi Iye mu imfa yake?” (Aroma 6:3). Anthu ambiri amakhulupilira kuti Yesu anachotsa machimo athu pa mtanda,

Page 354: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

354 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

komabe sitinganene kuti tilibe machimo m’mitima yathu ngati sitikhulupilira mu ubatizo mwa Yesu. Ngati tichita izi, tiri ndi tchimo lonena zonama kwa Mulungu ndipo amalakwira maganizo awo.

Tikadali ndi uchimo m’mitima yathu ngati sitipereka machimo athu pa Iye kudzera mukukhulupilira mu ubatizo wake. Ngati munthu payekha sakhulupilira Uthenga Wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi mtanda wake, azagwa mu miyambo ndipo adzafa ndi uchimo. Choncho ngakhale achite china chili chonse, monga kupembeza mumaphiri ndi kupembedzera chikhululukiro, amaona machimo amakhalabe m’mitima yao.

Yesu anati, “Simunthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye,’ amene adzaloœe mu ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloœe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna. Patsiku lachiweruzo anthu ambiri azidzanena kuti, Ambuye, Ambuye, kodi suja ife tinkalalika Mau a Mulungu m’dzina lanu? Suja tinkatulutsa mizimu

yonyansa potchula dzina lanu? Suja tinkhachita ntchito zamphamvu zambiri m’dzina lanu? Apo Ine ndidzaœauza poyera kuti, ‘Sindidaakudziœani konse. Chokani apa, anthu ochita zoipa.’” (Mateo 7:21-23).

“Kodi amene akuchita zinthu zopanda malamulo” ndi ati? Ndi amene sanalandire chiombolo chokwanira m’mitima yao chifukwa chokhulupilira za mtanda wokha. Tinali kutsatira kusamala miyambo ngati sitikhulupilira mfundo yoti Yesu anatipulumutsa kudzera mu ubatizo wake ndi mtanda wake. Sitinganene kuti tiri ndi chikhulupiliro choona ngati sitidziœa ubatizo wa Yesu ndi mtanda wake.

Yesu anati, ngati anthu akufuna kubadwanso kachiœiri, ndikotheka pokhapo kudzera mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera. Monga momwe anthu anaomboledwa kuchokera ku madzi osefuka monga okhao amene anali muchombo cha Nowa, mukhoza kukhala oomboledwa, ndi chikhulupiliro cha machimo onse, ndi kukhala ndi chikhulupiliro

Page 355: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

355 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

choona cha umoyo pokhapo ngati mukhulupilira Uthenga Wabwino wa madzi ndi wa Mzimu Woyera, simungalandire chikhululukiro cha machimo kapena kukhala ana a Mulungu.

Funso 8: Ndizoona kuti kukhulupilira mwa

Yesu ku nandipulumutsa. Ndinali ndi mtendere ndi kumvetsa mum’tima wanga, koma tsopano ndasokonezedwa ndi Uthenga wanu. Kodi ndiyenera kukhulupilira mu ubatizo wake ndiponso ndi mtanda wake kuti ndipulumutsidwe?

Yankho: Ngati simukhulupilira mwa ubatizo

wa Yesu, ndizodziœikiratu kuti muli ndi uchimo mum’tima. Mtumwi Yohane anati, “tikanena kuti tilibe tchimo, tikudzinyenga, ndipo mwa ife mulibe choona” (1 Yohane 1:8). Ngati m’manena kuti mulibe tchimo komabe muli nalo chifukwa simukhulupilira ubatizo wa Yesu, ndi tchimo

lolakwira maganizo athu ndipo choona sichili mwa ife. Kumvetsa za chikhulupiliro kumabwera ngati tilandira chikhululukiro cha machimo ndikulandira Mzimu Woyera monga ngati mphatso kudzera mukukhulupilira mwa ubatizo wa Yesu ndi imfa yake pa mtanda.

Mtumwi Paulo anati, “Koma palibe konse Uthenga Wabwino wina” (Agatia 1:7). Palibe wina koma Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu Woyera umene atumwi analandira kuchokera kwa Yesu ndi kuulalika kwa anthu ungatipulumutse ife kuchokera kumachimo athu onse. Ngati sitikhulupilira Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu Woyera, umene atumwi analalikira, tikadali ndi uchimo.

Kodi tingakhale bwanji wokhulupilira chipulumutso chathu pamene tikadali ndi uchimo? Pamene tionetsa khalidwe la bwino pa maso pa Mulungu, timadziœa kuti tili ndi chisangalalo ndi kuzindikira chipulumutso chathu, pamene tisowa kuzindikira ndi kukhala ndi mantha chifukwa cha

Page 356: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

356 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

kulema ndi machimo m’mitima yathu ndi pamene tichimwa. Ndichipulumutso chimene chimangidwa pa maganizo ndi zochitika zathu, osati zimene Mulungu wavomereza. Chipulumutso chimene chimangidwa pa maganizo athu chiyenera kukula pang’ono kudzera mukuyeretsedwa chifukwa cha chikhulupiliro cha machimo tsiku ndi tsiku .

Amene akhulupilira chipulumutso chonama amaganiza kuti tsiku lina adzapulumutsidwa, ngati apitiliza kukhala moyo woyera, kufunsira chikhululukiro masiku onse ndi kusunga malamulo kudzera mu ntchito zao. Ngakhale achite choncho, akadali wochimwabe ngati sanapereke machimo awo pa Yesu kudzera mu chikhulupiliro cha ubatizo wa Yesu.

Chipulumutso chimene Mulungu anapanga ndichokwanira, chimene chimatiuza kuti Yesu anachotsa machimo onse adziko lapansi kudzera mu chikhulupiliro cha ubatizo wake ndi Yohane Mbatizi mu mtsinje wa Yolodane ndi kuchotsa onse pamene anali pa mtanda.

Mtumwi Yohane anati, “Koma tikamavomereza kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupilira ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse” (1 Yohane 1:9). Ngati machimo athu onse sanakhululukidwe kudzera mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi wa Mzimu Woyera ngati sitidziœa izi, tiyenera kuvomereza pa maso pa Ambuye kuti ndife ochimwabe ngakhale tikhulupilire mwa Iye ndipo kuti tikupita ku gehena chifukwa machimo athu sangachotsedwe popanda Uthenga Wabwino wa madzi ndi wa Mzimu Woyera ndi m’mene tchimo lilitere. Uku ndi kuvomereza koona kwa machimo. Pamene tivomereza machimo athu munjira iyi, Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu Woyera achotsa machimo athu panthaœi imodzi ndi kutilungamitsa.

Tsopano ndi nthaœi yoyenera (2 Korinto 6:2). Aliyense amene akumva ndi kukhulupilira mu Uthenga Wabwino wa ubatizo wa Yesu ndi imfa

Page 357: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

357 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

yake pa mtanda ndi opulumutsidwa ku machimo ake onse, amakhala wolungama, ndipo ali ndi chikhulupiliro cholimba kotero kuti ndi okonzeka kuloœa mu ufumu wakumwamba nthaœi iliyonse Ambuye akabwera. Kumvetsa kwathu kwa ziphunzitsi ndi maphunziro a uzimu sizingatipulumutse kumachimo athu. Izi ndi njira zochenjera zimene Satana anaika mu maganizo a anthu. Tiyenera kubwerera ku Uthenga Wabwino wamadzi ndi wa Mzimu Woyera ndi kulandira chipulumutso choona cha Yesu kuchokera ku machimo amitima yathu. Uku ndi kum’konda iye ndiponso ndi ntchito zake.

Funso 9: Ngati kumvetsa kwanu kwa madzi

ndi Mzimu Woyera kunali kokhoza, ndiye kuti chipulumutso sichikanatheka kwa wakuba pa mtanda paja. Ngati kuti Mulungu siwachilungamo, chifukwa anapwanya yekha lamulo lolomera mu ufumu wakumwamba.

Kodi mungafotokoze bwanji za chipulumutso cha wakuba pa mtanda paja.

Yankho: Panthaœi ija, a Yuda onse anali

kudikira mupulumutsi amene Mulungu analonjeza, choncho, anali kudziœa za malamulo anjira yoperekera nsembe, imene Mulungu anapereka kudzera kwa Mose, kupambana kubwera moyenera malamulo a Mulungu, ndi kuti adzawaombola kumachimo ao onse.

Komabe, sanakhulupilire mfundo ya ubatizo wa Yesu ndi Yohane Mbatizi kuti unachoka kwa Mulungu ndipo kuti unali wopereka machimo onse adziko lapansi pa Yesu (Marko 11:27-33), koma analikuona Iye ngati kuti ndi munthu amene anatsogolera anthu kunjira yachabe ndipo anthu anampachika Iye pa mtanda.

Monga momwe Aroma anali kutetezedwa kunyoza kapena kupachika anzao monga mwa lamulo (Ntchito 22:25-29; 23:27), tikuona kuti akuba pa mtanda paja sanali Aroma ai koma a

Page 358: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

358 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

Yuda. Tikuonanso kuti wakuba uja anali mu Yuda amene anali kulemekeza Mulungu kuchokera ku mau ake adati, “Inu mukandikumbukire mukafika mu ufumu wanu” (Luka 23:42). Chifukwa Uthenga Wabwino wa ufumu wakumwamba siunali kulalikidwa kwa anthu amitundu kufikira Petro atalalika Uthengawo kwa iwo. (Ntchito 10:1—11:18). Wakuba anadziœa kale malamulo ndi njira yansembe yochotsera machimo, imene Mulungu anapereka kwa Mose. Ndipo anakhulupilira kuti mupulumutsi adzabwera motsatira malamulo a Mulungu.

Amene amabwera kwa Mulungu ayenera kuvomereza kuti ndi ochimwa, ndipo ndi oyenera kupita kugehena chifukwa cha machimo awo. Wakuba anavomereza machimo ake ndipo anati, “Tsonotu ife zikutiyeneradi zimenezi, tikulandira zolingana ndi zimene tidachita” (Luka 23:41). Tikhoza kuona kuti wakuba uja anali kuopa Mulungu ndipo chiyembekezo chake chinali kuopa Mulungu ndipo chiyembekezo chake chinali pa

ufumu wa Mulungu wakumwamba kuchokera ku mau ake, adati, “Ambuye, Inu, mukandikumbukire mukafika mu Ufumu wanu.” (Luka 23:42).

Iye adati, “Koma aœa sadachite cholakwa chilichonse” (Luka 23:41). Kodi wakuba uja adadziœa bwanji zimene Yesu adachita? Anakhulupilira kuti Yesu anabadwa mwa mphamvu ya Mzimu Woyera ndi mtsikana Maria, anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi, woimirira anthu onse, amene anachotsa machimo adziko lapansi, ndipo anapachikidwa pa mtanda. Anali mu Yuda amene anakhulupilira zimene Yesu anachita mum’tima wake, ngakhale anapachikidwa pa mtanda ndi kulandira zimene zinali zomuyenera pa zimene anachita pa dziko lapansi.

Kwa iwo amene analikuvomereza machimo awo kudzera mu ubatizo wa Yohane analikudziœa chilungamo cha Mulungu pamene anamva kuti machimo ao onse aperekedwa pa Yesu kudzera mu ubatizo wake. Koma iwo amene sanalandire ubatizo wa Yohane Mbatizi wolapa machimo

Page 359: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

359 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

anakana chifuniro cha Mulungu chifukwa sanakhulupilire ubatizo wa Yesu, mpang’ono pomwe (Luka 7:28-30).

Mosiyana, wakuba amene anapulumutsidwa anavomereza kuti zonse zimene Yesu anachita sizinali zolakwika ai, koma zinali zolungama koma ena Ayuda sanali kukhulupilira izi. Anali kunena kuti Yesu anali wolungama chifukwa anavomereza machimo ake kudzera mu ubatizo wa Yohane ndi kuti Yesu anachotsa machimo ake onse kudzera mu ubatizo wake. Ndizoona anali wopumutsidwa. Analinso munthu amene anakhulupilira mu Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu Woyera. Chifukwa Mulungu ndi wolungama, amalungamitsa iwo okhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi mtanda wake moyenera ndimalamulo ake.

Funso 10: Motero Mulungu ndi wachikondi

ndi wachifundo, sangatiyetse olungama

ngakhale tili ndi machimo m’mitima yathu ngati tikhulupilira mwa Yesu?

Yankho: Mulungu ndi chikondi ndiponso ndi

kulungama. Komanso, Iye ndi mosakondera ndipo amaweruza momwe tchimo lili (Aroma 6:23) akuti, Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Zitanthauza kuti munthu wochimwa ndi woyenera kupita kugehena ataweruzidwa. Amapatula olungama kuchoka kwa ochimwa monga ngati amachitira ndi masana ndi usiku. Mulungu amanena kwa iwo amene alibe uchimo kudzera mukukhulupilira kuti Yesu anachotsa machimo awo onse kudzera mu ubatizo wake ndi kupachikidwa pa mtanda ndi kuweruzidwa chifukwa cha machimo awo, kuti akhale olungama.

Komabe kwa iwo amene ali ndi uchimo mwa iwo, chifukwa sakhulupilira mu ubatizo wa Yesu, monga momwe anthu anachitira mumasiku a Nowa. Ngati Mulungu amaona kuti amene ali ndi

Page 360: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

360 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

uchimo ndi olungama ndi kuti alibe tchimo, ndiye kuti akunama ndipo sangaweruze kapena kulamulira zonse zolengedwa zake.

Iye anati, “Chifukwa ine sindidzakhululukira wochimwa” (Esksodo 23:7) ofooka ndi amene amadalira ndikutsatira miyambo ya anthu, kuika pambali Uthenga Wabwino wa madzi aubatizo ndi Mzimu Woyera, umene Mulungu anatiombolera kuchoka ku machimo athu m’njira yoyenera ndi yachilungamo. Yesu anati, “Ngolakwa paza kuchimwa, chifukwa sandikhulupilira” (Yohane 16:9). Ndi tchimo lokhala latsala pa dziko lapansi, tsono kusakhulupilira mfundo yoti Yesu anachotsa machimo athu onse kudzera mu ubatizo wake ndi imfa yake pa mtanda ndipo anakhala mupulumutsi wathu. Ili ndi tchimo lonyozera Mzimu Woyera, limene silingakhululukidwe. Palibe njira ina kwa iwo amene anyozera Mzimu Woyera kuti angapulumutsidwe chifukwa sakhulupilira kuti Yesu anachotsa machimo awo onse.

Mtumwi Yohane anati, “Aliyense amene

amachimwa, alinso ndi mlandu wakuphwanya malamulo. Paja kuchimwa nkuphwanya malamulo kumene. Mukudziœa kuti Khristu adaoneka kuti adzachotse machimo, ndipo mwa Iye mulibe tchimo. Munthu aliyense wokhala mwa Khristu, sachimwa. Aliyense amene amachimwa, sadamuwone ndipo sadam’dziœe” (1 Yohane 3:4-6). Ndikuchimwa kusakhulupilira mfundo yoti Yesu anachotsa machimo athu onse kudzera mu ubatizo wake ndi imfa yake pa mtanda, ndipo aliyense amene amachimwa ali ndi mlandu. Wophwanya malamulo ndi adzamukana patsiku lotsiriza.

Kwa iwo amene amakhala mwa Iye alibe tchimo ndipo ali pamodzi naye. Amene anapereka moyo wao wonse wamachimo pa Iye kudzera mu ubatizo wake alibe tchimo ngakhale akhalebe ndi uchimo chifukwa chakufooka kwa moyo wathupi.

Mulungu amanena kuti, amene anapereka machimo awo pa Yesu ndipo anakhala woyeretsedwa kudzera mu malamulo a Mzimu

Page 361: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

361 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

Woyera wa moyo, kuti akhale olungama. Ndipo amaœapatsa Mzimu Woyera ngati mphatso. Mzimu Woyera samabwera pa iwo amene ali ndi machimo m’mitima yao. Baibulo limati, “Inu sindinu Mulungu wokondwerera machimo. Simufuna zoipa pa maso panu” (Masalimo 5:4). Mzimu Woyera wa Mulungu siumakhala m’mitima ya iwo amene ali ndi machimo mwa iwo. Wochimwa amene alibe Mzimu Woyera mwa iye akhoza kunena kuti alibe tchimo motsatira ziphunzitso za Mau a Mulungu ndi maganizo ake. Motero, sanganene kuti alibe tchimo ndi kuti ndiwolungama mum’tima chifukwa chikhulupiliro ndi maganizo ake zimutsutsa.

Choncho, munthu wotero amanena kuti ndine wochimwa pa maso pa anthu ena, ndipo munthu wolungama pa maso pa Mulungu. Koma Mulungu samanena munthu wochimwa kuti ndi wolungama. Wochimwa ndi woyenera kukhulupilira Uthenga Wabwino wa madzi aubatizo ndi Mzimu Woyera.

Funso 11: Ngati tinena kuti Yesu anachotsa kale machimo athu akale, machimo atsopano ndi am’tsogolo motsatira mfundo ayi, nanga tsogolo la munthu lidakhala bwanji ngati adzapitiriza kuchimwa ndi kuganiza mfundo yoti machimo ake anakhululukidwa kale chifukwa chokhulupilira ubatizo wa Yesu ndi imfwa yake ya pa mtanda. Ngakhale kuti munthu uyu angaphe mnzake, adzadziœa kuti machimo ake anakhululukidwa ngakhale tchimo monga ili kudzera pa imfa ya Yesu pa mtanda. Choncho adzapitiriza kuchimwa popanda kubwerera ku mbuyo chifukwa chokhulupilira kuti Yesu anakhululukira kale machimo ngakhale machimo am’tsogolo. Choncho fotokozani bwino zinthu zimenezi.

Yankho: Choyamba pa zonse, ndikuthokoza

inu chifukwa cha, kufunsa mafunsa okhuza Uthenga Wabwino wa madzi a ubatizo ndi Mzimu Woyera. Mafunso amene mwa funsa ndi

Page 362: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

362 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

amaganizo amene akhristu ambiri amakhala nao asanabadwenso kachiœiri. Ndikudziœa kuti mafunso anu akuchokera mukuta yam’tima kapena kuda nkhaœa ngati ndikoyenera kuti wokhulupilira mwa Yesu apitiliza kuchimwa ngakhale m’tsogolo. Koma, ndikufuna kukuuzani kuti anthu amene akhulupilira Uthenga Wabwino wa ubatizo wamadzi ndi wa Mzimu Woyera sakwanitsa kukhala moyo ngati umene mwanenawu koma amachonetsa moyo woyera chabe.

Choyamba muyenera kuganizira za izi. Ngati ndi zoona kuti muli Mzimu Woyera mwa inu ndiye kuti mubereka zipatso za Mzimu Woyera ngakhale musafune. Munjira ina, ngati simuli ndi Mzimu Woyera m’kati mwanu simungabereke zipatso za Mzimu Woyera ngakhale muyetse bwanji. Kodi zingatheke bwanji kuti munthu abereke zipatso za Mzimu Woyera ngati iye ali mu m’tima wake Mzimu Woyera ngakhale akhulupilire mwa Yesu? Izi sizingatheke. Ambuye, akuti m’tengo woipa siungabereke

zipatso zabwino (Mateo 7:17-18). Tsopano ndikufuna kukufunsani funso ili ndipo

ndi perekatso yankho lake. Mukukhulupilirira mwa Yesu, koma mumakhaladi ndi moyo wogonjetsa machimo adziko lapansi? Kodi mukukhala ngati kapolo wolungama wa Mulungu wogonjetsa machimo adziko lapansi, kutumikira Ambuye ndi kutsogololera ena kuchipulumutso pofalitsa Uthenga Wabwino wa madzi aubatizo ndi Mzimu Woyera umene Ambuye akunena?

Kodi ndi olungama amene alibe ngakhale uchimo wina uli wonse pamene m’takhulupilira mwa Yesu? Chikulupiliro choona ndi Uthenga Wabwino umene ungakupatseni yankho loona pa funsoli kuti muyankhe kuti inde, Uthenga Wabwino wa madzi ndi Mzimu Woyera umene Ambuye anachitira umboni M’chipangano Chakale ndi M’chingapano Chatsopano.

Sindikufuna kuti ndikutengeni ku magule ena mwa amodzi achipembedzo mwa magule ambiri mwa iwo akupezeka panthaœi yalero ya

Page 363: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

363 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

chikhristu. Timachimwabe padziko lapansi ngakhale tikhulupilire mwa Yesu. Motero Ambuye athu anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi ndipo anakhetsa mwazi wake pa mtanda kuti atipulumutse ife ku machimo onse adziko lapansi. Choncho, Mulungu anachita ntchito yolungama kwa ife ndipo tili opulumutsidwa ku machimo adziko lapansi kudzera mu chikhulupiliro chathu mu chilungamo cha Mulungu ndi ubatizo wa Ambuye ndi mwa mwazi amene anachotsera machimo athu.

Ndikufuna kukufunsani funso lotsatira. Kodi muli omasuka ku machimo amumaganizo anu? Simunali ochimwa pamene musanakhulupilire mwa Yesu, monga momwe munalili poyamba mutakhulupilira mwa Iye? Ngati izi ndi zoona, ndiye kuti chifukwa simunadziœe za ubatizo wa madzi, ndi wa Mzimu Woyera. Choncho, mwagwa mu vuto ndikuchionongeko cha thupi chifukwa mulibe Mzimu Woyera mu m’tima wanu.

Ngakhale mukhale okhulupilira woona wa Yesu

mukhoza kuthaœa maganizo athupi chifukwa chochepetsa maganizo mu m’tima ndi kulandira Uthenga Wabwino wa madzi ubatizo ndi Mzimu Woyera. Muyenera kumvetsa nokha mu m’tima wanu ndi kubwerera ku Mau a Mulungu kuti mvetse mfundo ya Uthenga Wabwino wa madzi aubatizo ndi Mzimu Woyera kuti ndi woona.

Pali anthu ambiri mdziko lapansi amene amasintha malamulo a chipulumutso chimene Mulungu anatikonzera mu njira zambiri zimene akufuna, ngakhale anene kuti akukhulupilira mwa Ambuye. Ngati inunso muli ngati m’modzi mwa anthu aœa, m’nzatsiyidwa ndi Ambuye pa tsiku lotsiriza ndi kuyembekezera kuti izi siziyenera kuchitika kwa wina aliyense mu dziko lapansi. Ndikukhulupilira kuti inu ndinu anthu amene akhulupilira kuti imfa ya Yesu pa mtanda ndikukhetsa mwazi wake ndi njira yokhayo imene ingakupulumutseni, ndipo kuti mwafunsa mafunso awo kuchokera pam’tima wanu kuti nthaœi yotsalayi mukhale kutali ndi uchimo.

Page 364: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

364 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

Komabe, maganizo anu ndi maganizo athupi Paulo anati, “Anthu otere sagonjetsa malamulo a Mulungu, ndipo kunena zoona sangathedi kuœagonjera” (Arom 8:7). Ngati mfunitsitsa kukhala ndi chikhulupiliro chimene chingasangalatse Mulungu, muyenera kukhulupilira mu ntchito imene Ambuye anachita imene Iye anadzera pa dziko lapansi kudzera mwa namwali Maria, ndi kuchotsa machimo aanthu onse pobatizidwa mu mtsinje wa Yolodane analandira kuchokera kwa Yohane Mbatizi, ndi kukwaniritsa chilungamo chonse cha Mulungu.

Kodi muganiza kuti ndi ndani angakwanitse chilungamo chantchito ya Mulungu, munthu wolungama kapena wochimwa? Wochimwa akadali ndi uchimo chifukwa sanalandire chikhululukiro cha machimo pa maso pa Mulungu. Choncho munthu wotero akuchitira chiwerizo cha Mulungu chifukwa cha machimo ake. Mulungu sangalole ochimwa mu ufumu wake. Chifukwa ndi ichi, “Inu sindinu Mulungu wokondwerera

machimo. Simufuna zoipa pamaso panu.” (Masalimo 5:4). Mulungu anati ngati wochimwa wachoka pa maso pake ndipo akapempha kanthu kwa Iye. Iye sangamve kupembeza kwa ochimwa chifukwa, “Machimo anu adakulekanitsa ndi Mulungu wanu.” (Yesaya 59:1-2). Wochimwa nzoonadi adzapita ku gehena chifukwa mphatso ya uchimo ndi imfa. Ndi anthu okhao amene anakhaloyera ndi olungama ndiponso sakhala ndi uchimo m’kati m’mitima yao amene angachite ntchito zolungama. Moonjezerapo, Mzimu Woyera amakhala m’kati m’mitima ya anthu olungama amene sakhala ndi uchimo pamene akhulupilira mu ubatizo wa Yesu ndi imfa yake ya pa mtanda. Mtumwi Petro patsiku la Pentekositi anati, “Tembenukani m’tima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m’dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera” (Ntchito 2:38).

Ndime iyi ikunena kuti anthu amene ayenera kukhulupilira zoona mwa Yesu amene

Page 365: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

365 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi, ndi kuchotsa machimo onse, pambuyo pake ndi kukhetsa mwazi wake pa mtanda ndikuuka kwa akufa. Pamene akhulupilira mu izi, ayenera kulandira ubatizo kudzera mu dzina la Yesu Khristu monga ngati chitsanzo cha chikhulupiliro. Yesu analamula ophunzira ake kuti abatize aliyense m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mizmu Woyera (mateo 28:19).

Mopitirirapo, mtumwi Paulo anati, “Koma ngati munthu aliyense alibe Mzimu wa Khristu” (Aroma 8:9). Mulungu amapereka Mzimu Woyera kwa olungama kuti aonetse kuti iwo ndi ana ake. Mulibe Mzimu Woyera mwa anthu ochimwa chifukwa ali ndi uchimo. Mzimu Woyera sakonda tchimo koma amafuna chiyero (kukhala patali ndi tchimo.) Mzimu amatsogolera anthu olungama m’njira ya chilungamo ndiponso ndi kuœafikitsa ku chifuniro cha Atate. Motero, kodi chifuniro cha Atate ndi chiti? Ndi kufalitsa Uthenga Wabwino wa ubatizo wa madzi ndi wa Mzimu Woyera kwa

anthu a mtundu uli wonse ndi kuœabatiza monga momwe Yesu analamulira.

Matupi a olungama ndi ochimwa amachimwabe mpaka iwo atamwalira. Komabe, Ambuye anagwira ntchito yolungama yochotsa machimo onse amene anthu amachimwa ndi matupi awo ndiponso ndi mitima kudzera mu ubatizo ndi mwazi wake. Ichi ndi chilungamo cha Mulungu chimene Yesu anakwaniritsa. M’baibulo analemba motero, (Aroma 1:17) “Uthengawutu umatiululira m’mene anthu amapezeka kuti ngolungama pamaso pa Mulungu. Munthu wolungama pakukhulupilira adzakhala ndi moyo.” Munthu amene walandira chikhululukiro cha machimo atakhulupilira chilungamo cha Mulungu adzakhoza mayeso osafuna zoipa koma adzachimwa kudzera mu thupi komabe adzatsatira chilungamo. Izi zimatheka mwa mphamvu ya Mzimu Woyera, amene amadza pa iwo amene akhulupilira Uthenga Wabwino wa madzi aubatizo ndi Mzimu Woyera.

Page 366: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

366 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

Machimo onse akale, atsopano ndi am’tsogolo a munthu wolungama anaperekedwa pa Yesu pa nthaœi imene anali kubatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Thupi la munthu wolungama linafanso pamodzi ndi Yesu chifukwa cha machimo awo. Pamene munthu akhulupilira izi, amaphatikizana ndi Yesu mu imfa yake. Ichi chimakhalanso chiweruzo cha machimo ake (Aroma 6).

Choncho, ngakhale kuti thupi la munthu wolungama limene linafa pa mtanda pamodzi ndi Yesu lilibe kufuna zina koma kuchimwa kopitirira moyo wake wonse, Mzimu Woyera umakhala mu m’tima wake ndi kum’tsogolera iye kuti atsatire Mzimu Woyera. Munthu wolungama amatsatira Mzimu Woyera ndi kugwira ntchito yake chifukwa Mzimu Woyera amakhala mwa iye.

Ngakhale pa nthaœi ya atumwi anthu ambiri anali kukhulupilira kuti anthu amene akhulupilira Uthenga Wabwino wa madzi aubatizo ndi Mzimu Woyera sangakhale moyo wao wonse ndi makhalidwe oyera chifukwa m’mitima yao

munalibe tchimo. Komabe anthu otero ndi amene sanalikumvetsa za Uthenga Wabwino woona wa ubatizo wa madzi ndi Mzimu Woyera zimene atumwi analikufalitsa, monga ngati maganizo athupi. Motero, mtumwi Paulo anati kwa anthu awa, “Tsopano tinene chiyani? Kodi tinene kuti tizingokhalabe mu uchimo kuti kukoma mu m’tima kwa Mulungu kuchuluke? Iai, mpang’ono pomwe. Tidachita ngati kufa nkulekana ndi uchimo. Nanga tingakhalebe mu uchimowo bwanji?” (Aroma 6:1-2). Anapitiriza nati, “Tiyamike Mulungu! Adzandipulumutsa ndiye kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye athu! Motero ineyo, ndi m’tima wanga ndimatumikira malamulo a Mulungu, chonsecho ndikhalidwe langa lokonda zoipa ndimatumikira lamulo l uchimo” (Aroma 7:25).

Potsiriza, thupi la munthu wolungama silili lokwanira ndipo sitingasankhe koma kuchimwabe. Koma amatsatirabe mzimu Woyera, kufalitsa Uthenga Wabwino pa dziko lapansi lonse lapansi. Wolungama amayenda ndi Mzimu Woyera

Page 367: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

367 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

chifukwa mu m’tima yao ali ndi chisomo cha Mulungu. “Bwanji tsono? Kodi tizichimwabe popeza kuti chimene chimalamulira moyo wathu si malamulo, koma kukakoma m’tima kwa Mulungu? Iai, mpang’ono pomwe. Mukudziœa paja kuti mukadzipereka kuti mukhale akapolo a munthu nkumamvera, ndiye kuti ndinu akapolo a munthu womverayo. Tsono ngati ndinu akapolo a uchimo, mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo a Mulungu, mudzakhala olungama pamaso pake” (Aroma 6:15-16).

Monga momwe maluœo oona ndi osiyana ndi maluœa ochita kupangidwa ndi anthu, wolamulira m’mitima ya anthu olungama ndi wochimwa ndi osiyana. Motero olamulira mu m’tima wa munthu wolungma ndi Mzimu Woyera, akhoza kuyenda mu Mzimu Woyera ndi kutsatira choona chachilungamo mu umoyo wake, umene umsangalatsa Mulungu. Munjira ina, wochimwa alibe kusankha koma kupitiriza kuchimwa chifukwa womulamulira mu m’tima wake ndi

uchimo wokhao. Wochimwa sangakhale moyo woyera chifukwa alibe Mzimu Woyera chifukwa cha machimo ambiri amene ali ndi iye.

Chikhulupiliro choti okhulupilira Uthenga Wabwino wa madzi na ubatizo ndi Mzimu Woyera sangakhale moyo woyera ndi maganizo chabe ochokera ku thupi ai. Anthu ambiri lero sakumvetsa za moyo olungama ngakhale adzindikire Uthenga Wabwino wa madzi na ubatizo ndi Mzimu Woyera ngati Uthenga Wabwino woona, chifukwa saudziœa ndiponso sanaulandire m’mitima yao.

Kodi muganiza chiyani zokhuzana ndi ntchito yolungama yopereka zopereka ndi zinthu zambiri ndi nsembe kuti zifalitse Uthenga Wabwino wa aubatizo wa madzi ndi Mzimu Woyera chifukwa ali ndi Uthenga Wabwino?

Wolungama amachita zabwino kudzera muchikhulupiliro m’kati mwa zoona za chilungamo cha Mulungu. Amene akuyetsa kutsatira kuchita chilungamo ndi obadwa mwa

Page 368: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

368 Funso & Yankho

◄ Zam'kati ►

Mulungu. Tikufuna kuti anthu onse adziœe za Uthenga Wabwino umene Yesu anachotsera machimo anthu onse kudzera mu ubatizo wake ndi mwazi wake.

Mopitirirapo, chimene tikuyembeza ndi choti inu ndi anthu ena mulandire Uthenga wa Chipulumutso kuchokera ku machimo adziko lapandi kudzera mukukhulupilira Uthenga Wabwino wa ubatizo wa madzi ndi Mzimu Woyera.

Page 369: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

e-Bookse-Books

?

USER GUIDE

How to Read

Easier Way to Read

Cover Page

TheNewLifeMission

Page 370: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

370 Thandodzo kwaowerenga

Thandodzokwaowerenga ►◄

HOW TO READ

PAGING THROUGH THE BOOK

Page by Page

Skiping to a Page

Page 371: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

371 Thandodzo kwaowerenga

Thandodzokwaowerenga ►◄

PAGE BY PAGE

• KeyBoard

1) Page Up / Page Down Key Page Up = Previous Page, Page Down = Next Page

2) Arrow Key

← or ↑ = Previous Page, → or ↓ = Next Page

• Acrobat Reader Menu Button

◄ = Previous Page, ► = Next Page • Link

◄ = Previous Page, ► = Next Page Zam'kati = Go to Table of Contents

Page 372: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

372 Thandodzo kwaowerenga

Thandodzokwaowerenga ►◄

SKIPING TO A PAGE

1) Key Board

Ctrl + N Key : The number of page you want to go to.

2) Acrobat Reader Scroll Bar

Click and drag in the scroll bar until the page number in the number field matches the page you want to go to.

Page 373: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

373 Thandodzo kwaowerenga

Thandodzokwaowerenga ◄

EASIER WAY TO READ

Using Bookmarks

You can move easily where you want by using bookmarks

- Show bookmarks : Press F5 Key on your keyboard

- Hide bookmarks : Press F5 Key again

Page 374: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

◄ Zam'kati ►

www.nlmafghanistan.comwww.nlmafrikaans.comwww.nlmalbania.comwww.nlmamharic.comwww.nlmangola.comwww.nlmarabemirates.comwww.nlmarabic.comwww.nlmargentina.comwww.nlmarmenia.comwww.nlmaruba.comwww.nlmaustralia.comwww.nlmaustria.comwww.nlmbahamas.comwww.nlmbahrain.comwww.nlmbangladesh.comwww.nlmbelarus.comwww.nlmbelgium.comwww.nlmbengali.comwww.nlmbenin.comwww.nlmbhutan.comwww.nlmbolivia.com

www.nlmbotswana.comwww.nlmbrasil.comwww.nlmbriton.comwww.nlmbrunei.comwww.nlmbulgalia.comwww.nlmburkinafaso.comwww.nlmburundi.comwww.nlmcameroon.comwww.nlmcanada.comwww.nlmcebuano.comwww.nlmchichewa.comwww.nlmchile.comwww.nlmchin.comwww.nlmchina.comwww.nlmcolombia.comwww.nlmcongo.comwww.nlmcostarica.comwww.nlmcotedivoire.comwww.nlmcroatia.comwww.nlmczech.comwww.nlmdenmark.com

www.nlmdioula.comwww.nlmdominica.comwww.nlmdutch.comwww.nlmecuador.comwww.nlmegypt.comwww.nlmelsalvador.comwww.nlmequatorialguinea.comwww.nlmethiopia.comwww.nlmfinland.comwww.nlmfrance.comwww.nlmfrench.comwww.nlmgabon.comwww.nlmgeorgian.comwww.nlmgerman.comwww.nlmgermany.comwww.nlmghana.comwww.nlmgreek.comwww.nlmgrenada.comwww.nlmguatemala.com

A

B

C

D

E

F

G

Please find your vernacular websites below.

You can download Christian e-books and request Christian books for free.

Feel free to visit our websites below right now!

Please find your vernacular websites below.

You can download Christian e-books and request Christian books for free.

Feel free to visit our websites below right now!

Please find your vernacular websites below.

You can download Christian e-books and request Christian books for free.

Feel free to visit our websites below right now!

The Official Website of The New Life Mission

www.nlmission.comwww.nlmission.comor

www.bjnewlife.orgwww.bjnewlife.orgW

The New Life Mission

orldwide websites of

� Some of these websites may not work because they are still under construction.

Page 375: Kodi mwabadwadi mwatsopano mwa madzi ndi mwa Mzimu Woyera?

◄ Zam'kati ►

www.nlmgujarati.comwww.nlmhaiti.comwww.nlmhindi.comwww.nlmholland.comwww.nlmhonduras.comwww.nlmhungary.comwww.nlm-india.comwww.nlmindonesia.comwww.nlmiran.comwww.nlmiraq.comwww.nlmisrael.comwww.nlmitaly.comwww.nlmjamaica.comwww.nlmjapan.comwww.nlmjavanese.comwww.nlmkannada.comwww.nlmkazakhstan.comwww.nlmkenya.comwww.nlmkhmer.comwww.nlmkirghiz.comwww.nlmkirundi.comwww.nlmkorea.comwww.nlmlatvia.comwww.nlmluganda.comwww.nlmluo.comwww.nlmmadi.comwww.nlmmalagasy.comwww.nlmmalayalam.comwww.nlmmalaysia.comwww.nlmmarathi.com

www.nlmmauritius.comwww.nlmmexico.comwww.nlmmindat.comwww.nlmmizo.comwww.nlmmoldova.comwww.nlmmongolia.comwww.nlmmyanmar.comwww.nlmnepal.comwww.nlmnewzealand.comwww.nlmnigeria.comwww.nlmnorthkorea.comwww.nlmnorway.comwww.nlmpakistan.comwww.nlmpanama.comwww.nlmperu.comwww.nlmphilippines.comwww.nlmpoland.comwww.nlmportugal.comwww.nlmportuguese.comwww.nlmprcongo.comwww.nlmqatar.comwww.nlmromania.comwww.nlmrussia.comwww.nlmsaudiarabia.comwww.nlmserbian.comwww.nlmshona.comwww.nlmsingapore.comwww.nlmslovakia.comwww.nlmslovene.comwww.nlmsolomon.com

www.nlmsouthafrica.comwww.nlmspain.comwww.nlmspanish.comwww.nlmsrilanka.comwww.nlmsuriname.comwww.nlmswahili.comwww.nlmswaziland.comwww.nlmsweden.comwww.nlmswiss.comwww.nlmtagalog.comwww.nlmtaiwan.comwww.nlmtamil.comwww.nlmtelugu.comwww.nlmthailand.comwww.nlmtogo.comwww.nlmtonga.comwww.nlmturkey.comwww.nlmuganda.comwww.nlmukraine.comwww.nlmurdu.comwww.nlmusa.comwww.nlmvenezuela.comwww.nlmvietnam.comwww.nlmzambia.comwww.nlmzimbabwe.comwww.nlmzou.com

H

J

K

L

M

N

P

Q

R

S

T

U

V

Z

I

W The New Life Missionorldwide websites of